Text
stringlengths
292
6.6k
labels
int64
0
19
Wezzie: Chiphadzuwa chonenepa cha Mzuni Sukulu yaukachenjede ya Mzuzu University idasankha chiphadzuwa chonenepa Loweruka sabata yatha pomwe adali ndi chisangalalo chawo cha Social Weekend. Mtolankani wathu DAILES BANDA adacheza naye motere: Tikudziweni Chisale watuluka nkumangidwanso Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Ndine Wezzie Lwara ndipo ndimachokera mmudzi mwa Thom Lwara, kwa Inkosi ya Makhosi Mmbelwa mboma la Mzimba. Kwathu tinabadwa ana awiri ndipo ndine woyamba kubadwa. Ndili ndi zaka 20. Manthu wa ziphadzuwa: Lwara (pakati) ndi omutsatira ake Mbiri yako ya maphunziro ndi yotani? Ndidalemba mayeso anga a Fomu 4 pasukulu ya sekondale ya Ekwendeni, padakalipano ndikuphunzira zokopa alendo pa Mzuzu University. Ndili chaka chachiwiri. Udayamba liti za uchiphadzuwa? Kunena chilungamo aka nkoyamba kuchita izi. Mnzanga wina adangobwera kudzandiuza kuti ndikayese ndipo ndikhoza kupambana. Kuyesera ndi kupambana kudali komweko. Udazilandira bwanji za kupambana kwako? Sindikuchitenga chinthu chapafupi chifukwa sindidakonzekera kwambiri monga anzanga adachitira. Ndine wosanglala kwambiri makamaka chifukwa cha mphatso yomwe ndidalandira ya ndalama zokwana K50 000. Ndiye ukuwauza chiyani makolo ako? Kusukulu ya ukachenjede ndi komwe anthu amaphunzira ndi kuchita zinthu za msangulutso zambiri. Iyi ndi nthawi yomwe aliyense amene adapitako kusukuluzi amakumbikira kuti adasangalala. Atsikana uwalangiza zotani? Azilimbikira sukulu kuti adzafike malo ngati ano ndipo asamakhale ndi mtima odziderera. Pa atsikana amene tidapikisana, sikuti pasukulu pano atsikana onenepa ndife tokha ayi koma kumakhala kudzikaikira komwe kumatilepheretsa kuchita zinthu.
15
Akangalika ndi ulimi wa mthirira Mlimi wochenjera monga NELLIE NYONI wa mboma la Balaka amayambiratu ulimi wa mchilimwe mvula ikamapita kumapeto kuti asavutike kwambiri ndikuthirira. Tikunena pano adabzala kale chimanga komanso nyemba ndipo posachedwapa ziyamba kubereka. ESMIE KOMWA adacheza ndi mlimiyu motere: Ulimi wa mchilimwe umaposa wa mdzinja Kodi nchifukwa chiyani mumafulumira kuyambapo ulimi wa mthirira? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Choyambirira ndimafuna kuti ndigwiritse ntchito chinyezi chochuluka chomwe chimapezeka mvula ikangosiya kugwa kuti mbewu zikamadzafuna madzi owonjezera ndidzangothirira kanthawi kochepa basi zatheka. Chifukwa china nchoti ndimafuna ndizipezeka ndi mbewuzi pafupipafupi kuti ndizipeza phindu lochuluka. Nanga mudayamba liti ulimi wa mthirira? Ulimiwu ndidayamba mu 2004. Kodi chidakukopani pa ulimiwu nchiyani? Ndidaona kuti mbewu za mthirira zimagulitsidwa pa mtengo kusiyana ndi zodalira mvula ndipo ichi nchifukwa chomwe ndimazilimbikira. Nanga mumalima mbewu zanji? Ndimalima mbewu zosiyanasiyana monga tomato ndi kabichi koma kwambiri ndimaonjeza chimanga. Kodi mumalima mbewuzi pamalo okula bwanji? Malo womwe ndimachitirapo mthirirawu ndi wokwana ma ekala 6 ndi theka. Nanga zikayenda bwino mumapeza ndalama zochuluka bwanji pakamozi? Mbewu yomwe ndimaiwerengetsera bwino ndi ya chimanga chifukwa ndimailima mochuluka monga ndanena kale. Chimangachi chikakhwima ndikugulitsa chachiwitsi ndimatha kupeza K600 000 ndipo zikavutirapo K500 000. Kodi chinsinsi chanu chagona pati? Chinsinsi changa ndikusamalira mbewu kuti zichite bwino. Ndimaonetsetsa kuti zizipeza madzi wokwanira, ndimathira feteleza, ndimapalira komanso kuthana ndi zilombo zoononga kuti zichite bwino. Ubwino wa mbewu za mthirira ndiwoti zikangotheka ndimadziwiratu kuti zanga zayera. Kodi mumagwiritsa ntchito mthirira wanji? Kwa zaka zonsezi ndakhala ndikugwiritsa ntchito ma water cane kuthiririra mbewu zanga koma padakali pano ndagula pampu yopopera madzi yogwiritsa ntchito petulo. Nanga ndi mavuto anji omwe mumakumana nawo pogwiritsa ntchito mthirira woterewu? Kunena zoona mthirira wa mtunduwu ndiwopweka kwambiri. Tangoganizani kuti munthu ukwanitse kuthirira malo wokula motere sizamasewera koma khama langa pa ulimiwu ndilomwe limandichititsa kuti ndizilimbikirabe. Nanga ndi mavuto anji omwe mumakumana nawo pa ulimiwu? Vuto lalikulu ndikusowa kwa zipangizo za mthirira za makono zogwiritsa ntchito madzi ochepa. Vuto lina ndikusowa kwa madzi othiririra mbewu makamaka tikamayandikira nyengo yotentha zitsime zomwe timadalira nthawi zina zimaphwa ngati mvula siidagwe yokwanira. Izi zimachititsa kuti tidukize panjira nkumadikirira mvula mmalo moti tizilumikiza kwa chaka chonse. Chinthu chokhumudwitsa kwambiri nchoti ulimiwu timangozichitira popanda alangizi a mthirira ndipo ndimadabwa ngati alipo mdziko muno. Nanga masomphenya anu pa ulimiwu ndiwotani? Ndikufuna mtsogolomu nditaika mthirira wa makono uja amalumikiza mapaipi ndikumangotsegula madzi kuti azifikira mbewu okha. Mthirira woterewu umafuna mlimi akhale ndi matanki, zitsime zakuya ndi zopopera madzi zogwiritsa ntchito zipangizo zoyendera magetsi kapena mphamvu ya dzuwa. Izi zidzandithandizira kuti ndizitha kukhala ndi madzi kwa chaka chonse komanso kupopa mosavuta ndikumathiririra mbewu zanga. Kodi mudzapitiriza kulima mbewu zomwe mukulima panopazi? Ayi ndikufuna ndidzayambe ulimi wa kachewere chifukwa ndidamva kuti ndiwaphindu kwambiri koma ndimakanika kuyamba panopa chifukwa cha mavuto omwe ndanena aja. Kabitchi ndi mbewu ina yomwe ndimaganiza kuti ndidzaikirapo mtima. Nanga muchita chiyani kuti mukwaniritse masomphenyawa? Pa ine ndekha ndikuona kuti ndizovutirapo chifukwa zipangizo za mthirira wa mtunduwu ndizokwera ntengo kwambiri. Ndidakakonda padakapezeka mabungwe omwe akhoza kundithandiza kufikira masomphenyawa. Tidayetsera kuwafotokozera a ku nthambi yoona za ulimi wa mthirira koma adangotiyankha kuti tikuthandizani kutenga ngongole ku banki. Ngakhale adatilonjeza motere koma tikuona kuti izi sizingachitike choncho ndikupempha akufuna kwabwino kuti andithandize.
4
Phungu Adandaula ndi Kuchepa kwa Ndalama Zokonzera Miseu ya Mmizinda Wolemba: Sylvester Kasitomu a.mw/wp-content/uploads/2019/10/Jiya-170x170.jpg 170w" sizes="(max-width: 307px) 100vw, 307px" />Jiya: Misewu yambiri ikufunika kukonzedwa Phungu wa dera la pakati mu mzinda wa Lilongwe Alfred Jiya wadandaula ndi kuchepetsedwa kwa ndalama zokonzera miseu ya mmizinda ya dziko lino. Phungu-yu wati ndondomeko ya za chuma ya 2019 mpaka 2020, boma laika padera ndalama zokwana 2.2 billion kwacha kuti zigwire ntchito yokonza misewu ya mmizinda ya Lilongwe, Blantyre, Zomba komanso Mzuzu zomwe wati ndi zochepa poyerekeza ndi mmene ntchito yomanga misewu imakhalira. Iwo ati ndi ntchito ya iwo monga aphungu kuonetsetsa kuti chaka ndi chaka pasakhale mavuto monga miseu ya mmizinda yomwe ndiyofunika kwambiri ndipo sikufunika kukhala yoonongeka. Pali miseu yambiri yoti simadusika nthawi ya mvula monga nseu wa masafu kupita pa zebra komanso wakumagwero kufika ku 23 ndi ina yambiri miseu yi ikufuna kukonzedwanso nde ngati achepetsa ndalama nde kuti akunena kuti miseu ikhalebe yoonongeka zomwe ndizokhudza kwambiri, anatero Jiya. Mwazina iwo ati ngati boma silichitapo ayesetsa kupeza njira yolikakamiza kuti lithandizepo poonetsetsa kuti misewuyi yakonzedwa nyengo ya budgetiyi isanadutse.
17
Papa Ayendera Odwala- Ali Mdziko la Thailand w" sizes="(max-width: 453px) 100vw, 453px" />Papa pa chipatala cha St. Louis mdziko la Thailand Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko Papa Francisko anakayendera odwala pa chipatala cha St. Louis mu mzinda wa Bangkok pa ulendo wake omwe akucheza mdziko la Thailand. Polankhula ndi ogwira ntchito a pa chipatalachi okwana 700 iye anati ndi okondwa kuti anakayendera anthu pa chipatalachi omwe akusoweka thandizo makamaka la uzimu. Malipoti a wailesi ya Vatican ati chipatalachi anachitsegulira mu chaka cha 1898 ndipo mawu ake ochitsogolera ndi akuti Pamene Pali Chikondi, Mulungu Amakhalanso Pomwepo. Padakali pano chipatalachi chimayendetsedwa ndi madotolo, anamwino komanso ochita za kafukufuku ndi thandizo lochokera ku nthambi yoona za zipatala.
14
Maphunziro alowa nthenya Okhudzidwa ndi ngozi akuphuphabe Nthawi ili cha mma hafu pasiti leveni (11:30 am) ndipo kunja kukutentha koopsa. Ena mwa ophunzira pasukulu ya pulaimale ya Chikoja kwa mfumu Osiyana Mboma la Nsanje akuphunzirira pansi pamtengo wopanda masamba, ena ali mmatenti momwe mukutentha molapitsa. Ofesi ya aphunzitsi ili pansi pamtengonso umene masamba ake adayoyoka. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Posakhalitsa wophunzira wa Sitandade 4 wakomoka chifukwa chotentha ndipo ophunzira anzake akudzithira madzi kumutu pofuna kuziziritsa matupi awo. Awa ndiwo mavuto amene amanga nthenje pasukulu ya Chikojayi, yomwe idakhudzidwa ndi madzi osefukira. Nazonso sukulu za Chingoli mboma la Mulanje ndi Mvunguti mboma la Phalombe akukumana ndi zokhoma zokhazokhazi. Pamene patha miyezi 8 chichitikireni ngoziyi, nyumba za aphunzitsi, zimbudzi komanso mabuloko ndi maofesi a aphunzitsi sizidakonzedwe, zomwe zikupereka mantha kuti mavutowa angakhodzokere mvula ikayamba mwezi ukubwerawu malinga ndi azanyengo. Wachiwiri kwa mphunzitsi wamkulu pasukulu ya Chikoja, Clement Seda, akuti ngati mvula itayambe ndiye zivutitsitsa. Panopa tikupirira dzuwa, koma ngati mvula ikayamba ndiye palibe chabwino, sukulu idzatsekedwa kaye. Mboma la Nsanje, madzi osefukira adagwetsa sukulu ya Chinama ndi Namiyala. Izi zidachititsa kuti boma limange matenti kuphiri la kwa Osiyana kwa T/A Mlolo kuti ophunzira azikaphunzirirako pamene matenti ena adamangidwa kwa Chambuluka. Kumangidwa kwa matentiwa, chidali chimwemwe kwa aliyense kuti basi athana ndi mavuto osefukira kwa madzi, koma lero kwaipa pamene mavuto ena afika mkhosi. Seda akuti boma lidalonjeza kuti ayamba kuwamangira sukulu nthawi ya mvula isadayambe. Koma mpaka lero kuli chuu. Adatimangira matenti asanu ndipo makalasi ena akuphunzirira panja. Poyamba tinkadandaula ndi ana amene ankaphunzira panja, koma pano tikudandaulanso ndi matentiwa chifukwa mukutentha kwambiri. Mwaona nokha kuti mwana wina kuti Sali bwino, mavuto amenewa achulukira chifukwa matenda amutu si nkhani, adatero Seda. Seda adati aphunzitsi onse akukhala ku Fatima ndi Makhanga, womwe ndi mtunda wa makilomita osachepera 14. Tikafulumira kufika kuntchito ndiye kuti ndi 8:30 mmawa kusonyeza kuti piriyodi imodzi imadutsa tisanafike, komanso chifukwa chotentha, ophunzira amaweruka mofulumira dzuwa lisadafike powawitsa. Izi zikuchititsa kuti ana asaphunzire mokwanira, komanso ambiri sakubwera chifukwa cha mavuto amene tikukumana nawowa, adatero Seda. Iye adati izi zachititsa kuti zotsatira za mayeso a Sitandede 8 chaka chino zikhale zosokonekera. Mwa ana 40 amene adalemba mayeso a PSLC, ana 4 okha ndiwo adakhoza pomwe chaka chatha ana ana onse 35 adakhoza. Mu 2013 adalemba ana 85 ndipo onse adakhoza, mu 2012 ana 29 adalemba mayeso ndipo 27 ndiwo adakhodza. Sukuluyi yakhala ikuchita bwino kuyambira mmbuyo monse, adatero Seda, amene sukulu yake ili ndi ophunzira 900. Koma mneneri muunduna wa zamaphunziro Manfred Ndovi adati timupatse nthawi kuti afotokozepo zomwe boma likuchita kuti lipulumutse ophunzirawa. Nayo sukulu ya Chingoli pulaimale mboma la Mulanje akuti mavuto ndi ankhaninkhani malinga ndi DC wa mbomalo Fred Movete. Chimangireni matenti palibe chimene chachitikapo, mabuloko sadayambe kumangidwa moti zivuta kwambiri mvula ikayamba koma ndangomva kuti mapulani alipo kuti mabuloko amangidwa, adatero Movete. DC wa boma la Phalombe Paul Kalilombe akuti mbomalo mavutowa ndi ochepa kuyerekeza ndi maboma ena. Sukulu ya Mvunguti ndiyo idakhudzidwa, makalasi awiri okha ndiwo akuphunzira mmatenti koma ena ali mmabuloko, adatero Kalilombe. Maboma 15 ndiwo adakhudzidwa ndi ngozi ya madzi mu January chaka chino koma boma la Mulanje, Nsanje ndi Phalombe ndi omwe sukulu zidakhudzidwa.
3
Atukuka ndi kukwatitsa mitengo ya zipatso Masiku ano nkhani ili mkamwamkamwa paulimi ndi yogwiritsa ntchito mitundu ya mbewu zamakono zomwe akatswiri adayesa nkupeza kuti zili ndi kuthekera kotukula ulimi. Alimi a zipatso nawo adayambapo kutsata nzeruzi ndipo ena akusimba lokoma. Alimi a gulu la Taweni Farmers Club ku Mzimba akuchita nawo ulimiwu ndipo akudalira kwambiri kukwatitsa mitengo ya zipatso. Wapampando wa gululi Jester Kalua adafotokozera STEVEN PEMBAMOYO za ulimiwu motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mlimi pantchito yake: Kalua kukwatitsa mitengo ya zipatso Bambo, dzina ndani? Dzina langa ndi Jester Kalua wa mmudzi mwa Kamanga kwa T/A Mtwalo ku Mzimba. Ndine wapampando wa gulu la alimi la Taweni Farmers Club. Kodi kalabu imeneyi mumapanga zotani? Ife timapanga ulimi wa zipatso zosiyanasiyana monga malalanje, mapapaya, mango, mapichesi ndi mapeyala. Tili ndi malo aakulu kwambiri omwe timabzalapo mitengo yazipatsoyi ndipo timathandizana kusamalira ngati gulu. Inu mumabzala mitundu yotani ya zipatsozo? Pali ntchito ndithu chifukwa sitimangofesa basi nkumayembekezera kuti tidzaokere, ayi. Pali zambiri zomwe timachita koma kwakukulu nkukwatitsa mitengo yathu yazipatso. Mukutanthauzanji mukatero? Ndikutanthauza kuti timatha kufesa mitengo ina yomwe sivuta kumera nkusamala panazale koma kenako timaikwatitsa ndi mitengo ina yomwe imabereka bwino koma imavuta kafesedwe kake. Kukwatitsako mumtani? Tikafesa mitengo yathu timayanganira mpaka itafika pamsinkhu wokwatitsa. Pokwatitsapo timadula nthambi ya mtengo womwe tikufuna kuti ukwatidwewo nkuikapo nthambi ya mtengo womwe tikufuna nkumanga. Tikatero timapitiriza kusamalira. Ndiye mtengowo sungafe? Ayi. Zomwe timachita nzakuti sitidula nthambi zonse koma mwina imodzi nkusiya nthambi zina zoti zizipanga chakudya cha mtengowo uku ukugwirana ndi unzakewo. Zikagwirana bwinobwino timatha kudzadula nthambi zinazo kuti mtengo wokhawo womwe tikufuna upitirire kukula. Cholinga chake nchiyani? Timafuna kupeza phindu lochuluka paulimi wathu chifukwa mbewu yomwe timaphayo imakhala yobereka pangono kusiyana ndi mbewu yokwatitsayo ndiye timafuna kupindulapo pa mbewu inayo. Mungatchuleko mitundu ya mbewu zomwe mukukwatitsa pakalipano? Tikukwatitsa mandimu ndi malalanje, mango achikuda ndi achizungu komanso mapichesi achikuda ndi achizungu. Ndiye mwati kusiyana kwake nkotani? Kusiyana kwake nkwakuti mbewu zachizunguzi zimabereka zipatso zikuluzikulu komanso zimabereka kwambiri kuposa mbewu zachikuda. Koma sindikumvetsa pakakwatitsidwe ka mandimu ndi malalanje. Nchifukwa chiyani mumapha mandimu kuti mudzakolole malalanje? Pali zifukwa zingapo. Choyamba mandimu savuta kafesedwe kake poyerekeza ndi malalanje ndiye timafuna kuti mandimuwo atiyambire moyo wosavutawo kenako nkuupatsira ku malalanje. Chachiwiri, mandimu ndi malalanje chili ndi msika waukulu ndi malalanje ndiye munthu aliyense akamabzala mbewu zodzagulitsa amaganizira za msika choncho ife timaona chanzeru kulimbikira malalanjewo. Mwanenapo za kasamalidwe, kodi mumasamala bwanji mitengi yanuyo? Zoonadi mitengo imafunika chisamaliro chokwanira bwino chifukwa kupanda kutero simungapeze phindu. Chiopsezo chachikulu ndi moto wolusa womwe umayamba mosadziwika bwino choncho mpofunika kulambula bwinobwino munkhalango ya zipatso. Kupatula apo mitengo sichedwa kugwidwa ndi matenda osiyanasiyana choncho pamafunika kuyendera pafupipafupi kuti ngati mwaoneka chizindikiro cha matenda, vutolo lithetsedweretu. Nthawi yokolola mumatani? Choyamba sitingokolola chisawawa koma pamakhala nthawi yake yokololera ndipo timayamba taona ngati zipatsozo zafika poti tikhoza kukolola. Timakana kungokolola chisawawa chifukwa zipatso zokolola zanthete zimabweretsa maluzi chifukwa maonekedwe ake zikapsa amakhala osapatsa chikoka. Inu misika yanu ili kuti? Tili ndi misika yosiyanasiyana ya zipatso. Zipatso zina timapikulitsa kwa mavenda ndipo zina timapita nazo mmagolosale akuluakulu omwe amatigulitsira nkumatipatsa ndalama.
