Text
stringlengths
292
6.6k
labels
int64
0
19
Khansala wa DPP Wadandaula Ndi Kuchepa Kwa Chitukuko Mdera Lake Khansala wa dera la Chilaweni mboma la Blantyre Carlo Mdala wapempha boma kuti lithandize pa mavuto osiyanasiyana omwe ali mderalo. Mdala yemwe ndi wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) amalankhula izi pamene akulu akulu a mgwirizano wa zipani za UDF ndi DPP amachitisa msonkhano okopa anthu mderalo. Iye wati boma likuyenera kuthandiza derali pobweretsa chitukuko cha madzi, misewu, zipatala komanso magetsi. Mbewe: Anthu akavotere Mutharika Kuno ku Chilaweni ward vuto lalikulu ndi madzi. Midzi yambiri ilibe mijigo ndipo anthu ambiri akumwa madzi a mzitsime, chachiwiri misewu yambiri kuno ndiyowonongeka ndiponso magetsi sanakwanire mmadera ena mu ward ino, anatero Mdala. Poyankhapo pankhaniyi wachiwiri kwa mstogoleri wa chipani cha UDF, Lancy Mbewe wamema anthu a mderali kuti azavotere Peter Mutharika pa chisankho chatsopano cha President chomwe chikudzachi ndi cholinga choti mavutowa achepe mderali. Mmene tikudziwira kuti tonse tikuyembekeza chisankho cha president tikupempha anthu kuti akavotere Peter Mutharika kuti zitukuko zomwe zakhala zikuchitika mbuyomu zizichitikabe, anatero a Mbewe.
11
Asimbe lokoma ndani?: Civo, Manoma aswana mu Standard Bank Pali ntchito mawa pabwalo la Civo mumzinda wa Lilongwe pamene timu ya Civo United ichapane ndi Mighty Be Forward Wanderers mndime yotsiriza ya chikho cha Standard Bank. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Matimu onse adapatsidwa sabata imodzi yoti akonzekere masewerowa ndipo mawali ndi lomwe amene wotenga chikhochi adziwike. Silver Strikers ndiyo idatenga chikhochi chaka chatha itapuntha Azam Tigers 2-0. Civo yafika mndimeyi kawiri, mu 2009 pamene idakanganthidwa ndi Tigers kudzera mmapenote komanso mu 2010 pamene idakhaulitsidwa ndi Moyale kudzeranso mmapenote. Manager wa Civo, Rashid Ntelera wati palibe chatsopano chomwe timu yawo yakonzera osewera ngati angatenge chikhochi mawa. Malamulo athu ali momwe alili. Kupambana masewerowa ndiye kuti tili ndi K10 miliyoni, osewera adzagawana K6 miliyoni yomwe ndi ndalama yambiri, osewera akudziwa kale zoyenera kuchita komanso ubwino wotenga chikhochi, adatero iye. Wanderers yatengapo chikhochi kawiri, mu 2012 pamene idaumbudza Silver 2-0. Idachiteteza mu 2013 pokhaulitsanso Silver 1-0. Manager wa Wanderers Steve Madeira akuti chilichonse chakonzeka kuti mawali alange Civo ndi kutenga chikhochi kachitatu. Mukudziwanso kuti Wanderers ikamamenya mchikho imaikirapo mtima kwambiri. Komanso anyamata akudziwa kuti kungatenga K10 miliyoni ndiye kuti akatamukiratu. Tikudziwa kuti masewerowa akakhala ovuta komabe osapotera nyerere adziwe kuti tikachita zakupsa, adatero. Momwe matimuwa ayendera kuti afike mndimeyi. Wanderers ndiyo yasewera masewero ambiri chifukwa idachita kuvoteredwa ndiye idayambira mndime ya chipulula pamene idatulutsa Mafco 4-3 kudzera mmapenote. Mndime ya makotafainolo, Civo idachapa Dedza Young Soccer 2-0 pamene Wanderers idathowa Red Lions 1-0. Mndime ya semifainolo, Civo idalanga Bullets 2-1 pamene Wanderers idatuwitsa Blue Eagles 1-0. Lero matimu amene akhala akulanga anzawo mchikhochi akuyenera kulangana.
16
Malawi wapindulanji muzaka 49? Umphawi wankitsa ngakhale kuli ufulu Pamene dziko lino lero likukumbukira kuti lakwanitsa zaka 49 lili pa ufulu wodzilamulira, Amalawi ena ati ngakhale pali zina zolozeka kuti zikuyenda, zambiri zaphotchoka chifukwa cha dyera la andale ena omwe kwawo nkudzikundikira chuma. Maiko omwe sadasiyane ndi Malawi potenga ufulu wawo mu Africa muno ndi monga Botswana (1966, Mozambique 1975), South Africa (1961), Tanzania (1961) ndi Zimbabwe (1980). Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kadaulo wa ndale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College Joseph Chunga wati mu zaka za mma 1970 mpaka 1980 kusintha kumaoneka makamaka kumbali ya chuma. Kusinthaku akuti kumaonekanso mu 2005 mpaka 2006 zomwe wati zimapereka masomphenya kwa dziko lino kuti lifanana ndi abwenzi oyandika nawo. Dziko la Malawi lidalandira ufulu wodzilamulira mu 1964 chaka chimodzi ndi dziko la Zambia. Malinga ndi ndemanga Malawi ndiye akutsalira kwambiri ndi maiko omwe adalandira nawo ufulu moyandikana zaka. Maiko omwe sadasiyane ndi Malawi potenga ufulu wawo mu Africa muno ndi monga Botswana 1966, Mozambique 1975, Kenya 1963, Tanzania 1961 ndi Zimbabwe 1980. Koma Chunga wati mu zaka za mma 1970 mpaka 1980 kusintha kumawoneka maka kumbali ya chuma. Kusinthaku akuti kumawonekanso mu 2005 mpaka 2009 zomwe wati zimapereka masomphenya kwa dziko lino kuti lifanana ndi abwenzi oyandika nawo. Mzaka zimenezi timaonetsa kuti tikupita patsogolo, pena timabwerera mwinanso kungoima pamodzimodzi osasuntha. Kuyambira 2010 ndiye zimaonetsanso kuti tikubwerera chifukwa nkhani zachuma sizinali bwino. Komwe tikulowera sikukudziwika chifukwa bwezi pano tikumafananako ndi maiko omwe tidatengera nawo ufulu moyandikana. Zambia ndiwo abwenzi athu koma chuma chawo sichingafanane ndi Malawi. Ku Mozambique kudali nkhondo komabe sungafanize ndi Malawi, adatero Chunga. Iye adati vuto ndi atsogoleri athu chifukwa akulephera kunena komwe tikupita komanso kuti zomwe zikuchitikazo zitifikitsa pati. Izi ndiye ndakhala ndikunena kuti andale athu alibe mtima wotukula dziko lino. Zomwe amatiuza si zomwe amazichita, izi zikuchititsa kuti mpaka lero tikhalebe osauka, adatero Chunga. Senior Chief Kalonga ya mboma la Karonga yati ntchito za chitukuko zikuyenda motsimphina zomwe wati zikuchititsa kuti Malawi asamafanane ndi maiko ena. Vuto kwathu kuno nkuti pomwe chitukuko chabwera chimayenda pangonopangono, izi ndizo zikuchititsa kuti tisamafanane ndi anzathu. Tikufunika kuti tizilolerana, ngati wina akuyendetsa dziko tiyeni timupatse nthawi ndi kumuthandiza osati kumukankhira pansi kuti ifeyo tilamulire. Izi ndizo zikuchititsa kuti tizingokhalabe pamodzimodzi, adatero Kalonga yemwe akuti pomwe dziko lino limatenga ufuluwu nkuti alipo. Ndidamenya nawo nkhondo moti ndidali mgulu la anthu omwe adatentha ofesi ya DC ku Karonga kuno. Iye adali mzungu ndiye timawathamangitsa mpaka tidatentha katundu wake, adatero Kalonga. Senior Chief Tengani ya mboma la Nsanje yati Amalawi tichepetse ndale ngati tikufuna kuti tipite chitsogolo. Zolozeka sitingakane zachitika, kuchoka mmanja mwa atsamunda ndi chinthu choti utha kukamba komanso kukhala ndi mwayi woti munthu wakuda atha kukhala bwana ndi zokambika koma vuto ndi loti ufulu wathu sukutipindulira. Zikutenga nthawi kuti tizisunthira chitsogolo, pena tikumabwereranso. Izi zikuchitika chifukwa cha dyera lomwe andale ali nalo. Sakufuna kuthandiza anthu omwe akuwatsogolera kuti pakhale chitukuko koma kukokerana pansi, kutsutsana kwakula. Tichepetse izi, adatero Tengani, yemwe adati umphawi ndiwo wakakamira anthu mmidzi. T/A Champiti wa mboma la Ntcheu wati zingapo zasintha ndithu monga kupezeka kwa sukulu mmidzi, zipatala komanso misewu ngakhale izi sizokwana. Kale, achimwene, ku Ntcheu kuno kunalibe chipatala, zomwe zimasautsa amayi oyembekezera. Pano ngakhale sukulu ndi zipatala zili mtalimtali komabe tikunena kuti tili nazo. Boma libweretse zipatala pafupi ndi anthu chifukwa anthufe tachuluka pomwe zothangatira moyo wathu zikuchepa, adatero Champiti. Pangani Chimwaza wa mmudzi mwa Manjeza kwa T/A Kadewere mboma la Chiradzulu wati atsogoleri athu akumadzikundikira chuma, zomwe wati sizingapititse Malawi patsogolo. Atsogoleri athu sakufuna kutitukula ife koma kudzilemeretsa okha. Zambiri zikumakhala zawo koma tochepa tokha ndito akutigawira ife. Tamva za chuma cha mtsogoleri wapitayu momwe adalemerera pomwe ife tidamuika pampandopo tili chimodzimodzi. Choncho sitingayembekezere kuti tipita patsogolo, ndi bwino atsogoleri athu atukule ife iwo pambuyo, zikatere ndiye tizisuntha. Zomwe amalonjeza zimasemphana ndi zomwe akuchita pomwe ayamba kutilamulira, adatero Chimwaza. Ruth Samikwa, wa mmudzi mwa Mambala kwa T/A Kwataine mboma la Ntcheu, wati pena tikumapita patsogolo pena tibwerera chifukwa atsogoleri athu akumakhala ndi nkhuli yofuna kudzikundikira chuma nkuiwala Amalawi. Akakhala pamipando sakumalabadira za ena omwe anataya nthawi powavotera. Kumbali ya zachuma ndiye mavuto osasimbika, adatero Samikwa.
2
Pa Wenela pasintha zedi Tsikulo pa Wenela padali fumbi. Lazalo Watsika wabwera ndi moto ndithu. Abale inu, dzikotu ili limatembenuka zedi. Ndani ankadziwa kuti Lazalo nkusankha anthu mmipando yonona iyi? Ndani ankaganizako kuti tsiku lina iye ndi Male Chauvinist Pigs nkukhala pachiongolero? adafunsa Abiti Patuma. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo ANatchereza Ndipo sizinaoneke nkale lonse kuti nduna zochuluka za mfumu zikhale zochuluka zimene zili ndi udindo umodzi basi. Apatu si zoti munthu yekha maudindo mbwee, adayankhira Gervazzio. Abale anzanga, pajatu pofuna kusangalatsa anthu susangalatsa onse. Koma apapa Lazalo ndiye walephera ndithu. Zoona mpaka kusankha anthu a mphasa imodzi kuti amuthandize kulongosola zinthu! Apapatu watidyetsa galu ndithu, adatero mkulu adali ndi Abiti Patuma tsikulo. Pamenetu sindikumvetsa mpoti tsono kodi apa mumafuna kuti asankhe ndani? Ali dere nkulinga utayenda naye. Tiyeni tidikire tione kuti zitha bwanji, adatero Abiti Patuma. Chiyembekezo cha anthu pa Wenela chidali chokwera ndithu. Tuvana wati? Apapa ena mukundinena kuti ndalakwitsa. Inde ndalakwa ndipo ndalakwa ndithu. Awa ndikuwapatsa ntchito ndipo akuyenera kuyendetsa bwino. Kupanda apo, pakutha kwa miyezi, ena awona chikwanje, Lazalo adatero atafika malo aja timakonda pa Wenela. Kunena zoona, Moya Pete ndimusowa. Komanso ndimusowa Atipatsa Likhweru, mnyamata wa miyambi. I am not my own mindful, if some of you have come straight from the land of darkness. Together we crumble and together we succeed, adatero Chatsika. Komatu Vingerezi vanu muticheka navo. Tsono mukuti ife tizimvapo chiyani? Inuyo mukhala Martin Luther King Junior kapena Abraham Lincoln? Chonde tikhululukireni taweya, adatero mkulu adali ndi Abiti Patuma. Tsono pano pa Wenela zinthu zikusintha tsiku ndi tsiku, kuchita kusowa poyambira. Adatulukira Saulo Walima atanyamula fayilo yake. Sindili pano kuchotsa munthu ntchito. Mudzichotsa nokha. Ena munandinyoza, munanditukwana. Lero ndikukupemphani, dzisanthuleni nokha ndipo mukapezeka kuti simukukwanira, chokani nokha basi, adatero Saulo. Ndidaona mayi wina amene amadziwa kulira kwambiri, Shad Black akuzyolika. Sindikudziwa kuti amakhumudwa ndi chiyani! Nthawi imasintha. Pelete wafika. Batcha lalira. Gwira bango, upita ndi madzi iwe!.
15
Papa Apemphelera Bata Mdziko la Cameroon Wolemba: Thokozani Chapola p-content/uploads/2019/09/pp.jpg" alt="" width="580" height="328" />Papa pa ulendo wake wa mu Africa Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse PAPA FRANCISKO wati ndi khumbo lake kuti mavuto a ndale mdziko la CAMEROON athe kudzera mu zokambirana. Papa FRANSISKO walankhula izi la mulungu ku likulu la mpingowu ku VATICAN atatha mapemphero amasana a mthenga wa Mnjelo. Iye wati ndi khumbo lake kuti zokambirana zomwe zayamba lolemba mdziko la CAMEROON zomwe ndi zothandiza kubweretsa umodzi ndi mtendere mdzikolo. Pamenepa Iye wapempha anthu onse kuti apempherere mtendere ndipo kuti mavuto omwe okhudza kusamvana pa nkhani za ndale omwe akhala akuchitika mdzikomo kwa zaka zambiri athetsedwe ptsatira zokambiranazo. Mtsogoleri wa dzikolo a PAUL BIYA ndi amene wadzichepetsa ndi kuyitanitsa msonkhano wa zokambirana zofuna kuthetsa kusamvana pa nkhani za ndale komwe kwakhala kukuchitika mdziko la CAMEROON.
13
Mlenje wakhapa mlimi ku Dedza Mlenje wina wa mmudzi mwa Mbwindi mdera la Mfumu Kachere ku Dedza wavulaza mlimi wa mmudzi mwa Kuchikowa pamene nkhwangwa yomwe adaponya kuti ilase nkhwali itaphuluza nkumulasa pa mutu. Mlenjeyo, a Francisco Kwenda ndi mlimiyo, a Nachimwani Langisi, adalawirira aliyense kukagwira ntchito yake. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC A Langisi atatsiriza kuthirira mbewu zawo ku dimba, adatsikira kudambo kuti akasambe mmiyendo popeza mudali mutachita matope. Atangoyamba kusamba, adamva chinthu chawamenya pa mutu ndipo adagwa pansi. Mosakhalitsa adazindikira kuti adakhapidwa ndi nkhwangwa moti mmene anthu amabwera kudzawathandiza nkuti magazi atachita chosamba. Nkhaniyo idakatulidwa ku polisi popeza madotolo a pa chipatala chachingono cha Matumba mbomalo adakana kuwathandiza opanda chikalata chochokera ku polisi. A Kwenda, womwe adavomera kuti ndiwo adavulaza a Langisi adawatsekera. Pofotokozera apolisi, mlenjeyu adapempha mlimiyo kuti amukhululukire chifukwa adamulasa mwangozi. Ndidaponya nkhwangwa kuti ndiphe nkhwali koma mwangozi idaphuluza nkukakhapa mayi Langisi omwe sindimadziwa kuti akusamba ku damboko. Chonde ndapota nanu, ndikhululukireni, adatero a Kwenda. A Langisi ndi mafumu a mderalo adalandira kupepesako ndipo adapempha a polisi kuti amasule a Kwenda. Koma mafumuwo adalangiza alenje mderalo kuti adzisalama kwambiri posaka kuwopa kuvulaza kapena kupha anthu. Padakali pano a Langisi akupezako bwino.
18
Kwezani ndalama ku umoyoMHEN Mavuto a zaumoyo mMalawi muno ndiye ndi osayamba. Odwala kuthinana mzipatala, mankhwala kusowa, madotolo ochepa komanso zipatala zotalikana. Mkulu wa bungwe la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe, wati mavuto onsewa akudza chifukwa dziko lino silikuyika K15 ya K100 ya ndondomeko ya zachuma ku ntchito zaumoyo. Jobe adati maiko a mu Africa kuphatikizapo Malawi adasainira pangano ku Abuja mu 2001 kuti ndalama zoika ku zaumoyo zisamachepere K15 pa K100 iliyonse. Maiko adasayinira panganolo limene adalilimbikitsa ndi a bungwe loona zaumoyo padziko lonse la World Health Oragnisation (WHO). Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mzipatala zina mumakhala kuthinana kwambiri Kafukufuku wa Tamvani, wasonyeza kuti zaka zitatu zapitazi, ndondomeko ya zachuma mdziko muno yakhala ikupereka ndalama zosaposa K8.70 pa K100 iliyonse ndipo pandondomeko imene tikuyendera pano kudayikidwa ndalama zochepetsetsa kuposa zaka zonse. Jobe adati izi zikudzetsa mavuto a kusowa kwa mayendedwe (ma ambulansi), chiwerengero cha ogwira ntchito, kutalikana kwa zipatala ndi kusowa mankhwala. Amene adaphunzira ntchito za chipatala ambiri akusowa ntchito, adatero Jobe. Iye adati pmaiko adagwirizananso kuti pamayenera kukhala makilomita 8 kuchoka pachipatala china kukafika china ndipo posachedwapa mtundawu udatsitsidwa kufika pa makilomita 5 koma dziko la Malawi silikwanitsabe. Komanso misewu yake ndi yomvetsa chisoni zomwe zimakhudzanso nkhani ya mayendedwe. Ma ambulansi ndi osowa mzipatala ndipo akapezeka, umva kuti palibe mafuta, adatero iye. Iye adati vuto lalikulu ndi kasamalidwe ndi kayendetsedwe ka ntchito poyeza ndi kupereka mankhwala kwa odwala. Mankhwala ena boma limagula koma ena makamaka okhudzana ndi malungo amachokera kwa maiko otithandiza omwe ali ndi malamulo awo, adatero iye. Iye adati athandiziwo akapereka mankhwalawo amereka limodzi ndi zida zoyezera ndiye nthawi zina chifukwa chochuluka kwa odwala, a chipatala ena sayeza, amangogwiritsa ntchito zizindikiro. Adaonjeza: Akabwera otithandiza, amapeza kuti mankhwala atha, koma zoyezera zikadalipo tsono amavuta kuti apereke mankhwala ena msanga. Mneneri wa unduna wa zaumoyo Andrian Chikumbe adalephera kupereka ndemanga pa nkhaniyi Tamvani atamugogodera kuyambira Lachiwiri. Mneneri wa unduna wa zachuma, Alfred Kutengule, adati boma la Malawi limalephera kukwaniritsa zinthu zina chifukwa chakuchepekedwa. Chilungamo nchakuti mapezedwe athu ngovutirapo. Timayenera kukambirana ndi anzathu otolera misonkho kuti tiwone momwe tingagawire kochepa komwe atolelako nchifukwa chake zina timalephera, adatero Kutengule. Izi zili choncho, Amalawi ndi amene akusautsika kwambiri, patatha zaka zoposa 50 chilandirire ufulu wathu. Ena mwa anthu amene tidacheza nawo adandaula za kuthinana kuchipatala, kusowa mankhwala, kuyenda mtunda wautali ngati ena mwa mavuto amene amakumana nawo.
6
Tom sakufunanso ndalama? Kati deru kadazizwitsa mlenje. Ife aganyu tadzidzimuka ndi ganizo la mphunzitsi wa Flames Tom Saintfiet yemwe tsopano wanena kuti sakufunanso K3.3 miliyoni akakapuntha Nigeria pa 7 September. Ife tidayamba kutolera za mmageti kuti pofika pa 7 zikhale zitakwana koma lero kudzidzimuka akuti ndalama ayi. Ah ah ah! Zataninso wawa? Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pamene Uncle Tom amabwera adagwirizana ndi Fam kuti iwo abwera ngati mfalisi ndipo ntchito yawo ndiyokagwetsa Nigeria. Komabe Uncle Tom adalamula Fam kuti idzawapatse K3.3 miliyoni lotolo akalichenutsa. Lero Uncle Tom asintha maganizo, akuti iwo ndalama si nkhani ndipo ngakhale akatsotsomole Nigeria Fam isadzawapatsenso ndalamazo. Kodi pamene Uncle Tom amalamula ndalamazo samadziwa kuti iwo ndi andalama kale? Kapena mwadziwa kuti Fam imaphangirana ndi matimu potolera za pageti zomwe zingatenge nthawi kuti ndalamayo ikwane? Kapena mwazindikira kuti chitunda chimenechi sitingakakwerepo? Monga mwa mawu anu, aganyu sitikukayika kuti pa Nigeria tikadutsapo ngakhale mphunzitsi wa Nigeria wadzipereka kusiya ntchito yake akakagonja ndi Flames. Mwina osewera athu atengerepo phunziro kuti si bwino kumasewera ndi mtima wofuna kulandira kanthu koma mmalo mwake kufuna kupanga mbiri. Kukagwetsa Nigeria kwawo ndi nkhani yomwe ingatekese dziko lapansi. Izi zikutitsimikizira kuti ngakhale popanda malonjezano inu mukangogwira ntchitoyo.
15
ACJ Yati ndi Yokhudzidwa ndi Imfa ya Mlelemba Bungwe la atolankhani achikatolika la Association of Catholic Journalists (ACJ) lati ndi lokhudzidwa kamba ka imfa ya Martin Mlelemba yemwe anali mmodzi mwa mamembala a bungwe-li mdziko muno. Wapampando wa bungwe-li mchigawo chapakati a Sam Kalimba wanena izi pofotokozera Radio Maria Malawi. Iye wati bungwe la ACJ lataya munthu wofunika kwambiri pa ntchito zokweza bungwe-li. Malo amene wagona Mlelemba Polankhulanso wapampando wa bungwe lomenyera maufulu a atolankhani mdziko muno la Media Institute of Southern Africa MISA Malawi, Teleza Ndanga wati atolankhani onse mdziko muno ndi okhudzidwanso kamba ka imfa ya mtolankhaniyi kamba koti anali mmodzi mwa atolankhani omwe amathandiza pa ntchito zokweza atolankhani-wa mdziko muno. Malemu Martin Mlelemba anabadwa pa 24 December mchaka cha 1983 ndipo pomwe amasiyana ndi dziko lino mkuti akutumikira wa wailesi ya kanema ya mpingo wakatolika ya Luntha , koma kuti amagwira ntchito ngati mtolankhani wapadera wa wailesi ya Channell Africa Chichewa Service.
13
Apolisi akwidzinga anthu 10 ku Neno Akuwaganizira kuti adatengapo mbali kupha agogo anayi Apolisi mboma la Neno Lachinayi adanjata anthu 10 powaganizira kuti adatengapo mbali pa imfa za agogo anayi omwe adachita kuphedwa ndi anthu olusa powaganizira kuti ndiwo adalenga mphenzi yomwe idapha mtsikana wa zaka 17, Flora Kanjete, Lolemba lapitalo. Mneneri wa apolisi mbomalo, Raphael Kaliati, polankhula ndi Msangulutso Lachitatu lapitali, adati kufikira Lachitatulo apolisi adali asadamange wina aliyense wokhudzidwa ndi kuphwedwa kwa anthu okalambawo podikira kuti bata likhazikike kaye kuderalo kuti ayambe bwino kufufuza za imfazo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Koma mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, adalowererapo polamula mkulu wa apolisi Lexten Kachama kuti nkhaniyi aifufuze mmangummangu kuti chilungamo chioneke malinga ndi malamulo a dziko lino ndipo kuti ngati ena apezeka olakwa pamlandu wakupha alandire chilango choyenera. Malinga ndi chikalata chochokera kunyumba ya boma chomwe adachitulutsa Lachitatu, mtsogoleri wa dziko linoyu adati adali wachisoni komanso wokhumudwa kwambiri ndi imfa za agogowo kaamba kowaganizira za ufiti. Chikalatacho chidati: Pulezidenti [Mutharika] akuti anthu okalamba ayenera kulandira ulemu komanso chitetezo nthawi zonse ndipo boma lake silidzalola kuti okalamba azitonzedwa kapena kuvutitsidwa mnjira ina iliyonse mdziko muno. Ndipo pofika Lachinayi, malingana ndi mneneri wa polisi pa Neno, anthu 10, kuphatikizapo anyamata asanu a zaka za pakati pa 13 ndi 18, adanjatidwa ndipo ali mmanja mwa apolisi powaganizira kuti ndiwo adakonza upo wopha agogowo. Ena mwa omangidwawa ndi Staford Chifundo, wa zaka 36; Amosi Sida, wa zaka 32; Samuel Kaudzu, wa zaka 20; John Harry, wa zaka 21; ndi Lex Mayenda, wa zaka 19. Onsewa, kuphatikizapo anyamata achisodzerawo, akuti mpachibale ndi agogo adaphedwawo. Kaliati adati anthu khumiwa awatengera kubwalo la milandu la majisitireti ku Neno komwe akaipereke mmanja mwa bwalo lalikulu la High Court poti ndilo lili ndi mphamvu zozenga milandu ikuluikulu monga ya kupha. Iye adati zofufuza zidakali mkati ndipo pali chiyembekezo choti lamulo ligwirapo ntchito pa onse okhudzidwa ndi nkhani yoziziritsa nkhongonoyi. Nalo bungwe la Malawi Law Society lidati ndi lokhumudwa ndi imfa za agogowo, omwe adaphedwa pazifukwa zopanda mchere, pongowaganizira za ufiti kaamba ka ukalamba wawo. Omwe adakonza chiwembu chopha agogowa ayenera afufuzidwe bwinobwino ndipo akapezeka ayenera akayankhe mlandu kubwalo la milandu ndi kulandira chilango choyenera akapezeka olakwa. Bungwe lathu ndi lokonzeka kupereka maloya kuti athandize boma pozenga milanduyo, chatero chikalata chomwe a bungweli atulutsa pambuyo pa kumva za nkhani yomvetsa chisoniyi, chomwe chidasainidwa ndi pulezidenti wa bungweli John Suzi-Banda ndi mlembi Khumbo Bonzoe Soko. Oganiziridwawo adamenya agogowo mpaka kumpha zitangodziwika kuti mphenzi yapha mtsikanayo dzuwa likuswa mtengo. Malinga ndi Kaliati, anthuwo akukhulupirira kuti mphenziyo idali yokonzedwa ndi agogowo, omwe adali pachibale. Mboma la Neno muli vuto la mvula. Chiyambireni chaka chino, mvula yagwa masiku 8 okha koma mphenzi zakhala zikunganima ndi kupha anthu kumeneko. Agogowo ndi Eliza Enosi Kanjete, wa zaka 86; Elenefa Kanjete, wa zaka 76; Byson Kanjete, wa zaka 73; ndi Idesi Julias Kanjete, wa zaka 69. Onsewa adali a mmudzi mwa Chimbalanga 1. Agogowo adaikidwa mmanda Lachiwiri limodzi ndi mtsikanayo adaphedwa ndi mphenzi uja.
7
Adandaula zochitika kumgodi wa Kanyika Jere kuonetsa chizindikiro cha msamuko Anthu okhala mdera lozungulira Kanyika kwa T/A Mabulabo, mboma la Mzimba ati ndiokhumudwa ndi momwe dongosolo la kukumba miyala ya mtengo wapamwamba ya Niobium likuyendera mderalo. Anthuwa adati kuchokera pamene anauzindwa za dongosolo lokumba miyalayi, zaka zisanu ndi ziwiri zapitazo palibe chizindikiro chooneka kuti ntchito yokumba miyalayi ichitika mowapinduliranso. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Iwo adati kuyambira pamene boma linawauza kuti achoke pamalopa, anthuwa akhala akudikirira za nkhaniyi koma palibe dongosolo likuoneka pamaso pawo. Polankhula Lachisanu lapitalo pamsonkhano wa pakati pa akululuakulu oyanganira nkhani za chitukuko mderali omwe udapangitsindwa ndi bungwe la Church and Society ya Livingstonia Synod, mfumu Nkosana Yobe idnati kuyambira nthawi yomwe boma linawauza kuti asamuka pamalopa malinga ndi ntchito yokumba miyalayi, pakhala povuta kuti anthuwa apange chitukuko poganizira kuti adzachotsedwa. Iye adati chodabwitsa nchakuti nthawi yaitali yapita anthuwa asakuuzidwa chogwira mtima chilichonse pa zamsamuko wawo. Tili odandaula ndimene nkhani yokumba miyala kuno ku Kanyika ikuyendera. Tinauzidwa kuti tisapange chitukuko chilichose pamalopa chifukwa kutero sitidzapatsidwa chipukuta misozi pa chitikuko tachitacho. Koma mpaka pano palibe chimene chikuoneka. Izi zikuchititsa kuti tikhale anthu omangika, idadandaula mfumuyo. Padakalipano, anthu ozungulira Kanyikawa ndiodabwa kuti zaka 7 zapita kampani ya Kanyika Niobium Mining ikukumba miyala imene imati ndiyachiwonetsero, imene anthuwa akudabwa kuti imapita kuti? Mkulu wa za chitukuku mderali, Folger Nyirongo, adati ndi zokhumudwitsa kuti boma likumapanga ndondomeko yokumba miyala ya mtengo wapatali mdera lawoli popanda eni malo ozungulira mgodiwu kutenga nawo mbali. Iye adati izi zikutsutsana ndi zofuna za demokalase zotukula mphamvu yaulamuliro kwa anthu. Tikudabwa nazo kuti boma likamapanga ngwirizano ndi makampani odzakumba miyalayi sakumatitenga kukhala nawo ku zokambilanazo. Izi zikudabwitsa, ndipo zikutsutsana ndi dongosolo loyendetsa boma la mphamvu ku anthu, adatero Nyirongo. Koma poyankha nkhaniyi, mneneri wa ku unduna wa za migodi, Lazy Undi, adati iwo ndiwokhutira ndi dongosolo limene lilipo pakati pa anthu a kukanyikako ndi unduna wawo. Unduna wathu unali konko kukambirana nawo pa zatsogolo la mgodiwo. Ndipo ife ndiwokhutira ndi mmene ubale ukuyendera ndi anthu a deralo,adatero Undi. Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, potsegulira zokambira za Nyumba ya Malamulo posachendwapa adati boma lake lionetsetsa kuti pakhale ndondomeko zabwino zoonetsetsa kuti anthu a dziko lino akupindula ndi migodi imene ikhazikitsindwe.
11
Ulemu ulibe mkazi kaya mwamuna Ulemu ndi khalidwe lofunika pamoyo wa munthu wina aliyensewamwamuna kapena wamkazichoncho mtsogoleri wadziko lino sadaphonye kwenikweni masiku apitawa pomwe adakumbutsa amayi za kufunikira kwa ulemu pabanja. Kungoti langizo labwinoli lidakhala ngati lapotokera mbali imodzi, ya amayi, pomwe abambonso amayenera kuchitako mbali yawo popereka ulemu kwa akazi awo kuti banja liyende bwino. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kulankhula kotereku kungathe kupititsanso patsogolo maganizidwe aja oika udindo onse oonetsetsa kuti banja lilimbe uli mdzanja la mayi pomwe bambonso ali ndi mbali yaikulu yoti achite poonetsetsa kuti banja liyende bwino. Kuphatikiza apo, langizo lakukhala wa ulemu ndi limodzi mwa malangizo omwe amayi akhala akuuzidwa kwa nthawi yaitali, kuphatikizapo ena aja akukhala opirira komanso omvera. Kotero kuti kufunikira kwa ulemu amayi ambiri akhonza kukhala kuti akukudziwa bwino kuposa abambo chifukwa pachilangizo cha anamwali omwe atha msinkhu kapena omwe akulowa mmbanja, nkhani ya ulemuyi imanenedwa kwambiri. Amayi enanso ulemuwu saumvetsetsa bwino kotero kuti akamenyedwa salandula konse; mmalo mwake amapepesa bambo owamenyayo, ati ulemu; zomwe zikuchititsa kuti nkhanza za mbanja zisathe. Choncho mmalo mowirikiza za kufunika kwa ulemu, ndibwino titathandizana kumvetsetsa kuti ulemu ndi chani ndipo kuti uli ndi malire ati makamaka mokhudzana ndi zinthu zomwe siziyenera kuchitika mbanja monga nkhanza. Kuphatikiza apo, atsogoleri angathandize poika mtima kwambiri pankhani zomwe zikubwenzera mmbuyo moyo wa amayi ndi mabanja awo. Izi ndi nkhani monga kulephera kwa amayi ambiri kudziimira paokha pa chuma. Chiwerengero cha amayi omwe akungokhala kudikira kuti athandizidwe ndi abambo chikadali chokwera. Palinso amayi ambiri omwe akukakamira mabanja achizunzo podziwa kuti akalituluka banjalo alibe mtengo ogwira kumbali ya kapezedwe ka chuma. Apa pakufunika kukonza. Sindikuti amayi azichita mwano mmabanjamu. Mwano ngosathandiza pabanja ndipo ulemu ndiwofunika zedi. Koma, ulemuwu tiumvetse bwino ndipo uchokere mbali zonse ziwirimayi ndi bambochifukwa kukhala wa ulemu sikufunika kuti ukhale wa mkazi kapena wamwamuna ndipo aliyense amafuna kupatsidwa ulemu.
