Text
stringlengths
292
6.6k
labels
int64
0
19
Akhristu Awapempha Akonde Kuthandiza Radio Maria Malawi Wolemba: Glory Kondowe Akhristu a mpingo wa katolika mdziko muno awapempha kuti azithandiza Radio Maria Malawi. A Maxwell Chikafa omwe ndi mbusa wa dera la Mzimu Woyera 1 ku St. Marys Nzama Parish mu Diocese ya Dedza ndiwo alakhula izi, lamulugu lapitali pambuyo pa mwambo wa Thandizani Radio Maria omwe unachitikira ku tchalitchi cha Mzimu Woyera 1 Tsangano Turn Off komwe akhristu anathandiza wayilesiyi ndi ndalama yokwana Mk133, 860. Abusa Chikafa ati ngati anthu akonda kuthandiza Radio Maria, wayilesiyi singamakumane ndi mabvuto azachuma, ngati mmene ziliri zithu padakalipano, polingaliranso kuti wailesiyi yatha zaka 20 ikutumikira anthu pofalitsa nthenga wabwino. Wayilesiyi imatithandiza munjira zosiyanasiyana moti kufalitsa mnthenga wabwino wa Yesu khristu zomwe zimatipatsa chiyembekeza. Wailesiyi imasowa zinthu zosiyanasiyana ndiye tiyenera kuyithandiza pa nkhani ya zachuma. A Chikafa anatinso akhristu ena ayenera kuchita chotheka poyikapo chidwi kugwira ntchito ndi wailesiyi ndipo aliyese amene atenga nawo mbari pothandiza radio maria zingati kutenga nawo mbali kufalitsa uthenga wabwino pa zaka 20 zomwe wailesiyi yakhala ikufalitsa nthenga wabwino monga chitsulo chimodzi sichiwunda chulu. Iwo anathokodzaso anthu onse amene amagwira ntchito yozipereka ngati awulutsi komanso atolankhani awailesiyi ndi kuwapempha kuti apitilize ntchito yopambanayi.
13
Mtima pansiAPM Ngati aMalawi adali ndi chiyembekezo choti aona kusintha kwakukulu pachuma ndi zina ndi zina zokhudza moyo wawo pambuyo pa kulumbiritsidwa kwa boma latsopano lotsogozedwa ndi Pulezidenti Peter Arthur Mutharika ndi chipani chake cha DPP, asathamange magazi chifukwa izi sizitheka lero ndi lero. Izi zili choncho chifukwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika Lachiwiri adati aphungu a Nyumba ya Malamulo sakambirana ndondomeko ya chuma cha dziko lino (Bajeti) yomwe imayenera kuyamba pa 1 July, 2014 mpakana pa 31 June 2015. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Polankhula koyamba ngati mtsogoleri wa dziko lino mNyumbayo, Mutharika adati mmalo mwake ndondomekoyi adzaikambirana mwezi wa August pofuna kupereka mpata woti boma liunike bwinobwino kunthambi zosiyanasiyana zinthu zofunika mundondomekoyi. Iye adati mmalo mwake aphungu angokambirana za ndondomeko ya chuma chapadera chomwe boma ligwiritse ntchito kuyambira mwezi wa July mpakana September, 2014. Gawo 178 la malamulo oyendetsera dziko lino limalola kukhala ndi ndondomeko yongoyembekezerayi. Tinali ndi nthawi yochepa yokonza ndondomeko ya chaka chonse. Komanso tiyenera kuunikira bwino ndalama zomwe zatsala kuthunba la boma tisanakonze ndondomekoyi, adatero Mutharika. Nduna ya zachuma Goodall Gondwe akuyembekezeka kukapereka ndondomeko yoyembekezerayi sabata ya mawa. Tikapereka ndondomekoyi tikhala tikufunsa anthu zimene akufuna kuti tiganizire mundondomeko ya chuma ya chaka chonse, adatero Gondwe. Mwa zina, Amalawi ambiri chidwo chawo chagona poti boma la Mutharika litsitsa liti mitengo ya malata ndi simenti kuti osauka amene akugona nyumba zofoleredwa ndi udzu komanso zozira ndi donthi nawo athe kumanga zofolera ndi malata komanso zasimenti pansi. Pokopa anthu kuti adzachivotere chipanichi panthawi ya kampeni zisankho zisadachitike pa May 20, 2014, akuluakulu adalonjedza Amalawi kuti chipani cha DPP chikadzakhalanso mboma chimodzi mwa zinthu zoyambirira pofuna kutukula miyoyo ya Amalawi ku kutsitsa mitengo ya malata ndi simenti kuti aliyense azigona mnyumba yoyenerera. Akatswiri mnthambi zosiyanasiyana mdziko muno ati boma lingachite bwino pachitukuko cha dziko litatsata bwino mfundo zomwe Mutharika adanena potsegulira Nyumbayo. Akatswiriwa ati Mutharika adanena mfundo zabwino zokhudza chitukuko koma sadatambasule bwino momwe mfundozo bioma lidzakwaniritsire. Zina mwa mfundo zomwe akatswiriwa ayamikira ndi zotukula ntchito za umoyo, ulimi ndi maphunziro koma ati sizikutambasula bwino mmene zidzayendere. Dalitso Kubalasa, mmodzi mwa akatsiwiriwa, yemwe ndi mkulu wa bungwe la Malawi Economic Justice Network lomwe ntchito yake ndi kuona mmene boma likuyendetsera chuma kuti chipindulire aliyense, wati boma lakhazikitsa mfundo zabwino kwambiri koma lalephera kufotokozera Amalawi mmene zidzayendetsedwere. Mfundozi ndizabwino kwambiri pachitukuko cha dziko lino ndipo nzosangalatsa kuti mtsogoleri akudziwa za mavuto omwe alipo pachuma. Koma ngakhale zili choncho, pali mfundo zina zofunika kuwongoledwa bwino kuti zigwire bwino ntchito yake, adatero Kubalasa pocheza ndi Tamvani Lachiwiri lapitali. Pankhani za umoyo, Mutharika adati, mwa zina, boma lidzakhazikitsa chisamaliro chapadera cha anthu ogwira ntchito mboma komanso lidzatukula miyoyo ya anthu ogwira ntchito mboma pakakwenzedwe pantchto ndi malipiro. Mkulu wa bungwe loona kuti ntchito za umoyo zikufikira anthu onse mofanana la Malawi Health Equity Network (Mhen), Martha Kwataine, akuti boma laganiza bwino pokhazikitsa chisamaliro chapadera cha anthu ogwira ntchito mboma, koma wadzudzula kuti silidatambasule bwino makamaka pa nthawi yomwe ntchitoyi idzayambe. Izi ndi zomwe takhala tikumenyerera kwa nthawi yaitali ndipo apa boma laganiza bwino kwambiri makamaka pakulonjeza kutukula miyoyo ya anthu ogwira ntchito za chipatala. Koma chomwe ndingapemphe boma ndi kutambasula bwinobwino nthawi yomwe izi zidzayambe kusiyana ndi kuti anthu azingokhala mumdima, adatero Kwataine. Mutharika adatinso boma lidzalimbikitsa ntchito zotukula achinyamata pokhazikitsa malo ophunzitsa achinyamata ntchito zosiyanasiyana kuti azikhala odzidalira paokha. Nduna yakale ya zachuma, Mathews Chikaonda, adati boma likuyeneranso kubwera poyera mmene ntchito yotukula achinyamatayi idzakhalire. Iye adati achinyamata ndi ofunika kwambiri pachitukuko cha mdziko choncho nkofunika kuika patsogolo ntchito zowatukula.
11
Anayi Anjatidwa Kamba Kochitira Chiwembu Mzika yaku Pakistan Apolisi ku Lilongwe amanga anthu anai omwe akuwaganizira kuti abera mzika in ya mdziko la Pakistan pachiwembu chomwe anayichitira. Watsimikiza za nkhaniyi-Benjamin Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi mboma la Lilongwe Sergeant Foster Benjamin wati amunawo, Farouk Rahim, Lenias Wright, George Kasabola ndi Sautso Mandala awamanga lachinayi powaganizira kuti anaba ndalama zokwana 400 sauzande kwacha komanso lamya zammanja za ndalama pafupifupi 470 sauzande kwacha usiku wa pa 27 April chka chino. Sergeant Benjamin wati pakadali pano anthuwa awuvomela mlanduwu, ndipo apolisi akupitiriza kufufuza anthu ena omwe anali limodzi ndi akubawa omwe sanapezeke. Farouk Rahim wa zaka 33 ndi wa mmudzi mwa Mazengela mdera la mfumu yaikulu Malengachanzi mboma la Nkhotakota, Lenias Wright wa zaka 30, ndi wa mmudzi mwa Michenga mdera la mfumu yaikulu Mabuka ku Mulanje, George Kasabola wa zaka 30 ndi wa mmudzi mwa Moyo mfumu yaikulu Phambala komanso Sautso Mandala wa zaka 40 zakubadwa, ndi wa mmudzi mwa Chikadya kwa mfumu yaikulu Ganya mboma la Ntcheu.
7
Kwacha yagwa, valani zilimbe Anthu akumudzi ati boma lifulumire kuika njira zowatchinjirizira ku zomwe zingadze kaamba ka kugwa kwa ndalama ya kwacha. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Anthuwa ati ngakhale boma komanso akatswiri ena pachuma akulosera kuti kugwa kwa kwacha sikukweza mitengo ya zinthu moliritsa, izi zikhoza kukhala khambakamwa chabe. Anthuwa akuti katundu wina anayamba kale kukwera mtengo udyo banki yaikulu ya Reserve itangolengeza Lolemba kuti ndalama ya kwacha yagwa ndi pafupifupi theka la mphamvu yake. Tsopano pafunika K250 kuti munthu apeze $1 [Dollar] ya dziko la America, kuchoka pa K168. Kusinthaku kwadza ndalamayi itagwanso mu Ogasiti chaka chatha. Mlimi wa mzimbe, chimanga ndi mtedza wa mmudzi mwa Manjeza kwa T/A Kadewere mboma la Chiradzulu, Maginesi Banda wati kumeneko zinthu zinakwera Lolemba atangolengeza kuti Kwacha yagwa. Banda wati sopo wopaka yemwe adali K50 pano wafika pa K75 ndipo Shuga wachoka pa K230 kukagwa pa K300. Iye wati zina zomwe zakwera mtengo ndi mchere, nyemba komanso nsomba. Zinthu zakwera mtengo Mlimi yemwenso amachita bizinesi ya chimanga mmudzi mwa Mkombanyama kwa T/A Mwaulambia ku Chitipa wati kumeneko zinthu sizili bwino ndipo anthu akuvutika. Mkuluyo, Charles Kabaghe, wati malata a 32 geji aatali milingo 10 akugulitsidwa K5 900 kuchoka pa K2 800, pomwe thumba la fetereza wa 50kg la mtundu wa 23:21:0+4s tsopnao lafika pa K14 800 kuchoka pa K8 500. Kabaghe wati nkhuku zanyama zikugulitsidwa pa K1 500 kuchoka pa K700, pomwe dzira lili pa K80 kuchoka pa K30. Boma litithandize, watero Kabaghe. Katakwe wa phunziro la zachuma kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Ben Kaluwa, wati ngati mabungwe ndi maiko akunja atapereka thandizo kudziko lino, ululu wa kugwa kwa kwacha sungakhale woriritsa kwambiri. Kaluwa wati thandizo la maiko ndi mabungwe lingaombole akumudzi ndi ena osowa kudzera mu zingapo monga malipiro a ntchito za chitukuko cha mmidzi. Ntchitoyi ndi monga yolambula misewu yomwe ogwira amalandirako kangachepe. Kumayambiriro kuno zinthu zikhala zovutirako koma posakhalitsapa titha kusimba lokoma chifukwa chokonza ubale ndi maiko komanso mabungwe othandiza dziko lino pachuma. Anthu angolimbikira kulima mbewu zoti angathe kugulitsa kumaiko ena monga fodya, thonje komanso nyemba chifukwa tsopano katundu wathu akhala wogulika, adatero Kaluwa. Akumudzi atetezedwe Koma Gulupu Chisinkha ya mboma la Mulanje kwa T/A Mabuka yati anthu ali ndi mantha kuti zinthu zivuta. Iyo yapempha boma kuti lionetsetse kuti anthu akumudzi atetezedwe. Anthu sangamvetse zomwe akuluakulu ena komanso boma likutanthauza akamati zinthu sizikwera. Chofunika nkuti aonetsetse kuti zomwe akulankhula zichitike chifukwa aliyense kumudzi kuno ali ndi mantha, adatero Chisinkha. Koma Kaluwa msabatayi ananenapo kuti mitengo ya zinthu sikuyenera kukwera moboola mthumba chifukwa amalonda ena anakweza kale mitengoyo. Iye anati pomwe mabanki samapezeka ndi ndalama zakunja, amalonda amakapeza ndalama ya dollar pamtengo wokwera mmisika yosavomerezeka ndi boma. Kunja kwa mabanki ovomerezeka, anthu mmisika yosavomerezeka ndi bomayo amasintha $1 pa mtengo wokwera, mpaka ena kumafika pa K300. Izi akatswiri adati zidali zizindikiro zoti ndalama ya kwacha inali itagwa kale pa chilungamo chake koma kuti boma limangochita liuma kuvomera izi. IMF ikutinji Sabata yatha, mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda, adauza atolankhani kuti alola ndalama ya kwacha ichepetsedwe mphamvu ngati bungwe loyanganira zachuma padziko lapansi la International Monitory Fund (IMF) ndi banki yaikulu padziko lapansi ya World Bank angatsimikizire dziko lino za thandizo la chuma. Msabatayi, potsatira kulola kuti kwacha itsike mphamvu, abwenzi a dziko lino pachuma monga IMF analengeza kuti akukonza ndondomeko zothandizira dziko lino kuti osaukitsitsa asamve ululu wakusintha kwa zachumaku. Iwo anati izi zikutsatira kusintha kwa kayendetsedwe kachuma komwe boma la Banda labweretsa molingana ndi ndondomeko za IMF komanso banki yaikulu padziko lapansi. Dziko lino limadalira ulimi komanso ndi limodzi mwa angapo mu Africa odikira thandizo la maiko ndi mabungwe akunja pa kapezedwe ka ndalama zakunja. Mwachitsanzo, mwa K100 iliyonse yomwe dziko lino limapata kuchokera ku malonda wogulitsa kunja, K60 imachokera ku malonda a fodya. Mwa K100 iliyonse ya ntchito za pansi pa ndondomeko ya chitukuko, K40 imachokera ku thandizo la maiko ndi mabungwe akunja. Koma kuchokera pomwe mitengo ku misika ya fodya inalowa pansi komanso kusokonekera kwa ubale ndi maiko akunja, dziko lino lakhala pa mpanipani wa zachuma. Ndalama zakunja Mmwezi wa Juni chaka chatha, mkulu wa IMF ku Malawi, Ruby Randall, anati kafukufuku mmayiko a kumwera kwa chipululu cha Sahara adasonyezapo kuti Malawi adali limodzi mwa maiko atatu omwe mapezedwe awo a ndalama zakunja adali wotsikitsitsa. Bungwe la IMF lakhala likupempha dziko lino kuti litsitse mphamvu ya ndalama ya kwacha koma mtsogoleri wakale wa dziko lino, malemu Bingu wa Mutharika, adakhala akumenyetsa nkhwangwa pamwala, ati kutero kungakweze zinthu mtengo moliza Amalawi. Kukanaku kunali chimodzi mwa zomwe Mutharika ananyanyula nazo maiko ndi mabungwe akunja mpaka kufika podula thandizo lawo. Apa Mutharika adaika ndondomeko ya chuma ya dziko lino yosadalira maiko ndi mabungwe akunja. Ngakhale mabungwe ena a mdziko muno nawo amati kunali koyenera kuvomera kutsitsa mphamvu ya kwacha, Mutharika anati sizitheka. Iye anati maiko ndi mabungwe akunja amapanikiza Malawi pa zachuma ncholinga chogwiritsa ntchito mavuti otsatira izi kuti afoole Malawi ndipo dzikoli lilole makhalidwe onyasa ponyengelera thandizo la ndalama. Iye anatchulapo zinthu monga maukwati a amuna okhaokha komanso ena a akazi okhaokha kapena kuloleza zithunzithunzi ndi makanema olaula. Mutharika anaitanitsa mafumu 158 kunyumba yachifumu ya Sanjika pa 12 chaka chino komwe atsogoleriwo akuti adati Mutharika akane ganizo la IMF. Iye adatanitsanso abusa omwenso ati adagwirizana ndi ganizo lokana kutsitsa mphamvu ya kwacha.
2
Uve ndi gwero la linyonyo Mkulu wa bungwe la Heart to Heart Foundation(HHF) mboma la Machinga Derlings Phiri wati gwero la matenda a linyonyo ndi uve. Malingana ndi Phiri, linyonyo ndi matenda a maso omwe munthu akalekerera kwa nthawi yaitali amayambitsa khungu. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kusamba kumaso ndi sopo kumathandiza kupewa linyonyo Iye adafotokoza kuti kukanda kapena kugwira mmaso ndi mmanja mosatsamba kumaika maso pa chiopsezo cha linyonyo chifukwa mmanja mwa uve mumakhala tizilombo tingonotingono toyambitsa matendawa. Ndi bwino kuti nthawi zonse anthu azisamba mmanja ndi sopo akachoka ku chimbudzi, akamaliza kusintha ana matewera komanso akagwira chinthu china chilichonse asanagwire mmaso mwao, adatero Phiri. Mkuluyu adati anthu akaona zizindikiro za matendawa monga kutuluka misonzi pafupipafupi, kuyabwa, kufiira maso ndi zizindikiro zina azithamangira ku chipatala kuti akapimidwe ndi madotolo. Osathira mankhwala a zitsamba mmaso chifukwa zina zimakhala dziphe zomwe zikhoza kuononga maso, adatero mkuluyu. Phiri adati ngakhale linyonyo limagwira munthu wina aliyense, limayala maziko kwambiri pa ana. Iye adati izi zimakhala chomwechi chifukwa ana nthawi zambiri amasewera pa fumbi ndi malo ena omwe amakhala ndi tizilombo toyambitsa matendawa makamaka ngati sakumbukira kusamba mmanja asadakande mmaso. Ndi udindo wa makolo kuphunzitsa ana kuti azikupewa kukanda mmaso ndi mmanja mwa uve kuti linyonyo litheretu mdziko muno, adatero mkuluyu. Phiri adaphera mphongo potsindika kuti munthu wina aliyense azisamba kumaso ndi sopo akangozuka chifukwa manthongo amaitana tizilombo toyambitsa linyonyo.
6
Mzika ya Dziko la Ghana Injatidwa Itapezeka ndi Mankhwala Ozunguza Bongo Wolemba: Thokozani Chapola adiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/10/ADARKWA.jpg 607w" sizes="(max-width: 240px) 100vw, 240px" />Wapezeka ndi mankhwala ozunguza bongo-Adarkwa Apolisi ku bwalo la ndege la Kamuzu mu mzinda wa Lilongwe amanga mayi wina wa mdziko la Ghana kaamba kopezeka ndi mankhwala ozunguza bongo otchedwa Apomorphine. Mneneri wa apolisi ku bwalo la ndegeli Sub Inspector Sapulani Chitonde watsimikiza za nkhaniyi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Mankhwala ozunguza bongo otchedwa Apomorphine omwe apezeka ndi mayiyo Iye wati mayiyu Sally Adarkwa wa zaka 45 zakubadwa anafika mdziko muno masiku anayi apitawo ndipo lero ndi pomwe amabwelera mdziko la kwawo koma atafika pa bwalo la ndegeli apolisi anamupeza ndi mankhwalawa omwe ndi olemera 5.2 kilograms. Mayiyu yemwe amayembekezeka kukwera ndenge ya south african airways ananjatidwa pa malo a chipikisheni omwewo ndipo akawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa. Izi zikudza patangopita maola khumi ndi awiri, apolisi omwewanso atamanga mzika ya dziko la Nigeria pamene imafuna kudutsitsa mankhwala ozunguza bongo otchedwa Cocaine. Padakalipano mkulu wa apolisi woona za mabwalo a ndenge a Mabvuto Chiumbuzo achenjeza anthu kuti mabwalo a ndege si malo odusitsira zinthu zosayenera.
7
Ndithu chili ndi mwini Kusankha Balaba Kumukana Yesu Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Usapange mistake, chonde chonde Nyimbo ya Evans Meleka idali kuphulika pa Wenela tsiku limenelo. Ya Ndirande iyi! Machinjiri inayo! Za Lilongwe mpaka ku Area 18 mwinamo! Koma abale anzanga, ngati pali dera limene latchuka zedi zaka zimenezi ndiye ndi Area 18. Pajatu nanenso mizu yanga ili ku Upper Area 18, inde kuja kwa Senti! Chomwe ndimadabwa nchoti akaphika nsima imakoma ngati muli kale soya pieces. Abale soya akanakhalako ndi khalidwe. Akanangosankha chimodzi. Soya yemweyo ena akukonza mkaka. Soya yemweyo ena akukonza masoseji! Akanakhala ndi khalidwe soyayu. Kumukana Yesu Kufuna Balaba! Nyimboyi idavuta kwambiri pa Wenela tsiku limenelo potengera ndi zija zidaachitika kwa Chinsapo. Atitu kumeneko chigandanga china chotchedwa Balaba chidaphedwa nkuvulidwa chinochino. Ya Ndirande iyi! Ya Machinjiri iyo! Ya ku Area 18 inayo! Mkulu anali oopsa uyu. Ngakhale apolisi amamuopa, moti anthu akakanena kupolisi kuti Balaba akuwasautsa, apolisiwo amaneneratu kuti mukamugwira Balaba mumubweretse kuno. Mpake anthuwo anamupititsa Balaba wakufa kupolisiko, adatero Abiti Patuma. Kusankha Balaba Kumukana Yesu Usapange mistake, chonde chonde! Ndipo ndangomva kuti mkulu wina wa kampani ya alonda wapeza tender yolondera polisi ya pa Wenela. Koma zisatikhudze, adatero wa pamalopo, Gervazzio. Gervazzio adayatsa kanema. Padali MBC-TV ndipo adabwera Jeffrey Kapusa. Adali kuulutsa nkhani ya mwana wina amene adagwiriridwa ndipo apolisi komanso amene amayenera kumuthandiza ena sanatero, msungwana kumangolira. Anthu ogwirira anawa tikadatha kuwatchula kuti zitsiru, koma sititero chifukwa mawuwo siwoyenera kuwatchula pagulu. Choncho tingoti ndi wopusa. Si zitsiru ayi, Kapusa adali kutero. Mr Splash! Mawu ake ali mkamwa, adatulukira Moya Pete. Ndakwiya khwambiri. Anthu inu ndi zitsiru! Ndinu zitsiru kwambiri! Zitsiru zakumwa madzi wochapira ndevu, adali kutero Moya Pete. Kenako, adatenga cholembera, nkulemba pamalaya a Gervazzio: Chitsiru.
15
Zipani zikufuna mayankho pa zitupa za unzika Zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi Peoples Party (PP) zati kusowa kwa zitupa zina za olembetsa mkaundula wa unzika zidzasokoneza chisankho cha patatu cha 2019. Nthambi ya National Registration Bureau (NRB) yati mwa zitupa 1.7 miliyoni zomwe zidajambulidwa mgawo loyamba la zitupa za unzika, 1.5 miliyoni ndizo zatuluka. Izi zili choncho, bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati lidzagwiritsabe ntchito zitupazo polembera ovota. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mlembi wa PP Ibrahim Matola adati zitupazo sizimayenera kugwiritsidwa ntchito mkalembera wa ovota chifukwa ntchitoyi siyinakhazikike. Tangoyamba kumene ntchitoyi. Tisayidalire ayi bola mtsogolomu zikadzagwira msewu koma padakalipano tiyeni tigwiritse ntchito njira yomwe timagwiritsa nkale lonse, adatero Matola. Mneneri wa chipani cha MCP Eisenhower Mkaka adati zitupa za unzika zokha sizikuyenera kugwiritsidwa ntchito pa mavoti chifukwa zina zikusowa. Kudzazigwiritsa ntchito limodzi ndi zitupa zovotera osati pazokha ayi poopa libolonje, adatero iye. Phungu wa ku mmawa kwa boma la Dowa, Richard Chimwendo-Banda wa MCP, adati kufaifa kwa zipangizozo kukhoza kuchititsa kuti anthu ambiri mchigawo cha pakati asadzakhale ndi zitupa ndikulephera kudzaponya nawo voti. Mkaka: Alongosole Mneneri wa MEC Sangwani Mwafulirwa watsindika kuti zitupazo zidzagwiritsidwa ntchito popanga kaundula wa odzavota pa chisankho cha 2019. Munthu amene adzakhale ndi chitupa, nzachidziwikire kuti ndi nzika ndiye sitidzalimbana naye zambiri komabe tidzaona momwe tidzathandizire omwe alibe zitupa, adatero Mwafulirwa. Iye adati MEC ikuyembekezeka kudzayamba kukonza kaundula wa odzavota ndipo akukhulupilira kuti pofika nthawi yamavoti, nzika iliyonse idzakhala italandira chitupa chake. Mneneri wa nthambi ya NRB Norman Fulatira wati anthu asakhale ndi nkhawa pankhaniyo chifukwa zivute zitani, Amalawi onse adzakhala ndi zitupazo.
11
Abwatika bwalo, Polisi ku mangochi Fisi adakana msatsi. Mayi yemwe adauza abale kuti mwamuna wake amafuna kugulitsa mwana wawo wa chialubino wasintha Chichewa. Vanessa Manyowa wauza bwalo la milandu ku Mangochi kuti zomwe adanenazo zidali zopeka chifukwa panthawiyo nkuti atayambana ndi mwamuna wake pa nkhani za kumunda. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kadadzera: Nzokhumudwitsa Mayiyo adabereka mwanayo wa chialubino asadakwatiwe ndi mwamuna wake watsopanoyu. Padakali pano mwanayo ali ndi zaka 14. Nkhaniyo idachitika mwezi watha pamene Manyowa adauza achimwene ake kuti mwamuna wake, Nick Adams, wa zaka 38 amafuna kugulitsa mwanayo. Achimwenewo adatengera nkhaniyo ku polisi ya Mangochi moti Adams adamangidwa ndi mlandu woganiziridwa kugulitsa mwana wa chialubino. Lachinayi sabata yatha nkhaniyo adaitengera ku khoti la mbomalo komwe Manyowa adasintha Chichewa. Manyowa adauza bwalolo kuti adapeka nkhaniyo atayambana ndi mwamuna wakeyo chifukwa adamukaniza kutengapo gawo lake la chimanga ndi mtedza womwe akolola. Ndazindikira kuti ndidalakwitsa kwambiri. Mwamuna wanga sadanenepo zoti akufuna kugulitsa mwana wathu, Manyowa adauza bwalo. Izitu zidachititsa Manyowa ndi achimwene ake apemphe bwalolo kuti mlanduwo utsekedwe. Woweruza mlanduwo, Joshua Nkhono adadzudzula Manyowa popekera mwamuna wake nkhani. Nkhono adati nkhani zokhudza anthu achialubino nzovuta choncho mayiyo adalakwitsa. Apa woweruzayo adathetsa mlanduwo, koma adanenetsa kuti bwalo lilanga aliyense wopeka nkhani zokhudza anthu achialubino. Nawo apolisi ati ndiwokhumudwa kaamba koti Manyowa adawapusitsa. Mneneri wa apolisi mdziko muno James Kadadzera adati zomwe wachita Manyowa nzobwezeretsa zinthu mmbuyo. Kadadzera adati palibe chomwe apolisi angachite chifukwa mlandu watha. Polankhulapo mtsogoleri wa bungwe la anthu oyimira anzawo pa milandu la Malawi Law Society (MLS) Burton Mhango adati Manyowa ali ndi ufulu wotseketsa mlandu. Iye adati zimatengera kukula kwa mlanduwo, komanso umboni womwe ulipo. Pankhaniyi zikuonetsa kuti wodandaula yemwenso akadakhala mboni yaikulu ndi yemwe adafuna kuti mlanduwo utsekedwe, choncho ngakhale apolisi akadafuna kuti upitirire sizikadaphula kanthu chifukwa pakadakhala popanda mboni. Mlandu wopanda mboni umavuta, adatero Mhango. Koma Mhango adati zomwe wachita Manyowa zaika pachiopsezo moyo wa mwana wake chifukwa anthu akudziwa komwe akupezeka ndipo ena oyipa moyo akhoza kumuchita chipongwe. Choncho Mhango adapempha aboma kuti apereke chitetezo chokwanira kwa mwanayo kuti ambanda asalowererepo.
7
JB asankha Kachali Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda Lachitatu adasankha Khumbo Kachali kukhala wachiwiri wake. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kachali, yemwe ndi phungu wa ku Mzimba, ndi wachiwiri kwa Banda mchipani cha Peoples Party (PP). Kachali ndi wachinayi kukhala paudindowu kuchokera pomwe dziko lino lidayamba ndale za zipani zambiri mu 1994. Mmbuyomu, Justin Malewezi, Cassim Chilumpha ndi Banda adakhalapo paudindowu. Kusankhidwa kwa Kachali kudadza tsiku limene Banda adasuntha mlembi wamkulu muofesi ya mtsogoleri wadziko lino ndi nduna zake woona za madyedwe ndinso za HIV Dr Mary Shawa kupita kuunduna woona za amayi. Maudindo ambiri akhala akusinthidwa msabatayi kutsatira imfa ya mtsogoleri wakale wadziko lino Bingu wa Mutharika, yemwe adamwalira pa 5 Epulo kunyumba ya boma ku Lilongwe atadwala nthenda ya mtima. Thupilo adalitengera kuchipatala cha Kamuzu Centre mumzinda wa Lilongwe koma malinga ndi malipoti achipatala akuti Mutharika adali atamwalira kale pomwe amafika kuchipatalako. Madzulo a Lachinayilo, boma lidati Mutharika amutengera ku KCH komwe adati akudwala mtima. Lachisanu pa 6 mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bakili Muluzi komanso Banda adachititsa msonkhano pomwe adati malamulo adziko lino akuyenera kutsatidwa pa yemwe alowe mmalo mwa Mutharika ngati iye wadwalika kapena wamwalira. Lachisanu lomwelo cha mma 11 koloko usiku, akuluakulu ena aboma monga Patricia Kaliati, Nicholas Dausi, Kondwani Nankhumwa, Symon Vuwa Kaunda adachititsa msonkhano wa atolankhani ku Area 4 mumzinda wa Lilongwe. Pa msonkhanowo, Kaliati adatsutsa zomwe Muluzi komanso Banda adanena ndipo adati Banda sakuyenera kukhala mtsogoleri chifukwa adachoka mchipani chomwe chimalamulira cha DPP ndikukayambitsa chipani chake cha PP. Kaliati adakananso kuti sanena momwe Mutharika akupezera koma adangoti ali ku chipatala cha Milpark mdziko la South Africa. Apa nkuti nyumba zoulutsira mawu zamaiko ena zitalengeza kuti Mutharika wamwalira. Mmawa wa Loweruka Ofesi ya Pulezidenti ndi Nduna idalengeza kuti Mutharika wamwalira ndipo idati Amalawi akhuza malirowo kwa masiku khumi. Lowerukalo, yemwe adali wachiwiri kwa mtsogoleriyu, Joyce Banda adalumbiritsidwa kukhala mtsogoleri wa dziko lino. Mutharika yemwe adali mwana wa mphunzitsi adabadwa mu Febuluwale 1934 ndipo amachokera mmudzi mwa Kamoto mboma la Thyolo. Mutharika dzina lake adali Ryson Webster Thom ndipo adasintha dzinali mzaka za mma 1960. Malemuwa omwe adali katswiri pa zachuma adasankhidwa kukhala mtsogoleri wa dziko la Malawi mu 2004 kukhala mtsogoleri wa dziko lino ataimira chipani cha UDF.
11
Akufuna wogwirizira ufumu achoke, apepese Mafumu mdziko muno agwirizana ndi ganizo la mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda kuti magulupu ndi nyakwawa asiye kulandirira ndalama kubanki. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Banda adalankhula izi sabata yatha pasukulu ya Nsumwa mboma la Salima poyankha pempho la mfumu Ndindi kuti mafumu akuvutika pokalandirira ndalama kubanki. Polandira Banda, Ndindi adati ndondomeko yomwe idayambitsidwa mboma la chipani cha DPP kuti iwo adzikalandilira mswahala kubanki yazunza mafumuwa ponena kuti ndalamayo imathera ulendo. Apa Banda adati nyakwawa ndi magulupu asamakalandirirenso ndalama kubanki ponena kuti ndondomeko yapoyamba ibwezeretsedwa. Apa mafumuwa ati nkhaniyi iwathandiza chifukwa ndalamayo samaiwona ubwino wake malinga nkuti komwe kuli mabanki ndi komwe amakhala ndi mtunda wautali. Nyakwawa Kapoti ya kwa T/A Zilakoma mboma la Nkhata Bay yati kuchokera mmudzimo kukafika kuboma komwe kuli mabanki ndi mtunda omwe amalipira K2 000 kupita ndi kubwera. Mfumuyi yauza Tamvani kuti penanso akapita ndalamazo amakapeza zisadalowe. Ndimalandira K2 500 ndipo ndimaononga K2 000 kusonyeza kuti malipiro anga ndi K500. Apa tiyamike kuti tizilandira kumudzi kuno, idatero mfumuyo. Gulupu Chisinkha ya mboma la Mulanje kwa T/A Mabuka yati mfundo ya boma ili bwino bolani ndalamazo adziwapatsadi. Ndondomeko yapoyambayonso idali ndi mavuto ake pomwe pena malipiro sitimalandira. Ganizoli nlabwino bola tizilandira, adatero Chisinkha. Mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bingu wa Mutharika ndiye adalamula kuti aliyense wogwira ntchito mboma kuphatikiza mafumu adzikalandira malipiro awo kubanki.