4
Msika wa zondeni ngosayamba Katswiri wa zamadyedwe mdziko muno, Chrispine Jedegwa, akupanga ndi kugulitsa ufa wa mbatata ya kholowa yamakolo yotchedwa zondeni yomwe akuti ili ndi ufa wapamwamba wopatsa thanzi. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Anthu ambiri adazolowera kuti ufa umapangidwa kuchokera kuchimanga ndi chinangwa basi koma katswiriyu wati phindu lochokera mmbatata limachuluka mbatatayo ikagayidwa nkugulitsa ufa wake. Alimi ambiri sakonda kulima mbatata ya zondeni chifukwa sibereka kwambiri koma chomwe sadziwa nchakuti mbatatayi ili ndi mphamvu ya mankhwala ndipo muli ndalama zochuluka, adatero Jedegwa. Jedegwa: Ufa wa zondeni tikaukonza umakhala ngati uwu Iye adati mbatatayi ikacha ndipo mukaimuka bwinobwino mukaigaya mukhoza kupanga ufa wophikira phala kapena chakudya china chilichonse ndipo munthu akadya phalalo thupi lake limakulupala. Mkuluyu adati alimi alime mbatata ya mtunduwu kwambiri powatsimikizira kuti msika wake ulipo wosayamba. Pakalipano mbatatayi ikulimidwa kwambiri ndi alimi a ku Thyolo, Phalombe, Kasungu ndi Mchnji koma sakukwanitsa pomwe ife timafuna moti alimi omwe akufuna kupha makwacha alime mbatata yamtunduwu ndipo tikulonjeza kuti tidzawagula, adatero Jedegwa. Iye adatinso alimi atafuna mbewu ya mbatatayi yobereka kwambiri akhoza kukumana ndi akuluakulu a kampani ya C & NF omwe akupanga ufawu chifukwa mbewuyi alinayo yambiri. Alimi ambiri amadandaula kuti amalephera kulima mbewu zina polingalira nkhani ya msika koma Jedegwa watsimikiza kuti kampani yawo njokonzeka kugula mbatata yonse ya zondeni yomwe alimi angalime. Jedegwa adati kupatula kuti ndi chakudya, ufa wa mbatata ya zondeni ndi mankhwala othandiza kumatenda osiyanasiyana monga mtima, kuthamanga kwa magazi, shuga, zilonda zammimba ndi kuphwanya kwa minofu.
4
Kudali ku Presbyterian Church of Malawi Kudali kuphwanya mafupa ku Dream Centre Assemblies of God mumzinda wa Blantyre Loweruka pa 2 May pamene Faith Mussa amachititsa ukwati ndi bwenzi lake Brenda Chitika. Ndi kanamwali kopanda banga, kopanda chipsera. Thupi losalala komanso kathupi lomva mafuta. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ikokatu ndi ka mmudzi mwa Sikoya kwa T/A Chikumbu mboma la Mulanje. Iko ndi kachinayi kubadwa mbanja la ana asanu. Faith Mussa kuimbira namwali wake kanyimbo kachikondi Faith amene adatchuka kwambiri ndi nyimbo ya Desperate, akuti ubongo wake udasokonekera pamene adaona njoleyi Lamulungu mu 2009 pomwe mnyamatayu adapita kumpingo wa Brenda wa Presbyterian Church of Malawi (PCM) mumzinda wa Blantyre kukatsitsimuka. Faith adatsitsimuka zenizeni chifukwa kusalalanso kwa njoleyi kudaziziritsa mtima wake. Tsikuli Mulungu adakumana ndi chosowa chakedi. Ndili mumpingomo foni idaitana ndiye ndidapita panja kukayankha. Ndili panjapo kulankhula pa fonipo, ndidaona namwaliyu chapakataliko akutonthoza mwana, akutero Faith. Maso adali pa namwali, khuku lidali pa foni. Iye samasunthika ndipo pena Brenda akuti amathawitsa diso lake kuti asaphane maso ndi mnyamatayu koma Faith samasunthika. Izi zidatanthauza kanthu kena mumtima mwa Faith ndipo nkhani yonse idakambidwa patangotha mwezi. Titaweruka, ine ndi mchimwene wanga tidaperekeza namwaliyu. Ndinene apa kuti mwana amatonthozayo sadali wake. Poyamba Brenda amacheza ndi mbale wanga ndiye pamenepa ndidadziwiratu kuti ndikuyenera kuchita kanthu, adatero Faith. Pangonopangono awiriwa adakhazikitsa macheza ndipo Faith sadachedwetse koma kugwetsera mawu oti adzalumikize awiriwa kukhala banja. Padatha nthawi kuli zii, za yankho tidakayika koma pa 28 August 2009 ndidangolandira foni kundiuza kuti wagwirizana ndi [mbalume] zomwe ndidamuuza, adatero Faith wachiwiri kubadwa mbanja la anyamata atatu.
13
Tidadziwana tili ana Mtolankhani wa za masewero ku wailesi ya Voice of Livingstonia (VOL) Sylvester Siloh Kapondera adakumana ndi wokondedwa wake Annie Chivunga Kalasa ali ana mboma la Kasungu. Apatu nkuti Kapondera ali ndi zaka 11, mchaka cha 2001, ndipo ankacheza ndi achimwene a namwali wakeyu. Panthawiyo nkuti Kalasa naye ali wachichepere kwambiri. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ubwenzi wa anawatu udali bwino kwambiri chifukwa nawo makolo awo adali anansi pomwe onse ankaphunzitsa pa sukulu ya Mwimba, mboma la Kasungu. Siloh ndi Annisha: Zidayamba ngati chibwana Koma patadutsa zaka zingapo anthuwa adatayana pomwe adalowera malo osiyana. Koma mudali mchaka cha 2013 pomwe ndinkagwira ntchito kuwailesi ya Tigabane pomwe ndidayamba kumufuna namwaliyu! Panthawiyo nkuti akuchita maphunziro ake auphunzitsi ku Nkhamenya, mboma la Kasungu, adalongosola Kapondera. Iye adalongosola kuti atamuona Kalasa mtima wake udatumphatumpha mpaka kupempha nambala yake ya lamya yomwe adapatsidwa mosavuta chifukwa adali kale anansi. Nditabwerera ku Mzuzu ndidayamba kuchezetsa ndipo ndidamuuza mawu a chikondi komabe ndidakanidwa, ndidayesetsa koma zidavuta! Kenako kukhala ndekha kudandivuta ndipo ndidapeza mkazi wina! Komabe mtima wanga umakumbukirabe Annie! adatero Kapondera. Koma mwatsoka adasiyana ndi mkazi winayo ndipo Kapondera sadaupeze koma kubwerera kwa Kalasa komwe mtima wake udali. Nditasiyana ndi mkazi winayo kumayambirilo kwa 2017 sindidachedwe kupitaso kwa Kalasa komwe malingaliro anga adali! Apaso nayeso sadachedwe koma kundisekerera nkundilora ataona zoti sindimafuna kupanga naye chibwenzi wamba koma ubwezi woti timange banja, adalongosola Kapondera. Komatu ubwenzi wa awiriwa wakumana ndi zokhoma zosiyanasiyana monga kupekeredwa nkhani mwa zina. Chomwe chidandikopa kwambiri kwaiye ndichoti kupatula kuwala kwa namwaliyo, Ali ndi khalidwe lwabwino, ndi ofatsa komaso okonda kuseka moti sindimavutika kupeze nkhani yoseketsa kwambiri kuti mwina ndioneko mano ake, adatero Kapondera. Iye adati chikondi chawo chimalimba chifukwa chokhulupilirana komaso kulemekezana ndi kumvetsetsana! Polankhulapo, Kalasa adati adamukonda Kapondera chifukwa ankamuonetsera chikondi. Kalasa adati Kapondera amakondedwa ngakhale ndi abale ake. Ukwati wa awiriwa uliko pa April 28 kuholo ya sukulu ya sekondale ya Katoto. Kapondera ndi mwana wachiwiri kubadwa mbanja la ana asanu pomwe Kalasa ndi mzime mbanja la ana 6.
15
Tomato wabooka pa Bembeke Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Alimi ku Bembeke mboma la Dedza ayamba kufupa tomato wawo pamene wachoka pa mtengo wa K6 000 pa dengu kufika pa K1 000. Izi zikuchitika chifukwa cha kuchuluka kwa tomato amene akufika pamsikawu zomwe zachititsa kuti anthu opita ku Lilongwe kapena ku Blantyre azigula tomatoyu. Kutapa kutaya: Tomato amafunika kusamala Malinga ndi mmodzi mwa alimiwa, Akisa Magugu, mwezi wa March amagulitsa dengu pa mtengo wa K6 000 koma pano watsikiratu. Tikungofupa tomato, taganizani dengu lomwe timagulitsa K6 000 miyezi yangothayi lero latsika ndipo likupita pa mtengo wa K1 000 ndipo zikavuta akumagula pa mtengo wa K500. Taononga ndalama zambiri kuti tomatoyu tilime koma mapeto ake tangoyamba kufunano kwa anthu mopweteka kwambiri chifukwa tomato amene mumamuona pamsikawu sachoka pafupi, adatero Magugu. Kulira kwa Magugu mwina kungathe ndi ganizo lomwe mkonzi wa pulogalamu ya Ulimi wa Lero Excello Zidana, yemwe ndi mlangizi wa zaulimi, akunena: Vuto ndi alimiwa chifukwa amayamba kulima asadapeze msika. Ndi bwino alimi asadalime adziyamba aona msika momwe ulili komanso kumatchera nyengo yake chifukwa zimathandiza kuti idziwe nthawi yomwe mbewuyo imagulika bwino. Zidana akuti ndi bwinonso alimiwa aziyangana msika wina ngati zinthu zavuta choncho. Kuti upite madera ena upeza alimi akupha makwacha ndi mbewu yomweyo. Ayende misika ina ndithu akasimba mwayi, adatero.
2
Ndale zachibwana zalowa ku MCP Masapota a MCP sakudziwabe odzawatsogolera Kadaulo wa ndale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College Blessings Chinsinga wati chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chalowa chibwana, ndipo sichikudziwa momwe chingaongolere ndale mdziko muno. Chinsinga adanena izi Lachinayi potengera momwe chipanichi chikuyendetsera ndale pokonzekera chisankho cha 2014. Chipanichi chidalepheretsa msonkhano wake waukulu mu April ndipo masiku apitawa, chipanichi chidafuna kusefa ena mwa anthu 12 amene akufuna kudzapikisana nawo pampando wa yemwe adzaimire chipanichi pa chisankhocho. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chipanichi chidakhazikitsa komiti younika anthu amene akufuna kudzapikisana nawo. Wapampando wa komitiyo ndi Lingson Belekanyama yemwe Lachitatu adati atakumana adapeza kuti sikofunika kuchotsa ena mwa omwe amafuna kudzapikisana nawo, makamaka amene sadakhale mchipanicho kwa zaka zisanu. Izi zimasonyeza kuti Lazarus Chakwera, yemwe adali mtsogoleri wa mpingo wa Assemblies of God, Felix Jumbe yemwe adali mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) komanso Lovemore Munlo yemwe adali mkulu wa majaji mboma la Bingu wa Mutharika sakadapikisana nawo pachisankhocho. Chinsinga adati chipanichi chikupereka unthenga osiyanasiyana okhudza tsogolo lake kwa Amalawi zomwe zikusonyeza kuti atsogoleri ake alibe mphamvu zowongolera kayendetsedwe kachipani. Msabata ziwiri zokha apereka mfundo zotsutsana zingapo. Choyamba mtsogoleri wawo John Tembo ndi mneneri wawo Jolly Kalelo adasemphana pankhani ya tsiku ndi malo a msonkhano wawo waukulu omwe anthu ambiri akuyembekezera. Sabata yomweyo Tembo adanena pawailesi ya Zodiak kuti achepetsa chiwerengero cha ofuna kudzapikisana nawo pampando wa odzayimilira chipanichi pa chisankho koma komiti yomwe imaunika anthuwo yati palibe kuletsa munthu kupikisana nawo, adatero Chinsinga. Iye adatinso sabata yomweyo, Tembo adauza nyuzipepala kuti adadzipereka kutsika pa mndandanda wa anthu ofuna kudzapikisana nawo pampandowo koma komitiyi yakana kuti palibe yemwe adadzipereka kutsika pamndandandawo. Apa zikusonyezeratu kuti palibe mgwirizano pakati pa akuluakulu achipani. Izi zikusonyezeratu kuti ndale zathu ndizosakhwima, adatero Chinsinga. Mmodzi mwa ofuna mpandowu mchipanichi Felix Jumbe, yemwe adali mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) adati amkhalakale ena a mchipanichi akupanga ndale zapansipansi pofuna kuipitsa anzawo. Chinsinga adati MCP ikulakwitsa chifukwa mmalo motsata ndondomeko zokhazikika za chipanicho, akubweretsa zachilendo zimene akuzikonza ndi anthu ochepa. Iye adati nzodabwitsanso kuti Tembo adakana kulandira K600 0000 yomwe Chakwera adapereka ku chipani ngati msonkha wake kuthumba lodzayendetsera msonkhano waukuluwo. Okha adanena kuti amene akufuna kudzapikisana nawo akuyenera kusonkha ndalama ndiye apa chokanira ndalama zina ndikumalandira zina ndi chiyani? Chofunika apa chipanichi chikuyenera kumapanga fundo zolimbitsa chipani, adatero Chinsinga. Tembo adauza atolankani kuti adakana ndalamazo chifukwa Chakwera adapereka nthawi yomwe akuluakulu a chipanichi amakumana kuti akambirane za mmene angachepetsere chiwerengero cha okufuna kutsogolera MCP. Iye adati kulandira ndalamazo kukadasokoneza ntchito yomwe amagwira akuluakuluwo poti Chakwera ndi mmodzi mwa anthu 12 omwe akufuna kudzalimbirana nawo mpandowo. Chakwera wati iye samapereka ndalama ku nkhumano wa akuluakuluwo koma kuthumba la ndalama zodzayendetsera msonkhano waukulu. Sindidatenge ndalama ndekha kukapereka. Ndidatsata ndondomeko yomwe idakhazikitsidwa kuti ndalama ziziperekedwa kudzera mwa anthu omwe akuthandiza chipani kutolera ndalama ndipo ine ndidachita chimodzimodzi, adatero Chakwera. Polankhula ndi wailesi ya Zodiak Broadcasting Station (ZBS) Tembo adadzudzula mneneri wachipanicho Jolly Kalelo pofulumira kulankhula ndi atolankhani pa za tsiku komanso malo omwe msonkhanowo udzachitikire. Kalelo adauza nyuzipepala ndi mawailesi kuti msonkhano waukulu wa MCP udzachitika pa 9 August 2013 ku Natural Resources College koma Tembo adati akuluakulu a chipanicho adangokambirana za masikuwo koma adali asadatsimikize podikira zokambirana zina ndi akuluakulu a kumalo omwe akufuna kudzachitirako msonkhanowo.
11
MEC Yawunika 35% ya Maboma pa Chisankho Bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC) likupitilira kupereka zotsatira zotsimikizika za chisankho cha president chomwe chachitika lachiwiri lapitali. Kachale: Tizingosindikiza file imodzi kuti tichite changu Malingana ndi wapampando wa bungweli Justice Dr. Chifundo Kachale, pofika 11 koloko mmawa wa lero, bungweli lakwanitsa kupereka zotsatira za maboma khumi ndi limodzi okha mwa maboma 28 a dziko lino. Mwazina Dr. Kachale ati bungweli lipitilira kupereka zotsatirazi kudzera kwa wofalitsa nkhani wake Sangwani Mwafulirwa yemwe akhale akuchita mikumano ndi atolankhani kuwadziwitsa zotsatira zomwe zatsala mpaka pamapeto powulutsa zotsatira zonse. Chinthu china chomwe chikumatenga nthawi ndi chakuti pakumabwera ma file awiri a original kuchokera kuma district, ina imapita ku parliament kuti akasunge ma record a masankho, dongosolo limenelo taliwunikira ndipo tawona kuti limatenga nthawi kwambiri chifukwa choti ma record enawo a zipani alinawo kale ndiye kwa pano tizingosindikiza file imodzi, anatero Dr. Kachale. Iwo ati mwa maboma omwe awunikidwa kale zotsatira zawo, palibe madandaulo omwe sanayankhidwe moyenera. Wapampando wa bungweli Justice Dr. Chifundo Kachale akuyembekezeka kupereka zotsatira za chisankhochi mawa.
11
Mpingo ndi Anthu Omwe Amasonkhana ndi Kupemphera Limodzi-Papa Papa Fransinco yemwe ndi mtsogoleri wa katolika pa dziko lonse wakumbutsa anthu kuti ngakhale kuti panopa anthu akutsatira mapemphero osiyana-siyana kudzera mu njira za makono monga makina a intaneti chifukwa cha nthenda ya Covid 19, cholinga cha mpingo ndi kuti anthu azisonkhana ndi kupemphera limodzi mmatchalichi awo. Papa Francisco wapereka chenjezo ndipo walankhula izi lachisanu pa Misa yomwe anatsogolera ku likulu la mpingo ku Vatican pamene mliri wa Coronavirus wavutitsa kwambiri zomwe zachititsa kuti anthu asiye kupita ku matchalitchi awo ndipo mmalo mwake akumatsatira mapemphero osiyanasiyana kudzera mu njira za makono zofalitsira mauthenga monga makina a intaneti ndipo iye wati akhristu akuyenera kukumbukira kuti mpingo ndi gulu la anthu omwe amabwera pamodzi ndi kupemphera powonana maso ndi maso. Nkutheka kuti pa nthawi iyi ya mliri wa Coronavirus anthu apusisika ndi kumaganiza kuti ukatha mliriwu palibenso chifukwa chomasonkhanirana malo amodzi ndi kumapemphera, anatero Papa. Iye wati zomwe zikuchitika pano ndi za kanthawi kochepa kotero kuti pambuyo pa mliri wa Coronavirus anthu adzayenera kupitiriza kusonkhana malo amodzi ndikuchita mapemphero monga zinalili mliriwu usanabwere ndipo wati anthu akuyenera kukumbukira kufunika kolandira Ambuye Yesu wokhala mu Ukaristia komanso kufunika kwa masakramenti ena monga Sakramenti la kulapa ngakhale kuti iye wati akuzindikira kuti izi ndi zovutirapo pa nthawi iyi ya mliri wa Coronavirus.
13
Sitilemba akunjaAnsah Pamene kalembera wachisankho walowa gawo lachisanu, mkulu wa bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah wati Amalawi asade nkhawa, chifukwa anthu a kunja salembetsa nawo mkaundula. Ansah adanena izi potsatira ndemanga za ena kuti pali chiopsezo choti nzika zina za dziko la Mozambique zikhonza kulembetsa mkaundula mboma la Mulanje. Malinga ndi anthu ena, pali chiopsezo kuti anthu ena a ku Mozambique akhonza kufuna kulembetsa nawo, makamaka ku Limbuli ndi Muloza, komwe ndi dera la mmalire ndi Mozambique. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Koma Ansah adanenetsa: Taika ndondomeko zonse kuti pasakhale wakunja woti walembetsa. Izi tikuchita poonetsetsa kuti pali mamonitala a kuderalo amenenso adzaonetsetse kuti ofuna kulembetsa ali ndi chitupa cha unzika. Mkulu wa nthambi yoona za kalembera wa unzika mboma la Mulanje, Wellingtone Kalambo wati akumanapo ndi nzika za ku Mozambique zofuna kulembetsa nawo mavoti. Taonapo mafumu a ku Muloza akupereka umboni kuti munthu ndi mMalawi, koma kuwafunsitsa, tidapeza kuti ndi a ku Mozambique, adatero Kalambo. Kalembera wa chisankho adalowa mgawo lachisanu Lolemba ndipo likuyembekezeka kudzatha pa Malinga ndi MEC, anthu 3 271 744 adalembetsa mmagawo apitawa, pomwe MEC imayembekezera kulembetsa anthu 4 619 174. Izi zikusonyeza kuti anthu 81 mwa 100 alionse amene amayenera kulembetsa ndiwo adatero. Kutsika kwa anthu amene akulembetsa kwakhudza akadaulo, a mabungwe ndi zipani zandale zina. Katswiri wa zandale wa ku Chancellor College Ernest Thindwa wati mchitidwe wamphwayi kukalembetsa ukhonza kukhala kukhumudwa kwa Amalawi ndi mchitidwe wa andale omwe amasintha mawanga akasankhidwa mmaudindo. Mwina anthu adagwa mphwayi ndi nkhani za zisankho chifukwa amakhumudwa ndi mchitidwe wa atsogoleri omwe amalonjeza zinthu zina nthawi ya kampeni koma osazikwaniritsa akasankhidwa, adatero Thindwa. Koma zipani zandale, zaalunjika ponena kuti bungwe la MEC silinafalitse bwino uthenga wa kalembera chifukwa likulimbikira pofalitsa mauthenga pa wailesi ndi nyuzipepala basi, mmalo mopitanso kumaderawo. Mneneri wa chipani cha United Democratic Front (UDF) Ken Ndanga, wati kafukufuku wawo adaonetsa kuti bungwe la MEC silidafalitse uthenga mokwanira mmadera. Tikawafunsa bwanji sanalembetse, anthu mmadera amati samadziwa zoti kalembera wafika mdera lawo. Ngati chipani, tikumapita mmaderamu kumema anthu, adatero Ndanga. Mlembi wamkulu wag ulu la United Transformation Movement (UTM) Patricia Kaliati komanso mlembi wamkulu wa Malawi Congress Party (MCP) Eissenhower Mkaka adagwirizana ndi Ndanga podzudzula MEC. Ndikunena pano ndili ku Mulanje kumene kalembera ali mkati koma sindinaone galimoto ya MEc ngakhale chimkuzamawu kumema anthu kukalembetsa. Mkaka adati chipani chawo, chomwe chakhala chikupempha MEC kuti ibwereze kalembera mmadera ena, chimayembekezera kuti pofika gawo lachinayi la kalembera, zinthu zikhala zitasintha koma mmalo mwake zikunkira kuonongeka. Mgawo loyamba ndi lachiwiri, zidali zomveka kuti uthenga udali usadamwazidwe mokwanira koma mgawo lachinayi tizikamba nkhani imeneyi? Ayi sizoona MEC ikadawonapo bwino, adatero Mkaka. Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi zisankho la Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa adagwirizana ndi zipanizi kuti MEC yalephera kumwaza mauthenga a kalembera. Ndidali ku Thyolo ndi Luchenza komwe anthu samaonetsa chidwi ndipo ntafunsa, makhansala ngakhaleso anthu amati sadalandire uthenga uliwonse woti kukuchitika kalembera mdera lawo kutanthauza kuti ntchito ikadalipo, adatero Duwa. Koma malinga ndi Ansah, palibe kuwiringula kulikonse koti mauthenga sadamwazidwe chifukwa MEC ndi mabungwe ena monga National Initiative for Civic Education (Nice) Trust ayesetsa kumwaza mauthenga. Kupatula njira yomwaza mauthenga pa wailesi, timagwiritsanso ntchito galimoto zokhala ndi zimkuzamawu. Mgawo loyamba, tidagwiritsa ntchito galimoto 15, gawo lachiwiri galimoto 14, gawo lachitatu galimoto 18 ndipo gawo lachinayi galimoto 17, adatero Ansah. Iye adati bungweli lidzaunika pamapeto pa zonse ngati nkoyenera kubwereza ntchito ya kalembera mmaboma omwe sizidayende bwino.