1
Anthu 500 000 sadalembetse Zotsatira za kalembera wachisankho mgawo loyamba ndi lachiwiri zasonyeza kuti anthu 468 860 omwe amayenera kulembetsa sadalembetse nawo mkaundulayo. Malingana ndi zotsatira zochokera ku bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), mgawo loyamba, anthu 1 094 269 amayenera kulembetsa koma anthu 798 351 ndiwo adalembetsa kuimirira anthu 73 pa anthu 100 aliwonse. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mgawo Lachiwiri, anthu 1 048 080 ndiwo amayenera kulembetsa koma anthu 875 138 okha ndiwo adalembetsa kuimirira anthu 83 pa anthu 100 aliwonse ofunika kulembetsa. Apa zikutanthauza kuti mmagawo onse awiri, anthu 2142 349 ndiwo amayenera kulembetsa koma mmalo mwake, anthu 1 673 489 ndiwo adalembetsa kutanthauza kuti anthu otsala osalembetsa mmagawowa ndi 468 860. Mwa anthu omwe adalembetsawa, 901 060 ndi amayi pomwe 771 922 ndi abambo ndipo chiwerengerochi sichidasangalatse chipani chachikulu chotsutsa cha Malawi Congress (MCP) komanso bungwe lowona za ufulu wa anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR). MCP ndi CHRR adapempha bungwe la MEC kuti liganizire kudzabwereza kalembera mmaboma omwe mudachitika kalemberayu mmagawo awiriwa kuti anthu omwe adatsalirawa adzapeze mpata wolembetsa. Mneneri wa MCP Rev Maurice Munthali adati kalemberayo ngoyenera kuchitikanso mmaboma omwe adakhudzidwa chifukwa anthu omwe sadalembetse ndi wochuluka kwambiri. Sitingasiye anthu onsewa osalembetsa ayi ndiye kuti sitikudziwa chomwe tikupanga. MEC ikuyenera kudzabwerera mmaboma omwe akukhudzidwa mmagawo amenewa, adatero Munthali. Mkulu wa bungwe la CHRR Timothy Mtambo adati potengera kulemekeza ufulu wa anthu, mpoyenera kuti kalembera adzabwerezedwe mmaboma okhudzidwawa. Anthu ali ndi maufulu osiyanasiyana ndipo umodzi mwa maufuluwo ndi otenga nawo mbali posankha atsogoleri ngati momwe tikuyembekezera chaka cha mawachi. Apapa, zikuonetseratu kuti anthu ambiri sadalembetse kotero ufulu wawo odzasankha atsogoleri waphwanyidwa, adatero Mtambo. Mkulu wa MEC Jane Ansah adati kalembera mmagawo oyambirirawa adavuta chifukwa anthu adali asadamve mauthenga bwinobwino komanso padali mavuto okhudzana ndi zipangizo zomwe zimafaifa koma adati mavutowa adatha. Iye adapempha mabungwe ndi zipani zandale kuti zichilimike kumema anthu kukalembetsa mkaundula kuti akavote nawo chaka cha mawa pachisankho cha patatu. Mkulu wa bungwe loona kuti zisankho zikuyenda bwino la Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa adagwirizana ndi Ansah kuti mabungwe ndi zipani zandale athandizirepo kwambiri kumema anthu kukalembetsa kuti chisankho cha chaka chamawa chidzakhale chatanthauzo.
11
Madalaivala a Truck Awonjezeredwa Malipiro Madalaivala a Truck omwe amanyanyala ntchito alengeza kuti ayambiranso ntchito chifukwa boma lalonjeza kuti lithandiza pa madandaulo awo. Zinali chonchi nthawi ya sitirakayo, Ma truck tayimitsidwa mbali mwa nsewu ku Blantyre mu nsewu wa Blantyre Lunzu Mmodzi wa akulu-akulu a Truck Drivers Association a Masautso Chagomerana wauza mtolankhani wathu pambuyo pa nsonkhanowu omwe unachitikira kulikulu la boma ku Capital Hill mu mdzinda wa Lilongwe kuti ngakhale siokhutira kwenikweni ndi panganolo, iwo akonza kuti ayambirenso kugwira ntchito pofuna kubweretsa mtendere mdziko muno ndipo wapempha madalaivala onse kuti abwerere ku ntchito mwa mtendere. Wachiwiri kwa nduna ya za mtengatenga a Charles Mchacha komanso akulu-akulu a makampani a ma Truck komanso ochokera ku nthambi ya apolisi, anali nawo pa nsonkhano-wu. Zatheka asuntha minimum wage kuchoka pa 25 000 kufika pa 60 000 koma pali nkhani zambiri zoti tikambirana mu sabata ziwiri zikudzazi. Tachita izi kuti tingobweretsa mtendere mdziko muno, anatero a Chagomerana. Iwo ati akukhulupilira kuti kutsogoloku zinthu ziyenda mokomera onse. Mwazina madalaivalawa agwirizana ndi boma kuti ndalama zochulukitsitsa zomwe azilandira ndi 140, 000 kwacha ndipo wolandira ndalama zochepetsetsa izikhala 60, 000 kwacha.
14
Bungwe la TIPOLISO Lati Anthu Akumudzi Akupereweredwa Mauthenga a Coronavirus Bungwe la Tikondane Positive Living Support Organisation (TIPOLISO) lati lapeza kuti anthu a madera ambiri akumidzi mdziko muno sanaphunzitsidwebe mokwanira momwe angazitetezere ku kachilombo ka Coronavirus. Mkulu wa bungweli a Sellina Bomani anena izi loweruka ku Chipini mdera la mfumu yaikulu Mulumbe mboma la Zomba pomwe bungweli limapereka zipangizo za ukhondo kwa mafumu, sukulu za mkombaphala komanso kwa anthu ochita bizinezi ya njinga za kabaza pofuna kuti aziteteze ku mliriwu. Iwo ati ndi kofunika kuti ananso nawo aphunzitsidwe bwino njira zaukhondo zopewera kachilomboka. Kuno kwa T/A Mulumbe tapereka mabeseni, mapelo ndi sopo ndi cholinga chothandizira kupewa kufara kwa matenda a Coronavirus komaso tapereka kwa mafumu zina mwa zipangizozi, anatero Bomani. Iwo atinso anayitana a zaumoyo pa mwambowu ndi cholinga choti athandizire kupereka mauthenga amenewa potengera kuti derali ndi ku chigwa ndipo mauthenga ofunikirawa safika mu nthawi yake. Patsikuli, bungweli lapereka zipangizo zosambira mmanja kwa mabanja okwana 362 a mderalo ndipo mmawu ake Group Village Headman Kamoto inayamikira bungweli kaamba ka thandizoli lomwe yati, lithandiza kulimbikitsa ukhondo mdera lake Kulandira chithandizo ichi taona kuti boma lathandiza kwambiri chifukwa zina mwa zipangizozi zithandiza poweruza milandu, anatero a Gulupu a Kamoto. Iwo atinso zomwe alandirazi ziwathandiza chifukwa choti boma la Zomba linachita malire ndi Blantyre komwe kagwa nthendayi kwambiri.
6
Waganyu: Tisaloze chala Mtawali Sabata yatha zidatigwera, Junior Flames kupunthidwa ndi Zambia 2-1. Tisabise, Zambia idasewera bwino. Mwayi ndi goloboyi wathu, apo biii! tidakasamba zenizeni. Ganizo la Ernest Mtawali ndi lakuti akasinthe zinthu ku Zambia. Tingopemphera mwina chozizwa chikachitike koma kuona kwathu izi zikavutirapo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kukonzekera kwathu nkodandaulitsa. Mpikisano ngati umenewu koma tikungokhala ku Chiwembe pamapeto nkumati takonzeka kukapha Zambia. Timaganiza tionetsa chidwi pa anyamatawa polingalira kuti imeneyi ndi timu yomwe tidyere mawali. Timadandaula kuti sitichita bwino ku Afcon ndi timu yaikulu. Eya tikuyenera kudandaula chifukwa mpira wathu sitiyambira patali. Tili ndi osewera amene akumenya Flames yaikulu koma sadapondemo mu Under-17 kapena 20. Lero tili ndi anawa koma thandizo palibe. Mphunzitsi wa Zambia, Hector Chilombo, adati dziko lawo likupereka thandizo kwambiri kutimu yake chifukwa akudziwa kuti tsogolo lonse lili mwa achisodzera. Ndizodziwikiratu, pofika zaka zitatu zikudzazi Zambia idzakhala ikuchita bwino mukaona mmene akuchitira. Vuto lathu sitithandiza achisodzerawa. Mwachitsanzo, timu ya Flames yaikulu idalonjezedwa K100 000 aliyense akapha Benin. Koma anawa posewera ndi Zambia osawalonjeza kanthu. Flames yaikulu yakonzeredwa masewero ambiri opimana mphamvu koma anawa ayi. Mmalo mwake kumakumana ndi Azam Tigers kapena Mighty Wanderers.
16
Papa Wati Atsogolera Misa Ya Chaka cha Ukaristia Lamulungu Likudzali Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco lamulungu likubwerali adzatsogolera Misa ya chaka cha Ukaristia mtchalichi lalikulu la Saint Peters Basilica. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa adzatsogoleranso mwambo wopembedza Ambuye Yesu wokhala mu Ukaristia pambuyo pa misayo. Koma malinga ndi mliri wa Coronavirus ndi anthu ochepa chabe omwe adzawalole kukhala nawo pa miyamboyi. Akuyembekezeka kutsgolera misayo-Papa Francisko Lamulungu la pa 14 June ndi tsiku lalikulu mu mpingo wa katolika pa dziko lons kaamba koti ndi tsiku lomwe mpingo udzakhale ukuchita chaka cha Ukaristia, tsiku lolemekeza thupi ndi ma magazi a Ambuye Yesu. Chaka chimenechi chimadziwika kuti Corpus Christi mchiyankhulo cha chi Latin. Pali chiyembekezo kuti anthu pafupi makumi asanu (50) ndi omwe adzakhala nao pa mwambowo potsata ndondomeko zoyikika pofuna kupewa kufala kwa nthenda ya Covid 19. Akhristu a katolika pa dziko lonse ali ndi mwayi wodzatsata mwambo wa Misa komanso mwambo wopembedza Ambuye Yesu wokhala mu Ukaristia kudzera pa kanema ndi makina a intaneti. Misa pa tsikuli idzayamba quarter to ten mmawa nthawi ya ku Rome komanso Malawi. Papa Urban wa 4 ndiyemwe adalengeza mchaka cha 1264 kuti Mpingo wa Katolika pa dziko lonse uzichita chaka chimenechi. Chaka cha Ukaristia chimenechi chimafuna kutsindika mosapeneka konse kuti mu Ukaristia muli Ambuye Yesu kotero nkofunika kudzikonzekeretsa polandira Ukaristia popeza si chakudya wamba ngati zitumbuwa kapena zikondamoyo. Ndipo ndi msonkhano wa ku Trent mchaka cha 1551 umene udatsindika zoti mu Ukaristia mulidi Ambuye Yesu.
13
Moto buuu! 2019 yafukiza zipani Fumbi lachita kobooo! mzipani pamene kwangotsala chaka chimodzi kuti chisankho cha patatu chichitike mdziko muno. Chisankho cha patatu chidzakhalako pa 21 May 2019. Izi zili choncho, zikuoneka kuti mzipani mwabuka moto pomwe nkhondo yolimbirana wodzaimira zipanizo yakula. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kumsonkhano wa Aford ena adachita kugona komweko Pamene ena mchipani cha DPP akhala akunena kuti Peter Mutharika apereke mpata kwa wachiwiri wake Saulos Chilima kuti adzaimire chipanicho, mtsogoleri wadziko linoyo wati zivute zitani, adzaimirabe DPP. Ku chipani chachikulu chotsutsa boma cha MCP ndiye kokera kwako wayala nthenje pomwe mpaka lero sizikudziwika kuti msonkhano waukulu uchitika liti kuti akasankhe wochiimirira. Chipani cha UDF nacho kuli mkokemkoke pomwe mlembi wamkulu wachipanicho Kandi Padambo wati ngakhale chipanicho chikhale ndi msonkhano waukulu pa 1 August, chipanicho chagwirizana kuti Atupele Muluzi ndiye adzachitsogolere, chonsecho Lucius Banda wakhala akunena kuti akufuna kudzaimira chipanicho. Koma njerengo zili ku Aford komwe pofika Lachinayi kudali ochitsogolera awiri: Enoch Chihana ndi Frank Mwenifumbo. Zidaliko Lachiwiri kumsonkhano waukulu wa chipanicho pomwe adalephera kugwirizana kuti woyenera kuvota ndani ndipo mbandakucha wa Lachitatu otsatira Mwenifumbo adamusankha kukhala mtsogoleri. Masana a tsikulo, otsatira Chihana adamusankha kuti ndiye mtsogoleri. Chihana adati Mwenefumbo amabweretsa mamembala a DPP kumsonkhanowo kuti akavotenayenso Mwenefumbo adati Chihana adafika ndi anthu amene maina awo mulibe mu kaundula wa chipanicho. Uwu si msonkhano wa DPP. Iyi ndi Aford, ndine wokonzeka kuwauza anthu avote bolani akhale athu, adatero Chihana. Koma Mwenifumbo sadaimve: Aford si chipani cha banja kuti chilichonse chizichokera kwa Chihana basi. Ndipo ngakhale Mutharika wanenetsa kuti adzaimira DPP, omwe akufuna Chilima akuti ndi maloto chabe. Mmodzi mwa iwo, Bon Kalindo, wati achita zotheka kuti Mutharika asaime, koma Chilima. Tikukumana ndipo posakhalitsapa tilankhula zomwe takonza, koma dziwani kuti Chilima ndiye atitengere kuchisankho. Kodi nchifukwa chiyani tizikakamirabe Mutharika yemwe wakula? akudabwa Kalindo. Mneneri wa DPP Francis Kasaila adati chipani chawo chikudziwa kuti Mutharika ndiye atengere chipanichi kuchisankho. Mgwirizano wa zipani Pamene mkokemkokewu ukupitirira, zikuoneka kuti zipani zikudzigulira malo polowa mumgwirizano. Pofika mdziko lino kuchokera kunja kumene wakhala zaka zinayi chichokere pampando, adalandiridwa ndi otsatira PP komanso a MCP amene adakumana nawo kwa mphindi 30. Polankhula kwa anthu, Banda adakwanitsa kupereka moni kwa MCP: Tilandirenso anzathu a MCP amene tili nawo pano. Koma mlembi wa MCP, Eseinhower Mkaka adakana kuyankhapo za mgwirizano wa zipanizi. Ndisayankhe zimenezo koma nditsimikize kuti anthu athu adapita kukalandira mtsogoleri wakale wa dziko lino Joyce Banda. Uwu ndi ulemu wathu chifukwa adali mtsogoleri wa dziko lino, adatero Mkaka. Malinga ndi kadaulo pa zandale, Henry Chingaipe, nzosadabwitsa kuti zipani za MCP ndi PP zikhoza kulowa mumgwirizano. Chisankho cha 2014 chisadachitike, padali zingapo zoonetsa ubale wa chipani cha PP ndi MCP. Sindikudabwa kumva zomwe zidachitika pamene Banda amafika mdziko muno. Izi zingatheke, adatero Chingaipe. Ndipo pachisankho chapadera cha makhansala chimene chidachitika mmadera ena miyezi ingapo yapitayo, zipani za UDF ndi DPP zidayendera limodzi popatsana mpata mmadera amene ali ndi mphamvu. Ndipo atapambana, otsatira zipanizo amaimba nyimbo imodzi. Chingaipe adati zikuoneka kuti DPP ndi UDF angayendere limodzi mchisankhocho komabe wachenjeza UDF kuti uwu ungakhale ulendo wokutha ngati makatani. DPP ikulamula kale, ngati angachite ubale ndiye kuti UDF itha kumezedwa, zomwe zingazimitse banja la Muluzi pankhani ya ndale. Atha kuchita mgwirizano, koma asamale, adaonjeza motero.
11
Akhritsu Eni Ake Agwirizana ndi Ganizo la Maepiskopi Loyimitsa Mapemphero Bungwe la Akhristu Eni Ake mu arkidayosizi ya Blantyre lati likugwirizana ndi pempho la maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko muno loletsa kusonkhana pagulu ndi kumachita mapemphero. Wapampando wa bungweli a Joseph Kachala ndi omwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre. Iwo ati zomwe achita maepiskopiwa ndi zothandiza pochepetsa kufala kwa nthenda ya COVID-19 kwa akhristuwa ndi ansembe awo maka padakalipano pomwe chiwerengero cha anthu opezeka ndi kachilomboka chikuchulukira. Tinganene kuti nkhaniyi tailandira bwino ndipo popanga nkhaniyi panali cholinga chofuna kuteteza moyo wathu ndi ansembe athu, anatero a Kachala. Mmawu ake mlembi wa bungweli a Anderson Gama alangiza akhristu a mpingowu kupewa kunyoza maepiskopiwa kudzera mmasamba a mchezo pa nkhaniyi. Akhritsu eni ake tiwalimbikitse kuti azipemphera pawokha pamene tili mu nyengo yosapita ku tchalitchi imeneyi, anatero a Gama. Iwo apemphanso akhritsu kuti apeze njira zosamalira ansembe mu nyengoyi poganizira kuti kutseka kwa tchalitchi ndiye kuti anthunso samakhala ndi nthawi yopereka mphatso zapaguwa.
13
Amuna Awiri Afa Pokumba Golide ku Makanjira Anthu awiri afa nthaka itawakwilira kumalo oletsedwa omwe anthu akuchitako migodi ati pofuna kupeza miyala ya mtengo wapatali ya golide ndi ina mphiri la Namizimu mdera la mfumu yayikulu Makanjira mboma la Mangochi. Watsimikiza za ngoziyi-Maida Malingana ndi ofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Inspector Rodrick Maida anthuwo akuti akhudzidwa ndi imfayi dzenje lomwe amakumba pofukula miyala ya mtengo wapataliyo litagumukira ndi kuwakwilira. Amuna-wa ndi a Issa Saladi ndi a Matola Bakali onse anali a zaka 22 zakubadwa. Ngozi-yi inachitika pa 9 January 2019 mdera la Mtiule mbomalo. Matupi a anthuwo atawatengera pa chipatala cha Makanjira ndi komwe anatsimikizira achibale kuti amunawo anafa kamba kobanika. Malemu Issa Saladi komanso Matola Bakali anali ochokera mmudzi mwa Chiwoko mfumu yayikulu Makanjira mboma la Mangochi.
14
Tsogolo la fizi silikudziwika Zenizeni pankhani yoti fizi yokwera msukulu za sekondale ndi sukulu za ukachechenjede za boma ipitilire kapena ayi zidziwika posachedwapa unduna wa zamaphunziro ukamanga mfundo, mneneri wa undunawu wauza Tamvani. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Iyi ndi nkhani yomwe Amalawi ambiri akumva nayo litsipa polingalira kuti mwezi wamawawu akuyenera kubowola matumba pankhani ya fizi zomwe posachedwapa unduna wa zamaphunziro udalengeza kuti zakwera. Malingana ndi mneneri wa undunawu, Rebecca Phwitiko, undunawu ukudikira kalata yochokera ku Nyumba ya Malamulo yokhudza zomwe nyumbayi idamanga pankhaniyi. Ophunzira a pasekondale ya Zingwangwa mumzinda wa Blantyre. Ena sapitiriza sukulu kaamba ka kukwera kwa fizi Sukulu zonse ndi mtundu wonse Amalawi udziwitsidwa za tsogolo la nkhaniyi posachedwa tikalandira kalata ya ku Nyumba ya Malamulo pa zomwe idamanga, adatero Phwitiko. Nkhaniyi idakambidwa mNyumbayi pamkhumano womwe wangothawu pomwe aphungu otsutsa boma adadzudzula kukwenza ka fiziku kuti kwabwera panthawi yolakwika. Ngakhale padali zovuta zingapo, aphunguwo adakambirana nkhaniyo mpaka kugwirizana kuti ndi yofunika kuwunikidwa bwinobwino. Mneneri wa Nyumbayi Leonard Mengezi adati pakadalipano sangapereke yankho lokhudza zomwe aphunguwo adakambirana poti nkhani ikakambidwa mNyumbayi imayenda mndondomeko zosiyanasiyana isadakhazikitsidwe. Mmene zidakambidwira mNyumba ya Malamulo muja, nkhaniyi imayenera kupita mmanja mwa komiti ya zamaphunziro kenako komiti yovomereza mfundo za boma isanapite kuunduna ndiye chitsekereni mkhumano mpaka pano sindidamve kalikonse, adatero Mengezi. Iye adati nkomuvuta kulondoloza nkhaniyi ndi makomitiwo kaamba koti anthu ali patchuthi ndiye sangapereke yankho logwira pokhapokha atabwerera mmaofesi awo tchuthi chikatha. Nkhawa yaikulu fizi yokwerayi ikaloledwa ndi ana asukulu omwe alibe pogwira kaamba koti akhoza kulephera kuphunzira ngakhale atakhala anzeru. Koma Phwitiko adati nkhani ya mthumba isabweretse njengunje chifukwa pali ndondomeko zothandizira anthu ovutikitsitsa omwe sangakwanitse kulipira fizi zokwerazi. Tikudziwa kuti pali anthu ena ovutikitsitsa oti ngakhale fizi zisadakwere ankalephera kulipira, koma pali njira yothandizira anthu oterewa, monga ngongole kwa ophunzira a msukulu za ukachenjede komansothandizo la ulere kwa ophunzira a msukulu za sekondale, adatero Phwitiko. Iye adati ngakhale zili chonchi, pali ndondomeko yomwe ophunzira amayenera kutsata kuti apeze nawo mwayiwu pofuna kuti okhawo ovutikitsitsa ndiwo azipindula nawo. Kusankha anthu ovutikitsitsawa kumachitika mmaboma chifukwa ndimo muli anthu omwe amadziwa chilungamo cha anthuwo. Zimafunika mfumu ya kumudzi kwa munthuyo, ofesi ya DC ndi ofesi ya maphunziro (DEM),adatero Phwitiko.Phwitiko adati ophunzira ovutika koma omwe ali ndi abale omwe ali ndi njira zopezera ndalama sadawaike mgulu lopata ngongole kapena thandizo la fizi pofuna kupereka mpata kwa omwe alibiretu podalira. Iye adati thumba lomwe kumachokera ndalama zothandizirali ndi loperewera kufikira aliyense nchifukwa chake pali kusefaku. Tidachita dala kupereka ntchito yosefayi mmanja mwa maboma omwe ophunzirawo amakhala chifukwa ndiwo angadziwe wovutika weniweni chifukwa aliyense azifuna kupata nawo ndiye ife sitingadziwe kuti wovutika weniweni ndi uti, adatero Phwitiko.Iye adati kulengeza za tsogolo la fizi zitengera kuti zokambirana zatenga nthawi yaitali bwanji. Nkhaniyi ili apo, maofesi ambiri kuphatikizapo a mboma ali patchuthi cha Khrisimasi ndi chaka cha tsopano. Mabungwe omwe si aboma monga la mipingo la Public affairs Committee (PAC) ndi la zamaphunziro la Civil Society Education Coalition (CSEC) adati kukwenza fizi nkofunika kutengera momwe chuma chikuyendera. Mkulu wa bungwe la CSEC Benedicto Kondowe adati kukwenza fizi ndi njira yokhawo yotukulira maphunziro mdziko muno polingalira kuti zinthu zidakwera ndipo ndi momwe chuma chikuvutira mboma, mpovuta kutiboma palokha lingakwanitse kupereka ndalama zamaphunziro. Kondowe adati vuto ndi nthawi yomwe boma lakwezera fiziyi polingalira kuti anthu sadakonzekere.
3
Kusanthula gule wa likwata Likwata ndi mmodzi mwa magule amene amavinidwa pakati pa Ayao. Ndidali mboma la Chiradzulu mmudzi mwa Njeremba kwa T/A Mpama komwe adapezerera gule wa likwata, yemwe ena amamutcha kuti namkwakwala. Uyutu ndi gule amene amavina amayi komanso atsikana. Kodi uyu ndi gule wanji? Nanga adayamba liti? Mtolankhani wathuyu adakokera pambali mayi amene amatsogolera guleyu. Adacheza motere: Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Eee! Wefuwefu ameneyu kutopa kumene? Hahaha! Padalitu ntchito pamene paja. Si maseweratu kuvina gule ameneyu chifukwa akafika pakolasi timayenera tidzipinde basi. Tidziwane kaye. Ndine mayi Idesi Chiwaya, ndipo ndipo ndimatsogolera gululi. Kodi ndi gule wanji ameneyu? Ameneyu ndi gule wa namkwakwala, ena amati likwata. Cholinga cha guleyu nchiyani? Kusangalatsa anthu basi. Timavina tikasangalala monga zachitikira leromu kuti tangosangalala ndiye tidakumana kuti tivine basi anthu adyetse maso. Muli akazi okhaokha bwanji? Ameneyu ndi gule wa amayi, nchifukwa chake simudaonemo mwamuna kupatula awiri amene akutiimbira ngoma. Ndaonamonso tiasungwana, timeneti timaloledwanso kukhala mgulumu? Eya, amenewo ndiye eni gululi chifukwa ife takulatu ndiye timakhala nawo kuti Mulungu akatitenga iwowo ndiwo adzatsogolere gululi. Sitikufuna kuti gule ameneyu adzafe. Kodi guleyu saphunzitsa zoipa? Zoipa zanji? Ayi, ameneyutu ntchito yake ndi kusangalatsa anthu basi. Simukuona kuti guleyu angapangitse kuti tianamwali tija tisodzedwe mwachangu? Hahaha! Musandiseketse inu, amene aja ndi adzukulu anga. Ndimawayanganira ndipo palibe angachite zopusa ndi ana amenewa. Akukula mmanja mwanga. Dzina limeneli lidabwera bwanji? Dzina la guleli? Liti lomwe mukukamba? Ndikukamba la likwata Ndi dzina basi, kusonyeza gule wachikhalidwe pamene ena amati gule wa namkwakwala. Chifukwa chiyani kulipatsa dzina la likwata? Basi, nawonso makolo adakonda kuti apereke dzinali. Si zolaula zimenezi? Nanga mpaka likwata? Ayi, palitu maina a anthu ambirimbiri mdziko muno omveka ngati akulaulanso, kodi ndiye kuti anthuwo amachita zomwe dzinalo limatanthauza? Ife mukanena kuti likwata timatanthauza kuti ndi gule wosangalatsa basi. Kodi ndi gule wa chikhalidwe chiti cha anthu? Uyu ndi gule wa Anyanja. Ambiri akhala akunena kuti ndi wa Alhomwe, koma zoona zenizeni ndi zomwe ndikunenazi. Mavinidwe a guleyu andimaliza, tafotokozani momwe muchitira pamene mukuvina Ngoma ija ikamalira, ife timavina moitsatira uko tikuimba nyimbo zathu. Ndiye ikafika pakolasi, timachita ngati tikudumpha uko tikudula chiuno. Apa ndiye timagwadirira pansi ndi kuvina momatembenuka koma kumatembenuka ndi maondo kwinaku tikugundana ndi matako. Aka ndiye kavinidwe kake. Adakuphunzitsani ndani? Makolo athu. Ineyo makolo anga ankavina kwambiri ndipo atamwalira ndidapitiriza mpaka kupeza amayi anzanga. Tonse tilipo 10 kuphatikizapo ndi abambo a ngoma takwana 12. Abambo savina nawo chifukwa chiyani? Aaa! Inuyo mungakwanitse zomwe timachita zija? Eetu, nchifukwa timavina amayi okha. Mudayamba liti kuvina guleyu? Chaka ndiye sindingakumbuke koma ndimakumbukira kuti panthawiyo ndidali ndi zaka 33. Pano zaka zanga ndidaziiwala koma zaposa 50. Mumavina nthawi yanji? Timavina masana, moti nthawi zambiri timavina pazochitika monga pamisonkhano. Tavinirapo mtsogoleri wakale Bakili Muluzi komanso Bingu wa Mutharika. Atsogoleriwa amakwanitsa kuduka mchiuno chonchi? Ayi, amangochoka pampando ndi kumavina pangonopangono ndipo mapeto ake amapisa mthumba kutipatsa kangachepe. Kodi momwe munavinira apamu ndiye kuti mumathera pamenepa? Ayi, apatu tangovina kwa mphindi 5, koma tikati tivine moposera mphindi zimenezi mudakaona momwe timachitira. Malangizo kwa amene satsatira gule wa makolo Amenewo azikhala pafupi ndi makolo awo kuti asataye chikhalidwe cha makolo awo.
9
Amakonda ndalama Anatchereza, Ndakhala paubwenzi ndi msungwana wina koma vuto lake akuoneka wokonda ndalama. Tikangokumana, amandipempha ndalama. Timalankhulana nthawi zambiri pafoni koma mwezi ukangotha amati tikumane. Kodi ichi ndi chikondi? M, Lilongwe. Wokondeka M, Ameneyo sakuthandizani. Mkazi woika ndalama patsogolo si wa bwino. Taonani akuonetsa mawanga ake muli pa chibwenzi nanga mukadzakwatirana zidzatha bwanji? Mudzaona kuti pakati pa mwezi mavuto okha okha mbanja. Koma ukangotha mwezi si kusekerera ku chitsakano kwake. Mpeweni.
12
DPP idzudzula boma Chipani chakale cholamula cha Democratic Progressive (DPP) chati Amalawi angapitirire kusauka ngati boma la chipani cha Peoples (PP) silibwera msanga ndi ndondomeko zotukulira anthu mdziko muno potsatira kugwa kwa ndalama ya kwacha. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mneneri wachipanichi, Nicholas Dausi, komanso yemwe akufuna kudzaiimira PP pachisankho cha pulezidenti, Peter Mutharika, auza Tamvani msabatayi kuti boma latsopanoli lataya ndondomeko zina zomwe boma la DPP lidakhazikitsa kuti zitukule dziko lino. Malinga ndi Dausi, ulamuliro wa wa DPP udakhazikitsa ndondomeko zisanu ndi zinayi zotukulira dziko lino pansi pa chikonzero cha chitukuko cha Malawi Growth Development Strategy (MGDS). Izi ati nzachikwanekwane kuthandiza anthu koma boma la PP ati silikuzilabada ndipo mmalo mwake likungotsogoza kumanga komanso kuthothola anthu pantchito. Naye Mutharika, yemwe ndi mchimwene wa mtsogoleri wakale wa dziko lino Bingu, wati malinga ndikuchepa kwa chitetezo mdziko muno, anthu monga a bizinesi atekeseka ndi achipongwe komanso ambanda. Iye wati izi nzosakomera chuma cha dziko. Koma mneneri wa boma, Moses Kunkuyu, wati boma laika chidwi chachikulu pa mfundo zosankhika zokhazo zomwe zingapindulire Amalawi. Kuyambira pomwe chipani cha PP chidalowa mboma potsatira imfa ya Bingu wa Mutharika yemwe ankatsogoleranso DPP, chipani cha DPP chakhala chikudzudzula mfundo za boma la PP. Lamulungu pa 22 Julaye, Peter Mutharika pochititsa msonkhano mumzinda wa Lilongwe, adadzudzulanso boma la PP, ati mfundo zake nzosathandiza konse Amalawi. Koma Kunkuyu wati Amalawi ndiye mboni za boma la PP popeza ndi amene akudziwa choonadi pa nkhaniyi. Kodi tikhaliranji ndi ndondomeko zina zomwe sizikuoneka mutu wake? adafunsa Kunkuyu. Iye wati ndiwodabwa ndi phokoso lomwe chipani cha DPP chikuchita pomangodandaula koma osapereka maganizo pa momwe boma lingathetsere mavuto mokomera Amalawi. Dausi adati miyezi inayi ndiyokwanira kuti boma la PP lidayenera kuyamba kuonetsa zipatso zaulamuliro wake. Chongotenga boma, chipanicho chidayenera kuonetseratu kuti chikutsatira mfundo zotukula miyoyo ya anthu, adatero iye. Iye adati kuyesera kupereka maganizo kungakhale kusewera padiwa, ati boma latsopanoli, lomwe silikumva chidzudzulo komanso silikuchedwetsa unyolo, lingamukokere kundende. Apa Kunkuyu wati atsogoleri ena, monga mtsogoleri wakale wa dziko lino Bakili Muluzi komanso mtsogoleri wachipani cha MCP, John Tembo, akhala akupereka maganizo awo pa momwe boma latsopanoli lingakonzere zinthu koma ena, monga a DPP, akungolalata chabe, osaunikira zoyenera kuchita. Amalawi ndi amene angaweruze bwino pa za ulamuliro wa PP, adatero Kunkuyu. Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wachibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda, wati ngati lero Amalawi ali opemphapempha komanso osauka kwambiri nchifukwa cha ulamuliro woipa wachipani cha DPP. Iye wati boma la DPP silinkamva zonena anthu, kotero lisakhale ndi zolankhula chifukwa mmanja mwawo ndi mwakuda. Ngati akufuna kuti anthu amvere zolankhula zawo abwere kaye poyera nkupepesa Amalawi pa zomwe ulamuliro wa DPP udachita; Amalawi avutika. Bwezi tili poipitsitsatingothokoza kuti Mulungu amalikonda dziko lino, adatero Billy Banda. Banda adalangizanso boma la PP kuti lisaiwale komwe likuchokera kotero likuyenera kuika pamtima zofuna za Amalawi. Mfumu yaikulu Makwangwala ya mboma la Ntcheu yati kumeneko zinthu zili bwino ndipo anthu ndi mafumu akumana sabata ikudzayi kuti akambirane za ndondomeko ya chitukuko ya mthandizi. Mu ndondomekoyi, anthu amalandira ndalama pomwe agwira ntchito monga kulambula misewu. Edward Chimkwita wa mmudzi mwa Malika kwa T/A Likoswe mboma la Chiladzulu wati DPP ndi imene idaononga dziko, koma pano zikusintha. Koma mfumu ina mboma la Mwanza yati zomwe achipani cha DPP akunena nzoona kotero boma likonze pomwe sipali bwino. Mmatumba mwa anthu mulibe ndalama koma katundu wakwera mtengo. Chitetezo chastika ndipo akuba akumasula mbuzi za eni dzuwa likuswa mtengo. Apa zikungokhala ngati tabwereranso kale. Malonda nawo sakuyenda; kilogalamu imodzi ya nandolo tikugulitsa pa mtengo wa K30, zomwe sitikupindula nazo. Chikhalirecho, Fanta tikugula pa K90 mwinanso K120, idatero mfumuyo yomwe siidafune kutchulidwa. dzuwa likuswa mtengo.