8
Maliro pa chisangalalo Mwambo wa chikondwerero choti dziko lino latha zaka 53 lili pa ufulu wodzilamurira lidasanduka chisoni pomwe ana 7 ndi bambo mmodzi adamwalira pokanganirana kulowa mbwalo la za masewero la Bingu National Stadium kumene kumayenera kuchitika mpira waulere. Izi zidadziwika pomwe mtsogoleri wa dziko lino adatsogolera Amalawi pa mapemphero wolingalira za ufuluwo ku Bingu International Convention Centre (BICC) pomwe woyendetsa mwambowo mbusa Timothy Nyasulu adalengeza za omwalirawo. Iye adapempha anthu kuti akhale chete kwa mphindi imodzi polemekeza mizimu ya omwalirawo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wapolisi kuthandiza mmodzi mwa ana ku BNS Ndipo nduna ya zamalonda ndi mafakitale Joseph Mwanamvekha, yemwenso adali wapampando wa komiti yoyendetsa mwambowo, adatsimikiza za imfa ya anthuwo mapemphero ali mkati. Iye adati anthu oposa 40 adavulala pangoziyo. Nthambi yofalitsa nkhani za boma lidati anthu 65 adamwalira. Mutharika ndi mayi Gertrude Mutharika adakazonda anthu amene adavulala pa chipwilikiticho ku Kamuzu Central Hospital. Mutharika adati :Boma ndi lokonzeka kuthandiza pangoziyi. Dziko la Malawi limakumbukira kuti latha zaka 53 kuchokera pamene mtsogoleri wa dziko lino Dr Hastings Kamuzu Banda adakwanitsa kupeza ufulu kuchokera kwa Angerezi amene adayamba kulamulira dziko lino mzaka za mma 1890. John Chilembwe, mmodzi mwa Amalawi oyambirira kufuna kumenyera ufuluwo adamwalira mu 1915. Zikondwerero za chaka chino zinalipo kuyambira Lachitatu pa 5 July pomwe asilikali ndi achitetezo ena adayenda mmizinda ya Blantyre, Zomba ndi Mzuzu. Ndipo chikondwerero chimayenera kufika pa mponda chimera pa masewero a Nyasa Big Bullets ndi Silver Strikers amene amayembekezeka kuchitika kumalo a ngoziyo. Komatu galimoto za chipatala ndi zapolisi zidali kukangalika kuthandiza ovulala pa zisawawazo. Koma polankhula ndi Tamvani zisangalalozo zisanachitike, Amalawi ena adati ngakhale dzikoli latha zaka 53 likudzilamulira maloto ena amene adalipo pomenyera ufulu wa dziko lino. Yemwe adakhalapo sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Sam Mpasu adati mMalawi wa zaka 53 ali panayi: Zina zasintha pangono, zina sizinasinthe, pomwe zina zaima kapena kubwerera mmbuyo. Iye wati kunena mosapsatira zaka 53 sizidabweretse kusintha kwenikweni paulamuliro ndi kayendetsedwe ka maufulu a anthu mdziko muno. Mwa zina, iye adati ulamuliro wa Kamuzu Banda udayesera kubwezeretsa ulimi mchimake pamene adakhazikitsa makampani otulutsa zinthu zina kunja zimene mu ulamuliro wa atsamunda zimakapangidwa kunja, koma zina sizikuyenda. Adapereka zitsanzo za makampani a Sucoma, yomwe inkakonza shuga, Malawi Cotton yomwe inkaomba nsalu komanso British American Tobacco yomwe inkapanga ndudu ngati zina mwa zotsimikiza izi. Dziko lino lisanaladire ufulu, Mpasu adati zonsezi zinkabwera kuchokera kunja, ngakhale alimi ochuluka amene ankazilima mdziko muno ankatumiza kunja chifukwa adali Atsamunda. Kamuzu adayesetsanso kulimbikitsa msika wa mbewu kudzera ku Admarc ndipo adaonetsetsa kuti manyamulidwe a mbewu ngosavuta chifukwa kudali sitima za panjanji zomwe zimanyamula katundu pa mtengo otsika kupita ku misika, watero Mpasu. Ndipo mkulu wa bungwe loyanganira za momwe maphunziro akuyendera mdziko lino George Jobe wati pakutha pa zaka 53, Malawi amayenera kukhala ndi ntchito za umoyo za pamwamba motsatira chiyenerezo cha bungwe lalikulu loyanganira zaumoyo la World Health Organisation (WHO) koma mmalo mwake zinthu zambiri sizikuyenda. Mpaka pano sitidayambe kukwaniritsa mlingo wa WHO oti K15 pa K100 iliyonse mbajeti izikhala ya za umoyo. Chiwerengero cha ogwira ntchito za chipatala chikadali chotsika kwambiri poyerekeza ndi anthu omwe dokotala mmodzi amawona pa tsiku, watero Jobe. Ndipo kupatula zaumoyo, mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zamaphunziro, Benedicto Kondowe wati sizoona kuti zaka 53 zingathe ana asukulu makamaka a kuma Yunivesite nkumakhala pakhomo miyezi yambiri chifukwa cha mavuto msukulu zawo. Iye wati pa zaka zonsezi, atsogoleri amayenera kukhala atapanga njira zothandizira kuti kalendala ya sukulu kuyambira ku pulayimale mpaka ku Yunivesite isamasokonekere chifukwa kutereku nkulowetsa maphunziro pansi. Posachedwapa, aphunzitsi adali pa sitalaka pa nkhani ya maphunziro ndipo tikunena pano ophunzira mma Yunivesite sadatsegulire chitsekereni miyezi ingapo yapitayo nkhani yake kayendetsedwe, adatero Kondowe.
1
Sapereka chithandizo Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 21 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Amuna anga adandisiya ataona kuti ndili ndi pathupi ndipo mwana atabadwa adauzidwa koma mpaka pano sadabwereko kudzaona mwana wawo. Ndikawauza za chithandizo samayankha, amangozengereza. Chomvetsa chisoni nchakuti munthune ndimakhala ndi agogo okalamba poti makolo anga onse adamwalira. Ndithandizeni, ndipange bwanji? Pepa mtsikana, Apa zikuonekeratu kuti ngakhale ukuti amuna anga anthunu simunali pabanja ngakhale mumagonana mpakana kuberekerana mwana. Chimene chimachitika nthawi zambiri nchakuti atsikana akangogwa mchikondi ndipo mwamuna akangowauza kuti awakwatira, basi amaganiza kuti mwamuna ndi yemweyo basi ndipo amayamba zogonana naye ati pofuna kulimbikitsa chikondi kuti asamakaike za chikondi chawo, kumene kuli kulakwa kwakukulu. Atsikana ambiri aononga tsogolo lawo chifukwa cha mchitidwe wotere chifukwa anyamata kapena amuna ambiri ndi akamberembere, ongofuna kudzisangalatsa osalabadira za tsogolo la mnzawo. Akangomva kuti mtsikana watenga pathupi basi, chibwenzi chimathera pomwepo. Zikatero mtsikana zako zada. Koma dziko lino lili ndi malamulo okhudza maukwati ndipo ngati wina wakuchimwitsa, ali ndi udindo woti akusamale komanso mwana. Ndiye apa usazengerezepita ukadule chisamani kukhoti basi kuti chilungamo chioneke. Mwina amuna ena amene amakonda kuchimwitsa ana a eni akhoza kutengerapo phunziro! Ndinamugwira chigololo Anatchereza, Ndakhala pabanja zaka 25 ndipo ndili ndi ana anayi. Mwatsoka tsiku lina ndidapezerera akazi akuchita chigololo ndi mwamuna wina koma adathawa kotero kuti sindidathe kumulanda china chilichonse ngati umboni ndipo pachifukwa ichi mlandu sudandikomere, amfumu adagamula kuti nkhani yanga ndi yopanda umboni choncho banja siliyenera kutha. Ine kubanjako ndidachokako koma mkazi wangayo akumapepesa kuti ndimukhululukire. Ndithandizeni, nditani pamenepa? Achimwene, Pepani ndithu kuti banja lanu lagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirika kwa akazi anu. Kukhala mbanja zaka 25 si chapafupi ndipo kuti lero ndi lero banja lithe chifukwa choti wina wapezeka akuchita chigololo ndi chinthu chomvetsa chisoni zedi, makamaka chifukwa angavutike kwambiri ndi ana osalakwa. Kodi, achimwene, mumapephera? Ndafunsa choncho chifukwa ngati mumakhulupirira Mulungu, mawu ake kudzera mwa mwana wake Yesu Khristu, amatiphunzitsa za kukhululukira anzathu akatilakwira, osati kamodzi kapena kawiri kokha, ayi, koma maulendo 77 kuchulukitsa ndi 7 (77 x 7). Kodi inuyo mukufuna kunena kuti simudachimwepo ndi mkazi wina kapena mkazi wamwini chikwatirireni? Mwina mudachitapo chigololo koma simunagwidwe chabe! Ndiye apa, poti mkazi wanu wagwira mwendo kuti mumukhululukire, ine pempho langa ndi loti mutero ndithu, munthu salakwira mtengo, koma munthu mnzake. Ngati Mulungu amatikhululukira tikamuchimwira, ife ndani kuti tisakhululukire mnzathu akatilakwira? Mwachoka, kutali limodzi, chonde ganizani mofatsa. Komabe ndi mmene kunja kwaopsera masiku ano ndi mliri wa HIV/Edzi, ndi bwino ngati mungabwererane kuti mukayezetse magazi musanayambe kukhalira malo amodzi kuti mudziwe mmene mthupi mwanu mulili. n
15
Kuli zionetsero pa 13 December Lachitatu pa 13 December kukhala ali ndi mwana agwiritse mzigawo zonse zitatu za dziko lino pamene bungwe la mipingo la Public Affairs Committee (PAC) litsogolere zionetsero. Izitu ndi zionetsero zokakamiza boma kuti libweretse mabilo okhudza za chisankho mu Nyumba ya Malamulo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chilima (R) adawerenga kalata Mabilowo, mwa zina, akukamba kuti mtsogoleri wa dziko azisankhidwa ndi mavoti oposa 50 peresenti. Sinodi ya mpingo wa CCAP ku Livingstonia ndi sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu apsepserezera zionetserozi posindika kuti patsikuli akayenda ku msewu. Mbusa Levi Nyondo wati PAC ikulankhula zenizeni kotero nkofunika kuthandizana nayo pa nkhondo yokakamiza boma. Mamembala onse ampingo akupemphedwa kuti apite kumsewu kukachita zionetserozo, adatero Nyondo. Lamulungu lathali, wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima adawerenga kalata ya mpingo ku Parish ya St Patrick mu mzinda wa Lilongwe yomwe imapempha Amalawi kutengapo gawo pa ziwonetserozo.
11
Dayosizi ya Dedza Yati Akhristu Ake Adzipemphelera Panja Mpingo wa katolika mu dayosizi ya Dedza wapempha akhristu ake kuti adzichita miyambo ya nsembe za Misa panja pa tchalitchi ngati njira imodzi yopewera mliri wa Coronavirus. Malingana ndi kalata yomwe yatulutsidwa dzulo pa 6 July ndipo yasainidwa ndi mkulu owona za utumiki mu dayosiziyi bambo Peter White, izi zadza kaamba kofuna malo opemphelera otakasuka pofuna kuchepetsa kufala kwa nthendayi. Akuti anthu azipemphera panja pa tchalitchizi Bambo White ati ngakhale pali mavuto ena omwe ngadze kaamba kopemphera panja, akhristu akuyenera kupilira kusiyana ndi kuti atenge nthendayi. Milungu ingapo yapitayi tinawona kuti matchalitchi athu akutsatira zomwe a chipatala akunena koma chifukwa cha kuchepa kwa malo a mtchalicthi, anthu sakumakhala motalikirana ndipo apa ndi pomwe tinakhala pansi ndi kuona kuti akhritsu azisonkhana panja pa tchalitchi popeza kuti pali malo aakulu, anatero bambo White. Iwo ati pamene amapanga chiganizo chimenechi anaganiziranso mavuto omwe akhristu azikumana nawo maonga mphepo komanso kakhalidwe ka malo a panjapo komabe iwo ati akhristuwa akuyenera kupilira kusiyana ndi kuti atenge nthendayi kaamba kothithikana mtchalitchi.
13
kwa Ngombe zamkaka zimalira chisamaliro chokwanira Lasford Mbwana ndi mmodzi mwa alimi a ngombe zamkaka omwe akuchita bwino kwambiri kwa Bvumbwe mboma la Thyolo. Moti mlimiyu akuyenda chokhala kaamba koti adagula galimoto kuchokera mu ulimiwu. BRIGHT KUMWENDA adacheza naye motere: Tafotokozani, kodi ulimi wa ngombe zamkaka mudayamba liti? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ulimi wa ngombe zamkaka ndidayamba 2006 nditaona momwe anzanga amapindulira. Moti ngombe yanga yoyamba ndidagula K130 000 ndipo ndakhala ndikuonjezera mpaka zidafika 8. Kodi mwapindula motani ndi ulimiwu? Mbwana kudyetsa ngombe zake zizipereka nkaka wochuluka Phindu ndi losachita kunena. Ndikadakhala kuti sindikupindula sindikadaonjezera chiwerengero cha ngombe zanga. Ngombe za mkaka zimandipatsa ndowe zothira kumunda, ndalama zogulira chakudya, zovala ndi zinthu zina zosoweka pabanja panga. Panopa banja langa likuyenda chokhala chifukwa choti tidagula galimoto kuchokera mu ulimi womwewu. Nanga mungamulangize zotani munthu amene akufuna kuyamba ulimi wa ngombe zamkaka? Choyamba akhale ndi ndi chidwi ndi ziweto, malo wobzala nsenjere, amange khola labwino, akhale pafupi ndi madzi, komanso msika wa mkaka. Kodi mukati khola labwino mukufuna kunena chiyani? Khola labwino limakhala ndi malo wodyera, wokamira mkaka, womwetsera mankhwala, wosewerera, wokhalira mwana akabadwa, woti ngombe izikhala panthunzi ikafuna kupuma kapena kugona. Kodi patsiku mumakama mkaka wochuluka motani? Ngakhale ndili ndi ngombe 8 ndikukama zinayi zokha chifukwa choti zina ndi zazingono. Udzu, deya ndi masese zikamapezeka mosavuta ndimakama malita osachepera 100 patsiku omwe amandipatsa ndalama zokwana pafupifupi K500 000 pamwezi. Chinsinsi choti ngombe izitulutsa mkaka wambiri nchiyani? Kudyetsa mokwanira, komanso mtundu wa ngombezo. Ngombe sizisiyana ndi munthu. Kodi simukudziwa kuti mayi akamadya mokwanira mwana wake amasangalala chifukwa choti mkaka umatuluka wambiri? Ngombe zamakono zimatulutsa mkaka wambiri pofanizira ndi zachikaladi. Mukati ngombe zachikaladi mukufuna kutanthauzanji? Ukapereka umuna wa ngombe za Chizungu kwa ngombe zachikuda za Malawi Zebu, ana obadwa amakhala makaladisakhala azungu kapena achikuda. Amakhala a pakatikati. Moti mkaka omwe amatulutsa sukhala wambiri ngati wa ngombe ya Chizungu, komanso sukhala wochepa kwambiri ngati wa yachikuda. Kodi ngombe zanu ndi za mtundu wanji? Ngombe zanga ndi za mtundu wa Holstein. Alimi ambiri a ngombe za mkaka mdziko muno akuweta ma Holstein, Jersey kapena ma Friesian. Tafotokozani, kodi mumagula kuti ngombe zamkaka? Timagula kwa alimi anzathu. Ena amagula mmafamu a boma monga ku Mikolongwe ku Chiradzulu, Likasi ku Mchinji, Diamphwi ndi Dzalanyama ku Lilongwe ndi Dwambadzi ku Mzimba. Mabungwe a alimi a ngombe zamkaka a Shire Highlands Milk Producers Association (Shmpa), Central Region Milk Producers Association (Crempa) ndi Mpoto Dairy Farmers Association (MDFA) amathandizanso alimi kupeza ngombe zamkaka. Nanga munthu asungire zingati akafuna kugula ngombe zamkaka? Zimatengera ndi wogulitsa, komanso komwe ukukagula ngombezo. Alimi ambiri amagulitsa ngombe pamtengo wapakati pa K250 000 ndi K300 000. Ikakhala yabere imafika mpaka K400 000. Ndi mavuto otani omwe alimi a ngombe zamkaka amakumana nawo? Kusowa kwa madzi ndi zakudya makamaka miyezi ya pakati pa October ndi April. Nthawi imeneyi deya amasowa, komanso udzu umavuta kuwupeza. Moti alimi amayenda mitunda italiitali kuti apeze udzu wodyetsa ngombe zawo. Chaka chathachi thumba la deya tim0agula K6 000. Ngakhale adali wokwera mtengo, amavuta kupeza. Kuthimathima kwa magetsi kumawononga mkaka. Alimi a ngombe zamkaka amapanga magulu osiyanasiyana (bulking groups) omwe amasunga mkaka wawo mmalo ozizira, kudikira makampani kuti adzagule mkakawo. Magetsi akathima, mkaka ndi kuwonongeka asadadzautenge ndiye kuti alimi ali mmadzi. Kuphatikizira apo, mitengo yomwe makampani amatigulira mkaka ndi yotsika kwambiri. Ulimi wa ngombe zamkaka susiyana ndi wa fodya chifukwa wogula ndi amene amayika mtengo. Ndi matenda otani omwe amagwira ngombe? Chifuwa chachikulu, chigodola, zotupatupa ndi ena mwa matenda omwe amazunza ngombe. Nanga mawu anu otsiriza ndi wotani? Potsiriza ndikufuna ndipemphe anzanga kuti akumbe zitsime ndi kubzala nsenjere kuti asamavutike kupeza madzi ndi chakudya mudzinja.
4
Tikolola chimanga chochulukaNduna Nduna ya zamalimidwe komanso kuonetsetsa kuti mdziko muno muli chakudya chokwanira, Peter Mwanza yati undunawu ukulosera kuti chaka chino dziko lino likolola chimanga chochuluka ndikukhala ndi china chapadera. Polankhula Lachitatu mumzinda wa Lilongwe pomwe amafotokozera atolankhani za kholola wa chaka chino, ndunayi yati malinga ndi zolosera dziko lino lingapate matani 740 000 a chimanga apadera. Chaka chatha dziko lino lidapeza matani oposa 500 000 apamwamba. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Zolosera za ndunayi zikudza pomwe zadziwika kuti Dedza ndi madera ena kuchigawo cha kumpoto kwa dziko lino mvula yachita njomba ndipo alimi ali pachiopsezo kuti mwina galu wakuda awayendera kumeneko. Ngati zoloserazo zingatheke ndiye kuti dziko lino likhala ndi chakudya chambiri chapadera chifukwa dziko lino limafuna matani achimanga 2.6 miliyoni. Mwanza adati ichi ndi chisonyezo chabwino kuti dziko lino lapata chimanga chambiri chapadera ndipo adati boma liyesetsa njira ya zipangizo zotsika mtengo kuti dziko lino lipate chakudya chambiri. Mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda polankhula atangokwanitsa chaka akulamulira ku Lilongwe adati madera omwe akhudzidwa ndi njala ndi ochepa kotero boma liyesetsa kuti ulimi wa mthirira uyambike kuti njala ithe mdziko lino. Mu 2012 dziko lino lidapeza matani 3.624 miliyoni a chimanga ndipo chapadera adali matani 566 552 pomwe mu 2011 tidakolola matani 3.8 miliyoni ndi chapadera matani 1.2 miliyoni. Padakali pano boma kudzera mwa Banda lalengeza kale kuti ndondomeko ya makuponi ipitirira ndipo anthu omwe adzalandire makuponiwa ndi 1.5 miliyoni. Nambalayi idakwezedwa pomwe Banda adayamba kulamula kuchoka pa 1.4 miliyoni.
4
President Al-Sisi Akumana Ndi Ziwonetsero Zoyamba Wolemba: Thokozani Chapola mw/wp-content/uploads/2019/09/al-sisi.jpg" alt="" width="524" height="366" />Malamulo atsopano akumulora kulamulira dziko la Egypt mpaka 2030-Al-Sisi Apolisi a mdziko la Egypt agwiritsa ntchito utsi wokhetsa msozi pothamangitsa anthu ena omwe amachita zionetsero zotsutsana ndi ulamuliro wa mtsogoleri wa dzikolo ABDUL FATTAH AL-SISI. Anthuwa ati akufuna kuti Al-Sisi atule pansi udindo wake pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi katangale yemwe akuchitika mboma. Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, ziwonetserozi ndi zoyamba kuchitika chimusankhireni pa udindowu mchaka cha 2014. Padakalipano anthu asanu ndi omwe amangidwa pa ziwonetserozi. Mchaka cha 2013 AL-SISI anatsogolera asilikali a dzikolo pothetsa ulamuliro wa mtsogoleri woyamba mu mbiri ya democracy ya dzikolo MOHAMMED MORSI. Pa chisankho cha mchaka cha 2018 president AL-SISI anapambana ndi 97 percent kaamba koti panalibe munthu wachikoka kwambiri yemwe amapikisana naye. Mwezi wa April chaka chino anthu a mdziko la Egypt anachita voti ndipo anasankha kuti malamulo a dzikolo asinthe kuti athe kulora president AL-SISI kukhala pa udindowu mpaka chaka cha 2030.
11
MCP yatiphunzitsa zambiri Nkhani idali mkamwamkamwa miyezi ingapo yapitayi ndi ya msonkhano waukulu wa chipani cha MCP. Zimakaikitsa ngati kumsonkhanowo kukamangidwe mfundo zolemekeza maganizo a anthu. Chikaiko chidakula pamene mphekesera zidali mbweee! Makamaka chipanicho chitalephera kuchititsa msonkhanowo mwezi wa April. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chikaikocho chidakula zitamveka kuti chipanicho chikufuna kuti anthu ena, makamaka amene angobwera kumene mchipanimo asapikisane nawo pa\mpando wa pulezidenti. Komiti yapadera ndiyo idapereka mwayi onse kuti onse amene adapereka maina awo akhoza kupikisana nawo. Nkhani imodzi imene idatsalira idali yakuti John Tembo, amene malamulo amamuletsa kuti sangaime nawo chifukwa adaimira kale chipanichi kawiri, naye amafuna kupikisana nawo. Koma nthumwi za kumsonkhanowo, zitafunsidwa ngati angakambirane zosintha malamulowo, zidakana kwa mtuu! Wagalu. Izi zikudza pomwe zipani zina monga cha UDF, zidasintha malamulo kuti mwana wa mtsogoleri wakale wadziko lino Bakili Muluzi, Atupele, aimire chipanichi. Poyamba, Atupele sakadapikisana nawo chifukwa malamulo amaletsa kuti amene sadakwane zaka 35 asapikisane nawo. Nthumwi zidasintha malamulowo kuti Atupele aime. Ndipo nthawi yosankha atsogoleri itakwana, nthumwizo zidasankha amene amaoneka ngati alendo kuposa nkhalakale za chipanicho. Izi zikungosonyeza kuti demokalase ya mchipani yayala nthenje mu MCP. Koma chomwe tingalangize atsogoleri a chipanichi kuti akhale okhwima mundale ndi kumulandira Kusakhale kugawanikana monga zidalili Tembo atangogonjetsa Gwanda Chakuamba mu 2003.
11
Chalaka Kinnah Tom sangatole Aganyu tidagwiritsidwa utsi titalonjezedwa ndi yemwe anali mphunzitsi wa Flames Tom Santfiet kuti Flames ikavulaza Nigeria. Nigeria idatiumbudza 2-0. Iye adatulutsa Robin Ngalande poseweretsa Atusaye Nyondo yekha kutsogolo ngakhale timaluza. Kodi amatchinjiriza chiyani? Uyutu adali ndi kampeni. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Aganyu zikutiwawabe. Tom wapita atalephera kuchita chomwe chidamuchotsetsa ku Belgium. Ngakhale tikumva kuwawa, Fam ikusangalala chifukwa tathera nambala 2 mgulu lathu. Suzgo Nyirenda ndiye watero. Koma Nyirenda adziwe kuti palibe chosangalalira chifukwa panambalayi sitilandira kanthu komanso sitipita kulikonse. Aganyu tilikhwira Fam chifukwa zonsezi ndi iyo. Uncle Tom adawatenga kuti? Nanga mudadziwana naye bwanji? Mudatsimikizika bwanji kuti angatithandize? Ku Zambia adagonja kwa Angola ndi Zimbabwe. Ku Botswana adakagonjanso 1-0. Nigeria ndi iyo idamukodzetsa akuwonayo. Chanzeru wachita ndikupha Rwanda timu yomwe ndi ananso kwa ife. Tikuona kuti vuto ndi mtima woipa umene udabzalidwa mwa Fam pokhulupirira aphunzitsi akunja. Izi sizingatithandize, mmalo mwake mukuononga timu yathu. Mwatenga Tom koma wachoka atabalalitsa Flames. Joseph Kamwendo, Simplex Nthala adawathamangitsa ku timuyi. Sitikufuna tiyambe kuliriranso Kinnah Phiri chifukwa adachotsedwa akumanga timu.
16
Womuganizira kutaya khanda lake anjatidwa Anthu okhala mdera la Hilltop mmzinda wa Mzuzu adadzidzimuka Lamulungu lapitali, mayi wina wapabanja wochokera mderali atadziwika kuti adataya mwana mchimbudzi chokumba. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Malinga ndi anthu ozungulira nyumba ya Taona Chonga, wochokera mmudzi mwa Mzukuchonga, mboma la Mzimba, anthuwo adadabwa chimodzi mwa zimbudzi za pamalowa chikutulutsa fungo lodabwitsa. Malo ake ndi awa: Mmodzi mwa anthu okhala ku Hilltop kusonyeza dzenje la chimbudzi chomwe mudatayidwa khandalo Fungoli linatidabwitsa ndipo pokumbukira kuti Chonga adali ndi pathupi pomwe panasowa, tinadziwitsa a mfumu kuti afufuze, adatero mmodzi mwa anthuwo. Iwo adati mphekesera zili ponseponse kuti mayiyo adakangana ndi mwamuna wake yemwe amachita bizinesi ya kabaza. Akuti mwamuna wake amati pathupipo si pake ndipo mkaziyo azipita kwa mwini pathupipo, iwo adatero. Mkazi wa mfumu Chikundura ya deralo adati amayi anayamba kumudabwa mnzawoyo ataona kuti pathupi pomwe adali napo pasowa koma alibe khanda. Titamuona kuti alibe pathupi tili kumadzi, tidadabwa ndi kumufunsa komwe wasiya khanda lake, koma iye adakanitsitsa kuti adalibe pathupi, kunali kunenepa chabe, adatero mayi Chikundura. Iye adati apo ndi pomwe adadziwitsa akuluakulu kuti mnzawoyo wataya khanda. Ndipo nawo apolisi a mumzindawu atsimikiza kuti akusunga mchitolokosi Chonga, wa zaka 28, pomuganizira kuti adataya mwana mchimbudzi. Malinga ndi mneneri wa polisi ya Mzuzu, Martin Bwanali, Chonga, yemwe ali ndi ana asanu ndi mmodzi, komanso wina wakubere wa chaka ndi miyezi 7, adauza apolisi kuti adagwetsera chinthu mchimbudzimo atapita kokadzithandiza. Bwanali adati Chonga aonekera kubwalo la milandu masiku akubwerawa kukayankha mlandu wobisa pathupi. Iye adati mayiyo adamutengera kuchipatala cha Mzuzu Central kuti akamuyeze ngatidi adali ndi pathupi koma zotsatira zidali zisadadziwike pomwe tinkasindikiza nkhaniyi.
7
Ife toto takana! Mkozemkoze adanyula maliro aeni. Sinodi ya Livingstonia yatemetsa nkhwangwa pamwala kuti sipepesa monga momwe mafumu ena mboma la Rumphi alamulira. Pempho la mafumuwo likudza potsatira chipwirikiti chomwe chidachitika Lachiwiri msabatayi poyika mmanda thupi la malemu Chikulamayembe mbomalo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Nyondo akulankhula uku mafumu akukambirana zochita Sinodiyo idakolana ndi mafumu pa maliro a Chikulamayembe pamene idalamula kuti atsogoleri ena monga wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima ndi mtsogoleri wa zipani zotsutsa, Lazarus Chakwera alankhulepo pa malirowo. Ukali wa mafumuwo udaoneka pamene adakalanda mkuzamawu kuti mlembi wa sinodiyo Levi Nyondo asalankhulenso. Nyondo sadanjenjemere koma kuwauza mafumuwo kuti ayendetse mwambo wa mapemphero zomwe zidakakamiza mafumuwo kupepesa kuti mwambowo uchitike. Izi ndizomwe zakwiyitsa mafumuwo motsogozedwa ndi mwana wa Chikulamayembe, Mtima Gondwe yemwe wati sinodiyo idanyazitsa maliro a bambo ake. Nchifukwa chake tikupempha kuti sinodi ipepese pa zomwe zidachitikazo. Dziwani kuti adamwalirawo adali bambo anga, ndiye ine komanso akubanja tidakhumudwa nazo, adatero Gondwe. Naye gulupu Kawazamawe yemwe amalankhuliranso banja loferedwa adati mafumuwo ali ndi mfundo zitatu. Kusalemekeza maliro a mfumu. Kuyambitsa chipwirikiti pamaso pa mtsogoleri wa dziko lino komanso kunena kuti Chilima ndi Chakwera alankhule zomwe zikadayambitsa ndewu, adatero Kawazamawe. Koma izi sizikutekesa sinodiyo pamene yati ilibe nthawi yopepesa munthu pa zomwe zidachitikazo. Mmodzi mwa akuluakulu a mpingowo, mbusa Douglas Chipofya adati boma ndi mafumu ndiwo akuyenera kupepesa mpingo. Komanso paja mafumu adapepesa kale kusiwa kuja choncho nkhanizi zidatha basi, adatero Chipofya. Mawu a Chipofya adagwirizana ndi mawu a Nyondo amene adatsindika kuti mafumuwo ndi amene akuyenera kupepesa kumpingo. Kodi chichitike nchiyani pamene mpingowo wakana kupepesa? Gondwe adati aona chomwe achite koma sadanene chomwe angachite. Koma T/A Mwamlowe amene ali pansi pa Chikulamayembe adati pa mwambo wa Atumbuka, mfumu ikalankhula, palibenso amene amalankhula pamwamba pake. Naye T/A Mwamlowe adati kukadakhala kwabwino mbali zonse zikadadya khonde momwe ndondomeko ya mwambowo ikhalire. Bungwe lachikhalidwe la Mzimba Heritage Association (Mziha) lidati zikuoneka kuti anthu ena sadapitire kukalira Chikulamayembe. Mmodzi mwa atsogoleri a Mziha, Ndabazake Thole adati mwambo wakumudzi ulemu umaperekedwa kwa mafumu, ndipo ampingo amabwera nkumatonthoza anamfedwa. Naye DC wa boma la Rumphi Fred Movete adati nthawi zonse mfumu ya ndodo ikamwalira, ofesi yake imapanga ndondomeko yakayendetsedwe ka mwambo mogwirizana ndi a banja komanso unduna wa zamaboma angono.