11
Tidasala masiku 52 kuti Mulungu atiunikire Nthawi zambiri, anthu timatenga banja ngati sitepe pamoyo wathu basi koma tikalingalira momwe banja la mbusa komanso mlembi wa mkulu wa mpingo wa CCAP Reverend Vasco Kachipapa Banda ndi mkazi wake Madalitso Nyoli, mibadwo yobwerayi idzazindikira momwe banja la umulungu limakhalira. Awiriwa akuti adakumana mu 1992 onse atasankhidwa kupita kusukulu ya sekondale ya Mitundu ndipo chikondi chawo chidayamba mu 1994 koma uku sikudali kuyamba kwa banja poti zambiri zidadutsapo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Rev. Kachipapa adati mizati itatu ndiyo idagwira ntchito kuti awiriwa atseguke mmaso kutidi adalengedwa kudzakhala limodzi ndi kutumikira Chauta ngati bambo ndi mayi komanso odyetsa ndikusamala nkhosa zake. Kachipapa ndi Madalitso: Lero ndi banja Mzati woyamba, ineyo ndidadwala tikadali kusukulu mpaka ndidapita kunyumba. Nditapeza bwino nkubwerako, Madalitso adabwera kudzandizonda ndipo aka sikadali komaliza. Pamenepa ndidazindikira kuti ndi umunthu weniweni, adatero Kachipapa. Iye adati chikondichi sichidasanduke mapeto azonse ayi koma chiyambi cha kudzifunsa ndi kupempha utsogoleri wa Mulungu. Mchaka cha 1997, tonse awiri tidayamba mapemphero ndi kusala kwa masiku 52 (Loweruka lokhalokha) kupempha Mulungu kuti atiunikire ngatidi tidali oyenera kukwatirana. Ndi mzati wachiwiri ndipo mzati wachitatu udali nthawi yomwe ine ndimapanga maphunziro a zaubusa ku Zomba, mkazi wanga adali atayamba kale ntchito ndipo adandithandiza kupereka malowolo ake omwe, adatero Kachipapa. Iye adati Chauta atavomereza zonse, ndondomeko zoyenera zidatsatidwa kufikira nthawi ya chinkhoswe mchaka cha 1998 ndipo kenako ukwati woyera ku Ntchisi CCAP. Ndimakonda mkazi wanga kwambiri chifukwa cha mtima wake wabwino, amakonda kupemphera kwambiri ndipo simkazi wanga chabe koma mzanga muuzimu, adatero Kachipapa. Nawo mayi a kunyumba akuti (Madalitso) akuti abusawa ndi bambo wabwino wokonda banja lawo ndi wodziwa kusamala. Ndi bambo abwino kwambiri odziwa udindo wawo ndiokonda banja lawo komanso kusamala ana awo. Timapemphera limodzi, kuyenda limodzi, kudya limodzi mwachidule timapangira zinthu limodzi, adatero mayiwo.
13
Afa atamwa bibida wosadyera Mneneri wa polisi ya Nkhotakota Williams Kaponda watsimikiza kuti bambo wina kumeneko wakabzala chinangwa atapapira mowa osadyera. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kaponda adati malinga ndi achibale, Damson Wasiya, 34, malemuwo omwe ndi Francis Phiri adapita kukapopa mowawo Lamulungu pa 8 November mbomalo. Achibalewo auza apolisi kuti malemuwa adapezeka usiku akuchokera kopopa mowawo ali lamba! Mumsewu, zomwe zidakhudza ofuka kwabwino amene adamutengera kunyumba. Ataona kuti mbaleyo akuoneka moti samapeza bwino, adathamangira naye kuchipatala cha boma komwe madotolo adakatsimikiza kuti adali atafa, adatero Kaponda yemwe adati zotsatira za achipatala zidaonetsa kuti malemuwo adafa chifukwa chomwa wosadyera.
15
Zitupa zaunzika zina zasowa Zitupa 93 893 za uzika mboma la Kasungu zasowa. Tamvani itha kuvumbulutsa. Izitu zadziwika pamene bungwe lolembera unzika la National Registration Bureau (NRB) layamba kupereka zitupazi kwa eni. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mneneri wa wa bungwe la NRB Norman Fulatira watsimikiza izi ndipo wati: Ili si vuto lalikulu mtima ukhale mmalo. Maboma amene adayambirira kulembetsa za unzika a Mchinji, Dowa, Kasungu, Salima, Nkhotakota ndi Ntchisi ayamba kulandira ziphaso zawo zomwe zaonetsa kuti nkhope zina zikusowa. Anthu 93 893 amene amayembekezera kulandira zitupazi adadzidzimuka kuona kuti maina awo palibe pamene anzawo nkhope zawo zatuluka ndipo alandira zitupa. Anthu amene dzina lawo lasowa mbomalo ati chiyembekezo chawathawa ngati angalandire zitupa zawo. Lufeyo Mwanza wa mbomalo adauza Tamvani kuti chikhulupiriro pa NRB achotsa kuti zitupa zawo zidzapezeka. Inde akutilimbitsa mtima kuti zitupa zathu zibwera komabe chilimbikitso chimenechi nchosakwanira. Tikuganiza kuti zasowa ndipo mwayi wokhala ndi zitupazi watiphonya, adatero Mwanza. Iye adati pakhota nyani mchira nkuti anzawo amene adajambulitsira limodzi zitupa zawo zatuluka koma iwo zavuta. Komabe Fulatira akuti mwa maina 1.7 miliyoni omwe adalembedwa moyambirira, mayina 1.5 miliyoni okha ndiwo adatumizidwa kuti akatulutse zitupa ndipo maina enawo amaunikidwa ngatidi ali a Malawi. Anthu [asathamange magazi] kuti zitupa zawo zasowa, chifukwa tikukonza ndipo alandira zonse zikatheka bwinobwino, adatero Fulatira. Iye adatinso zitupa 200 000 za mndime yoyamba ya kalemberayu ndizo sizidakonzedwe ndipo anthu omwe zitupa zawo zasowawo akhoza kukhala mgululi. Pologalamuyi ndi ya a Malawi choncho timayenera kuunika maina bwinobwino kuti tisapezeke zoti tikupeleka ziphaso kwa alendo. Zonse zikatheka, aliyense yemwe ndi nzika ya dziko lino ndipo adalembetsa, adzalandira chiphaso, adatero Fulatira. Senior Chief Kaomba ya mboma la Kasungu idati iyo siyikuonapo vuto pa nkhaniyi chifukwa zitupa zomwe zikusowa nzochepa poyerekeza ndi zomwe zapezeka. Aka nkoyamba boma kupanga kalembera ngati uyu ndiye pa mayina 1.5 miliyoni, kusowa maina okhawo si chodandaulitsa kwenikweni ndipo tikuyenera kumvetsetsa, adatero Kaomba. Iye adapempha anthu kuti adekhe chifukwa NRB ikulongosola. Boma lidakhazikitsa ntchito ya kalembera wa unzika kuti lizitha kuzindikira anthu ake makamaka powathandiza pa ntchito zofunika ngati za umoyo, maphunziro komanso kuwapeza mosavuta akasowa kapena kutsakamira mmaiko a eni. Kalembera yemwe ali mkati pano adayamba pa 24 May chaka chino ndipo akuyembekezeka kutha mu December. Malinga ndi Fulatira, ntchitoyi idzakhala ikupitilira mpaka kalekale. Iyi idali ndime yokhazikitsira ndipo aliyense amayenera kulembetsa mmalo omwe tikuchita kukhazikitsa koma kuyambira January chaka chamawa, omwe sadalembetse, aziloledwa kukalembetsa mmaofesi athu a mmaboma kapena kotumizira makalata [post office] yomwe angayandikane nayo, adatero Fulatira. Iye adatinso amene ayambe kulembetsa chaka chamawa koyamba azidzalembetsa ulere pamene kwa omwe adasowetsa chitupa ndipo akufuna china, azidzapemphedwa kupereka kangachepe. Kwa amene amakhala kutali ndi post office sadzavutikanso chifukwa NRB idzidzayendera mmadera kuthandiza Amalawi malinga ndi Fulatira.
11
Akhristu Alumikizana Pothandiza Atumiki Bungwe la akhristu eni ake mu arkidayosizi ya Blantyre lati likufuna kulimbikitsa ntchito zotukula arkidayosizi-yi komanso kusamalira atumiki amu mpingo-wu. Wapampando wa akhristu mu arkidayosizi-yi a Joseph Kachala ayankhula izi pomaliza pa msonkhano omwe anali nawo Loweruka pa 29 February ku Limbe Cathedral Mu mzinda Wa Blantyre. Iwo anati ntchito yawo ndi kuwonetsetsa kuti akhristu akudziwa udindo wawo pothandiza mpingo komanso atumiki mu mpingowu monga asisitere, ansembe, abulazala ndi ena ambiri. Timakambirana kuti ngati akhristu tikuyenera kuwonetsetsa kuti atumiki mu mpingowu akusamalidwa moyenera mmoyo wawo wa thupi kuti azititumikira mopanda chowabwezeretsa mmbuyo, anatero a Kachala.
13
Zipani za moyo zionekeCMD Kodi zipani zinazi zili moyo? Nthawi yofukula yakwana mzipani pamene bungwe loona mgwirizano wa zipani zosiyanasiyana la Centre for Multiparty Democracy (CMD) lalengeza zokumana ndi akuluakulu a zipani. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Bungweli laitana zipani 41 zomwe zidalembetsedwa koma zilibe aphungu mNyumba ya Malamulo. CMD ikuchita izi kutsatira kudutsa kwa bilo yokamba za kayendetsedwe ka zipani imene mwa zina ikuti zipani zimene sizikuoneka zichotsedwe mkaundula pakatha miyezi 12. Tenthani: Tiwaimbira Kalata yomwe CMD yatulutsa ikuti eni zipanizo atumize ku bungwelo maina a mtsogoleri wawo ndi mlembiatumizenso nambala, madera amene akukhala. Mkulu wa bungwelo, Kizito Tenthani adati zipanizo zikatumiza maina ndi manambalawo adzawaimbira kuti akumane nawo kuti awafotokozere zomwe zili mbiloyo. Iye adati: Ngati satiyankha mwina zisonyeza kuti kulibe munthu. Pakatha miyezi 12 ndiye kuti zisonyeza kuti chipanicho chazimirirakusonyeza kuti osindikiza zipani atha kuchifufuta. Mwa zipani zomwe zaitanidwa ndi cha The Malawi Democratic (MDP) chomwe mwa ena amene adachiyambitsa ndi Kamlepo Kalua yemwe lero ali ku PP. Chipani china ndi cha Malavi Peoples Party (MPP) chomwe adayambitsa ndi Uladi Mussa amene akungoyendayenda. Adali ku UDF asadasinthe golo kupita ku DPP. Madzi atachitako katondo adalumphamo kugwera mu PP, lero wasinthanso golo kubwerera ku DPP. Titamuimbira foni ngati alembere bungweli monga iye mtsogoleri, Mussa adayankha modabwa. Malavi ndiye chiyani? adafunsa. Aaa! Nanga ine mesa ndidachokako, ndidali ku PP pano ndili ku DPP. Inuyo mungopitako mukaone atsogoleri amene apitawo osati muzindifunsa ine, adatero. Koma Tenthani ali ndi chikhulupiriro kuti zipanizi ziwalembera. Ine ndi mkulu wa CMD, nditachoka lero sizikutanthauza kuti CMD yatha, atsogoleri otsalawo ndiwo angayankhepo ngati atafunidwa. Titsimikiza kuti mzipanizo mudatsala ena amene atilembere, adatero. Mndandanda wa zipanizi ndi womwe udalembetsedwa mdziko muno kuti ndi zipani zokhazikika. Zina mwa zipani zoitanidwazo zidamveka pachisankho cha 1994 osamvekanso. Izi ndi monga cha Congress for the Second Republic cha Kanyama Chiume, Malawi Democratic Union cha Amunandife Mkumba, United Front for Multiparty Democracy, Malawi National Democratic Party ndi zina zotero. Dziko lino lili ndi zipani zoposera 50.
11
Wofuna kugulitsa alubino achimina Bwalo la milandu la Mzuzu majisitireti lalamula Philip Ngulube, wa zaka 21, kuti akakhale kundende ndi kukagwira ntchito yakalavulagaga kwa zaka 6 atamupeza ndi mlandu wofuna kuba msungwana wachialubino ndi cholinga chofuna kumupha. Ngulube, yemwe adali mphunzitsi wodzipereka pasukulu yapulaimale ya Mongo mboma la Mzimba, adagwirizana zomanga banja ndi msungwanayo, wa zaka 17, yemwe ankaphunzira pasekondale ya Mzimba. Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Ngulube (akukokera kabudulayo) kutuluka mkhoti ulendo wa kundende Koma mphuno salota, Ngulube adali ndi maganizo ogulitsa msungwanayo kwa munthu wajohn chirwa malonda yemwe ndi mbadwa ya mdziko la Tanzania. Koma msungwnayo adapulumukira mkamwa mwa mbuzi mbadwa ya ku Tanzaniayo itakatsina khutu apolisi za malonda omwe Ngulube adali nawo. Apolisi ndi luntha lawo, adapita kwa Ngulube ngati ofuna kugula mualubinoyo. Apa mpamene Ngulube adakwidzingidwa ndi unyolo zitapezekadi kuti amagulitsa mtsikana wachikondi wakeyu pamtengo wa K6 miliyoni. Nkhani idapita kubwalo la majisitireti Gladys Gondwe komwe adazengedwa mlandu wofuna kuba munthu ndi cholinga chofuna kumupha, womwe adaukana. Koma Lolemba lapitali, Gondwe muchigamulo chake chomwe chidatenga mphindi zisanu zokha, adalamula kuti Ngulube akagwire gadi kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Gondwe adati mlandu womwe amazengedwa Ngulube uli ndi chilango cha zaka zisanu ndi ziwiri. Iye adati adaganiza zopereka zaka 6 ndi cholinga chakuti Ngulube adziwe kuipa kwa mchitidwe wofuna kuba munthu. Woweruzayu adati nzomvetsa chisoni kuti msungwanayo adasiya sukulu chifukwa cha kusowa mtendere ndi zomwe adachita Ngulube. Iye adati izi nzotsutsana ndi malingaliro a mabungwe ndi boma polimbikitsa maphunziro a asungwana. Wozenga mlandu wamkulu kuchigawo cha kumpoto, Christopher Katani, adati ndi wokondwera ndi chigamulo chomwe bwalo la milanduli lidapereka. Iye adati zaka 6 ndi zokwana potengera kuti mlandu womwe amazengedwawo umayembekezereka kulandira chilango cha zaka 7. Katani adatinso ndi wokhurira poti nkoyamba kumpoto bwalo lamilandu kutumiza munthu kugadi chifukwa cha mchitidwe wakuba anthu achialubino. Ngulube polandira chilangochi, adaoneka kuti adali woyembekezera matherowo chifukwa sadaoneke kudodoma kulikonse.
7
Ndi Udindo wa Amalawi Kutetedza Chilengedwe- SVP Bungwe la zachifundo mu mpingo wa katolika la St. Vincent De Paul (SSVP) lati kusintha kwa nyengo kwakhala gwero lalikulu la mavuto ambiri amene anthu mdziko muno akukumana nawo kuphatikiza kusowa kwa malo okhala abwino komanso chakudya. Bungwe la SVP kupereka zofunda kwa ovutika Bungweli lanena izi lamungu pa 22 February 2020 ku likulu lake mdziko muno mu mzinda wa Blantyre pothilira ndemanga pa mapurojeketi omwe bungweli lili nawo mchaka chino. Mkulu wa bungweli mdziko mu a Charles Kimu anati anthu ambiri omwe bungweli lawafikila mbuyomu ndi anthu amene anakhuzidwa ndi kusintha kwa nyengo monga kusefukila kwa madzi komanso chilala, choncho vutoli ndi lalikulu pakati pa mzika za dziko lino. Tapelera katundu osiyanasiyana kwa mawanja amene anakhuzidwa ndi madzi otsefukila komanso kwa anthu okhuzidwa ndi ngamba ochuluka ntchaka cha 2019 choncho vutoli likuvutitsa miyoyo ya anthu ambiri dziko muno, anatero a Kimu. A Kimu anati kupatatula kuwapasa zinthu zokhazikika anthu amene anakhuzidwa ndi kusintha kwa nyengo komanso osowa, ndi kofunika kwambiri kuti dziko lino liyike chidwi chake posamalira chilengedwe pozindikira kuti chilengedwe ndi gwero la zofunika zambiri pa umoyo wa munthu. A Kimu kupereka zovala kwa ovutika Iwo anati chaka cha 2020 Bungweli lilindimalingaliro okonzera nyumba za anthu omwe anakhuzidwa ndi mvula yamphavu mchaka cha 2019 ndipo ndondomekoyi iyambila mu akidayosizi ya Blantyre. Anthu amene anakhuzidwa ndi mvula ya mphavu chaka chatha akukhalabe mnyumba zamavuto monga zamingalu choncho ndikofunika kuti kuwafikila anthuwa, anaonjezera motero a Kimu. Mwazina bungweli mchaka cha 2020 liphunzitsanso ntchito zamanja mwaulele anthu ochokera ku mabanja ovutikikitsitsa ngati mbali imodzi yowalimbikitsa anthuwa kuimba paokha pa chuma. Bungwe la SVP kupereka chimanga kwa anthu osowa Wapampando wabungweliyu anapitiliza kupempha anthu amene amalandira thandizo losiyanasiya kuchokela kwa akufuna kwabwino kuti azisamala thandizolo chifukwa kutelo zimaonetsa mtima othokoza. Zimamvetsa chisoni kuona anthu akugulitsa katundu yemwe alandira kwa akufuna kwa bwino, anadandaula choncho a Kimu. Bungwe la St. Vincent de Paul liyamba mdziko muno ku Zomba dayosizi pa 17 Okotobala, mchaka 1970 ndi bambo Berck a mdziko la France.
18
Kutentha koonjeza kuzinga maiko A nthambi yoona za nyengo mdziko muno auza Amalawi kuti alimbe mtima chifukwa nyengo yotentha yomwe yakhala mdziko muno kwa sabata ziwiri zapitazi, kupitirira kwa sabata zikubwerazi. Kuchokera sabata yatha, dziko lino lakhala likutentha ngati nganjo ya moto moti madera a kunsi kwa chigwa cha mtsinje wa Shire kutenthaku kumafika pa 450C pomwe madera ena kumafika pa 350C. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Anthu akhala akudandaula kuti kutenthaku kukusowetsa mtendere. Zikuoneka kuti nyengo yotenthayi yatikakamira chifukwa a nthambi yoona zanyengo adalengeza Lolemba kuti Amalawi angovala zilimbe chifukwa nyengoyi ipitirira kwa sabata zikubwerazi. Komatu si dziko lino lokha lomwe lakhaula ndi kutenthaku chifukwa maiko ena ambiri a mdera la kummwera mu Africa la Southern African Development Community (Sadc) monga Botswana, Eswathini, Mozambique ndi ena. Malinga ndi kalata yomwe idatulutsa nthambi yoona za nyengo mbungwe la Sadc Lolemba pa October 28, yachenjeza anthu kuti kutentha molapitsa mmaiko a mderali. Pomwe kalata yochokera ku nthambi yoona za nyengo mdziko muno ya Climate Change and Meteorological Services yomwe adatulutsa ndi mkulu wa nthambiyo Jolamu Nkhokwe idalongosola kuti kuchokera Lamulungu pa October 27 kufika pa November 3, kutentha ndi dzuwa kupitirira. Kalatayo yati sabata yapitayi madera monga Lengwe National Park mboma la Chikwawa kudatentha 45C pomwe ku Mwanza ndi Nsanje kudafika 44C. Koma kuchokera Lachitatu pa November 30, mitambo iyamba kumangana mmadera ena a dziko lino zomwe zikhonza kubweretsa mvula ya mphepo ya mkuntho komanso ziphaliwali, ikutero kalatayi. Malinga ndi Nkhokwe aka si koyamba kuti mdziko muno mutenthe chonchi maka mmadera a kunsi kwa chigwa cha mtsinje wa Shire koma kuti chaka chino ndi dziko lonse lomwe latentha. Nkhokwe adati ana ndi anthu achikulire ngofunika chisamaliro kwambiri pa nthawiyi. Katswiri pa nkhani za sayansi, chilengedwe yemwenso amadziwa bwino za kusintha kwa nyengo, Professor Sosten Chiotha adati kutenthaku ndi zina mwa zizindikiro za kusintha kwa nyengo. Timadziwa kuti timakhala ndi nyengo zosiyana nthawi ndi nthawi ndipo ndi mmene zikuyenera kukhalira, koma kusinthaku kukakhala kowonjeza kuposa mmene zikuyenera kukhalira, zimalowa mgulu la kusintha kwa nyengo, adalongosola Chiotha. Koma iye adalongosolanso mwachindunji kuti nyengo ikangosintha kamodzi sikusintha kwa nyengo koma kusinthaku kumayenera kukhale kwa nthawi yaitali. Malinga ndi Chiotha, malipoti a zanyengo mdziko muno akuonetsa kuti kusinthaku kwakhala kukuchitika kwa nthawi yaitali ndithu. Naye bwanamkubwa wa mboma la Karonga, Frank Kalilombe adati bomalinso kwakhala kukutentha molapitsa kuchokera sabata yapitayi. Iye adati mpofunika kupeza njira zoti ana ndi achikulire adziwe zoyenera kuchita panthawiyi poopa ngozi zodza mwadzidzidzi monga kukomoka ndi zina kaamba ka kutenthaku.