11
Mowe Pati: Amuna ndi dothi Tsikulo, mkulu wina adati tipite mtauni tikaone umo zikukhalira chifukwa mikangano ya oitanira basi komanso oyanganira mzinda ikukhala bwanji. Tidafika kumasitandi kumenetu kudali nkhondo yaikulu ati kulimbirana kuti amaminibasi ziwathera bwanji. Kodi azilipira kuti? Vuto lidalipo ndi lakuti kodi oyendetsa minibasi ndi mabwana awo, angakhale ndi zikwanje zakuthwa ndani? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zitayeni. Lidali tsiku la amayi padziko lonse ndipo tidakhala malo aja timakonda pa Wenela. Adatulukira Mowe Pati kuchoka kwawo kwa Mkando, apooo! Kweeni, munasowatu zedi. Zikuyenda bwanji? adafunsa Gervazzio, wapamalopo. Ndilipo. Kodi mwakumbuka zija ndinkanena za agalu athu ndi zothamangitsa anthu a ku China? Zija ndinkanena kuti atibwezere agalu athu. Ndidali mwana masiku amenewo, adatero Mowe Pati. Koma mwati amuna ndi chiyani? adafunsa Abiti Patuma, uku akumvera nyimbo ya Nilibe Pulobulemu. Abale, amuna ndithu ndi dothi. Ndipo musamawatchule kuti amuna ndi ana monga mwakhala mukunenera. Zitheretu, adatero Mowe Pati. Inu, ndithu kumanja kudali Coca-Cola, koma ankamwa Fanta munthu wa mayi. Aaaaargh! Mowe, mukunena zoona? Munganene kuti amuna ndi dothi? Chifukwa chiyani? adafunsa Abiti Patuma. Eya, amuna ndi dothi, nanga si Mulungu adawalenga kuchoka kudothi! adayankha. Koma kuganiza kwinaku ungamangoti munthu uyu amasuta wamkulu fodya. Tsono mukatero, ndiye kuti bambo a kunyumba aja nawonso ndi dothi? Nanga ana anu aamuna aja nawonso ndi dothi? ndidafunsa. Mwati bwanji? adafunsa Mowe Pati. Ndikuti, mukamati amuna ndi dothi mukutanthauza kuti uja adaimba nyimbo ya Nilibe Pulobulemu mokopera, inde Moya Pete, nayenso ndi dothi? adafunsa Abiti Patuma. Mowe Pati adangoti duu! Ngati akumangidwa madiledi. Abale anzanga, inetu izi sindingayankhireko kanthu. Kodi si ngati zija amanena za kunena kwa ndithendithe Nanthambwe nkudzitengera. Dr Getu Getu wa Moya Pete.
15
Aliza abale pa Khrisimasi chifukwa cha mowa Chaka chilichonse, 25 December ndi tsiku lachisangalalo koma chaka changopitachi lidali lachisoni mbanja la a Moses a kwa Chinthambwe mfumu yaikulu Chilowoko mboma la Ntchisi. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Patsikulo, mmodzi mwa a pabanjalo, Steven Moses wa zaka 47, adamwalira atamwa mkalabongo wochuluka komanso osadyera. Mngono wa malemuyo yemwe amakhala kufupi naye ku Area 25 mumzinda wa Lilongwe, Amos Moses, adati mbale wakeyo adavomereza za nkhaniyo ndipo adati adamva kuchokera kwa wina kuti mbale wakeyo sanali bwino. Amos: Idali imfa yowawa Iye adati mmbuyomo sadalandireko lipoti lilironse loti mbale wakeyo samamva bwino ndipo atamva uthengawo adathamangira kunyumba ya malemuyo komwe adakapeza atauma kale. Tidamupeza atauma pamphepete pake pali mabotolo a mkalabongo, ena mulibe kanthu ena osayamba. Idali imfa yowawa, adatero Amos. Mneneri wapolisi ya Kanengo, Alfred Chimthere, adatsimikiza kuti bamboyo adamwalira kaamba ka mowa. Titalandira uthenga wa imfayo, tidathamangirako ndipo titatengera mtembowo kuchipatala cha Kamuzu Central, madotolo adatsimikiza kuti imfayo idachitika kaamba ka mowa oposa mlingo, adatero Chimthere. Aaron Tsokwe, yemwe amagulitsa kanyenya mumsika wa Nsungwi komwe malemuyo amakonda kumwera mowa adati mkuluyu amakonda mowa wa kachasu ndi wa mmasacheti ndipo ngakhale amakonda mowa choncho, adalibe mbiri ya ndewu. Anthu ambiri tidamuzolowera kuti amakhala chiledzerere. Iye kwake kudali kulongolola, osati ndewu, adatero Tsokwe. Mkulu wa bungwe lolimbana ndi mchitidwe ogwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo la Drug Fight Malawi yemwenso amayendetsa mgwirizano wolimbikitsa kuti pakhale ndondomeko zoyendetsera kagwiritsidwe ntchito ka mankhwala wa Malawi Alcohol Policy Alliance, Nelson Zakeyu, adati imfa zotere zikunka patsogolo kaamba kosowa ndondomeko zoyenera. Iye adati izi zikadatha boma likadakhala ndi ndondomeko zoyenera komanso njira zamphamvu zoonetsetsa kuti ndondomekozo zikugwiradi ntchito. Timatsogoza kunena kuti anthu azidyera akafuna kumwa mowa mmalo mongoletsa kuti anthuwo asamamwe, adatero Zakeyu. Mneneri wa polisi mdziko muno James Kadadzera adauza Msangulutso Lachinayi kuti ali mkati mosonkhanitsa ngozi zomwe zachitika mkatikati mwa nyengo ya zisangalalo ntchito yomwe ikukhudza kusonkhanitsa chiwerengero cha imfa zokhala ngati ya Steven. Iye adati apolisi amagwira ntchito usana ndi usiku kuwonetsetsa kuti anthu akutsatira malamulo ndi cholinga chopewa zinthu zosakhala bwino monga imfa zopeweka ngati za uchidakwa. Malamulotu alipo monga pamlingo wa zaka zovomerezeka kumwa mowa, nthawi yomwera mowa komanso mamwedwe oyenera. Ichi nchifukwa chake nthawi zina apolisi amayendera malo omwera kufuna kuona ngati ndondomeko zikutsatidwa, adatero Kadadzera.
15
Osinthasintha zipani ngosadalilikaAkadaulo Andale osinthasintha zipani ndi osadalilika, ndipo amachita izi chifukwa cha dyera, atero akadaulo ena a zandale. Koma ena mwa andalewo atsutsa izi. Akadaulowo, Mustapha Hussein, Happy Kayuni ndi Ernest Thindwa adanena izi polankhula ndi Tamvani paderapadera potsatira mchitidwe wa andale ena wosamuka mzipani zawo ndi kulowa zina umene umachulukira makamaka nthawi ya chisankho ikayandikira. Mwachitsanzo, Lamulungu Brown Mpinganjira, Ken Lipenga ndi Henry Phoya, omwe adakhalapo nduna za boma mmaulamuliro a zipani zina mmbuyomu, adalengeza kuti alowa chipani cha DPP limodzi ndi mbusa Daniel Gunya. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mutharika (Pakati) kulandira anayiwo Lamulungu Izi zili choncho, miyezi ingapo yapitayo Sidik Mia, yemwe adakhalaponso nduna mmaboma a mmbuyomu, naye adalengeza kuti walowa MCP ndipo akufuna mpando wa wachiwiri kwa mtsogoleri wachipanicho. Hussein adati andale osinthasintha zipani ndi wosadalirika chifukwa phindu lawo ndi losaoneka ndipo adangotsala maina okha. Iye adati anthu akudziwa kale kuti ndi wosakhazikika kotero kuwatsatira nkudzipachika wekha. Ndimaina aphindu koma sangasinthe zinthu mchipani chifukwa cha mbiri zawo zoyendayenda. Adayamba ndale kalekale ndipo anthu amawadziwa komanso amadziwa mbiri zawo, adatero Hussein. Polankhulapo za akuluakulu akhamukira ku DPP, Kayuni adati anayiwo akungofuna kudzawolokera pamsana pachipanicho kuti apeze mipando ya uphungu pachisankho cha chaka chamawa. Anthuwa akuchokera mmadera momwe DPP ili ndi mphamvu ndipo akudziwa kuti kuimira chipani china pampando wa uphungu, akhoza kugwa. Iwo akungoponya khoka kozama. Komabe sitikuwadabwa chifukwa ndimo alili, watero Thindwa. Malinga ndi Kayuni, pambali posintha zipani ngati malaya chifukwa cha dyera, vuto lina ndi la kusowa mfundo kwa zipani. Iye adati zipani za mmaiko ena zimakhala ndi mfundo zokhazikika choncho munthu amadziwiratu zomwe chipanicho chimafuna kukwaniritsa, osati kuphinduka monga zimachitira zipani za ku Malawi. Chipani chimakhala ndi mfundo zokhazikikazimene amatsata. Koma kuno kwathu chipani chimayamba mfundo iyi, kenako nkutembenuka. Amene amatsatira mfundo imene yasiyidwa amatuluka chipanicho kukalowa china, adatero Kayuni. Iye adati kubwera kwa alendowo kumangobweretsa chilimbikitso nthawi yochepa chifukwa ngosadalilika. Ndipo kubwera kwawo kukhonza kubweretsa nthenya mzipani akulowazo chifukwa a mkhalakale amaona ngati akufuna kulandidwa mipando. Izi zaoneka kale kuchipani cha MCP kumene kubwera kwa Mia kwadzetsa mpungwepungwe, pomwe wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipanicho Richard Msowoya ndi akuluakulu ena adzudzula mtsogoleriyo Lazarus Chakwera pogodokera khosi kwa Mia. Asanalowe chipani cha MCP, Mia adakhalapo mzipani za UDF, DPP komanso PP. Polankhula ndi Tamvani, iye adatsutsa zoti dyera ndilo lamukokera ku MCP. Iye adati chiyambireni ndale, sadakhaleko ndi mtima odzinthangatira yekha koma kutumikira anthu nchifukwa chake adalowa mchipani cha MCP chomwe mfundo zake nzokomera Amalawi. Mpinganjira adali mu UDF ndipo adachoka kukayambitsa chipani cha NDA. Chipani cha PP chitalowa mboma, iye adalowera komweko koma zinthu zitavuta pachisankho cha 2014, iye adachitaya. Iye adati mbiri yake isakhale chomuyezera pandale ndipo adati walowa DPP pofunanso kutumikira Amalawi. Boma ili limaika mtima pamiyoyo ya anthu, nchifukwa chake ndikufuna kugwira nalo ntchito ndipo ndidzakhala nacho pamtendere ndi pamavuto pomwe, adatero Mpinganjira. Lipenga wakhalako mmipando ya unduna kuyambira mboma la chipani cha UDF chomwe adachisiya kukalowa DPP momwenso adali nduna koma adachitsika mtsogoleri wa chipanicho Bingu wa Mutharika atangomwalira mu 2012 nkulowa PP yomwe idalowa mbwalo.Samayankha foni yake. Phoya adayamba ndi chipani cha UDF momwe adali nduna ndipo adasintha thabwa kulowa DPP kenako adalowa MCP, kumene sadakhalitseko. Iye adafunsa kuti timutumizire mafunso, amene sanayankhe.
11
MLS yalasa! Bungwe la akadaulo a za malamulo mdziko muno la Malawi Law Society (MLS) ladzudzula zipani za ndale, mkulu wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), apolisi komanso okonza zionetsero pa mkokemkoke umene wabuka kutsatira zolengeza za chisankho cha pa 21 May. Bungwe la MEC motsogozedwa ndi Jane Ansah lidatulutsa zotsatira za chisankho pomwe lidati mtsogoleri wa chipani cha DPP Peter Mutharika ndiye adapambana chisankhocho motsatizana ndi Lazarus Chakwera wa MCP pomwe Saulos Chilima wa UTM adali wa chitatu. Koma Chakwera ndi Chilima adatengera kukhoti MEC ndi DPP ponena kuti chisankhocho sichidayende bwino. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ansah: Ndiwayankha a MLS Pambuyo pa izi, mgwirizano wa mabungwe omenyera ufulu wa anthu wa Human Rights Defenders Coalition (HRDC) wakhala ukukonza zionetsero zofuna kuti Ansah atule pansi udindo. Pazionetserozo pakhala pakuchitika zipolowe ndipo katundu wina wa boma komanso wa anthu ena wakhala akuonongedwa. Lachitatu MLS idalembera kalata Mutharika, Chakwera, Chilima, Ansah, mkulu wa HRDC Timothy Mtambo, sipikala wa Nyumba ya Malamulo Catherine Gotani Hara komanso mkulu wa apolisi Rodney Jose, kutambasula zolakwika zimene iwo akuona. Chikalatacho adasayinira ndi mlembi wa MLS Martha Kaukonde ndipo chidati chikudabwa kuti ngakhale pali ziwawa zoti Ansah achoke, iye sakuchoka. Katundu akuonongeka wochuluka. Bwanji osangotula pansi udindowo? idatero kalatayo. MLS idadzudzula atsogoleri a ndalewo ati chifukwa sakuuza bwino owatsatira kuti mlandu umene uli kukhoti ukhonza kukomera aliyense. Tikudabwa kuti andalewo akuchititsa misonkhano ngati ndi nthawi ya kampeni mmalo mowakonzekeretsa owatsatira kuti khoti likhoza kugamula mosawakomera malingana ndi zonenedwa mukhoti. Tikumbutsane kuti ndi MEC komanso bwalo la milandu lokha limene linganene ngati chisankho chidayenda bwino kapena ayi. Zopereka maumboni pa mchezo wa Internet sizitithandiza, idatero kalatayo. Kalatayo idadzudzulanso Mutharika kaamba kolola otsatira chipani chake kuchita zionetsero za mpikisano motsutsana ndi amene akuti sadapambane. Sabata yatha, otsatira chipani cha DPP adayenda mumzinda wa Blantyre ndipo adakathera kunyumba ya Sanjika kumene Mutharika adawatsimikizira kuti chipani chake chipitiriza kulamula mpaka 2084. Iyo idati HRDC iyenera kulingalira mozama za zionetsero zimene yakhala ikukonza ngati zingapindulire mtundu wa Amalawi. MLS idadzudzula apolisi polephera ntchito yawo yoteteza Amalawi ndi katundu wawo nthawi ya zionetserozo. Pamene ofuna kuti Ansah achoke adachita zionetsero, otsatira ena adamenya anthuwo ndipo apolisi amangoyangana. Asirikali a Malawi Defence Force (MDF) ndiwo adaletsetsa anthuwo. Chofunika tsopano nchoti pakhale kukambirana pakati pa onse okhudzidwa kuti bata ndi mtendere zibwerere mdziko muno, idatero kalatayo. Pempho loti pakhale kukambirana likudza pomwenso bungwe la mipingo loona momwe zinthu zikuyendera mdziko muno la Public Affairs Committee (PAC) lakumana kale ndi Chakwera komanso Chilima amene avomereza kukambiranako. Wapampando wa bungwelo Ambuye Thomas Msusa ndiye akuyenera kuluzanitsa atatuwo ndipo akuyenera kukumana kaye ndi Mutharika kuti akonze tsiku la zokambiranazo. Polankhula ndi mtolankhani wathu, Chakwera adati adalandira kalatayo koma amayembekezera kumva kuchokera kwa alangizi ake pa za malamulo asanayankhepo kanthu. Chilima naye adati adalandira kalatayo koma adati mneneri wa chipani chake Joseph Chidanti-Malunga ndiye angayankhe. Koma Malunga adati sanakambirane zoti anene. Ansah adati ayankha a MLS pa zomwe adalembazo. Mlandu wa chisankho ulowanso mbwalo Lachisanu likubwerali mumzinda wa Lilongwe. MLS ikutenga nawo mbali pamlanduwo pounikira bwalolo zina ndi zina zokhudza malamulo.
7
Msilikali wa Ndende Anjatidwa ku Zomba Wolemba: Thokozani Chapola Apolisi ku Zomba lachinayi agwira msilikali wina wogwira ntchito ku ndende yaikulu ya Zomba pomuganizira kuti amathandizira mkayidi wina kulowetsa ma simukadi a foni ya mmanja mu ndendemo. Wofalitsa nkhani za apolisi mchigawo chakumvuma, Inspector JOSEPH SAUKA komanso wofalitsa nkhani za ndende mdziko muno Supretendent CHIMWEMWE SHAWA atsimikiza za kumangidwa kwa msilikali wa ndendeyu STEVEN CHINGANDA. Inspector Sauka wati apolisi anamva mphekesera yoti anthu ena akumabera anthu powalembera mauthenga pa phone zawo za mmanja kuwanamiza kuti awina mphotho. Iwo ati anayamba kufufuza za nkhaniyi ndipo adapeza kuti anali mkayidi wina dzina lake GOODSON MANDALA yemwe akugwira ukayidi wake ku ndende ya Zomba ndipo anamupeza ndi ma simukadi a airtel okwana makumi asanu ndi limodzi 60. Wofalitsa nkhani za apolisi mchigawo chakummawayu wati mukufufuza kwawo anapeza kuti ma simukadi onsewa anali olembetsedwa ndi chiphaso cha unzika cha JAFALI KAPHULA ndipo yemwe amalembetsa anali mkazi wake wa mkayidiyu. Sauka wati atafufuzabe anapeza kuti Steven Chinganda yemwe ndi msilikali wolondera akayidi ku ndende ya Zomba ndi yemwe amatumikira kukasiya ma simukadi kwa mkayidiyu mu ndendeyo. Padakalipano a Steven Chinganda awatsekulira mlandu wolowetsa zinthu zoletsedwa ku ndende komanso kugwiritsa ntchito ofesi yake molakwika. Chinganda amachokera mmudzi mwa JEZE mfumu yaikulu MPONDA mboma la Mangochi.
7
Amalawi alemekeza Bingu Amalawi mzigawo zonse mdziko muno apereka ulemu wawo wotsiriza kwa yemwe adali mtsogoleri wa dziko lino, Bingu wa Mutharika. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mutharika adamwalira pa 5 Epulo atadwala mtima. Thupi lake lomwe lidatengeredwa mdziko la South Africa, lidafika mdziko muno Loweruka pa 14 kudzera pabwalo la ndege la Kamuzu mumzinda wa Lilongwe. Kuyambira Loweruka mpaka Lasabata, akuluakulu aboma ndi abanja motsogozedwa ndi mtsogoleri wadziko lino, Joyce Banda, adapereka ulemu wotsiriza kwa malemuwa. Lolemba pa 16, thupili lidatengedwa ku Nyumba ya Malamulo mumzindawo komwe Amalawi akuchigawo chapakati adapereka ulemu wawo mpaka pa 17. Thoko Loga wa ku Kawale yemwe amapenta galimoto adati adzakumbukira Mutharika kumbali ya chimanga komanso kumangidwa kwa misewu ndi nyumba akuluakulu mumzindawo. Nditangoona nkhope ya malemu ndidagwidwa ndichisoni ndipo ndidalephera kudzigwira koma kukhetsa msonzi. Lachitatu pa 18, thupili adalitengera ku Mzuzu komwenso anthu adapereka ulemu wotsiriza mpaka Lachinayi. Bob Pota yemwe ali mumzinda wa Mzuzu ndipo akuchita maphunziro aukachenjede a Community Development akuti sadzaiwala Mutharika pothetsa njala mdziko muno. Lachinayi cha mma 12 koloko masana thupiro limayembekezereka kunyamulidwa kupita ku Blantyre komwe anthu akuchigawo cha kummwera akapereke ulemu wotsiriza. Thupilo likuyembekezeka kunyamuka lero kupita ku munda wa Mutharika wa Ndata mboma la Thyolo ndikukalowa mmanda Lolemba pa 23.
11
Sukulu ya Mkombaphala Ikufewetsa Ntchito ya Aphunzitsi Wolemba: Sylvster Kasitomu Kutumiza ana ku sukulu za mkombapahala ati kukuchepetsa ntchito ya aphunzitsi pomwe apita ku sukulu za primary. Mlangizi wa aphunzitsi amsukulu za primary mu zone ya Chimwala mboma la Mangochi mayi Nancy Ndazamo ndi omwe anena izi powuza mtolankhani wathu. Iwo ati ndi khumbo lawo kuti sukulu iliyonse ya pulaimale ikhale ndi sukulu ya mkombaphala komwe ana angaphunzireko mmene angulumikizirane ndi aphunzitsi zomwe zikuchititsa anawa kuti akapita ku primary azikachita bwino. Mwazina mayi Ndazamo apempha makolo kuti azipititsa ana awo ku sukulu za mkomba phala kuti azakhale ana anzeru pomwe apita ku primary. Ana omwe akuchokera ku sukulu za mkombaphala akuthandiza kwambiri pa tchito yophunzitsa maka ife aphunzitsi a ku primale kaamba koti amakhala kuti pamene akukayamba sukulu akudziwa kupinda chilembo zomwe zimachititsa kuti aphunzitsiwa asakhale ndi ntchito yomudziwitsa kugwira kwa pensulo, anatero mayi Ndazamo. Malinga ndi mkulu wa zamaphunziroyu, madera ambiri mdziko muno amkumana ndi vuto la kusowa kwa sukulu za mkomba phala kaamba kosowa thandizo loti athe kusamalira anawa.
3
Otsutsa adzudzula MEC Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) liyenera kutambasula bwino za pangano lake ndi bungwe limene likupereka zitupa za unzika la National Registration Bureau (NRB) pa zoti lidzagwiritsa ntchito zitupazo pa kalembera wa chisankho cha 2019, watero kadaulo pa ndale Mustafa Hussein. Zipani za ndale, makamaka zotsutsa boma zakhala zikunena kuti chikonzero cha MEC nkufuna kudzathandiza chipani cha DPP kubera mavoti. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kalembera wa nzika ali mkati Mwati mudzagwiritsa ntchito zitupa za unzika kuti Amalawi alowe mkaundula wa zisankho. Apatu mpofunika kuti pamveke bwino chifukwa anthu akusokonekera, adatero Hussein. Zipani zotsutsa boma zakhala zikudandaula ndi ganizo la MEC lodzagwiritsa ntchito zitupa za unzika kuti munthu adzalowe mkaundula wa chisankho cha 2019. Zipanizi zakhala zikubweretsa nkhaniyi mNyumba ya Malamulo momwe aphungu akukambirana za bajeti ya 2017/18 ndipo moto weniweni udabuka lolemba lapitali pa nkhumano yomwe bungwe la MEC lidapangitsa kuti lifotokozerane ndi zipani nkhani yokhudza chisankhochi. Nthumwi za zipani zotsutsazi makamaka za Malawi Congress Party ndi Peoples Party, zidabooleza kuti zikukhulupilira kuti ganizoli ndi njira imodzi yofuna kudzabera chisankhochi ndipo zidanenetsa kuti sizilola kuti pulaniyi idutse. Phungu wa kummawa kwa boma la Dowa Richard Chimwendo-Banda wa Malawi Congress Party (MCP) adati akuona kuti MEC ikukonza zodzathandiza chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) kubera chisankho. Iye adati ndiwodabwa ndi kukakamira kwa bungwe la MEC kuti lidzagwiritse ntchito zitupa za unzika popanga kaundula wa anthu odzaponya voti chonsecho silikutengapo gawo lililonse pa zakapangidwe ka zitupazi. Bungwe la MEC lidali kuti pomwe nthambi yopanga kalembera wa zitupazi imayamba ntchito yake? Tili ndi chikhulupiliro kuti ali ndi mapulani odzabera chisankho ndipo ndikuuzeni kuti ulendo uno sitikulekelerani, adatero Chimwendo-Banda. Iye adati bungwe la MEC lisiye kulowerera ntchito za eni ndipo lipange pologalamu yake yakalembera wa mkaundula wa chisankho mmalo modalira kuwolokera pamsana pa anzawo. Wampampando wa bungwe la MEC Jane Ansah yemwe ndi woweruza milandu ku khothi lalikulu la apilo sadakondwe ndi zomwe adanena aphunguwo ndipo adawadzudzula kuti nawo akulephera udindo wawo posafotokozera anthu awo za kufunika kwa zitupazi. Iye adatsutsa zoti bungweli lili ndi maganizo odzabera chisankho mwanjira iliyonse koma kuti likufuna kuti anthu ovomerezeka okha ndiwo adzaponye voti mu 2019. Nduna ya za mdziko ndi chitetezo Grace Chiumia adavomera kuti kalembera wa zitupa za unzika ikukumana ndi zokhoma monga kufaifa kwa zipangizo zogwiritsa ntchito.
11
Ayamikira Boma Kamba Komanga Opalamula Mu Ulamuliro wa DPP Anthu komanso mabungwe osiyanasiyana ati sakuona vuto lililonse pamene anthu ena omwe anali mboma lapitali akumangidwa ndi apolisi kamba kowaganizira kuti anapalamula milandu yosiyanasiyana mu mthawi ya ulamuliro wa chipani cha Democratic Progressive (DPP) chomwe padakalipano chinatuluka mboma. Mmodzi mwa anthu omwe amangidwa-Chisale Mmodzi mwa anthu omwe anapikisana nawo pa mpando wa uphungu wa nyumba ya malamulo mdera la kumpoto chakumadzulo kwa boma la Phalombe Kelvin Jumbe wanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Blantyre. Iye wati pakufunika anthu omwe ali mmaudindo osiyanasiyana mboma azilemekeza malamulo komanso kuchepetsa mchitidwe owononga chuma cha dziko maka pa nthawi yomwe ali mmaudindo osiyanasiyana othandiza pa ntchito zotukula dziko lino Izi zikuza pamenenso magulu ena akudzudzula boma ati kamba komanga anthu ena omwe anali mboma la chipani cha DPP zomwe akuganiza kuti ndi zikuchitika pa zifukwa za ndale.
7
Lule adachita chokongontha Lipoti la chipatala lomwe dotolo wotchuka pa zofufuzafufuza, Charles Dzamalala, watulutsa latsimikiza kuti woganiziridwa kusowetsa mwana wa chialubino, Buleya Lule adachita kuphedwa ndi shoko ya magetsi. Izi zikutsutsana ndi zomwe apolisi adatulutsa kuti imfa ya Lule idali ya chilengedwe ndipo palibe adatasa manja ake pa iye. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Akuti achitepo kanthu: Jose Lule adafa ali mmanja mwa apolisi. Iwo atamunjata pomuganizira kuti amakhudzidwa ndi kusowetsedwa kwa Goodson Makanjira, 14, yemwe adali mwana wachialubino wa mboma la Dedza.
15
Imfa ya Chikulamayembe yautsa mapiri pachigwa Mkangano wabuka mbanja la a Gondwe pa za munthu yemwe akuyenera kulowa ufumu wa Chikulamayembe. Mpungwepungwewu wayamba potsatira imfa ya Walter Gondwe, yemwe adali mfumu Chikulamayembe. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malemu mfumu Chikulamayembe Mfumu Chikulamayembe idamwalira pa November 29 2018. Isadamwalire idasankhiratu mwana wake, Mtima Gondwe, kuti ndiye adzalowe ufumu wake ndipo mafumu ena adavomera nkusainira panganoli ndi Chikulamayembe asadatsikire kulichete. Koma atamwalira zinthu zidasokonekera kaamba koti mafumu ena akuti Mtima sangalowe ufumu mmalo mwa atate wake kaamba koti ufumuwu si wa banja limodzi, koma umazungulira mmabanja 12. Mafumu Achitumbuka akuti kuchokera mu 1795 pamene ufumu wa Chikulamayembe adaukhazikitsa, wazungulira mmabanja 9. Mabanjawa ndi a Gonapamuhanya, Kampungu, Pitamkusa, Bwati woyamba ndi wachiwiri, Bamantha, Mkuwayira ndi Mujuma. Mabanja atatu omwe atsala kuti nawonso alongedwe ufumu wa Chikulamayembe ndi a Mkupa, Mzakwacha ndi Bongololo. Pachifukwa ichi, mabanja ena akuti ufumuwu sukuyenera kubwerera mbanja la Walter moti akadandaula ku bwalo lalikulu la milandu mu mzinda wa Mzuzu. Iwo akuti ufumu wa Chitumbuka, umasiyana ndi wa Chingoni, kaamba koti sukhala wa banja limodzi. Pofuna kumvetsetsa nkhaniyi, Msangulutso udacheza ndi mafumu 6 a mbanja la a Gondwe omwe ndi a Chikalamba, Bongololo, Mkupa, Kalizga, Tawona ndi a Webster omwe atsimikiza kuti adakasumadi ku khoti. Mneneri wa mafumuwa, Stowel Kalizga Gondwe, adalongosola kuti ufumu wa Chikulamayembe wakhala ukuzungulira mbanja limodzi kuchokera nthawi ya John Hardy Gondwe mu 1977. Atamwalira John Hardy ufumu sumayenera kupita kwa mwana wake, Walter Gondwe, koma kwa Bwati Gondwe. Koma chifukwa choti Walter amakhala bwino ndi anthu, komanso adali wophunzira mafumu adaganiza zomulongabe ufumu, adatero gogo Chikalamba. Apa mpomwe padapindika nkhani. Padakali pano ife aku banja la a Gondwe tikufuna ufumu wathu uyambenso kuzungulira monga momwe zidaliri mmbuyomu Angoni asadatithire nkhondo. Tikufuna dziko lidziwe mwambo wa ufumu wathu, koma anzathu a gulu la Mtima Gondwe sakugwirizana nazo, adatero Kalizga Gondwe. Iye adati banja la a Gondwe likuyenera kusankha mfumu kuchokera mmabanja atatu otsala aja. Titakatula madandaulo athu kwa bwanamkubwa wa boma lino, adatibwenza potiuza kuti sagwira ntchito ndi mafumu wamba. Pachifukwa ichi tidalemba kalata ku boma yofotokoza madandaulo athu, koma mpaka lero sadatiyankhebe. Titaona kuti masiku akudutsa osayankhidwa, mmwezi wa March tidakasuma ku bwalo la milandu ndipo pakadali pano tikungodikira masiku, adatero Kalizga Gondwe. Iye adati asadapite ku khoti, mabanja onse okhudzidwa adakhala pansi ndi mafumu Mwamlowe, Katumbi, woimira anthu pa milandu Victor Gondwe, komanso abizinesi ena monga Alfred Longwe ndi Malopa Gondwe kuti akambirane mwamtendere. Kalizga adati adagwirizana zoti Mtima apitirize kulamulira, koma akadzangochoka, ufumu udzayambenso kuyenda mmabanja. Koma zomwe zidachititsa kusintha maganizo mpaka poti tikafike ku khoti ndi zoti titachoka kuzokambiranazo, komwe Mtima sadabwereko koma adangotumiza nthumwi, iye adatero. Mmodzi mwa mafumuwo, Tawona Gondwe, adati zinthu zidalakwika pachiyambi pamene malemu Walter adasankhiratu mwana wake kuti ndiye adzalowe mmalo mwake akadzamwalira. Polankhulapo imodzi mwa mafumu omwe adawakhazika anthuwa pansi, Mwamlowe idati nzokhumudwitsa kuti nkhani za ufumu zizipita ku bwalo la milandu. Iye adati kuzokambiranaku mafumuwa adadandaula za khalidwe la Mtima. Koma tidagwirizana kuti popeza adasainira kale Walter asadamwalire kuti mwana wakeyu ndiye mlowammalo, angopitiriza kuti adzayambe kutsatira mwambo wawo Mtima akadzachoka. Sindikudziwa kuti chidachitika nchiyani kuti ayambenso kuwatukwana anzake. Ngati mafumu, tikhalanso pansi kuti tikambirane chifukwa mfumu imayenera izilemekeza anthu ake, izikhala ya bata, komanso yodzichepetsa, adalongosola Mwamlowe. Polankhulapo ndi Msangulutso, Mtima Gondwe adati sakudziwa zomwe mafumuwo akukamba. Inetu adachita kundiitanita mchaka cha 2012 kuti ndidzakhale mfumu kuno chifukwa ndinkagwira ntchito ngati community development officer mu unduna woona zoti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, adalongosola motero Mtima. Iye adati ufumu wa Chikulamayembe ndi wake.