1
Wa zaka 18 akaseweza zaka 18 Bwalo lamilandu mumzinda wa Mzuzu lagamula Mulolo Nkhata wa zaka 18 kukakhala kundende zaka 18 atamupeza wolakwa pamlandu wogonana ndi mwana wa zaka 6. Zidamveka mbwalolo kuti mnyamatayo ankagwira maganyu kunyumba kwa makolo a mwana ochitidwa chipongweyo ndipo kaamba ka kubwerabwera kwake pakhomopo adayamba kudziwana ndi yo. Nkhata ndi wochokera mmudzi mwa Chikwina T/A Nyalubanga mboma la Nkhata Bay. Mneneri wa polisi mumzinda wa Mzuzu Patrick Saulosi adati Nkhata adavomera kulakwa kwake pamlanduwo. Iye adati woimira boma pamlanduwu, sub-inspector Lyson Kachikondo, adapempha bwalo lamilandu kuti chigamulo chikhale chokhwima kaamba kakuti mlanduwu ndiwaukulu komanso zomwe wamudutsitsa mwanayo ndi chinthu chomwe sangadzaiwale moyo wake onse. Ogamula mlanduwu, Tedious Masoamphambe adavomereza zomwe adanena Kachikondo ndipo adati chigamulo chachikulu chithandiza kuchepetsa kuchuluka kwa milandu ya ntunduwu, adatero Saulosi. Izi zili choncho bambo wa zaka 47, Wilson Nyirenda, wa mboma la Nkhata Bay wagamulidwa kukhala ku ndende zaka 14 atagonana ndi mwana wa zaka 12. Mneneri wa polisi wa mboma la Nkhata Bay Ignatius Esau adati mwezi wa August, Nyirenda yemwe ndi wochokera mmudzi mwa Chikalanda T/A Chikulamayembe ku Rumphi adamuitanira mwanayo mu nyumba mwake momwe adamugwiririra. Mwanayo adatuluka mnyumbamo akulira zomwe zidachititsa anthu kuti amufunse zomwe zamuchitikira ndipo mwanayo adaulula, adatero Esau. Iye adati Nyirenda adakana mulanduwo koma adapezeka wolakwa anthu anayi atachitira umboni za nkhaniyi. Iye adati anthu ankamunamizira chifukwa amachita naye nsanje poti siochokera mmudzimo. Adauzanso bwalolo kuti adali ndi matenda a chinzonono ndipo adauza makolo a mwanayo kuti apite naye kuchipatala. Adapitiriza kuti adakhala nthawi yaitali asadagonane ndi mkazi ndipo ngati adagwiririradi mwanayo ndiye kuti adampatsa mimba, adatero Esau. Iye adati ogamula mlanduwu, Billy Ngosi, adati milandu yogwiririra ikukula ndipo olakwa akuyenera kupatsidwa chigamulo chonkhwima kuti chikhale chiletso kwa ena.
7
Amayi Ali Ndikuthekera Kothana Ndi Kusintha Kwa Nyengo-CADECOM Bungwe loona za chitukuko mu mpingo wakatolika la CADECOM mu dayosizi ya MANGOCHI lati amayi ali ndi udindo pa ntchito yothana ndi vuto la kusitha kwa nyengo komanso kuonongeka kwa nthaka. Mlangizi wamkulu wa bungweli a PETER NTHENDA ndi yemwe wanena izi polankhula ndi mtolankhani wathu yemwe amafuna kudziwa momwe kusintha kwa nyengo kumakhudzira amayi mu dayosiziyo. A NTHENDA ati amayi ndi ndi amene amatenga gawo lalikulu mu ntchito zosiyanasiyana mdziko monga , ulimi , komanso ntchito zapakhomo , choncho ali ndi kuthekera kothana ndi vuto lakusintha kwa nyengo , komanso kubwezeretsa nthaka pochita ulimi wa kasakaniza. Tikanena zakusintha kwa nyengo ku malawi kuno zinthu zimene zimayambitsa ndi ulimi komanso zankhalango, tiona kuti amayi ndiwo amatenga gawo lalikulu pa ulimi kuno ku malawi chachiwiri nchoti amayi ndiwo amatanganidwa kukonza chokudya pakhomo zomwe zimafuna khuni zambiri ndiye tikuwapempha azimayi kuti azigwiritsa mbaula zosalirana nkhuni zambiri komanso tikuwapempha azimayi kuti azigwiritsa ma basiketi a sungu kapena amulaza osati ma pulasiti komanso kubvala mitengo pofuna kubwezeretsa thaka anatero a Nthenda. Polankhulapo mayi VIOLET KANDULU kuchokera ku Arch dayosizi ya BLANTRYE ati amayi kuti sakuyenera kutaya zinthu zomwe zimaononga nthaka mwachisawawa ndi cholinga chakuti ayiteteze. Atiphunzintsa manphunziro akulu monga azimayi timataya zinyalala mmakwalala mwathu moma kutaya ma pampa komanso ma pulasitic zomwe zikupangitsa kuti nthaka yathu iwonongeke. Choncho tikhale oyamba kuchotsa zinyalala zomwe zimaonnga chilengedwe pakutero anthu azaphunzirira kwa ife anatero mayi Kalundu.
18
Kabwira Alimbikitsa Sukulu za Mkomba Phala Wolemba: Glory Kondowe nt/uploads/2019/10/Kabwira.jpg" alt="" width="201" height="250" />Kabwira: Tiona momwe zithere Dr. Jessie Kabwira ati kulimbikitsa ntchito za sukulu za mkomba phala komanso kuika chidwi pa ndondomekoyi kungathandize kutukula maphunziro mdziko muno. Dr. Kabwira omwe anali phungu wa kunyumba ya malamulo mdera la kumpoto chakuzambwe kwa boma la Salima ati ngakhale sanachite bwino pa zisankho zomwe zinachitika mdziko muno mmwezi wa May chaka chino, ngati mzika yokonda dziko lake, akuyenera kuthandizirapo kuti zinthu zina zidziyenda bwino. Iwo ati dziko kuti litukuke pakuyenera kukhala ndondomeko zabwino kuti anthu adzikhala ndi chakudya komanso madzi a ukhondo. Zili kwa iwowo anthu kusiyanitsa ntchito zomwe ndagwira kwa zaka 5 ndi wina amene amusankhayo. Anthu a mboma la Salima kumpoto chakumadzuro ndi mboni yanga ikakhala nkhani ya madzi, malo komanso chakudya pakadali pano akudziwa Mulungu. Tiona kuti zitha bwanji, anatero Dr. Kabwila. Iwo ati zomwe zimawakhuza kwambiri ndi khani ya njala ndipo apemphanso kuti chitukuko cha sukulu, madzi ndi chakudya chipite patsogolo mderalo.
3
Ku Nkhoma sakugona ndi mthirira Amati mmera mpoyamba. Ukalephera kukonzekera koyambirira ntchito yonse imayenda mwapendapenda mpaka zipatso zake zimakhala zokhumudwitsa. Ino ndi nyengo ya dzinja ndipo ulimi wagundika ndi wamvula, koma alimi ochangamuka pano ayamba kale kukonzekera za mthirira wachilimwe chomwe chikubwera kutsogoloku. Ena mwa alimi omwe akuonetsa chitsanzo chabwino pakukonzekera mthirira wamtsogolo ndi a ku Nkhoma mboma la Lilongwe. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi wapampando wa gulu la alimiwa, Lingilirani Chikhwaya pazomwe akuchita, motere: Chikhwaya: Sitivutika kumbali ya chakudya Ndikudziweni wawa Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Lingilirani Chikhwaya ndipo ndine wapampando wa alimi a mthirira omwe amathandizidwa ndi bungwe la Vision Fund Malawi kudzera mthumba la ngongole za ulimi la Mthirira Loans. Mulipo alimi angati? Tonse tilipo alimi 222 omwe timathandizidwa ndi Vision Fund Malawi koma aliyense ali ndi munda wakewake momwe amalima mbewu yomwe iye akuona kuti imuchitira bwino ndipo apindula nayo. Ndi mbewu zanji zomwe zimalimidwa kwambiri? Ambiri amalima chimanga, nyemba, tomato, anyezi ndi ndiwo zamasamba zosiyanasiyana. Ambiri mwa ife timakonda kasakaniza monga kubzala chimanga limodzi ndi nyemba kapena kugawa kuti mbali ina tomato, ina anyezi ndipo ina masamba monga chomoliya, mpiru kapena kabichi. Ulimi umenewu ukukupindulirani bwanji? Ulimiwu tikupindula nawo kwambiri chifukwa usadabwere, ambirife tinkavutika kwambiri kupeza zipangizo zaulimi dzinja likafika kusowa pogwira, koma pano zinthu zidasintha. Tikamachita mthirira wathu timakhala tikusunga pangonopangono ndalama mwinanso nkumaguliratu zipangizo zaulimi nkumasunga. Tikatero, dzinja ngati lino likafika timakhala tilibe nkhawa. Kupatula apo, sitivutika kumbali ya chakudya chifukwa timati tikamadya zamvula, zamthirira zikucha kuti zamvulazo zikamadzatha, tidzayambe kudya zamthirira. Mukuoneka kuti muli kalikiriki mmunda wa mthirira pomwe lino ndi dzinja simukupotoza pamenepa? Ayi ndithu, umu ndimo timachitira. Kuteroku tayambiratu kukonzekera mthirira wachilimwe chikubwerachi. Pali zambiri zomwe timayenera kupangiratu monga kusunga madzi okwanira, kuteteza maiwe anthu kuti asadzadze komanso kutchingira mmalo momwe mumathamanga madzi kuti asaononge nthaka. Kungolekerera nthaka imakokoloka ndiye poti munthu udzayambe kulima ulimi wamthirira zofuna zimachuluka monga kusonkhanitsa manyowa obwezeretsera nthaka yomwe idakokolokayo. Panopa yakula ndi ntchito iti? Monga ndanena kale, pakalipano ntchito yaikulu ndi yosunga madzi. Ulimi wathu wamthirira timadalira msinje ndiye chaka ndi chaka ngati panopa timatchingira kuti madzi asathawe. Timapanganso mizere ikuluikulu yotchinga madzi kuti azilowa pansi kuti mvula ikadzatha, pansi padzakhale chinyezi kwathawi yaitali tisadayambe kuthirira. Tafotokozankoni nkhani ya misika, mumagulitsa kuti zokolola zanu? Ambiri mwa ife timadalira kugulitsa kumisika ndi kupikulitsa kwa anthu omwe amakagulitsa kumsika. Si misika yodalirika, ayi, komabe timapezamo kangachepe. Pakalipano omwe amatithandiza ndi ndalama za ngongole a Vision Fund Malawi akutithandiza kuyangana misika yodalirika moti posachedwapa tikhala tikusimba lokoma. Mudalingalirako zopanga magulu ogulitsira katundu wanu pamodzi? Maganizo amenewo ndiwo tikupanga tsopano nchifukwa chake tili kalikiriki kusakasaka misika yokhazikika komanso paja ndati pakalipano mlimi aliyense ali ndi ufulu wolima mbewu yakukhosi kwake ndiye tikufuna kuti tikapeza msika wokhazikika, tizidziwa mbewu zoyenera kulima. Nanga si msika wapezeka kale? Kaya tsogolo la ulimi wanu mukuliona bwanji? Tsogolo ndi lowala kwabasi chifukwa momwe tidayambira ndi pomwe tili pano zikusiyana kwambiri. Mbewu zomwe tinkakolola kale ndi zomwe timakolola pano zimasiyana kwambiri chifukwa pano tidapatsidwa upangiri wapamwamba ndi alangizi odziwa ntchito yawo. Chiyembekezo chathu nchakuti mzaka zikudzazi tizidzalima ndi kukolola mbeu zoti mwinanso nkumadyetsa chiwerengero cha anthu ochuluka chifukwa, mwachitsanzo, chaka chino tathandiza anthu ambiri ndi chimanga chomwe tidalima kusikimu ndipo nafenso tapeza phindu lochuluka kwambiri. Malangizo anu ndi otani kwa alimi anzanu? Malangizo anga ndi oti alimi asamakonde kukhala pansi ayi. Ntchito yathuyi imasiyana kwambiri ndi ntchito zina chifukwa ife ndiye timadyetsa mtundu wonse. Tizionetsetsa kuti mvula ikamapita kumapeto, ntchito ya kusikimu yayamba ndipo chilimwe chikamapita kumapeto, tizionetsetsa kuti tayambiratu kukonzekera ulimi wa mthirira wotsatirawo ngati momwe tikuchitira ifemu. Izi tikuchita apazi ndi chiyambi chabwino chifukwa sitidzakhala ndi ntchito yambiri mthirira ukamadzayamba.
4
Ofesi ya Zaumoyo ku Blantyre Yati Ilimbikitsa Chitetezo cha Antchito Ake Ofesi yowona zaumoyo mu mzinda wa Blantyre yati ndi yokonzeka kulimbana ndi kachilombo ka Coronavirus popereka zipangizo zokwanira, zozitetezera ku matendawa kwa omwe akugwira nchito zachipatala mu mzindamo. Kawalazira: Tiyenera kuteteza miyoyo ya ogwira ntchito zachipatala Malingana ndi Mkulu wa zaumoyo mu mzinda-wu, Dr. Gift Kawalazira, ofesiyi yakhazikitsa njira zabwino pofuna kuteteza anthu ogwira ntchito zachipatala omwe akuthandiza anthu omwe akhuzidwa ndi nthenda ya COVID-19. Iwo ati chipatala cha Queen Elizabeth ndi komwe anthu azachipatala azithandizidwa ngati akhudzidwa ndi nthendayi pomwe anthu ena onse azikasamalidwa ku chipatala cha Kameza mu mzinda omwewo wa Blantyre. Choyamba tiyenera kuteteza miyoyo ya ogwira ntchito zachipatala mu mzinda wa Blantyre kuti atumikire moyenera choncho chipatala cha Queen Elizabeth Central ndi chomwe chizithandiza anthuwa, ndipo anthu ena onse okhala mu mzindawu azithandizidwa kwa Kameza komwe kuli sukulu ya anamwino ya Kamuzu College of Nursing, anatero a Kawalazira. Pamenepa Dr. Kawalazira anati chiwerengero cha odwala matendawa chikamachuluka akafikira msukulu zosiyana siyana ndi cholinga chopeza malo okwanira osamalira odwalawa.
6
Nkhanza zapolisi zanyanya Ophunzira 24 a kusukulu za ukachenjede apereka maina awo ku bungwe la maloya la Malawi Law Society (MLS) za nkhanza zimene achitiridwa panthawi yomwe amachita zionetsero zokwiya ndi kukwera mtengo kwa fizi. Iwo adachita izi MLS itawapempha kuti apereke mainawo potsatira nkhanza zimene apolisi adachitira ophunzirawo amene akwiya kuti fizi zakwera kuchokera pa K275 000 kufika pa K400 000. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Apolisi kuponda mwana akufuna kutolera mabotolo ku Kamuzu Stadium Nkhanzazo zidafika pambalambanda kwambiri ena atajambula pa vidiyo wapolisi wina ataomba khofi wophunzira wa chaka cha chinayi Mayankho Kapito, yemwe ndi mwana wa mkulu wa bungwe loona zaufulu wa anthu ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito. Kapito wati asumira apolisiwo. Mtsogoleri wa ophunzira ku Chancellor College Ayuba James adatsimikiza kuti pofika Lachitatu chiwerengero cha ophunzira omwe adapereka maina awo adali atafika pa 24. Talandiradi mainawo koma tikudziwa kuti chiwerengero chayenera kukhala chokwera kwambiri chifukwa ambiri apitapita mmakwawo. Nkovuta kuti uthengawu uwafikire, adatero James. Chikalata cha MLS chidapempha ophunzira amene angakhale ndi umboni wa nkhanzazo kuti apereke maina awo. Ngakhale mneneri wa bungwelo Khumbo Soko adatsimikiza za ntchitoyo, adakana kuthirirapo ndemanga chifukwa ati akadali mkati mopeza mainawo. Nthawi ya zionetsero za ophunzirawo, apolisi akhala akumenya ophunzirawo ndipo amangapo angapo pa zipolowe zomwe zakhala zikuchitika msukulu zomwe zili pansi pa University of Malawi (Unima). Izi zili apo, mabungwe ena a zaufulu wa Amalawi ati nkhanza zankitsa kupolisi ndipo ati izi zikusemphana ndi zimene amalengeza kuti adasintha. Sabata yatha, dotolo wodziwika bwino Dr Frank Taulo adalemba pa Facebook kuti adapeza apolisi akumenya anthu amene adawapeza akungoyenda mu Limbe mumzinda wa Blantyre nthawi itangokwana 6 koloko madzulo. Nditawafunsa chifukwa chiyani amamenyera anthuwo, adandikuta. Nditawauza kuti ndine wakuti, sadalabadire ndipo adandionongeranso galimoto langa, adatero Taulo. Posakhalitsapa, mwini malo ena a chisangalalo ku Chigumula mumzindawu, Sharat Gondwe adatinso apolisi adamumenya atabwera kudzatseka malo akewo, Pitchers Club. Anthu ena amene tidacheza nawo ku Lilongwe nawo adasimba za nkhanza za apolisi. Gift Potani wa kumsika wa ku Area 24, Andrew Mwenye wa mumsika wa Tsoka komanso Alinafe Matthias wa ku Area 22 adanena kuti apolisi akumanga anthu kapena kuwakwapula kumene opanda chifukwa chenicheni. Nthawi zina amapeza anthu malo omwera masanasana nkuwaphaphalitsa, ena kutengedwa osapatsidwa mpata wofotokoza zomwe akuchita, adatero Potani. Si ana a sukulu kapena Amalawi wamba amene akudandaula za nkhanzazi. Nawo amayi oyendayenda ati amakumana ndi nkhanza za apolisi akagwidwa pantchito yawoyi. Mneneri wa bungwe loyimilira amaiwa, Zinenani Majawa, adati pakati pa apolisi pali Chichewa choti Dzipulumutse kutanthauza kuti wogwidwayo apereke kena kake kapena akakhala mzimai asinthitse thupi lake ndi ufulu. Apolisi akatigwira vakabu amati dzipulumutse wekha kutanthauza kuti akufuna ndalama ndipo ngati palibe amamumenya kapena kumugona mzimai popanda chitetezo chilichonse ndiye poti ndi wapolisi, kokanena kumasowa, adatero Majawa. Mkulu wa bungwe la zaufulu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) Timothy Mtambo adati apolisi akadaunika mofatsa magwiridwe awo antchito kuti pomwe akuteteza miyoyo ndi katundu, asamaphwanye ufulu wa ena. Mneneri wa apolisi mdziko muno Nicholas Gondwa adaikira kumbuyo apolisi ndipo adati akugwira ntchito yawo potsata malamulo. Mawuwo adadza pomwe apolisi adalengezanso kuti akufufuza za wapolisi wothyapa khofi mwana wasukulu. Tikafika poponya utsi okhetsa misozi ndiye kuti zionetsero zafika pa zipolowe pofuna kuteteza anthu amene sizikuwakhudza ndi katundu wawo. Komanso kumanga ena mwa anthuwo kumakhala kuziziritsa zipolowezo, adatero Gondwa.
7
Zili bwinoPAC Nduna yakale ya zaulimi George Chaponda yamangidwa patatha masiku 43 kuchokera pamene nthumwi kumsonkhano wa Public Affairs Committee (PAC) lidapatsa boma masiku 30 kuti limange ndi kuzenga mlandu ndunayo poyiganizira kuti idachita zachinyengo. Imodzi mwa mfundo zimene nthumwizo zidamanga pamsonkhano umene udachitika mumzinda wa Blantyre pa 7 ndi 8 June, idali yoti Chaponda amangidwe malinga ndi kafukukufuku amene makomiti a Nyumba ya Malamulo adachita ndi kupeza kuti ndunayo idachita za chinyengo pogula chimanga ku Zambia. Komiti ina imene adakhazikitsa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika idapezanso kuti Chaponda adachita ukapsala. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chaponda (Kumanja) ndi Tayub kufika kukhoti Lachinayi Bungwe la ACB Lachitatu lidamanga Chaponda limodzi ndi mkulu wa kampani ya Transglobe Rashid Tayub komanso wapampando wa bungwe loona za malonda a mbewu zosiyanasiyana la Grain Traders Association of Malawi, Grace Mijiga Mhango. Lachinayi, oyimira Chaponda adapempha bwalo la majisitileti kuti lichotse chikalata choti mkuluyo amangidwe koma bwalolo lidakana pempholo choncho adagonanso mchitokosi. Mhango adapatsidwa belo Lachitatu. Ndipo madzulo a tsiku lomwelo, bwalolo lidapereka belo kwa Chaponda ndi Tayub. Mneneri wa PAC Peter Mulomole adati akuyembekezera kuti ACB ipitiriza ntchito imene ayiyambayi mpaka kumapeto kuti chilungamo chidziwike. Uku ndiko kukhala. Aliyense aziyesedwa ndi mlingo umodzi chifukwa palibe yemwe ali pamwamba pa malamulo. Chiyembekezo chathu tsopano nchoti momwe zateremu, ACB ikoka nkhaniyi mpaka kumapeto, adatero Mulomole. Mkulu wa bungwe la Centre for the Development of People (Cedep), Gift Trapence, wati zomwe yachita ACB zaonetsa kuti bungweli layamba kugwira ntchito mosaopsezedwa. Uku ndiye timati kukula. Bungwe la ACB siliyenera kugwira ntchito mwamantha kuopa maina. Apa tikuyembekezera kuti zonse ziyenda bwino mpaka chilungamo chioneke, adatero Trapence. Mwezi wathawu, Chaponda adanena poyera kuti iye ndi wokonzeka kunjatidwa ngati Amalawi akuona kuti ndiwolakwa koma iye adabwereza kuti akudziwa kuti akufera kuthandiza Amalawi omwe akadafa ndi njala.
11
Anatchezera Wamboni, ine Msilamu Zikomo Anatchereza, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndinagwa mchikondi ndi mtsikana wa Mboni za Yehova mpaka ndinamuchimwitsa moti ndikunena pano kuli mwana wamphongo. Makolo ake atamufunsa ananditchula ineyo ndipo atandiitana ndi akwathu ndidavomera mlanduwo. Makolo a mtsikanayu adati ngati ndikufuna kuti zithe bwino ndilowe mpingo wawo kuti asakandisumire kukhoti komanso kuti ndizisamalira mwana wangayo. Ine sindikufuna kulowa mpingowo, koma mtsikanayu akuti akhoza kulola kulowa Chisilamu ngati makolo ake angalole. Kodi apapa ndiye nditani kuti mwanayu ndizimusamalira popanda kulowa mumpingo wawowo? Kodi nditani kuti mkaziyu ndimukwatire? BJ, Lilongwe BJ, Mwazingwadi, achimwene a BJ. Vuto lili apa ndi loti inuyo simufuna kulolera zofuna za makolo a mkazi munamuchimwitsayo koma mukufuna zanu ziyende basi! Sizikhala choncho mukafuna kulowa moyo wa banja. Kulolerana ndiye gwero la banja. Mkazi munamuchimwitsayo waonetsa kale chikondi chake kwa inu chifukwa akulolera kuti atha kukutsatirani ku Chisilamu bola makolo ake amulole, koma inu chikondi chanu nchoperewerako pangono chifukwa mukumenyetsa nkhwanga pamwala kuti simungayerekeze kulowa mpingo wa mkazi wanuyo. Mulungu ndi mmodzi, baba, mipingo ndiye njambirimbiri! Langizo langa apa ndi loti zonse zimatha nkukambirana. Ngati akuchikazi nawonso sakulolera zoti mwana wawoyo alowe Chisilamu, monga inuyo mmene mwakanira kuti simungalowe mpingo wa Mboni za Yehova, kwatsala njira imodzimuthabe kulowa mbanja, koma aliyense akhale ndi ufulu wokapemphera koma akufuna. Zikakaniza apo, ndiy kaya. Ndakhala ndikunena nthawi zambiri kuti banja si masewera; pamakhala zambiri zofuna kutsatidwa musanalowane, koma mukadya mfulumiza, mavuto ake amakhala ngati amenewa. Koma, baba, nzoona mungalephere kuthandiza mwana wanu kaamba ka kusiyana mipingo? Mwana adalakwa chiyani? Nzoona makolo a mkazi akukuletsani kuthandiza mwana wanu kaamba koti simunalowe mpingo wawo? Chonde, mwana yekhayo asavutike chifukwa cha nkhani yanu. Muzimuthandiza mjira iliyonse, makolo a mkazi ndikhulupirira sadzaona cholakwika mwana wanu akamalandira thandizo kuchokera kwa bambo ake omubereka. Amandikakamiza zogonana Agogo, Ndine mtsikana wa za 17 ndipo ndili ndi chibwenzi chomwe chimandikakamiza kuti tiyambe kugonana. Nditani? Mwana wanga, musiye ameneyo, sadzakuthandiza! Ndipo wachita bwino kundiuza msanga za nkhawa yako. Anzako ambiri amakopeka ndi zautsiru ngati zimene akukukakamiza bwenzi lakolo ndipo mapeto ake ndi kutengapo mimba kapena matenda opatsirana pogonana. Anyamata kapena abambo ambiri si okonzeka kuvomereza kuti ndiwo akupatsa pathupi kapena matenda ndiye chimakutsalira, tsogolo lako nkupiratu pamenepo. Fatsa, mwana wanga, sunga khosi ndipo mkanda woyera udzavala! Ukadzisunga udzaona kukoma moyo wako onse utapeza mwamuna weniweni amene adzakukonde ndi mtima wake wonse, osati kamberembere amene akuti muzigonana panopa muli pachibwenzi. Umuuziretu kuti iwe si chidole choseweretsa. Asaa! Ofuna mabanja Ndikufuna mkazi wa zaka 19-23 komanso woopa Mulungu0881 131 533 Ndine mkazi wa zaka 33 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Ndili ndi kachilombo ka HIV koma ndikumwa mankhwala. Ndikufuna mwamuna wa zaka 35-37. Wondifuna aimbe pa 0882 617 531 Ndine mwamuna wa zaka 35 ndipo ndi ana awiri. Ndikufuna wachikondi woti ndikwatire, akhale Mkhristu wa zaka 25-30 wokhala ku Lilongwe konkuno. Akhale wokonzeka kukayezetsa magazi. Wondifuna andiimbire pa 0882 511 934.
12
Amalawi apindulanji ndi kutsogolera Sadc Doko la Nsanje: Kodi liona kuwala tsopano? Akuluakulu pa zachuma komanso mafumu mdziko muno ati mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda afunika masomphenya kuti dziko lino lipindule pamene ali wapampando wa mgwirizano wa maiko a kumwera kwa Africa wa Southern Africa Development Community (Sadc). Banda wangosankhidwa sabata yathayi pamsonkhano wa Sadc omwe umachitikira ku Lilongwe komwe atsogoleri a maiko 14 adasonkhana. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Aka sikoyamba mtsogoleri wa dziko la Malawi kusenza udindo wotsogolera mabungwe a maiko angapo. Mtsogoleri wakale Bakili Muluzi adalinso mtsogoleri wa Sadc. Ndipo mnthawi yaulamuliro wake, Bingu wa Mutharika adali wapampando wa African Union (AU). Koma monga akunenera nduna yakale ya zachuma Friday Jumbe komanso kamuna pa zachuma ku bungwe la Malawi Equity Justice Network (MEJN) Dalitso Kubalasa, Banda akuyenera akhale ndi masomphenya ngati akufuna kuti dziko lino lipindule panthawiyi. Utsogoleri wa Banda ukudza pamene boma lake lili kalikiliki kukozanso chuma cha dziko lino kuti Amalawi ayambe kusimba lokoma. Panthawiyi ali ndi mphamvu yokwaniritsa zomwe amalakalaka zitachitika mdziko muno. Chitsanzo mtsogoleriyu wakhala akukamba za malonda a dziko lino ndi maiko ena zomwe zingatheke nthawiyi. Chikufunika ndi kukhala ndi masophenya chifukwa mphamvu zonse ndiye zili mmanja mwake komanso kuti Economic Recovery Plan itheke nthawi yake ndi imeneyi, adatero Kubalasa. Mfumu yayikulu Kwataine ya ku Ntcheu yati uwu ndi mwayi kuti nkhani za uchembere wabwino zipite patsogolo mdziko muno ndi maiko ena. Nkhani za uchembere wabwino komanso ulimi zikufunikira ukadaulo, kukaphunzira momwe anzathu amachitira mmaiko akunjawo. Pamene apulezidentiwa ali mtsogoleri wa Sadc tikukhulupirira kuti zinthu zimenezi tipita chitsogolo komanso nduna zawo zizikhudzidwa ndi nkhanizi, adatero Kwataine yemwe adayamikira mapulani a mtsogoleriyu. Naye Malemia wa ku Nsanje wati kumeneko adayandikana ndi dziko la Mozambique zomwe wati zithandiza maka kumbali ya ubale. Asodzi a ku Mozambique amabwera ku Malawi komanso ife timapita mzipatala za dziko lawo. Izi kuti zidzichitika zimafunika ubale wabwino pakati pa mayiko awiriwa.Tikukhulupirira kuti izi zilimbikitsa ubale wathu, adatero Malemia. Jumbe wati Banda ali ndi mwayi kuti wakhala mtsogoleri pamene dziko lino likukumana ndi mavuto achuma komanso mikangano ya nyanja ndi dziko la Tanzania zomwe wati zingatheke ngati atagwiritsa bwino nthawiyi. Mkangano wa nyanja ungakambidwe bwino pamene akutsogolera Sadc. Komanso amakamba za zokopa alendo zomwe zingathandize nkhani zachuma. Pakufunika kuti panthawiyi misonkhano ikuluikulu izichitika ku Malawi kuno kuti nkhani zokopa alendo zipite patsogolo, komanso pakufunika kuti akhazikitse mgwirizano wabwino wa dziko lino ndi maiko omwe ali mu Sadc kuti zamalonda zipite patsogolo monga iye mkhalapampando, adatero Jumbe. Poyangana mmbuyo pamene Muluzi adali wapampando wa Sadc, Jumbe wati panthawiyo dziko lino lidapindula pankhani ya ubale wa dziko lino ndi maiko ena. Ngati ubale wa maiko uli bwino, malonda amayenda bwino komanso anthu amalowa ndi kutuluka mdzikomo momasuka popanda chiopsezo, adatero Jumbe. Banda yemwe wachiwiri wake ndi mtsogoleri wa dziko la Zimbabwe Robert Mugabe watenga udindowu kuchokera kwa mtsogoleri wa dziko la Mozambique Armando Emilio Guebuza. Kusankhidwa kwa atsogoleriwa akuti kumachitika malinga ndi zomwe ofesi ya Sadc imagwirizana. Amawafunsa pambali ngati angakhale mtsogoleri wa Sadc, akavomera ndi pamene amadzasankhidwa kuti akhale mtsogoleri. Maiko osauka ambiri ndiwo amatengeka ndi utsogoleriwu koma maiko ochita bwino monga South Africa satengeka nazo. Mungaone kuti Muluzi adakhalapo, pano Joyce Banda wangolowa kumene koma lero tikukamba kuti ndi mtsogoleri wa Sadc, adatero Jumbe. Mdziko muno muli mapulojekiti omwe atatha angathandize Amalawi monga doko la Nsanje. Ntchito pa dokoli zidayima chifukwa chosagwirizana zingapo ndi dziko la Mozambique. Angoni alirira mafumu GEORGE SINGINI Angoni a ku Mzimba ati kumwalira kwa mfumu yawo yaikulu kwambiri Inkosi ya Makosi Mmbelwa ndi mfumu yaikulu Jalavikuwa chaka chino kudzetsa mavuto pankhani ya ulamiro pakati pa Angoni. Inkosi Mmbelwa adamwalira mu February pamene Jalavikuwa adamwalira sabata yathayi. Mafumuwa ndi omwe adali aakulu mu zaka ndipo kumwalira kwawo kwapangitsa kuti ulamuliro wa Chingoni ukhale mwa achinyamata. Inkosi Mabulabo yemwe ndi mfumu yachinyamata wati mtundu wachingoni wasokonekera mmaganizo ndi imfa za mafumu awiriwa omwe amwalira motsogozana. Mabulabo adati mafumu awiriwa adali ofunika paulamuliro wa Chingoni chifukwa adali okhwima nzeru ndi maganizo. Mfumuyo idati poti kwangotsala achinyamata zikhala zovuta paulamuliro wa chingoni. Pano sitikudziwa kuti atisogolere ndani. Tataya atsogoleri ofunikira kwambiri. Atsogoleri otha kuyanjanisa anthu, opemphera komaso odzichepesa, adatero Mabulabo. Mfumu ina ya Chingoni, Inkosi Mpherembe adati atha nzeru ndi imfa za mafumu awiriwa ndipo adati Jalavikuwa adali mgodi wa chikhalidwe cha Chingoni ndipo akanathandiza kwambiri kuyanjanitsa Angoni ndi mmene anamwalira a Mbelwa. Timalira kufa kwa Inkosi ya Makosi Mmbelwa yomwe inali mfumu yathu yaikulu. Ndi kumwalira kwawo timadalira a Inkosi Jalvikuwa kuti ndi omwe azitithandiza pa ulamuliro. Iwo anali ofunikira kwambiri popereka uphungu komanso kuyanjaniza anthu, adatero Mpherembe. Iye adati kuti zinthu zisasokenekere kwambiri akhala okakamizidwa kusaka anthu achikulire a chingoni kuti aziwathandiza mmaganizo. Koma anthuwa sangawafaninze ndi mmene akanachitira mafumu. Mlembi wa mkulu wa CCAP Synod of Livingstonia mbusa Levi Nyondo wati Angoni ali pamavuto aakulu ndipo monga mpingo awaika mmapemphero kuti zinthu zikhale mchimake. Bwanamkubwa wa Mzimba mbusa Moses Chimphepo wati kupita kwa mafumuwa kusokonezaso ntchito zaboma kamba koti anali olimbikira pachitukuko. Wachiwiri kwa nduna ya maboma angno ndi chitukuko cha mmidzi a Godfrey Kamanya agwirizana nazo kuti angoni ali pa mavuto aakulu chifukwa ataya odziwa chikhalidwe.