18
Episkopi Apempha Amayi Adzipereke Pofalitsa Mthenga Wabwino Episcope wa dayosizi ya Chikwawa Ambuye Peter Musikuwa apempha amayi akatolika mdziko muno kuti akhale odzipereka pa ntchito yofalitsa uthenga wabwino ku matchalitchi amene amayiwa akupezekako. Ambuye Musikuwa omwenso ndi mkulu woona zachipembezo ku likulu la mpingo wa katolika mdziko muno amalankhula lamulungu pambuyo pamwambo wa misa yotsekera msonkhano wa amayi mdziko muno womwe umachitikira ku sukulu ya ukachenjede ya DMI mu dayosizi ya Mangochi. Umodzi mwa misonkhano ya bungwe la amayi Iwo ati mpingo ukuyembekeza kusitha kwakukulu kuchokera kwa amayiwa pambuyo pa msonkhanowu monga pankhani zosamalira zachilengedwe, zaumoyo komanso kukonda ndi kulimbikitsana kuwerenga bukhu loyera. Tikuyembekezera kuti zinthu zikasintha ku maparishi komwe amayiwa akuchokera. Tikukhulupilira kuti tiwona kusintha pa nkhani ya zokhudza kusamalira chilengedwe ndi zina zambiri, anatero Ambuye Musikuwa. Polankhulapo wachiwiri kwa wapampando wa bungwe la amayi mdziko muno mayi Magdalene Masamba Nkhope apempha amayi omwe anafika ku msonkhanowu kuti akagawane ndi anzawo mmadayosizi awo mfundo zomwe atenga ku msonkhanowu. Msonkhanowu omwe unali wa masiku asanu unayamba lachitatu pa 11 mpaka lamulungu pa 15 December 2019 ndipo wachitika pamutu wakuti Amayi akatolika tayitanidwa kukhala oyera mtima kuti tiyeretse dziko lapansi kwathunthu.
13
Bwanamkubwa Wapempha Mabungwe Athandize Khonsolo Polimbana Ndi Coronavirus Bwanamkubwa wa boma la Zomba Dr. Raphael Piringu wapempha mabungwe omwe akugwira ntchito zawo mboma la Zomba kuti athandidze ndi zipangizo zosiyanasiyana zothandiza anthu kuti asatenge kachirombo ka Coronavirus. Piringu: Anthu owona odwala mchipatala akuchuluka Dr. Piringu amayankhula idzi lachitatu ku Zomba pomwe amakumana ndi akulu akulu a mabungwe komanso oyimililira zipembedzo (Pastors Fraternal). Iwo apemphanso mabungwewa kuti apereke uthenga mzipatala kuti anthu owona odwala asamachuluke. Dr Piringu ati misika yambiri ya mbomalo ilibe mipanda choncho apemphanso mabungwewa kuti aphunzitse anthu nkhani yosamba mmanja. Mmau ake wapampando wa mabungwe omwe si a boma mboma la Zomba a Newton Sindo apempha mabungwewa kuti akamapereka zinthu kwa anthu mmadera akumidzi ndibwino kuti adziwaphunzitsa kagwiritsidwe ntchito kazinthu zomwe aperekazo.
6
Aphungu ku Uganda Akufuna Mkazi wa Mtsogoleri wa Dzikolo Akonze Maphunziro Nyumba ya malamulo mdziko la Uganda yati ikufuna mkazi wa mtsogoleri wa dzikolo, Janet Museveni afotokoze bwino pa nkhani ya kusayenda bwino kwa maphunziro mdzikolo. Malipoti a wailesi ya BBC ati speaker wa nyumbayi Rebecca Kadaga analembera kalata Museveni yemwe ndi nduna yowona za maphunziro kuti akawonekere mnyumba ya malamuloyi lachiwiri ndi kukafotokoza bwino chomwe chikuchititsa kuti dongosolo latsopano la maphunziro lisayende bwino. Museveni akuti sanapite ku nyumbayi ndipo wati apitako lachinayi likudzali. Aphungu a nyumba ya malamulo mdziko la Uganda akudzudzula unduna wa za maphunziro poyambitsa dongosolo latsopano la maphunziro mdzikomo ngakhale nyumba ya malamulo inalamula kuti dongosololi liyimitsidwe kaye ponena kuti ndi lolowetsa pansi maphunziro. Aphunguwa akuti ndi okudzidwanso kwambiri kaamba ka kusowa kwa mabukhu komanso kusaphunzitsidwa bwino kwa aphunzitsi pa dongosolo latsopanoli.
3
Khama Khwiliro: Katakwe pa nyimbo zauzimu Khama Khwiliro ndi mmodzi mwa oimba nyimbo zauzimu amene ambiri otsata nyimbozi amamudziwa. CHIMWEMWE SEFASI adakumana naye ndipo adacheza motere: Ndikudziwe Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dzina langa ndine Khama Khwiliro, ndidabadwa pa 15 April 1983. Kwathu ndi mmudzi mwa Mtengula, kwa T/A Chikowi ku Zomba. Kodi udakwatira? Maso patsogolo: Khwiliro Khama ali pabanja ndipo adakwatira Jackina Meleka ndipo adadalitsidwa ndi mwana mmodzi, dzina lake Tawina. Kodi zoimbaimba udayamba liti? Ndidayamba kuimba mma 1990. Koma mu 2010 mpamene ndidatulutsa chimbale changa choyamba chomwe mutu wake ndi Nthawi Yanga Yakwana. Kodi uli ndi zimbale zingati? Inetu ndili ndi zimbale ziwiri: Nthawi Yanga Yakwana komanso Ndaona Kuwala. Uthenga wako wagona pati nanga umaimba zamba zanji? Uthenga wagona pa za mawu a Mulungu okamba zoyenera kuchita monga Akhristu makamaka nthawi yotsiriza ino. Nyimbo zikulukidwa mu zamba monga manganje, kwaito ndi zamba zina za kwathu kuno. Pambali poimba umagwiranso ntchito ina? Nanga umakonda chiyani ngati sukuimba? Inetu ndimagwira ntchito ku Blantyre Synod Health and Development Commission komanso ndikakhala kuti ndili ndi mpata, ndimakonda kucheza ndi anthu osiyanasiyana. Kumbali ya zakudya, ndimakonda nsima ya chisoso ndi chambo. Kuimba umafuna utafika nako pati? Ndimafuna kuimba kutafika ngati mmene anzathu akunja amachitira komanso anthu azitha kukwanitsa kusamala mabanja awo kudzera mkuimba ndi kupeka nyimbo.
13
Muyambitsi Wa Radio Maria Pa Dziko Lonse, Wamwalira Yemwe anayambitsa wailesi za Radio Maria pa dziko lonse a Emmanuel Ferrario amwalira ali ndi zaka 90 zakubadwa. A Ferrario amwalira masana wa pa 08 July 2020 mdziko la Italy ndipo pa nthawi ya imfa yawo, anali ali president opuma wa World Family of Radio Maria. Muyambitsi wa Radio Maria pa dziko lonse-Ferrario Dongosolo lokhudza maliro ndi Nsembe ya Misa yotsanzikana ndi malemu President Emmanuele Ferrario lilengezedwabe. Radio Maria Malawi idzawakumbukira malemu President Emmanuele Ferrario ngati tate amene amakonda ndi kufunitsitsa kuti Radio Maria Malawi ikule ndi kufikira madera ambiri a kuno Malawi. President Ferrario pamodzi ndi anthu ena anayambitsa Radio Maria ngati ka wayilesi kakangono ka Parish ya Erba mdziko la Italy mchaka cha 1982. President Ferrario adali munthu mmodzi yemwe amakonda Amayi Maria koposa ndipo chidwi chake chofuna kutsekula wailesiyi chinayamba pomwe anachita malonjezo kwa Amai Maria pa matenda a mkazi wake kuti ngati adzachiritsidwa ku nthenda ya cancer, iye adzagwira ntchito mosalekeza yofalitsa mthenga wabwino wa Amayi Maria. Mkazi wake atachiritsidwa iye adagulitsa imodzi mwa kampani zake, ndalama zake nayendetsera wayilesi imene imafalitsa za Amai Maria a ku Medjugorje imene inakhazikitsidwa mchaka cha 1983. Pambuyo pa imfa ya mkazi wake mchaka cha 1984, President Ferrario anapitiriza kuthandiza komanso kutumikira ku wayilesiyi yomwe idali ya Parish. Pambuyo pake adagulitsa kampani yake ina yopanga zakudya zochokera ku mkaka ndi kuyika chuma chake chonse mu ntchito zokulitsa ka wayilesi kameneka. Mchaka cha 1986 ndi pamene adakhazikika mu ntchito zoyendetsa wayilesi ndipo mchaka chotsatira iye adasankhidwa kukhala President wa wayilesi imeneyi. Mchaka cha 1987 adakumana ndi bambo Livio Fanzaga, wansembe wina yemwenso adali wokonda wayilesi-yi ndipo limodzi adagwirizana mfundo zikulu zikulu ziwiri zoyendetsera wayilesi yi imene idali itayamba kukula. Mfundo yoyamba inali kukana kuchita malonda amtundu wina uliwonse pa wayilesiyi ndipo mfundo yachiwiri inali kukonza dongosolo la mapologalamu omwe tsinde lake lagona pa mapemphero, Katekisimu komanso Misa. Ichi ndiye chidali chiyambi cha mulakuli wa mphamvu wotchedwa Radio Maria umene unakula kuchoka pa wayilesi ya pa Parish kufika pa wayilesi ya yomveka mdziko lonse la Italy. Kudzera mu uneneri wa Amai Maria wailesiyi yakwanitsa kufikira mmaiko 80 pa dziko lonse lapansi ndipo ikuyembezeka kupita patsogolo maka kufikira maiko a ku Middle East ndi ena ambiri. Mzimu wa President Emmanuel Ferrario uwuse mu mtendere wosatha.
14
Mulungu Amasankha Munthu Ndi Cholinga-Papa Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco, wati Mulungu amasankha munthu ndi cholinga. Malinga ndi malipoti a Vatican Radio, Papa walankhula izi lachitatu ku likulu la mpingo ku Vatican. Iye wati Mulungu anasankha Davide kukhala mfumu ngakhale kuti pa nthawiyi Davide anali wachichipere popeza Mulungu anali naye cholinga. Papa Francisco wafotokoza kuti Davide anali mbusa wa ziweto ku tchire koma Mulungu anamusankha kuti asiye kusamalira ziweto ndipo kuti mmalo mwake akhale mbusa wa anthu. Iye wati zimene Mulungu amaona mwa munthu pompatsa udindo ndi zosiyana ndi zomwe anthu angaone ndi maso awo. Iye wati Davide anali ndi zofooka zake ngati munthu komabe Mulungu anamusankha kukhala mfumu. Papa Francisco wati chinthu chochititsa chidwi ndi chakuti ngakhale Davide anali ndi zofooka zake iye anali kukonda kupemphera. Ndipo Chifukwa chokonda kupemphera nthawi iliyonse akachimwa Davide anali kulapa machimo ake kuti Mulungu amukhululukire. Pamenepa iye watsindika za kufunika kwa mapemphero mmoyo wa munthu aliyense. Papa Francisco wati munthu amene amakonda kupemphera amatsogoleredwa mmoyo wake ndi Mulungu.
13
Lamulo la chuma cha pulezidenti liunikidwenso Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mmodzi mwa akatswiri a za malamulo Edge Kanyongolo wati lamulo lomwe likukamba za katundu ndi chuma cha atsogoleri a dziko liunikidwenso ndi cholinga chopatsa mphamvu zochuluka kwa Amalawi akafuna kufufuza atsogoleri omwe akugwiritsa ntchito maudindo awo podzikundikira chuma. Izi zadza pamene dziko la Malawi ladzidzimuka ndi kuchuluka kwa chuma cha mtsogoleri wakale wa dziko lino malemu Bingu wa Mutharika ngakhale kuti adakhala pampandowu kwa kanthawi kochepa. Kwa zaka 8 zokha zimene Mutharika adakhala pulezidenti wa dziko lino, chuma chake chidawonjezekera modabwitsa kuchoka pa K150 miliyoni panthawi imene asankidwa kukhaka pulezidenti kufika pa K61 biliyoni mmene ankamwalira, zomwe Amalawi ambiri akuti zachulukitsa poyerekeza malipiro amene mtsogoleri wa dziko amalandira pamwezi. Malamulo a dziko lino amafotokoza kuti Pulezidenti ndi wachiwiri wake sakuyenera kudulidwa msonkho pamalipiro awo apamwezi. Kuphatikiza apo, ndi misonkho ya anthu osauka, atsogoleriwa amakhala ndi bajeti yogulira chakudya komanso ziwiya za mnyumba zawo. Pakatha zaka zisanu zilizonse, atsogoleriwa alinso ndi ufulu woitanitsa kuchokera kunja galimoto imodzi ya kumtima kwawo popanda kupereka msonkho wotchedwa Duty ku bungwe lotolera msonkho la Malawi Revenue Authotiry (MRA). Kwa nthawi yaitali, atsogoleri ena akhala akugwiritsa ntchito mphamvu ndi ufulu umene lamulo limawapatsa poitanitsa katundu wochitira bizinesi zosiyanasiyana koma osapereka msonkho ku MRA, zomwe zikutsutsana ndi malamulo a dziko lino. Pofuna kuthana ndi mchitidwewu, boma lidakhazikitsa bungwe lapadera la Special Law Commission (SLC) mchaka cha 2006 ndi cholinga choti liunikenso bwino gawo 88 la malamulo a dziko lino. Ntchito yake yaikulu inali kukonza lamulo lokakamiza Pulezidenti, nduna komanso akuluakulu ena ogwira ntchito mboma kunena poyera mmene chuma chawo chilili asanalumbiritsidwe pamaudindo osiyanasiyana. Kafukufuku wa bungweli adasonyeza kuti kupatula lamulo lokakamiza atsogoleri kubwera poyera pakatundu yemwe ali nawo, maiko monga Uganda, Kenya ndi Tanzania adaikanso ndondomeko ndi mfundo zowonjezera zothandiza munthu akafuna kudziwa kapena kutsatira momwe chuma cha atsogoleri awo chikuchulukira kudzera mumaudindo awo ngati pulezidenti, nduna kapena phungu wa Nyumba ya Malamulo. Mwa mfundo zina, bungweli lidavomereza kuti munthu wogwira ntchito mboma sakuyenera kugwiritsa ntchito udindo wake podzikundikira yekha chuma kapena anzake; asagwirenso ntchito zina kupatula yomwe adalembedwa ndi boma; apewe kugwira ntchito zomwe sizikugwirizana ndi udindo wake komanso asagwiritse ntchito udindo wake kapena katundu wa boma molakwika. Ngakhale izi zili choncho, zikuwoneka ngati Amalawi alibe mphamvu komanso lamulo lomwe lingawaikire kumbuyo akafuna kulondoloza chuma cha atsogoleri awo. Izi zikupereka mwayi kwa atsogoleriwa kugwiritsa ntchito maudindo awo momwe angafunire popanda wina kuwafunsa. Kanyongolo adati izi zikusonyeza kufooka kwa malamulo a dziko lino nchifukwa chake atsogoleri akutengerapo mwayi. Iye adati lamulo lokhudza katundu ndi chuma cha Pulezidenti, wachiwiri wake ndi nduna za boma ndi lokwanira, koma likusowekera nsanamira zake zimene anthu wamba angagwiritse ntchito polondoloza chumacho. Mkuluyu adafotokoza kuti poonjezera lamulo limene lilipo kale, Nyumba ya Malamulo iganizirenso zokhazikitsa lamulo lina lokakamiza atsogoleri kubweranso poyera ndi chuma chimene apeza pamene akuchoka mmaudindo awo. Kanyongolo akuti akadakonda mabungwe a Financial Intelligence Unit (FIU) ndi Malawi Revenue Authority (MRA) atapatsidwa mphamvu zounika mmene chuma cha atsogoleri chilili pamiyezi inayi iliyonse kapena pakutha pa chaka kuti Amalawi azidziwa ngati atsogoleriwa sakugwiritsa ntchito maudindo awo molakwika. Ndikunena izi chifukwa chipanda nkhani ya msonkho womwe mtsogoleri wakaleyu sanapereke ku MRA, dziko lino silikadadziwa kuti a Mutharika anali wolemera chonchi, Kanyongolo adatero. Katswiri wina pa zamalamulo, Justin Dzonzi, wati gawo 88 la malamulo a dziko ndi lopanda ntchito chifukwa silikupatsa mphamvu ndi chitetezo kwa nzika imene ikufuna kulondoloza momwe chuma cha atsogoleri chilili. Dzonzi adati ku Uganda nzika zili ndi mphamvu zofufuza atsogoleri awo mmene akugwiritsira ntchito udindo wawo komanso chuma cha boma. Koma mkulu wa bungwe la owerengera ndalama la Society of Accountants in Malawi (Socam) Evelyn Mwapasa akuti Amalawi atha kulondoloza katundu wa atsogoleri awo kudzera mmakalata ndi mapepala okhudzana ndi misonkho kuchokera ku MRA. Koma Mwapasa adatsindika kuti vuto lalikulu mdziko muno ndi kasungidwe ka mafayilo okhudzana ndi misonkho. Mmaiko ena, munthu sungapikisane nawo pampando wa pulezidenti kapena phungu wa ku Nyumba ya Malamulo pokhapokha utatulutsa umboni wosonyeza kuti umalipira msonkho, Mwapasa adatero. Iye adati pofuna kuthetsa katangale, bungwe lotolera msonkho liyenera kulimbikitsa ntchito yosunga mafayilo a misonkho. Ndipo akaona kuti atsogoleri athu akulemera modabwitsa, MRA ikuyenera kufufuza ndi cholinga choti wina asamadyere masuku pamutu Amalawi osauka, Mwapasa adatsindika. Mkulu wa Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito wapempha Amalawi kuti asataye nthawi kulimbana ndi chuma chimene Mutharika adazikundikira. Mmalo mwake, Kapito adati anthu akuyenera kukhala tcheru ndi boma la Peoples Party (PP) womwe akuti uli ndi kuthekera kowononga chuma chambiri ngati sipangapezeke njira zolitchingira. Si zodabwitsa kuti malemu Mutharika adapeza chuma chochuluka motere. Ifeyo ndi amene takhala tikumenya nkhondo yokakamiza atsogoleri kuti aulule chuma chawo, koma mmalo motithandiza pankhondoyi, tikutanganidwa ndi zinthu zina zopanda pake, iye adatero.
11
Osamalira Odwala Akhale Achifundo-Papa Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati anthu omwe amasamalira odwala akuyenera kukhala achifundo. Iye walankhula izi mu uthenga wake wapa tsiku lomwe mpingo wa katolika pa dziko lonse umakumbukira odwala, lomwe ndi 11 February. Mu uthengawo, omwe mutu wake ndi Bwerani Inu Nonse Olema, Papa wati anthu osamalira odwala akuyenera kutengera chitsanzo cha Yesu Khristu pokhala achifundo. Papa wati Yesu Khristu akupereka uthenga wa chilimbikitsowu popeza kuti naye anadutsa mu mazunzo aakulu. Iye wati ngakhale sizikhala chomwechi mzipatala zambiri pa dziko lonse, komabe odwala akuyenera kulandira chisamaliro chokwanira. Mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu wati mpingo ukuyenera kukhala msamaria wina wachifundo popereka chisamaliro kwa anthu odwala ndi ovutika mnjira zosiyanasiyana. Mpingo wa katolika umachita chaka chokumbukuira odwala onse pa 11 February tsiku lomwenso mpingowu umakumbukira amayi Maria aku Lourdes.