11
Kumawachenjeza anawa Ndimakumbuka kuti masiku adzanawo, nkhani zogwiririra anazi zisanafale kwenikweni, mayi wanga ankatikhazika pansi, ine ndi achemwali anga, kutiuza kuti kunjaku kuli anthu ena aupandu omwe amakhoza kuseweretsa matupi a ana nkuwachita chipongwe. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Apatu nkuti tili achichepere; zaka zathu zili pakati pa zisanu ndi khumi. Adachenjeza mayi kuti pali ziwalo zina pathupi zomwe munthu wina tisamamulole kuzigwira ndipo adanenetsa kuti wina atakugwira modabwitsa-kaya ndi malume, mlongo wako kapena mphuzitsi-ukuwe, uthawe nkuwadziwitsa mayi kapena munthu wina wachikulire. Adachenjezaso kuti aphuzitsi amphongo osazolowerana nawo kusukulu. Adanenetsa kuti aphuzitsi aamuna usakakhale nawo wekha muofesi, kaya mkalasi ndipo adati akakutuma kuti ukasiye makope kunyumba kapena kuti ukawasesere kunyumbako, uwakanire ndipo akakati wachita mwano adzathana ndi mayiwo. Adakambaponso za aphuzitsi opereka malikisi ochuluka pomwe mwana walakwa. Adati oterewa tikachenjere nawo chifukwa izi sachita zaulere; amafuna malipiro tsiku lina. Zomangolandira timphatso ngati switi, bisiketi kaya ndalama kwa anthu osawadziwa bwino adakaniza mayi. Pakhomo ngati pali mnyamata kapena bambo wogwira ntchito, padalinso malire pakachezedwe naye popewa kuti angatikole msampha. Padali zambiri zomwe mayi ankatilankhula, mwina ankaonjeza kumene, koma adatitsegula maso za kuopsa kwa anthu mdziko limene timakulamo. Malangizowa adakhazika mmitu mwathu kotero kuti sikudali kwapafupi kuti wina atitchere ndale chifukwa mayi adali ataunikira za nzeru zosiyanasiyana zomwe anthu amagwiritsa nthito pofuna kuchita nkhanza kwa ana. Choncho nthawi zonse ndikamva kapena kuwerenga za mwana amene wagwiriridwa sindilephera kulingalira ngati makolo a mwanayo adayesapo kumuchenjeza za mchitidwewu womwe ukukhala ngati wafalikira mdziko lathu. Malangizowa sangagwire ntchito nthawi zonse chifukwa nthawi zina anawa amangokakamizidwa mwadzidzidzi ndi munthu wamphamvu zoti sangalimbane naye. Komatu kawirikawiri tikumva kuti anthu omwe akugwiririra anawa amawanyengerera ndi switi, ndalama ndi zina zoterozo. Kusonyeza kuti amabwera momuwenderera mwanayu pokambirana naye momupusitsa.
15
Wogona ndi mwana wake pofuna mfumba agwidwa Ndani adanena kuti chizimba cha mfumba ndi kugona ndi mwana wako? Izi zachitika ku Dedza komwe apolisi anjata bambo wa zaka 49 pomuganizira kuti adagona ndi mwana wake, wa zaka 17, kuti achulutse zokolola. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Tikunena pano akuti mkuluyu wapha kale ngolo ziwiri za chimanga pomwe zaka zapitazi ankakolola osakwana ndi ngolo imodzi yomwe. Iye wati wangokolola theka chabe la mundawo. Njondayi, Levison Dickson, ya mmudzi mwa Chimalira kwa T/A Kachere mbomalo, akuti ili ndi ana asanu ndi mmodzi (6), amuna awiri akazi anayi. Idagona nayeyu akuti pano ali ndi mthunzi wa miyezi isanu. Mneneri wapolisi ya Dedza, Edward Kabango, wati Dickson adauza apolisi kuti adapita ku Mozambique kukasaka mfumba yoti ulimi wake wa mtedza, chimanga, soya ndi nyemba uzimupatsa zokolola zamnanu. Adati kupatula kutsira fetereza ndi kusamalira zokolola zake pamayenera mfumba igwire ntchito. Adauza apolisi kuti anthu ena akuchita zimenezi ndipo zikuwayendera, adatero Kabango. Mneneriyu adati mkuluyu atafika mdzikolo adakumana ndi nganga yomwe idamutemera mterawo koma chizimba chake kudali kukapumira pamwana wake mpaka mwanayo atakhala ndi pathupi. Ntchito yokwaniritsa chizimbacho akuti idayambika mu January chaka chino. Akuti mlimiyu adamasuka chifukwa mkazi wake nkuti ali kwa apongozi ake komwe amachereza matenda. Kabango wati mkazi wa mkuluyu atabwera adadabwa ndi momwe msungwanayu amaonekera chifukwa amaonetsa zizindikiro zoti ali ndi pathupi. Mayiwo adamupanikiza ndipo adaulula kuti bambo ake ndiwo mwini wa pathupipo. Iye adawauza kuti bambowo adamuuza kuti agone nawo kuti akolole zochuluka. Mayiwo atadzatifotokozera izi pa 25 May tidanjata mkuluyu. Iye adavomereza kuti adagonadi ndi mwanayo kuti kumunda akolole dzinthu dzochuluka, adatsindika Kabango. Woganiziridwayu adakawonekera kubwalo la milandu Lachinayi lapitali komwe iye adavomera mlanduwo. Chilango cha mlanduwu ndi kukakhala kundende zaka zisanu. Zimatengera momwe mlandu wakhalira. Malamulo amati ngati msungwanayo adali wosaposa zaka 16, woganiziridwayo akaseweze moyo wake wonse, zakazi zingasinthe ndi momwe woweruza mlandu angagamulire, adatero Kabango.
19
Mwayi kuthima kwa magetsi Pomwe ena akudandaula za kuthimathima kwa magetsi, ena akusimba lokoma kuti adapatirapo mwayi wabanja. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Victor Mpunga yemwe pa 28 December 2015 adapanga chinkhoswe ndi Mary Makhiringa, akuti adayamba kulankhulana pagolosale pomwe Mary amakagula chakudya atachita ulesi kusonkha moto magetsi atathima. Victor ndi Mary adakumana pagolosale Victor akuti nthawi zambiri amakonda kucheza pagolosale yamnzake pafupi ndi pomwe Mary amakhala ndipo amangomezera malovu msungwanayu akamadutsa popita ndikuchokera kuntchito. Iye akuti mwayi udapezeka tsiku lina madzulo magetsi atathima pamenepo Mary akuchokera kuntchito ndipo mmalo mosonkha moto kuti aphike nkhomaliro, adangoganiza zokagula chakudya pagolosaleyo ndipo nkuti Victor ali pomwepo. Ndidangoti bowa bwanga nthawi yomweyo nkuyambitsa macheza. Ndimaona ngati andinyoza malinga ndi mmene amaonekera koma ayi ndithu tidacheza bwinobwino mpaka chinzake chidayamba, adatero Victor. Iye adati chinzakecho padali polowera chabe chifukwa patangotha nthawi pangono chibwenzi chidayamba mpaka makolo kudziwitsidwa nkuyamba kupanga dongosolo la chinkhoswe. Iye adati ulemu amamusangalatsa kwambiri chifukwa cha mawonekedwe, khalidwe ndi luntha pofuna kupanga chinthu ndipo salola kupanga chinthu chomwe sakuchimvetsetsa zomwe iye amaona ngati mphamvu. Mary adati kwa iye chachikulu nchakuti Mulungu adamulozera mwamuna yemwe amayembekezera moti ali ndi chiyembekezo chakuti adzakhala pabanja lokoma ndi losangalatsa kwambiri. Ndimamukonda kwambiri Victor chifukwa ndi mwamuna wachitukuko. Ndi munthu uja oti akaganiza kapena kunena chinthu amayesetsa mpaka chichitike basi ndiye ndimadziwa kuti ali nkuthekera kwakukulu, adatero Mary. Awiriwa akuti akuyembekezera kumanga ukwati woyera chaka chino cha 2016 ndipo zokonzekera zili mkati.
15
Nigeria, Malawi agwilana manja Pamene dziko la Malawi lili mkati mwazokambirana ndi dziko la Tanzania pa nkhani ya umwini wa nyanja ya Malawi yomwe akuti muli mafuta, dziko la Nigeria lati ndilokonzeka kuthandiza dziko lino kuwenga mafutawa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mtsogoleri wa dziko la Nigeria Goodluck Jonathan adanena izi Lolemba pamene amafika mdziko muno kudzacheza kwa masiku awiri motsagana ndi akuluakulu ena 143 ochokera ku Nigeria komweko. Dziko la Nigeria ndilimodzi mwa mayiko omwe amawenga mafuta ambiri pa dziko lapansi ndipo Jonathan adati dziko lawo ndilokonzeka kutumiza akatswiri antchito zowenga mafuta kuchokera kudziko lawo kuti adzathandize ntchito zowenga mafuta mu nyanja ya Malawi. Dziko la Nigeria lakhala likuwenga mafuta kwa zaka zambiri ndipo padakali pano tili ndi akatswiri odziwa bwino za ntchito yowenga mafuta omwe tikhoza kuwatumiza kuti adzathandize pa ntchito yotere kuno, adatero Jonathan.
2
Muluzi Wamema Anthu AKu Machinga Adzavotere Mutharika Mtsogoleri wa chipani cha United Democratic Front (UDF), Atupele Muluzi wapempha anthu a mboma la Machinga kuti adzavotere Professor Peter Mutharika pa chisankho cha president chomwe chikuyembekezeka kuchitika pa 23 mwezi uno. Muluzi pa msonkhano wokopa anthu Muluzi walankhula izi pa misonkhano yake yokopa wanthu yomwe wachititsa mbomalo. Iye wati anthu a mbomalo akuyenera kudzavotera mtsogoleri wa mu mgwilizano-wu kaamba koti ndi amene ali ndi kuthekera kothandiza pa ntchito zolimbimbikitsa ufulu weniweni wa demokalase ndi chitukuko cha dziko lino. Mwa zina pa misonkhano-yi a Muluzi anapita ndi kukayendera mnyamata amene anavulala pa chipolowe chomwe chinachitika mbomalo, pomwe anthu ena mbomalo anatsekera njira ndi kuyamba kulimbana ndi mtsogoleri wa chipani cha UTM, Dr. Saulos Chilima kuti asadutse mdelaro. Pamenepa Muluzi wapempha apolisi kuti afufuze bwino pa za momwe apolisi a zachitetezo cha Dr. Chilima yemwe ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, anagwilira ntchito zawo zokhazikitsa bata pa malowa.
11
Ngozi idazamitsa chikondi chathu Anthu adavulala, ena adataya miyoyo yawo. Koma kwa Joseph Chirwa ndi Towera udali mwayi kuti awiriwa akumane ndi kumanga woyera. Lero ndi thupi limodzi, koma nkhani yano imaseketsabe akakumbuka za ngozi yomwe idachitika mu 2010 mboma la Zomba, iyo idali ngozi ya basi. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Towera adali mbasimo ndipo adavulala ndi kutengeredwa kuchipatala. Panthawiyo nkuti awiriwa atakumana kale ndi kupatsana manambala koma zolota kuti akapizana mawu a chikondi panalibe. Joseph ndi Towera lero ndi banja Joseph yemwe akugwira ntchito kunthambi yoona za anthu olowa ndi kutuluka mdziko muno atamva kuti Towera wapanga ngozi, adakhudzidwa ndipo samati waimbanso liti foni komanso kukamuona. Chifukwa choimbaimba, tidakhala pachinzake kwambiri, kenaka tidayamba kufunana, adatero Joseph pamene adamudikira Towera achire kaye kuti nkhani yachikondi ilowe mbwalo. Joseph akuti pamene izi zimachitika nkuti awiriwa atakumana kale ku Masintha CCAP komwe onsewa amapemphera. Apo Joseph nkuti ali mtsogoleri wa achinyamata, Towera adali membala wagulu la maimbidwe. Komabe panthawiyo zoti angadzakhale thupi limodzi sizimadziwika. Zidatengera ngozi ya ku Zomba kuti zenizeni zioneke. Mu 2012 Towera adali atachita, ndipo Joseph adaponya Chichewa. Pounguza chikondi chomwe mtsogoleriyu adachionetsa pa nthawi ya matenda, Towera sadazengereze koma kuvomera. Joseph ndi oopa Mulungu. Wachikondi komaso wosamala. Iye amalingalira mwakuya ndipo ndidapeza tsogolo langwiro mwa iye, adatero Towera. Naye Joseph adabwekera kuopa Mulungu kwa njoleyo: Towera ndi oopa Mulungu, ali ndi maonekedwe abwino ndipo ndisanamepo mkazi wanga ndi nthwani. Ukwati udali pa 31 October 2015 ku Masintha CCAP ndipo madyerero adali ku ku Lilongwe Golf club.
15
Namrukhunua: Nyumba ya chilhomwe Kalelo makolo adali ndi njira zawo zochitira zinthu kuti azisangalala ndi kukhala wotetezedwa. Alhomwe nawo ali ndi zimene makolo awo adayambitsa ndipo zina zimapitirirabe mpaka pano. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi wotsata chikhalidwe cha Alhomwe mumzinda wa Lilongwe, Fustafu Mbewe. Adacheza motere: Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pa mtundu wa Alhomwe pali mawu akuti Namurukhunua, kodi tanthauzo lake nchiyani? Imeneyi ndi nyumba yozungulira yomwe makolo pa mtundu wa Chilhomwe adayambirira kumanga kalelo nkumakhalamo. Kanyumba kameneka kamakhala kakangono ndipo kamakhala kopanda chipinda. Pomanga amagwiritsa ntchito zipangizo zanji? Timagwiritsa ntchito mitengo, tsekera, khonje, zilambe, matope ndi namgoneka (zokhala ngati zilambe ndipo ena amalukira mipando). Masiku ano enanso amagwiritsa ntchito misomali. Chitseko chimakhala cha kaphe, kabala wake mtengo omwe umapingasa pachitseko. Ndiye mwati imakhala nyumba yaingono, mumakhala anthu angati mmenemo? Namrukhunua mumakhala anthu awiri (banja) ndipo ngati pali wachitatu ndiye kuti ndi mwana wa mnyumbamo. Ngati pali anthu ambiri, amamanganso tinyumba tambiri pamodzimodzi ngati banja limodzi koma katundu yense wakukhitchini, ziwiya za madzi ndi madengu a ufa amakhala mnyumba momwemo. Pomanga zimakhala bwanji? Pamalo akasosapo bwinobwino amatenga chingwe ndi mitengo nkuyamba kuyeza muja amachitira akafuna kumanga nkhokwe. Akakwanitsa kupimako, amazika mitengo mmphepetemo ndikuyamba kuphoma ndi matope ndipo akamaliza amafolera ndi tsekera nkukonza chitseko. Pachibale pawo akalakwirana nkhani zake zimayenda bwanji? Monga ndanena kale, pachibale amamanga nyumba zawo pamodzimodzi kupatula makolo, omwe amamanga patali pangono koma poonekera ndiposavuta kufikapo. Pakachitika mapokoso, amakauza makolo olo ngati zili za mbanja, amauza ankhoswe ndikukamba koma zikalephera ndiye zimakafika kwa amfumu kuti athandizepo. Nanga amuna a Chilhomwe zida zawo ndi chiyani? Alhomwe zida zawo ndi chikwanje (koma chimakhala ndi ngowe), nsompho (nkhwangwa) ndi mpeni omwe amautchinjiriza ndi kachikwama kopangidwa ndi chikopa cha nyama. Mpeni wa Mlhomwe suonekera chisawawa amaubisa ndipo umatuluka pokhapokha ngati ukufunika kuti ugwire ntchito. Alhomwe ntchito yawo yaikulu ndi chiyani? Alhomwe amakonda kulima. Mbewu zomwe amakonda kulima kwambiri ndi kalongonda, chinangwa, nandolo, mbatata, nzimbe, chimanga, mapira ndi tchana. Chakudya chawo chodalilika ndi nsima ndi zipatso; amakondanso nandolo osakaniza ndi makaka. Nanga mavalidwe awo? Amayi a Chilhomwe amakonda kuvala nsalu, andiloko (iyi ndi siketi yaitali yomwe ena amati makisi), bulauzi ndi mpango ndipo amakonda kusokera nsalu ya biliwita (yakuda). Abambo amakonda kabudula ndi malaya osokedwa ndi nsalu ya khaki. Tangomalizani ndi ena mwa magule otchuka pa chilhomwe. Pali magule monga tchopa, sekhere ndi jiri. Povina Tchopa amavala zikopa za nyama komanso amaberekera tinthu tokhala ngati nyama kumsanaku mmiyendo muli mawerewesa oti azipanga kaphokoso povina. Povina sekere amavala mikanda paliponse ndi mkhosi momwe komanso amadzikongoletsa nkhope yonseyi. Jiri ndi gule yemwe amavinidwa usiku kuli mwezi ndipo amavina ndi amuna ndi akazi. Mwachidule magule ndiye alipo ambiri osangalatsa pa mtundu wa Alhomwe.
15
Zipolowe Zalepheretsa Chilima Kuchita Misonkhano ku Machinga Anthu ena omwe akuwaganizira kuti ndi otsatira zipani za DPP ndi UDF asokoneza misonkhano yoyimayima yomwe wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulosi Chilima amayembekezeka kuchititsa mmadera ena a mboma la Machinga. Nsewu wa Bakili Muluzi Highway unatsekedwa ndi zigawenga Kutsatira izi Chilima yemwe akuyima pa chisankho chomwe chikudzachi ndi Dr. Lazarus Chakwera pansi pa mgwirizano wa zipani wa Tonse, walepheretsa misonkhano yonse yomwe amayenera kuchitayi. Polankhula ndi Radio Maria Malawi phungu wakale wadera la pakati mboma la Machinga yemwe mbuyomu anali wa chipani cha DPP koma tsopano analowa mchipani cha UTM, Ellock Maotcha Banda wati mtsogoleriyu anayimitsa misonkhanoyi kaamba koti samafuna anthu osalakwa avulale kaamba ka misonkhano yake. Anyamata a DPP ndi UDF anapatsidwa ndalama ndi atsogoleri a chipani chawochi kuti asokonezeze msonkhano omwe umafuna uchitike mu madera a nselema, Ntaja, Nsanama, Ulongwe ndi Mangochi Turn Off ndipo izi zinapangitsa kuti a president athu a UTM asapangitsenso msonkhanowu pofuna kutetza miyoyo ya anthu osalakwa, anatero aMaotcha. Iwo ati kulephereka kwa msonkhanowu sikodandaulisa kweni kweni chabe kuti chipani cha DPP chikuluza mavoti mmaderawa ponena kuti chipani cha UTM tsopano chili ndi anthu ambiri ochitsatira mchigawo chakumvuma.
14
Ochita Bizinesi pa Songani Ayamikira Boma Powamangira Msika Wamakono Ochita malonda pa nsika wa Songani mboma la Zomba ayamikira boma kamba kowamangira msika wamakono omwe ukuyembekezeka kutha pambuyo pa miyezi itatu ikubwerayi. Mkhalapampando wa komiti ya anthu ochita malonda mu msika wa Songani a Wilard Allan anena izi lachitatu pomwe akuluakulu ochokera ku unduna wa za maboma angono anakayendera zitukuko zosiyanasiyana zomwe khonsolo ya boma la Zomba ikugwira. Iwo anati mmbuyomu akhala akukumana ndi mavuto osiyanasiyana monga kusowa kwa zimbudzi zaukhondo pa msikawu. Mavuto omwe timakumana nawo mmbuyomu atha ndipo tikuyamikira boma chifukwa cha msika wamakono umenewu, anatero a Allan. Iwo ati ndi okhutira ndi mmene ntchito yomanga msikawu ikuyendera ndipo ati ndi okonzeka kugwira ntchito limodzi ndi mafumu kuti ntchitoyi iyende msanga.
2
Dziko la Zimbabwe Lichotsa Ntchito Anamwino 77 70w" sizes="(max-width: 419px) 100vw, 419px" />Ena mwa anamwino omwe amachita ziwonetsero mdzikolo Dziko la Zimbabwe lachitatu lachotsa ntchito anamwino 77 kaamba kowaganizira kuti ndi omwe amakolozera kunyanyala kwa ntchito kwa anamwino mdzikomo. Malinga ndi malipoti a BBC ogwira ntchito za umoyo akhala akunyanyala ntchito pokakamiza boma la dzikolo kuti liwaonjezere malipiro omwe akuti ndi ochepa kwambiri. Kunyanyala ntchitoku kunayamba mwezi wa September chaka chino ndipo mwezi watha, bwalo lalikulu la milandu mdzikolo, linalamula kuti ogwira ntchito za umoyowa abwelere ku zintchito zawo. Padakali pano anamwino mazanamazana ali pa chiopsezo choti nawonso atha kuchotsedwa ntchito potengera zomwe zachitikazi. Dziko la Zimbabwe ndi limodzi mwa maiko kuno ku Africa omwe akukumana ndi mavuto a zachuma.
6
Moto buu! Ku Swaziland Kochi wa timu ya dziko lino ya Malawi Flames, Ernest Mtawali, wati timu yake yakonzeka kuonetsa zakuda timu ya Swaziland yomwe aphane nayo mumpikisano wa Africa Cup of Nations (Afcon) mawa lino pa Somhlolo Stadium mumzinda wa Lobamba. Malawi ili mgulu L momwe muli Swaziland, Guinea ndi Zimbabwe. Awa ndi masewero achiwiri a Flames mumpikisanowu chigonjerreni 2-1 ndi ndi Zimbabwe pa Kamuzu Stadium pa 13 June chaka chino. Panthawiyo kochi adali Young Chimodzi, yemwe adachotsedwa ntchito kaamba ka kugonjaku. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma Mtawali akuti anyamata ake ali bwino ndipo akuyembekezera kuphophola Swaziland, timu yomwe mmasewero ake oyamba idakatikita Guinea kwawo komwe. Ndili ndi chikhulupiriro mwa anyamata amene ndawatenga. Tikufuna kumwetsa zigoli chifukwa njira yabwino yoteteza golo lanu ndi kumenyera mpira kutsogolo kuti tikapeze zigoli, adatero mmene ankanyamuka mdziko muno Lamulungu lapitali kupita ku South Africa komwe idalepherana ndi Mbombela United 2-2 pamasewero apaubale pokonzekera Swaziland. Malawi yakumanapo ndi Swaziland maulendo 18 ndipo yapambana katatu, kugonja ka 10 ndi kulepherana mphamvu kasanu. Mumpikisanowu chaka chatha Malawi sidachite bwino pamene idakumana ndi matimu akuluakulu mgulu lawo monga Algeria, Mali ndi Ethiopia. Pamasewero onsewo, Malawi idangokwanitsa kupeza mapointi 7 itapha Mali pakhomo komanso Ethiopia ndi kulepherana ndi Ethiopia kwawo. Koma Mtawali akuti timu yomwe ali nayo pano ndi ina ndipo chiyembekezo chilipo kuti mawa alandira zotsatira zabwino kuchokera kwa anyamata ake. Mtawali watenga Limbikani Mzava, Stanly Sanudi, Yamikani Fodya, Wonder Jeremani, John Lanjesi, Pilirani Zonda, Yamikani Chester, Isaac Kaliati, Chimango Kaira, Chawanangwa Kaonga, Chiukepo Msowoya, Muhammad Sulumba, Manase Chiyesa, Robin Ngalande, Robert Ngambi, John CJ Banda, Chikoti Chirwa, Micium Mhone, Gerald Phiri jnr Richard Chipuwa Bright Munthali. Amkhalakale monga Joseph Kamwendo, Fischer Kondowe, Esau Kanyenda, Frank Banda, Lucky Malata, Harry Nyirenda, Zicco Mkanda, Atusaye Nyondo, MacDonald Harawa ndi Charles Swini atsala. Masewero a Zimbabwe, Malawi idachinya kudzera mwa John Banda amene mawali akhalenso ndi ntchito yaikulu pakati pa Flames.
16
Chimanga cha k1bn chaola ku admarc Komiti ya za malimidwe ku Nyumba ya Malamulo yatulukira kuti chimanga cha ndalama zokwana K1 billion chaola mu nkhokwe za Admarc. Koma mkulu wa Admarc, Margaret Roka Mauwa, wakana kuthirirapo ndemanga pa lipotilo kaamba koti sadalilandire. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Admarc iyenera kupeza njira zosamalira chimanga chake Popereka lipoti lake ku nyumbayo, komitiyo yati ngakhale izi zili choncho, Admarc ikugulitsabe kwa anthu chimangacho. Komiti yathu yapeza kuti chimanga cha ndalama zosachepera K1 biliyoni ndipo ncholemera matani 7 000 nchoola mu nkhokwe za Admarc. Chokhumudwitsa nchoti Admarc ikupitiiriza kugulitsa chimangacho kwa anthu, likutero lipotilo. Lipotilo lidawerengedwa ndi Sameer Suleman ndi Werani Chilenga. Komitiyo idatulukira izi pomwe imakumana ndi akuluakulu ochokera mmabungwe omwe ali pansi pa unduna wa zamalimidwe pokonzekera kukambirana bajeti ya 2019/20. Koma Mauwa adati nkovuta kuthirirapo ndemanga pa nkhaniyo kaamba koti sadalandire lipotilo. Pakhala povuta kuti ndiyankhe kaamba koti lipotilo sindinalione, komanso kudalibe komwe amaliwerenga. Pakatipa zambiri zakhala zikundidutsa kaamba koti ndinali mchipatala, adatero mkuluyu. Katswiri wa zaulimi, Tamani Nkhono Mvula, adati nzokhumudwitsa kuti Admarc ikugulitsa chimanga choonongeka kwa anthu. Mkuluyu adati zaka zowerengeka zapitazo Admarc idakumana ndi vuto ngati lomwelo ndipo anthu amayembekezera kuti adatolapo phunziro. Kodi nzoona tizimva kuti chimanga chaonongeka ku Admarc? Kodi chifukwa chiyani sititolapo phunzira pa chimanga chaboma chomwe chidaonongeka posachedwapa nkupeza njira zothandiza kuthana ndi vutoli? Kodi zimatheka bwanji chimanga kumaolera mu nkhokwe za Admarc anthu akumabwerera mmisika yake kaamba kosowa chimanga? Ndimamva chisoni kwambiri ndi dziko lathu, adatero Nkhono. Katswiriyu adati Admarc siikuyenera kugulitsa chimanga choonongeka kaamba koti nchoopsa pa moyo wa munthu. Kafukufuku akuonetsa kuti mbewu zoola zimakhala ndi chuku chomwe chimayambitsa matenda osiyanasiyana kuphatikizirapo a khansa. Mu 2013 chimanga cholemera matani 60 000 chidaoleranso mu nkhokwe za Admarc ngakhale pa nthawiyo anthu ambiri amagona mmisika yake kufuna kuchigula. Aphungu a komitiyo apempha boma kuti lipereke ndalama ku Admarc zoti igulire matani 96 000 a chimanga kuti anthu asafe ndi njala mdziko muno. Malingana ndi lipoti la Mvac, anthu oposa 3.3 miliyoni akumana ndi vuto la chakudya chaka chino. Mwa anthuwa, 1.8 miliyoni ndi ochokera mchigawa cha kummwera. Alimi ambiri mchigawochi sadakolole mokwanira kaamba ka ngamba, komanso vuto la madzi osefukira womwe adasesa mbewu zawo. Komitiyo yapezanso kuti Admarc ikulipira anthu pafupifupi 900 omwe sagwira ntchito ku bungwelo moti yapempha boma kuphwasula bungwelo nkuipanganso pofuna kuthana ndi vutolo. Komitiyi yapemphanso boma kuti liwonjezere anthu omwe akuyenera kupindula ndi zipangizo zotsika mtengo kuchokera pa 900 000 nkufika pa 1 miliyoni. Padakali pano ndondomeko ya zipangizo zotsika mtengo adaipatsa K35.5 biliyoni.
2
Anatchezera Ndimamukonda Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndinali pachibwenzi ndi mkazi wina ndipo zaka ziwiri zatha pomwe tinasiyana. Pano ali ndi mwana yemwe wabereka mwezi watha ndiye akumabwera kwa ine nkumati tibwererane. Kodi pamenepa ndithani, agogo? Mkaziyo kunena zoona ndimamukonda, koma pano ndinalimba mtima. Nditani? Ine Amfumu, Zingwangwa Amfumu, Nkhani yanu ndi yovuta kuitsata bwinobwino chifukwa simukumasula kuti vuto lanu ndi chiyani kwenikweni. Poyamba mwanena kuti mkaziyo munasiyana naye zaka ziwiri zapitazo, munasiyana chifukwa chiyani? Mwati pano mkaziyo akuti mubwererane ndipo inu nomwe mukuti kunena zoona ndimamukonda. Komanso inu nomwenso mukuti pano munalimba mtima, mukutanthauzanji? Mwatinso mkaziyo ali ndi mwana wa mwezi umodzi, nchachidziwikire kuti mwanayo si wanu-poti mwanena nokha kuti chibwenzi chanu chidatha zaka ziwiri zapitazo. Apatu, kunena zoona, Amfumu, mayankho muli nawo ndinu. Ngati mkaziyo mukuti mumamukonda, chovuta nchiyani kuti mubwererane? Koma mukuti mwalimba mtima, kulimba mtima kotani? Nchifukwa chake ndikuti zonse zili ndi inu kuti mubwererane kapena ayi poti zifukwa zake zomwe mudalekanirana mukuzidziwa ndinu. Mwakula mwatha, Amfumu. Akungosereulana nane? Anatchereza, Ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina amene ndikufuna kukwatira koma zochitika zake zikundidabwitsa. Chaka chatha adandijejemetsa pamene adati ali ndi mimba ndipo amati akufuna achotse chifukwa akuopa makolo ake. Ndidamuuza kuti asayerekeze kuchotsa pathupipo chifukwa ine ndidali wokonzeka kumukwatira, zivute zitani. Kenaka, patapita kanthawi adati amangocheza, alibe mimba. Mwezi wathawu adandiza kuti adakayezetsa magazi ndipo amupeza ndi kachilombo ka HIV ndipo nkofunika kuti nane ndikayezetse. Kunena zoona, sindinapite kukayezetsa koma ndidangomunamiza kuti ndakayezetsa ndipo sanandipeze ndi kachilombo. Pano wandiuza kuti amangonama, sadakayezetse magazi. Kodi iyeyu ndi mtsikana wotani? Ndipitirize naye chibwenzi? YB, Lilongwe Zikomo YB, Pali zinthu ziwiri: Bwenzi lakolo mwina ndi wokonda kusereula komanso mwina ndi kamberembere. Koma zili ndi iwe kupeza choona chenicheni mwa iye. Koma tiyeni tione mbali zones ziwirizi. Poyamba, ngatidi amakonda kusereula, umuuze kuti pali zina zoti angathe kusereula nawe koma nkhani za mimba ndi HIV si nkhani zosereula nazo. Ngati akufuna aone ngati umamukondadi pali njira zina, osati kunamizira mimba kapena kuti amupeza ndi kachilombo. Kusereulana si kolakwika mukakhala pachibwenzi chifukwa ndi njira ina yokometsa chibwenzi chanucho, koma pali malire. Komanso mwina, monga ndanena, akhoza kukhalanso kamberembere ameneyo. Nkutheka mwina adachotsadi mimba ameneyo. Ngati adaterodi, cholinga chake chidali chotani? Wofuna banja amachotsanso pathupi mwadala? Ayi. Tsono pankhani yokayezetsa magazi, bwanji mutapita kuti mukayezetse limodzi kuti mudziwe momwe mulili nonse? Kwa anthu ofuna banja lansangala, losakaikirana, kuyezetsa magazi ndi njira imodzi yothandiza kuti mudziwe ngati muli ndi kachilombo pena ayi. Mukatere mumadziwa chochita pankhani ya kasamalidwe ka banja lanu.
12
Boma Lichenjeza Anthu Ochitira Nkhanza Ana Wolemba: Thokozani Chapola kwelepeta-200x110.jpg 200w" sizes="(max-width: 540px) 100vw, 540px" /> Boma lawopseza kuti silidzalekelera anthu onse omwe amaphwanya ma ufulu a ana munjira ina ili yonse. Wachiwiri kwa nduna yowona zoti palibe kusiyana pakati pa amayi ndi a bambo, ana komanso anthu wolumala, mayi GRACE KWELEPETA ayankhula izi ndi atakayendera mwadzidzidzi mwana wina wa zaka zinayi (4) zakubadwa amene mayi ake ndi a mzawo amuchitira nkhanza pomumwetsa mowa wa kachasu ku CHIRIMBA mu mdzinda wa BLANTYRE. A KWELEPETA ati ataona zithunzi pa makina a internet pa zimene amayiwo anamuchitira mwanayu ati zinawakhudza kwambiri ndipo anaganiza zokazonda mwanayo. Iwo athokodza apolisi kamba kochita chotheka ndi kumamanga amayi atatuwo kamba koti zomwe anachita kwa mwanayo zinali zosayenera. Nkhani yabwino ndi yoti amayi atatu onsewo amangidwa ndipo lamulo ligwira ntchito yake, anatero mayi Kwelepeta. Iwo adzudzula onse omwe ali ndi khalidwe ngati la amayi atatuwa kuti alekeretu.