10
Akagwira Jere Zaka Zinayi Kaamba Kobaya Mlamu Wake Bwalo la Mangochi First Grade Magistrate lalamula bambo wina wa zaka 28 kuti akakhale ku ndende kwa zaka zinayi kaamba kobaya ndi kuvulaza mlamu wake. Bwaloli linamva kuchokera kwa woyimira boma pa mlandu, Sub Inspector Regina Makwinja kuti mkuluyu Joseph Kamanga anabaya mlamu wake Prisca pa nthawi yomwe amateteza mchemwali wake Mwandida pomwe amamenyedwa ndi mamuna wakeyu. Makwinja anati pa 11 March 2020, Joseph amamwa mowa pa malo ena pa msika pa Mpondasi mbomalo ndipo mkazi wake anafikanso pamalopo kudzapereka chakudya kwa mchemwali wake. Mkaziyu akuti anayamba kumwa mowa ndipo ataledzera anayamba kucheza ndi amuna ena omwe anali pamalopo zomwe zinakwiyitsa mamunayo ndi kuyamba kumumenya. Pamene Prisca adaganiza zolanditsa mchemwali wakeyo, ndi pamene Joseph adatenga galasi ndi kumubaya mlamu wakeyu pakhosi. Popereka chigamulo chake, First Grade Magistrate Roy Kakutu anati wapereka chilango cha mtunduwu kuti ena atengerepo phunziro. A Joseph Kamanga amachokera mmudzi mwa Mtalimanja mfumu yaikulu Mponda, mboma lomwelo la Mangochi.
7
Mswati adakali mfumuBoma Boma, kudzera mwa mneneri wa unduna wa maboma aangono ke Muhlabase Mughogho, lati ngakhale pali kukokanakokana pa ufumu wa Gomani V, boma likuvomerezabe Mswati Gomani wachisanu kuti ndiye mfumu. Mughogho adanena izi pamene mbali ina ya banja la Gomani motsogozedwa ndi Dingiswayo yalengeza kuti Dingiswayo ndiye mfumu, kulanda ufumuwu kwa Mswati. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Gomani V Lachiwiri akuluakulu ena abanja adatsutsa zomwe Dingiswayo adalengeza kuti Mswati adakalibe mfumu. Koma patangodutsa tsiku abanjawa atalankhula, Dingiswayo adachititsanso msonkhano wa atolankhani kuti zomwe adanena abanjawa ndizabodza ndipo iye ndiye mfumu yatsopano. Panopa ofesi ya Gomani yasamuka kuchoka ku Lizulu ndipo tikulankhulamu ili kwa Nkolimbo, adatero Dingiswayo. Koma malinga ndi Mughogho, Mswati ndiye mfumu. Boma likudziwa Mswati kuti ndiye mfumu, izi zili choncho chifukwa mfumu ikasankhidwa ndi abanja, boma limavomereza ndipo mwambo udachitika wodzoza Mswati kukhala Gomani wachisanu. Izi sizidasinthe mpaka lero. Gawo 11 (1) la malamulo okhudza mafumu, Chiefs Act la mchaka cha 2000 limati pulezidenti wa dziko ndiye ali ndi mphamvu yochotsa Paramount Chief, Senior Chief, Chief komanso Sub Chief. Mswati adadzozedwa mu pa August 10, 2012 kukhala Gomani wachisanu kutsatira imfa ya bambo ake.
11
Akudyerera obwela A malawi akhala akuingidwa ngati nkhuku mmaiko ena akafuna thandizo la chipatala, koma nzika zakunja kumadzawamwera mazira zikafika mdziko muno ponama kuti ndi nzika za dziko lino. Izitu zakhala zikuchitika chifukwa chosowa chiphaso cha unzika, koma lero mpumulo wafika kwa Amalawi pamene akhale ndi mwayi wokhala ndi chiphaso chosonyeza unzika wa dziko lino. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kuthithikana mzipatala zina kumadza chifukwa cha anthu a kunja Zili chonchi malinga ndi ntchito yomwe bungwe la National Registration Bureau (NRB) poyamba kalembera wa unzika amene adayamba ndi akuluakulu aboma komanso maboma 11. Monga akufotokozera Senior Chief Kanduku wa mboma la Mwanza, boma lake limalandira nzika zambiri kuchokera mdziko la Mozambique. Anthu pafupifupi atatu mwa 10 alionse amene amafuna thandizo lachipatala kuno amakhala a ku Mozambique. Vuto ndiloti kuyambira pa Zobue mpaka ku Tete mdziko la Mozambique palibe chipatala, posowa kolowera, anthu adera limeneli amathandizidwa mzipatala za dziko la Malawi, adatero Kanduku. Ngakhale tayandikana ndi dzikolo, satilola kupita mdziko lawo kukalandira thandizo la chipatala. Amalawi angapo akhala akuthamangitsidwa, ndipo suthandizidwa chifukwa anzathuwo ali ndi zitupa za unzika, adaonjeza motero. Naye Senior Chief Kabunduli ya mboma la Nkhata Bay, adati kumeneko nzika za maiko a Tanzania zimalowa pafupifupi tsiku lililonse ndi kumalandira thandizo lomwe Amalawi amayenera kulandira. Akafika kuno amakhala ndi maina a Chimalawi zomwe ndizovuta kuwakaikira kuti si nzika zathu. Mankhwala pachipatala amatha mwachangu ife ndi kumavutika pamene iwo kwawo ali ndi zipatala zomwe zingawathandize, adatero Kabunduli. Kungofika pa Chintheche pali anthu ambiri amaiko a Burundi, sangapitenso kwawo ndipo akulandira chithandizo chilichonse chomwe chimayenera chipite kwa Amalawi. Kwawo sungayerekeze kupanga zimenezi koma ifeyo amationa kupusa, adaonjeza Kabunduli. Kuti munthu ulandire thandizo lachipatala cha boma mmaiko monga Zambia, Zimbabwe, Mozambique ndi Tanzania, umayenera kuonetsa chitupa chosonyeza kuti ndiwe nzika koma kuno kwathu izi sizichitika chifukwa kulibe ziphasozi. Monga akufotokozera Norman Fulatira yemwe ndi mneneri wa NRB, iyi mwina nkukhala mbiri yakale chifukwa Mmalawi weniweni azidziwika ndi chiphaso chomwe adulitse. Mavuto amenewa akhala mbiri yakale posakhalitsapa pamene ntchito yodula ziphaso za unzika yayamba. Gawo loyamba tayamba kupanga ziphaso za aphungu a Nyumba ya Malamulo, akuluakulu mboma, komanso midzi 27 mmaboma 11, adatero Fulatila. Mabomawa ndi Chitipa, Mzimba, Nkhotakota, Lilongwe, Salima, Dowa, Mchinji, Blantyre, Mangochi, Chikwawa ndi Thyolo. Zitupazo azidula mmidzi iwiri pa boma lililonse. Ili ndi gawo loyamba, gawoli likufuna lingotithandiza momwe ntchito ikhalire, ili ngati ntchito yoyeserera kaye koma anthu alandira ziphaso zawo. Mudzi ulionse takonza zoyamba ndi anthu 200 ndipo gawoli likamatha, anthu 5 000 akhala ndi ziphaso zawo, adatero mneneriyu. Iye adati gawo lachiwiri la ntchitoyi, anthu 95 000 ndiwo adzakhale ndi mwayi wokhala ndi ziphasozi ndipo gawoli likuyembekezereka kudzatha mu December chaka chino. Chaka chamawa, bungweli likuyembekezera kuti ntchitoyi idzafalikira dziko lonse pomwe anthu 9 miliyoni akuyembekezeka kulandira zitupa zawo. Fulatira adati aliyense amene wakwanitsa zaka 15 ndiye akuyenera kudulitsa ziphasozi. Iye watinso ngati uli nzika ya dziko lino, uyenera kudulitsa ziphasozi posatengera zikhulupiriro zako kapena mpingo. Naye mkulu wa bungwe loona zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe wati ntchitoyi ipindulira Amalawi komanso boma. Apapa ndiye kuti thandizo la mabungwe ndi boma lizipitadi mmanja mwa Amalawi enieni kusiyana ndi poyamba pamene timaphangirana ndi obwera, adatero. Kwa amene ataye chiphasochi akuti ayenera kudzalipira K3 500 kuti amupangirenso chiphaso china. Koma malinga ndi Fulatira, mtengowu ukhala ukusinthasintha.
2
Ophunzira Akatolika pa CHANCO Akhazikitsa Mlozo Wolemba: Thokozani Chapola tent/uploads/2019/11/bishop-tambala.jpg" alt="" width="306" height="357" />Wayamikira ophunzira a katolika pa Chancellor College-Bishop Tambala Episikopi wa mpingo wa katolika mu diocese ya Zomba Ambuye George Desmond Tambala wayamikira ophunzira a mpingo wa katolika kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor kamba kokhadzikitsa mulozo (Stratrategic Plan) woti uwathandize kupititsa patsogolo ntchito zotukula mpingowu ndi chikhristu chawo ku sukuluyi. Ambuye Tambala amayankhula izi pa mwambo wokhazikitsa mulozowu ku sukulu-yi. Iwo alimbikitsa mgwilizano wabwino pakati pa ophunzira-wa ponena kuti kuchita izi ndi komwe kungathandizire ophunzira-wa kuti athe kukwanilitsa mapulani a ntchito zawo potsatira mulozo-wu. Poyankhulapo yemwe adali mlendo wolemekezeka pa mwambo-wu Dr. Mary Shawa analimbikitsa ophunzira-wa pa za moyo wawo wa uzimu. Mmau ake mmodzi atsogoleri a aophunzira achikatolikawa Gift Muyayi wati ngati ophunzira ayesetsa kukwanilitsa mapulani a ntchito zosiyanasiyana omwe ali mu Strategic Plan imeneyi. Pa sukulu ya Chancellor College pali ophunzira pafupi fupi 2000 omwe ndi ampingo wa katolika.
3
Kuchitsedwa ntchito ndi zina Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mourinhao ndi mmodzi mwa anzanga amene ndimacheza nawo pa Wenela. Sindikudziwa kuti nchifukwa chiyani mkuluyu amakonda Arsenal. Momwe amaonekera, nzeru zake, ndimadabwa kuti iyeyu ndi Arsene Wenger adadyetsana mankhwala a mtundu wanji. Nchifukwa chake nthawi zambiri tikamukumbutsa kuti patha zaka 10 timu yakeyo isanachite zakupsa potenga chikho amakwiya zedi! Koma iyo ndi nkhani ya tsiku lina. Tsono Mourinhao adatopa ndi kuitanira minibasi, ndipo adapempha mwini minibasi ina kuti amupezere ntchito. Mwini minibasiyo adali dotolo. Pambali pothandiza odwala ku Gulupu, dotoloyo amakaphunzitsanso kusukulu ina ya anamwino. Apa zili bwino Tade. Kukhosi kwanga kuchita kusalala. Bakhalani ndi kuitanira kwanuko mpaka day yobwera Yesu. Uku kukumakhala kudya za tswayitswayi osati masewera, adandiuza tsiku lina atatizungulira pa Wenela. Koma ngati adathako sabata zitatu? Ndidangoona akubwera tsiku lina atazyolika. Bwanjinso nanga? ndidamufunsa. Ndailephera ntchito. Andichotsa, adayankha mwa chidula. Apa mpomwe adafotokoza momwe ntchitoyo idathera. Ndimagwiranso ntchito yokonza mnyumba mwa dotoloyo: kukolopa, kusesa, kukonza mufiliji ndi zina zotero. Tsiku lina, ndidapeza kuti liver ina idakhalitsa mfilijimo. Ndidaaitenga kukaotcha kunyumba. Atabwera mkulu uja adandifunsa: Ndinasiya katundu umu, watenga ndani? Ndipo ndidati sindikudziwa, adafotokoza mkulu uja. Adamezera malovu, nkupitiriza: Nthawi ya nkhomaliro adandifun-sanso, ndidakananso. Ngakhalenso madzulo adandifunsa ngati ndidaona katundu wake, ndidakananso. Pobwera madzulo tsiku linalo, adabwera ndi mowa umene adandigaila. Akuti mkuluyo ataona kuti Mourinhao wayamba kuledzera adamufunsanso: Ndinasiya katundu wanga. Watenga ndani? Ndipo Mourinhao adayankha: Mukunena nyama ija? Ndaotchera, pepani. Mkulu uja adangoti: Chinalitu chiwindi cha munthu ndimati ndikaphu-nzitsire. Abale anzanga, tikakhala pantchito sib wino kusolola ngakhale zimene tikuziona kuti nzazingono. Tikadakhala kuti tonse tilibe mtima osolola, nkhani ngati zotengera abale ndi alongo kunja moononga ndalama, kubwereka ndege yaufiti ngati kabanza si bwenzi zikutisautsa. Hallo Tade, wasowatu. Ndalanga wina uku, adatero Abiti Patuma, msungwana wosowa ngati Adona Hilida pano pa Wenela. Zinakhalanso bwanji? adafunsa Gervazzio, mmalo moika nyimbo ya Nakulenga. Amakula mtima, ati mkazi wake amamukhulupirira koopsa ndipo iyeyo kanali koyamba kuti apusitse mkazi wakeyo pocheza ndi ine. Poti anali ataledzera modziiwala, ndinatenga mapepala onse amagwiritsa ntchito nkuwaika mthumba la buluku, adatero Abiti Patuma. Adaonjeza kuti mawa lake, adangomva kuti ukwati wamkuluyo watha.
7
Boma Lapereka 35 Milion ku Khonsolo ya Dedza Khonsolo ya boma la Dedza yalandira ndalama zokwana 35 Million Kwacha kuchokera ku boma la Malawi zothandizira kuchepetsa kufala kwa matenda a COVID-19. Bulukutu: Atolankhani atithandize pofalitsa uthenga Bwanamkubwa wa bomali a Emanuel Bulukutu alankhula izi pamene khonsoloyi imaunikira atolankhani za mmene angalembere nkhani zokhudza matendawa. A Bulukutu ati ngakhale kuti khonsoloyi yayika ndondomeko zoyenera zodziwitsira anthu kapewedwe kamatenda-wa anawona kuti nkofunikira kuti atolankhani akhale patsogolo chifukwa wailesi zimafikira anthu ambiri mdziko muno. Tikufuna atolankhani akhale patsogolo potithandiza kufalitsa uthenga umenewu chifukwa wailesi zimafikira anthu ambiri mdziko muno, anatero a Bulukutu. Iwo ati mabungwe enanso monga World Vison, GIZ, United Purpose ndi ena athandizanso bomali ndi ndalama komanso katundu wosiyanasiyana.
2
Katswiri Wayamikira Nduna Zatsopano, Nduna Imodzi Yakana Udindo Katswiri pa nkhani za ndale mdziko muno Dr. Boniface Dulani wati ali ndi chikhulupiliro kuti nduna zomwe zasankhidwa ndi President wa dziko lino Dr. Lazarus Chakwera, zigwira ntchito zawo bwino popeza kuti zili ndi zowayenereza kugwira ntchitoyi. Dulani: Ndikukhulupilira kuti agwira bwino Dr. Dulani yemwenso ndi mphunzitsi wa zandale ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor, wauza Radio Maria kuti anthu ayike chikhulupiliro mwa ndunadzi pofuna kuti zigwire ntchito yawo bwino. Iwo ati mwachitsanzo, wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulosi Chilima, mu ulamuliro wa Professor Peter Mutharika mchaka cha 2014, adagwiraponso unduna ngati omwewu ndipo adagwira ntchito yawo mwaukadaulo. Tidikirebe kuti tiwone kuti akagwira ntchito yotani komano a Vice President tikuziwa tonse kuti anagwirapo ntchito mu undunawu ndipo anayigwira bwino ntchito, komanso mukuwuona kwanga boma lasankha ndunazi kuti chitetezo cha mkati mwadziko bwino chikhale choyenerera, anatero a Dulani. Msiska: Ziwoneka ngati akundipatsa mphatso Padakalipano yemwe anasankhidwa kukhala nduna yowona za chilungamo ndi malamulo a Modecai Msiska awukana udindowu ponena ena aganiza ngati a Chakwera akuwalipira pa ntchito yomwe anathandizira chipani cha MCP kuti chipambane pa mlandu wa chisankho cha president. Iwo anapitirizanso kunena kuti pali achinayamata ambiri omwe angati kugwira ntchito pa udindowu osati iwo omwe ndi achikulire.
11
Mugwiliranji bere la mwini? Masiku apitawa mtsikana wina adandifotokozera za momwe mphongo ina idagwirira bere lake pa msewu mumzinda wa Lilongwe. Mtsikanayu adali akungodziyendera mutauniyo pomwe adangodzidzimuka mkono wa bambo yemwe amabwera kutsogolo kwake uli pabere lake. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mmene amati azilankhula, bamboyo nkuti atayamba kuyenda kupitiriza ulendo wake ngati sadachite kalikonse. Mtsikanayo adangoti kakasi, kenaka adangopitiriza ulendo wake ali cheucheu kuti bambo wina asamuonererenso. Nkhaniyi idandikumbutsa zomwe zidandionekera mutauni ya Limbe, ku Blantyre, zaka zinayi kapena zisanu zapitazo. Anthu adali pilingupilingu mmawa wa Loweruka limenelo ndipo ndidali pandawala kukwakwera basi pomwe ndidangozindikira mkono wa mnyamata wina, yemwe ndidali ndisadamuoneko chibadwire, uli pabere langa. Ndikudzidzimuka, mnyamatayo, yemwe timayenda mosemphana, adapitirira ulendo wake akumwetulira ngati sadachite chilichonse chodabwitsa. Ndidangoti kakasi, kusowa cholankhula mnyamatayo akulowelera mgulu la anthu omwe anali akuyenda pamalopo. Amayi ndi atsikana omwe zangati izi zidawaonekerapo angachitire umboni za mkwiyo ndi manyazi omwe amadza zoterezi zikakuchitikira, poti ena zawachitikira mmaofesi, kusukulu ndi malo ena. Kwa nthawi yaitali ndidakhala ndikudzifunsa za mmene ndikadakhaulitsira ndoda yachipongweyo. Ndikadakuwa? Koma ndi changu chimene mnyamatayu adachita, ndimakaika ngati ena omwe amadutsa pamalopo adaona zomwe zidachitika. Akadandikhulipilira ndani? Umboni sukadavuta kodi? Kapena ndikadamumenya? Koma mwachidziwikire akadabwenzera ndipo mwinanso nkadavulazidwa ndine ndemwe. Ena nkumati atsikana mukumadziitanira mavuto nokha kaamba kamavalidwe kosadzilemekeza, koma ichi sichifukwa chokwanira mpangono pomwe choti anthu ena azichita zomwe afuna ndi matupi a amayi. Kaya wina atavala zoonetsa mawere ake, palibe choyenereza bambo kapena mnyamata kugwira mawerewo. Tisaiwale kuti mdziko muno muli ufulu wa kavalidwe. Kwa amayi, ndikukhulupilira kuti kungopenya ngati momwe ndidachitira ine ndi msungwana wa ku Lilongweyu, sikungathandize kwenikweni. Ngati pali chomwe mungathe kuchita kuti abambo oterewa aonekere poyera, chitani, kuti aone polekera.
15
Papa Wayamikira Akayidi a Ndende ya padua Mdziko la Italy Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wathokoza akayidi a pa ndende ya Padua mdziko la Italy. Papa pa umodzi mwa maulendo ake oyendera akayidi Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, iye anathokoza akayidiwa pokonza mapemphero a njira ya mtanda ya chaka chino zomwe wati zawonetsa ukulu wa Mulungu pakati pawo. Pamenepa Papa wati apitiriza kupemphelera akayidiwo kuti Mulungu adziwatetedza mu njira zosiyanasiyana pomwe ali ku ndendeko.
14
Dziko la Turkey Likuthamangitsa Obwera jpg" alt="" width="413" height="275" />Anthu obwera akuwafanizira ndi zigawenga izi Dziko la Turkey layamba kuthamangitsa mzika za mmaiko ena zomwe likuziganizira kuti zikukhudzidwa ndi gulu la zauchifwamba la Islamic State. Malipoti a wailesi ya BBC ati ngakhale maiko ena aku Ulaya sakufuna kulanda ziphaso za umzika kwa anthuwa, koma maiko monga Germany, Denmark komanso United Kingdom alanda kale ziphaso kwa anthuwa omwe analowa gulu la zauchifwamba la Jihadists. Padakali pano dziko la Turkey likusungira asilikali mazanamazana ochokera mmaiko ena mu ndende zake ndi cholinga chakuti afufuzidwe bwinobwino ngati sakukhudzidwa ndi gulu la zigawengali. Kumayambiliro a mwezi uno boma la dziko la Turkey linatsindika kuti libweza asilikaliwa mmaiko a kwao ngakhale kuti anandidwa ziphaso za unzika wao.
14
Osaiwala kuteteza mtedza ku chuku Pamene mbewu ya mtedza yacha, katswiri wa mbewu za mtunduwu kwa Bvumbwe Richard Andasiki akuti alimi ateteze mbewuyi ku chuku pamene akukolola, kuyanika, kusenda komanso kusunga. Malinga ndi katswiriyu, mtedza umachita chuku mlimi akafulumira kapena kuchedwa kukolola, ukanyowa poyanika, mlimi akauviika mmadzi ndi cholinga choti asende mosavuta kapena akasunga pachinyontho. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mtedza wopanda chuku umayenda malonda Tisaiwale kuti tikapitiriza kukhala ndi mtedza wa chuku sitingakhale ndi mwayi wogulitsa ku maiko akunja choncho miyoyo yathu komanso dziko lathu silingatukuke. Chinthu china chomwe chikuyenera kutipatsa mantha nchoti chuku chimatulutsa poizoni yemwe amayambitsa matenda a khansa ndi kunyentchera, iye adatero. Kuonjezera apo, mphunzitsi wa ku nthambi ya za ulangizi wa mbewu ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar), Paul Fatch adati poizoniyu amachepetsa chitetezo cha mthupi komanso chilakolako cha zakudya. Poizoniyu akachuluka mthupi, amachepetsa mphamvu yobereka, adatero Fatch. Pofuna kupewa zonsezi, Andasiki adati choyambirira alimi akolole mtedza wokhwima bwino, akaukumba awuyanganitse kumwamba kufikira utauma ndipo akachoka apo, athothole ndikuuika mmatumba ndikusunga pouma. Katswiriyu adafotokoza kuti mlimi akolole mtedza akaona kuti mkati mwake makoko achita madontho akuda. Pofuna kutsimikiza izi, iye adati mlimi akuyenera kukumba mapando okwana 10 mwapatalipatali ndipo akamaliza, athothole mtedza ochepa pa phando lililonse ndikuwusenda. Mlimi akapeza kuti mwa mtedza 100 omwe waswa, wosachepera 80 makoko ake ali ndi madonthowa ndiyekuti wakhwima ndipo ayambe kukumba, adafotokoza motero. Iye adati pamene mlimi akukumba mtedza akuyenera kuwuzonditsa kuti uyangane kumwamba ndi cholinga choti uwume bwino ndi dzuwa. Mlangizi wa za ulimi wa mbewu ku Dowa Sangayemwe Kausiwa adati alimi akuyenera kusamala pokumba kuti wambiri usasalire mmunda. Poyambirira, iye adati mlimi apewe kudzula mtedza koma azigwiritsa ntchito khasu. Pokumba, mlimi aziima pakati pa mzere ndikukuma mbali zonse ziwiri mwa mphamvu ndi cholinga choti onse unyamuke bwino, adatero Kausiwa. Mlangiziyu adati kuyenda mmunda ndikumatolera osalira kumathandizira kuti pafupifupi mtedza wonse uchokemo. Iye adaonjeza kuti alimi apewe kuviika mtedza mmadzi kuti usavute kuswa chifukwa izi zimakolezera chuku. Andasiki adafotokoza kuti alimi apewe kusunga mtedza wosenda kwa nthawi yaitali chifukwa umaonongeka. Malo wosungira mbewuyi akhale ouma komanso alimi ayiteteze ku makoswe, adatero katswiriyu. Moses Tanazio wa mboma la Ntcheu ndi mmodzi mwa alimi omwe amatsatira bwino kwambiri malangizo pa ulimi wa mbewuyi. Iye adati padakali pano sadayambe kukolola kufikira ukwaniritse zomwe alangizi adamuuza. Mtedza wanga ukakhwima, ndimakumba ndikuuyanika mmunda momwemo powuzondotsa ndipo ndimathothola pokhapokha ukauma bwino. Mtedza owuma bwino umachita phokoso ukamautafuna choncho ukafika apa, ndimathothola, kuusankha, kuulongeza mmatumba abwino ndikuunga, iye adatero.
4
Zomba District Health Office launches its strategic plan. By : Judith Sonkho Formulation and implementation of a Strategic Plan (SP) is said to be one of the key ways and interventions for addressing a number of Health issues gripping the country. Acting Director of Health and Social Services in Zomba district, Dr. Raphael Piringu was speaking at a media briefing organized by Zomba District Health Office with an aim of updating journalists on the progress of their Strategic Plan implementation in the district. Dr. Piringu, said for the first time in the history of the Ministry of Health in the country, Zomba District Health Office launched its first-ever Strategic Plan to address a number of challenges affecting delivery of quality Health Care Services in the district. We are intensifying the fight against maternal mortality rate, infant mortality rate and fertility rate, among other thematic areas of this Strategic Plan, said Dr. Piringu. Acting Director of Health and Social Services in Zomba district, Dr. Raphael Piringu The Acting Director of Health and Social Services said maternal mortality rate is on the increase in the district, thereby fueling maternal deaths, and their target is to reduce the vice by 20 percent by the year 2022. According to Dr. Piringu, the SP will also be looking into a global problem of HIV/AIDS and Tuberculosis, but at district level. He also said his office will strengthen partner collaboration and community ownership of the Strategic Plan to ensure effective implementation of the same to achieve desired goals. As one way of strengthening this, we have formed the SP together with the community and the stakeholders and we are planning to implement and review it together, continued Dr. Piringu. The Strategic Plan has a lifespan of five years, from 2017 to 2022 and will be drawing its inspiration from the Ministry of Healths Strategic Plan which is currently being implemented at a national level.
6
Alimbikitsa Achinyamata Asamalire Chilengedwe Achinyamata a mu parish ya Bembeke mu dayosizi ya Dedza awapempha kuti athandize mpingo poteteza chilengedwe. Mkulu wa achinyamata mparishiyi a Ignasicius Chalanda ndi omwe amalankhula izi potsekera mbindikiro wa masiku atatu omwe anali nawo, pofuna kuwawunikira achinyamatawa zakuipa kowononga zachilengedwe. A Chalanda awunikiranso achinyamata kuti azigwiritsa ntchito makina a computer moyenera pofuna kupewa zinthu zoipa zomwe zikufalitsidwa kudzera pa makinawa. Tikuwasula kuti akhale achinyamata odalilika mu mpingo. Tikuwalimbikitsanso kuti atenge mbali posamalira chilengedwe, anatero a Chalanda. Polankhulapo mmodzi mwa achinyamata omwe anatenga nawo gawo pa mbindikirowu Olifeyo Christiano anati wapindula kwambiri ndi mbindikirowu. Tazindikira ntchito zomwe tikuyenera kuchita ngati mbali yathu mu mpingo, anatero Christiano. Iye wati pa mbindikirowu achinyamatawa alimbikitsidwanso kuwerenga kwambiri baibulo monga chaka chomwe Papa anakhazikitsa kuti chikhale cha baibulo.
18
Kawangi CDSS Iyendera ndi Kuthandiza Radio Maria Malawi By Richard Makombe Akhristu mdziko muno awalimbikitsa kuti azitenga nawo mbali pothandiza Radio Maria Malawi kamba koti imasowa thandizo pa ntchito yake yofalitsa uthenga wa Mulungu. Patron wa achinyamata a gulu la Young Catholic Students (YCS) pa sukulu ya Kawangi CDSS mboma la Dowa a Emmanuel Maseko ayankhula izi pomwe anadzayendera ku Radio Maria Malawi. A Maseko ati ndiokhutira ndi momwe Radio Maria imagwilira ntchito zake choncho nkoyenera kuti akhristu aziyithandiza kuti ipitilize kugwira ntchito zake. Ndife okhutira ndi kagwiridwe ntchito ka wayilesiyi ndipo tikuona kuti wayilesiyi imadzipereka pogwira ntchito zake choncho ndikoyenera kuyithandiza kuti ipitirize ntchito yabwino yomwe ikugwira, anatero a Maseko. Mmawu ake mmodzi mwa achinyamatawa Ezara Lazaro wati waphunzira zambiri paulendo wake ku Radio Maria, ndipo wati wadziwa zambiri za momwe wayilesiyi imagwilira ntchito zake. Ndikufuna ndipemphe achinyamata anzanga kuti nawonso tsiku lina adzabwere kuno kudzaona momwe wayilesiyi imagwilira ntchito zake komanso kudzaithandiza chifukwa ikusowekra thandizo la wina aliyense, anatero Lazaro. Achinyamatawa apereka ndalama zokwana 10 thousand kwacha kuti zithandize kupititsa patsogolo ntchito za wayilesiyi.
13
Makanja aphofomoka Makanja, chilombo chomwe chimayenda monyangwa poti chimayangana wina aliyense pamutu kaamba kotalika, chidaona zakuda masiku apitawa chitagwa pamsonkhano wa nduna ya zamalonda. Pomwe pabwera guleyu anthu amayembekeza kusangalala chifukwa amaoneka modabwitsa komaso amavina modolola mtima. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zidali chomwecho Lachiwiri ku Wovwe mmboma la Karonga, komwe nduna ya zamalonda Joseph Mwanamvekha, kazembe wa dziko la Japan ku Malawi, Shuichiro Nishioka ndi alendo ena olemekezeka adakayendera alimi a mpunga. Pofuna kuti alendowo asangalale, anthu kumeneko adakonza magule. Ataitanidwa, makanja anabwera pamalo a msonkhano monyangwa. Guleyu adayendera pabwalo modzithemba asanayambe kuvina. Apa anthu adayembekezera kuti patuluka fumbi koma zachisoni guleyu atangoyamba kuvina adapeperuka ndi kugwa chagada mwendo umodzi utathyoka. Pofuna kudzichosa manyazi guleyo, adayamba kunamizira kuvina pansi koma anthu otsogolera guleyo adaona kuti zavuta ndipo adapita kukamudzutsa. Kaamba ka ululu ndi manyazi, guleyo adachoka mbwalo motsimphina ndi kukatsamira galimoto ya nduna kwinaku akumverera ululu. Guleyu adaoneka wosowa mtendere kaamba koti anzake anatenga malo nkuthyola dansi mododometsa kwinaku akufupidwa ndi nduna ndi kazembe wa ku Japan. Anthu odzigwira adamumvera chisoni makanjayo, koma aphwete adaseka kaamba koti zidali zachilendo kuona makanja akuthyoka mwendo gule ali mkati. Utatha msonkhano nkhani idali pakamwa idali ya kuphofomoka kwa makanja. Ngakhale Mwanamvekha ndi anthu a ku unduna wake, komaso DC wa boma la Karonga, Rosemary Moyo, sadapirire koma kukambirana za kugwa kwa gule wamtaliyo. Mwanamvekha adati chidali chinthu chodabwitsa komaso chanchilendo kwa iwowo kuona gule akugwa.
19
HRC Yati Ithandiza Pomenyera Ufulu wa Ofalitsa Nkhani Bungwe lowona za maufulu a anthu mdziko muno la Human Rights Commission lati liwonetsetsa kuti likuthandiza pomenyera maufulu a wanthu pa ndondomeko ya zofalitsa nkhani kuti asapitilire kuphwanyidwa. Semphere: MACRA izibwera poyera Mkulu wa bungweli a Patrick Semphere wanena izi pambuyo pa mkumano womwe bungweli lachita ndi bungwe la loyanganira nyumba zofalitsa nkhani mdziko muno la Malwi Communication Regulatory Authority (MACRA), komanso unduna wa zofalitsa nkhani. Iye wati bungwe la MACRA likuyenera kugwira ntchito mosakondera kuti ntchito yolemba ndikuwulutsa nkhani ipite patsogolo. Pamene pali madandaulo a nyumba yowulutsa mawu ina, MACRA izibwera poyera ndi kuthandiza pa madandaulo amene alipo monga mmene anthu amadandaulira anthu kwambiri nkhani ya mapologalamu a pa MBC, anatero a Semphere. Pa zokambiranazi bungwe la bungwe la Human Rights Commission (HRC) lapempha bungwe la MACRA kuti lidzigawana malipoti a ntchito zawo ndi bunweli, komanso lilimbilitse mabungwe ena kuti adzigwira nayo ntchito limodzi pofuna kuti ntchito zake zizikhala zokomera wina aliyense.