14
Gondwe azaza pamsonkhano Nduna ya za chuma Goodal Gondwe Lolemba idazaza pamwambo wosayinirana pangano la ngongole ndi banki ya zachitukuko mu Africa ya African Development Bank (AfDB) itazindikira kuti akuluakulu a kuundunawu sadabweretse mapepala osayinira panganolo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndunayi imayembekezera kusayinira pangano la ndalama zokwana US$22 miliyoni (pafupifupi K16 biliyoni) mmalo mwa boma ndi oyimilira bankiyi Andrew Mwaba ku likulu la undunawu ku Lilongwe. Adakwiya: Gondwe Cholinga cha ndalamazi nkupititsira ntchito za ulimi patsogolo ndi kutukulira achinyamata paulimi. Gondwe adakhumudwa ndi kulephera kwa akuluakulu a kuundunawu kuzindikira kuti mwambowo udayamba palibe mapepala ofunikirawo ndipo adadula mkamwa oyendetsa mwambowo Alfred Kutengule kuti za mapepalawo zilongosoke. Zitheka bwanji kusayinirana pangano popanda mapepala ofunikira? Tisayina pati? Mapepala ali kuti apa? Adafusa Gondwe. Ndunayi itangolankhula izi, kudali yakaliyakali akuluakuliwo kuthamangathamanga mmawofesi kusaka mapepalawo kuti mwambo upitilire ndipo pomwe mapepalawo amapezeka, makina achinkuza mawu omwe amagwiritsidwa ntchito pa mwambowo adasiya kutulutsa mawu.
11
Ndidakamira kufunda nawo ambulera Padali pa 5 February 2014, kunja kuli mvula yamphamvu ya mabingu pomwe Devlin Nazombe kapena kuti Mmisiri Wopanda Zida yemwe amagwira ntchito ngati muulutsi kunyumba youlutsa mawu ya Angaliba komanso amaongolera zochitika monga zikwati ndi zina adakumana ndi mkazi wake Gloria Muhiwa. Ndipo Nazombe yemwe tsiku lina adaona koyamba Gloria atafunda ambulera kuphelera mvulayo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Devlin ndi Gloria pa tsiku la ukwati wawo Apatu Nazombe sakadachitira mwina koma kumuimitsa namwaliyo nkumupempha kuti afunde nawo. Ndidamuimitsa kuti ndifunde nawo chifukwa ndidali ndikunyowa kwabasi. Nditamuimitsa adanyogodola koma sindidaimve, ndidakakamira kufikira pomwe adandiloleza kufunda nawo, adalongosola Nazombe. Komatu Nazombe sadapitire kufunda nawo ambulera kokha chifukwa adayamba kumupempha Gloria nambala yake ya lamya. Gloria adakanitsitsa kuti sangandipatse nambalayo. Koma ndidamukakamiza kuti chabwino angotenga nambala yanga ndipo adailemba mmanja kuti akakafika kwawo akaisunge, Nazombe adatero. Iye adawonjezera kuti atafika posiyana adamuchondelera namwaliyo kuti ayankhulane naye madzulo atsikulo chifukwa adali ndi chikaiko chachikulu. Koma Nazombe adati padadutsa sabata ziwiri asadamuyankhule ndipo adaiwalanso zoti adapereka nambala. Tsiku lina ndidaona uthenga woti ndiimbire munthu lamya ndipo nditamufunsa kuti ndi ndani adati Gloria, ndidabalalika kwambiri mpaka kufunsa kuti wakuti? Ndiye adandilongosolera kuti ndidamupatsa nambala yanga. Koma nditakumbukira, tidayamba kucheza, iye adatero. Patadutsa kanthawi awiriwo akucheza, Nazombe adamufunsira mkaziyo yemwe akuti adavuta kwambiri kuti amulole, komabe pamapeto pa zonse adavomera ndithu. Kuchokera nthawi imeneyo takhala tikukumana ndi zokhoma zochuluka monga chibwenzi kutha nkudzayambiranso; anzake amamuuza kuti sindingamukwatire chifukwa ndine wotchuka ndipo anthu otchuka sakhala ndi mkazi mmodzi koma chosangalatsa nchoti Gloria samazitengera zonsezo, Nazombe adalongosola. Koma awiriwo omwe amanga ukwati wawo pa August 31 pa mpingo wa South Lunzu CCAP ndipo madyelero adali ku Grace Garden ku Machinjiri, mumzinda wa Blantyre akulangiza anthu onse omwe ali mchikondi kuti asamamvere zokamba za anthu komanso chikondi chao chizikhala chotsogoza Mulungu kut mzonse azikula. Iwo adati akakumana ndi vuto lililonse amakhala pansi ndikukambilana modekha kuti wolakwa avomereze ndikupepesa ndipo zikatha amagwada pansi ndikumupempha Mulungu kuti awayanjanitse. Awiriwa amakhala ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre ndipo Gloria amagwira ntchito ku sitolo za PEP komanso ali ndi salon komwe amamanga anthu tsitsi.
10
Anatchereza Ndikufuna kuchoka Zikomo Anatchereza, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndidabwera kutauni kudzafuna ntchito ndipo ndidasiya mkazi wanga kumudzi. Ntchito ndidaipeza koma abale amene ndimakhala mnyumba yawo akuti ndisachoke kukafuna nyumba ya lendi ati sakufuna mkazi wangayo abwere. Kodi nditani kuti ndituluke mnyumba yawoyo? Thandizeni. Ine F. Zikomo a F, ndinu mwamuna kotero pena sibwino kumvera zilizonse. Apapa zikuonetseratu kuti abale anuwo samufuna mkaziyo. Ngati mkaziyo ali ndi vuto ndibwino anene kuti vutolo mulikonze, koma kumuletsa si yankho. Achibale ena amafuna kulowerera chilichonse chokhudza moyo wa munthu, pena ndibwino kuti munthu azikhala ndi ufulu wosankha chomwe akufuna komanso kuchita. Musalolere, ngati pali vuto kambiranani. Gogo, Ndili ndi mwana wa kunjira ndipo ndidakwatira mkazi wa mwana kale. Koma iyeyo adabweretsa mwanayo ine ndidasakudziwa ndipo chichitire izi, sakundilabadiranso. Nditani? Zikomo pa funso lanu lomveka. Choyamba ndifunse, kodi mayiwo adakuuzani kuti ali ndi mwana kunjira? Ngati sadakuuzeni ndiye kuti pali nkhani ziwiri, yoyamba imeneyo yachiwiri yoti abweretsa mwana mwa dzidzidzi. Bambo dziwani ichi kuti kholo lomwe aliyense amapanga zofuna zake silamoyo, kotero musalole kuti mpaka kude mutayambana ndi mkazi wanu. Mukhazikeni pansi ndipo akumasuleni nkhani yeniyeni. Ngati sakulankhula, kauzeni ankhoswe. Anatchereza, Ndili ndi zaka 28 ndipo ndili pabanja. Koma nthawi zonse ndikati ndikhale mchikondi ndi mkazi wanga, amanena kuti watopa. Ndingatani. M, Lilongwe. Zikomo bambo M, Tikati banja timanena kuchipinda, ngati wina akukana kulowa kuchipinda ndiye kuti akukaniza banja. Mumufunse kuti kuchipindako akumalowako ndi ndani? Zikuonetseratu kuti pali tambala wina amene asangalala mwa mayiyo. Kodi zavuta? Auzeni ankhoswe ndipo amasule bwalo pamene pali vuto. n Ndikufuna mwamuna Ndine mayi wa zaka 52, ndimakhala ku Dedza. Mwamuna wanga adamwalira mu 2003. Ndikufuna mwamuna amene angandikwatire koma akhale wopemphera. Chonde imbani 0992256715.
12
Ogwira Ntchito ku Ndende Ayamba Kunyanyala Ntchito Asilikali ogwira ntchito mmaudindo angonoangono mu ndende za mdziko muno ayamba kunyanyala ntchito pofuna kukakamiza boma kuti limve madandaulo awo. Malinga ndi mtolankhani wathu, kummawaku kunali mpungwepungwe ku Zomba Central Prison pakati pa asilikali a maudindo angonoangono ndi mabwana awo pomwe akuluakuluwo analawira kuyamba kugwira ntchito asilikali a maudindo otsika asanafike. Pamenepa asilikaliwa anathamangitsa mabwana awowa ndipo anatseka chipata cholowera ku ndendeyi moti padakalipano anenetsa kuti adzayamba kugwira ntchito madandaulo awo akamveka ndi kuyankhidwa bwino. Padakalipano apolisi omwe amatenga anthu oganiziridwa ku bwalo la milandu alephera kukatenga akayidi omwe amakhala akuyembekezera kupita ku khothi chifukwa chipata cha ndendeyi chinali chotseka. Malinga ndi malipoti, anthuwa akufuna ogwira ntchito a pansi kwambiri awakweze pa ntchito, awapatse ndalama zowonjezera chifukwa miyoyo yawo ili pa chiwopsezo ndi kubwera kwa mliri wa Coronavirus. Iwo akuti akufunanso kuti akuluakulu a ndende asiye kuchita tsankho, ponena kuti pali asilikali a ku ndende ambiri omwe akupindula chifukwa akuchokera mbali yomwe akuchokera akulu-akulu a nthambi-yi. Padakalipano wofalitsa nkhani za nthambi ya ndende mdziko muno Chimwemwe Shawa wati kunyanyala ntchito komwe akuchita asilikali otsika mmaudindowa ndi kosavomerezeka chifukwa sanatsate ndondomeko yake.
14
Alimbana ndi ntchemberezandonda ku Zomba Unduna wa zamalimidwe wati ntchemberezandonda zomwe zabuka mboma la Zomba zisatayitse anthu mtima chifukwa akatswiri apita kale mmadera omwe akhudzidwa ndi mbozizo. Mbozizo zapezeka kale mmadera ena mboma la Zomba mkulu wa zaulimi kumeneko Patterson Kandoje watsimikiza koma mneneri wa unduna wazamalimidwe Hamilton Chimala adati gulu la akatswiriwo likafikanso mmadera achigwa cha Shire. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Padakalipano nduna ndi gulu la akatswiri ali kale kalikiliki kulimbana ndi mbozizo ndipo iwo ndi amene angakhale ndi zonena zambiri pammene zinthu zilili, adatero Chimala. Ntchemberezandonda zimaononga masamba ofunika pokonza chakudya cha mbewu Nduna ya zamalimidwe Dr Allan Chiyembekeza adatsimikiza kuti iye pamodzi ndi akatswiri ali kalikiliki kulimbana ndi vutoli koma adati padakalipano sanganene kuti vutolo ndi lalikulu motani popeza akadali mkati mofufuza. Anthu angokhala ndi chikhulupiliro chifukwa akatswiri omwe akugwira ntchitoyo ndiwodziwa kwambiri moti ali ndi chikhulupiliro kuti vutoli silipita patali lisadagonjetsedwe, adatero Chiyembekeza. Ndunayo idati chongodandaulitsa chakuti mbozizo zimaononga kwambiri panthawi yochepa komanso vuto lake ndilakuti zimadya masamba omwe mbewu zimadalira popanga chakudya motero kakulidwe ka mbewu kamasokonekera. Ntizilombo tachabe kwambiri chifukwa timaononga masamba a mbewu choncho kuchedwa kutigonjetsa kukhoza kukhala ndi zotsatira zowawa kwambiri, adatero Chiyembekeza. Kandoje adati pamalo okwana mahekitala 34 omwe akhudzidwa, mahekitala 6 ndiwo adali atapoperedwa pofika Lachiwiri ndipo adapempha anthu kuti akhale tcheru kuti akangoona mbozi zobiriwira zokhala ndi mizere yoyera akauze a zaulimi chifukwa maonekedwe a ntchemberezandonda ndi wotero. Chiyembekeza: Tikuthana nazo Madera ozungulira malo a zaulimi a Mpokwa kwa T/A Mwambo makamaka midzi ya Saiti, Masambuka, Kwaitana, Mamphanda, Kabwere, Kumpatsa, Havala, Mlomwa ndi Chaima ndi ena mwa midzi yomwe yakhudzidwa. Ntchemberezandondazi zabuka panthawi yomwe alimi akudandaula kale ndi ngamba yomwe ikutha pafupifupi sabata zitatu tsopano ndipo mbewu zambiri zanyala kale mminda moti pali chiyembekezo choti ngambayi itati yapitirira ndiye kuti alimi akhoza kudzabzalanso. Ngambayo yadza kaamba ka mphepo ya El Nino yomwe yasokoneza magwedwe a mvula makamaka mmaiko a kummwera kwa Africa zomwe zapangitsa madera a mchigawo cha kummwera kwa Malawi akhudzidwe kwambiri.
4
Njengunje pothana ndi matenda a khansa Muli ntchito yaikulu mdziko muno kuti odwala matenda a khansa apeze mpumulo. Izi wanena ndi yemwe adapulumuka ku matendawa, Blandina Khondowe. Khondowe adaononga K5 miliyoni kuti apulumuke ndipo adachita kupita mdziko la India zitakanika kuti athandizidwe mdziko muno. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mpaka zafikatu pamenepa, amayi kufola pa mzere kuti ayezetse khansa Malinga ndi mkulu woyanganira ntchito za umoyo mu unduna wa zaumoyo Charles Mwansambo, zipatala za Kamuzu Central ndi Queen Elizabeth ndi zokhazo zomwe zili ndi ukadaulo wa matendawa. Kutanthauza kuti kupatula malowa, kulibenso kwina komwe wodwala angapite mdziko muno. Boma lidakhazikitsa ntchito yomanga malo wothandizita anthu odwala khansa mu 2007 koma mpaka pano malowa sadayambe kugwira ntchito. Kwa Khondowe, ili ndi vuto lalikulu lomwe likuika pachiopsezo odwala matendawa. Kupatula kuti tili ndi zipatala zochepa, vuto lina ndi la zipangizo, adafotokoza, ineyo ndidazindikira kuti bere langa limalimba mchaka cha 2011 ndipo kwa zaka ziwiri ndimayenda mzipatala koma amangondiuza kuti ndi chotupa, mpaka pamene ndidaganiza zopita ku India. Khondowe adaonjeza, nditapita ku India, ndidaononga K5 miliyoni. Ndi angati angakwanitse ndalama zoterezi? Pokhapokha titapereka mphamvu zambiri ku zipatala zathu, anthu apitirirabe kufa ndi khansa. Mmodzi mwa akadaulo pa matendawa, Leo Masamba adati pakali pano, chaka ndi chaka, anthu pafupifupi 18 000 amapezeka ndi khansa. Iye adati mwa anthuwa, amene ali pamoto ndi anthu akumudzi omwe chuma ndi chowavuta. Kuperewera kwa zipatala kukuzuza kwambiri anthu akumudzi chifukwa alibe ndalama kuti akapeze thandizo, adatero Masamba. Iye adati chofunika ndi kumema Amalawi kuti athandize boma kukwaniritsa pologalamu yokhazikitsa malo othandizirako anthu a vuto la khansa mzigawo zonse za dziko lino. Malinga ndi iye, mankhwala oyenera, zipangizo zogwirira ntchito, ogwira ntchito odziwa bwino ndi galimoto zokwanira zonyamula anthu osowa mayendedwe ndi zinthu zomwe zikufunikira. Akatswiri pa za umoyo ati pokhapokha patachitika chozizwa, Amalawi apitilira kupululuka ndi matendawa chifukwa cha kusowekera kwa zipangizo komanso zipatala. Mkulu woyanganira nthambi yothandiza ku matenda a khansa pa chipatala cha Kamuzu Central, Richard Nyasosela wati chipatalachi chimalandira anthu osachepera 30 sabata iliyonse. Steady Chasimpha wa ku nthambi yowona za matenda a khansa wati ku Queen Elizabeth Central Hospital, anthu ofuna thandizo sachepera 22 pa sabata imodzi. Iye wati nambala zochuluka chotere nzowopsa poyerekeza kuchepa kwa ogwira ntchito ku nthambi za khansa ndi zipangizo zothandizira anthu ovutikawo. Nambala imeneyi ikusonyeza kuti zinthu sizili bwino, ndipo tikatengera vuto la ogwira ntchito ndi zipangizo, thandizo loperekedwa silingakhale loyenera, adatero Chasimpha. Kusowekera kwa zipatala kwachititsa kuti anthu ena mmidzi azipita kwa asinganga kukalandira thandizo. Mtsogoleri wa asinganga mdziko muno, Frank Manyowa akuti patsiku amalandira anthu pafupifupi asanu atatu odwala khansa. Ambiri mwa anthuwa sapulumuka chifukwa asingana ena amangofuna adyepo ngakhale sangakwanitse, adatero. Anthu pafupifupi 52 ndiwo amapezeka ndi matenda a khansa pa sabata mdziko muno, pakutha pa mwezi, anthu pafupifupi 204 ndiwo amapezeka ndi matendawa. Koma Khondowe akuti kutengera zomwe madotolo adamuuza ku India, khansa ndiyochizika ikapezeka mmasiku oyambilira komanso thandizo loyenera likakhala pafupi. Apo ayi ndiye amakangodula chiwalo mukachedwa kulandira thandizo. Lero Khondowe adayambitsa bungwe la Think Pink lomwe limapita mmadera osiyanasiyana kuphunzitsa anthu za khansa ndi kuwalimbikitsa kuti azikayezetsa.
6
Chifunga pa za boma la fedulo Nkhungu yowirira yakuta tsogolo la boma la fedulo (Federalism) lomwe magulu ena mdziko muno akufuna pamene ena sakugwirizana ndi maganizo otero. Maganizo a boma la fedulo adabwera chifukwa choti anthu ena akuganiza kuti pali tsankho pa kagawidwe ka maudindo ndi chitukuko mdziko lino. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Jessie Kabwila Mbusa Peter Mulomole, yemwe ndi mneneri wa bungwe la anthu a chipembezo la Public Affairs Committee (PAC) lomwe lidasankhidwa ndi boma kuti limve maganizo a wanthu pa za boma la fedulo, wati anthu akusiyanabe maganizo pankhaniyi chomwe chikusonyeza kuti ambiri sakudziwabe tanthauzo la boma la fedulo. Iye adati ichi ndi chipsinjo ku bungwe la PAC. Takhala tikugwira ntchito yofufuza maganizo a anthu pa nkhaniyi kuyambira mwezi wa November chaka chatha koma mpaka pano tsogolo lenileni silikuwoneka chifukwa tikulandira maganizo osiyanasiyana, adatero Mulomole. Iwo adati akumanapo ndi magulu osiyanasiyana mchigawo cha pakati komwe adamva maganizo osiyanasiyana ndipo padakali pano ali mchigawo cha kumpoto komwenso magulu osiyanasiyana akupereka maganizo awo. Tikukumana ndi mafumu, a mipingo, mabungwe, andale, amabizinesi, ogwira ntchito mboma ndi mmakampani komanso akatswiri mmagawo osiyanasiyana monga zandale, zachuma ndi zamalamulo. Anthu amenewa akutiwuza maganizo awo mosaopa, adatero Mbusa Mulomole. Mneneriyu adati anthu asayembekezere zotsatira msanga chifukwa nkhaniyi ndiyokhudza dziko lonse choncho nkofunika kuti bungweli litolere maganizo a anthu mofatsa nkupeza chenicheni chomwe akufuna. Mulomole wakana mphekesera zoti boma ndilo likupereka ndalama zopangitsira misonkhanoyi. Iwo adati ngati mbali imodzi yokhudzidwa pa nkhaniyi, boma likadapereka ndalama kubungwe la Pac zoti ligwirire ntchitoyi, zotsatira zake sizikadapereka tanthauzo. Ife ngati bungwe loyima palokha, sitikutenga mbali ili yonse pa nkhaniyi. Ntchito yathu ndiyongofufuza zomwe anthu akufuna; choncho sitikuyenera kulandira ndalama zogwirira ntchitoyi kuchoka ku mbali ili yonse yokhudzidwa, adatero a Mulomole. Iwo adapitiriza kunena kuti bungwe lawo pamodzi ndi bungwe la chi Katolika lowona za chilungamo la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) akugwira ntchitoyi ndi thandizo lochokera ku bungwe la United Nations Development Programme (UNDP). Nkhani ya fedulo idadzetsa mtsutso waukulu kuyambira miyezi ya August ndi September chaka chatha pamene mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika adasankha nduna zake zomwe zambiri zidachokera mchigawo cha kummwera. Zipani zotsutsa boma ndi magulu ena, makamaka a mchigawo cha kumpoto ndi pakati, adati kuli bwino dzikoli litagawidwa kutengera zigawo ndi cholinga choti chigawo chiri chonse chidzidzipangira chokha ndondomeko za chitukuko. Phungu wa dera la Hora mboma la Mzimba a Christopher Ngwira komanso wa dera la kuvuma mbomalo a Harry Mkandawire, omwe ndi a chipani cha Peoples Party (PP), ndi ena mwa anthu omwe adayambitsa komanso kulimbikitsa maganizo a boma la fedulo. Chipani cha Malawi Congress Party (MCP) nachonso chidagwirizana ndi maganizo oyambitsa boma la fedulo. Mneneri wa chipanichi a Jessie Kabwila adati boma la fedulo lidzapangitsa kuti madera onse a dziko liko atukuke. Kafukufuku yemwe Tamvani adapanga adasonyeza kuti aphungu ambiri aku nyumba ya malamulo sakugwirizana ndi maganizo oterowo kamba koti atha kugawa dziko. Koma boma lidati anthu apatsidwe mwayi wonena zakukhosi kwawo ngati akufuna boma la fedulo kapena ayi. Boma silikufuna kupondereza maganizo a wanthu pa nkhani ya boma la fedulo. Aliyense ali ndi ufulu opereka maganizo ake koma izi zichitike poganizira udindo omwe munthu aliyense ali nawo, adatero a Kondwani Nankhumwa, omwe ndi mneneri wa boma. Pogwirizana ndi a Mulomole, a Nankhumwa adati boma sililowelera pa ntchito yomwe bungwe la PAC likuchita yophunzitsa anthu kapena kufufuza maganizo awo pa za boma la fedulo. A Nankhumwa adatinso boma silidaperekeo ntchitoyi mmanja mwa bungwe kapena nthambi ili yonse koma lidangotsegula chitseko kwa mabungwe ndi ena omwe angakwanitse kuphunzitsa anthu kuti adziwe ubwino ndi kuyipa kwa boma la fedulo. Bomatu silidakane kapena kuvomereza boma la fedulo, koma kuti anthu apereke maganizo awo komanso aphunzitsidwe mokwanira. Ichi ndi chifukwa tidalekera mabungwe omwe angakwanitse kuti agwire ntchitoyi ndi ndalama zawo, adatero Nankhumwa. Koma a Ngwira adati akukaika kuti boma lili ndi chidwi pa nkhani imeneyi. Tawonapo nkhani zikuluzikulu zikufera mmazira ngakhale komiti yoona nkhanizi itakhazikitsidwa. Kukadakhala kuti boma liri ndi chidwi, likadapereka chithandizo choti anthu omwe akugwira ntchitoyi agwiritse, adatero a Ngwira. Polankhula ndi Tamvani, katswiri wa zandale ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College a Blessings Chinsinga adachenjeza kuti nkhani ya boma la fedulo siyofunika kupupuluma. A Chinsinga adati nkhaniyi ndiyofunika iyende mundondomeko zingapo isadafike pokhazikitsidwa choncho mpofunika kuunika bwino kuti zinthu zidzayenda motani bomalo likadzavomerezedwa. Choyamba, anthu akufunika kuphunzitsidwa za tanthauzo la boma la fedulo ndi cholinga choti apereke maganizo awo pachinthu chomwe akuchidziwa bwino. Zikatero, ngati anthu avomereza, pakuyenera kukhala voti ya liferendamu. Pofika popangitsa chisankho cha liferendamu, palinso zofunika kuchita zingapo monga kuunika mmene chuma chizigawidwira, komanso mmene malamulo aziyendera monga kukhala ndi malamulo amodzi dziko lonse kapena chigawo chiri chonse chikhale ndi malamulo ake zomwe sizapafupi, adatero Chinsinga.