14
Amalawi ati boma la PP likusakaza chuma Akuluakulu ena ati boma la chipani cha Peoples Party (PP) motsogozedwa ndi mtsogoleri wake, Joyce Banda kudzanso wachiwiri wake, Khumbo Kachali lataya chipangano pomwe lasiya kulabada miyoyo ya anthu ake koma kumangoononga chuma cha dziko ngati chiswe. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkulu wa Malawi Watch, Billy Banda komanso katswiri wa zandale, Henry Chingaipe, adauza Tamvani msabatayi pomwe amawunguza momwe boma likuonongera misonkho ya anthu pofuna kudzikundikira lokha pomwe Amalawi ali pamoto. Chitsanzo iwo amalankhula momwe misonkho ya anthu yaonongedwera ndi ulendo wa ku United Nations (UN) womwe mtsogoleriyu watenga anthu oposa 40 kuphatikiza mafumu. Ounikirawa ati pomwe nkhani za chuma zisadakhazikike mdziko muno, ndikosafunika kuti boma litenge mafumu paulendowo komanso anthu ochuluka amvekere uku ndikuononga chuma posaganizira Amalawi. Kusakaza ngati chiswe Malinga ndi malipoti omwe nyuzipepala ya The Nation ya Lachiwiri sabata yatha idapeza, pafupifupi K308 miliyoni ndiyo ionongedwe paulendowo. Ndalamayi ingakwanire kugulira matumba 616 000 a fetereza wotsika mtengo. Ndalamazi mwazina ndi zolipirira matikiti a ndege komanso ndalama zapadera za omwe wayenda nawo zomwe akuti ndi K84 000 pa munthu mmodzi patsiku. Koma mneneri wa boma, Moses Kunkuyu, wati sizoona kuti boma akudzikundikira ndipo aiwala Amalawi chifukwa chilichonse chomwe boma likuchita ndichokomera Amalawi. Pali maulendo omwe akufunika achitike ndithu ndiye sikuti taiwala. Ndizoonadi kuti paulendowo pali mafumu ena monga Malemia yaku Nsanje koma pali kufunika kwake. Mukudziwa kuti bomali likugwira ntchito ndi mafumu pa nkhani ya uchembere wabwino komanso zina ndiye chomwe tikufuna nkuti akathe kumva momwe mayiko ena zikhalira, adatero Kunkuyu. Izi zikuchitika pomwe amabungwe omwe siaboma komanso anthu adzudzula mamulumuzana abomawa kuti achepetse maulendo. Bomali likumbuke komwe lachokera, zikuonetsa kuti atsogoleriwa ali pachinyezi ndipo ayiwala Amalawi. Tinkadzudzula boma la DPP zoononga misonkho ndipo ichi sichachilendo kwa iwo koma ife tikudabwa kuti nawonso ayamba zomwezo. Apa asanduka Agalatiya, adatero Banda. Maulendo achuluka Naye Chingaipe wati bomali likulephera kuchepetsa ndalama zogwiritsidwa ntchito maka pamaulendo. Iye adati ndibwino kuti maulendo ena aboma zizipita nduna zokha kuti ndalama zogwiritsidwa ntchito zichepe. Ulendo wa ku UN ndi ulendo wa boma ndipo omwe akuyenera kupita ndi omwe akukhudzidwa ndi nkhani za boma koma zikudabwitsa kuti ulendowo kwapita mafumu ndi ena. Kuulendowu kwapita anthu ambiri komanso akukakhala masiku ambiri zomwe ziononge ndalama, adatero Chingaipe. Francis Lunga wa mmudzi mwa Malasa 1 kwa T/A Malengachanzi mboma la Nkhotakota wati kumeneko zinthu zaipa pomwe anthu akusowa kopezera ndalama chikhalirecho zinthu zikukwera mtengo. Tidayamba ntchito yolima msewu ndipo timalandira K300 patsiku koma pano ntchitoyo yayimanso ndipo sitikudziwa mutu wake. Kuno sitikudziwa kuti vuto lenileni kuti zinthu zidzivuta chonchi ndi chani. Izi zili choncho tikungomva kuti alowera uku kapena uko. Maulendo aonjeza, adatero Lunga. Abraham Kamanga wa mmudzi mwa Kandeya kwa T/A Kadewere mboma la Chiradzulu wati akuganiza kuti boma lidangowanyenga kuti anthu akumudzi salira ndikugwa kwa ndalama ya Kwacha ponena kuti pakhala zowatonthoza. Iye adati nzodandaulitsa kuti pamene mavuto akula, maulendo akudya ndalama ankitsa. Misewu yomwe imakambidwayo sitikulima, palibe chopezera ndalama. Thumba lachimanga lolemera makilogalamu 50 lafika pa K3 600 kuchoka pa K2 500. Chonsecho anthu osafunikira akuyenda nawo mmaulendo osawayanja, adatero Kamanga. Zinthu ngati madzi zikusowa Tifinesi Manjaaluso wa ku Embangweni ku Mzimba ndipo akuchita bizinesi ya zovala wati mavuto sadasiye phazi kumeneko pomwe kuli mavuto amadzi. Zinthu zikungokwera mtengo, madzi mmipope akusiya pena mwina Embangweni yonse zomwe zikutikakamiza kukamwa madzi osatetezedwa. Boma lichitepo kanthu, adatero. Mu mwezi wa Meyi chaka chino, boma lidatsitsa mphamvu ya Kwacha ndi K49 pa K100 iliyonse.
11
Idali nthawi ya mapemphero Mtsikana akadzakulembera SMS yoti I care for you ndiye kuti zatheka chifukwa uthengawu ndi waukulu kwambiri. Zidayambanso choncho ndi Alison Banda wa Dziko FM yemwe akukaveka mphete Chifundo Namale pa 30 July 2016. Awiriwatu akuti akhala akukumana nthawi ya mapemphero ku Calvary Family Church ku Falls mumzinda wa Lilongwe. Inde ndi nthawi ya mapemphero komabe Alison amaponya maso moti pa 30 July kuli kanthu ku Area 36 kulikulu la dziko lino. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Alison ndi Chikondi amangitsa woyera ku Lilongwe Mapemphero ali apo, Alison akuti mmutu mwake mudabwera mawu achikondi kuti akuyenera aponye pa namwaliyu. Zidatheka koma adamukana. Mphini yobwereza ndiyo imawala, adabweranso ndi nzeru zina koma namwaliyo adapukusabe mutu kukanitsitsa kuti sakufuna zachibwana. Mkazi adavuta kuti alole, amaona ngati poti ndine wotchuka sindili siliyasi, adatero Alison wa mmudzi mwa Kapindula kwa T/A Kaomba mboma la Kasungu. Ndidayata chikhulupiriro. Kenaka kudabwa wanditumizira uthenga ati wandisowa. Ine chiyani? Kenakanso watumiza uthenga wina ati I care for you. Ndidadziwiratu kuti basi ndawina mtima wake, adatero. Mosachedwa, akuti adapanga kaulendo kuti akumane ndi namwaliyu, yemwe ndi wa mmudzi mwa Gonjo kwa T/A Mthiramanja mboma la Mulanje, ndipo pa 19 February adakumana ndi namwaliyu kuseli kwa NBS Bank mumzindawo ndipo chibwenzi chidayamba. Chifundo amene ndi mphunzitsi kukoleji ya Exploits University akuti adalola Alison chifukwa cha khalidwe lake. Ndinene chiyani ine? Alison ndi munthu wolemekezeka, wokonda, wansangala, ndipo pali zambiri zomwe ndinganene zokhudza mnyamatayu. Pamene ndimati ndimudziwe kaye ndi pamenenso ndimagwera mchikondi, komanso amakonda Mulungu, adatero Chifundo.
13
Papa Wavomereza Mlozo Wa Maphunzitso A Mpingo Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wavomereza mlozo wa maphunzitso a mpingo komanso kafalitsidwe ka uthenga wa chipulumutso. Malinga ndi malipoti a Vatican Radio bungwe la ku likulu la mpingo ku Vatican lomwe limaona za chibalalitso cha mpingo mnyengo ino ya makono ndi lomwe latulutsa mlozowu. Mlozowu ukutsatira mlozo wina wa 1971 ndi 1997. Mlozowu ukutsindika zinthu zingapo; Poyamba mgwirizano womwe ulipo pakati pa kuphunzitsa anthu maphunzitso a Mpingo ndi kafalitsidwe ka uthenga wa chipulumutso. Kachiwiri mlozowu ukutsindika kuti mkhristu aliyense wobatizidwa ndi mmishonale woyenera kulalika ndi kufalitsa uthenga wa chipulumutso. Chigawo choyamba cha mlozowu chikukamba za aphunzitsi a uthenga wa chipulumutso ndi kufunika koti anthuwa azisulidwa kokwanira. Pamene chigawo chachiwiri cha mlozowu chikukamba za kaphunzitsidwe ka uthenga wa chipulumutsowu. Chigawo cha chitatu chikukamba za maphunzitso a Mpingo mma parish osiyana-siyana.
13
Ras Chikomeni sizidamukomere Pofika Lachisanu Ras Chikomeni Chirwa adali yakaliyakali kusakasaka K2 miliyoni kuti akapereke ku bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC). Izi zimadza pamene bungwelo lidabweza Chirwa ponena kuti adali asadapereke ndalamayo komanso adali asadasayinitse mmaboma 9 chomwe ndi chomuyenereza china. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chikomeni ndi mayi ake akuti alibe chilichonse Komabe Chirwa adati siwokondwa ndi zomwe MEC idachita chifukwa zidaonetsa kuti anthu olemera okha ndi amene akuyenera kuimira ngati pulezidenti wa dziko. Ndinabwera kudzaonetsa ufulu wanga koma akundikana chifukwa ndine wosauka. Sindingakwanitse kupeza ndalama imeneyo ndiye poti ndine wosauka andikanira, adatero Chirwa. Izi zidachititsa kuti bungwe la Centre for Human Rights Education Advice and Assistance (Chreaa) lilowere kubwalo lamilandu kukatenga chiletso kuti MEC ilandire mapepala a Chirwa. Mkulu wa Chreaa Chikondi Chijozi adati K2 miliyoni nchimodzimodzi kukaniza chirwa kuti asapikisane nawo pa mpando wa pulezidenti. Ndalama zachuluka ndipo uku ndikuletsa anthu osauka kuti asapikisane nawo koma olemera okha, adatero Chijozi. Lachisanu kudalinso zoseketsa pamene MEC idabwezanso Smart Swira wochokera mboma la Chitipa amene amafuna kupikisana nawo. Swira atafika ku holo ya Comesa adaseketsa anthu chifukwa adalibe wachiwiri wake ndipo amati wathamangira kuchipatala ndi mwana amene amati akudwala. Koma mkulu wa MEC Jane Ansah adakana kulandira makalata a Swira ponena kuti sadalembetse mkaundula wa zisankho, komanso alibe chizindikiro kuti ndi Mmalawi. Swira adati pachipanda MEC kumubweza bwezi atakwapula onse [amene akupikisana nawo pa mpandopo.
11
Chikondi cha nkhwangwa DPP, UDF akumana pachisankho chachibwereza Ubale wa pakati pa chipani cholamula cha DPP ndi chotsutsa cha UDF mNyumba ya Malamulo, womwe umaoneka ngati ukhala wa mpakana imfa kuwalekanitsa, wayamba kuwonekera mawanga ake. Zipanizi zanenetsa kuti aliyense aima payekha mchisankho cha makhansala chachibwereza chikubwera mwezi wamawawu. Kasaila: Aliyense aona za mchipani chake Mneneri wa chipani cha DPP, Francis Kasaila, wauza Tamvani kuti palibe mgwirizano uliwonse pakati pa zipani ziwirizi kunja kwa Nyumba ya Malamulo monga momwe anthu ambiri amaganizira. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Polankhua Lachitatu lapitali, Kasaila adati pachisankho chomwe chichitike pa 25 August, chipani chilichonse chili pachokha ndipo aimiriri awo adzakumana maso ndi maso. Aliyense aona za mchipani chake chifukwa mgwirizano womwe ulipo ndi wothandizana mNyumba ya Malamulo basi, osati kunja. Chipani chilichonse chipanga ganizo pachokha kuimitsa munthu kapena ayi, koma palibe zoimitsa munthu mmodzi [kuimira zipani ziwirizi], adatero Kasaila. Naye mneneri wa chipani cha UDF, Ken Ndanga, adati chipani chawo chikupanga zake pankhani yokhudza chisankho chachibwerezachi. Ndanga adati pakalipano atsogoleri a chipani cha UDF mmaboma akuyendetsa zonse zokhudza kukonzekera chisankhochi ndipo a kulikulu adzalandira maina a omwe adzaimire chipanichi posachedwapa. Palibe mgwirizano uliwonse wokhudza za chisankho. Ubale nku Nyumba ya Malamulo basi, kunja kuno aliyense ali ndi zake moti kukutsimikizirani pachisankhochi tidzaimitsa makandideti athu, adatero Ndanga. Katswiri wa za malamulo Edge Kanyongolo adati mgwirizano wa zipanizi sukuwamanga chifukwa sadasayinirane paliponse koma adangokambirana basi. Iye adati zipanizi zili ndi ufulu wosankha odzaziyimirira mmodzi kapena aliyense kukhala ndi odzaimirira wawo popanda chiletso chilichonse. Palibe chowamanga chifukwa mgwirizano wake sudalembetsedwe. Zili ndi eni ake kukambirana ndi kumvana chimodzi, adatero Kanyongolo. Mneneri wa bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC), Sangwani Mwafulirwa, adati bungweli silikhudzidwa ndi kasankhidwe ka opikisana nawo pachisankho. Ife sitilowerera nawo pankhani imeneyo. Chomwe ife timayangana nchakuti opikisana nawo ankhale ndi chizindikiro, basi, kaya akuima payekha kaya akuyimira chipani kapena mgwirizano, akuyenera kukhala ndi chizindikiro, adatero Mwafulirwa. Chipani cha UDF chidasankha kugwira ntchito ndi chipani cha DPP mNyumba ya Malamulo ndipo nkhaniyi idachititsa kuti mabungwe komanso zipani zina zipemphe sipikala wa nyumbayi kuti achotse aphungu 11 a UDF potsatira gawo 65 la malamulo a dziko lino, koma mpakana pano sipikalayu sadagamule chilichonse pankhaniyi. Gawoli limati phungu yemwe adali mchipani china panthawi yakusankhidwa kwake adzasiya udindowu ngati walowa chipani china chomwe chilinso mNyumba yomweyi. Mmodzi mwa akuluakulu a mabungwe omenyerera ufulu wa anthu, Billy Mayaya, adalembera kalata sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Richard Msowoya, kuti aphunguwo adaphwanya gawo 65 ndiye achoke mNyumbayi. Mneneri wa chipani cha MCP, Jessie Kabwila, naye adati mpovuta kuti aphunguwo akhalebe mNyumbayi chifukwa mbali yawo yeniyeni sikudziwika. Chipani cha UDF chidakana kuti aphungu ake asintha chipani koma adangoganiza zogwira ntchito ndi chipani cholamula cha DPP, basi. Chilengezereni nkhaniyi, chipani cha UDF chidalandidwa ufulu woyankhapo pankhani za boma ngati chipani chotsutsa boma mNyumba ya Malamulo. MEC idatulutsa ndondomeko ya momwe chisankho cha chibwereza cha mmadera 5 chidzayendere ndipo ikuyenera kumaliza kulandira zikalata za odzapikisana nawo pa 28 July uno. Mwafulirwa adati zokonzekera zonse zikuyenda bwino ndipo anthu ayembekezere chisankho chapamwamba ngakhale kuti bungweli lili ndi ndalama zochepa zoyendetsera chisankhochi. Chisankho chonse chimafunika K400 miliyoni ndipo ife tili ndi K141 miliyoni koma palibe chogwedeza chilichonse. Zonse zidzayenda bwinobwino, adatero Mwafulirwa. Mmadera momwe muchitike chisankhochi ndi Luchenza, dera la pakati ku Zomba, Msikiti ku Mangochi, Chibanja ku Mzuzu ndi Khwawa mboma la Karonga.
15
Wopanda chiphaso cha nzika sadzavotaMEC Bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) latsimikiza kuti chiphaso chakale chovotera sichidzanunkha kanthu pachisankho cha 2019. Wapampando wa komiti yoona zophunzitsa anthu ndi kumwaza mauthenga a kavotedwe Commissioner Moffat Banda wati mmalo mwake bungwelo ligwiritsa ntchito zitupa za unzika. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Iye wati iyi ndi njira yokhayo yomwe bungweli lingathanirane ndi zachinyengo zomwe zimapezeka panthawi yachisankho ndipo ndiyokomera anthu ndi zipani zonse. Njira yogwiritsa ntchito zitupa za unzika idzatithandiza kupewa anthu osafika zaka 18 kuti asadzaponye nawo voti komanso idzaonetsetsa kuti ndi Amalawi okhaokhadi omwe adzaponye voti, watero Banda. Iye wati apa, mpofunika kuti Mmalawi aliyense akalembetseretu ndi bungwe lolemba za unzika kuti asadzavutike panthawi yoponya voti kaamba koti zitupa zina zonse sizidzagwira ntchito. Koma mkulu wa bungwe loyanganira zamomwe zisankho zimayendera la Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa wati bungwe la MEC likhoza kudzikola lokha ngati siliyendetsa bwino za nkhaniyi. Duwa wati kugwiritsa ntchito ziphaso za unzika, ndi njira yothandiza kuchepetsa zachinyengo koma potengera malamulo oyendetsera zisankho, Amalawi akadali ndi ufulu ogwiritsa ntchito zitupa zosiyanasiyana. Malingana ndi lamuloli, munthu yemwe ndi Mmalawi ndipo adafika pamsinkhu woponya voti, akhoza kugwiritsa ntchito zitupa monga choyendetsera galimoto, choyendera mmaiko ngakhalenso kalata yochokera kwa amfumu, mbale wodalirika kapena kuntchito. Pokhapokha akumane nkusintha lamuloli msanga chifukwa malamulo omwe ife timadziwa amalola anthu kugwiritsa ntchito umboni uliwonse kuti ndi Amalawi choncho mposavuta ena ozindikira kudzatengera MEC kukhoti, adatero Duwa. Iye wati pakali pano bungwe la MEC likhoza kumalengeza zomwe lakonza popanda anthu kulankhulapo koma pamakhala ena akudikira kuti zinthu zikamadzapsa mpomwe adzayambe kusokosa. MEC izikonzeratu mokhota monse chifukwa sizingadzakhale bwino kuti nthawi yothaitha adzayambe kulimbana ndi anthu mmakhoti pankhani yophweka ngati iyi, watero Duwa. Zipani zina za ndale zati zilibe mangawa ndi bungwe la MEC chachikulu bungwelo lidzaonetsetse kuti munthu aliyense woyenera kuvota ndipo waonetsa khumbo, adzalandire mpata. Zanjirazo ife tilibe nazo ntchito koma tikungofuna kuti bungwe la MEC lidzapereke mpata kwa Amalawi ogwiritsa ntchito ufulu wawo oponya voti. Pasadzapezeke kuti nkhani yachitupa yalepheretsa munthu kuponya voti, watero Mlembi wa Malawi Congress Party (MCP) Eisenhower Mkaka. Mneneri wa chipani cha Peoples Party (PP) Noah Chimpeni adagwirizana ndi Mkaka kuti chofunika nchoti Amalawi asadzaphwanyiridwe ufulu wawo oponya voti. Nthawi ilipo, ngati akufunitsitsa kudzagwiritsa ntchito njira imeneyo, ndiye kuti awonetsetse kuti Amalawi onse apatsidwa mpata wolembetsa mkaundula wa unzika, adatero Chimpeni. Wapampando wa bungwe la MEC Jane Ansah adati bungwelo lakonza ndondomeko yoti munthu aliyense sadzamanidwa mpata malingana ngati watsatira malangizo. Tikudziwa kuti si Amalawi onse omwe angakhale atalembetsa pofika tsiku loponya voti komanso ena akhoza kukhala kuti adalembetsa koma zitupa zawo sizidatuluke onsewo tawaganizira. Tapanga njira ziwiri, yoyamba, omwe alembetsa koma chiphaso sichidatuluke adzabwere ndi tiketi yolembetsera imene idzatithandize kuwazindikira mkaundula, yachiwiri, pochita kalembera wathu tidzakhala ndi ogwira ntchito ku bungwe la kalembera wa unzika omwe azidzathandizira, adatero Ansah.
11
Anthu Atatu Achira COVID-19 Anthu atatu omwe ali mu gulu la anthu omwe anapezeka ndi kachilombo ka Coronavirus akuti atawayeza awapezeka kuti tsopano alibe kachilomboka mthupi mwawo. Watsimikiza za anthuwa-Mhango Nduna ya zaumoyo a Jappie Mhango amalankhula izi pomwe amapereka lipoti lokhudza momwe zinthu zikuyendera pa ntchito yolimbana ndi kachilomboka mdziko muno . Masiku asanu apitawa sitinalandire uthenga wina uliwonse okhuza matendawa ndipo titayeza palibe anapezeka nawo koma dzulo kwapezeka munthu mmodzi wa zaka 70, mu mzinda wa Blantyre yemwe wapezeka ndi matendawa, anatero a Mhango. Pamenepa ndunayi yati anthu atatuwa akuyembekezereka kukayezedwanso kachiwiri kuti astimikizidwe kuti achiladi. Iwo ati tsopano onse omwe apezeka ndi matendawa mdziko muno alipo 17 koma awiri mwa iwo anamwalira.
6
Chimanga kulibe amalawi adandaula ndi Admarc Pamene njala ikupitirira kukantha mmadera ena, zadziwikanso kuti mmisika ya Admarc yambiri mdziko muno mulibe chimanga ndipo anthu ku Ntcheu, Dedza, Mzimba, Chitipa ndi Blantyre alirira boma kuti lichitepo kanthu. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Anthu omwe alankhula ndi Tamvani msabatayi ati ndikale adagula kapena kuona chimanga ku Admarc, zomwe zikuwakakamiza kugula kwa mavenda pa mtengo wa K5 500 kusiyana ndi K3 000 yomwe amagulira thumba la makilogalamu 50 ku Admarc. Koma mneneri wa bungwe la Admarc, Agnes Chikoko adati timutumizire mafunso ndipo pomwe timalemba nkhaniyi nkuti asadayankhe. Ngakhale bungwe la Admarc lidalengeza mmbuyomu kuti pasapezeke ogula makilogalamu oposa 25 ku Admarc, wachiwiri kwa nduna ya zaulimi, Ulemu Chilapondwa wati dziko lino lili ndi chimanga chochuluka koma vuto ndilakuti chikakasiidwa ku Admarc mavenda ndiwo akumagula mwa machawi. Iye adati boma pakadali pano likuyesayesa kupeza njira zothana ndi mavendawa asadatumizenso china ku Admarc-ko. Chimanga changotha ku Admarc osati kulibe. Tili ndi matani 31 miliyoni omwe akusungidwa. Pasakhalitsapa tidatumiza matani 10 000. Vuto ndi mavenda, adatero Chilapondwa. Misika ya mmadera Titamupatsa madera omwe tapeza kuti mulibe chimanga iye adakana kuti sizingatheke. Florence Nsangu wa mmudzi mwa Chapita 2 kwa T/A Masasa mboma la Ntcheu ali ndi ana 8. Iye akuti pa chaka, banja lake limafunika matumba pafupifupi 20. Zaka za mma 2000 akuti matumbawa amawapeza akachita ganyu koma chifukwa cha kusintha kwa nyengo akulephera kukolola chimanga chokwanira. Zikavuta akuti amapeza asanu koma chaka chatha adapeza atatu chifukwa cha vuto la mvula ndipo pofika October chimangacho nkuti chitatha. Zikavuta chonchi kothamangira ndi ku Admarc chifukwa mtengo wake sukhala woboola mthumba. Koma ndakhala ndikupita ku Admarc ya ku Lizulu komanso ku Bembeke kukayangana chimanga koma kulibe. Tatopa ndikuyendera ndiye tikungogula mwa mavenda, adatero mayiyu yemwe akuti mu 2011 ndimo adagula chimanga ku Admarc. Iye wati akumachita ganyu yolimitsa kuti apeze ndalama yogulira chimanga koma zikavuta akugonera mbatata. Patsiku akumapanga K500 ndiye tikakhalapo angapo tikumapeza ndalama yochuluka komanso maganyuwo akusowa, adatero mayiyu yemwe adati boma liyike chimanga ku Admarc. Tamvani itayendera Admarc ya ku Lunzu komanso pa Matindi idapeza malowo otseka. Anthu omwe tidakumana nawo adati ngati tikufuna chimanga tikagule mwa mavenda chifukwa ku Admarc sichinabwere. Ena adati tipite pa Takondwa Commodities pamsika wa Lunzu komwe amati amagulitsa pamtengo wotsika. Pa Takondwa Commodities tidapeza anthu oposa 30 akufuna kugula chimanga. Pamenepo akuti amagulitsa K4 700 thumba la makilogalamu 50. Dolasi Kabotolo wa mmudzi mwa Manjombe kwa T/A Kapeni mboma la Blantyre tidamupeza pamenepo ndipo adati mwina apeza chipulumutso apo. Sindingakumbukenso tsiku lomwe ndidagula ku Admarc koma kawiri pa sabata ndimakapondako kukafunsa ndipo yankho lake nkuti chimanga kulibe. Ngati pa Takondwa chatha ndiye timalira kwambiri chifukwa timakagula kumsika komwe akupanga K5 500 pa thumba. Ngakhale apa chili chotsika komabe timavutika magulidwe chifukwa mavenda ndiwo amachuluka kudzagula, adatero Kabotolo yemwe ali ndi ana 6 ali pamzere. Panthawi yomwe timacheza naye nkuti akudikirira mkulu wina yemwe adabwera ndi galimoto ya matani awiri akugula matumba 15. Nako ku Dedza mavutowa akuti sadasiye malo. Rashida Mathews wa mmudzi mwa Mkajenda kwa T/A Tambala wati kumeneko adasiye kupita ku Admarc chifukwa chimanga chidasiya kufika mu 2011. Anthu akuvutika Gulupu Lodzanyama wa kumeneko watinso anthu akuvutika chifukwa cha kusowa kwa chimanga ndipo mwa mavenda mtengo wake sangakwanitse. Iye wati kumeneko kuli njala chifukwa anthu sapindula ndi fetereza wa makuponi. Sanudi Tambula wa ku Ulongwe mboma la Balaka wati kumeneko chimanga samagula ku Admarc koma mwa mavenda chifukwa ku Admarc sichibwera. Ku Mzimba nako akuti kulibe. Tomasi Manjaaluso wa mmudzi mwa Takumanapo kwa T/A Mzukuzuku wati anthu akugula kwa mavenda chifukwa chikabwera ku Admarc mavendawo ndiwo akumakagula. Charles Kabaghe wa mmudzi mwa Mkombanyama kwa T/A Mwaulambia mboma la Chitipa wati ku Admarc yakumeneko kulibe chimanga ndipo akumakagula ku Tanzania chifukwa kumeneko ndichotchipa. Ku Tanzania tikugula K1 500 thumba la makilogalamu 50. Kupita ndikubwera ndi K2 000 komabe nanga titani? adatero Kabaghe. Mwa madera ena ndi Nsanje, Chikhwawa, Chiradzulu, Mwanza, Neno momwe akuti mavutowa achuluka. Mwambiri akuti chimanga chikafika chimagulidwa ndi mavenda ndipo anthu wamba sakupeza mpata kuti agule. Izi zikudza pomwe kholola wa 2011/2012 amasonyeza kuti dziko lino tapata matani 3.9 miliyoni pomwe dziko lino limafuna matani 2.4 miliyoni. Mu kholola wa 2010/2011, dziko lino lidapata matani 3.2 miliyoni.
6
Ambuye Msusa Adzudzula Zipolowe Pa Ndale Mkulu wa mpingo wa katolika mdziko muno Archbishop Thomas Luke Msusa wadzudzula mchitidwe wa zipolowe zokhudza ndale zomwe zikuchitika mmadera osiyanasiyana mdziko muno. Msusa: Tili ndi nkhawa Ambuye Msusa omwenso ndi arkiepiskopi wa mpingo wa katolika mu arkidayosizi ya Blantyre amayankhula izi kwa Bvumbwe mboma la Thyolo pambuyo pa mwambo wa malumbiro oyamba a Sister Agnes Magombo a chipani cha Divine Providence. Tili ndi nkhawa kuti zitha bwanji chifukwa cha kampeni imene ikuchitika yomwe sikulemekeza ufulu wa munthu. Sikulemekeza kuti munthu atha kupita kulikonse kukapereka uthenga wake. Kuli nkhanza, ziwawa, kuononga zinthu zaena komanso kulemberana malire zomwe ndi zoipa ndipo ndikudzudzula mchitidwe umenewu chifukwa zinatha kalekale nthawi ya atsamunda, pano tili pa ufulu wa democracy, anatero ambuye Msusa. Ambuye Msusa mwapadera anayamikira bata lomwe linalipo bwalo la milandu linapereka chigamulo chake pa nkhani ya chisankho cha president zomwe akuti zikusiyana ndi momwe zinthu zilili padakalipano. Pamenepa ambuye Msusa adzudzulanso boma ndi zipani za ndale polephera kutsatira njira zabwino zopewera matenda a COVID-19.
14
Atatu Afa pa Ngozi Ziwiri ku Ntcheu Anthu atatu afa ndipo ena avulala modetsa nkhawa pa ngozi ziwiri zomwe zachitika masiku osiyananso mboma la Ntcheu. Malinga ndi wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sub-Inspector Hastings Chigalu, ngozi yoyamba yachitika usiku wa lachiwiri pa msika wa Biriwiri pafupi ndi msewu wochoka ku Dedza kupita ku Ntcheu pomwe galimoto inawomba anthu oyenda pansi omwe amawoloka nsewu-wu. Ndipo ngozi inayi yachitika usiku wa dzulo pa mlatho wa mtsinje wa Liwazi omwe uli pafupi ndi msika wa Kasinje mu nsewu wochoka ku Balaka kupita ku salima pomwe galimoto ya mtundu wa truck inaphonya nsewu ndi kugwera mu mtsinjewu. Zoonadi kuti pali Ngozi yomwe inachitika zulo usiku lachitiatu yomwe imakhuza galimoto ya BR8698 yomwe amayendesa a Moses Chikolosa azaka 30 anawomba anthu atatu pa Biriwiri Trading Centre ndipo anafera ku chipatala, anatero Sub Inspector Chigalu. Iwo atinso mu nsewu omwewu munachitikaso ngozi ina ya galimoto yomwe amayendetsa ndi a Davie Malamba a zaka 69 ndipo galimotoyo inagwera mu mtsinje zomwe zinapangitsa kuti mwa anthu 6 omwe anatenga, 5 avulale ndipo mmodzi wamwalira. Mwazina Sub Inspector Chigalu wapempha kuti oyendetsa galimoto azikhala chidwi ndi pa nsewu kuti apewe ngozi.
17
Chipatala chiutsa mapiri pachigwa Akuluakulu ena a khonsolo ya Lilongwe ndi kontilakitala yemwe akumamanga chipatala cha Biwi mumzinda wa Lilongwe, ayankha mafunso zitadziwika kuti pantchitoyi pakukhala ngati padayenda zachinyengo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nduna ya maboma angonoangono Kondwani Nankhumwa wanenetsa kuti ena anjatidwa pankhaniyi kafukufuku akatha. Chomwe chautsa mapiri pachigwa nchakuti chipatalacho chayamba kale kugwa mbali imodzi chisadathe komanso makoma ali mingalu yokhayokha. Nankhumwa (Kumanzere) sadakhulupirire kuona mmene ntchito ya Chipatala cha Biwi ikuyendera Nankhumwa adanenetsa kuti pantchitoyi, yomwe ndi ndalama zokwana K198 miliyoni, padayenda chinyengo chachikulu chomwe iye akuti ndi Kashigeti ndipo wati ofufuza akamaliza, onse okhudzidwa adzayankha mlandu wosakaza ndalama za boma. Polojekiti yaikulu ngati imeneyi idayamba bwanji popanda pulani iliyonse? Chimenechi ndiye chinyengo choyambirira. Chachiwiri, zidatheka bwanji kumusiya kontilakitala kuyamba kumanga mpaka kufika pokhoma malata osazindikira kuti akupanga chinyengo? adatero Nankhumwa akuthambitsa akuluakulu a khonsolo ya Lilongwe ndi mafunso Lolemba lapitali. Panthawiyi ndunayi idakayendera chipatalachi itamva kuti chagwa mbali imodzi ndipo mkati monse ndi mingalu yokhayokha komanso zitseko ndi zimbudzi zidaphotchokaphotchoka ngakhale kuti chipatalacho sichidathe. Iye adati unduna wake sulekera pomwepa koma ufufuza momwe kontilakitalayo adapatsidwira ntchitoyo ndi zonse zomwe zakhala zikuchitika pachipatalapo ndipo pakapezeka zachinyengo chilichonse, onse okhudzidwa adzazengedwa mlandu. Tikukamba apazi ndi ndalama zambiri zedi ndipo nzodabwitsa kuti nthawi yonseyi kontilakitala amagwira ntchito yosaoneka bwino ngati iyi akhonsolo adali kuti? Ichi nchinyengo chachikulu ndipo tifufuza mpaka ena azengedwapo mlandu apa, adatero Nankhumwa. Ndalama zomangira chipatalachi zidachokera kudziko la Japan ndipo Nankhumwa adati ndi momwe zakhaliramu, boma silikudziwa koti lingatenge ndalama zokonzeranso chipatalachi kuti chilongosoke. Mkulu wa khonsolo ya Lilongwe, Moza Zeleza, adavomereza kuti ntchito yomanga chipatalayo sidayendedi bwino ndipo kuti kontilakitala sadagwire nthawi yomwe amayenera kumaliza ntchitoyo. Iye adavomereza kuti ntchitoyo idagwiridwa mwa mgwazo, kontilakitala adagwiritsa ntchito zipangizo zosayenera, adaphonya nthawi komanso khonsolo idalephera pantchito yoyanganira kumangidwa kwa chipatalacho. Ntchitoyi sidayendedi bwino, ayi, moti tidakamangala kale kubungwe la a zomangamanga la Malawi Institute of Engineers (MIE) omwe adatipatsa chilolezo cholemba katswiri woti aunike bwinobwino chipatalachi ndi kutiuza choyenera kuchita, adatero Zeleza. Iye adati khonsoloyi singachitire mwina koma kudikira zomwe adzanene katswiriyo ngakhale kugwetsa chipatala chonsecho nkuyambiranso chifukwa momwe chilili, nchiwopsezo chachikulu kumiyoyo ya anthu. Zeleza adati chipatalachi chikadayenda bwino nkutha, chikadachepetsa chiwerengero cha amayi a mmadera asanu ndi awiri (7) omwe amayenda mtunda akafuna thandizo la chipatala. Ena mwa madera omwe akadapindula nawo chipatalachi chikadatha ndi Biwiyo, Area 36, Area 24, Area 22, Chipasula ndi Kaliyeka, madera omwenso kumachokera anthu ambiri mumzindawu. Kupatula chipatala cha Kawale, chipatala china chomwe anthu a mmadera asanu ndi awiriwa amadalira ndi cha Bwaila ndipo nchokhacho chomwe amayi oyembekezera a mmaderawa amakachilirako. Chiptala chomwe tikukamba panochi [Biwi], chidakakhalanso ndi malo ochilirako amayi, kutanthauza kuti mavuto ena monga othithikana ku Bwaila akadachepa, adatero Zeleza. Mneneri wa unduna wa maboma angonoangono Muhlabase Mughogho adati undunawu utakayendera chipatalachi koyamba chaka chatha udapeza kuti pansi ndi makoma mudali mingalu yochititsa mantha. Iye adati atatsina khutu akhonsolo, adapitako ndipo adakapeza ogwira ntchitoyo akutchinga mingaluyo ndi matayilosi komabe sizidathandize chifukwa matayilosi ena amapotoka pomata.