14
Mkangano pakati pa asilamu ndi a gule Mkokemkoke udakula ku Mitundu mumzinda wa Lilongwe Lamulungu lathali pomwe a gule wamkulu adayamba kukokanakokana ndi anthu a chipembedzo cha Chisilamu. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkokemkokewo udayamba pomwe kudamveka kuti kuchipatala china kumeneko mayi wina wabereka mwana wokhala ngati gule wamkulu. Izo zidachitika mwamuna wina yemwe ati ndi mwamuna wa mayiyo adakatentha zibiya za gule wamkulu. Apa a kudambwewo adalamula Asilamuwa kuti apereke ngombe zisanu, akapereke phulusa la zomwe adatenthazo kwa mfumu komanso kuti avinire achinyamata Achisilamu omwe adakhudzidwa ndi nkhaniyo. Nkhaniyi pano ili mmanja mwa bwanamkubwa wa Lilongwe, Paul Kalilombe, yemwe wati adakumana ndi mbali ziwirizi ndipo pali chiyembekezo kuti iwo asiye kumenyana. Kalilombe wati mbalizi zauzidwanso zolemekeza chikhalidwe komanso chipembedzo cha aliyense malinga ndi malamulo adziko lino. Naye mlembi wa mkulu wa gulu la Achewa la Chewa Heritage Foundation (Chefo), Amos Chinkhadze, adatulutsa chikalata chopempha mbalizi kuti zisiye kuponyerana Chichewa ndikulola zokambirana kuti zichitike.
13
Chisiki: Mchezo wa amayi Chikondano: Amapatsana zinthu mwachinsinsi Pamoyo wathu pali njira zambiri zomwe timalumikizirana pophunzitsana, kugawana nzeru ndi kuunikirana. Umu ndimo moyo ulili. Ngakhale izi zili choncho, ambiri amaona ngati okhala nawo pafupi ndiwo angakhale abwenzi awo, koma maganizo oterewa akutsutsidwa ndi mchezo wa amayi womwe amautcha chisiki. Ndidacheza ndi Miriam Chikondano, yemwe akulongosola za chisiki motere: Moni mayi ndipo ndikudziweni. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Zikomo, bambo. Ine ndili bwino ndipo dzina langa ndine Miriam Chikondano wammudzi mwa Chimoka ku Lilongwe. Ndili pabanja ndipo ndili ndi ana 4anyamata atatu ndi msungwana mmodzi, mzime. Mudapalanako ubwenzi ndi mayi mnzanu? Kwabasi, moti padakalipano ndili ndi abwenzi achizimayi ambiri zedi omwe ndimagawana nawo nzeru ndi kucheza nawo. Ubwenzi woterewu mumawuona bwanji? Choyamba ndimasulire tanthauzo la mawu akuti ubwenzi chifukwa masiku ano anthu amaganiza mothamanga ndiye ena amadzayamba kutanthauzira mawuwa mwawomwawo. Mawu akuti ubwenzi amatanthauza chinzake pakati pa anthu awiri kapena kuposerapo. Mukafunsa za mmene ndimauonera ubwenzi woterewu yankho langa ndi lakuti ndi njira imodzi yabwino kwambiri yomwe anthu amagawanirana nzeru, kulangizana ndi kulumikizana pankhani zosiyanasiyana. Kodi mgwirizano wa amayi umatchedwa kuti chiyani? Mgwirizano wa amayi umatchedwa kuti chisikileti koma mwachidule amangoti chisiki ndipo mzimayi mmodzi amatha kukhala ndi zisiki zingapo panthawi imodzi popanda vuto kapena madandaulo alionse. Dzinali limachokera pati? Dzinali lisakuzunguzeni, ayi, limachokera pa mawu Achingerezi oti secret koma ndi longofuna kusiyanitsa maubwenzi ena ndi ubwenzi umene tikukambirana panowu. Dzinali limabwera potengera zomwe zimachitika paubwenziwo. Apa ndikutanthauza zomwe mayi ndi bwenzi kapena abwenzi ake amapangirana paubwenzi wawo. Mungatambasule zomwe zimachitikazo? Panthawi ya ubwenziwo amayi amagulirana mphatso zosiyanasiyana mwamseri nkumapatsana mokhala ngati mobisa zija mChingerezi amati secret monga ndanena kale, ndiye pofuna kusazungulira amangoti chisiki basi. Chisiki chimayamba bwanji? Pali njira zambiri zomwe chisiki chimayambira koma mfundo yaikulu yagona pakuti anthuwa amakhala paubwenzi. Chisiki china chimayamba chifukwa anthu amachokera kumodzi, china chimayamba chifukwa chakuti anthu amayendera limodzi kapena adakumana kumalo kapena kuzochitika zina zake monga kutchalitchi, kumpalano wa magule, kumsonkhano ndi malo ena. Ndiye zimayamba bwanji? Ngati anthu agwirizana magazi amatha kukambirana kuti ayambe chisiki koma nthawi zina wina amangoyamba kutumizira mnzake mphatso kenako winayo amabweza basi chisiki chayamba chikatero. Phindu lake ndi lotani? Pali phindu lalikulu kwambiri, makamaka pamoyo wa munthu wamayi. Amayi amakhala ndi nkhawa komanso milandu yambiri mumtima kuposa abambo ndiye ngati mzimayi alibe mnzake womukhuthulira nkhawa ndi milandu yotere, moyo wake umakhala wokwinyirira ndiponso zinthu siziyenda koma akakhala ndi mnzake ngati siki wake amatha kukhuthulira khawa ndi mavuto otere kwa mnzakeyo, mtima nkumapepuka. Basi phindu lake nkukhuthula nkhawa ndi mavuto? Ayi, chomwe ndikutanthauza nchakuti pamakhala nkhawa ndi madandaulo ena ofunika kutanthauziridwa kapena kulimbitsidwa mtima ndiye amayi awiriwo pausiki wawo amakhala pansi nkukambirana za nkhani ngati zimenezi nkuthandizana nzeru kuti zinthu ziziyenda mndondomeko yake. Nanga chisiki chimatha kapena nchamuyaya? Chikhoza kutha malingana ndi zifukwa zake koma osangoti kwacha mmawa basi nkumati ndikuthetsa chisiki popanda chifukwa kapena mlandu uliwonse. Chifukwa chachikulu chagona pakusungirana chinsinsi monga ndanena kale kuti amayi omwe ali pachisiki amatha kuuzana za mavuto osiyanasiyana okhudza moyo wawo ngakhalenso a mbanja. Ndiye ngati wina akunka nalengeza za mavuto a mnzake chisiki sichingapitirire chifukwa palibenso ulemu kapena chinsinsi. Mungawauze chiyani amayi za chisiki? Mawu ndiwochepa. Mpofunika kusamala posankha bwenzi la chisiki basi. Ndi bwino ukaona kuti mnzako ali ndi chidwi choti mukhale pachisiki kumufufuza bwino lomwe kupewa kuti mudzayambane nkudana patsogolo.
15
Madise Walangiza Makomishonala Atule Pansi Maudindo Awo Mmodzi mwa akatswiri pa nkhani za malamulo mdziko muno Dr. Sunduzwayo Madise walangiza makomishonala a bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) kuti atule pansi maudindo awo. Dr. Madise yemwenso ndi mphunzitsi wa za malamulo ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor amayankhula izi pothilirapo ndemanga pa zomwe wanena mmodzi wa ma Commissioner a bungwe la MEC, Dr. Jean Mathanga pa msonkhano wa atolankhani lachiwiri, pomwe anati sangatule pansi udindo wake pokhapokha contract yake itatha. Odziwa ntchito mdziko muno si okha-Madise Iwo awuza ma Commissioner kuti ntchito yomwe akugwira siyawo koma ndi yothandidza mtundu wa a Malawi choncho sipofunika kuti akakamilire kugwira ntchito. Akuyenera kudziwa kuti ntchitoyi ndi yotumikira a Malawi ndipo ngati zavuta, yawavuta ndi ofesi ya ukamishonalayo osati alephera ndi iwowo ngati munythu ayi, anatero Dr. Madise. Pamenepa Dr. Madise atinso ngati makomishonalawa akakamirebe kudzayendetsa chisankho chikubwerachi ndiye kuti padzakhalanso mpungwepungwe chifukwa anthu sadzawakhulupiliranso. Apapa kukakamiraku akungopereka mpata wa mpungwepungwe winanso. Mdziko muno odziwa ntchito si okha ayi akanasiya maudindo ena ayendetsenso, anatero Dr. Madise.
11
Alowerera paesiteti ya Kawalazi T/A Kabunduli wa mboma la Nkhata Bay wadandaula ndi anthu pafupifupi 500 omwe adalowerera ndi kukhazikika paesiteti ya tiyi ya Kawalazi mbomalo. Kabunduli wati anthuwa, omwe awutcha mudziwo Joni(potengera mzinda wa Johannesburg mdziko la South Africa), ndi aupandu chifukwa sadatsate dongosolo loyenera lopezera malo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Anthuwa adandipeza zaka zoposa zisanu zapitazo kupempha malo ndipo ndidawauza dongosolo loyenera, koma zodabwitsa ndi zoti adakalowerera malo a esiteti, adatero Kabunduli. Mwambi uja amati tikhale nawo adalanda malo ukupherezera pankhaniyi pomwe Kabunduli akulongosola kuti anthuwa si mbadwa za boma la Nkhata Bay koma ndi obwera kuchokera maboma ena a mhigawo cha kumpotochi. Kabunduli adati ali ndi nkhawa ndi mkanganowu chifukwa esitetiyi ndi mpamba wa anthu ake. Ndikuopa kuti mkanganowu ungakhudzenso ntchito za anthu a mdera langa amene amagwira kuesitetiku, Kabunduli adatero. Ndipo DC wa bomali, Fred Movete, adati anthuwa, omwe ambiri mwa iwo amaotcha makala chifukwa derali lili ndi mitengo yachilengedwe, amati adalowerera malowa chifukwa omwe adagula esitetiyi mzaka za mma 1970 sanawapatse makolo awo chipepeso. Movete adati ngakhale anthu ena akutero, ofesi yake idalandiranso malipoti oti anthuwa si mbadwa za mboma la Nkhata Bay koma ochokera kumaboma ena. Iye adalongosola kuti nkhaniyi yakhala ikulowa mbwalo la milandu kangapo konse makamaka pomwe anthu olowererawa adaphwanya galimoto, kulanda wapolisi mufti (yomwe idapezeka) ndi kuvulaza ogwira ntchito pakampaniyi. Padakalipano, tikukambirana ndi mbali ziwirizi kuti tibweretse mgwirizano chifukwa nkhanizi zikafika kukhoti, zinthu zimaonongeka, adatero Movete. Poyankhulapo akuluakulu a esitetiyi adati mchitidwewu ndi wobwezeretsa chitukuko mmbuyo. Wachiwiri kwa mkulu wa kampaniyi, Kenneth Kabaghe, adati anthuwa aika kampaniyi pampani. Iye adati ncholinga cha kampani yake kukhala mwabata ndi anthu oizungulira, koma izi zikuvuta ndi anthu a mudzi wa Joni.
7
Kukana kuba Woimba Joseph Nkasa mnyimbo yake ina, amaneneratu kuti aliyense ayenera kugwira ntchito ina iliyonse kupatulapo kuba. Ngakhale Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi sunganeneretu kuti kuba ndi ntchito, kupewa tchimoli kuli ndi njira zambiri. Apa tikuona mnyamata wina kumsika wa Limbe kugulitsa zinkhupule poopa kuba. Ntchito nzosiyana, koma tisaiwale ndalama ndi imodzi.
9
Mai Mutharika ati amayi akhale odzidalira Mkulu wa bungwe la Beautify Malawi Trust (Beam Trust), Gertrude Mutharika, walimbikitsa amayi mdziko muno kuti akhale odzidalira pachuma. Mutharika adalankhula izi masiku apitawa pomwe amakhazikitsa tsiku lokumbukira ntchito za mabizinesi la World Entrepreneurship Day mdziko la Amerika. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mutharika: Tayika ndondomeko zingapo Mutharika adati Beam Trust ikufuna kulimbikitsa amayi kutengapo gawo lalikulu pantchito za mabizinesi ngati njira imodzi yowalimbikitsira kudziyimira paokha. Tayika ndondomeko zingapo zomwe cholinga chake nkupititsira amayi ndi atsikana mmabizinesi. Beam Trust ilimbikitsanso amayi ndi atsikana kutengapo gawo lalikulu pantchito zolimbikitsa ukhondo mmatauni ndi mizinda, adatero iye. Iye adatsindika kuti kusowa mpamba woyambira bizinesi ndi chikole ndiye mavuto amene amayi ndi asungwana omwe akufuna kuyamba mabizinesi akukumana nawo mu Africa. Choncho, iwo adapempha mabungwe omwe ndi mabanki kuti aganizire kufewetsa mfundo zawo kuti amayi ndi atsikana adzitha kupeza ngongole mosavuta. Ena mwa atsogoleri omwe adakhala nawo pamsonkhanowo ndi mkazi wa pulezidenti wa ku Namibia Penehupifo Pohamba ndi mkulu wa bungwe la UN Foundation Cathy Calvin.
11
Papa Wapempha Anthu aku Japan Amupempherere Wolemba: Sylvester Kasitomu Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha anthu a mdziko la Japan kuti ateteze moyo komanso apemphelere ulendo wake wopita mdzikolo. Papa walankhula izi lero kudzera pa uthenga wake wa kanema ndipo wati chitetezo chomwe iye akupempha ndi chochokera mu mtima. Pamenepa Papa wati akukhulupilira kuti anthu a mdziko la Japan amazindikira ubwino wokambirana ngati pali kusamvana ndi cholinga chofuna kuteteza umoyo wa anthu. Iye anati dziko la Japan ndi lodalitsidwa ndi chikhalidwe chabwino chomwe chimasonyeza umoyo wabwino. Pomaliza mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu anayamikira onse omwe akuchita dongosolo lokonzekera ulendo wake ndipo anati apitiliza kupemphelera aliyense.
13
Papa Wayamikira Asisiteli a Chipani cha Vincent De Paul Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wayamikira asisiteri a chipani cha Vincent De Paul Woyera kamba ka ntchito yotamandika yomwe akhala akugwira ku likulu la mpingowu ku Vatican. Asisteri a chipani cha Vincent de Paul Woyera Papa Fransisco walankhula izi loweruka pa Misa yomwe anatsogolera kulikulu la mpingo ku Vatican. Iye wayamika asisiteliwa chifukwa cha ntchito yawo yomwe amagwira potumikira modzipereka ndimosatopa ndipo wati Tiwapemherere kuti Mulungu awapatse chaulere kamba ka ntchito yomwe amagwira. Chakachi poyamba chimachitika pa 15 March koma chinasinthidwa ndipo chimachitika pa 9 May mu nyengo ya Pasaka.
13
Anthu Okwiya Apha Munthu Pomuganizira Kuti Waba Mbuzi Bambo wina wa zaka 28 zakubadwa wa mboma la Chikwawa, waphedwa ndi anthu ena okwiya pomuganizira kuti anaba mbuzi. Wachiwiri kwa wofalitsa nkhni za apolisi mboma la Chikwawa Sergeant Dickson Matemba wati 11 koloko ya usiku wa tsikuli, mkuluyu Paul Fulyton amayendetsa njinga yamoto atanyamula mbuzi yokupha kale ndipo anthu ena a mmudzi mwa Nsanjama atamufunsa anakanika kufotokoza bwino za komwe watenga mbuziyo. Izi zinachititsa kuti anthuwo ayambe kumumenya ndipo kenaka anamuyatsa iye pamodzi ndi njinga yamotoyo. Apolisi ndi a zachipatala anafika pamalopo ndipo zotsatira za ku chipatala ati zasonyeza kuti mkuluyu wafa kaamba kotaya magazi ambiri chifukwa cha kuvulazidwa mmutu. Padakalipano apolisi mbomalo achenjeza anthu kuti aleke kutengera malamulo mmanja mwawo ndipo mmalo mwake azikanena ku polisi nkhani iliyonse yomwe yachitika ku dera kwawo.
14
Kusanthula ulamuliro mmasiku 100 a Banda Boma la mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda, likuyenera kukhwimitsa chitetezo mdziko muno, kuchepetsa kumanga anthu chisawawa komanso kuchepetsa kuchotsa anthu pantchito. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Atsogoleri azipani, mabungwe, mafumu komanso anthu otumikiridwa atero msabatayi pomwe amaikira ndemanga pazomwe mtsogoleriyu wachita mmasiku 100 akulamulira dziko lino. Koma mneneri waboma, Moses Kunkuyu, wati kusintha kwa maundindo ndi ntchito zina sikolakwika chifukwa mtsogoleri wa dziko akamalowa pampando amasankha anthu oti agwire nawo ntchito. Nayo nduna yazamdziko, Uladi Mussa yati boma likuyesetsa kuti chitetezo chikhwime mdziko muno. Iye adati nkutheka alipo ena omwe akufuna kuti ayalutse boma la Banda kuti lilibe chitetezo. Posangalala kuti watha masiku 100 akulamula dziko lino kuchokera pa 7 Epulo pomwe adamulumbiritsa mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu wa Mutharika atamwalira mwadzidzidzi, kudali mapemphero komanso zochitika zosiyanasiyana. Banda adayamba kulamula dziko lino litakutidwa mmavuto ndi mikwingwirima monga kusowa mafuta, ndalama zakunja, shuga ndi zina zotere. Nthawi ya ulamuliro wa Mutharika ndi chipani chake cha Democratic Progressive Party (DPP) kudadzanso malamulo ena amene amaoneka kuti ndiopondereza, monga lamulo limene limapatsa mphamvu apolisi kuchita chipikisheni opanda chikalata chaboma, lamulo lopereka mphamvu kwa nduna kutseka nyuzipepala kapena wailesi yodzudzula boma komanso kusokonekera kwa ubale wa dziko lino ndi maiko ena. Banda ndi chipani chake cha Peoples Party (PP) atangotenga boma, mavuto enawo adazilala. Koma malinga ndi ena, bomali lili ndi zolakwika zake. Manthu a mavuto Mneneri wa DPP, Nicholas Dausi, wati pamasiku 100, chipani chawo chaona zokhoma, manthu wamavuto komanso kulira chifukwa cha mpanipani womwe Banda wauchita kwa anthu achipanichi. Dausi wati sakuona chifukwa chomwe Banda angaonongere chuma cha boma posangalala kuti watha masiku 100 chikhalirecho zinthu mdziko muno sizili bwino. Chisangalalocho chikudabwitsa, kodi akusangalalira kuti Bingu adamwalira? Sitikuona kuti pali chosangalalira chifukwa ngakhale akuti mdziko muno muli mafuta komanso ndalama zakunja, moyo wa munthu wakumudzi sudasinthe chifukwa zinthu ndiye zakwera mtengo, adatero Dausi. Iye adati mdziko muno anthu achotsedwa ntchito komanso kumangidwa. Adapereka zitsanzo za omangidwa: mkulu wa bungwe lothana ndi ziphuphu la Anti-Corruption Bureau (ACB) Alexious Nampota, gavanala wa DPP kumpoto Christopher Ngwira, mkulu wa achinyamata mu DPP Lewis Ngalande, kalaliki wamkulu wa Nyumba ya Malamulo Matilda Katopola, mkulu woyanganira nyumba zaboma Edward Sawerengera ndi wachiwiri wake Nector Mhura, mkulu wapolisi Peter Mukhito komanso mkulu wa banki ya Malawi Savings Bank. Boma lakana kulembanso ntchito yemwe anali mkulu wa nthambi yaboma yoona za olowa ndi kutuluka mdziko muno Elvis Thodi. Kuchotsana ndi kumanganaku kukutidabwitsa, adatero Dausi. Mneneri wa chipani cha UDF, Mahmudu Lali, wati kupezeka kwa mafuta agalimoto, ndalama zakunja, kuchotsedwa kwa malamulo oipa komanso kubwezeretsedwa kwa mbendera ya dziko lino kwasonyeza kuti utsogoleri wa Banda zinthu zayamba bwino. Koma Lali wati boma lisakomedwe chifukwa zina zayamba kale kusokonekera: Chitetezo chasokonekera, taonanso momwe bomali layendetsera gawo 65 la malamulo adziko lino kuti angochita momwe boma la DPP lidachitira. Litawonanso kuti zipangizo zophunzirira ndizokwana msukulu komanso masitalaka akuyenera kutha. Zikuyenda bwino Malinga ndi kusintha kwa boma, aphungu ena achipani cha DPP adakhamukira kumbali ya boma mnyumba ya malamulo, koma ngakhale malamulo amati aphungu otere achitsedwe pamipando yawo ndipo kukhale chisankho cha chibwereza, Banda komanso akuluakulu a DPP ati izi nzosayenera chifukwa zingaononge ndalama komanso chifukwa boma lokhazikika ndilo likufunika. Mkulu wa bungwe loona zaumoyo la Malawi Health Equity Network (MEHN) Martha Kwataine wati ngakhale masiku 100 ndiochepa kukonza zinthu, boma la Banda layesetsa. Iye wati Banda akuyenera kuchenjera ndi anthu omwe amuyandikira chifukwa ndi anthu omwewo omwe adayandikira Mutharika. Tipemphe kuti bungwe la ACB lizifufuzanso anthu omwe ali mboma osangoti lidzifufuza omwe siali mboma, adatero Kwataine. T/A Chekucheku ya mboma la Neno yati sabata yathayi kwawoko amalandira cheke cha ndalama zoti amangire nyumba za aphunzitsi komanso kukonza sukulu yawo kumeneko zomwe wati ndichitsimikizo kuti zinthu zikuyenda. Iye wati umbava ndi umbanda wakula kudera lake kotero boma likuyenera kuchita kanthu. Mfumu yaikulu Malemia ya mboma la Nsanje yati zinthu zili bwino mmidzi chifukwa boma lati liyambitsa ntchito zachitukuko mmidzi zomwe wati zitukula anthu akumudzi. Addition Mawononga wa mmudzi mwa Matiya kwa T/A Nkumbira mboma la Zomba wati boma likhwimitse chitetezo. Chitetezo chacheperatu, Lamulungu pa 15 akuba adandibera K10 000 ndipo siine ndekha anthu akulira mdziko muno. Komanso tikumva kuti mkulu wa apolisi mdziko muno Lot Dzonzi wauza apolisi kuti asamawombere akuba; izi sizonena kulankhula pagulu, bwezi atangowauza apolisiwo koma momwe ateremu ndiye kuti chitetezo chimasukiratu, adatero mkuluyu.
11
Achinyamata akambirana za mmanifesto Nthambi ya achinyamata ya chipani cha Malawi Congress Party (MCP) yakambirana mfundo zokhudza achinyamata zomwe chipani chawo chiyike mmanifesto yake yokopera anthu pachisankho chikudzachi. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Woyanganira za achinyamata Richard Chimwendo Banda watsimikiza izi ndipo mneneri wachipanichi mbusa Maurice Munthali wati kupatula achinyamatawa, chipanichi chikulandira maganizo kuchokera ku magulu osiyanasiyana. Ena mwa achinyamata amene adafika kumsonkhanowo Tili mkati mopanga manifesto yathu poonjezera zomwe tidaiwala mu 2014. Imodzi mwa nthambi zomwe taikapo mtima kwambiri ndi achinyamata tsono tidaona kuti nkwabwino akambirane okha mfundo zowakhudza nkutipatsa, watero Munthali. Achinyamata a MCP a mchigawo chapakati ndi nthumwi za mzigawo zina amakumana kulikulu la chipanichi pa 23 ndi 24 August mumzinda wa Lilongwe kukambirana mfundozo ndipo Chimwendo Banda wati msonkhano ngati omwewu ukachitikaso mzigawo zina. Pamsonkhanowu, tidali ndi achinyamata 1 000 ochokera mmadera onse oyimiliridwa ndi aphungu mchigawo chapakati ndi mphepepete mwanyanja komanso nthumwi za mmakomiti a mzigawo. Misonkhano ngati yomweyi ikachitikanso mzigawo zina, adatero iye. Iye adati kumsonkhanoko, achinyamata adatulutsa nkhani zambiri zowakhudza nkuzikambirana ndipo adamanga mfundo za momwe akuonera kuti nkhanizi zikhonza kukonzedwa ndi atsogoleri. Iye wati chipanichi chidachita izi ngati njira imodzi yoperekera mphamvu kwa achinyamata kupanga ziganizo za momwe dziko lingayendere bwino ndipo wati ali nchikhulupiriro kuti atsogoleri a chipanichi akhutitsidwa ndi mfundozo. Pothirirapo ndemanga, Munthali adati komiti yaikulu idasangalala koposa ndi momwe msonkhano wa achinyamatawo udayendera komanso mfundo zomwe adamanga nkupereka ku likulu. Mfundo zomwe adatipatsa zikusonyeza kuti mchipanimu tili ndi achinyamata akupsa mmaganizo omwe angathandizedi pachitukuko cha dziko. Mfundo zawo tazitenga ndipo tiziphatikiza mmanifesto yathu chifukwa nzokomera achimata onse mdziko muno, watero Munthali. Woyendetsa gulu la mphala ya achinyamata la Youth Consultative Forum Edward Chileka Banda wayamikira zomwe chipani cha MCP chapanga ndipo wati zingakhale bwino zipani zonse zitatengera mchitidwewu. Zimenezi nzomwe timafuna ngati achinyamata kupatsidwa mphamvu osati kumangogwiritsidwa ntchito ngati osapota chipani kapena zida za zipolowe ndi andale ayi. Uku ndiye kuphunzitsa achinyamata utsogoleri, watero Chileka Banda. Iye wati kupatula momwe chipani cha MCP chapangira, mpofunikaso kuti achinyamata azipatsidwa mpata wokwanira ogwira ntchito zogwirizana ndi maluso awo osati kumangowaponderedza.
11
Kulandira Mawu a Mulungu ndi Kulandira Yesu-Papa Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wati povomera kulandira mawu a Mulungu akhristu amalandira Yesu Khristu yemwe. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa walankhula izi lamulungu ku likulu la mpingowu ku Vatican. Iye wati fanizo la wofetsa mbewu ndi lothandiza akhristu kuwunika za moyo wawo maka umo mmene alandilira mau a Mulungu. Mu zolankhulalankhula zake pa tsiku lamulungu la 15 mu nyengo ya pa chaka Papa Francisco wafotokozera Uthenga Wabwino womwe unawerengedwa pa tsikuli omwe ndi fanizo la wofetsa mbewu. Iye wati sikungakhale kulakwitsa kunena kuti fanizo la wofetsa mbewu ndi manthu wa mafanizo opezeka mu Baibulo popeza ili ndi fanizo lomwe likunena mwa mvemvemve zakufunika komvetsera Mau a Mulungu. Papayu wapitiriza kunena kuti Mau a Mulungu ndiye Yesu Khristu kotero amene amvetsera ndikuvomera Mau a Mulungu ndiye kuti akuvomera ndi kulandira Yesu Khristu amene. Iye wati Mau a Mulungu omwe ndi mbewu mu fanizoli ndi Yesu Khristu amene ndi Mau a Mulungu odzipangidwa munthu. Papa Francisco wati akhristu akuyenera kulandira Mau a Mulungu monga nthaka yabwino yomwe ichititsa mbewu kumera, kukula mpaka kubereka zipatso. Iye wati Mawu a Mulungu ali ngati mbewu imene Mulungu amafetsa pakati pa anthu ake. Papa Francisco wati munthu aliyense ali ngati nthaka pomwe mbewu yomwe ndi Mau a Mulungu amagwerapo ndipo kuti zili kwa munthu aliyense kusankha kuti akhala nthaka yotani. Ichi ndi chisankho chomwe munthu aliyense akuyenera kuchita pa moyo wake wa chikhristu.
13
Msusa Alimbikitsa Akhristu Kulemekeza Masacrament Wolemba Richard Makombe w/wp-content/uploads/2019/09/msusa.jpg" alt="" width="310" height="263" />Msusa: Mabanja sakuchedwa kutha Akibishop Thomas Luke Msusa wa akidayosizi ya Blantyre wapempha akhristu kuti akhale okonda kusunga ma sacrament. Akibishop Msusa amayankhula izi lamulungu pa mwambo wa chibalalaitso cha mpingo omwe unachitikira ku St. Pius Parish mu akidayosizi ya Blanytre . Bishop Msusa wati nkofunika kuti akhristu akhale olemekeza komanso kusunga bwino ma sacrament makamaka sacrament la ukwati. Ndizodandaulitsa kuona kuti tikadalitsa ukwati koma pakangotha chaka chimodzi uona kuti ukwati uja watha, choncho sibwino, anatero bishop Msusa. Bishop Msusa anatengerapo anathokoza parish ya St Pius kamba kokhala parish ya chitsanzo povomera kuchititsa mwambo wa chaka achino wa chaka cha chibalalitso. Ndithokoze akhristu komanso ansembe onse popemphelera mwambowu kuti ukhale opambana, anatero Akibishop Msusa. Chaka ndi chaka mpingo wa katolika umachititsa mwambo wa chibalalitso cha mpingo omwe cholinga chake ndikufunakupeza thandizo la ndalama zothandizira kukulitsa mpingowu pa dziko lonse.
13
Ndalama zakale zitha pa 23 May Banki yaikulu yakumbutsa mabanki a mdziko muno kuti ndalama zakale za Chilembwe dziko lino zisiya kugwira ntchito pa 22 May. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mchikalata chimene mkulu wa bankiyo Mary Nkosi adalembera mabanki a mdziko lino, bankiyo idalengeza pomwe limakhazikitsa ndalama zatsopanozo pa 23 May chaka chatha kuti pofika pa 22 May, ndalama zakale zikhala zitasiya kugwira ntchito. Koma ngakhale ndalama zapepala zisiye kugwira ntchito patsikulo, ndalama zachitsulo zidzakhala zikugwira ntchito mpaka mtsogolo muno, adatero Nkosi. Mchikalatacho, Nkosi adapempha mabanki kuti asamapereke ndalama zakalezi kwa makasitomala awo. Mabanki ayenera kutenga ndalama zakalezo ndi kukazisiya ku Reserve Bank akazilandira. Chenjezo kwa mabanki ndilakuti ayenera kusamala ndi ndalama zachinyengo, adatero Nkosi. Ambiri ati Chilembwe ngakhale idali khobili lokongola tsamba lake lidali lalikulu kotero simakwana bwino mu matumba komanso mzikwama zosungila ndalama poyenda (waleti).
2
Chenjerani pokolola Mbewu ya chimanga nayo imafuna kuyichengetera nthawi yokolola kuti zokolola zikhale zochuluka ndi zopatsa kaso. Wachiwiri kwa mkulu woona za kafukufuku wa mbewu ku Bvumbwe Research Station, Frank Kaulembe akuti nankafumbwe amaononga ngati alimi akolola chimanga chawo mochedwa kapena mofulumira. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Namkafumbwe amachecheta mosavuta chimanga chokololedwa mofulumira Mwachitsanzo, iye adati kukolola mbewuyi isadaume, mlimi akaiyanika imafota ndipo zotsatira zake nankafumbwe amaboola mosavuta. Mlimi akaichedwera, nankafumbwe wamkulu amayamba kuionongera kumunda komweko, iye adatero. Iye adaonjeza kuti kukolola chimanga chosauma nthawi yoyanika chimakumana ndi ndi mavuto monga kunyowa ndi mvula yowaza komanso kukachita chifunga mmawa, chimayamwa chinyontho mapeto ake chimachita chukwu, iye adatero. Pothirirapo ndemanga pa zomwe adayankhula Kaulembe, Paul Fatch, mphunzitsi wa kunthambi ya za ulangizi ya ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar), adati chimanga chimayenera kukololedwa chikakhwima komanso kuuma bwino ndipo chizindikiro chake nchoti chimaloza pansi. Pomwe, chimanga chimakhala chaumiratu ndipo kutonola chochepa ndi kuchiponya pansi chimachita phokoso, iye adatero. Ngakhale izi zili chomwechi, Fatch adati madera ena amayenera akololebe mwachangu kuopetsa akuba, chiswe komanso makoswe kotero alimi oterewa amayenera akachiumitse akafika nacho kunyumba pogwiritsa ntchito nkhokwe zoumitsira kapena dzuwa. Kaulembe adafotoza kuti mlimi sakuyenera kulowa mmunda ndi kuyamba kukolola chimanga tsiku lomwe kwachita mitambo ndipo kukuonetsa kuti nthawi ina iliyonse kukhoza kugwa mvula. Iye adati chimanga chikanyowa ndi mvula chimachita chukwu. Kaulembe adati ngati nthawi yokolola yafika koma kunja kukugwabe mvula, mlimi ayenera kuthandizira chimanga chomwe sichidaloze pansi kuti chitero ndi cholinga choti madzi asalowe mchimanga muja koma azingotsetsereka kufikira ataona kuti mvula yaleka. Ichi nchifukwa chake kale makolo ankasanja chimanga chawo mnkhokwe molozetsa pansi kotero ngakhale mugwere mvula, sichimaonongeka, iye adatero. Kuonjezera pa nankafumbwe yamwe amatha kuyamba kuononga chimanga chikakhalitsa mmunda,Kaulembe adati alimi asamakolole mochedwa kwambiri kuopetsa chiswe ndi moto olusa. Pokolola, mlimi aziona pomwe akuika chimanga chake chifukwa chikakhala pafupi ndi chulu, chimagwidwa ndi chiswe komanso akaika pachidikha, chinyontho chimaononga, iye adatero. Mlimi wa chimanga mboma la Salima Matiyasi Banda adati saphuphulumira kukolola chimanga chake chifukwa amafuna kuti chiumiretu, akangofikira kutonola, kuthira mankhwala ndi kuchisunga. Ndidaona kuti kuyanika ndi ntchito ina yolemetsa yapadera kotero ndimangochisiya mmunda momwemo kuti chiumiretu. Ndimakolola pokhapokha makoko ake akamaoneka ouma kwambiri, iye adatero. Mlimi wina wa mboma la Lilongwe Dust Chikumbutso adati amakolola mwamsanga kuopetsa akuba.