11
Tadeyo Mliyenda: Ulendo wa ku Mzuzu Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tsikulo Abiti Patuma adandipeza pa Wenela kuti ndimuperekeze ku Mzuzu kumene amakacheza ndi Paparazzi komanso anzake. Tidakwera basi yausiku pa Wenela monga mudziwa kuchoka pa Wenela kukafika ku Mzuzu ndi mtunda wautali zedi. Mudali kuphulika nyimbo za mnyamata uja woukira, Jaso, inde mnyamata amene aliyense akudziwa bwino kuti amacheza kwambiri ndi Mpando Wamkulu koma lero akuti sakufuna kumvana Chichewa ndi mdzukulu wake wa Mpando Wamkulu, inde Atipatsa Likhweru. Chilipo chikuchitika kuti lero lino Jaso azioneka kuti akuukira Atipatsa Likhweru ndi anzake ena onse ku Ukafuna Dilu Fatsa. Ulendo uli mkati, Abiti Patuma adayamba kukamba zodziwa yekha. Palibe icho ndimatola pankhani zimene iye amakamba. Komatu zinaliko uku ku Kanjedza. Paja mudziwa Lazalo Chatsika uja wa Male Chauvinist Pigs masiku apitawa anamuuziratu Moya Pete kuti zomwe ananena zimakhala ngati zonena mlezi. Ndiye anyamata a Dizilo Petulo Palibe anamutengetsa ku Kanjedza, kufuna kumumenya, adali kutero Abiti Patuma. Palibe icho ndidatolapo. Koma ndiye kunali kukwenyana anyamata, kutsala pangono kutulutsirana nkhwangwa, adapitiriza. Abale anzanga, zovuta kumvetsa izi. Tidayenda ulendowo bwino lomwe ndipo pa Jenda tidafika cha mma 2 koloko usiku. Chilankhulo chidayamba kusintha. Mpando wathu tidakhala anthu atatu. Kuwindo kudali Abiti Patuma, ine pakati ndipo mbali inayi kudali mkulu wina amene ankaoneka kuti wangofika kumene kuchokera ku Joni. Mkuluyo adandifunsa: Kasi mukuluta nkhu? Ndidamvapo nthawi ina kuti apa akutanthauza kuti mukupita kuti? Ine kuyowoya Chitumbuka nikuyowoya koma kweni kuti nipulike, nikutondeka chomene, ndidayankha. Ambiri mubasiyo adali mtulo. Kamphepo kadali katawakokera kutulo. Mwadzidzidzi, tidamva wina akukuwa: Choka! Choka! Iwe choka! Mayooooo! Aliyense mubasimo adadabwa kuti chikuchitika nchiyani. Ngakhale amene amagona adadzidzimuka. Mkulu uja adadzidzimukanso kutulo kwakeko ndipo tonse tidaseka chikhakhali. Atafunsidwa kuti amalota chiyani, iye adangoti: Ndimalota anthu a mapazi ngati nkhwangwa komanso malilime ngati mipeni, adayankha mkulu uja.
15
ANatchereza Sakufuna kukaonekera Gogo Natchereza, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Mnyamata wina adandifunsira chibwenzi ndi cholinga choti tidzakwatirane. Padakali pano padutsa zaka zinayi tili paubwenzi, koma palibe chomwe amandiuza chokhudza ukwati. Mnzangayu amangofuna tizigonana basi. Gogo ndithandizeni. Kodi ndimutaye mnyamatayu? TTK TTK, Mutaye! Mnyamatayu zomwe akufuna nzongogonana basi osati za banja. Anyamata ambiri amabwatika atsikana powauza kuti adzawakwatira koma akudziwa kuti zaukwati ali nazo kutali. Chakumtima kwawo chikaphwa, atsikana aja samawawerengeranso. Nawo atsikana vuto lawo lalikulu nkutengeka poganiza kuti akakana kugona nawo awasiya nkukapeza ena. Apatu ine ndikuona kuti mnyamatayu ndi kamberembere. Mutaye asakutaitse nthawi yako pachabe. Gogo Natchereza Bwenzi langa chimasomaso Gogo Natchereza, Ndidakumana ndi mtsikana wina mu mzinda wa Mzuzu zaka zitatu zapitazo, tidapatsana nambala za foni ndipo takhala tikuimbirana mpaka ubwenzi udayamba. Mtsikanayu amagwira ntchito pa ku banki ina mu mzindawo moti ali ndi mnyumba yakeyake yomwe amakhala. Gogo, mnzangayu ndamupezapo katatu konse ali pa chikondi ndi amuna osiyanasiyana, koma wakhala akundipempha kuti ndimukhululukire ndipo ine ndimakhululukadi. Gogo, mtima wanga ndiwosweka chifukwa mnzangayu ndimamukonda kwambiri moti maganizo, moyo ndi mphamvu zanga zonse zidali pa iye. Nditani, gogo? Chonde ndithandizeni! HKA HKA Mtsikanayu ndi njinga simungapitirire kukhala naye paubwenzi. Mutha kutero mwakufuna kwanu, koma mudzanongoneza bondo mtsogolo muno chifukwa khalidwe la chimasomaso sindikuona akusiya. Ngati akuchita ukathyali muli paubwenzi, zidzatha bwanji mukadzamukwatira? Ndikudziwa kuti nzopweteka kusiyana ndi wokondedwa wanu, koma limbani mtima.
12
Zipani za MCP, UTM Zadzudzula Boma Kamba Kotayilira pa Nkhani ya Coronavirus Mgwirizano wa zipani za UTM ndi MCP wadzudzula boma kaamba kolephera kukwaniritsa ndondomeko zoyenera zomwe zikuyenera kuchitika kusanachitike mbindikiro ofuna kuchepetsa kufala kwa nthenda ya COVID-19 mdziko muno. Chikalatachi chati masiku asanu ndi awiri omwe bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) komanso anthu ena anatenga chiletso choyimitsa ganizoli, unali mpata oti boma likonze ndondomeko zoyenera pokonzekera mbindikirowu. Boma lalephera kuika njira zina zomwe zingapangitse kuti nthendayi isafale kwambiri mdziko muno komanso kulephera kukhazikisa komiti yoti iwunike bwino za nthendayi, chatelo chikalatacho. Padakalipano Judge Kenyatta Nyirenda yemwe amamva nkhani yokhudza chiletsochi wati azapereka chigamulo chake pa nkhaniyi lachitatu likudzali.
11
Mdipiti wa Galimoto za Chilima Wachita Ngozi; Anayi Afa Anthu anayi afa ndipo awiri avulala pa ngozi yomwe yachitika kwa phalula mboma la Balaka. Malinga ndi mneneri wa apolisi mboma la Balaka Inspector Felix Misomali, imodzi mwa galimoto za pa mdipiti wa wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino yagundana ndi galimoto ina mu nsewu wa Zalewa. Imodzi mwa galimoto zapa mdipitiwo Iye wati ngoziyi siyinakhudze wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko linoyu kaamba koti galimoto yake inali itadutsa kale koma yomwe inachita ngoziyi ndi galimoto yomwe inali kumapeto kwa mdipitiwu. Galimoto ya mtundu wa Toyota Vitz Saloon nambala yake BW 8173 yomwe amayendetsa ndi Tamara Kamanga imadutsana ndi convoy ya Vice president koma chifukwa choti imathamanga kwambiri dalaivalayu analephera kuwongolera bwino galimotoyo zomwe zinachititsa kuti akawombane ndi galimoto yomwe inali kumapeto kwenikweni kwa mdipiti umene wa Vice President-wu, Toyota Rand Cruiser nambala yake BW1732 momwe munali dalaivala ndi wapolisi mmodzi, anatero Inspector Misomali. Inspector Misomali ati kutsatira ngoziyi amayi awiri omwe anakwera galimoto ya Vitz yi omwe sakudziwika mayina awo, afera pa malo a ngoziwo komanso bambo wina yemwe anali mu galimoto yomweyo wamwalira atangofika naye pa chipatala cha Phalula ndipo pamapeto pake dalaivala wa galimotoyo wamwalira atafika ku chipatala cha boma la Balaka. Anthu awiri omwe anali mu galimoto yapa mdipitiwo avulala ndipo padakalipano awatengera ku chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe.
14
Anthu 10 Apezeka ndi Coronavirus, Chiwerengero Chafika pa 33 Nduna ya zaumoyo a Jappie Mhango omwenso ndi wapampando wa komiti yapadera yowona za matenda a COVID-19 alengeza kuti anthu ena khumi 10 apezeka ndi matenda a COVID-19 mdziko muno. Malingana ndi Mhango, anthu onsewa ndi ochokera kwa Kaliyeka mu mzinda wa Lilongwe, zomwe zafikitsa chiwelengero cha anthuwa pa 33 pomwe atatu amwalira, enanso atatu achira ndipo anthu omwe padakali pano akudwala matendawa ndi okwana 27. Malinga ndi kafukufuku yemwe wachitika poyeza anthuwa, apeza kuti anthuwa anali pafupi kapena anakhudzana ndi mmodzi mwa odwala yemwe wamwalira dzulo ndi matendawa mu mzinda wa Lilongwe.
6
Papa Wapempha Akhristu Kukhala a Chikhulupiriro Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wati akhristu akuyenera kuyika chikhulupiliro chawo mwa Mulungu yemwe ndi wa chifundo komanso wa chilungamo. Papa Francisko Papa Francisco walankhula izi lolemba pa Misa yomwe watsogolera ku likulu la mpingo-wu ku Vatican. Iye wati ndi koyenera kuti akhristu azikumbukira kuti ngakhale amachimwa, mulungu ndi wa chifundo komanso wa chilungamo. Papa Francisco wati Mulungu ndi wa chifundo komanso wa chilungamo ndipo amasintha anthu oipa kukhala anthu abwino. Mwazina pa misayi Papa Francisco wapempherera onse omwe adzadzidwa ndi mantha chifukwa cha nthenda ya Covid-19 yomwe yakhudza dziko lonse lapansi ndipo wakumbutsa anthu kuti Mulungu sataya anthu ake koma amakhala nawo nthawi zonse.
13
Zokonzekera za Mayeso a Katekisimu wa Ana Zatha Zokonzekera za mayeso a Katikisimu wa ana a Tilitonse omwe akuyembekezeka kuchitika loweruka pa 16 May kudzera pa Radio Maria Malawi, ati zafika kumapeto tsopano. Mkulu wa mu oofesi yowona za mabungwe a utumiki wa a Papa mdziko muno ya Pontifical Mission Societies (PMS) bambo Vincent Mwakhwawa, anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi mu mzinda wa Lilongwe. Iwo ati pakadali pano ofesi yawo yomwenso yakonza mayesowa,yaika chilichonse chofunikira patsikuli kuti lidzakhale lopambana kwa anawa. Zokonzekera mayeso a ana omwe akuyembekezereka kuchitika pa 16 May zafika pamapeto ndipo mayesowo takonza komanso mphatso tayika mchimake, anatero bambo Mwakhwawa. Iwo apempha makolo komanso ana kuti akonzekere bwino powerenga zomwe anaphunzira komanso makolo powagulira ma units okwanira kuti azatenge nawo gawo pa tsikuli.
13
Maneb ikhutila ndi mayeso a sitandade 8 Bungwe loyendetsa mayeso la Malawi National Examinations Board (Maneb) lati lakhutira ndi mmene mayeso a Sitandade 8 ayambira. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkulu wa bungweli Roy Hauya adanena izi Lachinayi atayendera malo angapo komwe ophunzira amalembera mayeso kuyambira Lachitatu. Lachitatu Hauya adayendera sukulu zina ku Blantyre ndipo Lachinayi adali ku Lilongwe. Takondwa ndi mmene mayeso ayambira. Nditsimikizire dziko lonse kuti mayeso akuyenda bwino. Anzathu achitetezo akugwira ntchito yawo bwino ndipo ophunzira akulemba momasuka.Tikufuna zipitirire chonchi Mmene tikhale tikuyamba mayeso ena mwezi ukubwerawu,adatero Hauya. Koma iye adavomereza kuti alandira lipoti lochokera mboma la Mchinji loti munthu wina amalembera wophunzira wina mayeso. Pakadalipano tingati talandira mlandu umodzi wa mayesowa.Wolembera mnzake mayeso amugwira ku Mchinji, adatero Hauya. Ophunzira adamaliza mayeso awo dzulo Lachisanu.
3
Zikhulupiriro zina Zisokoneza mdulidwe Zikhulupiriro zosiyanasiyana zikusokoneza ntchito ya mdulidwe wa abambo womwe unduna wa zaumoyo komanso mabungwe akulimbikitsa, Msangulutso wapeza. Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Ku Nsanje, Dowa komanso ku Nkhata Bay ndi maboma ena amene zikhulupirirozi zachititsa kuti abambo asamapite kuchipatala kukalandira mdulidwewu. Malinga ndi Senior Chief Dzoole ya mboma la Dowa, anthu ati samvetsa komwe kumapita kachikopa kamene adulako, zomwe zimawapatsa mantha. Anthu amaganiza kuti kachikopa kamene akadulako amakakachitira mankhwala. Maganizo awa ndi amene amachititsa anthu kuno kuti asapite kukalandira mdulidwe. Komanso anthu okwatira amaganiza kuti pamene akalandira mdulidwe, ndiye kuti akazi awo aziwayenda njomba chifukwa akawadula sangakakhale malo amodzi ndi mkazi wawo, ati panthawi iyi amaganiza kuti mkazi wawo akhoza kuawayenda njomba, adatero Dzoole. Mdulidwe wa abambo wakuchipatala ndi njira imodzi yothandiza kupewa kufala kwa HIV Dzoole adati mdera lake, mwa amuna 10, amuna anayi okha ndi amene amalandira mdulidwe. Kampeni ili mkati moti mafumufe atiphunzitsa kuti timeme anthu akachititse mdulidwe, koma ndi amuna ochepa amene akupita kukalandira mdulidwe, adatero Dzoole. Senior Chief Kabunduli wa mboma la Nkhata Bay wati kampeniyi yakanika kumeneko chifukwa anthu amaganiza kuti akakalandira mdulidwe ndiye kuti alowa chipembedzo cha Chisilamu. Ambiri kunoko amaganiza kuti amene alandira mdulidwe ndiye kuti ndi achipembedzo cha Chisilamu. Maganizo amenewa ndi amene akuchititsa kuti anthu asakhale nazo chidwi zokalandira mdulidwezo, adatero Kabunduli. Titafunsa mfumuyi ngati ikumemeza anthu ake kuti akachititse mdulidwe, iyo idati: Ukawauza kuti kachitsitseni mdulidwe, akufunsa ngati iweyo unapanga. Ndiye ine pa msinkhu wangawu sindingapite kumdulidwe. Ndinetu munthu wamkulu, ndiye ndikakalandira mdulidwe lero, balalo lidzapola liti? ..sindingapange zimenezo komanso kampeni imeneyi ine sindikuchita nawo. Ku Nsanje, malinga ndi McKnowledge Tembo, HIV/Aids co-ordinator pachipatala cha boma, zikhulupiriro za anthu kumeneko zimati munthu akalandira mdulidwe ndiye kuti amaafooka kuchipinda. Kunoko tinaphunzitsa mafumu, amipingo ndi azaumoyo za ubwino wa mdulidwe, koma mukamayenda muja, anthu amafunsa zambiri zokhudza zikhulupiriro zawo ndi mdulidwe. Palibe amene adabwera poyera kudzatiuza kuti akufooka kuchipinda chifukwa walandira mdulidwe. Komabe anthu upeza akulankhula, ndi zabodza ndipo palibe umboni wake. Zoona zake nzoti macheza amakhalanso bwino mbanja mwamuna akakhala kuti adalandira mdulidwe, adatero Tembo. Nayenso Simeon Lijenje wa PSI akuti ndi bodza la mkunkhuniza kuti amuna amene alandira mdulidwe amafooka ndipo wati amuna amene adulidwa ndiwo amachitanso bwino kuchipinda kusiyana ndi osadulidwa. Palibe umboni wa zomwe anthuwo akunena. Dziwani kuti mwamuna amene walandira mdulidwe ndiye amasangalala kuchipinda chifukwa amakwaniritsa bwino chilakolako cha mkazi wake, adaphera mphongo Lijenje. Iye adati kampeni ya mdulidwewu idayamba mu 2012 ndipo kuchokera mu October 2014 mpaka September 2015 pafupifupi abambo 93 642 ndiwo alandira mdulidwe mbomalo. Achipatala amati ngati abambo alandira mdulidwe, ndiye kuti pali mwayi woti chiwerengero cha anthu otenga kachilombo ka HIV podzera mkugonana chingachepe ndi anthu 6 mwa 10 alionse (60%), malinga ndi mabungwe a WHO komanso UNAIDS. Kuyambira mu 2007, mabungwewa akhala akubwekera kuti mdulidwe umathandize kwambiri kuti kachilomboka kasafale kwambiri. Malinga ndi mabungwewa, maiko 14 a kummwera kwa Afrika komanso kummawa, ndiwo ali kalikiriki kupangitsa kampeni kuti amuna azikalandira mdulidwe. Mdulidwe wa abambo ndi pamene achipatala amadula kachikopa kakutsogolo kwa chida cha abambo. Kachikopaka kamasunga zoipa, koma ngati walandira mdulidwe, amakhala waukhondo. Zoipazo zimakhala zasowa malo oti zisungidwenso, lidatero lipoti la UNAids, nkuonjera kuti mdulidwe umathandiza kuchepetsa matenda a khansa ya khomo la chiberekero cha amayi.