6
Boma Lati Lisamalira Anthu Okhudzidwa Ndi Mphepo Wolemba: Thokozani Chapola /wp-content/uploads/2019/09/botomani.jpg" alt="" width="211" height="239" />Wapereka ma 3000 kwacha kwa anthu okhudzidwa-Botomani Boma lati liwonetsetsa kuti anthu onse omwe nyumba zawo zidagwa ndi mphepo yankuntho kumayambiliro a Mwezi wa November chaka chino Mdera la Zomba Chisi Boma la Zomba alandire chisamaliro chokwanira Nduna ya zofalitsa nkhani a Mark Botomani anena idzi loweruka ku Zomba pomwe amayendera anthu a mdera la Group Village Headman Chingondo komanso Tchete mdera la Zomba Chisi omwe nyumba zawo zidasasuka ndi mphepo yamkuntho. A Botomani omwenso ndi phungu waku nyumba ya malamulo mdera la Zomba Chisi ati Nyumba 112 ndi zomwe zidawonongeka ndi mphepo ya mkuntho mderalo. Iwo atsimikizira anthu a mdera lawo kuti boma lipereka chisamaliro chokwanira monga chokudya kwa anthu okhudzidwawo Poyankhulapo mmodzi mwa anthu omwe nyumba yawo idasasuka denga a Laston Kachingwe akwa Group Village Headman Chingondo mbomalo ati adakumana ndi ngozi yampheyi madzulo apa 7 November pomwe Malata a nyumba yawo adachoka ndi mphepo ndipo khoma la nyumba lidawagwera ndi kuwavulaza mutu. Ndunayi yapereka thumba la ufa, mapepala aplastic komanso ndalama yokwana 3,000 kwa munthu wina aliyense yemwe adakhudzidwa ndi ngoziyo.
14
Milandu ya maalubino Izipita kukhothi lalikulu Milandu yokhudza kuphedwa kapena kusowetsedwa kwa maalubino tsopano akuti izikakambidwira mukhothi lalikulu lomwe lili ndi mphamvu yopereka chilango chokhwimirapo kuposa khothi la majisitireti lomwe chilango chomwe lingapereke nchochepa, Msangulutso utha kuvumbula. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Milanduyi sizitengera kuchepa kapena kukula kwake pofuna kuteteza maalubino, omwe miyoyo yawo ili pachiswe kaamba ka zikhulupiriro za anthu ena zoti mafupa ndi ziwalo za anthuwa ndi zizimba za mankhwala olemeretsa. Mneneri wa nthambi ya makhothi Mlenga Mvula wati ngakhale sadalandire kalata yotsimikiza izi, makhothi angonoangono a majisitireti ndi ovomerezedwa kusamba mmanja pankhani zotere kuti nkhothi lalikulu ligwire ntchito. Sindidalandire kalata iliyonse pankhani imeneyi koma kutengera momwe zinthu zilili pankhani yokhudza maalubino, mamajisireti ndi omasuka kusamba mmanja pamilandu yokhudza maalubino kuti khothi lalikulu ndilo limve ndi kupereka chigamulo ndi chilango, adatero Mvula polankhula ndi Msangulutso Lachitatu lapitali. Bwaloli tsopano lizizenga milandu yokhudza maalubino Iye adati mndondomeko za makhothi, khothi lililonse lili ndi mlingo womwe silingabzole popereka chilango ndiye potsatira madandaulo a anthu kuti kuzunza maalubino kukunka mtsogolo kaamba ka zilango zochepa, nkofunika kuti khothi lalikulu ndilo lizizenga milanduyi. Majisitireti sangapitirire mlingo wina wake popereka chilango, ndiye kutengera zilango zomwe anthu akufuna kuti ozunza maalubino azilandira, majisitireti akuyenera kutumiza mlanduwo kukhothilalikulu, adatero Mvula. Chitsanzo cha nkhaniyi chapezeka ku Mchinji komwe majisireti Rodwell Mejja Phiri wasamba mmanja pamlandu wa Zione Gabina Kamngola, wa zaka 25, yemwe akuzengedwa mlandu womuganizira kuopseza msuweni wake, Gertrude Ulaya, wa zaka 22, yemwe ndi wachialubino. Mneneri wa polisi ku Mchinji, Moses Nyirenda, wati Kamngola akumuganizira kuti adanena msuweni wakeyo kuti iye ndi ndalama ndipo akadakhala mwana wake akadamupha. Nkhaniyi akuti idaopsa msuweni wakeyo ndi mayi ake, Mary Ulaya, omwe adakadandaula kupolisi. Iye adati apolisi atafufuza za nkhaniyi, adatsegulira Kamngola mlandu woopseza munthu ndi mchitidwe womwe ungayambitse chisokonezo. Malinga ndi Nyirenda, majisitireti Mejja Phiri adanena kuti nkhaniyo idamukulira malingana ndi mlingo wa chilango chomwe angapereke ndipo mmalo mwake adapereka kalata ya limandi ndipo mayiyo ali ku Maula kuyembekezera kukaonekera kukhothi lalikulu ku Lilongwe. Titamufunsa ngati sikumulakwira wozengedwa mlandu waungono ngati uwu kumutumiza kubwalo lalikulu mlandu wake usanazengedwe kubwalo la majisitireti, Mvula adati pakhothi lililonse, munthu amalandira chilungamo mofanana chifukwa mbali zonse ziwiri zokhudzidwa zimakhala ndi mpata wonena mbali zawo ndipo chigamulo chimachokera pa zokamba zawozo. Zilibe kuti ndi khothi la majisitireti, khothi lalikulu kapena la Supreme, ayi. Kulikonse mbali zokhudzidwa zimapatsidwa mpata wonena mbali zawo ndipo chigamulo chimachokera pamenepo, adatero Mlenga. Iye adatsindika kuti nkhani yaikulu yagona pokhwimitsa chitetezo cha maalubino kuti anthu akaona zilango zikuluzikulu zomwe zikuperekedwa ayambe kukhala ndi mantha ndipo mchitidwe wozunza maalubino uthe. Potsirapo ndemanga, katswiri wa zamalamulo kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Edge Kanyongolo, adavomereza kuti mlandu wotere ndi mlandu waungono woyenera khothi la majisireti, koma zikutengera mfundo zomwe iye wagwiritsa ntchito posamba mmanja. Umenewu ndi umodzi mwa milandu ingonoingono potengera malamulo ogamulira milandu ndipo umayenera kugamulidwa ndi majisireti chifukwa chilango chake nchochepa. Ngakhale zili chonchi, zimatengera kuti iye wawonaponji pankhaniyo chifukwa pazifukwa zina akhoza kuutumiza kukhothi lalikulu, adatero Kanyongolo. Naye mlembi wa bungwe la maloya Khumbo Soko adagwirizana ndi kanyongolo ponena kuti majisitireti aliyense ali ndi mpata wofunsa chiunikiro cha khothi lalikulu ngati akuona kuti nkhaniyo ikuposa mphamvu zake. Posamba mmanja pa mlanduwo pa 3 June, 2016, Mejja Phiri adati adauzidwa kuti milandu yonse yamtunduwu aziitumiza kukhothi lalikulu kuti anthu opezeka olakwa azilandira chilango chokwanira. Gawo 88 (1) la milandu ndi zilango zake yokhudza mlandu woopseza munthu ili ndi magawo awiri omwe kaperekedwe ka chilango chake nkosiyana. Mlandu woopseza womwewu, munthu akhoza kumangidwa mpakana moyo wake wonse ngati adatchulapo za kupha, pomwe ngati adangoti ndikumenya poopsezapo, chilango chachikulu chomwe angalandire ndi zaka zitatu kundende, adatero Nyirenda. Iye adati chokhacho chotchula kupha ndi kutengera kuti woganiziridwayo adaopseza munthu wa mtundu womwe dziko lonse lapansi likudandaula kuti uli pachiwopsezo chachikulu ndi mlandu waukulu.
7
Akatswiri Adzudzula Anthu Opereka Chitseka Pakamwa Kwa Majaji Akatswiri pa ndale ati zomwe zamveka kuti anthu ena okhudzidwa pa mlandu wa chisankho amafuna kupereka chiphuphu kwa ma jaji omwe akumva mlanduwu ndi zomvetsa chisoni. Akatswiriwa George Phiri komanso Humphreys Mvula ati kupereka chitseka pakamwa kwa oweruza kuti adzagamule mokomera mbali imodzi, posatengera umboni omwe bwalo la milandu lalandira ndi chidzindikiro cha kuti akudziwa kuti sanapereke umboni wokwanira ndipo mlandu wawayipira. Mvula: Ndi zomvetsa chisoni komanso zochititsa manyazi Zikusonyeza kuwola kwa atsogoleri omwe tili nawo mdziko muno. Ngati akuchita izi ndiye kuti akudziwa kuti ndi olakwa pa mlanduwu, anatero George Phiri yemwe ndi mphunzitsi wa zamalamulo pa sukulu ya ukachenjede ya Livingstonia. Naye mkhalakale pa ndale Humphreys Mvula anati, Ndi zomvetsa chisoni komanso zochititsa manyazi kwambiri. Amenewa ndi maganizo oyipa, upandu komanso mtima wa usatana. Ndemangazi zikudza pomwe zadziwika kuti majaji akubwalo lalikulu la milandu omwe akumva mlandu wa chisankho akadandaula ku bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu mdziko muno la Anti Corruption Bureau (ACB) kuti pali anthu ena omwe amafuna kuwapatsa ziphuphu kuti adzagamule mlandu mowakondera.
11
Kusowa kwa shuga kudzetsa kulira kwa Amalawi Amalawi mdziko muno ati sakudziwa chomwe chikuchitika mdziko muno kotero boma likuyenera kubweretsa mayankho mwachangu zinthu zisadavute. Izi zadza pomwe mmizinda ikuluikulu yadziko lino ya Blantyre, Lilongwe ndi Mzuzu mudali mizere ya anthu ofuna shuga. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ndemangazi zadza msabatayi pomwe mavuto a kusowa kwa shuga adayala paliponse mdziko muno. Anthuwa ati boma likuyenera kuganizira moto wa anthu chifukwa ndiwo adasankha bomali kuti lidzitandiza zomwe akukumana nazo. Ruth Samikwa wa ku Ndirande mumzinda wa Blantyre wati kumeneko pofika Lachitatu amagula sugar woyera pa mtengo wa K400. Zinthu zavuta ndipo sindikudziwa ngati sitithawa mdziko muno. Shuga wa bulawuni adasowa kalekale pano yemwe akupezeka mwa apo ndi apo akupanga K400, adatero Samikwa. Thocco Loga wa ku Kawale mumzinda wa Lilongwe wati kumeneko ndiye zafika ngati akusaka mafuta agalimoto. Moyo wasinthiratu moti chifukwa tiyi ndidamwa kale. Shuga akupezeka koma uyambe wavutika ngati ukufuna umupeze ndipo akugulitsidwa pa K450, adatero Loga. Mwezi wangothawu shuga wa dziko lino wakhala akugwidwa ku Tanzania ndi maiko ena.
2
MEC Yati Yakonzeka Kuchititsa Chisankho Chapadera Bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati ndilokonzeka kudzachititsa chisankho chachibweleza kudela la ku madzulo kwa boma la Liiongwe pa 30 January chaka chino. Bungwe lake lakonzeka kuchititsa chisankho chapadera-Ansah Chisankhochi chidalepheleka kawiri konse potsatira imfa ya mmodzi mwa omwe ankayimila ku delali pa zisankho zapatatu za pa 21 May chaka chatha Mai Agnes Penemlungu a chipani cha UTM, komanso zipolowe zokhudza chisankhochi zomwe zinachitika mdelaro. Polankhula kwa atolankhani lolemba mu mzinda wa Lilongwe, wapampando wa bungwe-li Justice Dr. Jane Ansah anati bungwe la MEC lichita izi potsatira makalata awiri omwe owatsimikizira kuti delali kuli bata ndipo chisankhochi tsopano chitha kuchitika. Pakadalipano, bungwe la MEC latinso lidzachitsa chisankho chachibweleza ku ward ya Liwawadzi kumpoto kwa boma la Balaka pa 5 March chaka chino.
11
Chipatala cha Bangwe Chatsekedwa Chipatala cha Bangwe mu mzinda wa Blantyre chatsekedwa kutapezeka ogwira ntchito awiri omwe apezeka ndi kachilombo ka Coronavirus. Chikhala chotseka kwa masiku awiri Mkulu wa kuofesi yowona za umoyo mu mzindawo Dr. Gift Kawalazira watsimikiza za nkhaniyi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Iye wati anthu onse ozungulira derali tsopano akuyenera kumakapeza thandizo la mankhwala ku chipatala cha Limbe mmasiku awiriwa, pomwe a zaumoyo akhale akupopera mankhwala mchipatalachi. Kawalazira: ogwira ntchito awiri apezeka ndi kachilomboka Pa kawuniwuni yemwe tikuchita poyeza anthu tapeza kuti anthu awiri ogwira ntchito ku chipatala cha Bangwe apezeka ndi kachilombo ka Coronavirus. Choncho pa ndondomeko yake tikuyenera chipatalachi tichitseke tithiremo mankhwala kuti chiyambirenso kugwira ntchito pakatha masiku awiri, anatero Dr. Kawalazira. Iwo ati akugwira ntchito yofufuza anthu onse omwe anakhudzana ndi azachipatalawa kuti nawonso ayezedwe ngati atenga kachilomboka. Ogwira ntchito athu a zachipatala ndi ophunzira bwino ndipo nthawi zones amavala moziteteza kuti asapatsire ena matenda ndiye ngati pali anthu ena omwe akhudzana nawo, amenewo tiwafufuza kuti nawonso ayezedwe, anatero Dr. Kawalazira.
6
Mavuto a kusowa zipatala anyanya Gogo ndi chidzukulu paulendo wa makilomita 26 kukapeza thandizo la chipatala Ngakhale boma likuyesetsa kuti pofika 2016 likhale litamanga zipatala kuti anthu asamayende mtunda woposa makilomita 8 popita kuchitapala, Tamvani yapeza kuti ganizoli livutirapo kutheka chifukwa mpaka lero palibe chachitika mmadera ena. Izi ndi malinga ndi mavuto amene akhodzokera mmidzi kaamba kakusoweka kwa zipatala. Anthu akuyenda mitunda yaitali kupita kuchipatala. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Anthu amene apezeka ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ndiwo ali pamoto chifukwa akuyenera azipitapita kuchipatala kukalandira mankhwala otalikitsa moyo. Mu 2011 dziko la Malawi lidakhazikitsa lingaliro kuti pofika 2016 likhale litamanga zipatala kuti pasadzapezeke munthu woyenda makilomita oposa 8 popita kuchipatala. Anthu a mboma la Neno ndi ena mwa anthu a kumudzi amene akusowekera thandizo la chipatala. Midzi yoposa 34 mbomalo kwa gulupu Soka T/A Dambe akuyenda mtunda wautali kuti apeze thandizo la chipatala. Mmidzi ya Ntaja ndi Leketa amene achita malire ndi dziko la Mozambique, akuyenda makilomita 26 kuti akafike pachipatala cha Neno boma. Kuderali kulibe chipatala chachingono chomwe angapite. Gogo Emelesiya Piyo ali ndi zidzukulu zingapo zomwe amasamalira ndipo chimodzi mwa izo, makolo ake onse adamwalira ndi matenda a Edzi. Chidzukuluchi [sitichitchula dzina] chomwe chidasiyidwa chili ndi miyezi iwiri, chidabadwa ndi kachilomboka. Mwanayu pano akusamalidwa ndi agogo akewo ndipo amayenera kuyenda makilomota 26 kuti akafike kuchipatala cha Neno kuti akalandire mankhwala otalikitsa moyo a ARV. Ndimadzuka 4 koloko ulendo kuboma la Neno kukatenga mankhwala. Tikanyamuka 4 mbandakucha timakafika mma 4 koloko madzulo. Pamene ndikupita ndimatengeratu chofunda komanso chakudya chifukwa ndimakaphikira komweko. Tikalandira mankhwala timapempha malo kuchipatala komweko kuti tigone, mmawa timadzukirira kumabwera kumudzi. Mwanayu ndimayenda naye chifukwa ndikamusiya palibe angamusamale, adatero gogoyu yemwe ali ndi zaka 75. Nkhawa yanga imakhala poti mankhwalawo kulibe. Ngati kulibe ndimayenera ndidikire mpaka atapezeka chifukwa ndikamadzafika kuno miyendo imakhala yatupa moti sindingapitenso. Pemphero la gogoyu ndilakuti akhale ndi moyo kuti asamale chidzukulu chake: Mulungu akadandilola kuti ndisafe mpaka mwanayu atasinkhuka, bola atangofika poti akuyenda yekha kukatenga mankhwalawo kuchipatala. Mneneri wachipatala cha Neno Ganizani Mkwate akuti kaamba ka mavuto amene anthuwa akukumana nawo, iwo pamodzi ndi thandizo la Partners in Health ayamba kuyendera midziyo kuti aziwathandiza ngati pafunika. Timapita komabe thandizo lenileni silikuwafikira. Kwambiri timapita nthawi yomwe mvula kulibe chifukwa ngati kuli mvula galimoto singayende. Anthu akukumana ndi mavuto moti kuwayankha mavuto awo ndikungowamangira chipatala chachingono, adatero Mkwate yemwe akuti akanyamuka 6 koloko mmawa pa galimoto amakafika mma 1 koloko masana. Ndizovutabe nanga atakhala kuti munthu wadwala mwadzidzidzi angafike bwanji kuno? adadabwa iye. Achikhala ganizo la boma linali zochitika, lero sibwenzi gogo Piyo akukhumata akaona chidzukulu chawo. Mmalo moyenda masiku awiri kuchipatala bwezi akugwira ntchito zina. Mwandipeza ndikuchokera ku Mozambique komwe ndimakalimitsa chakudya, sindilola kuti mwanayu agone ndi njala chifukwa amayenera adye asanamwe mankhwala, akutero gogoyu. Kodi ganizo la bomali lili pati? Mneneri muunduna wa zaumoyo Henry Chimbali adati ntchito ili mkati komabe palibe chipatala chamangidwa. Lingaliro lathu timati kuyambira 2013 ndi 2014 tikhale titamanga zipatala 15, koma nzachisoni kuti palibe chipatala tingaloze kuti chatha. Izitu zachitika chifukwa cha kusowa kwa ndalama, adatero Chimbali. Kodi ganizo loti pofika 2016 anthu asamadzayenda makilomita 8 litheka? Chimbali akuyankha: Zikhala zovuta chifukwa cha mavuto a zachuma amene takumana nawo. Ngati zipatala 15 sizinathe, ndiye zivutirako komabe patakhala ndalama mwina ntchitoyi ingagwirike mwachangu. Ndondomeko ya zachuma ya 2014/2015 mwina ndiyo idakapereka chiyembekezo kwa anthuwa koma kuyangana ndalama zomwe zaikidwa ku unduna wa zaumoyo ikuwonetseratu kuti mavuto sangathe lero. Mndondomekoyo, undunawu udalandira K65.2 biliyoni mmalo mwa K130 biliyoni kuti ikonzere mavutowa. Mkulu wa bungwe loona zaumoyo la Malawi Equity Network (Mhen) Martha Kwataine chiyembekezo palibe ndipo anthu ngati a ku Neno apitilira kuvutika. Mndondomeko yapita, undunawu udalandira 12 pa 100 ya ndalama zomwe zidayikidwa mndondomeko yazachumayo, pano tabwerera mmbuyo pamene undunawu walandira 8 pa 100 ya ndalama zomwe zayikidwa mndondomekoyi. Mavutowa angathe ngati boma litakwanitsa lingaliro lathu kuti unduna wa zaumoyo ulandira 16 pa 100 ya ndalama zomwe zili mndondomeko ya zachumayo. Koma momwe zililimu ndiye basi tidikire nthawi ina, adatero Kwataine mokhudzidwa ndi mavuto a ku Neno. Kufotokoza kwa Kwataine ndiye kuti anthunso a ku Chikwawa mmudzi mwa Kaloga kwa T/A Ngabu akuyenera kudikira ndondomeko ya zachuma ya 2015/16 kuti apume ku mavuto adzaoneni amene akukumananawo. Iwo akuti amapita kuchipatala cha Chipwaira Health Centre chomwe chili pa mtunda wa makilomita 28. Malinga ndi Lucia Dauleni wa mmudzi mwa Kudzanji akuti ngati pa chipatalapa sathandizidwa, amapita kuchipatala cha Ngabu chomwe ndi makilomita 33.
6
Ambuye Stima Apempha Akhristu, Ansembe Azivala Zozitetezera ku COVID-19 Episkopi wa dayosizi ya mpingo wa katolika ya Mangochi ambuye Montfort Stima wapempha akhristu mu dayosizi-yi kuti adzivala chotchinga kukamwa ndi mphuno pomwe akukasonkhana ndi anzawo nthawi ya mapemphero kuti adzitetedze ndi kutetedza ena ku kachilombo ka Coronavirus. Stima: Nambala ya omwalira ikukwera Ambuye Stima alankhula izi mu uthenga wawo wapadera wolimbikitsa njira zopewera kachilomboka. Iwo atinso pamene muthu akunva zizindikiro kapena kupezeka kumene ndi kachilomboka akuyenera kukhala pakhomo ndikuleka kukasonkhana ndi anzake, ndi cholinga choti atetedze ena ku kachilomboka. Nambala ya anthu omwalira ikukwera, nambala ya anthu omwe matendawa awapeza ikukweranso ndiye zoyezeranso akuti zikutha. Ndiye tiyeni tipitirize kumvera malangizo a akulu athu a zaumoyo nthawi zonse. Tikakhala mtchalitchi muja tivale mask. Kwa amene akudwala, asabwere ku tchalitchi kuno alandira Ambuye Yesu mu uzimu. Palibe cha nzeru kuti upite ku tchalitchi ukapereke matenda kwa ena, anatero AMbuye Stima. Iwo ati tsopano nthawi yakwana kuti anthu azindikire kuti matendawa alikodi ndipo si nkhani ya nkhambakamwa.
6
Likwata: Amuna aimba ngoma, amayi navina Likwata ndi mmodzi mwa magule amene amavinidwa pakati pa Ayao. BOBBY KABANGO adali mboma la Chiradzulu mmudzi mwa Njeremba kwa T/A Mpama komwe adapezerera gule wa likwata, yemwe ena amamutcha kuti namkwakwala. Uyutu ndi gule amene amavina amayi komanso atsikana. Kodi uyu ndi gule wanji? Nanga adayamba liti? Mtolankhani wathuyu adakokera pambali mayi amene amatsogolera guleyu. Adacheza motere: Eee! Wefuwefu ameneyu kutopa kumene? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Hahaha! Padalitu ntchito pamene paja. Si maseweratu kuvina gule ameneyu chifukwa akafika pakolasi timayenera tidzipinde basi. Tidziwane kaye. Ndine mayi Idesi Chiwaya, ndipo ndipo ndimatsogolera gululi. Kodi ndi gule wanji ameneyu? Ameneyu ndi gule wa namkwakwala, ena amati likwata. Cholinga cha guleyu nchiyani? Kusangalatsa anthu basi. Timavina tikasangalala monga zachitikira leromu kuti tangosangalala ndiye tidakumana kuti tivine basi anthu adyetse maso. Muli akazi okhaokha bwanji? Ameneyu ndi gule wa amayi, nchifukwa chake simudaonemo mwamuna kupatula awiri amene akutiimbira ngoma. Ndaonamonso tiasungwana, timeneti timaloledwanso kukhala mgulumu? Eya, amenewo ndiye eni gululi chifukwa ife takulatu ndiye timakhala nawo kuti Mulungu akatitenga iwowo ndiwo adzatsogolere gululi. Sitikufuna kuti gule ameneyu adzafe. Kodi guleyu saphunzitsa zoipa? Zoipa zanji? Ayi, ameneyutu ntchito yake ndi kusangalatsa anthu basi. Simukuona kuti guleyu angapangitse kuti tianamwali tija tisodzedwe mwachangu? Hahaha! Musandiseketse inu, amene aja ndi adzukulu anga. Ndimawayanganira ndipo palibe angachite zopusa ndi ana amenewa. Akukula mmanja mwanga. Dzina limeneli lidabwera bwanji? Dzina la guleli? Liti lomwe mukukamba? Ndikukamba la likwata Ndi dzina basi, kusonyeza gule wachikhalidwe pamene ena amati gule wa namkwakwala. Chifukwa chiyani kulipatsa dzina la likwata? Basi, nawonso makolo adakonda kuti apereke dzinali. Si zolaula zimenezi? Nanga mpaka likwata? Ayi, palitu maina a anthu ambirimbiri mdziko muno omveka ngati akulaulanso, kodi ndiye kuti anthuwo amachita zomwe dzinalo limatanthauza? Ife mukanena kuti likwata timatanthauza kuti ndi gule wosangalatsa basi. Kodi ndi gule wa chikhalidwe chiti cha anthu? Uyu ndi gule wa Anyanja. Ambiri akhala akunena kuti ndi wa Alhomwe, koma zoona zenizeni ndi zomwe ndikunenazi. Mavinidwe a guleyu andimaliza, tafotokozani momwe muchitira pamene mukuvina Ngoma ija ikamalira, ife timavina moitsatira uko tikuimba nyimbo zathu. Ndiye ikafika pakolasi, timachita ngati tikudumpha uko tikudula chiuno. Apa ndiye timagwadirira pansi ndi kuvina momatembenuka koma kumatembenuka ndi maondo kwinaku tikugundana ndi matako. Aka ndiye kavinidwe kake. Adakuphunzitsani ndani? Makolo athu. Ineyo makolo anga ankavina kwambiri ndipo atamwalira ndidapitiriza mpaka kupeza amayi anzanga. Tonse tilipo 10 kuphatikizapo ndi abambo a ngoma takwana 12. Abambo savina nawo chifukwa chiyani? Aaa! Inuyo mungakwanitse zomwe timachita zija? Eetu, nchifukwa timavina amayi okha. Mudayamba liti kuvina guleyu? Chaka ndiye sindingakumbuke koma ndimakumbukira kuti panthawiyo ndidali ndi zaka 33. Pano zaka zanga ndidaziiwala koma zaposa 50. Mumavina nthawi yanji? Timavina masana, moti nthawi zambiri timavina pazochitika monga pamisonkhano. Tavinirapo mtsogoleri wakale Bakili Muluzi komanso Bingu wa Mutharika. Atsogoleriwa amakwanitsa kuduka mchiuno chonchi? Ayi, amangochoka pampando ndi kumavina pangonopangono ndipo mapeto ake amapisa mthumba kutipatsa kangachepe. Kodi momwe munavinira apamu ndiye kuti mumathera pamenepa? Ayi, apatu tangovina kwa mphindi 5, koma tikati tivine moposera mphindi zimenezi mudakaona momwe timachitira. Malangizo kwa amene satsatira gule wa makolo Amenewo azikhala pafupi ndi makolo awo kuti asataye chikhalidwe cha makolo awo.
9
Ambuye Tambala Ayamikira Asisteri a Daughters of Wisdom Kamba ka Chitukuko Dayosizi ya mpingo wa katolika ya Zomba, yayamikira asisiteri a chipani cha Daughters of Wisdom kaamba ka ntchito zomwe akugwira mu dayosiziyo. Bishop Tambala kudula duwa kusonyeza kutsekulira nyumbazo Episkopi wa dayosiziyi Ambuye George Desmond Tambala ndi omwe anena izi pa mwambo wolandira nyumba za tsopano zokhala anthu ogwira ntchito pa chipatala cha Mayaka chomwe chimayendetsedwa ndi asisteri a chipanichi.
13
Mawu supports non-fiction writers The Malawi Writer Union (Mawu) has thrown its weight behind the establishment of a separate writers body, the Malawi Union of Academic and Non-fiction Authors (Muana). Muana is the third body of writers after Mawu and the Poetry Association of Malawi (Pam). Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Sambalikagwa Mvona With support from the Norwegian Non-Fiction Writers and Translators Association, the new body was established to promote non-fiction and academic research and publication after noticing that Mawu and Pam were mainly promoting fiction writing. As Mawu we are happy with the establishment of the new body. In fact, it did not come as a surprise as we have been part of a series meetings that have given birth to Muana, explained Mawu president Sambalikagwa Mvona. He said despite that, it has affected the Mawu membership, he is happy as the establishment of a new body is a step in the right direction. We have lost a few of our members, but in the positive because they have formed an equally important body. This is good for the nation and we are empowering others to grow wings, he said. Muana is headed by Max Iphani, who is book editor at the Malawi Institute of Education. Some of Muanas goals include ensuring that there is sound professional and legal relationships between authors and publishers, assist authors in publishing contracts as well as striving to build capacity of non-fiction and academic authors and lobby for increased numbers of Malawian textbooks in institutions of learning.
3
Apempha Amayi mu Dayosizi ya Dedza Akonde Kuwerenga Baibulo Amayi a chikatolika mu dayosizi ya Dedza awapempha kuti adzikonda kuwerenga mawu a Mulungu. Mlangizi wa bungwe la amayi mu dayosiziyi, bambo Peter Kasonkanji ndi omwe anena izi ku parishi ya Ntcheu pa msonkhano wa nthumwi za bungweli kuchokera mmaparishi onse amu dayosiziyi. Iwo ati munthu akamakonda kuwerenga mawu a Mulungu amakhala wa mtendere mu mtima ndiponso amakulitsa chikhulupiriro chake mwa Mulungu. Dayosizi iliyonse mMalawi muno, gulu la amayi tinakhazikitsa kuti amayi onse asulidwe ndipo aphunzitsidwe kuwerenga baibulo ndipo tinayitana bambo Anthony Kadya-mpakeni omwe ndi mphunzitsi wa za baibulo ku Zomba ku St. Peters ndipo aphunzitsa atsogoleri amenewa amene akaphunzitsire anzawo, anatero bambo Kasonkanji. Polankhulapo mayi Prisca Nasiyaya anati maphunzirowa anali ofunikira kwambiri kaamba koti amayiwa adzindikira kufunika kowerenga baibulo. Ansembe atatu omwe ndi bamboo Peter Kasonkanji, bambo Gift Selemani komanso bamboo Anthony Kadyampakeni ndi amene asula amayiwa.
13
Nthalika amema mamembala a CMO Kuti Achilimike Wolemba: Sylvester Kasitomu wp-content/uploads/2019/09/nthalika.jpg" alt="" width="330" height="247" />Wapempha bungwe la abambo lichilimike mu mpingo-Nthalika Bambo mfumu a parishi ya Nthawira mu arkidayosizi ya Blantyre bambo Elizeo Nthalika loweruka alimbikitsa bungwe la abambo la Catholic Men Organization (CMO) ku Holy Trinity Matawale Parish mu Dayosizi ya Zomba kuti lidzitenga nawo gawo padzochitika-chitika za mpingowu. Bambo NTHALIKA alankhula izi pa mbindikiro wa tsiku limodzi wa bungwe la abambo la Catholic Men Organization (CMO) a mparishiyo. Iwo ati abambo ali ndi udindo waukulu mu zochitikachitika za mu mpingo kotero ndikofunika kuti adzikhala patsogolo pazochitika zilizonse mu mpingowu. Azibambo ali ndi gawo lalikulu mumpingo kaamba koti iwo ndi amene ali mutu wa mawanja awo ndiye akuyenera kuti akhale patsogolo kulimbikitsa akazi awo kutenga nawo gawo mu zochitika chitika zamumpingo, anatero bambo Nthalika. Poyankhulapo wapampando wa Bungwe la abambo la ku Holy Trinity Matawale Parish dayosizi ya Zomba a Nicholas Mwisama ati anakonza ndi cholinga chofuna kuti Bambo wina aliyense adziwe udindo wake mu Mpingo. Abambo akuyenera kudziwa kuti iwo ali ngati mutu wa mpingo ndipo akuyenera kukhala patsogolo kuphunzitsa anthu onse zabwino zachikhristu monga kutenga nawo gawo mmiyambo ngati iyi anatero a Mwisama. Mwazina mbindikorowu unasonkhanitsa nthumwi za mbungwe la abambo ochokera mu ma tchalitchi onse amuparishiyi.