4
Bambo Anjatidwa Kamba Kogwililira Gogo wa Zaka 75 Apolisi mboma la Chikwawa amanga bambo wina wa zaka 27, pomuganizira kuti wagwililira gogo wa zaka 75 pamalo ena omwera mowa mbomalo. Malinga ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sergeant Dickson Matemba, mkuluyu Yesani Chumachawo, anapalamula mlanduwu usiku wa pa 31 May 2020, pomwe iye ndi gogoyu anali limodzi pa malo ena omwera mowa. Gogoyu atanyamuka pa malowa kubwelera kwawo, mkuluyu akuti anamutsatira, atafika kutali ndi anthu, mkuluyu anakokera gogoyu pa tchire ndi kuchita naye zadama. Ndizoona tatsekera mchitokosi bambo wina wa zaka 27 yemwe anagwililira agogo wazaka 75 usiku wina mchaka chino cha 2020, anatero Sergeant Matemba. Mwapadera apilosi ayamikira a chitetezo chakumidzi kaamba kothandizana ndi apolisiwa kupeza mkuluyu yemwe anathawa atachita izi. Padakalipano mkuluy akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa kuti akayankhe mlanduwu.
7
Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati maso ake akadali otsegula ncholinga choti boma la Tonse Alliance lisaphwanye ufulu wa Amalawi. Mkulu wa bungweli Gift Trapence wauza Tamvani kuti HRDC iwonetsetsa kuti mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera wakwaniritsa zomwe adalonjeza Lolemba kuti achepetsa mphamvu zake. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Trapence: Maso adakali otsegula Chakwera adapereka lonjezolo pamwambo wokondwerera kuti dziko la Malawi latha zaka 56 lili pa ufulu wodzilamulira. Mtsogoleriyu adalonjezanso kuti azipita ku Nyumba ya Malamulo kukayankha mafunso okhudza momwe akuyendetsera dziko lino. Chakwera adati awonetsetsanso kuti lamulo loti anthu akupeza mauthenga a boma mosavuta (Access to Information) layamba kugwira ntchito ncholinga cholimbikitsa kuchita zinthu poyera, komanso kuchepetsa ziphuphu ndi katangale. Adalonjeza kuti achotsa mphamvu zina za Pulezidenti ndipo mphamvu zimenezi zikhudze ku nthambi ya zachitetezo. Pulezidenti akakhala ndi mphamvu zambiri, nthambi ya chitetezo imasanduka ngati yake osati ya dziko, adatero Trapence. Iye adapempha Chakwera kuti awonetsetse ku mboma lake mulibe katangale ndi ziphuphu. Mphekesera za katangale zifufuzidwe ndipo mutu wake uzioneka, iye adatero.
11
CMO Iyamikra Abambo a Parish ya Mwanza es="(max-width: 564px) 100vw, 564px" />Abambo a Mwanza parishi kujambulitsa limodzi ndi abambo a ku Nthawira parishi Bungwe la Umodzi wa Abambo la Catholic Men Organisation (CMO) mu arkdayosizi ya Blantyre layamikira abambo a chikatolika a mparishi ya Mwanza ya mpingowu kamba kobwera mwaunyinji ndi kuzamvera mfundo, zolinga ndiponso masomphenya a bungweli Mkulu wa bungweli mu arkdayosizi ya Blantyre a Martin Chiwaya alankhula izi ku parishiyi lamulungu pa 1 December, 2019 pokhazikitsa bungweli ku parishiyi. Iwo ati akhutira ndi momwe abambo a mparishiyi mmene anatulukira ku zamvera mfundo zothandizira kupititsa patsogolo ntchito za bungwe latsopanoli Abambo aku Mwanza bungweli alirandira kwambiri, taona kuti abambo ambiri ochokera mmatchalitchi omwe ali pansi pa parishiyi anatsalira kuti amve zolinga za bungweli,anatero a Chiwaya Pamenepa iwo ati zoterezi zithandiza abambo a mu mpingowu kugwira nawo ntchito za mumpingo mmalo mosiyira amayi okha. A Dausi kufunsa mafunso pa zolinga za bungwelo Chidwi chomwe abambo akuchionetsa zikutilimbikitsa kwambiri kuti tsopano abambo ayamba kutulikira poyera ndi kukhala patsogolo pothandiza mpingo, anapitiliza a Chiwaya. Mau ake mmodzi mwa abambo a mparishiyi wolemekezeka a Nicholas Dausi omwenso ndi nduna ya boma komanso phungu waderali anati kubwera kwa bungweli kuthandizira abambo a mparishiyi kukhala pamodzi ndi kukweza miyambo ya chipembedzo komanso zochitika mu mpingo. Pamenepa a Dausi alimbikitsa abambo onse achikatolika kulowa nawo mbungweli mmaparishi awo Talimbikitsa kuti abambo ambiri tilowe mu bungweli kuti potero tizithandizana, tizizuzulana komanso tizizutsana wina mwa ife akagwa kuti mapeto ake tonse tikalowe mu ufumu wa Mulungu anatero a Dausi. Bungwe la Umodzi wa abambo mu arkdayosizi ya Blantyre likupitilizabe kuyendera maparish osiyanasiyana ndi cholinga choti lifikire mmaparish onse 43 amu arkdayosiziyi. Lamulungu la pa 8 December, 2019 bungweli kudzera mmakomiti okhazikika a mmaparishi ena ayendera ndikukhazikitsa bungweli mmaparishi za Lunzu, Mkhwayi, Nyungwe komanso Thunga.
13
Amangidwa Kamba Kogwilira Msungwana Ozelezeka Apolisi mboma la Chikwawa akusunga mchitokosi bambo wina wa zaka 35 zakubadwa Charles Mikeyasi kamba komuganizira kuti wagwilira mtsikana wa zaka 18 zakubadwa yemwe ndi wozelezeka. Malinga ndi wachiwiri kwa mneneri wa apolisi mbomali Sergeant Dickson Matemba, izi zachitika pa 18 mwezi uno, pomwe bamboyu yemwe amachokera ku mowa anakumana ndi msungwanayu pomwe anamukokera pa tchire lina la kufupi ndi komwe mtsikanayu amachokera ndi kumugwilira. Anthu ozungulira ndi omwe anagwira bamboyu ndi kukamutula mmanja mwa apolisi. Ndizoonadi kuti apolisi kuno ku Chikwawa tamanga bambo wina yemwe wagwirira mzimayi wa zaka 18 yemwe ali ndi ulumali wa mu ubongo pamene amachokera ku mowa, anatero Sergeant Matemba. Iwo ati bamboyu akawonekera ku bwalo la milandu posachedwa ndipo pakadali pano apolisi achenjeza anthu ku derali kuti adzisamalira ana awo omwe ali ndi ma ulumali onga awa pomayenda nawo limodzi. A Charles Mikeyasi amachokera mmudzi mwa bwalo mfumu yaikulu Kasisi mboma la Chikwawa.
7
Chipembedzo cha Chisilamu Chayamikira Kalata ya Maepiskopi Bungwe lowona za ufulu wa anthu ku chipembezo cha chisilamu la Muslim Forum for Democracy and Peace, layamikira chikalata maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko muno alemba momwe alankhulapo pa momwe zinthu zikuyendela mdziko muno. Kawinga ndi akuluakulu ena a bungwe la MFDP Mkulu wa bungweli Sheikh Jafah Kawinga wauza Radio Maria Malawi kuti ndi udindo wa mpingo kulankhulapo pa momwe zinthu zikuyenera kuyendera komanso momwe mzika zikuyenera kuchitira pofuna kukweza dziko lino. Sheikh Kawinga ati munthu ndi thupi ndi mzimu pamodzi choncho ndi koyenera kuti pamene mpingo ukupereka chiwuniko cha uzimu, pomweponso mpingo upereke zofunika ku thupi. Mpingo ukuyenera kulankhulapo pamene zikuchita bwino komanso pamene zisakuchita bwino chifukwa ukakhala chete ndiye kuti ukugwirizana ndi zomwe zikuchitikazo, anatero Sheikh Kawinga. Iwo adzudzulanso anthu ena omwe amanena kuti mpingo wa katolika ukulowelera ndale ponena kuti anthuwo sadziwa mbiri ya zipembedzo kaamba koti ati zimenezi zimachokera mu baibulo komans Quaran.
13
anatchezera Akuti tibwererane Anatchereza, Ndinali pambanja ndi mwamuna wa ku Nsanje ndipo ndili naye mwana mmodzi. Koma ndikati tiyeni tikaone kwanu amangoti tidzapitabe chikhalireni palibe ndi tsiku ndi limodzi lomwe abale ake anabwerapo pakhomo pathu ndiponso banja lathu ndi losagwirizira chinkhoswe. Kumudzi kwathu mwanuna wangayu amakananso kukaonako. Panopa tinasiyana chifukwa samagona mnyumba. Mowa samwa komanso fodya sasuta. Ndiye panopa akukakamira kuti tibwererane, apo bii ndimupatse mwana wake, koma ineyo ndikukana. Gogo, ndithandizeni. Nditani pamenepa? Mwati mudali pabanja, koma banja lanu padalibe chinkhoswe? Ndiye lidaali banja lotani lodziwa awiri nokhanu? Apa mukuchita kudabwa kuti a kwawo kwa mwamuna wanu sadabwerepo pakhomo panu ngakhale tsiku limodziakadabwerapo bwanji ngati akukudziwani? Munasiyana koma pano mwati akukakamira kuti mubwererane, pachifukwa chiti? Mwachidule, ndinene kuti mmphechepeche mwa njovu sapita kawiri. Kubwererana ndi mwamuna wotere kuli ngati galu kubwerera kumasanzi akepalibe chanzeru. Koma ngati watsimikiza kuti amakukonda ndipo nawenso umamukondabe, ulendo uno muyesetse kuti akwawo ndi akwanu akumane ndi kukambirana kuti pakhale dongosolo lenileni, chinkhoswe kenaka ukwati wovomerezeka ndi mbali zonsezonse. Pokhapo ndiye kuti mutha kumanga banja, osati zachibwana zimene mudachita kupatsana mwana kenaka wina aziti tibwererane apo bii undipatse mwana wanga. Banja si masanje, chonde! Zikomo, Natchereza Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Akuthawathawa Anatchereza, Mwezi wa April 2011 ndinapeza mwamuna ndipo sindinagonane naye kufikira 6 July 2012 pamene tinakaonekera kwa makolo a tonse. Tsiku limneli andiuza kuti tigonane koma ndinawauza kuti tikayezetse kaye HIV koma adakana ponena kuti iwo ndi blood donor choncho ndisawakaikire ndipo zinatheka. Titasiyana tsiku limenelo adandiuza kuti tikadziwe komwe amagwira ntchito ku Zomba. Nditapita andiuza kuti ndisabwererenso tiyambiretu banja koma ndinakana ndipo ndidabwerera. Patapita masiku adabwera ndi amalume awo kudzafunsira mbeta ndipo zinatheka. Pambuyo pake tidayamba banja ndipo posakhalitsa ndidaima. Mwanunayu adandiuza kuti mmamawa azidya phala ndipo nsima izikhala ya mgaiwa. Chodabwitsa chinali choti phala likafika patebulo limasintha mtundu kukhala lobiriwira (green) koma kuwafunsa samandiyankha zomveka. Nditalimbikira anandionetsa mabotolo awiri momwe munali zinthu za ufa za green koma anakana kundiuza ntchito yake, ati sizimandikhudza. Tsiku lina ananditenga kuti tikayezetse magazi koma titafika kumneko anandiyeza ndekha ati iwo adyezetsa kale. Anandipeza ndi kachilombo ka HIV. Kuyambira tsiku lomwelo anandiuza kuti banja latha ndizipita kwathu. Ndinakatula nkhaniyi kwa amalume awo koma palibe chikuchitika. Nditani? M Zikomo M, Sindidziwa kuti kachilombo ka HIV mudatatenga bwanji, koma sindikukaika kuti mwamuna wanuyo ndi amene adakupatsirani kachilomboko ndipo zikuonetseratu kuti amachita izi uku akudziwa kuti ali ndi HIV. Ndatero chifukwa cha zochita zakeakuonekeratu kuti alibe chilungamo mzochitika zake. Nanga timabotolo ta mankhwala obiriwira amathira mphalato ntachiyani? Nanga amakana kukayezetsa chifukwa ninji? Pano inu mwapezeka ndi HIV akuti banja latha, zoona? Ndithu, ngati iyeyo adali walungalunga, akadatha kuchitapo china chake kuonetsa kuti wakhumudwa kuti inuyo ndi amene mwamupatsira kachilomboko. Pali malamulo mdziko muno, oti wina akapatsira mnzake kachilombo ka HIV mwadala, ameneyo ali ndi mlandu. Ndithu, pitani nayoni nkhaniyi kwa odziwa malamulo kuti akuthandizeni.
12
Kuthana ndi vuto Kwa zaka 20, gulu la alimi a ngombe za mkaka la Namahoya la mboma la Thyolo silimapeza phindu mnyengo ya mvula chifukwa limangogulitsa mkaka wokwana magawo 10 pa 100 aliwonse nthawi zina osagulitsa ndikomwe. Wapampando wa gulili Taulo Chisoso adati izi zimachitika chifukwa ogula akayeza mkaka umaupeza uli ndi madzi wochuluka. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Wyson kudyetsera udzu ngombe yake Koma padakali pano, mkuluyu adati vutoli adathana nalo. Kwa zaka zonsezi, nyengo ya mvula ikafika kwambiri tinkangodyetsera udzu wauwisi chifukwa umapezeka wochuluka osadziwa kuti tikuzionongera msika, adatero Chisoso yemwe gulu lake lili ndi mamembala 550. Mu 2016 tidapeza ulangizi woti kudyetsera kwambiri ngombe za mkaka msipu wobiriwira, kumachulukitsa madzi ku mkaka ndipo titaleka, taona kuti chaka chonse chatha mpaka lero sudabwererepo pamsika, adatero Chisoso. Mlimiyu adati kampani yomwe imawagula, imafuna mkaka wabatala loyambira magawo 20 pa 100 aliwonse. Akalephera kukwaniritsa izi, amaubweza. Membala wa gululi, Chrissie Wyton, adati mmbuyomu nyengo ya mvula ikafika amadyesera msipu wauwisi wabwiri chifukwa deya amakwera mtengo, komanso samapanga mfutso wa ziweto. Padakali pano, ndidaleka kudyetsera udzu wauwisi wochuluka chifukwa ndimapanga mfutso pophatikiza msipu wa mitundu yosiyanasiyana kuti zikamadya, zizipeza michere yokwanira mthupi. Kuonjezera apa, ndimasunga madeya chifukwa ndazindikira kuti ulimiwu ndi bizinesi choncho ndikuyenera kumaikirapo mtima, iye adatero. Mlangizi wa ziweto ku Mzuzu Agriculture Development Division (Mzaad), Jacob Mwasinga, adafotokoza kuti kudyetsera kwambiri ngombe za mkaka msipu wa uwisi kumakhala ngati mlimi akuzipatsa madzi ambiri, koma chakudya chochepa. Izi zili chomwechi chifukwa msipuwu, umangochuluka madzi, koma michere imachepa. Mkaka umakhala wochuluka, koma ngakhale kungouyangana, umaoneka ngati wathiridwa madzi choncho sungayembekezere zabwino pamsika, iye adatero. Mwasinga adafotokoza kuti udzu umakhala ndi michere yochulukirapo mapeto a mwezi wa February kapena mayambiriro March. Iye adati izi zili chomwechi chifukwa umakhala wakula ndipo ukupita kokhwima kotero umakhala ndi michere yochulukirapo. Mlangiziyu adati ichi nchifukwa chake alimi amayenera kupanga mfutso wa ziweto udzu ukafika pamenepa. Pothirirapo ndemanga, mphunzitsi wa ziweto wa ku Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar), Jonathan Tanganyika, adati ngakhale msipu ndi wodalirika pa ulimi wa ziweto, alimi azichulutsa chakudya choonjezera mu nyengo ya mvula.
4
2018: Chaka cha ululu Mu February 2018, Dorothy KampaniNyirenda amagwiritsira magetsi a K2 500 pa mwezi. Kufika mu October mpaka lero, Nyirenda akugwiritsira magetsi a K5 000 pa mwezi. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kukwera mtengo wa mafuta kudaliza Amalawi Mayiyo amene amakhala ku Bangwe mumzinda wa Blantyre, adati mu February, 2018 amagwiritsira ntchito K700 kulipirira minibasi kuti akafike ku Trade Fair komwe amapanga bizinesi. Lero zasintha pamene akugwiritsira K1 000 mtunda womwewo. Uwu ndiye ululu umene anthu akhala akuumva mchaka cha 2018 kutsatira kukwera mtengo kwa mafuta agalimoto komanso kukwera kwa magetsi komwe kudapangitsa kuti zinthu zikwerenso. Malinga ndi malipoti a Centre for Social Concern (CfSC), banja la anthu 6 mchaka cha 2017, limafunikira likhale ndi K183 000 pa mwezi. Izi zimachitika pamene ndalama yotsikitsitsa yomwe munthu amalandira idali pa K19 000. Koma mu 2018, banja la anthu 6 limayenera likhale ndi K190 549 pa mwezi pamene ndalama yotsikitsitsa yomwe munthu amalandira idali pa K25 000. Kutanthauza kuti banja la anthu 6 okhala mtauni amalowa mmasautso osaneneka kuti athe mwezi umodzi chifukwa zomwe amapeza zimasiyana ndi zomwe zimafunikira. Magetsi akhale akukwera mchakachi. Pamene timamaliza 2017 nkuti mafuta a petulo akugulitsidwa K888 00 pa lita imodzi ndipo dizilo adali pa K890 90 pa lita imodzi. Mafutawo adakwera kanayi mchakachi ndipo petulo adafika pa K990 50 pamene dizilo adafika pa K990 40 pa lita. Izi zidachititsa kuti maulendo a minibasi akwere ndi 5 pelesenti mdziko muno. Mu October, bungwe logulitsa magetsi la ESCOM lidakweza magetsi ndi ndi 31.8 pelesenti. Kwa amene amagwiritsira magetsi a K7 714 pa mwezi adayamba kugwiritsira ntchito K10 105 pa mwezi. Zinthu zambiri zofunikira pamoyo wa munthu zidakwera mtengo monga thumba la chimanga lolemera ndi makilogalamu 50 lidafika pa K10 000 kuchoka pa K5 000 mu June mchakacho. Kwa KampaniNyirenda, chakachi chidali chowawa chifukwa mitengo ya zinthu zidakhazikike. Vuto lalikulunso nkuti bizinesi simayenda ndiye kuti upeze ndalama yogulira chakudya pakhomo ndi yoyendera kwakhala kovuta, adatero. Mkulu wa bungwe loona za anthu ogula la Consumer Association of Malawi (Cama), John Kapito adati ngakhale mchakachi ndalama ya kwacha idaoneka kuti idali ndi mphamvu, komebe izi sizidathandize ogula. Anthu akuvutika kuti agule katundu, nthawi iliyonse mitengo ikungosintha. Boma likuyenera libweretse yankho kuti chaka chino anthu asavutike, adatero. Kapito adati chaka cha 2019 chingakhale chabwino kwa anthu ngati boma litaonetsetsa kuti mitengo ya zinthu zofunikira kwambiri pamoyo wa munthu sizikukwera mwachisawawa.
2
Zampira zenizeni ndi CJ Banda John CJ Banda ndi kaputeni wa Blue Eagles, komanso ndi katundu wofunika ku Flames. Iye wapeza mwayi wokasewera ku Jomo Cosmos mdziko la South Africa. Kodi apita liti? Nanga mbiri yake ndi yotani? BOBBY KABANGO akucheza naye. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzina lonse ndi ndani? Banda: Amanditcha CJ Dzina langa ndi John Banda koma ondikonda amati John CJ Banda. Okukonda ake ati? Nanga CJ akutanthauzanji? Anthu a kwathu ku Nkhata Bay ndiwo adandipatsa dzina la CJ, chidule cha Christopher John Banda amene ankasewera mu Big Bullets. Ati timasewera mpira wofanana. Ena amaganiza kuti adali bambo anga koma ayi, padalibenso chibale ndi ine. Tamva kuti ukupita ku South Africa, unyamuka liti? Ulendo mwina ulipo kapenanso ayi. Izi zili chonchi chifukwa eni akewo adamaliza nambala ya osewera akunja amene amayenera alembe komanso nkhani yeniyeni yomwe ndikudziwa ine ndi yakuti sadamalize kupereka ndalama kutimu yanga yomwe adagulira Micium Mhone. Koma zonse zikatheka ndiye mu May muno tipitako komanso dziwani kuti pali matimu ena amene akundifuna ngakhale matimuwo sindingawatchule maina awo pano. Koma mayeso mudakhozadi? Kwambiri, ngakhale mutafunsa eni timu akuuzani kuti zidatheka, ntchito tidagwira. Tandiuzako za chiyambi chako pa chikopa. Ndidayamba kusewera mpira ku Eagle Strikers mu 2008. Tidali osewera amene tidailowetsa muligi ndipo idatha chaka osatuluka. Mu 2010 ndidachokako ulendo ku Police Training School. Kuchoka uko ndi pomwe ndimadzayamba kusewera mu Blue Eagles. Tidawina Standard Bank Cup mu 2011, Carlsberg Cup mu 2012 ndi Fama Cup mu 2012. Nanga mbiri yako ku Flames? Ndidatengedwa kukasewerera Flames mu 2011 pamene timamenya ndi Kenya. Ndasewera magemu 46 ndipo ndachinya zigoli 10, chaka chathachi ndidachinya zigoli zinayi kuposa osewera aliyense mu Flames. Koma ndimasewera pakati. Uli pabanja? Mkazi uyo akumvayo, dzina lake Jane komanso mwana alipo dzina lake Sean. Kodi udindo wako ndi wotani ku polisiko? Ndine Inspector kulikulu la polisi ku Area 30.
16
Kalembera wafika kummwera Kalembera wa mkaundula wachisankho cha chaka cha mawa wafika mchigawo cha kummwera tsopano ntchitoyi itakumana ndi zokhoma zosiyanasiyana mmaboma a mchigawo chapakati pomwe idayambirira. Boma la Ntcheu ndi boma lomaliza la mchigawo chapakati komwe kwafika kalemberayu mgawo lachinayi ndipo mgawo lomweli muli maboma a mchigawo cha kummwera monga a Blantyre, Mwanza ndi Chikwawa. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ntchito ya kalembera Kalemberayo adayamba Lachinayi ndipo adzatha pa 29 August. Malingana ndi mkulu woyanganira zisankho ku Malawi Electoral Commission (MEC), Sam Alfandika, pali chiyembekezo choti pamene ntchitoyi ikupitirira, mavuto omwe amaoneka mmagawo atatu oyambirira achepa kwambiri chifukwa anthu aphunzira mokwanira za kalemberayu. Kumayambiriro kuja tidali ndi vuto loti anthu ambiri adali asadadziwitsitse za kalemberayu koma pano ndi mauthenga omwe akhala akuperekedwa, anthu ambiri akudziwa ndipo chiyembekezo nchachikulu kuti ziyenda bwino, adatero Alfandika. Iye adapempha kuti zipani zitengepo mbali yaikulu yomema anthu kuti akalembetse chifukwa anthu omwewo ndiwo mavoti awo. Mkulu wa bungwe lophunzitsa anthu la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust, Ollen Mwalubunju wati bungwelo lipitiriza kuphunzitsa anthu mmadera momwe mukulowera kalemberayu kuti cholinga chenicheni cha demokalase chidzawoneke pachisankho cha chaka chamawa. Zimakhala zofoola nkhongono kuona kuti anthu ochepa ndiwo avota kusankha atsogoleri chifukwa zimakhala ngati ena aja angokakamizidwa kutsogoleredwa ndi anthu omwe sadawafune, ndiye tikufuna ulendo uno, aliyense yemwe ndi woyenera kuvota akavote. Chiyambi cha zonse ndi kulembetsa, adatero Mwalubunju. Iye adati ndi wokondwa ndi momwe kalembera adayendera mgawo lachitatu lomwe limachitika ku Lilongwe ndipo adati izi zidatheka chifukwa bungwelo ndi mabungwe ena komanso mipingo ndi zipani adagwirana manja kumema anthu. Poyamba kalemberayu mmaboma a Kasungu, Salima ndi Dedza, padali mavuto aakulu okhudza kufaifa kwa zipangizo mpakana anthu ambiri sadalembetse. Mavutowa adapitirira mgawo lachiwiri ku Mchinji, Dowa, Ntchisi ndi Nkhotakota moti chipani cha Malawi Congress (MCP) ndi mabungwe ena monga la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) adapempha MEC kuti idzabwereze kalembera mmabomawa. Mavutowa adadzachepa mgawo lachitatu lidatha sabata yatha koma padapezeka mavuto ena monga anthu kulandidwa ziphaso komanso miyambo yamakolo yomwe imabwezera kalembera mmbuyo.
11
Mavuto a madzi akula mu October ku Lilongwe Pomwe anthu mumzinda wa Lilongwe akubangula ndi vuto la kuzimazima kwa magetsi, kampani yopereka madzi ya Lilongwe Water Board yachenjeza kuti madzi nawo avuta mwezi ukudzawu. Mneneri wa bungweli, Bright Sonani, watsimikiza za nkhaniyi koma wati anthu asade nkhawa kwambiri chifukwa madzi azitulukabe ngakhale mwa apo ndi apo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Sonani wati bungweli litulutsa ndondomeko ya mmene madzi azitulukira kuti anthu azitunga nkusunga madzi okwanira mmakomo mwawo panthawiyi. Mwezi umenewu tikhala tikukonza ena mwa mathanki omwe timasungiramo madzi. Tikuchita izi malingana ndi kuti anthu ogwiritsa ntchito madzi akuchuluka ndiye tikufuna kukhala ndi mosungira mokwanira, adatero Sonani. Malingana ndi chikalata chomwe bungweli lasindikiza, madzi azidzasiya 6 koloko mmawa ndi kuyambanso kutuluka 6 koloko madzulo ndipo tsiku loyamba kusiya ndi Lolemba pa 28 September. Potsirapo ndemanga, wapampando wa mabungwe a anthu ogwiritsa ntchito madzi mumzinda wa Lilongwe, Bentry Nkhata, wati nkhaniyi ndi yoopsa polingalira kuti anthu amadalira madzi pamoyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Iye adati madzi akasowa matenda, makamaka ammimba monga kolera ndi kamwazi, amabuka kaamba koti anthu amamwa ndi kugwiritsa ntchito madzi osatetezedwa. Nkhani yowonjezera mosungira madziyo ndi yabwino chifukwa zikutanthauza kuti mtsogolo muno madzi sazidzavutavuta koma nkhawa ili pakuti anthu azigwiritsa ntchito chiyani? Nthawi zambiri madzi akasowa kumakhala mavuto aakulu, adatero Nkhata. Unduna wa zaumoyo wati nkhaniyi isachititse anthu kutayirira ndipo wati chofunika nkusunga madzi okwanira mmakomo mwawo kapena kugwiritsa ntchito njira zotetezera madzi. Pafupifupi mdera liilonse muli alangizi a zaumoyo choncho tiyeni tonse tiziwafunsa momwe tingatetezere madzi kuti tipewe matenda ammimba panyengoyi, adatero mneneri wa unduna wa zaumoyo, Adrian Chikumbe. Nthawi zambiri madzi akasowa, anthu amadalira zitsime kapena mitsinje yomwe madzi ake amakhala ndi dothi komanso tizilombo toyambitsa matenda ammimba.
6
Boma Lati Liyamba Kusunga Chiwerengero cha Anthu Ovutikisitsa Boma lati ndi koyenera kukhala ndi nambala ya anthu onse omwe ndi ovutikitsitsa mdziko muno. Makungwa: Pano tikupereka Mtukula Pakhomo Nduna ya za chiwerengero, mapulani ndi chisamaliro cha anthu mayi Mary Clara Mkungwa anena izi lachisanu ku Zomba pomwe amayendera ofesi yowona za kalembera ya National Statistical mu mzinda wa Zomba. Iwo ati kudziwa nambala ya anthuwa kuzithandiza kuti boma lidzitha kuwafikira anthuwa moyenera ndi thandizo losiyanasiyana lokhudza miyoyo yawo. Unduna umenewu ukugwira ntchito zake bwino kwambiri chifukwa sitipeka. Mwachitsanzo panopa timapereka Mtukula Pakhomo pomwe padakali pano timapereka kwa mabanja 28, 800 ndipo tufuna tizidziwa ngati tikufikiradi anthu ovutikisitsa mMalawi muno, anatero mayi Makungwa.
14
Chipatala Cha Pirimiti Chasankhidwa Kuti Chizisunga Odwala Nthenda ya COVID-19 Chipatala cha Pirimiti chomwe ndi cha mpingo wa katolika mu dayosizi ya Zomba chasankhidwa ndi boma kuti chikhale ndi malo osungira anthu omwe angapezeke ndi kachirombo ka Coronavirus. Mkulu wa chipatalachi Sister Mary Njukuna atsimikiza za nkhaniyi poyankhula ndi Radio Maria Malawi. Iwo ati padakali pano ntchito yokonza malowa ilimkati ndipo ayamba kugwira ntchito posachedwapa, pamene boma komanso bungwe la Save the Children alonjedza kuti athandiza ndi zipangizo zogwiritsira ntchito monga mabedi, ma face mask, ma glovesi ndi zina zambiri. Pirimiti inasankhiswa ndi boma kuti ikhale Isolation Center koma padakali pano siinayambe kutero popeza zipangizo sizinafike, anatero Sister Njukuna. Iwo ati akuyemnekezera kulandira chithandizochi kuchokera ku boma komanso kwa mabungwe omwe si aboma.
6
Anatchezera Sakuthandiza Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 21 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Amuna anga adandisiya ataona kuti ndili ndi pathupi ndipo mwana atabadwa adauzidwa koma mpaka pano sadabwereko kudzaona mwana wawo. Ndikawauza za chithandizo samayankha, amangozengereza. Chomvetsa chisoni nchakuti munthune ndimakhala ndi agogo okalamba poti makolo anga onse admwalira. Ndithandizeni, ndipange bwanji? JS Mulanje Pepa JS, Apa zikuonekeratu kuti ngakhale ukuti amuna anga anthunu simunali pabanja ngakhale mumagonana mpakana kuberekerana mwana. Chimene chimachitika nthawi zambiri nchakuti atsikana akangogwa mchikondi ndipo mwamuna akangowauza kuti awakwatira, basi amaganiza kuti mwamuna ndi yemweyo basi ndipo amayamba zogonana naye ati pofuna kulimbikitsa chikondi kuti asamakaike za chikondi chawo, kumene kuli kulakwa kwakukulu. Atsikana ambiri aononga tsogolo lawo chifukwa cha mchitidwe wotere chifukwa anyamata kapena amuna ambiri ndi akamberembere, ongofuna kudzisangalatsa osalabadira za tsogolo la mnzawo. Akangomva kuti mtsikhana watenga pathupi basi, chibwenzi chimathera pomwepo. Zikatero mtsikana zako zada. Koma dziko lino lili ndi malamulo okhudza maukwati ndipo ngati wina wakuchimwitsa, ali ndi udindo woti akusamale komanso mwana. Ndiye apa usazengereze-pita ukadule chisamani kukhoti basi kuti chilungamo chioneke. Mwina amuna ena amene amakonda kuchimwitsa ana a eni akhoza kutengerapo phunziro! Akundikakamira Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 19 zakubadwa, vuto langa ndi lakuti pali mnyamata wina wake amene amandifuna koma ineyo sindimamufuna olo pangono. Iye samafuna kuti angondisiya moti pano miyezi itatu yakwana akundifunabe. Nthawi zina ndimayesetsa kuti ndimuonetse nkhope yosangalala koma mtima wanga umakana. Ndiye nditani poti ine ndili naye kale amene ndimamukonda ndi mtima wanga wonse? Chonde ndithandizeni. MT Zomba Zikomo MT, Ndithudi akadakhalapo atsikana ambiri amaganizo ngati akowa bwenzi zinthu zikoma. Atsikana ambiri masiku ano amakonda kukhala ndi zibwenzi zambirimbiri ati kuti pamapeto adzasankhepo mmodzi. Chimenecho si chikondi ndipo mapeto ake ambiri amasokonezeka, mwinanso kutenga pathupi pa mnyamata amene samamukonda. Apa iwe waonetsa kale kuti ndiwe wokhwima mmaganizo ndipo ndikufuna kuti ndikulimbikitse kuti chikondi sakakamiza. Ngati uli kale ndi mnyamata amene umamukonda ndi mtima wako wonse palinso chifukwa chanji choti uzitaya nthawi ndi wina amene ulibe naye chidwi? Komabe nthawi zina chimachitika nchoti amene umamukonda kwambiri iye alibe chikondi, angofuna kukuseweretsa ndi kukometsa mawu a pakamwa ndipo amene sukumukonda ndi amene ali ndi chikondi chozama pa iwe. Ndiye apa chimene ungachite uyambe waona kuti bwenzi lakolo ndi munthu wotani? Ndi wamakhalaidwe otani? Ndi waulemu kapena ayi; ndi yo kapena wodzilemekeza; cholinga chanu ndi chiyani pa ubwenzi wanu? Chimodzimodzi amene ukuti akukukakamira chibwenziyo, kodi ndi munthu wotani? Cholinga chake ndi chiyani? Ndi wakhalidwe kapena mvundulamadzi chabe? Ukalingalira zonsezo bwinobwino mpamene ungasankhe chochita, chifukwatu nthawi zina umatha kukakamira mtunda wopanda madzi nkusiya munthu wachikondi weniweni.