15
DPP, Kasambara trade barbs, witnesses scared There was drama in the High Court in Lilongwe yesterday when a former student and her lecturer locked horns across the divide of the prosecution and defence in the ongoing Paul Mphwiyo shooting trial. Private practice lawyer and accused person Ralph Kasambara and Director of Public Prosecutions (DPP) Mary Kachale exchanged tough words, with the former minister of Justice and Constitutional Affairs accusing the prosecution of personal persecution. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Kachale (L): The allegations are far from the truth Kasambara belittled Kachales concerns that he and other accused persons had intimidated State witnesses who, she said, fear for their lives. But Kasambara said the DPP was just being dramatic. Said Kasambara: The drama being played by the DPP is obvious. She knew she was dealing with elusive witnesses. All this is for dramatic effect to castigate us. All this is intended to play with the public and the media, all just to attack me. He alleged that a police officer from Blantyre, Alex Phiri, had been making night phone calls threatening his wife and brother-in-law with prosecution if they did not comply to testifying against the senior counsel, but Kachale vehemently denied the allegations. Kasambara during an earlier court appearance Kasambara further accused Kachale of favouring another accused person, Oswald Lutepo, who is not subject of bail revocation. She shot back that as her former boss and trainer, she had a lot of respect for Kasambara; hence, she could not have a personal vendetta against him. This [prosecuting Kasambara] was not an easy decision for me to take, but I took it. The allegations he is making here are far from the truth. We do not intend, as the State, to call his wife as a State witness. These serious allegations are casting a slur on my character as well, Kachale charged back. On allegations of favouring Lutepo, Kachale said if he were her favourite, she would not have added him to the case once she examined the evidence and affidavits when she came into the office of the DPP. Kachale insisted that the prosecution had evidence to show witness tampering, but in the meantime, they would ask the court to subpoena them to appear in court by force even though they might become hostile witnesses. Another defence lawyer, John-Gift Mwakhwawa, intervened in the heated exchange and recommended that the State should use the machinery at its disposal to bring the State witnesses to court. Earlier, the DPP told the court that State witnesses were not willing to testify against the six accused persons, claiming that they fear for their lives. Some of the witnesses have been given police protection, but they said they are still afraid to testify against Kasambara, Macdonald Kumwembe and Pika Manondo who are answering charges of attempted murder and conspiracy to commit murder. Kachale said she was forced to ask for an adjournment after the witnesses lined up to testify, including a Chalunda and Defeneya, a ballistics expert from the Malawi Police Service, a police investigator and officials from Airtel Malawi who have since been withdrawn as witnesses. Chalunda and Defeneya approached the prosecution and recorded statements in which they made allegations of intimidation from the accused persons only to change tact and claim that the prosecution was forcing them to change witness statements. She added that the prosecution had concrete evidence to show the level of intimidation the witnesses have undergone. Presiding High Court judge Michael Mtambo is yet to make a ruling on an application to revoke bail for the accused persons who she accused of engaging in mafia-like operations to intimidate witnesses and prevent them from testifying against them. The other accused persons are Dauka Manondo, Lutepo and Robert Kadzuwa whose bail has since been revoked for failing to show up for trial for two consecutive sessions.
11
Papa Akuyembekezeka kuchita Misa Yopemphelera Anthu Othawa Kwawo Wolemba: Glory Kondowe Mtsogoleri wa mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisko lamulungu wati anthu ndi mayiko akuyenera kumadzipereka pothandiza anthu othawa kwawo. Papa walankhula izi ku likulu la mpingowu ku Vatican. Mwazina Papayu wakumbutsa anthu kuti la mulungu likubwera-li pa 29 September ndi tsiku la nambala 105 lokumbukira anthu othawa kwawo kotero akuyenera kukonzekera bwino kuti tsikuli lidzakhale latanthauzo. Papa wati adzakumbukira tsikuli pa mwambo wa msembe ya Misa yomwe adzatsogolere pa bwalo lalikulu la SAINT PETERS SQUARE ku likulu la mpingowu ku Vatican.
13
Osabweza ngongole ya Mardef ali mmadzi Anthu amene sadabweze ngongole ya Malawi Enterprise Development Fund (Mardef) ali mmadzi pamene ayamba kuona zakuda. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ngongole ya Mardef idayamba nthawi ya ulamuliro wa Bingu wa Mutharika pomwe amapereka ndalama kwa achinyamata kuti ayambire bizinesi. Koma ambiri mwa anthuwo sanabweze ngongoleyo. Malinga ndi anthu ena amene tacheza nawo mboma la Kasungu, anthu amene sadabweze ngongoleyi ayamba kumangidwa pamene ena akuwalanda katundu. Mneneri wa Mardef Isaac Mbekeani watsimikiza kuti bungwe lawo layamba kutoleradi ngongoleyo mboma la Kasungu ndi maboma ena. Koma iye adati timupatse mpata kuti afufuze kuchuluka kwa anthu amene akuwafufuza ngakhalenso ndalama zimene zikufu nika. Tumizireni mafunso ndipo ndikuyankhani tsatanetsatane wake za nkhaniyi, adatero Mbekeani Lachinayi koma pofika Lachisanu nkuti asadayankhe mafunsowo. Koma nyakwawa Alamu ya pamsika wa Nkhamenya adatsimikizira Msangulutso kuti anthu ena anjatidwa koma sadapereke zambiri pankhaniyi. Mmudzi mwanga mulibe amene ali ndi ngongoleyi chifukwa iwo amene adakongola nawo adabweza kale ngongoleyo, koma madera ena mboma lino ndiye anthu ali pakalapakala, idatero mfumuyo. Mayi ena amene sadafune kutchulidwa koma akukhala pamsika wa Nkhamenya mbomalo, adati anthu amene sadabweze ngongoleyi ayamba kubisala. Pamene zidamveka mwezi watha kuti amene sadabweze ngongoleyi ayamba kuwamangitsa, anthu ena asamuka kuno pamene ena akumabwera usiku wokhawokha ndi ena athawiratu. Ngati sudabweze ngongoleyi akumakumangitsa, apo ayi ena akumawatengera zinthu monga mwa mgwirizano wa ngongoleyo, adatero. amene adakongola nawo adabweza kale ngongoleyo, koma madera ena mboma lino ndiye anthu ali pakalapakala, idatero mfumuyo. Mayi ena amene sadafune kutchulidwa koma akukhala pamsika wa Nkhamenya mbomalo, adati anthu amene sadabweze ngongoleyi ayamba kubisala. Pamene zidamveka mwezi watha kuti amene sadabweze ngongoleyi ayamba kuwamangitsa, anthu ena asamuka kuno pamene ena akumabwera usiku wokhawokha ndi ena athawiratu.
2
Chipani cha Sacramentine Chichita Chaka cha Asisteri Atatu Wolemba: Thokozani Chapola Chipani cha asisteri cha Sacramentine chachita chaka pomwe asistweri awiri amalumbira malumbiro a ku nthawi zonse pomwe sisteri mmodzi amakondwelera kuti wakwnitsa zaka 50 akuctumikira mulungu ngati sisteri mu chipanichi. Sister Francesca Cortinovice a mdziko la Italy akwanitsa zaka 50 mu utumiki komanso Sister Veronica Chilemba ndi Sister Theresa Misomali alumbira malumbiro a ku nthawi zonse. Mwambowu unachitikira ku parishi ya Ntcheu mu dayosizi ya Dedza ndipo anatsogolera mwambowu ndi mkulu woyendetsa ntchto za dayosiziyi bambo John Chithonje. Mmawu awo bambo Chithonje alangiza makolo kuti atengerepo chitsanzo cha asisteriwa polimbikitsa ana awo pa nkhani ya maphunziro. Zipani zikamatenga ana oti alowe mu chipani, chimodzi mwa zinthu ziomwe amayangana ndi sukulu yomwe anachita. Choncho makolo akuyenera kulimbikitsa ana awo pa maphunziro, anatero bambo Chithonje. Mmodzi mwa akuluakulu a chipani cha sacramentine kuno ku malawi sister hellen matchado ati iwo ndi okondwa kuti mwambowu watheka ndipo wapempha asisteriwa kuti akhale odzipereka pa utumiki wawo. Adutsa mwambiri koma izi ndi zazikulu zomwe mulungu watichitira powatsogolera mpaka lero pomwe atsimikiza kuti ali okonzeka kutumikira Mulungu, anatero sister Matchado. Polankhulapo mmodzi mwa asisteri omwe achita malumbiro awo a ku nthawi zonse sister terteza misomali athokoza mulungu powathandiza kukwaniritsa maloto awo. Si mphamvu kapena nzeru zathu koma timadalira chithandizo cha Mulungu kuti tifike pamenepa, anatero Sister Misomali. Chipani cha sacramentine kuno ku malawi chikupezeka mmadayosizi awiri mwa ma dayosizi 8 omwe alipo mdziko muno omwe ndi a Dedza ndi Mangochi.
13
Papa Yohane Paulo Wachiwiri Anali Wokonda Kupemphera, Wachilungamo Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wati Papa Yohane Paulo Wachiwiri Woyera anali munthu wokonda kupemphera komanso wokonda chilungamo. Papa Yohane Paulo Wachiwiri Woyera Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican Papa Francisco walankhula izi lolemba ku likulu la mpingo ku Vatican pa Misa yokumbukira kuti papita zaka 100 pamene Papa Yohane Paulo Wachiwiri anabadwa. Iye wati Papa Yohane Paulo Wachiwiri ngati mbusa, anali wokonda kukhala pafupi ndi anthu, wokonda kupemphera komanso wokonda chilungamo. Lolemba pa 18 May Papa Francisco watsogolera Misa yomwe yachitikira pa manda a Papa Yohane Paulo Wachiwiri Woyera. Iyi inali Misa ya padera yothokoza Mulungu chifukwa cha mphatso ya mtengo wa patali ku dziko la pansi ya Papa Yohane Paulo Wachiwiri. Pa Misayo Papa Francisco wati Papa Yohane Paulo Wachiwiri anali mbusa yemwe amakonda nthawi zonse kukhala pafupi ndi anthu, wokonda kupemphera komanso wokonda chilungamo. Mulungu amakondadi anthu ake. Mulungu anayendera anthu ake zaka 100 zapitazo kudzera mwa mwana yemwe anabadwa ku Poland. Anakula nakhala wansembe, episkopi mpaka kukhala Papa. Zoonadi Mulungu amakonda anthu ake ndipo amawayendera anthu akewo, watero Papa Francisco pa Misayo. Papa Francisco wati Papa Yohane Paulo Wachiwiri anali wokonda kupemphera chifukwa anadziwa kuti ntchito yoyamba ya episkopi ndi kupemphera. Papa Yohane Paulo Wachiwiri anali wokonda kukhala pafupi ndi anthu nchifukwa chake anayenda maulendo ambiri mmaiko osiyana-siyana kukalimbikitsa akhristu komanso kukasaka nkhosa zotayika ndipo iye watinso Papa Yohane Paulo Wachiwiri anali wokonda chilungamo kuonetsetsa kuti mmaiko muli mtendere komanso anali wa chifundo popeza chilungamo ndi chifundo zimayendera limodzi. Pomaliza Papa Francisco wati ngati lero anthu akukamba za chifundo cha Mulungu (Divine Mercy) ndi chifukwa cha Papa Yohane Paulo Wachiwiri. Papa Yohane Paulo Wachiwiri Woyera anabadwa pa 18 May, 1920 ku Poland. Iye anakhala Papa kwa zaka 27 kuyambira 1978 mpaka kumwalira kwake mchaka cha 2005. Ngati Papa anayenda maulendo 104 mmaiko osiyana-siyana kuphatikizapo dziko la Malawi mchaka cha 1989 kuyambira pa 4 mpaka 6 May.
13
HRDC Siyipepesa-Mtambo Nduna yazofalitsa nkhani a Mark Botomani anapempha speaker wa nyumba ya malamulo kuti ayitanitse ku nyumbayi wapampando wa bungwe la HRDC a Timothy Mtambo kuti akapepese pa mau omwe ati adalankhula lachiwiri pomwe amatuluka kunyumba-yi. Mtambo ndi Trapence pa tsiku lomwe analowa mnyumba ya malamulo A Mtambo akuti adauza atolankhani pomwe amatuluka ku nyumbayi kuti aphunguwa ndi achibwana mawu omwe ndunayi yati ndi osayenera. Pamenepa, a Botomani anati ndi koyenera kuti a Mtambo apite kunyumba-yi ku komiti yomwe a speaker angasankhe kuti iwo akapepese pa mauwa. Iwo amalankhula izi masana a lachitatu kunyumba ya malamulo pomwe nyumbayi imayamba zokambirana zake. Kwa ineyo ndikuona kuti mawu amenewa ndi achipongwe, polankhula kuti ifeyo ndi anthu azibwana komanso ndife ana amene ndi mawu oti sakuyenera kulankhulidwa ndi munthu aliyense kwa nzake, potengera kuti analankhulira kuno ku paliyamenti ndikupemphanso asipikala kuti asankhe komiti yoti a Mtambo akapepeseko pa chipongwe chomwe achitachi, anatero a Botomani. A Botomani ati nkhaniyi yafika kale kwa sipikalayu ndipo anaena kuti achitapo kanthu akakambirana bwinobwino koma iwo apempha asipikala wa kuti achite machawi powayitanitsa a Mtambo ku komiti yomwe asankheyi kuti azapepese poti chipongwechi chalankhulilidwa ndi kwa sipakala omwe anyumbayi. Koma polankhula ndi imodzi mwa wailesi zina mdziko muno wacbiwiri kwa mkulu wa bungwe la HRDC a Gift Trapence ati sangapepese ndipo aphungu a mbali ya bomawa ndi omwe akuyenera kupepesa powatchula iwo kuti ndi zigawenga.
11
CCJP Yadzudzula Mchitidwe wa Ziwawa pa Ndale Mdziko Muno Bungwe la chilungamo ndi mtendere la Catholic Commision for Justice and Peace (CCJP) lati ndi lokhudzidwa ndi mchitidwe wa ziwawa pa ndale umene ukuchitika mdziko muno pomwe anthu ali mkati mokonzekera chisankho chatsopano cha mtsogoleri wa dziko lino chomwe chidzachitike pa 2 July chaka chino. Wasayinira chikalatacho-Chibwana Bungweli lanena izi kudzera mu chikalata chake chomwe latulusa podzudzula mchitidwe-wu. Chikatatachi chati ndi zomvetsa chisoni kuti andale ena sakutenga nawo gawo pophunzitsa anthu owatsatira za kuipa kwa mchitidwe wa ziwawa zomwe zikuononga dziko lino. Bungweli lati mzika za dziko lino zikuyenera kuti ziwunike bwino andalewa pomwe akuyembekezeka kukaponya voti pa chisankho cha president wa dziko pa 2 July chaka chino. Mwazina chkalati chatsindika zina mwa ziwawa komanso zamtopola zomwe zachitika mmadera ena mdziko muno monga kuphwanyidwa kwa zipangizo za bungwe la MEC ku malo ochitira kalembera, kuwotchedwa kwa nyumba, komanso kuphedwa kwa anthu ena, zomwe anthu akuganizira kuti akuchita izi ndi a chipani cha Democratic Progressive (DPP).
11
NB Idandaula ndi Kugula Luso la ICT Lakunja Wolemba: Thokozani Chapola Banki ya National yalangiza makampani owona za chuma mdziko muno kuti aganizire kupereka mwayi kwa achinyamata a mdziko muno omwe ali ndi ukadaulo okhudza luso la makono ndi cholinga chowathandiza kukweza luso lawo komanso kutukula dziko lino. Wapempha kampani zizitenga anthu a luso la ICT a mdziko muno-Kawawa Mkulu wabanki ya National a Macfussy Kawawa ndi yemwe wanena izi lachinai mboma la Mangochi pa mkumano wa akadaulo a luso la makono la ICT omwe unachitikira ku Sunbird Nkopola kumenenso bankiyi inapereka mphotho kwa omwe achita zinthu za luso pa nkhani za ICT. A Kawawa anena izi potsatira dandaulo la anthu ena kuti kampani zambiri zoona za chuma mdziko muno zikumakonda kupereka mwayi kwa kampani za ICT zakunja kuposa za mdziko muno. Pamenepa a Kawawa alangiza achinyamata a luso la mtunduwu mdziko muno kuti adzigwira ntchito limodzi ndi cholinga choti luso lawo liwonekere patali kwa anthu omwe angathe kulifuna. Polankhulapo mtsogoleri wa bungwe la Information Communication Technology Association Of Malawi (ICTAM) a Bram Fudzulani ati ndi okondwa ndi mmene ntchito za ICT zikukulira mdziko muno koma wati akuyesetsa kuti awonetse poyera ntchito zomwe amagwira kuti makampani akonde kupereka mwayi kukampani za ICT za mdziko muno kusiyana ndi za kunja.
2
Alimbikitsa Makatekist Amvetse za Baibulo Makatikisti a mu dayosizi ya Mangochi awapempha kukhala zitsanzo zabwino powerenga komanso kuphunzitsa ena baibulo. Bambo Samuel Malamulo ndi omwe anena izi pa maphunzirowa omwe anachitikira ku St. Marys Pastoral Centre mu dinale ya Mpiri pa mutu woti Baibulo Ndi Nyale Ya Moyo Wanga. Iwo anatinso ma catechist azikhala ndi chidwi chowaphunzitsa akhristu ena ndipo akabwerera ku maparish kwawo akathandize ena kumvetsa baibulo. Iwowa ngati atsogoleri akuyenera kuti akachoka pano akathe kuphunzitsa akhristu ku madera kwawo zokhudza baibulo choncho akuyenera kumvetsa bwino cholinga cha maphunziro amenewa, anatero bambo Malamulo. Mmodzi mwa ma katekist omwe anachita nawo maphunziro-wa a Matthews Mchakulu ati maphunzirowa akawathandiza kuwaphunzitsa akhristu a mma PARISH mwawo kumvetsa baibulo. Maphunziro amenewa atithandiza kwambiri ndipo atithandiza kumvetsa bwino za baibulo. Tikabwelera ku parish kwathu tikatha kuphunzitsa bwino akhristu athu, anatero a Mchakulu.
13
Mafumu sanunkha kanthu pandale Kafukufuku amene achita akadaulo a zandale mdziko muno wasonyeza kuti ngakhale mafumu ena amayesetsa kusanthula momwe Amalawi akuganizira pandale, Amalawi salabadira zonena za mafumuzo. Mmodzi mwa akatswiriwo, Happy Kayuni amene amaphunzitsa ukadaulo pandale ku Chancellor College, adati zotsatira zimene adapeza adzazikhazikitsa pa 17 March ku Sunbird Mount Soche mumzinda wa Blantyre. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mafumu sayenera kuika mlomo pankhani za ndale Izi zikudza patangotha sabata kuchokera pamene anthu ena adakuwiza Paramount Lundu pamaliro a mfumu Kabudula ku Lilongwe pomwe mwa zina adati chipani cha MCP chidalamulira dziko lino zaka 31 ndipo sichidzalamulilanso kuchokera mu 1994 pomwe chidachoka mboma. Lundu adatinso chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) ndicho chidzalamulire mu 2019. Koma polankhula ndi Tamvani, Kayuni adati kafukufukuyo adapeza kuti mafumu amalemekezedwa ndi kukhulupiliridwa pankhani za miyambo yawo osati popanga ganizo la ndale. Tikatulutsa zotsatirazo, anthu adzadzionera okha kuti anthu amalemekeza ndi kukhulupilira mafumu pankhani za chikhalidwe chawo koma alibe chikoka pakapangidwe ka ganizo la munthu amene asankhe pa ndale, adatero Kayuni. Kayuni adakana kutambasula bwino kuti kafukufukuyu adamuchita nthawi yaitali bwanji, ndi anthu angati, njira yomwe adatsata pofunsa mafunso komanso mafunso amene amafunsidwa. Iye adati zonse adzazitambasula bwino akamukhazikitsa. Iye wati chanzeru chomwe mafumu angachite nkuphathirira ku udindo wawo ndi kumalimbikira ntchito yawo mmalo motaya nthawi ndi zandale powopa kutsukuluza ulemu omwe ali nawo. Pa zomwe mafumu ena akhala akunena kuti amayenera kukhala mbali yaboma, Kayuni wati ichi nchilungamo chokhachokha koma waunikira kuti mpofunika kutanthauzira bomalo molondola. Mpofunika kutanthauzira bwinobwino liwu lakuti boma chifukwa mwina mafumu oterowo amaona ngati boma nchipani cholamula pomwe si choncho. Boma limagawidwa patatu: Mtsogoleri ndi nduna zake, aphungu a Nyumba ya Malamulo komanso mabwalo oyendetsa. Akamati amakhala mbali ya boma, sakulakwa koma aziganizira tanthauzoli kuti iwo ngopanda mbali ndipo ntchito yawo nkutsogolera anthu awo pankhani zamakhalidwe ndi chitukuko. Ndale nza anthu ena, adatero Kayuni. Polankhula ku maliro a T/A Kabudula, Senior Chief Lundu adaweruziratu kuti chipani cha DPP ndicho chidzapambane pachisankho cha 2019 ndipo kuti kaya wina afune kaya asafune, mafumu ena mdziko muno sadzaleka kusapota mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ndi chipani cha DPP. Ngati tili pansi pa ulamuliro wa Mutharika ndi chipani cha DPP, chotiletsa kumusapota nchiyani? Choti mudziwe nchakuti chipani cha DPP chikuyenera kulamula mpaka 2019 ndipo chidzapitiliza kuchoka apo, adatero Lundu kumaliroko. Iye adapitiriza kunena kuti chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chomwe mtsogoleri wake Lazarus Chakwera adali pa maliro pomwepo chisamalote zodzalamuliranso ndipo kuti kwake kudatha momwe chidatuluka mboma ngati chipani cholamula. Chakwera atafunsidwa ndemanga yake ndi Tamvani pa nkhaniyi adati alibe mau aliwonse kenako nkuseka. Oyendetsa nkhani za mafumu ku unduna wa Maboma angonoangono Lawrence Makonokaya adati timutumizire mafunso omwe tikuyembekezera mayankho ake. Zotsalira Tikuchezanso ndi kadaulo wina amene adacchita nawonso kafukufukuyo.