13
MCP, UTM asainira mgwirizano Kudali khwimbi la anthu ku Kamuzu Institute for Sports ku Lilongwe Lachinayi pomwe zipani zotsutsa zimasayinira mgwirizano wawo motsogozedwa ndi Lazarus Chakwera wa Malawi Congress Party (MCP) ndi Saulos Chilima wa UTM Party. Mumgwirizanowu muli zipani za MCP, UTM Party, Peoples Party, Aford, Mafunde, Umodzi Party, Petra, Freedom Party ndi PPM. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chakwera ndi Chilima kupatsana moni Kadaulo pa ndale George Phiri wati mgwirizano wangati umenewu sudachitikeponso mdziko la Malawi ndipo iye adati zipanizi zikapitirira kuyenda limodzi chonchi, palibe chokaikitsa kuti adzapambana pachisankho chobwereza chomwe chikubwera mtsogolomu. Mukakumbuka, ndidanenapo mmbuyomo chisadachitike chisankho cha pa 21 May 2019 kuti mgwirizano wa zipani za MCP ndi UTM ndiwoopsa ndiye pano tikunena za zipani zingapo, amenewo simasewera, adatero Phiri. Padakalipano, minofu ya mgwirizanowo ikadali yobisika ndipo yemwe adayendetsa mwambowo Richard Chimwendo Banda adati pakhala tsiku lapadera lomwe zipanizo zidzalengeze momwe maudindo akhalire mumgwirizanowo. Mgwirizanowo adasayinira ndi Chakwera ndi Chilima komanso alembi a zipanizo Eisenhower Mkaka ndi Patricia Kaliati ndipo mtsogoleri wakale wadziko lino Joyce Banda adasayina ngati mboni ya MCP pomwe Enoch Chihana wa Aford adasayina ngati mboni ya UTM Party. Chakwera ndi Chilima onse polankhula kwa khwimbiro adati tsiku losayinirana mgwirizanowo lidali potembenukira pa dziko la Malawi kuchoka mmavuto adzawoneni nkuyamba kulunjika ku dziko la mkaka ndi uchi. Chilima yemwe adayamba kulankhula adati ulendo omwe mgwirizanowo udayamba ndi wopita ku nyumba ya boma kuti akayendetse dziko mwangwiro. Ulendo wathuwu tikulowera kunyumba ya boma. Mmodzi mwa ife akakhala kumeneko chifukwa ulendo uno palibe zoti wina abera chisankho. Tamva kale kuti akuyesayesa njira zoti akoke mphamvu za mafoni kuti azikazisokonezera ku nyumba imene ija pachisankho, adatero Chilima akuloza nyumba ya boma ya ku Lilongwe. Chakwera adatsimikizira anthu kuti nthawi yotenga boma yakwana ndipo adawalimbikitsa kuti asadandaule chilichonse. Iye adadzudzula zomwe adapanga mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika pokana kusayina mabilu oyendetsera chisankho komanso kunyazitsa komiti yoona zosankha anthu mmaudindo ena mboma (PAC) pokana kuchotsa makomishona a MEC. Chavuta apa nkufunitsitsa kudzikundikira mphamvu ngakhale mphamvuzo zikuwakana. Chomwe timadziwa ife nchoti mphamvu ndi za wanthu ife atsogoleri ndi wongotumikira, adatero Chakwera. Iye adatenga kanthawi kuphunzitsa anthuwo za matenda a coronavirus.
11
Amayi akhale odzidalira Mkulu wa bungwe la Beautify Malawi Trust (Beam Trust), Gertrude Mutharika, walimbikitsa amayi mdziko muno kuti akhale odzidalira pachuma. Mutharika adalankhula izi masiku apitawa pomwe amakhazikitsa tsiku lokumbukira ntchito za mabizinesi la World Entrepreneurship Day mdziko la Amerika.stevggg Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mutharika adati Beam Trust ikufuna kulimbikitsa amayi kutengapo gawo lalikulu pantchito za mabizinesi ngati njira imodzi yowalimbikitsira kudziyimira paokha. Tayika ndondomeko zingapo zomwe cholinga chake nkupititsira amayi ndi atsikana mmabizinesi. Beam Trust ilimbikitsanso amayi ndi atsikana kutengapo gawo lalikulu pantchito zolimbikitsa ukhondo mmatauni ndi mizinda, adatero iye. Iye adatsindika kuti kusowa mpamba woyambira bizinesi ndi chikole ndiye mavuto amene amayi ndi asungwana omwe akufuna kuyamba mabizinesi akukumana nawo mu Africa. Choncho, iwo adapempha mabungwe omwe ndi mabanki kuti aganizire kufewetsa mfundo zawo kuti amayi ndi atsikana adzitha kupeza ngongole mosavuta. Ena mwa atsogoleri omwe adakhala nawo pamsonkhanowo ndi mkazi wa pulezidenti wa ku Namibia Penehupifo Pohamba ndi mkulu wa bungwe la UN Foundation Cathy Calvin.
2
Libya Yakhululukira Akayidi 400 Dziko la Libya lamasula akayidi okwana 4 Hundred okhala mu ndende zamdzikolo pofuna kuchepetsa kuthinana kuti apewe kufala kwa kachilombo ka Coronavirus mndende za mdzikolo. Malipoti a wailesi ya BBC ati Libya ndi dziko lokhalo lachiluya lomwe lawonetsa chidwi pomasula akayidiwa ndi kuwateteza kuti asapatsirane kachilomboka. Dziko la Libya lachita izi pofunanso kugwirizana ndi maiko ena omwe achitapo kale kanthu pomasula akayidi mdende za mmaiko awo monga Saudi Arabia, Brahrain, Iran, Syria komanso Egypt. Mwa akayidi omwe atulutsidwawa anthu omwe anapalamula milandu pa nkhani za ndale ndi ochepa kuyerekeza ndi omwe anapalamula milandu ina mdzikolo. Magulu omenyera maufulu a anthu mdzikolo ayitanidwa kuti akalandire abale awo omwe anamangidwa ndipo omwe ali mu gulu la anthu omwe amasulidwawa.
14
Apolisi akupitirirabe kuphwanya malamulo A polisi atatu agwidwa ndi kutsekeredwa mchitolokosi chawo chomwe mumzinda wa Zomba powaganizira kuti adathandizira mayi wina yemwe akuti adaba ndalama mdziko la South Africa kutuluka mchitolokosi. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Apolisiwa ndi Sub Inspector Khudze, Sergeant Mbalame ndi Mankhwala omwe akuganiziridwa kuti adathandiza mayiyo yemwe akuti adaba ndalama zokwana pafupifupi K17 miliyoni kwa bwana wake mdzikolo. Izi zidachititsa apolisi a dzikolo kulumikizana ndi a dziko lino omwe mwaukadaulo wawo adamugwira mayiyo, koma ena mwa apolisi omwewo akuti adapezerapo mwayi wotakata ndipo anamutulutsa mwamseri. Ndipo ku Zomba konko wapolisi wina ,yemwe akungodziwika kuti Kalipinde, adamangidwanso poganiziridwa kuti adachita zakatangale. Izitu zachitika patangodutsa sabata imodzi wapolisi winanso, Constable Kamoto atatsekeredwa mchitolokosi cha polisi ya Soche mumzinda wa Blantyre pomuganizira kuti adasowetsa mfuti ataledzebwa pamalo ena omwera mowa. Pakadalipano apolisi akuti mfuti idasowayo idapezeka. Ngakhale izi zikuchitika, anthu mdziko muno amadalira apolisi pankhani yosungitsa lamulo komanso chitetezo. Kwa zaka zingapo tsopano, apolisi akhala akupezeka ndi milandu yosiyanasiyana, monga kulowetsa anthu omwe alibe ziphaso mdziko muno podzera njira zosavomerezeka, umbava ndi umbanda komanso kuzunza ena mwa anthu omwe amagwidwa akuyenda usiku. Ndipo nthawi yonseyi, boma komanso akuluakulu awo akhala akutsimikizira mtundu wa a malawi kuti izi zikhala mbiri yakale kaamba koti kagwilidwe ntchito ka apolisiwa kanaunikidwanso. Polankhulapo mneneri wa polisi mdziko muno James Kadadzera adavomereza kuti ena mwa apolisi akupitirizabe kuswa malamulo ndi kusasunga mwambo. Kadadzera adati koma akuluakulu a apolisiwa sakusekerera izi ndipo akulanga opezeka akuswa malamulowo pogwiritsa ntchito njira ziwiri. Iye adati ena akumalangidwa pogwiritsa ntchito njira zawo za polisi pomwe ena akumalangidwa pogwiritsa ntchito malamulo a dziko lino. Mwachitsanzo apolisi anayi omwe sindiwatchula maina awo, adatsekeredwa mumzinda wa Zomba titalandira dandaulo lakuti adakhudzidwa ndi zakatangale, ndipo alangidwa potengera malamulo a dziko lino, pomwe Kamoto akulangidwa pogwiritsa ntchito malamulo athu, adatero Kadadzera. Iye adakana kuyankhulapo mwatsatanetsatane za milandu ya anayiwa. Kadadzera ngakhale izi zili chomwechi, chiwerengero cha apolisi opezeka akupalamula chikuchepera. Koma musaiwale kuti ngakhale alipo apolisi omwe akugwira ntchito yawo molimbika ndi modzipereka, aliponso ena omwe akuswa malamulo. Choncho tili ndi nthambi yoyangana kagwiridwe ka ntchito mwaukadaulo ya Profession Standard Unit (PSU) yomwe ikulimbikitsa kusunga mwambo mupolisi, adatero Kadadzera. Ndipo nduna ya za mdziko Grace Chiumia adati atsirirapo bwino ndemanga pankhanizi akamva tsatanetsatane wa nkhani zomwe zidachitika ku Zombazi kuti akhale ndi umboni wonse. Sindidalandire lipoti lililonse lokhudza nkhani za ku Zombazi. Ndifufuze kaye kuti zidayenda bwanji, adatero Chiumia. Koma mkulu wa bungwe lopereka upangiri ndi thandizo pa maufulu a anthu la Centre for Human Rights, Education, Advice and Assistance(CHREAA), Victor Mhango, adati mchira wanyani udakhota pachiyambi pomwe ena mwa apolisiwa ankalembedwa ntchito. Mhango adati ambiri adalowa ntchitoyi chifukwa chodziwana ndi ena mwa andale ndipo alibe chidwi chenicheni chogwira ntchito yachitetezo koma kudzilemeretsa. Iye adati enanso mwa apolisiwa amaona ngati lamulo silingawakhudze ndipo akhoza kupalamula ngakhale kuzunza anthu umo angathere popanda kulandira zilango zamtundu uliwonse. Akavala yunifolomu ija ndi kutenga unyolo mmanja amaona ngati basi palibe angawakhudze, adatero Mhango. Iye adati nzamanyazi kuti ena mwa apolisiwa akumafika pamlingo wochita nawo za umbava ndi umbanda mmalo moteteza anthu.
7
Sukulu za Katolika Zikhale ndi Zizindikiro Ofesi yowona za maphunziro mu dayosizi ya Mangochi ya mpingo wa katolika yati ndi koyenera kuti sukulu zake zikhale ndi zizindikiro maka pa nkhani ya utsogoleri. Imodzi mwa sukulu za mpingo wa katolika Mkulu wa mu ofesiyi a Felix Masamba, anena izi pamene ofesi yawo mogwirizana ndi mafumu, makomiti a sukulu komanso ansembe, akupitiliza kupeza njira zothana ndi kusamvana komwe kukumakhalapo pa kayendetsedwe ka sukuluzi pamene ophunzira a zipembedzo zina akhala akufuna kumabweretsa malamulo a zipembedzo zawo msukuluzi. A Masamba ati ena mwa malamulowa ndi monga kuyika atsogoleri a mpingowu mmakomiti a sukuluzi komanso pa zikwangwani zolembedwa dzina la sukuluzi padzikhala mawu osonyeza kuti sukuluzi ndi zachikatolika. Pa nkhani ya school identity tikunena kuti sukulu zikuyenera zizikhala ndi zizindikiro kuti zizidziwika kuti sukulu izi ndi za chikatolika pazilembedwanso pompo kuti Mangochi Diocese, anatero a Masamba. Iwo atinso zikakhala sukulu za chikatolika anthu azidziwira chikwangwani polemba kuti mawu oti Catholic School komanso mphunzitsi wamkulu ndi otsatira wake azikhala achikatolika okha okha.
3
Boma Lilimbikitsa Phunziro la Sayansi Wolemba: Thokozani Chapola Boma lati lipititsa patsogolo phunziro la sayansi mdziko muno. Wachiwiri kwa mkulu woona za maphunziro apamwamba mdziko muno Dr. Valentine Zimpita anena izi ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor pa mwambo wopereka ma certificate kwa ophunzira okwana 43 omwe atsiriza maphunziro awo a za sayansi, omwe limachititsa bungwe la Skills Development Initiative. Iwo ati msukulu zambiri za mdziko muno mulibe anthu a luso okhala mma laboratory, choncho anthu omwe alandira ma certificate-wa akagwira ntchito yotamandika mma laboratory a msukulu za mdziko muno. Ku unduna wathu tikulimbikitsa phunziroli ndipo pali ndondomeko yomwe ilipo kale yayamba yomwe tizipititsa ku training achinyamata kuti akhale ndi luso la sayansi. Anthuwa tikuyembekezera kuti akagwira bwino ntchito yawo msukulu zosiyanasiyana kaamba koti aphunzitsidwa bwino, anatero Dr. Zimpita. Lihoma: Tipitiriza kupereka maphunzirowa Mmawu ake mkulu wa bungwe Skills Development Initiative mdziko muno a Grant Kumtumanji ati ndi okondwa kuti bungwe lawo layamba kutulutsa achinyamata omwe adzikagwira ntchito mma laboratory a msukulu zosiyanasiyana za mdziko muno. Tinayamba mongoyesera koma tawona kuti zikutheka ndipo tipitiriza kupereka maphunzirowa kuti msukulu zathu za sekondale mukhale akadaulo a sayansi osati kungolemba ntchito anthu omwe sakuzitsata zinthu, anatero a Kumtumanji. Bungwe la Skills Development Initiative lati lili ndi malingaliro oyambitsa maphunziro ena omwe azipereka ma Diploma.
3
Anatchezera Sakundilipira Zikomo gogo, Ndakhala ndikugwira ntchito kukampani ya alonda ina kwa miyezi 11 popanda masiku opuma. Mwezi ulionse amatidula K500 ati ya yunifolomu. Ndidasiya ntchito mwezi wa December chifukwa amachedwa kulipira. Pakatha miyezi iwiri amatipatsa za mwezi umodzi. Ndalama za mwezi wa December mpaka lero sanandipatse. HP, Zomba. HP, Kampani imeneyo ndithu mukhoza kuitengera kukhoti la makampani. Poyamba amakuberani kukulipiritsani yunifolomu. Izi ndikunena chifukwa yunifolomuyo imakhala ya kuntchito osati yanu. Idali ngati chimodzi mwa zipangizo zanu za ntchito. Kodi angakuduleni malipiro chifukwa mukugwiritsa ntchito chibonga cha kampani? Mukhozanso kukadandaula kuofesi ya zantchito mboma lanu ndipo akakuthandizani. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zonse ndine Gogo wanga, Ndimagwira ntchito ya mnyumba koma chilichonse pakhomo ndimachita ndine kuyambira kusamala mnyumba, kuphika, kusesa panja, kusamala mwana kutsegula pageti, kuchapa ndipo zonse ndimagwira mwana ali kumsana olo akhalepo makolo a mwana sakundilandira mwana wawoyo. Ndithandizeni, Anatchereza, nditani pamenepa? TM, Mulanje Zikomo TM, Inuyo pamene munkafunsira ntchito kwa bwana wanu mudafunsira ntchito yanji? Ndafunsa choncho chifukwa nthawi zonse munthu ukamafunsira ntchito bwana amakufunsa kuti ukufuna ntchito yanji? Tsono ngati pali ntchito yoonjezera mumachita kugwirizana malipiro ake. Koma mmene mwayalira nkhani yanu zikuoneka kuti abwana anu ngovuta ndipo alibe chikondi. Kagwiridwe ka ntchito motere ndi ukapolo. Makamaka zandimvetsa chisoni kumva kuti chilichonse mumagwira nokha mwana ali kumsana ngakhale makolo ake alipo. Uku ndiye nkusowa chikondi ngakhale kwa mwana wawo yemwe. Tsono ngati chili chizungu kuti chilichonse azisiyira watchito, tsiku lina adona mnyumbamo adzasimba tsoka. Ndaonapo ine abambo ena akukwatira mtsikana wantchito kusiya mkazi wawo ati wantchito akukwaniritsa chilichonse mnyumbamo. Amayi otere, omwe amasiyira wantchito chilichonse pakhomo iwo ali tambalale kumapenta milomo ndi zikhadaba pamkeka kapena pasofa, asadandaule zikawachitikira zotere. Amuna ambiri amalakalaka atadyako zophika akazi awo, koma haa, zonse amvekere wantchito aphika! Basopo! Samalani nazo zimenezo. Tsono inu a TM, musadandaule kwenikweni kuti ntchito ikukuchulukirani, pitirizani kugwira modzipereka, simudziwa chomwe Mulungu wakukonzerani. Tsiku lina mudzalandira mphotho yanu chifukwa cha kulimbikira ntchito pakhomo. Ndemanga Anatchereza, Ndati ndiikirepo ndemanga pankhani yomwe munalemba chaka chatha ya mzimayi yemwe akuti mwamuna wake amamubisira kuti amamwa ma ARV. Mayiwa athokoze Mulungu kwambiri pakuti apulumuka ku likukumwe la matenda ndipo asachedwenso, apite kukhoti kukamangala. Mwamunayo ndo woopsa kwambiri akufunika chilango chachulu Ine Mzungumbuli, Lilongwe.
12
Bungwe la CFM Ladandaula Ndi Mchitidwe Wogwiritsa Ntchito Achinyamata Pa Zipolowe Za Ndale Bungwe la mabanja mu mpingo wa katolika mdziko muno la Christian Family Movement (CFM) lati ndi lokhumudwa ndi atsogoleri ena a ndale omwe akumagwiritsa ntchito ana komanso achinyamata poyambitsa zipolowe za ndale. Wapampando wa bungweli mdziko muno banja la a Kelvin ndi Eunice Chifunda auza Radio Maria Malawi kuti apeza kuti pa ziwawa zomwe zakhala zikuchitika mmadera osiyanasiyana mdziko muno, zakhala zikutsogoleredwa ndi ana komanso achinyamata omwe akhala akugenda atsogoleri ena kuti asafike ku madera awo kuzachititsa misonkhano yokopa anthu. Pamenepa iwo alangiza atsogoleri a ndale kuti apewe kuchita izi ponena kuti kulimbikitsa ziwawa pakati pa ana ndi achinyamata kumadzala makhalidwe oyipa mwa anawa zomwe anatinso ndi chiwopsezo chachikulu ku tsogolo la dziko lino. Ifeyo ngati mabungwe a mabanja tinene zoona kuti za ziwawazi zikutikhuza kwambiri chifukwa choti banja ndiye maziko a dziko ndipo pamene mabanja ali pa kalikiliki kulera ana awo moyenera, atsogoleri a ndale akumakhala akutenga anawo kuti akayambitse ziwawa, anatero Chifunda. Iwo apempha atsogoleri a ndale kuti atsatire zomwe atsogoleri a mipingo angawalangize kamba pa nkhani yothandiza achinyamata kupewa ziwawa ponena kuti anawa ndi atsogoleri a mawa.
11
Asilikali 89 Afa Mdziko la Niger Chiwerengero cha asilikali omwe afa pa chiwembu chomwe gulu lina laza uchifwamba la chisilamu linachita mdziko la Niger lachinayi sabata yatha ati chafika pa 89 tsopano. Malingana ndi wailesi ya BBC boma la dzikolo laika masiku atatu okhudza maliro a asirikali-wa. Nduna yofalitsa nkhani mdzikolo Zakaria Abdourahame yati pambuyo pa ntchito yofufuza anthu omwe afa pachiwembuchi apeza kuti anthu ena a mugulu lazauchifwambali okwana 77 afanso pa chiwembuchi. Chiwembuchi chachitika patangotha mwezi umodzi gulu lachisilamu litachita zamtopola pa malo ena mdzikolo chomwe chinaphetsa asirikali aboma akwana 71 a dzikolo. Maiko a Chad, Mali, Niger, Burkinafaso komanso Mauritania akhala akugwirana manja pofuna kuthetsa za mtopola zomwe zakhala zikuchitika mmaikowo kwa zaka zochuluka zomwe akuganiza kuti magulu achisilamu ndi omwe akhala akuchita izi.
14
Sankhani Mkandawire kulavula moto Sankhani Mkango Plus Mkandawire adachoka ku Nyasa Big Bullets chaka chino kupita ku Tanzania komwe akusewera Mbeya FC. Iye adachoka limodzi ndi Owen Chaima ndipo ulendowo udali ndi zokamba zambiri. BOBBY KABANGO adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mkandawire: Kumalankhulidwa zambiri Tidziwe mbiri ya Sankhani Ndimachokera ku Dwangwa mboma la Nkhotakota. Ndine wachisanu mwa ana 7. Ndine wosakwatira koma posakhalitsapa mumva nthungululu. Ena amanditchula Mkango Plus, dzinali adandipatsa ndi sapota wa Bullets ati chifukwa omwetsa zigoli amavutika akakumana nane. Ndidayamba kusewera Bullets mu 2007 kuchokera ku Dwangwa United. Ndaseweranso Carara Kicks ku South Africa. Moyo uli bwanji ku Mbeya? Zonse zili bwino, moyo ndi choncho, pena ziwawe pena kukoma koma ndili bwino. Ku Mbeya ndikusewera pafupifupi masewero alionse. Kuchoka kwako ku Bullets padali zokamba zambiri, zidatere chifukwa chiyani? [Waseka..] Bobby aliyense amanena choncho koma pamene ndimachoka ku Bullets nkuti atagula [John] Lanjesi, [Emmanuel] Zoya komanso adali ndi [Miracle] Gabeya omwe akadagwira ntchito yanga. Kumbukiranso adali ndi George [Nyirenda]. Ndidaona kuti idali nthawi yabwino kusuntha chifukwa ndakhala ndi timuyi ilibe kanthu mpaka pamene ndimachoka itapeza ndalama. Umawathawa anzakowa? Ayinso, koma kuona moyo wanga komanso kutimuko kumalankhulidwa zambiri zomwe zikadasokoneza tsogolo langa ndiye ndidafuna ndisunthe kuti ndikaone zina. Tinene kuti tcheya wakale Sam Chilunga ndiye adapangitsa? [Waseka] Amene uja adali ndi masomphenya, sindingakuuzeni zambiri koma taganizani poyamba ndimalandira K33 000 ngati malipiro anga a pamwezi. Anthu amatamanda za luso langa koma kumaposedwa ndalama ndi wonenerera basi, zoona izi? Munthu uja adakweza malipiro ndiye padalakwika? Umadandaula kuti Chilunga adachotsedwa? Ndizomvetsa chisoni kumene, tinene chilungamo Chilunga adali kamuna. Adapeza ma sponsor, adakweza ndalama yolandira tikasewera gemu komanso simungamumve Chilunga akulankhula mmanyuzipepala kupempha thandizo. Kodi ukudana ndi mtsogoleri wapanoyu Noel Lipipa? Sindikuteronso, koma Lipipa adziwe kuti akuyenera kukhala wa mphamvu chifukwa [Bullets] imakhala yosiirana. Aonetsetse kuti osewera akusangalala ndipo zikatere amupatsa zomwe akufuna, dzina lake litchulidwa paliponse chifukwa Chilunga amaganizira osewera kwambiri.
16
Kunalibe kubera mu 2015Maneb Wapampando wa bungwe loona za mayeso la Malawi National Examinations Board (Maneb) John Saka wati bungweli ndi lokondwa kuti mchaka cha 2015 mayeso onse amene bungweli limayendetsa adayenda bwino chifukwa padalibe zobera. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polankhula kwa atolankhani ku Sunbird Mount Soche mumzinda wa Blantyre Lachiwiri, Saka adati ali ndi chikhulupiriro chonse kuti bungweli lathetsa kubera mayeso. Akuti zobera mayeso zikuchepa Iye adati pamayeso onse atatu a Primary School Leaving Certificate of Education (PSLCE), Junior Certificate of Education (JCE) ndi Malawi School Certificate of Education( MSCE) lidakumana ndi vuto limodzi lokha lokhudza kubera mayeso pa JCE. Saka adati: Iyi ndi nkhani yosangalatsa kwambiri poyanganira momwe zakhala zilili pankhani yobera mayeso mdziko muno zaka zingapo zapitazo. Ndife okondwa kuuza dziko lonse kuti mayeso a mchaka cha 2015 ayenda bwino kwambiri ndipo sanabedwe. Zotsatira zimene zidatuluka ndi zoona zenizeni za mmene ophunzira aliyense adalembera mayeso ake. Tipitiriza kuonetsetsa kuti mayeso asadzabedwenso. Wapampandoyo adati izi zidatheka chifukwa cha mgiwrizano umene ulipo pakati pa magulu osiyanasiyana amene amatengapo mbali poyendetsa ntchito za mayeso mdziko muno monga apolisi, asilikali a nkhondo, aphunzitsi, boma ndi ena onse. Iye adaonjezera kuti chitetezo cha mapepala amayeso chakwera kwambiri chifukwa cha njira yatsopano imene idakhazikitsidwa mchitidwe wobera mayeso utafika poipa.
3
Chaola Wati Agwira Ntchito ndi Boma la Tonse Alliance Phungu wa kunyumba ya malamulo mdera la Ntcheu Bwanje North, Nancy Chaola Mdoka wati agwira ntchito ndi boma komanso adzikhala kumbali ya boma nyumba ya malamulo ikamakumana. Mdoka: Sindikufuna udindo ayi Chaola yemwe ndi phungu woyima payekha mboma la Ntcheu, wanena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Iye wati wachita izi potsatira mfundo zomwe anawuza anthu a mdera lawo pa nthawi ya misonkhano yokopa anthu. Sindinachite izi pofuna kupatsidwa mpando uliwonse ayi koma monga phungu woyima payekha ndili ndi ufulu osankha mbali yomwe ndizigwira nayo ntchito, anatero mayi Mdoka. Iwo atinso mafumu a mdera lawo asangalala atamva kuti adzigwira ntchito ndi boma.
11
Navitcha Alonjeza Kufufuza Chiwembu cha Mayi Wachialubino ku Mzimba Nduna yoona zoti palibe kusiyana pakati pa amunandi akazi Mai Mary Thom-Navicha ati achita chotheka kuti anthu omwe adachitira chiwembu mayi wa khungu la chi alubino ku Mzimba kuti alandire chilango chokhwima. Sitisekelera mchitidwewu-Navicha A Navitcha awuza Radio Maria Malawi kuti padakalipano unduna wawo mogwirizana ndi magulu ena okhudzidwa akuchita chotheka kuti mayiyu athandizidwe. Anthu ena achipongwe adadula zala zamayiyu yemwe ndi wakhungu la chi alubino. Ndikufuna ndinene kuti ife sitisekerera aliyense yemwe akuchitira nkhanza anthu akhungu la chialubino kuti onnse akapezeka tiwamanga kuti alandile chilango kaamba koti akuchitazi nzoipa kwambiri kwa anthuwa, antero mayi navitcha. Pamenepa iwo ati ndi udindo wa aliyense mdziko muno kuteteza anthu akhungu la chialubino kuti umoyo wawo usakhale pachiopsezo chofuna kuphedwa ndi anthu ena a nkhanza.
14
Ambuye Ziyaye Apempha Ansembe Akhale Odzipereka Arkiepiskopi wa arkidayosizi ya Lilongwe, Ambuye Tarcizio Ziyaye wapempha ansembe mdziko muno kuti akhale odzipereka pa ntchito yotumikira Mulungu monga momwe Ambuye Yesu Khristu anali kuchitira pa utumiki wake. Ziyaye: Unsembe ndi mphatso Ambuye Ziyaye anena izi ku tchalitchi la Padre Pio Woyera yomwe ndi nthambi ya St. Andrea Kaggwa Parishi mu arkidayosiziyi, pa mwambo wodzodza dikoni Benard Mwayi Ligomeka kukhala wamsembe. Iwo ati unsembe ndi mphatso ndipo ansembewa akuyenera kutumikira monga amachitira Yesu Khritsu. Unsembe ndi mphatso ndiponso mitseri yodabwitsa kwambiri ndipo ife ngati anthu opatulika Mulungu anatigawirako mphatso ina ndipo wansembe akadzodzedwa amasanduka wansembe wina, anatero Ambuye Ziyaye. Polankhulapo bambo Ligomeka anati ndi okondwa kuti maloto awo ofuna kutumikira Mulungu mu njira ya usembe, akwaniritsidwa. Ine chimwemwe changa ndi chopambana chifukwa choti Mulungu wandigawira sacramenti la ukulu, anatero bambo Ligomeka. Wansembe wa tsopanoyu akatumikira mdziko la Tanzania ku sukulu ya achinyamata ya Capuchin Boys komwe akakhale bambo mlangizi pa za uzimu pa sukuluyi.
13
Kupewa kutsegula mmimba Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nthenda ya kutsegula mmimba ndi imodzi mwa matenda omwe amakonda kufala kwambiri mnyengo ino ya mvula. Malinga ndi dokotala wa pachipatala cha St Lukes mboma la zomba Siwale Shaime, kutsegula mmimba ndi pamene munthu akuchita chimbudzi cha madzi mopitirira kanayi pa tsiku. Iye adati, nthawi zambiri chomwe chimayambitsa matendawa ndi tizilombo tingonotingono tosaoneka ndi maso tomwe pa Chingerezi amatitchula kuti germs. Zithaphwi zimasunga majelemusi otsegula mmimba Nyengo ino ya mvula, matendawa amachuluka chifukwa tizilomboti timakonda kupezeka pamalo a chinyontho ndipo timafala mosavuta ndi madzi komanso ntchetche, adatero dotoloyo. Shaime adati mvula ikagwa, madzi othamanga amakokolola tizilomboti pamalo onyasa ndi kukatisiya mmisinje, mzitsime ndi malo ena okhala madzi. Munthu akamwa kapena kugwiritsa ntchito madzi oterewa, tizilomboti timalowa mthupi mwake ndi kuyambitsa matendawa, adatero Shaime. Iye adaonjezanso kuti ntchentche zimachuluka kwambiri nthawi ya mvula ndipo zimakatenga tizilomboti pamalo pomwe pali nyansi ndi kukaziika pa chakudya. Ntchentche zikamva fungo la chinthu choola zimathamangira ndi kukatera pomwepo, pochoka zimanyamulapo tizilomboti ndi kukatiika pa chakudya ndipo wodya chakudyachi akhonza kutsegula nacho mmimba, adatero Shaime. Iye adati ngakhale matendawa ndi oopsa, ndiopeweka ndipo ukhondo ndiye chida cha mphamvu. Anthu akuyenera kusamba mmanja ndi sopo akangochoka kuchimbudzi, asanakhudze chakudya, akasintha mwana thewera, pofuna kuyamwitsa komanso kudyetsa mwana; kukhala ndi chimbudzi cha ukhondo pakhomo, kupewa kuchita chimbudzi paliponse, kusamala ndi kutaya zinyalala moyenera, kuvindikira chakudya, kutsuka zipatso asanadye, komanso kuteteza madzi akumwa pophitsa kapena kuthira mankhwala opha majeremusi, adatero dotoloyo.
6
DPP Yalonjeza Kampeni ya Bata Chipani cha Democratic Progressive (DPP) chati chipereka uthenga wa chitukuko komanso woyanjanitsa a Malawi nthawi ino yokopa anthu pofuna kuti anthu akavotere mtsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika. Nduna ya zofalitsa nkhani a Mark Botomani ndi omwe anena izi lachinayi pa bwalo la zamasewero la Naisi mboma la Zomba pomwe amakhazikitsa nyengo yokopa anthu ya chipani cha DPP mbomalo. A Botomani ati anthu ayembekezere misonkhano yokopa anthu ya mtendere komanso kuyendera zitukuko zosiyanasiyana mmadera onse a mboma la Zomba. Kampeni ya chaka chino ndi yosiyana ndi ina yonse. Tikuyendera zitukuko, tikuchita door to door campaign. Nthawi yatha pano tsopano tikulowa kwambiri mmidzi tiwafotokozere anthu nkhani za chitukuko osati kutukwana kapena kunyozana, anatero a Botomani. Iwo ati mgwirizano wa zipani za DPP ndi UDF ulibe mbiri ya ziwawa motero iwo apempha anthu kuti adzavotere mgwirizano wa zipani ziwirizi. Polankhulanso pa msonkhanowo, nduna yowona za kusasiyana pakati pa amayi ndi abambo yemwenso ndi phungu wa derail Grace Kwelepeta anati boma lamanga msika wa Songani komanso kumanga chipinda chophunzilira pa sukulu ya Kanjedza mbomalo. Iye anatinso boma likuyembekezeka kumanga nsewu wa phula kuchokera pa Songani kukafika kwa Kasonga ndipo anapempha anthu kuti avotere mgwirizanowu kuti chitukukochi chitheke.