12
Pepa Gaba, Malata Chalaka bakha nkhuku siyingatole. Nkhani ya Gabadinho Mhango ndi Lucky Malata ndiyo yatinenetsa mwambiwu. Msabatayi nkhani idawawasa ndi ya anyamatawa omwenso amasewera Flames. Akamunawa akadatola chikwama pangonongono ku Joni koma ena alepheretsa. Aganyu sitinadandaule koma pena sitikumvetsa njomba yomwe yaseweredwa apa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ife sitidamvepo wosewera chigawo cha pakati atalowera kummwera kukayesa mwayi ndi Blantyre United koma pakutha pa mwezi kumva kuti wayesera mwayi ndi Big Bullets, Mighty Wanderers, Azam Tigers mpaka kufunanso kukadoda ku Evirom. Lero Gaba wapita ku Joni koma museweretseni matimu ambirimbiri. Kodi zidatero chifukwa chiyani? Kodi timu zonsezi zimamufuna pakamodzi? Kodi zimachitika mwa chiponyeponye kuti kugwere mwayi ndi komweko? Tikumva kuti matimu ena amafuna wosewera ngati Didier Drogba osati luso la Gaba. Koma izi ndi zoona? Ngati amafuna woteroyo bwanji osangopita ku Ivory Coast kukatenga Drogba? Kodi ndizotheka Gaba kusewera ngati Drogba? Gaba ndi Gaba ndipo Drogba ndi Drogba, sangafanane. Tikuganiza kuti chilipo chomwe chimachitika kuti Gaba ndi Malata azingowavinitsa. Ku Amazulu pa magemu 5 Gaba adachinya zigoli 4 ndiye apapa akufunanso chiyani? Komanso tikudabwa kuti bwanji Fam imangowonerera izi zikuchitika? Komadi Fam ndi manthu wa zamasewero mdziko muno? Kodi zidachitikapo zoterezi? Tithokoze kuti mwabwerako muli moyo. Pepani kuti mwavina moteromo koma dziwani kuti chitseko chitha kutseguka. Dekhani timu zokoma zipezeka. Osadanda posakhalitsa tidzikuwonerani pa SuperSport mukumakana ndi Messi kapena Ronaldo.
16
Khonsolo ya Zomba Isankha Anthu Olondoloza Chitukuko Wolemba: Thokozani Chapola Khonsolo ya boma la Zomba yayamba ntchito yosankha anthu oyanganira zitukuko mmadera a mafumu aakulu onse mbomalo. Polankhula pa chisankhochi mfumu yaikulu Mlumbe yalangiza adindo atsopanowa kuti apewe kukondera pa ntchito yawo. Iwo apemphanso aphungu a kunyumba ya malamulo komanso makhansala kuti azigwiritsa bwino ntchito ndalama za chitukuko zomwe amalandira ponena kuti pali zitukuko zina zomwe zimalephereka kaamba koti adindowa asokoneza ndalamazi. A ndale amayima pa chulu kulengeza kuti achita chakuti pomwe ndi zabodza. Zomwe akaupanga a ndalewa akutipha ife anthu a kumudzi zomwe zikuchititsa kuti dera langa la Zomba Changalume lisatukuke. Ananenapo kuti atsegulira police unit, bridge komanso sukulu ya sekondale zonsezo zili za bodza zenizeni palibe chomwe chamngidwa olo ndi chimodzi chomwe, inadandaula motero mfumu yaikulu Mlumbe. Polankhulapo yemwe wasankhidwa kumene pa udindowu mdera la mfumu yaikulu mwambo a Frederick Naoje alonjeza kuti agwira ntchito yawo posayangana mtundu kapena chipani. Ntchito yanga ndi yolondoloza chitukuko ndip ndiwonetsetsa kuti pasakhale tsankho koma aliyense apindule pa chitukuko chilichonse chomwe chingabwere ku dera kuno, anatero a Naoje. Chisankhochi chachitika ndi thandizo lochoka ku Local Government and Accountability Performance (LGAP).
2
Bullets yayamba ndi ukali Timu ya Big Bullets, yomwe ikuteteza chikho cha TNM Super League, yayambanso ndi ukali mndime yachiwiri ya ligiyi, kupitiriza zomwe idachita mndime yoyamba. Timuyi idachapa Mafco ku Dwangwa komwe ndime yachiwiri ya ligiyi idakakhazikitsidwa. Bullets idapambana 1-0 ndipo pano yaonjezera mapointi kufika pa 35. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Bullets ili ndi mapointi 7 pamwamba pa Azam Tigers, yomwe ili ndi mapointi 28. Koma Azam yamenya magemu ochuluka ndi imodzi kuyerekeza Bullets. Azam idalepherana mphamvu ndi Kamuzu Barracks komanso Epac FC kuti ibwerere ku Blantyre ndi mapointi awiri kuchokera ku Lilongwe. Mmodzi wa makochi a timu ya Bullets, Mabvuto Lungu, adati chomwe akufuna kuchita nkuteteza mbiri yawo yosagonja. Bullets sidagonjepo mndime yoyamba ya ligiyi. Matimu onse akonzekera zofuna kugonjetsa Bullets, ndipo akubwera mokonzeka kuti akwaniritse zomwe akufuna. Komabe tiyesetsa kuti mbiri yathu isasinthe, adatero Lungu pouza Tamvani. Mawa timuyi iswana ndi Red Lions pa Kamuzu Stadium. Mndime yoyamba Bullets idalepherana mphamvu ndi timuyi 1-1 ku Zomba. Timu yomwe Bullets imalimbirana nayo ufumu mumzinda wa Blantyre, Mighty Be Forward Wanderers, yayamba moipa mmdimeyi pamene idagonja ndi Civo United 1-0 pa Kamuzu Stadium sabata yatha. Lero Wanderers, yomwe ili ndi mapointi 26, ndipo ili pa nambala 5, pamndandanda wa momwe matimu akuchitira mligiyi, ichapana ndi Kamuzu Barracks, yomwe ili ndi mapointi 23. Masewerowo ali pa Kamuzu Stadium. Matimu ena amene ayamba molakwika ndi Dedza Young Soccer, yomwe idagonja ndi Red Lions. Mawa Young Soccer ndi Silver Strikers pa Silver Stadium. Anyamata a ku Dedzawa ali panambala 11 ndi mapointi 15. FISD Wizards nayo yayamba ndi kulira pamene idaswedwa ndi Civo 1-0 pa Kamuzu Stadium. Lero FISD itengetsana ndi Moyale ku Mzuzu ndipo mawa ikutikitana ndi Mzuni FC pabwalo lomwelo. FISD ili kunsonga kwa ligiyi ndi mapointi 9 okha. Mzuni ili panambala 15 ndi mapointi 11 pamene Moyale ili pa nambala 10 ndi mapointi 19. Mzuni ndi Moyale onse adaswedwa ndi Silver sabata yathayi. Nayo Airborne Rangers idathotholedwa nthenga nkugwa itatibulidwa ndi Blue Eagles 3-0. Lero Airborne ikulandira Epac ku Dwangwa pa Chitowe. Timuyi ili ndi mapointi 13 ndipo ili panambala 12, pamene Epac ili panambala 13 ndi mapointi 12. Lero maso akhale pa Kamuzu Stadium ngati Bullets ipitirire kuchita bwino pamene ikuswana ndi mikango ya ku Zomba, Red Lions.
16
Zipani zikufuna machawi pa chisankho Zipani zandale zati bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lichititse msanga chisankho chobwereza kudera la kummwera cha ku mmawa kwa Lilongwe kuti anthu akuderari akhale ndi phungu owayimirira ku Nyumba ya Malamulo. Izi zikutsatira chigamulo cha bwalo lalikulu la apilo kuti chisankho cha phungu wa deralo chichitikenso litaunika dandaulo la yemwe ankayimirira chipani cha Malawi Congress Party (MCP) Ulemu Msungama kuti chisankhocho sichidayende bwino. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Sipikala wa Nyumba ya Malamulo Richard Msowoya watsimikiza kuti kutsatira chigamulochi, deralo tsopano lilibe phungu. Bwalo lomwe lagamula ndi lalikulu mdziko muno kutanthauza kuti kulibenso komwe nkhaniyo ingalowere. Apa, zikutanthauza kuti kuderako kulibe phungu nchifukwa chake kuchitikenso chisankho, adatero Msowoya. Pachisankho cha pa 20 May, 204, bungwe la Mec lidalengeza kuti Bentley Namasasu yemwe ankayimira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndiye adapambana koma Msungama adakamangala kubwalo la milandu za chigamulochi. Wachiwiri kwa mlembi wa chipani cha MCP Eisenhower Mkaka adati bungwe la MEC lisakoke nkhaniyo koma kuthamangitsa chisankhochi kuti anthu a mderalo akhale ndi phungu owayimilira ku Nyumba ya Malamulo. Mneneri wa chipani cha Peoples Party (PP) Noah Chimpeni adati MEC iyambirepotu kusakasaka ndalama zopangitsira chisankhochi mawu omwe adagwirizana ndi a mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga. Apa MEC iyambiretu kusakasaka ndalama zopangitsira chisankhochi munthawi yake kuti ikwaniritse ntchito yake malingana ndi malamulo, adatero Ndanga. Chikalata chomwe MEC idatulutsa Lachitatu, chidati pali z ofunika kutsata chisankhochi chisadachitike. Aka kakhala koyamba kuti chisankho cha mtundu uwu chichitike mumbiri ya Malawi. Motero, tikuyenera kuunika bwino chigamulochi ndi malamulo oyendetsera chisankho kuti akutinji, chidatero chikalatacho. Mneneri wa bungwelo Sangwani Mwafulirwa adati malamulo sanena nthawi yeniyeni yofunika kutenga kuti chisankho chotere chichitike ndipo mmalo mwake akhoza kugwiritsa ntchito lamulo lomwe limati pasadathe masiku 60. Mwafulirwa adatinso mwa zina, bungweri likufunika kuti lisake ndalama zopangitsira chisankhochi chifukwa mundondomeko ya chuma ya 2016 mpaka 2017 mulibe pologalamu yachisankhochi.
11
Ambwandira msilikali ku Salima Apolisi a chigawo chapakati abatha msilikali wa nkhondo ndi anthu ena awiri powaganizira kuti adapezeka ndi chamba popanda chilolezo. Msilikaliyu, Alex Kanjanga wa zaka 23 wagwidwa ndi majumbo 16 a chamba pachipikisheni cha polisi pa Thavite mboma la Salima. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mneneri wa polisi mchigawo chapakati Noriet ChihanaChimala watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati tsiku lomwe msilikaliyu adagwidwa pa 3 April 2018, apolisiwo adagwiranso Lawrent Medson Tambala wa zaka 30 atamupeza ndi majumbo 11 achamba komanso Mary Mwambane wa zaka 28 atamupeza ndi katundu yemwe akuganiziridwa kuti adabedwa. Chimala wati apolisi adakhazikitsa malo achipikisheni adzidzidzi pa Thavite ndipo katundu yenseyo adapezeka pachipikishenicho ndipo anthu onsewa akawonekera ku khoti kafukufuku akatha. Kanjanga yemwe akugwira ntchito ku Engineers Battalion yomwe ili mboma la Kasungu amachokera mmudzi mwa Msongola kwa mfumu Kwataine mboma la Ntcheu. Tidamupezanso ndi njere za chamba, adatero Chimala. Iye adati pamalopo, adagwiranso Tambala akuchokera ku Nkhotakota ndipo iye adabisa majumbo achambawo mchikwama chomwe amayenda nacho paulendowo. Malingana ndi Chimala, Tambala amachokera mmudzi mwa Kapangalika, kwa mfumu Khongoni mboma la Lilongwe ndipo naye akuyembekezera kafukufuku wapolisi kuti akawonekere ku khoti. Awiriwa awatsegulira mlandu wopezeka ndi chamba popanda chilolezo chilichonse. Pachipikisheni china patsikulo, apolisi adapeza zipangizo zowotchererera mchikwama cha Mwambane koma iye adalephera kufotokoza komwe adatenga zipangizozo ndipo apolisiwo adamutengera ku polisi ya Salima. Ndi ntchito yapolisi kulondoloza komwe katundu wachokera, ngati munthu akulephera kuonetsa malisiti ogulira kapena kufotokoza bwino komwe watenga katundu yemwe alinaye, amayenera kutengedwa kuti akalongosole bwino za katunduyo, watero Chimala. Mwambane amachokera mmudzi mwa Mbuna, kwa mfumu Kanyenda mboma la Nkhotakota ndipo akuyembekezeka kudzayankha mlandu wopezeka ndi katundu oganiziridwa kuti adabedwa kafukufuku wapolisi akatha.
15
Papa Apempha Madotolo Kuti Akhale Okhulupirika Wolemba: Sylvester Kasitomu Papa Francisko lachisanu lapitali wapempha madotolo kuti apewe mchitidwe wothandizira odwala kuti amwalire mwamsanga powapatsa mankhwala olakwika, ponena kuti kutero ndikuonetsa khalidwe loipa. Papayu wayankhula izi pa nkumano wake ndi ma madotolo omwe anakamuchezera kulikulu la Mpingowu ku Vatican. Iye wati mchitidwe wothandizira odwala kuti amwalire mwamsanga maka kubaya kapena kupereka mankhwala olakwika ndi wonyazitsa ulemerero wa munthu womwe ndi tempile ya mulungu. Mtsogoleri wa mpingo wakatolikayu mwazina watsindika za kufunika kolemekeza moyo wa munthu wina aliyense maka pozindikira kuti Mulungu ndiye mwini moyo ndipo kuti palibe munthu yemwe ali ndi mphamvu yothandizira kuti munthu amene akudwala amwalire mwa msanga chifukwa chakukula kwa matenda komanso palibe yemwe ali ndi mphamvu yochotsa moyo wa munthu. Iye wati ndi Mulungu yekha yemwe amapereka moyo ndipo ndi yemweyo amatenganso moyo pa nthawi yake. Papayu wapitiriza kunena kuti kusamalira wodwala sikungopereka mankhwala kokha komanso kumvetsera ndi chidwi nkhawa za wodwala aliyense payekhapayekha. Iye wakumbutsa madotolowo kuti nthawi zonse ayenera kukumbukira malamulo a ntchito yawoya udotolo. Pamwambowo panali madotolo ochiza matenda osiyanasiyana okwana 350 a mdziko la Italy.
6
Magufuli Wati Chiwerengero Cha Atsikana Otenga Mimba Chakwera Kwambiri Ku Tanzania Wolemba: Sylvester Kasitomu 9768" src="http://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/10/magufuli.jpg" alt="" width="537" height="358" />Wauza apolisi amange aliyense opeereka mimba kwa atsikana apasukulu-Magufuli President wa dziko la Tanzania a John Pombe Magufuli wati ndi wokhudzidwa kaamba kakukula kwa chiwerengero cha atsikana omwe akutenga pathupi ali pa sukulu chomwe akuti chafika pa 2 hundred 29 mu chigawo chimodzi chokha cha dzikolo. President Magufuli wati ndi zomvetsa chisoni kwambiri kuti azibambo ena sakuona kufunika kolimbikitsa maphunziro a tsikana mdzikolo ndipo mmalo mwake akukhala patsogolo powononga tsogolo lawo. Malinga ndi BBC, Magufuli wadzudzula azibambo omwe akupezeka ku chigawo cha kuzambwe kwa dzikolo kuti ndi omwe akukhala patsogolo kwambiri kumagonana ndi ansungwana omwe ali msukulu zosiyanasiayana mdzikolo. Pamenepa President Magufuli walamula asilikali adzikolo kuti amange azibambo onse omwe apezeke olakwa popereka mimba kwa atsikana apasakulu. Dziko la Tanzania limapereka maphunziro aulere kwa atsikana opezeka msukulu zosiyanasiayana mdzikolo.
14
Bonongwe Wadzudzula Boma Kamba Kosaika Chidwi pa Ulimi Mmodzi mwa anthu omwe amalankhulapo pa nkhani zokhudza ulimi mdziko muno Mathius Bonongwe wadzudzula boma kaamba kosayika chidwi chokwanira pa nkhani za ulimi mdziko muno. Bonongwe walankhula izi pothilirapo ndemanga pa ndondomeko ya za chuma ya 2020/2021 yomwe nduna ya za chuma a Joseph Mwanamvekha anapereka ku nyumba ya malamulo lachisanu pa 12 June 2020. Akuti boma silinaganizire alimi ngati awa Mu ndondomekoyo boma layika 194.9 Billion kwacha ku gawo la za ulimi ndipo mwa ndalamazi, 48.8 Billion kwacha ndi zogulira chimanga, kuyendetsera ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya FISP komanso kulimbana ndi tizilombo towononga mbewu. Pamenepa Bonongwe wati ndalama zomwe boma layika ku gawo la za ulimi ndi zochepa poyerekeza ndi mavuto omwe alimi mdziko muno akukumana nawo. Boma limayenera liyangane kwambiri mavuto amene ali mmidzi kamba koti mMalawi muno anthu ambiri ndi osauka koma atenga anthu ochepa chabe kuti apindule mu ndondomeko imeneyi ya feteleza sabuside, anatero a Bonongwe. Iwo apemphanso unduna wa zaulimi kuti uyike ndondomeko zokhwima ndi cholinga choti mchitidwe ogula ma kuponi kwa alimi uchepe kamba koti anthu omwe amagawa ma kuponi ndi omwewonso amapita kumakawagula alimi ovutika makuponi mmidzimo zomwe akuti ndi zochititsa kutu umphawi usathe mdziko muno.
4
A ku Mozambique akulembetsa mavoti Mwafulirwa: Ndi mlandu waukulu Nzika zina za mdziko la Mozambique zikulembetsa nawo mkaundula wa mavoti ku Dedza popofuna kuti zidzavote nawo pa chisankho cha magawo atatu chomwe chilipo pa 20 May, 2014. Mneneri wa polisi ku Dedza Edward Kabango wati panopa apolisi anjatapo kale nzika imodzi ya dzikokolo, Edward Tenganibwino, wa zaka 28, wochokera mmudzi mwa Golongozo yemwe amafuna kulembetsa mkaundulayu mwachinyengo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kabango wati Tenganibwino adanamiza akalaliki ochita kalemberayu kuti ndi Mmalawi ndipo amachokera mmudzi mwa Katsekaminga ku Dedzako koma akalalikiwo adamuzindikira msanga ndi kumuneneza kupolisi. Bungwe logwira ntchito zophunzitsa anthu la National Initiative for Civic Education (Nice) lati nzika zambiri za ku Mozambique zalowa mdziko muno kufuna kudzalembetsa nawo koma zina zidabwezedwa akalaliki a kalemberayu atazitulukira. Mkulu woyendetsa za maphunziro kubungweli, Patrick Siwinda, wauza Tamvani kuti asanu agwidwapo kale koma ena akadali zungulizunguli mbomalo kuyesayesa kuti alembetse mkaundulayu. Iye wati ambiri mwa anthuwa akuti amafuna ziphaso zoponyera voti ndi cholinga choti azidzatha kutenga ngongole zotukulira ulimi wa kachewere kumabanki a mdziko muno. Siwinda wati ambiri mwa anthu achinyengowa akumagwiritsa ntchito ziphaso zolowera ndi kutuluka mdziko za Malawi komanso ziphaso zoponyera voti za mndondomeko ya chisankho cha chaka cha 2009 ngati umboni kuti awalembe. Pa 2 November, bambo wina wa ku Mozambique adabwera ndi chiphaso cha ku Malawi kuti alembetse koma adabwezedwa, adatero Siwinda. Iye adati nthumwi za bungweli zati mchitidwewu ukuoneka mmalo olembetserako 13 a mdera la Bembeke. Siwinda wati madera omwe akukhudzidwa ndi mchitidwewu ndi Katsekaminga CDSS, Mazanjala, sukulu zapulayimale za Kapesi ndi Magaleta, sukulu zasekondale za Umbwi, Msambiro, Dedza Muslim Jamat, sukulu ya asungwana Achisilamu ya Dedza, Dedza CCAP, Dedza LEA, Dedza Community Hall ndi mudzi wa Dauya. Bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) lati mchitidwe wolembetsa kapena kuthandizira munthu yemwe sali woyenera kulembetsa kuti alembetse ndi mlandu waukulu ndipo wolakwa akhoza kunjatidwa. Wofalitsa nkhani mbungweli Sangwani Mwafulira wati pofuna kuchepetsa mchitidwewu, zipani ndi mabungwe azisankha oyanganira ndondomeko ya chisankho (monitors) kuchokera mdera lomwe kukuchitikira ntchitoyi kuti azitha kuzindikira anthu ofuna kuchita zachinyengo. Ndi bwino kusankha nthumwi za mdera lomwe kukugwiridwira ntchitoyi chifukwa sizivuta kuzindikira anthu. Komanso anthu akuyenera kuzindikira kuti kuperekera umboni wabodza kuti munthu ndi Mmalawi pomwe si Mmalawi woyenera kulembetsa mkaundula ndi mlandu waukulu woti munthu akhoza kulipira ndalama zokwana K500, 000 kapena kukakhala kundende zaka ziwiri, watero Mwafulirwa.
11
Mdima wanyanya mmakhonsolo Zomwe anena a makhonsolo a mizinda ya Lilongwe Blantyre ndi Mzuzu zikusonyeza kuti vuto la mdima mmisewu ya mizindayi litenga nthawi kuti lithe kaamba koti, ngakhale akuyesetsa kuti akonze zinthu, anthu ena akubwezeretsa zinthu mmbuyo poononga dala zipangizo za magetsi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Escom in free-for-all fuel scam Khonsolo ya mzinda wa Lilongwe yati vuto lalikulu ndi nthawi yomwe kampani ya magetsi ya Escom imatenga kuti ikalumikize magetsi ntchito yozika mapolo ikatha. Mneneri wa khonsoloyi, Tamala Chafunya, wati khonsolo ikamaliza kuzika mapolo nkulumikiza nthambo za magetsi, zimakhala mmanja mwa Escom kuti idzamalizitse ntchitoyo polumikiza magetsiwo. Gawo lathu pa ntchito imeneyo idachitika ndipo kuchedwaku ndi kampani ya Escom. Khonsolo idalipira kale ndalama zolumikizira magetsi koma zaka zikungopita ngakhale kuti timayesetsa kutokosako, adatero Chafunya pouza Tamvani pa nkhani ya vuto la mdima mmisewu yambiri mumzindawu. Chafunya adati kuchedwaku kumapereka danga kwa anthu amaganizo olakwika kuti aziononga mapolowo ndipo chipsinjo chimagweranso pamsana pa khonsolo kukonzanso mapolowo. Mneneri wa kampani ya Escom Kitty Chingota adavomereza kuti khonsoloyi idalipiradi ndalama zolumikizira magetsi koma akatswiri ake atakayendera malo ofunika kulumikiza magetsiwo adapeza zolakwika zambiri. Iye adati pofuna kupewa ngozi za magetsi, kampaniyi idalangiza khonsoloyi kuti ikonze molakwikamo magetsewo asadabwere koma palibe chomwe achitapo. Mmalo ena mapolo adadutsa mmunsi mwenimweni mwa nthambo zathu za magetsi ndipo malamulo a Escom salola kulumikiza magetsi mmalo oterewa. Mmalo ena mapolo adatalikirana kwambiri chifukwa ena adagwetsedwa ndi anthu opotoka maganizo ndiye mpovuta kulumikiza magetsi mmalo oterewa, adatero Chingota. Koma Chafunya adati nthawi zambiri mapolowo akawonongedwa kumakhala kovuta kuwabwezeretsa chifukwa ndalama zomwe zimalowa nzochuluka kwambiri. Kukonza polo ya simenti imodzi yokha, kuyambira kuwumba mpaka kukaizika, imatenga ndalama zokwana K400 000 ndiye muwerengere kuti msewu umodzi umadya ndalama zingati za mapolo, nanga anthu akawononga kuti tikabwezeretse ndiye kuti zitukuko zina ziimiratutu, adatero Chafunya. Mumzinda wa Blantyre nkhani ndi yokhayokhayi; mmisewu yambiri ndi mdima wokhawokha kaamba koti mapolo ambiri adagwtsedwa ndi akuba, zomwe zikuchititsa kuti ena azichitidwa chipongwe chifukwa cha kusowa kwa kuwala usiku. Mneneri wa khonsoloyi Anthony Kasunda adati nzoona kuti mumzindawu muli vuto la magetsi mmbali mwa misewu chifukwa ambanda adaba zipangizo pamapolo. Ili ndi vuto lalikulu chifukwa anthu amayenda mwamantha usiku. Pamene khonsolo ikuyesetsa kuti ngati mzinda tipite patsogolo ndi chitukuko, anthu ena amaganizo olakwika akubwezeretsa chitukuko mmbuyo pomaba zipangizo ngati zothandizira magetsi a pansewu, adatero Kasunda. Iye adati ngati khonsolo akupempha a makhoti kuti pamene munthu wagwidwa ndi katundu wa khonsolo, ameneyo azilandira chilango chokhwima kuti asadzabwerezenso, komanso kuti ena atengerepo phunziro. Komanso tikufuna tipeze njira imene tingachite kuti zipangizo za magetsi zisamabedwe monga pogwiritsa ntchito magetsi oyendera mphamva ya dzuwa ija pa Chingerezi amati solar powered system. Pempho lathu ngati khonsolo ndilakuti tiyeni tonse titengepo gawo poteteza katundu kapena zipangizo zimene khonsolo imaika mmalo osiyanasiyana kuti zitumikire anthu okhala mumzinda wa Blantyre. Isakhale ntchito ya khonsolo yokha koma tonse, adatero Kasunda. Namonso mumzinda wa Mzuzu nyimbo ndi yokhayokhayoambanda ali kaliriki kuononga zida za magetsi mmbali mwa misewu moti malo ambiri mdima uli bii usiku ukagwa. Zinthu zidayamba kusonya pamene magetsi oyamba mmisewu ya mmataunishipi monga Zolozolo, Chimaliro, Katawa ndi Msongwe adayatsidwa mu 2012 ndi 2013, koma pano zinthu zabwerera mmbuyo chifukwa anthu ena adayamba kuba nthambo za magetsiwa. Wogwirizira mpando wa mkulu wa khonsoloyi, Victor Masina, adati ili ndi vuto lalikulu ndithu moti pano a khonsoloyi akufuna ndalama zosachepera K3.5 miliyoni kuti akonzenso zipangizo zoonongekazo monga ma transformer ndi mapolo ogwetsedwa ndi galimoto zikaphuluza msewu.
2
HRDC Yapempha Boma Kuti Liyimitse Chiganizo cha Lockdown Bungwe lomenyera ufulu wa anthu mdziko muno la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati boma liyimitse kaye ganizo lake loletsa anthu kuyendayenda ndi kuchita ntchito zawo kapena kuti Lockdown pachingerezi kuti lipereke kaye tsatanetsatane wa mmene lithandizire anthu mu nthawiyi. Wachenjeza boma-Trapence Boma, lidalengeza kuti kuyambira pakati pa usiku wa loweruka pa 18 mwezi uno mpaka pakati pa usiku wa pa 9 May chaka chino anthu asayendeyende,omwe ndi masiku 21,pofuna kuchepetsa kufala kwa nthenda ya COVID-19. Polankhula pa msonkhano wa atolankhani lero mmawa, wapampando wa bungweli Gift Trapence,wati bungweli lawuza kale maloya ake kuti apite ku bwalo la milandu kuti lilowelerepo pa nkhaniyi ponena kuti boma ladya mfulumira polengeza za ganizoli lisadaike mfundo zothandizira anthu osauka pa nthawi yosayendayendayi.
11
ECM Yati Mapemphero a Sabata Yoyera Achitika Likulu la mpingo wakatolika mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM) lati miyambo yonse ya mapemphero mu Sabata Yoyera mu nyengo ya Lent ichitika potsatira dongosolo loti pa miyamboyi pasamakhale anthu oposera zana limodzi (100). Alemba chikalatacho-Bambo Saindi A kulikulu la mpingowu ku Episcopal Comference Of Malawi ECM ndi omwe anena izi kudzera mu chikalata chomwe atulutsa ndipo chasainidwa ndi mlembi wamkulu wa bungwe la maepiskopi a mpingowu mdziko muno, bambo Henry Saindi.
13
Chipwirikiti ku Malawi Kuphwanya ndi kusalemekeza malamulo kwayala nthenje mdziko muno. Anthu akungopha ngati akupha nkhuku, kugwiririra, kuononga ngakhalenso kuyatsa katundu. Sabata yatha, anthu awiri adakhapidwa ndi kuphedwa ku Neno powaganizira kuti ndi mfiti ndipo sipanathe nthawi pomwe anthu enanso adaphedwa kwa Chitukula ku Lilongwe pamkangano wa malo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Naye adagendewa: Mayaya Izi zili apo, Akhristu ndi Asilamu adalikitana ku Balaka pomwe sukulu ya mpingo wa Anglican ya Mmanga idaletsa atsikana kuvala mipango yotchinga kumutu potsatira chipembedzo cha Chisilamu. Ndipo izi zili mkamwamkamwa, msilikali wina adapha asilikali anzake awiri ku Ntcheu ndipo naye adaomberedwanso ndi apolisi a kuusilikali. Ndipo si kale pomwe nyumba 21 zidaotchedwa ku Nkhata Bay ndipo anthu 4 adaphedwa pa zipolowe. Si kale pomwe anthu otsatira chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) adagenda ndi kuvulaza mmodzi mwa omenyera ufulu wa anthu Billy Mayaya pa zionetsero zimene bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) limachita pofuna kukakamiza mkulu wa bungwe la Malawi E;ectoral Commission (MEC) Jane Ansah atule pansi udindo. Ndipo wapolisi wina adaphedwa ku Nsundwe mboma la Lilongwe pomwenso apolisi ena akuwaganizira kuti adagwirira ndi kulanga amayi ndi asungwana ena. Nako ku Karonga, pofuna kusatsalira pa mpungwepungwe wabukawu, kudali anthu ena kuvula amayi ndi atsikana ngati avala mathalauza ndi siketi zazifupi mbomalo. Izi zikuchitika ngakhale lamulo loyendetsera dziko lino limati kuli ufulu wa kavalidwe. Ndipo amabungwe oteteza ufulu wa anthu monga Foundation for Community Support Services (Focus) adzudzula mchitidwewu ndipo apempha apolisi kuti atsekere mchitokosi wachinyamata aliyense amene akuvula amayi. Pakadalipano mkulu wa apolisi mbomalo Sam Nkhwazi wati sadamangeko munthu pokhudzana ndi nkhaniyi. Malinga ndi Mfumu Malema 2 ya mboma la Karonga, iwo adakhazikitsa malamulo woti ana a sukulu (anyamata ndi atsikana) asamapezeke kunyanja chifukwa zinthu zidafika poipa ndipo anawa amachita zolaula kunyanjako. Iye adati atakhala pansi adakhazikitsa gulu lomakayendera kunyanjako ndi kumagwira tiana tomwe amatipeza komanso adapeza galimoto yomwe idalengezetsa Lachisanu lapitalo kuti anawa asapezeke kunyanja ndipo akangopezeka agwidwa. Tidachita izi chifukwa anawa adaonjeza kuthawa kusukulu nkumabwera kunyanja kukamwa mowa ndi kugona ndi amuna. Chidatikhudza kwambiri ndi choti mwana wina wa zaka 13 adamwetsedwa mowa patsiku la anakubala ndi kugonedwa ndi anyamata ambiri. Anawa amakhala oti athawa msukulu, adatero Malema. Koma iye adakanitsitsa kuti adakhazikitsa malamulo oti amayi asamavale mathalauza ndi siketi zazifupi mbomalo. Izo akupanga ndi akabaza kumsika ndipo ife sizikutikhudza, adatero iye. Pomwe mayi wina yemwe adaona mnzake akuvulidwa, Christobel Shaba, adati zikuchitika mbomalo ndi zoopsa ndipo amayi akukhala ndi mantha akulu. Polankhulapo pa chipwirikiti chomwe chikuchitikachi, mphunzitsi wa ufulu wa anthu pasukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia George Phiri adati zonsezi zikungosonyeza kuti utsogoleri wa dziko lino walephera. Phiri adatinso nzokhumudwitsa kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika sakuonetsa chidwi chofuna kuthetsa mavuto mdziko muno ndipo wangoti duuu! Tangoganizani, wamkulu wa apolisi adabwera poyera nkunena kuti apolisi alibe kuthekera kopereka chitetezo mdziko muno, kodi mtsogoleri wa dziko lino adachitapo chiyani izi zitanenedwa? Kodi mtsogoleriyu akuona zikuchitikazi? Nanga bwanji wangoti duuu! ndipo palibe chomwe akuchitapo? adatero Phiri. Koma nduna ya zofalitsa nkhani Mark Botomani idatsutsa kwa mtu wa galu kuti utsogoleri wa dziko lino walephera. Botomani adati ngakhale akugwirizana ndi zoti zikuchitika mdziko muno ndipotsa mantha komanso zoziziritsa thupi chifukwa anthu akungotengera malamulo mmanja mwawo, koma mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika akuyesetsa kukonza zinthu kuti zibwelere mchimake.