11
Mfundo mbweee kumtsutso Makandideti 11 amene adasonkhana ku mtsutso wa atsogoleri usiku wa Lachiwiri msabatayi alonjeza zodzasintha moyo wa anthu akumudzi ngakhale makandidetiwa akulepherabe kunena zomwe adzachite kuti zomwe alonjezazo zidzachitike. Zikuoneka kuti atsogoleriwo amangonena mawu okoma pokopa anthu. Mwachitsanzo, mtsogoleri aliyense adalonjeza kuti moyo wa anthu akumudzi udzasintha powonetsetsa kuti aliyense wakumudzi ali ndi chochita koma osanena kuti akumudziwo azidzachitanji chomwe chidzasinthe moyo wawo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Boma la PPM lidzaonetsetsa kuti banja lililonse kumudzi lili ndi chochita zomwe zidzachepetse umphawi. Mavuto ambiri tili nawo vuto ndi umphawi, kungothetsa umphawi ndiye kuti zambiri zakonzedwa, adatero Mark Katsonga mogwirana mawu ndi George Nnesa wa Tisintha Alliance. Kuwalonjeza anthu akumudzi zokoma chonchi sizidayambe lero. Mu 1994 Bakili Muluzi adakhazikitsa Vision 2020 ponena kuti pofika chaka cha 2020 Malawi adzakhala akudzidalira payekha zomwenso zidzasinthe moyo wa anthu akumudzi. Kufika pano kwangotsala zaka 6 koma umphawi ukupitirizabe kusasantha anthu akumudzi ngakhale kuchoka panthawiyo pabwera maboma a DPP ndi PP omwenso amalonjeza mwakuya kuti moyo wa anthu akumudzi ndiwo udzayanganidwe kwambiri. Poyankhapo zomwe boma lawo lidzachite pa zakagwiritsidwe ntchito ka zinthu zaboma komanso anthu ogwira ntchito mboma, atsogoleriwa adatha mawu kukamba ndondomeko zomwe boma lilipo likutsata komanso zakubedwa kwa ndalama mboma. James Nyondo wa National Salvation Front (Nasaf) yemwe poyankha amatha nthawi kuphwasula ndondomeko zomwe maboma apita akhala akutsata komanso lilipoli, adati vuto ndi kuchita zinthu mobisa. Tili ndi vuto loti mboma mulibe chilungamo ndi kusachita zinthu moti Amalawi adziwe.Mavuto a dziko lino adayamba 1994, tisabisenso, adatero. Mukavotera Nyondo ndiye kuti ndalama iliyonse izidzatsatidwa.Kungoba ndalama, kaya ndi K20 yeniyeniyi udzanjatidwa, ndipo ukaseweze kundende zaka zosachepera 20. Atsogoleriwa adadzudzulanso zipani polowetsa ndalama pa kasankhidwe ka anthu ogwira ntchito mboma. Davis Katsonga wa Chipani cha Pfuko akuti vuto nthawi zonse amakhala mtsogoleri. Ngati pulezidenti akukana kuwulula chuma chake ndiye kwa anthu ogwira ntchito mboma angatani?Ineyo ndidzayesetsa kuti ndidzakhale chitsanzo, adatero Katsonga. Mfundoyi idavomerezedwanso ndi Friday Jumbe wa New Labour Party (NLP) ndi Kamuzu Chibambo wa Petra. Lazarus Chakwera wa MCP mogwirizana ndi Atupele Muluzi wa UDF komanso John Chisi wa Umodzi ndi Helen Singh wa United Independent Party (UIP), adati adzaonetsetsa kuti anthu amene akusankhidwa mmaudindo mboma akhale amaphunziro okwanira posatengera kochokera kapena chipani. Tidzakhala ndi anthu amene mbiri yawo ndiyabwino, adatero Singh pamene Peter Mutharika wa DPP adati boma lake lidzapana akuluakulu aboma kuti pamene ayenda afotokoze bwino ndalama ndi katundu amene wagwiritsidwa ntchito. Atsogoleriwa, amene aliyense ali ndi ludzu losintha momwe zinthu zikuchitikira mboma, adalonjezanso kuti nkhani ya migodi idzatsatidwa ndi chidwi kuti Amalawi azidzapeza phindu. Muluzi adati adzaonetsetsa kuti Malawi ikutenga K30 pa K100 iliyonse ya phindu lomwe boma tidzapeze, Jumbe adati Malawi izidzatenga K49 pa K100 iliyonse ndipo Singh akuti K51 pa K100 idzakhala ya dziko lino. Iwo adatinso adzaonetsetsa kuti anthu amene ali mdera lomwe mukukumbidwa migodi ndiwo adzakhale oyambirira kupindula komanso kuonetsetsa kuti apeza akadaulo enieni amene amatsatira momwe ntchitoyi imagwirikira. Anthu amene ntchito yokumba migodi ikuchitikira tidzawamangira misewu yabwino, magetsi adzakhalapo komanso sukulu ndi zipatala osati kumangowasiyira mabwenje, adatero Chibambo mogwirizana ndi Singh komanso Chakwera. Ngakhale sadafotokoze bwinobwino zomwe adzachite kuti dziko lino lasiya kudalira thandizo la maiko akunja, atsogoleriwa adalonjezabe zodzachoka munsinga yongodalira thandizo lakunja. Mtsutso womaliza uchitika Lachiwiri likudzali ku Comesa Hall mumzinda wa Blantyre. Mkulu wa bungwe loona ufulu wa atolankhani la Misa Malawi, Anthony Kasunda yemwe akutsogolera mtsutsowu, akuti uwu ndi mwayi kuti Amalawi amve zomwe atsogoleri awo akonza. Munthu ukamalembedwa ntchito umayenera ufunsidwe mafunso.Pano Amalawi akuyenera akufunseni mafunso asadakulembeni ntchitoyi. Kwa iwo amene sadabwere zili kwa Amalawi [kuweruza], adatero Kasunda. Sizikudziwikabe ngati mtsogoleri wa dziko lino yemwe adzaimire PP adzakhale nawo pamtsutsowu chifukwa mtsutso woyamba adakana kuti sangakhale nawo.
11
Akupha makwacha ndi zipatso Chaima Banda, mlimi wa zipatso kwa Manondo, T/A Nkukula ku Lilongwe, akusimba lokoma ndi ulimi wake womwe wakhala akuchita kwa zaka 10 tsopano ndipo akuti kudzera muulimiwu iye wamanga nyumba yamakono, wagula galimoto ndi kuphunzitsa ana ake msukulu zapamwamba. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chaima, yemwe adayamba ulimiwu ngati bizinesi ya nazale za mitengo ya zipatso zosiyanasiyana akuti tsopano ali ndi makasitomala ambiri omwe amadzagula zipatso ndi mbande za mitengo kumunda wake. Adatswirika pa ulimi wa zipatso: Banda Mlimiyu adali ngati mlimi wina aliyense wongoyeserera koma kenako adakachita maphunziro a ulimi wa bizinesi ndi momwe angalimire zipatso kuti azipindula pantchito yomwe amagwira chaka chathunthu. Poyamba ndinkachita ulimi monga momwe amachitira alimi anzanga ndipo zinthu sizimasintha kwenikweni mpaka pomwe ndidakachita maphunziro a ulimi wa zipatso ngati bizinesi ya mbande ndi zipatso zenizenizo, adatero Banda. Iye adati zipatso zomwe amalima zimakhala zochita kukwatitsa ndipo mtengo wake umakhala wabwino kuyerekeza ndi zipatso zamakolo zomwe alimi ambiri amadalira komanso zimakhala ndi nyengo yake. Kwa chaka chathunthu Banda amakhala akusamalira mbande zokwatitsakwatitsa ndipo ikafika nyengo yadzinja akuti amapha makwacha ambiri pogulitsa mbandezo kumabungwe ndi anthu ena ofuna kubzala mitengo paokha. Mwachitsanzo, mbande imodzi ya mtengo wa mango ndimagulitsa pamtengo wa K500 pomwe mapapaya ndi maolanje kapena malalanje ndi magwafa ndimachita K350. Chaka chino ndili ndi mbande 5 000 za mango, 3 000 mapapaya ndipo 2 000 magwafa zomwe ndayamba kale kugulitsa. Mabungwe ndiwo amandigula kwambiri moti ena amandipatsiratu chiwerengero cha mitengo ndi mitundu yake yomwe adzafune. Apa zikutanthauza kuti ndimayamba kulima ndi kudziwa kale msika ndi ndalama zomwe ndikuyembekezera, adatero Banda. Kudzera mu bizinesi ya ulimi wa zipatso womwewu, Banda adagula makina opopera madzi omwe amachitira mthirira nyengo yadzuwa.
2
Boma Lapempha Makolo Ateteze Ana ku COVID-19 Boma lapempha makolo mdziko muno kuti ayanganire mwatcheru ana pofuna kuwonetsetsa kuti sakukhala pa chiwopsezo chotenga nthenda ya COVID-19 kamba koti mmodzi mwa anthu asanu ndi atatu omwe apezeka ndi Coronavirus mdziko muno ndi mwana wa zaka khumi ndi ziwili (12). Navicha: Tetezani ana anu Polankhula pa msonkhano womwe komiti yowona za matendawa inachititsa mu mzinda wa Lilongwe, nduna mu unduna woona zoti sipakukhala kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, ana ndi olumala, mayi Mary Navicha ati makolo akhale tcheru kupereka chisamaliro ndi chitetezo chokwanira kwa ana awo powonetsetsa kuti sakukhala ndi kusewera mmalo a chiwopsezo chotenga kachilombo ka Coronavirus. Komititiyi patsikuli, yalengezanso kuti anthu ena atatu atsopano apezekanso ndi kachilomboka ndipo mmodzi wamwalira. A Navicha ati nthawi yomwe ana ali pakhomo amakhalanso pa chiopsezo pa nkhani zochitiridwa nkhanza zosiyanasiyana monga kugwiliridwa ndi zina zomwe wati makolo akuyeyra kutengapo gawo lowateteza ku izi. Msonkhanowu wauza atolankhani zomwe boma likuchita padakali pano pofuna kuthana ndi Coronavirus ku mbali zosiyanasiyana monga pa za chitetezo makamaka ku zinthu zolowa mdziko muno, komanso kupezeka kwa zipangizo za chipatala. Padakali pano anthu asanu ndi atatu ndi omwe atsimikizika kuti apezeka ndi nthenda ya COVID-19 mdziko muno.
6
Za Jessica Bwira ndi zina Mvula idagwa tsikulo pa Wenela si ndiyo. Kaya inkachokera kuti kaya! Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Abale anzanga, musandifunse za Jessica Bwira, Mwano Mkangama komanso Pierre Chamkhwatha. Zoziyamba dala! Kodi mwati foni ingalande ufumu wa Mose? Zidaliko pa Wenela tsikulo. Inetu za WhatsApp ndi zina zotero ndilibe nazo gawo. Komabe ndikudabwa kuti asirikali awa pa Wenela adayamba liti kulowetsa anthu kozizira pofuna kuwachenjeza. Zachilendo ndithu, adatero Abiti Patuma. Ukungonena iwe. Kuchezatu kwaphweka ndipo kwatchipa. Kunena zoona, ngakhale Male Chauvinist Pigs akudziwa bwino lomwe kuti ana a Farao adagwiritsa ntchito kwambiri foni kuthamangitsa Farao ku ma pyramid a ku Gizeh. Umamudziwa Cheops iwe? Nanga chidathyola mphuno ya The Great Sphinx nchiyani? Sindikukambatu za Great Sphinx of Quartz, adatero mkulu adali naye tsiku limenelo. Kaya ndi sukulu kaya ndi chiyani koma sindikudziwa kuti ankakamba chiyani. Iye ankalankhula mokuluwika ngati Moya Pete. Zonse zili apo, apatu zangosonyezeratu kuti ku Male Chauvinist Pigs kuli amthirakuwiri. Nanga achina Niko adziwa bwanji izo amakambirana kuchipinda cha foni? adafunsa Abiti Patuma. Zoona. Koma mpaka kuwamanga kuti awachenjeze? Chadza ndi yani? adafunsa mkulu uja. Nkhani imene idatifika pa Wenela idali ya kutengedwa kwa Jessica, Mwano ndi Pierre. Iyitu ndiyo nkhani idaphimba za mneneri Bushi Minor amene waletsedwa kugawa nandolo ndi chipere chifukwa Moya Pete wakhuta kwambiri ndipo sakumvanso njala. Sakufunanso kumva zakuti wina wagona ndi njala. Koma ndiye zinaliko! Khoba ngazingazi kuchita zawo zija pa Lilongwe apa! Mumayesa masewera? adailowa nkhani Gervazzio. Kodi Moya Pete simesa adatiuza kuti zomangana za ziii pano pa Wenela ayi? Nanga apa alonda ake akuti chiyani? adafunsa mkulu adali ndi Abiti Patuma. Adakuuzani zomangana zokhazo? Musaiwaletu kuti adabweretsa ana ake aja kuti mukhulupirire kuti iyeyo sadagwe mumtengo wa papaya. Lero anawo angabwerenso pano pa Wenela kuti adzafe ndi njala ngati gogo uja? adafunsa Abiti Patuma. Langatu lidali khutu chabe. Mlomo wanga udali womangidwa ndi loko ngati sefa ya ku Reserve Bank. Ndiye ndikumva kuti mayi wathu amupatsa tsamba lapamwamba, unganga wodziwa kusesa ndi kukolopa zimbudzi, adaisintha nkhani Abiti Patuma. Simukudziwa inu. Pamene mukubwebweta za njala simukudziwa kuti iyi ndi njira yothetsera phokosolo? Zinyalala momwe zachulukira pano pa Wenela wina nkumalandira nazo masamba? Koma abale, misalatu yachuluka pano pa Wenela, adatero mkulu uja. Abale anzanga, musandifunse za zinyalala pano pa Wenela. Nokha simukuona? Fungo lochoka mumtsinje wa Mudi silitseka mfuno zanu? Mfemvundikunena mphemvusizinaberekane phwamwamwa pano pa Wenela? Tsono ngati akulandira tsambali, amene amasesa mumsewu awapatsa chiyani? adafunsa Abiti Patuma. Pamene mukuti kuli njala, simunamve kuti tikutseguliranso msewu uja adatsegulira Adona Hilida? Simudamve tikutseguliranso msewu uja adausintha dzina Mpando Wamkulu? Zochita kuphiri ziliko zambiri. Zikuyenda pa Wenela, adatero mkulu uja, uku akuvula malaya ake kuti ationetse T-shirt yake ya mtundu wa thambo pali zitsononkho zitatu.
11
Amalawi aona sabata yakuda Pomwe Amalawi akuyembekeza zotsatira za mlandu wa chisankho, sabata ikuthayi kwakhala kuli mpungwepungwe ku Malawi. Kwa Msundwe ku Lilongwe kudali nkhondo yoopsa pakati pa apolisi ndi anthu mpaka wapolisi mmodzi Usumani Imedi adaphedwa ndi miyala. CSOs in Pay Back Our Money campaign Govt to review Genset deal Govt moves to audit firearms Anthuwo amachita zionetsero zokwiya kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika amachititsa msonkhano ku Lilongweko atatsegulira ndondomeko yomanga sukulu zasekondale 250 mdziko muno. Mneneri wapolisi James Kadadzera adavomereza kuti wapolisiyo yemwe adali wotsogolera anzake pokakhazikitsa bata, adafera pantchito. Amachokera pa C Company ku Lilongwe ndipo adatumidwa kukatsogolera gulu la apolisi okakhazikitsa bata kwa Msundwe koma adangozindikira anthu amuzungulira nkuyamba kumumenya nkumamugenda mpaka adafa, adatero Kadadzera. Kumeneko kudali kutentha mateyala komanso kuswa magolosale ndi kutseka msewu kuti odutsa azilipira ngati akukhoma msonkho. Kwa Msundwe zili mkati, kwa Mpingu nako mboma lomwelo la Lilongwe kudali utsi okhaokha anthu atakwiya ndipo zidatengera asilikali a nkhondo kuti anthuwo abalalike. Mutharika adapanga msonkhano wachitukuko woyamba mchigawo pabwalo la Kamuzu Institute chilumbilireni ngati mtsogoleri wa dziko chitachitika chisankho cha pa 21 May 2019. Kadadzera adati pofika madzulo Lachiwiri pomwe zonsezi zimachitika, apolisi adali atamanga anthu 12 oganiziridwa kuti adatenga nawo mbali pazipolowezo. Mtsogoleri wachipani cha Malawi Congress Party (MCP) Lazarus Chakwera adati zoti adapanga chiwembu chopha wapolisi ndi ndani kapena wachipani chanji zilibe ntchito koma zomwe zidachitikazo nzolakwika. Ku Lilongwe kukuyaka choncho, ku Blantyre nako kudali chisokonezo pomwe mavenda a ku Limbe amachita zionetsero zaukali.
15
Masauko Chipembere phase III starts end November Blantyre City Council (BCC) has said phase III of the Masauko Chipembere Highway project is set to resume at the end of this month as the contractor has already been identified and the signing of the contract took place on October 30. The third phase, from Yiannakis Rouandabout to Standard Bank Limbe Branch, will be upgraded to dual carriage way. In Limbe central business district, the project will include upgrading of the one-way Livingstone Avenue up to the roundabout near Illovo Sugar (Malawi) Limited head office. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo CSOs in Pay Back Our Money campaign Phase 1 of Masauko Chipembere Highway Presenting a report from the chief executives office to be considered and adopted by councillors during the first ordinary council meeting held at the council chamber on Thursday, BCC chief executive officer Ted Nandolo said the amount made available for the phase is about $6 million (about K3 billion). The final phase will start from Yiannakis Roundabout going through Limbe up to Illovo Roundabout. The contractor, World Kaihatsu Kogyo Company Limited [WKK] will be available by the end of the month, he said. Nandolo also reported to the meeting that vehicles for the mayor and deputy mayor have been procured. He said the mayors official vehicle, Kia Sorento, has been delivered whereas that for the deputy mayor is yet to be supplied due to some delays in registration. He said the mayors vehicle is worth K29 million while the deputy mayors vehicle, a Toyota Corolla, is valued at K19 million. Blantyre City deputy mayor Wild Ndipo, making a statement on behalf of mayor Noel Chalamanda who was not present at the meeting, commended the council members for their dedication and zeal shown in attending various committee meetings and asked them not to become complacent but rather, strive to become agents of meaningful change in their communities. Ndipo said while the Keep Blantyre City Clean and Green campaign was launched last Saturday, it is pleasing to note that the residents and the corporate world are all eager and willing to work with the council in transforming Blantyre into a beautiful, clean, and green city it once was.
17
COM Ipereka Mipando, Matebulo 563 Msukulu Zitatu ku Mangochi Wolemba: Thokozani Chapola NDO-KUMANZERE-NDI-A-MZUNGA-KUMANJA.jpg 1080w" sizes="(max-width: 427px) 100vw, 427px" />Dr. Mipando (kumanzere) kupereka tebulo kwa a Mzunga (kumanja) Sukulu ya ukachenjede yosula madokotala mdziko muno ya College of Medicine yapereka mipando komanso matebulo okwana 563 msukulu zitatu za mboma la Mangochi. Polankhula popereka thandizoli mkulu wa sukuluyi Dr. Mwapatsa Mipando ati apereka thandizoli pofuna kuthokoza anthu a mderali kaamba koti ndi malo amene ophunzira a kusukulu ya ukachenjedeyi amakakhala ngati njira imodzi yophunzira za ntchito yawo. Iwo anati patha zaka 27 kuchokera pomwe sukulu ya ukachenjedeyi inayamba kugwira ntchito ndi anthu a mderali komwe ophuzira ake amakakhalako kwa sabata kuphunzira moyo wa anthu komanso kuchita kafukufuku wosiyanasiyana. Talandira katundu watsopano kuchokera ku boma choncho tinawona kuti katunduyi yemwe timagwiritsa ntchito kale koma ndi wabwinobwino tizapereke kunoko kwa anthu omwe takhala tikugwirako ntchito kwa zaka 27 osati kuzangowapempha kuti tizachiteko research ndi zina basi ayi koma nafenso tiwathandize ndi zomwe tili nazo, aantero Dr. Mipando. Iwo apempha makampani ndi mabungwe ena kuti awathandize kukonzetsa katundu yemwe anali woonongeka ndipo akufunitsitsa ataperekanso ku sukulu zina kuti athandizire ophunzira kulimbikira maphunziro. Sukulu zomwe zalandira zipangizozi ndi za Mikombe, Miwawe komanso Lungwena zomwe zikupezeka mu zone ya St. Joseph mdera la mfumu yaikulu Namabvi mbomalo. Dr. Mipando: Tipitiriza kuthandiza Polankhulapo mmodzi mwa akuluakulu a kuofesi yoona za maphunziro mbomalo a Noel Mzunga anati thandizoli lithandiza kuchepetsa mavuto a kusiyira sukulu panjira mderali. Ndife okondwa kwambiri ndi thandizoli. Mbuyomu ana amalembera mayeso pansi zomwe ndi zomvetsa chisoni kwambiri. Ana amasiya sukulu chifukwa amawona kuti akapita ku sukulu akakhala pansi pomwe kunyumbanso amakhala pansi ndiye zomwe talandirazi zikhala chilimbikitso kwa anawa, anatero a Mzunga. Iwo apempha aphunzitsi, ophunzira, makolo komanso anthu okhala mmidzi yozungulira sukuluzi kuti atenge gawo posamalira katunduyu. Kupatula mipando ndi matebulo zomwe zaperekedwa kwa ophuzira, College of Medicine yaperekanso mipando ndi tebulo zapamwamba za mu ofesi ya mphunzitsi wamkulu komanso ofesi ya aphunzitsi ayikamo mipando yokwana 15 pa sukulu iliyonse mwa sukulu zitatuzi.
3
Chilengedwe chibwerere ku Mwanza Mapiri, nkhalango komanso madambo ali mbulanda. Anthu adagwetsa mitengo ndi kuotcha makala. Koma lero nkhani yasintha. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pangonopangono boma la Mwanza layamba kuvala, kubisa kusambuka kwake komwe kudadza pootcha makala. Pulogalamu yolimbana ndi kusintha kwa nyengo yomwe ikutchedwa Enhancing Community Resilience Programme (ECRP) ndiyo ikusintha maonekedwe a bomalo komanso maboma ena. Bungwe la Centre for Environmental Policy and Advocacy (Cepa) ndi lomwe labweretsa kusinthako. Pulogalamuyi imalimbikitsa anthu kuti atsatire njira zosiyanasiyana zomwe zingawatukule uko akusamala nkhani zachilengedwe. Alibe nthawi yootcha makala: Kheli ndi mkazi wake kutulutsa mbuzi Mwa zinthuzi ndi kuchita ulimi wa ziweto, wa kumunda, kugwiritsa ntchito mbaula zamakono, kuchita bizinesi, kutsatira njira zamakono zakalimidwe monga mtayakhasu komanso kulowa magulu obwereketsana ndalama banki mkhonde. Amene akuyanganira momwe pulogalamuyi ikuyendera paboma ku bungwe la Cepa, Stephen Chikuse akuti ngati aliyense ali ndi chochita, nkovuta kuti mitengo isakazidwe. Anthu alibe zochita, alibe popezera ndalama. Kungowauza kuti siyani kudula mitengo si zimveka. Ndi bwino kuwapezera chochita monga tikuchitira, adatero Chikuse. Izi zasintha mabanja ambiri. Pakhomo pa James Kheli wa mmudzi mwa Sudala kwa Senior Chief Kanduku tsopano ndi pa mwana alirenji. Nzeru za Cepa, lero Kheli ali ndi mbuzi 10, wayamba kukolola matumba 50 a chimanga kuchoka pa 15. Kheli ndi banja lake wabzala mitengo 300; akupanga ulimi wa mleranthaka komanso ali ndi munda wa chinangwa momwe akupha ndalama. Ndikulipirira mwana wa folomu 3 ndipo pa telemu ndi K20 000. Ndamanga nyumba ya malata, ndagula wailesi komanso mpando wa pamwamba, adatero Kheli. Nthawi yopanga makala monga ankachitira kale alibe, ndipo nthawi zonse amakhala kumunda, kubusa komanso banja lake limakhala kumsika kugulitsa mandasi momwenso akupha ndalama. Monga akufotokozera mkazi wake Sineliya, kale amadalira makala koma lero nkhani idasintha. Kale, timapeza ndalama pootcha makala. Lero tili ndi njira zambiri zopezera ndalama, adatero iye. Pulogalamu ya ECRP idakhazikitsidwa ndi Christian Aid komanso Concern Universal (Discover) koma thandizo la ndalama limachoka ku UK, Irish ndi boma la Norway. K21 biliyoni ndiyo idaikidwa. Nkhani ya Kheli ndi chitsanzo chabe cha zomwe zikuchitikanso mmaboma a Nsanje, Chikwawa, Mulanje, Thyolo, Mwanza, Machinga, Balaka, Salima, Dedza, Kasungu ndi Karonga komwe CEPA ikugwiramo ntchito.
18
Amanga wometa mnzake kumanyazi Zachilendo akuti zachitika ku Mangochi komwe apolisi amanga mkulu wina pomuganizira kuti adameta mnyamata wa fomu 4 malo aulemu. Mneneri wa polisi ya Mangochi Rodrick Maida watsimikiza za kumangidwa kwa Kenneth Chimombo, wa mmudzi mwa Mtalimanja, kwa T/A Mponda mbomalo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Maida wati apolisi amutulutsa mkuluyu pabelo pamene kufufuza zenizeni za nkhaniyi kukupitira. Iye akuti amutsekulira mlandu wogwira munthu malo osayenerera (indecent assault). Maida adati Chimombo adakumana ndi mnyamatayo Lachitatu pa 23 March pomwe adagwirizana kuti akachezerane. Mnyamatayo adauza apolisi kuti wakhala nthawi asakupita kunyumba kwa Chimombo ndipo patsikulo atakumana, Chimombo adamuuza kuti abwere kunyumba kwake kuti akacheze, adatero Maida. Cha mma 10 koloko mmawa wa tsikulo, mnyamatayo, amene ali ndi zaka 18, akuti adapita kunyumbako ndipo adamupeza Chimombo ndi mwana wina kunyumbako. Maida adati mnyamatayu wauza apolisi kuti adauzidwa ndi Chimombo kuti apite kuchipinda komwe ati kudachitika zoda mutuzi. Akuti panthawi yomwe amauzidwa izi, thupi lake lidafooka, zomwe zidamuchititsa kuti achite chilichonse chomwe amalamulidwa. Kuchipindako akuti adayamba kumusisita pamimba ndipo adayamba kumumeta pamimba. Akuti panthawiyi adafooka ngati wabaidwa jakisoni wa dzanzi. Akumumeta choncho akuti adadzidzimuka pamene Chimombo adayamba kumugwira malo obisika kuti amumete, adatero Maida. Apa akuti ndi pamene adazindikira ndipo adatuluka mnyumbamo ulendo kukanena kwa makolo ake. Panthawiyo akuti adayamba kusanza ndipo adafooka kwambiri. Makolo a mnyamatayu akuti ndiwo adapita ndi mwana wawo kupolisi ya Mangochi kukadandaula kuti awametera mwana wawo. Kupolisi adavula kuti tione, ndipo tidaonadi kuti adali wometedwa. Ndiye tidamanga Chimombo tsiku lomwelo pomuganizira kuti wachita izi ndi iye chifukwa ndiyenso amatchulidwa, adatero. Koma Chimombo, wa zaka 29, akuti wauza apolisi kuti adametadi ndi iyeyo pamene adauzidwa ndi mnyamatayu kuti amumete. Sadakane kupolisi, iye wati adachita kutumidwa ndi mnyamatayu kuti amumete. Tidamutengeranso kubwalo la milandu komwe amakauzidwa za mlandu womwe akuzengedwa, adaonjeza Maida. Ngati Chimombo akapezeke wolakwa pamlanduwu, atha kukakhala kundende zaka zitatu, malinga ndi malamulo a dziko lino.
15
Kudali ku mapemphero a Scom Patha zaka zisanu tsopano Dyson Milanzie yemwe ndi mkonzi wa mapologalamu kuwailesi ya kanema ku MBC-TV ali pabanja ndi njole yake Jane. Awiriwatu adamangitsa woyera pa 30 July 2011 ku Word Alive Garden mumzinda wa Blantyre. Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Adakumana ku BSS: Dyson ndi Jane Dyson amakhulupirira kuti Mulungu ndiye adagwira ntchito yonse kuti iwo akumane ndi kumanga woyera. Iwo adadziwana mchaka cha 2003 pomwe Jane amaphunzira kusukulu ya sekondale ya Blantyre (BSS), Dyson ali kusukulu ya pulaiveti ya Kamacha koma onse nkuti ali Fomu 2. Mchakachi sukulu ya Dyson idakonza mapemphero a Students Christian Organization Malawi (Scom) omwe amakachitikira ku sukulu ya BSS. Kupatula mapemphero, Dyson adagwiritsira ntchito nzeru zachibadwidwe pamene adaponya maso pa Jane. Macheza okhudza mapemphero adayambira pomwepo, koma mosakhalitsa zinthu zidasintha, Dyson adaganiza zolankhula nkhani ina kwa njoleyi ndipo mu 2004 Dyson adafunsira njoleyi koma tsoka ilo adakana. Izi akuti zidabalalitsa Dyson chifukwa maso ake amalasalasa pa njoleyi kotero kudali kovuta kuti ayangane kwina. Mnyamatayu sadalekere pomwepo, adayeserabe kuponya Chichewa chake ngakhale chimakanidwa koma mu 2005 pamene njoleyi imaphunzira pa koleji ya Polytechnic, akuti mpomwe idalola Chichewa cha Dyson. Jane akuti loto lake lidali lodzagwa mchikondi ndi mwamuna wokhulupirira Mulungu. Iye akuti ataonanso kuti kupemphera kwa Dyson sikudali kwachinyengo, adaganiza zomulola. Kukhulupirira Mulungu akuti ndicho chakhala chinsinsi chawo kuti lero angakwanitse zaka zisanu popamba kuponyerana mapoto kapena kuitana ankhoswe kuti adzaweluze milandu. Awiriwa ati achinyamata azizisunga ngati akufuna kudzagwa mmanja a munthu woopa Mulungu. Dyson Milanzie ndi wa mmudzi mwa CheMgundo kwa T/A Kumtaja mboma la Blantyre ndipo ndi wa 9 mbanja la ana 11.
13
Ndale zosadula chitukuko zikhumudwitsa aMalawi Ntchito za ulimi wamthirira za Greenbelt zidaima Kudula ntchito zimene adayambitsa atsogoleri akale a dziko lino kukuchititsa kuti Amalawi azingosaukirabe chifukwa ndalama zambiri zimangolowa mmadzi ntchitozo osamalizidwa. Mkulu wa bungwe loonetsetsa kuti chilungamo chikutsatidwa la Justice Link Justine Dzonzi adanena izi Lachinayi mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda komanso yemwe adzaimire chipani cha MCP atanena kuti nkofunika kuti mtsogoleri wina amene watenga mpando asamadukize ntchito za chitukuko zimene adayambitsa mtsogoleri amene wachoka pampandowo ngati zili zopindulira Amalawi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mapulojekiti a boma kapena othandizidwa ndi maiko ndi mabungwe ena amadilizika zipani zolamula zikasintha. Mwachitsanzo, loto la boma la UDF loti umphawi udzakhale utatheratu pofika mchaka cha 2020 lidataidwa chipanicho chitachoka mboma ndiponso ntchito zoti mudzi uliwonse uzitulutsa katundu wakewake ya One Village One Product (Ovop) zidalowanso pansi UDF itachoka mboma. Ndipo chipani cha DPP, motsogozedwa ndi Bingu wa Mutharika adakhazikitsa ntchito ya ulimi wa mthirira ya Greenbelt Initiative koma boma la Joyce Banda ndi chipani chake cha PP sakukambapo kanthu pa nkhani yolimbikitsa ulimi wakathithi mmadera oyandikira mitsinje ndi nyanja za dziko lino. Mmalo mwake, Banda wabwera ndi ntchito zakezake monga yotukula madera a kumidzi ya Mudzi Transformation komanso yogawa ngombe kwa osauka ya One Family One Cow. Izi zili choncho, ntchito ya boma ndi thandizo la ndalama zochokera ku World Bank kuti amphawi apeze malo ya Kudzigulira Malo, yalowa pansi pamene bankiyo idamaliza kupereka thandizo mchaka cha 2011 ndipo ena mwa omwe adagula malo pa pulojekitiwo akubwerera kwawo. Nayo pulojekiti ya ulimi wamthririra ya Smallholder Irrigation Project (Ship) idafa banki yachitukuko ya African Development Bank (ADB) itapereka masikimu a mthirira atapereka sikimu za ulimiwu kwa anthu eni ake. Dzonzi wati vuto ndi atsogoleri athu chifukwa alibe masomphenya kuti pofika zaka zikudzazi Malawi adzaoneke mwa mtundu wina. Iye wati pa zaka 20 zapitazi dzikoli likadakhala ndi masomphenya, likadakhala pena pake koma zonsezi zikukanika chifukwa chosowa masomphenya. Aliyense akubweretsa zomwe akufuna zomwenso sizikupitirira, tidakabwera ndi ganizo limodzi kuti pofika chaka chakuti tikhale titakwanitsa ndi kufikira pamene takonza, pakutha pa zaka 20 bwezi dziko lino litatukuka. Nchifukwa chake tikungosaukirabe ngakhale tatha zaka 50 tili odzilamulira, adatero Dzonzi. Koma Dzonzi adati nzovuta kunena kuti dziko lino laononga ndalama zingati ndi kudukiza kwa ntchito za chitukukozi. Mmodzi mwa akadaulo pa za chitukuko, Jephter Mwanza yemwe ndi mkulu wa Kalondolondo Programme, adati kusowa umwini ndiko kumalowetsa pansi ntchitozi. Anthu amaona ngati ntchitozi ndi za boma, osati za iwo eni. Mwachitsanzo, anthu akhoza kumanga nyumba yopemphereramo okha ndikumaisamalira koma anthu omwewo amakanika kusamala mijigo kapena milatho yomangidwa ndi boma kapena mabungwe, adatero Mwanza. Iye adati kuyambitsa mapulogalamu ndi kuwaimika pa zifukwa za ndale kumaonongetsa ndalama za boma chifukwa ndalama zambiri zimakhala zitalowapo kale. Pulogalamu ikangoyamba, ndiye kuti ndalama zimakhala zikupita. Choncho kungoimitsa pulogalamuyo nkunyika, adatero iye. Mkulu wa Ovop Tamia Kaluma-Sulumba adati pofuna kuonetsetsa kuti ntchito za bungweli sizikufa ndi kusintha kwa utsogoleri, amene ali mtsogoleri wa dziko lino amakhala wapampando wa bungweli. Zoonadi ntchito zina zimafa mtsogoleri akasintha. Tayesetsa kuti ntchito zathu zisafe ndi kusintha kwa utsogoleri moti tikunena pano tili ndi magulu 105. Amene angakhale mtsogoleri wa dziko lino amakhala wapampando wa bungweli, nchifukwa chake taona atsogoleri atatu kuchokera mu 2003, adatero Kaluma-Sulumba. Malinga ndi Banda, si bwino kudukiza mapulogalamu chifukwa cha kusintha kwa chipani cholamula. Nchifukwa chake ndayesetsa kuti ndisataye ntchito zimene adayambitsa [Bingu wa] Mutharika chifukwa zina mwa izo zili ndi gawo lalikulu lotukulira dziko lino, Banda adauza abusa amene adakamuyendera. Ndipo polankhula pamsonkhano ku Kasungu, Chakwera ntchito za chitukuko ziyenera kuchokera kwa Amalawi eni ake. Nzachisoni kuti dziko lino ndi losaukitsitsa mdera lino la Africa. Izi zili choncho makamaka chifukwa chodukiza ntchito za chitukuko. Tiyenera kukhala ndi masomphenya kuti podzafika 2020 dziko lathu lidzakhala lili pati, adatero Chakwera.
11