15
Anatchezera Akundifunanso Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Telemu yotsiriza ya Fomu 3 ndidapalana ubwenzi ndi mtsikana wina pasukulu yathu ku Mulanje. Koma tikuyandikira kulemba mayeso a Fomu 4, bwenzi langalo lidanditumizira uthenga palamya kundiuza kuti chibwenzi chatha chifukwa sindine mwamuna. Iye adaonjezera kuti pomwe ankandilola nkuti ali ndi chibwenzi china. Izitu zidandiwawa kwambiri chifukwa tinkalonjezana kuti tidzakwatirana. Chondivuta nchoti atangomva kuti ndayamba ntchito adayambanso kundiimbira foni nkumandiuzakuti chikondi chake pa ine sichidathe. Ndichite chiyani pamenepa? DF, Mulanje. DF, Nthawi zonse ndimalangiza amene ali msukulu kuti ayenera kupewa mchitidwe wokhala ndi zibwenzi. Izi ndimanena makamaka chifukwa zimasokoneza maphunziro. Taonani apa mukuti mtima wanu udasweka mutayandikira kulemba mayeso a Fomu 4 mkaziyo atathetsa chibwenzi. Sindikukaika konse kuti izi zidakhudza momwe mudakhonzera mayeso a Fomu 4. Simukadakhonza kuposa momwe mudachitira mutakhumudwa ndi kuthetsa kwa chibwenzi kumene mudakumana nako. Tsono funso lanu mukuti muchitenji? Langizo langa ndi loti, musataye nthawi ndi mtsikanayo chifukwa waonetseratu kuti ndi wamadyeramphoto komanso ali ndi mtima wa chimasomaso. Adakuuzani kuti adakulolani ngakhale adali ndi chibwenzi china panthawiyo. Tsono, muli ndi chitsimikizo chotani kuti mukadzakwatirana naye sakapezanso mwamuna wina wamseri? Taonani adati inu si mwamuna pomwe amathetsa chibwenzi. Tsopano akukusakani chifukwa mwapeza ntchito. Kodi mutakwatirana naye, ntchitoyo nkutha ameneyo sadzakuthawani? Samalani naye mkazi wa chimasomaso! Zikomo Gogo, Ndidapanga chibwenzi ndi mkazi wina yemwe ali ndi mwana mmodzi. Chithereni ukwati wake woyamba, patha chaka ndi miyezi ingapo. Mgwirizano wathu ndi woti tidzamange banja. Koma tsiku lina ndikuchokera kuntchito ndidangolowa mnyumba osagogoda ndipo ndidamupeza akulankhula pafoni. Adadzidzimuka nkudula foniyo koma nditamulanda ndidaona kuti amalankhula ndi mwamuna wake woyambayo. Ndidamuuziratu kuti chibwenzi chatha ndipo azipita kwawo. Adagwada nkulira kunena kuti ndimukhululukire sadzayambiranso. Iye adati mwamunayo amaimba kufuna kudziwa njira yopita kwa mayi anga kuti akaone mwana. Ndichitenji, mundiyankhe pafoni pomwepa. G, Lilongwe Zikomo a G, Poyamba, ndikukumbutseni kuti ndi zovuta kuti aliyense amene wandifunsa ndi zimuyankhanso pafoni. Izi zili choncho chifukwa ndimalandira mafunso ambiri choncho kuti aliyense ndizimuyankha pafoni sizingatheke. Palinso ena amafulasha, tsono ine kuti ndiziimbira aliyense amene akufulasha, ndiwo ndigula? Tsono kubwera ku funso lanu, poyamba ndikudabwa kuti mukukhala bwanji ndi mkazi amene simunalongosole zaukwati? Kodi mutapatsana mimba, sipakhala mavuto ena? Izi zili choncho, mudziwe kuti mkaziyo akunama kuti amapereka njira ya komwe mayi akukhala kwa mwamuna wake wakale. Tiziti nthawi yonse adali limodzi, mpaka mwana mwamunayo samadziwa pakhomo pa mayi a mkazi wake? Akadakhala kuti amakambirana za njira bwanji adadula foniyo? Samalani. Ofuna mabanja Ndikufuna mkazi koma akhale wa zaka 17. Pepani sindiika nambala yanu chifukwa mwati mukufuna mkazi wa zaka 17. Ameneyo si mkazi koma mtsikana ndipo malamulo a dziko lino akuletsa kuti ana osakwana zaka 18 asamakwatiwe. Ndine mwamuna wa zaka 28 ndipo ndili pantchito ku Lilongwe. Ndikufuna mkazi wopanga naye ubwenzi mpaka banja.
12
Kumisasa kwabuka matenda a maso, mphere Nyumba zawo zudagwa, minda idakokoloka ndipo katundu wambiri kuphatikizapo ziweto zidanka ndi madzi osefukira. Anthu miyandamiyanda, maka akuchigwa cha Shire, adathawira kumtunda kuti apulumutse miyoyo yawo, koma komwe adathawirako nakonso kwaopsakwagwa mliri wa matenda amaso ndi mphere mmisasa ya ku Nsanje ndi Chikwawa. Mneneri wa unduna wa zaumoyo Henry Chimbali watsimikiza izi, koma wati unduna wake ukufufuzabe za anthu amene akhudzidwa ndi matendawa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Msasa wa Bitirinyu kwa T/A Nyachikadza mboma la Nsanje ndiwo wakhudzidwa kwambiri ndi matenda a mphere pamene misasa ya Bereu ndi Kalima kwa T/A Maseya mboma la Chikwawa ndiwo watekeseka ndi matenda a maso. Msasa wa Bitirinyu ukusunga anthu pafupifupi 6 000. Pamene Tamvani idazungulira pamsasa wa Bereu ambiri adali koyenda koma mayi Elube Jeke wa mmudzi mwa Chikutireni adali pamalopo akutonthoza ana ake. Mwana wamngonoyu wayamba kumene [kudwala maso] pamene wamkuluyu ndiye adayamba masiku atatu apitawo. Sakupeza bwino, maso atupa komanso akumadandaula kuti akumva kuwawa. Akapeza mtendere ndiye kuti wagona. Sitinalandirepo thandizo chiyambireni matendawa, zomwe zachititsa kuti pakhale kupatsirana, adatero Jeke uku akufunditsa mwana wokulirapoyo amene ati sakupita kusukulu chifukwa cha mavutowo. Mavuto sakukata kwa Jeke chifukwa pamene amabwera pamsasawo nkuti nyumba yake itagwa ndi madzi a mvula ndipo katundu wake limodzi ndi munda zidakokoloka. Poti athawitse moyo, lero wakumana nazonso pamene matenda agwera ana ake. Sindingakhalenso ndi lingaliro lobwerera kumudzi chifukwa kumenekonso ndiye sikuli bwino. Madzi sadaphwere, adatero Jeke, kusowa mtengo wogwira. Mkulu woyanganira za umoyo pa msasawu, Rodrick Rivekwa, akutsimikiza za matendawa ndipo wati pofika Lachisanu pa 13 March nkuti anthu 15 atapezeka ndi matendawa. Iye adatinso anthu 10 ndiwo apezeka ndi mphere pamsasawo. Koma boma lachitapo machawi pofuna kuthana ndi vutoli. Adatitumizira mankhwala moti anthu onse amene akudwala maso ndi mphere alandira thandizo lachipatala, adatero Rivekwa. Iye adati kuchulukana kwa anthu pamsasa wa Bereu lingakhale vuto lina lomwe ladzeetsa mavutowo. Tili ndi anthu 1 024, koma malo ogona adali ochepa. Komanso kupeza madzi ndi aukhondo lidali vuto lina. Panopa bolako chifukwa atipatsa zipangizo zosungiramo madzi komanso matenti adationjezera, adatero Rivekwa. Nakonso kumsasa wa Kalima mavuto a matenda amaso sadasiye, malinga ndi John Yobe wa mmudzi mwa Kalima kwa T/A Maseya mbomalo. Yobe adathawa mmudzi mwake ndi kukakhala nawo kumsasawo. Iye akuti adali ndi ziweto monga nkhuku, mbuzi ndi nkhumba zomwe zidatengedwa ndi madzi. Pokakhala pamsasawu akuti amati ndi chisomo ndipo ankaganiza kuti wapulumuka, koma mwadzidzidzi adadabwa kuona ana ake asanu ndi mmodzi atagwidwa ndi nthenda ya maso. Yobe akuti pano zinthu zasinthako chifukwa thandizo la chipatala lidafika mofulumira ndipo nthendayi ati sidafale kwambiri monga amaopera. Malinga ndi nyakwawa Katandika, matendawa adza chifukwa chothithikana pamsasawu, zomwe anthuwa akhala akudandaula. Koma Chimbali adati unduna wake wafika kale mmalowa kukapereka thandizo la chipatala ndipo zinthu zikusintha. Talandiradi malipoti okhudza matenda a maso. Ambiri amene akhudzidwa ndi matendawa ndi ana. Msasa wa Bitirinyu kwa T/A Nyachikadza ndiko talandira malipotiwa. Koma zinthu zasintha chifukwa thandizo lapitako, adatero Chimbali. Iye adatinso mavutowa amveka mmaboma a Chikwawa ndi Nsanje kokha pamene mmaboma ena monga Thyolo ndi Mulanje komanso ku Balaka kulibe nkhaniyo. Mneneriyo adatinso matenda otsekula mmimba abukanso mmisasayi koma unduna wawo wapereka kale thandizo.
6
Anatchezera Sagona mnyumba Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndili ndi zaka 20 ndipo amuna anga sagona mnyumba ndiye chonde, ndithandizeni. Akuti ndikawauza ankhonswe banja langa litha. Ukwati tapanga chaka chatha. Ndine A Blantyre Zikomo A, Mwamuna wakoyo ngwachibwana zedi! Mwangokwatirana kumene ndipo ukuti sagona mnyumba, ndiye amakagona kuti? Ukapanda kusamala naye ameneyo akugwetsa mmavuto aakulu-ndikunenatu matenda oopsa, kuphatikizapo HIV/Edzi. Ngati wayamba kale kunena kuti ukakanena kwa ankhoswe banja lithapo ndiye kuti iye za banja alibe nazo ntchito koma kusangalatsa chilakolako cha thupi lake basi. Ndiye usazengerezepo apa, pita kaitule nkhaniyi kwa ankhoswe, umve zimene anene. Ngati akufuna kuti banjali lithe, lithe basi. Mwamuna wachimasomaso ndi woopsa kwambiri ndipo safunika kumusekerera.
12
Kuchoka kwa Phoya kutisokoneza, atero ena Anthu mmadera osiyanasiyana msabatayi ati kuchoka kwa phungu wa chipani cholamula cha DPP mdera la ku mmawa mboma la Blantyre, Henry Phoya kwasiya mafunso ambiri mmitu yawo zomwe ati zingawasokoneze podzavota mchaka cha 2014. Anthuwa ati kuchokako kukusonyeza kuti kuchipani cholamula kwavunda zomwe ati zawachititsa kakasi kuti aone komwe angadzaponye voti yawo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma katswiri wa za mbiri ya kale, Chijere Chirwa wati andale amachokachoka mzipani zawo kapena kuyambitsa chipani chawo kotero izi sizikuyenera kusokoneza anthu. Iye adati kuchoka kwa Phoya ukhale mwayi wa chipani cha DPP kuti apeze anthu ena atsopano omwe angamange chipanicho. Phoya Lachiwiri adalengeza kuti walowa chipani cha MCP. Iye adalengeza izi pa msonkhano wa atolankhani omwe udachitikira kunyumba ya mtsogoleri wa chipanichi, John Tembo. Pomwe Phoya amalengeza nkhaniyi, wachiwiri kwa mneneri wa chipani cha UDF, Ken Msonda adalengeza kuti wasiya ndale ndipo akukalera ana. Mmodzi mwa anthuwo, Florence Kamvamtope wa mmudzi mwa Kanyumbaaka kwa T/A Nsamala mboma la Balaka wati kuchoka kwa Phoya kupita kuMCP kukulozera kuti pena pake paola ku DPP polingalira kuti Phoya adali msalamangwe kuchipaniko. Sitinganene kuti kupita ku MCP kungabweretse chitukuko. Izi zingotisokoneza mavotedwe chifukwa tikusowa chipani chomwe tingachione ngati chithandiza, adatero Kamvamtope. Ndipo Frank Chibambo wa mmudzi mwa Chibwana kwa T/A Chikulamayembe mboma la Rumphi adati izi zikuonetsa kuti ku DPP kwaipa. Apa pakuoneka kuti pali chikaiko kuchipani cholamula zoti iwo amalimbikitsadi ufulu wa demokalase. Zikundipatsa nkhawa kuti kodi zikhala zolongosoka? sakukhulupirira Chibambo. Koma Chirwa akuti munthu akatuluka chipani, chipanicho chikuyenera kutengerapo mwayi, pounguza ndi kupeza anthu omwe angapititse patsogolo chipanicho. Phoya adachotsedwa kuchipani cholamula ndiye ali ndi ufulu kupita kuchipani chilichonse nthawi yomwe adatsutsana ndi lamulo loletsa kutengera chiletso boma ndi ogwira ntchito mboma. Tikatengera demokalase padalibe cholakwika chifukwa ngakhale uli kuchipani cholamula utha kumaperekerabe maganizo osemphana ndi ena, adatero Chirwa. Koma poyankhapo, Phoya wati anthu asadandaule chifukwa adziwa zoona zake posakhalitsapa. Sitikuvota mawa, ndiye tikhala tikulankhula ndi anthuwa kuti adziwe zingapo. Ndigwira ntchito yomwe akufuna. Ngati boma lingabwere ndi mabilu ena omwe sakomera Amalawi tiona kuti tithana nawo bwanji. Aboma akabweretsa zokomera anthu tiwathandiza koma ngati zikhale zosakomera anthu ndiye zioneka, adatero. Phoya adali phungu kuchipani cha UDF mu 1999 mpaka 2004 ndipo adakhalapo nduna muulamulirowo. Iye adalowa hipani cha DPP ndipo adakhalaponso nduna muulamuliro wa chipanicho.
11
Ulendo wa chisankho wapsa Zipani zina zati bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) liyenera kukwaniritsa zomwe lidalonjeza sabata yatha kuti chisankho cha 2019 chidzayenda mosakondera mbali. MEC idakhazikitsa ulendo wa chisankho chimene chidzakahalepo pa 21 May 2019 ndi lonjezo limodzi: Palibe kukondera. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wachiwiri kwa mlembi wamkulu wa chipani cha Malawi Congress (MCP) Eisenhower Mkaka adati lonjezo lotereli limanenedwa nthawi zonse kumayambiriro kwa ulendo ngati kuno koma pamapeto pake zimaoneka ndi zina. Tili ndi chikhulupiliro kuti ulendo uno, MEC isunga lonjezo lake ndipo tiziyanganira kuti lonjezoli akulikwaniritsa motani? Vuto ndiloti timamva lonjezo lomwelomwelo nthawi zonse koma kumapeto timaona zina, adatero Mkaka. Mneneri wa chipani cha Peoples Party (PP) Noah Chimpeni wati nkhawa yawo ili pakusasunga lonjezo kwa bungwe la MEC lomwe nthawi zambiri limawoneka kuti limapereka mpata waukulu ku mbali ina. Nthawi zonse amatero koma sitidaonepo umboni oti akwaniritsa lonjezoli. Ngati akunena za chilungamo, ndiye awonetsetse kuti chipani chilichonse chizikhala ndi mpata ofanana ngakhale pa MBC osati olamula okha ayi, adatero Chimpeni. Iye adati pakhalenso ndondomeko yoonetsetsa kuti aliyense azikhala ndi mpata wa msonkhano kulikonse komwe wafuna chifukwa nthawi zina misonkhano ina amayiletsa nthawi yothaitha ponena kuti kumaloko kukupita mtsogoleri wa dziko. Chipani cha United Democratic Front (UDF) chati aka sikoyamba chipanichi kumva lonjezo lotere kuchokera ku bungwe la MEC koma chomwe chimavuta nkukwatitsa lonjezoli ndi zochitika. Mneneri wachipani cha UDF Ken Ndanga adati chipani chawo chimafuna ntchito zooneka ndi maso osati mawu chabe. Sikoyamba kumva mawu amenewa kuchoka pakamwa pa MEC. Zakhala zikunenedwa koma chimavuta nkukwaniritsa mawuwo. Nkhani yaikulu ndi ntchito osati mawu chifukwa anthu timakhala tikuona zochitika, adatero Ndanga. Mlembi wamkulu wa chipani cha Alliance For Democracy (Aford) Christopher Ritchie wati chipani chawo chitsatira ndondomeko zomwe MEC yakhazikitsa koma nacho chiyembekezera MEC kukwaniritsa mbali yake monga mwa lonjezo. Paliponse pamafunika chilungamo kuti zinthu ziyende bwino ndipo ife a Aford timakhulupilira chilungamo. Choncho, titsatira ndondomeko koma nawonso akwaniritse zomwe alonjeza osati tidzawone zina kumapeto, adatero Ritchie. MEC idatsegulira ulendowu pa 20 February 2018 ndipo zipani za ndale zati kupatula zokonzekera zina ndi zina, maso awo ali pa lonjezo lomwe bungweli lidapereka kuti chisankhocho chidzakhala chopanda zitopotopo. Wapampando wa MEC Jane Ansah adalonjeza kuti chisankho cha 2019 chidzakhala chokomera aliyense chifukwa bungwelo lilibe mbali iliyonse yoti mwina ena azikayika kuti pangadzakhale kukondera. Bungwe la MEC ndilodzipereka kuchititsa chisankho cha mtendere ndi chokomera aliyense. Paulendo onse mpaka kumapeto, pakhala chilungamo ndi kuika zinthu pamtetete ndipo sitidzasekerera ogwira ntchito ku MEC aliyense opanga zautambwali, adatero Ansah. Iye adati bungwelo likuyembekezeranso mgwirizano kwa onse okhudzidwa ndi chisankho chomwe chikudzachi ndipo kuti zikatero, nalo (bungwe la MEC) lidzayesetsa kuti lisaopsezedwe kapena kutumidwa ndi mbali kapena mphamvu iliyonse. Ansah adati makomo a MEC akhala otsegula paulendo onse ndipo bungwelo lidzalandira ndi kuchitapo kanthu pa dandaulo lililonse lomwe okhudzidwa angadzabweretse mosaona nkhope. Koma zipani zina za ndale zati zamva lonjezoli koma maso ake akhala akuyanganitsitsa pa MEC kuti zione komwe lonjezoli lizilowera mpaka komwe likathere. Bungwe loona za kayendetsedwe ka ndale za zipani zambiri la Centre for Multiparty Democracy (CMD) lati paulendowu mpofunika kugwirana manja pakati pa mbali zosiyanasiyana kuti tikafike bwino. Wapampando wa bungwelo Kandi Padambo adati magulu monga zipani za ndale, nyumba zofalitsa nkhani ndi boma makamaka oyanganira thumba la chuma akuyenera kutengapo mbali kwambiri. Ku mbali ya boma, mpofunika kupereka ndalama zoyendetsera chisankho zokwanira nthawi yabwino, adatero Padambo.
11
Woganiziridwa kuba khanda anjatidwa ku Mzuzu Mayi wina zake zada mumzinda wa Mzuzu atamugwira ataba khanda la psuu la mnzake pachipatala chachikulu cha Mzuzu sabata yatha. Koma make mwanayo pano akumwetulira chifukwa khanda lakelo lilinso mmanja mwake! Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Mzuzu, Cecelia Mfune, watsimikiza za kumangidwa kwa Mary Pundi Nyirenda, wa mmudzi mwa Chisi, T/ A Mpherembe mboma la Mzimba, yemwe akumusunga palimandi kundende ya Mzuzu komwe akudikirira kukaonekera kubwalo la milandu komwe akayankha mlandu woganiziridwa kuba khanda masiku akubwerawa. Alinso limodzi: Wayisoni ndi mwana wake atapezeka Komatu khandali likadapita pakadapanda Maganizo Banda, mlonda wa kampani ya Stallion, yemwe ankalondera malowa usikuwo. Banda adati adakhala tcheru ataona Nyirenda akutuluka ndi khanda kuchokera muwodiyo nthawi itatsala pangono kukwana 12 koloko usiku. Mayiyu adatuluka katatu konse kulowera wodi ya amayi apakati, yomwe ili moyandikana kwambiri ndi wodi ya makandayi, atanyamula khanda lomwe adalikulunga mushawelo yoyera. Amati kutuluka nkulowa. Apa ndidadziwa kuti china chake chasokonekera chifukwa kunja kudali kukuzizira ndipo mayi wanzeru sakadatuluka ndi mwana nthawi ngati imeneyo ndipo sindidamulole kuti atuluke, adatero Banda. Pocheza ndi Msangulutso make khandalo, Mercy Wayisoni, wa zaka 27 yemwe amachokera ku Elunyeni mboma lomwelo koma kumudzi kwawo ndi kwa Nazombe, T/A Nazombe mboma la Phalombe, adafotokoza kuti adafika pachipatalapo Loweruka pa February 20 wopanda wina aliyense womudikirira. Iye adati Loweruka lomwelo adakumana ndi mayi wina kukhitchini yemwe adamufunsa ngati ali ndi womudikirira ndipo iye atamuuza kuti adalibe aliyense womusamalira pachipatalapo, mayiyo adamupempha kuti akhale mnzake kuti aziphika ndi kudya limodzi osadziwa kuti adali zolowere nkudyere mwana. Apa mpomwe ubwenzi wathu udayambira. Kwa masiku asanu ndi limodzi tinkadyera limodzi, adatero Wayisoni koma adati adadabwa kuti Lolemba nthawi yochira itakwana Nyirenda adamuletsa kuitana wachibale aliyense kuti amuthandizire ndipo adamuuza kuti wachibale aliyense asadziwe zoti nthawi yake yochira idali itakwana kaamba koti iye alipo ndipo amuthandiza. Wayisoni adati Nyirenda adali kumutsatira kulikonse komwe amapita patsikuli mpaka kuchipinda cha opaleshoni komwe adanamiza adokotala kuti adali wolandirira mwana ngakhale adokotalawo adamuletsa kulowa mchipindamo. Iye adati asadatuluke kuopaleshoniko, adokotala adamudziwitsa kuti adali ndi mwana wamwamuna. Wayisoni adati adazizwa pomwe adadzidzimuka pakati pa usiku ndi kupeza kuti mwana wake salinso kumtima kwake koma mnzakeyo adali atamusunthapo. Adandiletsa kumuyangana mwana wanga ndi kundiuza kuti khandalo silidali langa koma lake kaamba koti langa lidapitirira. Izi zidandikwiyitsa ndipo ndidauza oyandikana nawo kuti Nyirenda wanditengera mwana ndipo adasinthitsa nsalu ine ndili mtulo, adalongosola Wayisoni. Iye adati nawo achipatala atamva kuti muwodimo mwauka mpungwepungwe adabwera ndi kutsimikiza kuti khandalo lidali la Wayisoni.
7
Chilimikani pa ulimiKazembe Malinga ndi ngamba imene yasautsa mmadera ambiri mdziko lino, wachiwiri kwa kazembe wa limodzi mwa maiko a ku Ulaya la Flanders, Nikolas Bosscher wati boma la Malawi liyenera kuika mtima potukula ulimi mdziko muno. Bosscher adanena izi Lolemba pa msonkhano wa dzidzidzi wa komiti ya National Agricultural Content Development Committee (NACDC). Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Iye adati kuti dziko lino lithane ndi mavuto akudza chifukwa cha kusintha kwanyengo, nkofunika kubweretsa chitukuko chachikulu kumbali ya ulimi. Dziko la Malawi silikuchita chitukuko chenicheni kumbali ya ulimi chifukwa ndalama zambiri zikumapita kundondomeko yopereka zipangizo zaulimi motsika mtengo ndi kugula chimanga zomwe sizingamange maziko olimba otukula ulimi, adatero iye. Iye adati ulimi ukumakhudzidwa ndi china chilichonse chokudza monga ngamba, tizilombo toononga mbewu, matenda ngakhale kusowa kwa misika kumene. Choncho boma liyenera kuika patsogolo ndikubweretsa chitukuko kumbali ya ulimi. Monga madera omwe chimanga chaumiratu, mlimi ayenera kuuzidwa kuti azule chimangacho ndikubzala mbewu zina monga chinangwa ndi mbatata, adalongosola Bosscher. Mkulu wa nthambi ya ulangizi ku unduna wa zaulimi Jerome Nkhoma yemwe adali nawo pa msonkhanowo adati boma laika kale mtima pa chitukuko ndipo mwazina lidaika mlozo womwe kampani zingatsate pobweretsa chitukuko kumbali ya ulimi. Nkhoma adati nkofunika kuti alimi apatsidwe uthenga oyenera mwachangu okhudzana ndi ulimi pothana ndi vutoli. Ndipo Farm Radio Trust, bungwe lomwe limathandiza kufalitsa uthenga kwa alimi, yomwe idaitanitsa msonkhanowo idati zinthu sizili bwino mdziko muno ndipo alimi ambiri akhudzidwa ndi ngamba ndi mbozi zomwe zikuononga mmera. Ngakhale tidauzidwa kuti kukhala ngamba komanso mbozi zoononga mmera, sitimayembekezera kuti vutoli likhala lalikulu chonchi, adatero George Vilili wochokera ku bungwelo. Pomwe mkulu wa nthambi yoona zanyengo Jolamu Nkhokwe adati nthambi yake idanena kuti chaka chino kukhala ngamba komanso madzi osefukira mwezi wa September chaka chatha. Nkhokwe adati mvula ikadali kugwa, ndipo Madera ena omwe mudagwa ngamba, alandira mvulayi komabe adalimbikitsa alimi kutsatira uthenga omwe nthambi yake imapereka nthawi ndi nthawi.
4
Akufuna chakudya ku Nsanje Ngakhale maboma ambiri zikuoneka kuti apata chakudya mnyengo ya ulimi yangothayi, anthu ena mboma la Nsanje ati akufuna thandizo la chakudya lomwe mabungwe ndi boma amapereka lipitirire kwa miyezi ina itatu chifukwa sanakolole chimanga chokwanira ndipo ali pa njala. Phungu wa dera la kummwera kwa bomali, Thomson Kamangira, adanena izi pamsonkhano wa chitukuko omwe nduna yofalitsa nkhani Nicholas Dausi idachititsa podziwitsa anthu pulojekiti ya boma yoonetsetsa kuti netiweki ya lamya ikupezeka mmaboma onse mosavuta yotchedwa Malawi National Fibre Backbone sabata yatha. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Dausi: Tiyesetsa anthu asafe Kamangira adati ngamba yomwe inagwa chimanga chitangomasula ngayaye inasokoneza mbewu mbomalo. Tikusowa zambiri koma pakali pano vuto ndi la njala. Izi ndi kaamba ka ngamba osati madzi osefukira. Mabungwe asiya kupereka chakudya, koma tikuwapempha kupitiririza kwa miyezi itatu kuti tipulumuke ku njala yomwe itisause posachedwapa, adatero Kamangira. Pothirira ndemanga, khansala Robert Chabvi adati anthu mderalo chaka chinonso zawavuta kumunda ndipo boma ndi mabungwe awapase zida zochitira ulimi wamthirira. Sikuti ndife opemphetsa koma chimanga chatilakanso chaka chino. Boma ndi mabungwe tipatseni zida za ulimi wamthirira zoyendera mphamvu ya dzuwa kuti tilimenso uku mukutipatsa thandizo la chakudya. Pokhala kumudzi, anthu alibe chuma chogulira chimanga kwa mavenda kapena ku Admarc, adatero Chabvi. Poyankhapo, Dausi adati anthu asadere nkhawa chifukwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika achita zotheka kuti aliyense asafe ndi njala. Izi zikusemphana ndi lipoti la boma la mu February lomwe linati chimanga chikololedwa chochuluka matani 3.2 miliyoni kusiyana ndi chaka chatha 2.3 miliyoni. Malinga ndi mkulu wa Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira Banda nzosadabwitsa kuti anthu ena ku Nsanje adandaule za njala. Zolosera pa zokolola sizimasonyeza momwe zinthu zilili, adatero iye.
6
Richard Mbulu: Chilombo cha Mafco FC Dzina la Richard Mbulu lasanduka nyimbo ya mizinda yonse chifukwa cha ntchito zake zomwetsa zigoli. Pano Mbulu akutsogola mu TNM Super League ndi zigoli 11, adamwetsanso zigoli 17 mu Presidential Cup. Kodi Mbulu ndani? BOBBY KABANGO akucheza naye. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mbulu: Chilombo pankhani yokankha chikopa Wawa Mbulu Mbuluyo ndiye ineyo, mani. Kodi ndi Mimbulu? Kapena Mbulu basi? Ndine Mbulu, koma dzina limeneli likuchokera ku dzina loti Mimbulu, tinyama tovuta kwabasi. Ndiye iwe ndiwe wovuta? Kumbali ya mpira basi, kuvuta kwanga ndi kumeneko, koma zinazi ndiye ndine munthu wabwinobwino. Timudziwe kuti Mbulu ndani? Mbulu ndi ineyo, mnyamata wochokera ku Mangochi, woyamba kubadwa mbanja la ana asanu. Mbiri yako pachikopa ndiyotani? Poyamba ndimasewera ku Navy FC kapena kuti Marine MDF, nditachoka kumeneko, ndidakatera ku [Big] Bullets komwe ndidakhalako kwa miyezi iwiri. Ku Navy ndidachokako nditangolemba mayeso a Form 4 mu 2013. Zidayenda bwanji ku Bullets? Sadandipatse mwayi woti ndisewerere mtimuyo, panthawiyo amati ndine mwana. Ndidachoka ulendo ku Mafco FC komwe adandilandira bwino. Chipitireni ku Mafco wachinya zingati? Ndachinya zigoli 108 za ligi ndi makapu omwe, apatu ndikutanthauza kuyambira 2013 mpaka lero. Mphekesera zikuti mwayi wapezeka wokasewera ku Baroka FC ku Joni, ndi zoona? Zili choncho koma sindingayankhe zambiri pankhaniyi. Ineyo ndine msirikali ndiye oyenera kuyankha pankhani imeneyi ndi mabwana anga.
16
Wachitetezo wa Mutharika; Chisale Wamangidwa Apolisi amanga yemwe anali wamkulu wa achitetezo kwa mtsogoleri wakale wa dziko lino Peter Mutharika, a Norman Paulos Chisale. Ali mmanja mwa apolisi-Chisale (wavala jekete ya blue) Wofalitsa nkhani za apolisi mdziko muno, James Kadadzera watsimikiza za nkhaniyi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Ndizoona kuti ali mmanja mwathu kuno ku Lilongwe maka maka ofesi yofufuza fufuza nkhani yokhuza chuma. Ife apolisi timayitana anthu omwe tikuwaganizira pa nkhani inayake ndi kumawafusa kudikira kuti tipeze umboni weni weni,anatero Kadadzera. Kadadzera: Tinenabe zifukwa zomwe tawamangira Malipoti akusonyeza kuti a Chisale amangidwa pokhudzidwa ndi nkhani yolowetsa cement mdziko muno opanda msonkho. Koma mneneri wa apolisiyu wakana kunena zifukwa zomwe awamangira a Chisale ponena kuti akufufuzabe.
7
Papa Apempha Akhristu Apempherere Msonkhano wa ma Episcope ku Amazon Wolemba: Sylvester Kasitomu Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko lamulungu wapempha akhristu a mpingo-wu pa dziko lonse kuti apemphere ma Episcope a mpingo-wu ndi adindo ena ku Amazon omwe ayamba kuchita msonkhano wawo wa sinodi. Papa Francisco walankhula izi ku likulu la mpingo-wu ku Vatican. Iye wafuniranso zabwino atsogoleri ndi adindo ena omwe akuchita nawo msonkhano-wu, ndipo wapempha ma episcopi-wa kuti pomwe akuchita msonkhano-wu awonetsetse kuti agunda ndi kukambirana mfundo zabwino zomwe zingathandize pa ntchito zokweza mpingowu mu sinodi-yo. Iye wapereka pempholi patangopitanso miyezi yochepa pomwe dziko la Brazil lakhala likumana ndi ngozi ya moto pomwe nkhalango yayikulu ya Amazon yomwe mbali yaikulu iri mdzikoli inatenthedwa zomwe zinachititsa kuti zachilengedwe zambiri zionongeke.
13