8
Boma Lilimbana ndi Mchitidwe Odzembetsa Anthu Wolemba: Sylvester Kasitomu Unduna owona za chitetezo cha mdziko wati uyesetsa pa ntchito yolimbana ndi mchitidwe ozembesta anthu (Human Trafficking) umenenso wakula kwambiri mdziko muno. Nduna mu undunawu a Nicholas Dausi anena izi mu mzinda wa Lilongwe pa mwambo wokumbukira tsiku lolimbana ndi mchitidwe wozembetsa anthu pa dziko lonse. A Dausi ati ndizomvetsa chisoni kuti mchitidwe-wu ukuchitikira aliyense ngakhale anthu ophunzira kumene zomwe zikuyika pachiopsezo miyoyo ya anthu ambiri choncho ati unduna wawo ugwirana manja ndi magulu onse okhudzidwa polimbana ndi mchitidwewu. Zomatenga anthu kuti tili ndi ntchito zoti mukagwoire mmaiko wena pamapeto pake ndikumakawagwiritsa ntchito za uhule ndi zina tikudzidziwa ndipo tikufuna kuti zitheretu mdziko muno, anatero a Dausi. Ndipo polankhulapo mkulu oyanganira nkhani zozembetsa anthu ku nthambi ya bungwe la united nations yoona nkhani zokhudza makhwala ozunguza ubongo mdziko muno a Maxwel Matewere anati nthambi zonse zoona za malamulo mdziko muno ziwunika nkhaniyi kuti itheretu ndipo anthu omwe apezeke akhudzidwe ndi mchitidwewu kuti amangidwe. Anthu ena amangidwa kale pokhudzidwa ndi milanduyi ndipo ena anchajidwa kale ndipo ine ndi osangala kuti boma latengapo gawo pofuna kuteteza anthuwa, anatero a Matewere. Anthu amangidwa pokhudzidwa ndi milanduyi ndi okwana 32 ndipo mwa anthuwa 16 ndi omwe milandu yawo inatha ndipo akugwira ukaidi kundende za mdziko lino.
14
Voti yotengera zigawo ilipobe Amalawi akadali ndi mtima wovota potengera chigawo chomwe amachokera ndi munthu kapena chipani chomwe akulumikizana nacho mnjira inayake makamaka mtundu. Mwachitsanzo, pa zisankho ziwiri zapitazi za 2014 ndi 2019, chipani cha DPP chakhala chikupeza ma voti ambiri ku mmwera, MCP mchigawo chapakati pomwe kumpoto kudavotera kwambiri zipani za UTM and PP. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Duwa: Anthu ali kale ndi mbale Zotsatira za chisankho cha chaka chino zawonetsa kuti kavotedwe ka anthu sikadasinthe kwenikweni ndipo zangokhala ngati mkopera wa zotsatira za chisankho cha 2014 makamaka kwa zipani za MCP ndi DPP zomwe zimapikisana kwambiri. Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi zisankho la Malawi Electoral Support Network (Mesn) Steve Duwa wati izi zili choncho chifukwa anthu saphunzitsidwa mokwanira za momwe angasankhire atsogoleri komanso zipani za ndale zimalephera kutambasula mfundo zake kuti anthu asinthe maganizo pambali yovotera. Anthu ali kale ndi mbali potengera zigawo zochokera chifukwa aliyense amafuna kukokera kwake koma malingaliro oterewa akhonza kusintha potengera momwe anthu aphunzitsidwira pa kasankhidwe ka atsogoleri komanso momwe zipani zatambasulira mfundo zake, adatero Duwa. Katswiri pa ndale Ernest Thindwa adati kuvota kwa malingaliro otere kawirikawiri kumachititsa kuti mtsogoleri azisankhidwa ndi anthu ochepa zomwe ngakhale zimaloledwa mdziko muno potengera malamulo achisankho, nzosayenera mu demokalase. Demokalase imatanthauza kuti anthu azisankha mtsogoleri yemwe akufuna ndipo azisankhidwa ndi anthu ambiri. Mwachidule, opitirira theka la anthu onse omwe adaponya voti ndiye kuti demokalase ikuyenda, adatero Thindwa.
11
Dz Young Soccer, Mighty adutsa Chikho cha Standard Bank chayamba ndi moto pamene matimu a asirikali a Kamuzu Barracks ndi Mafco FC aona msana wa njira atakwapulidwa ndi Dedza Young Soccer FC komanso Be Forward Wanderers kudzera mmapenote. Chikho cha K10 miliyonichi chidayamba modabwitsa Lachitatu pamene timu ya Kamuzu Barracks idaona mdima pa Civo Stadium itachitidwa chiwembu ndi Dedza Young Soccer kudzera mmapenote. Masewerowo adathera 2-2 ndipo nthawi ya mapenote Young Soccer idalimba chifu pokakamizabe asirikaliwa kuti atuluke mchikhochi. 10 kwa 9 ndi momwe mapenotewo adathera, kukomera anyamata a ku Dedza. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Lachinayi udalipoliponso pabwaloli Wanderers kulimbana ndi asirikali a Mafco. Masewerowanso adatheranso mmapenote atalepherana duu kwa duu ndipo Wanderers idapuntha Mafco 4-3 mmapenotewo. Mafco idali ndi mwawi wambiri moti ikadatha kuchinya zigoli mphindi 90 koma zonse zidangothera hiii! Iyitu idali ndime yachipulula ndipo matimu amene achita bwinowa alowa mndime ya makotafainolo. Apa ndiye kuti Dedza iphana ndi Civo mndimeyi pamene Wanderers ikumana ndi Red Lions. Mmakotafainolo ena, timu yomwe ikuteteza chikhochi, Silver Strikers, ikwapulana ndi Blue Eagles pamene Moyale Barracks ikumana ndi Big Bullets. Kochi wa Wanderers Elia Kananji adati ali ndi chiyembekezo kuti timu yake ichita zakupsa mchikhochi. Adali masewero ovuta koma Mulungu adali mbali yathu. Tikukhulupirira kuti Mulungu yemweyo akhala nafe mumpikisanowu mpaka kumapeto, adatero Kananji. Naye Pofera Jegwe, kochi wa Dedza Young Soccer, adati kupambana kwawo ndi chithokozo kwa masapota awo. Mukudziwa kuti tidachita kuvoteredwa kuti tisewere mchikhochi, ndiye kupambanaku ndi njira imodzi yothokoza amene adativoterawo, adatero Jegwe. Bungwe la FAM lomwe likuyendetsa mpikisanowu litulutsa masiku amene makotafainolowa aseweredwe.
16
Minibasi zikwera Mwachinunu Nthawi zonse minibasi zikamakweza mtengo, makamaka mafuta akakwera, bungwe la eni minibasi limalengeza, ndi kuika mitengo ya minibasi kuti aliyense adziwe. Koma kuchokera Loweruka lapitalo, mitengo ya minibasi mmadera ena idakwera mwachinunu. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izi zidachitika patangotha tsiku limodzi kuchokera pomwe oyendetsa minibasi adanyanyala ntchito zawo ati pokwiya ndi zilango zina zimene amalandira akaphwanya malamulo a pamsewu. Amalawi amene tacheza nawo ku Blantyre, Lilongwe ndi Mzuzu adati ndiokhudzidwa ndi kukwezaku, komwe cholinga chake sichikumveka. Mandiya: Okwera akuyenera kupereka yochuluka basi Mmodzi mwa anthu omwe akhudzidwa ndi mitengoyi, Sydney Chingamba wa ku Chilomoni yemwe amagwira ntchito ku Ginnery Corner mumzinda wa Blantyre, wati ichi ndi chitonzo ndipo okwera akuyenera kuchitapo kanthu kuti mitengo ibwerere. Kafukufuku wa Msangulutso wapeza kuti mitengoyi yakwera ndi K50 kapena K100 mmadera osiyanasiyana mmizindayo. Malingana ndi mmodzi mwa madalaivalawa mu Limbe, Fatchi Madani, iyi ndi njira yoti galimoto itulutse ndalama zomwe eni minibasi amafuna patsiku ngakhale pali malamulo okhwimawa. Okwera akuyenera kupereka ndalama yochuluka basi. Patsiku bwana amafuna K10 000 ndipo kutenga atatu pampando pa K500 kukawasiya kwa Goliati ndi phada ameneyo. Ngakhale tisatenge anayi-anayi pampando ndalama izipezeka yokwanira chifukwa cha mitengoyi, adatero Madani. Naye Phillip Bwanali, woyendetsa galimoto pakati pa Limbe ndi Blantyre, adati akweza mitengo chifukwa sakuloledwa kunyamula katundu [chimanga, mtedza ndi zina] yemwe okwera amamulipira mwa padera. Tatero kuti tisavutike ndi kupewa ena kuyamba kuba ndi umbanda. Mmene chilili chuma cha dziko lino anthu ambiri sangakwanitse kutenga katundu pa matola omwe ndi okwera mtengo kusiyana ndi maminibasi, iye adatero. Poyankhapo, mkulu wa bungwe la eni minibasi la Minibus Owners Association of Malawi (Moam), Coaxley Kamange adati ndi odabwa ndi zimenezi ndipo wangomva mphekesera kuti madalaivala achita moteremu. Izi sizikutikhudza. Aliyense akhoza kuchita chili chonse ndi mitengo chifukwa lamulo likulola anthu kutero. Takhala tikudzudzulidwa ndi bungwe la Competition and Fair Trading Commission (CFTC) pamene timakonza mitengo mmbuyomu ndipo tidasiya, adatero Kamange. Iye adati izi ndi zosokoneza anthu chifukwa akudziwa zakusinthaku ali mminibasi kapena padepoti. Timayenera kutenga gawo pa chiganizochi kuphatikizapo okwera kuti mitengo ikhale yokomera onse. Bungweli [CFTC] lidati tisamakonze mitengo ya minibasi, koma padakalipano ndondomeko yabwino palibe, adatero Kamange. Mkulu wa bungwe loona ufulu wa okwera la Passengers Welfare Association of Malawi (Pawa), Don Napuwa, adati izi ndi zokhumudwitsa ndipo madalaivala sakuyenera kukweza mitengo ya galimoto chifukwa boma langokhwimitsa ndi kuyamba kutsatsa malamulo omwe adalipo kale. Madalaivala akusokoneza. Ngakhale kunyanyala ntchito komwe adachita sabata yatha eni galimoto sadadziwitsidwe. Mitengoyi imakwera potengera mtengo wa mafuta ndipo mafuta sanakwere. Oyendetsawa alibe danga lokweza mitengo, adatero Napuwa.
15
Katsoka: Mtsogoleri wa alakatuli Ulakatuli ndi limodzi mwa maluso omwe akuphukira kumene mdziko muno. Zaka zambiri zapitazo, anthu samatenga ndakatulo ngati njira yofalitsira uthenga kapena kuphunzitsa monga momwe zikukhalira pano. Pazaka zochepa zokha, alakatuli mdziko muno atumphuka ndipo anthu ambiri ayamba kukonda ndakatulo. Alakatuliwa adakhazikitsa bungwe lawo lomwe mtsogoleri wake ndi Felix Njonjonjo Katsoka. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Katsoka ndi mlakatuli wodziwa kuluka mawu Tandiuza dzina lako ndi komwe umachokera. Ine ndine Felix Njonjonjo Katsoka. Ndimachokera mmudzi mwa Chingamba mboma la Ntcheu koma pano ndikukhala ku Nkhotakota. Ndidaphunzira za uphunzitsi koma ndimagwira ntchito ya zaumoyo kumbali ya zakudya zamagulu. Utsogoleri wa alakatuli udaulowa liti? Ndidauyamba mchaka cha 2009. Malingana ndi malamulo athu, timayenera kukhala ndi zisankho zaka zisanu (5) zilizonse moti panopa tili kalikiriki kuthamangathamanga kuti tipeze ndalama zopangitsira nkhumano ina komwe tidzakhalenso ndi zisankho. Kodi bungwe limeneli lidayamba liti? Bungweli lidayamba mchaka cha 1997 pomwe alakatuli adakumana kubwalo la masewero la Kamuzu Stadium. Ena mwa akatakwe omwe adali kumeneko ndi monga Laurent Namarakha, malemu Aubrey Nazombe, Edward Chitseko ndi malemu George Chiingeni. Pa 4 September, 1998, bungweli lidalembetsedwa kunthambi ya kalembera wa mabungwe. Cholinga chake nchiya? Cholinga cha bungweli ndi kufuna kutukula luso la ulakatuli mMalawi muno komanso kufuna kufalitsa mauthenga ndi kuphunzitsa anthu kudzera mndakatulo monga momwe amachitira azisudzo kapena oyimba. Kodi munthu amafunika chiyani kuti akhale mlakatuli? Choyambirira ndi kudzipereka kukhala ndi mtima ofunitsitsa kukhala mlakatuli. Sizilira kupita kusukulu, ayi, ndi luso ndithu lachibadwa. Ine sindidaphunzireko ndakatulo komanso alakatuli ambiri omwe ndimadziwa sadachite maphunziro a ndakatulo, ayi.katsoka Nanga ndakatulo yabwino imafunika kukhala ndi chiyani? Ndakatulo yabwino imayenera kukhala ndi phunziro, msangulutso komanso izigwirizana ndi zachikhalidwe kapena nkhani yomwe ikunenedwa. Mundakatulo muli ufulu wosankha mmene ukufunira kuti mavume azimvekera. Palibe malamulo akuti ndakatulo izimveka motere, ayi. Kwathu kuno, ndakatulo zambiri zimakhala zokhudza chikhalidwe cha Chimalawi, makamaka potengera chiphunzitso ndi malangizo.
0
Chikondi chidayambira kuubwana Akuti chikondi chidayambira kuumwana kalelo pomwe ankasewerera limodzi nkumakula pa Kalera ku Salima ndipo lero akhala thupi limodzi. Francis Tayanjah-Phiri, mtolankhani wodziwika bwino yemwe akugwira ntchito kukampani ya Times Group, sabata yathayi adamanga chinkhoswe ndi nthiti yake, Stella Kamndaya, yemwe ndi mphunzitsi ku Lumbadzi mboma la Dowa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tayanjah ndi dona wake Stella kugonekerana khosi patsiku la chinkhoswe Tayanjah adati mzaka za mma 1980 mayi ake ankaphunzitsa pasukulu ya pulayimale ya Kalera limodzi ndi bambo ake a Stella ndipo mabanja awiriwa adali pachinzake cha ponda-apa-nane-mpondepo, zomwe zidabzala mbewu ya chikondi mwa ana awo. Pa anzanga onse yemwe ndinkagwirizana naye kwambiri adali iyeyu kufikira pomwe ndidapita kukapanga maphunziro a utolankhani ndipo naye adakapanga kozi ya uphunzitsi. Kuyambira pamenepo tinkangomva kuti wina ali uku ndipo wina ali uku, adatero Tayanjah. Iye adati kutalikiranako sikudafufute chikondi chomwe adali nacho pakati pa wina ndi mnzake ndipo ankaganiziranabe nthawi zonse mpakana mwamwayi adakumana aliyense akuyendera zake mumzinda wa Lilongwe, nkukumbukira kale lawo. Chifukwa cha chikumbumtima cha kale lathu, titakumana padalibe chilendo chilichonse ndipo tidayambiranso kucheza, koma ndidaona kuti ubale womwe adatiphunzitsa makolo athu kalelo tiuonetsere kudziko, adatero Tayanjah. Iye adati nyengo ikupita ndi machezawo adapereka maganizo a banja ndipo mtima wake udadzadza ndi chimwemwe choopsa Stella atavomera. Naye Stella adati kwa iye adali ngati maloto okoma oti ukadzuka zomwe umalotazo zikuchitikadi uli maso. Ndidalibe chifukwa chotengera nthawi kuti ndikaganize kapena kuti ndimuone kaye chifukwa ndakula naye ndipo nzeru zake, khalidwe lake, chikondi chake zonse ndidali ndikudziwa kale kuchokera tili ana, adatero Stella. Iye adati ali ndi chiyembekezo cha banja lapamwamba ndi Tayanjah ndipo pemphero lake ndi lakuti Mulungu awapatse luntha lomwe adapatsa makolo awo pakasungidwe ka banja ndi kaleredwe ka ana. Tayanjah amachokera mmudzi mwa Rubeni, T/A Kambwiri ku Salima ndipo Stella kwawo ndi kwa Daniel, T/A Maganga ku Salima komweko.
15
ankawerenga nkhani pa mij Ndi mawu okha, MarcFarlane Mbewe wa Capital Radio adachiritsidwa. Awa ndi makumanidwe a mnyamatayu ndi Lisa Lamya, mtolankhani wa Yoneco FM (YFM). Nkhaniyi idayamba mu 2014, apo nkuti Lisa akugwira ntchito ku MIJ FM. Kumeneko, namwaliyu ankawerenga nkhani. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Lero ali ndi mwana mmodzi, Evan: Macfarlen ndi Lisa Ena mwina amangomva namwaliyo akamawerenga nkhani, koma kwa MarcFarlane, zimamupatsa uthenga wina. Mawu ake ozuna komanso Chingerezi chake chothyakuka zidanditenga mtima, adatero MarcFarlane. Ndidafunitsitsa nditapalana naye ubwenzi. Mwachangu ndidamusaka pa Facebook. Ndidamutumizira pempho kuti akhale mnzanga. Macheza akuti adayamba. Koma mnyamatayo atapempha nambala, Lisa adamukaniza. Ndidaponya mfundo ndipo mapeto ake adandipatsa nambalayo, adatero. Apo zidayamba kusongola ndipo mathero ake kudali kukumana pamene mfundo zenizeni zidaumbidwa. Lero Lisa akubwekera posankha mnyamatayu. MarcFarlane ndidamukonda chifukwa ndi ndi wanthabwala zedi koposa zonse amakonda kupemphera, idatero njoleyo. Pamene MarcFarlane akuti: Lisa ndi mkazi wokoma mmaso komanso wakhalidwe. Awiriwa ali ndi mwana wa miyezi isanu dzina lake Evan. Ukwati akuti apangitsa chaka chikudzachi koma chinkhoswe ndiye chidali pa 5 March 2017. MarcFarlane, woyamba mwa ana atatu ndi wa kwa Chimaliro mboma la Thyolo. Lisa, woyamba mwa ana awiri ndi wa kwa Ben Chauya ku Ntcheu.
15
Ndimamupitirira Wawa gogo, Ndili ndi zaka 17 ndi[po pali mnyamata wina wa zaka 20 yemwe akundifuna. Ndimamukonda koma vuto ndi lakuti iyeyo ndi wamfupi kuposa ine. Ndimachita manyazi ndikamayenda naye. Ndimulole? C Zikomo C, Sindikuonapo vuto loti musamulolele! Kutalika kukhale nkhani? Chikondi chimachoka mumtima ndipo sichiyenera kuona ngati wina ndi wamtali kapena wamfupi, woonda kapena wonenepa, woona kapena wosaona ndi zina zotero. Chabwino nchiyani kuti mudzapeze mnyamata wamtali ngati inu kapena kukuposani koma alibe chikondi kapena kukhala ndi mwamuna ameneyu yemwe amakukondani nanunso kumukonda. Muloleni ameneyo basi.
12
Apolisi Akusasaka Opha Mkazi Wake Wakale Wolemba: Sylvester Kasitomu ntent/uploads/2019/09/chigalu.jpg" alt="" width="397" height="264" />Chigalu: mayiyo amakana kuti abwelerane Apolisi ku Ntcheu akusakasaka mkulu wina amene wapha yemwe anali mkazi wake kaamba kokana kuti abwelerane pa ubwenzi. Mneneri wa apolisi mbomalo Hastings Chigalu wati mamunayo ndi Ndaipa Odala ndipo mayiyo ndi Idesi Lyson wa zaka 19. Chigalu wati awiriwa anali pa ubwenzi ndipo anapatsana pathupi koma mamunayo anakana kuti mimbayo siyake. Kwa nthawi yonseyi mayiwa akhala akuvutika okha ndi mwanayi kufikia sabata latha pomwe bamboyu anayamba kuzachonderera kuti abwerere pa banja ndi malemuwa. Malemuwa atakana zobwerera pa banja ndi oganiziridwawa zinawakwiyitsa ndipo anaganiza zowadikirira panjira pomwe malemuwa amyenda mu nsewu wina ndikuwabaya ndipo anafera pamalo amwewo, anatero Chigalu. Malipoti akuchipatala atsimikiza za imfayi ndipo ati mayiyu wafa kaamba kotaya magazi ambiri.
7
Ndi Walter, Mijiga Kapena Yabwanya? Atatsatsa mfundo zawo masiku apitawa, omwe akulimbirana maudindo kubungwe loyendetsa masewero a mpira wa miyendo la Football Association of Malawi (FAM) akhala akukumana maso ndi maso pazisankho zomwe zikuchitika lero. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nthumwi zokwana 36 zochokera kunthambi za FAM ndi zomwe zitaponye voti pamsonkhano waukulu womwe ukuchitikira mboma la Mangochi. Akuimanso: Nyamilandu Omwe akupikisana paudindo wa pulezidenti ndi yemwe pakalipano ali pampandowu, Walter Nyamilandu, Wilkins Mijiga komanso a Willy Yabwanya Phiri. Akuluakuluwa sabata yathayi adali kalikiriki kupereka mfundo zawo pazomwe akufuna adzachite akasankhidwa paudindowu. Polankhula mumzinda wa Lilongwe, Nyamilandu adalonjeza kuti akapambananso adzakhazikitsa ndondomeko zoonesetsa kuti mpira wa mmakwalala ukupita patsogolo komanso kuti mpira ukubweretsa ndalama zochuluka maka mmakalabu osiyanasiyana. Wakonzeka: Mijiga Kumbali yake Yabwanya adalonjeza kuti adzasula aphunzitsi a mpira ambiri omwe azitha kuphunzitsa anyamata achisodzera ndi cholinga choti luso lawo lipite patsogolo. Naye Mijiga pomema anthu kuti amusankhe, adati adzakhazikitsa njira zopezera ndalama ndi cholinga choti osewera, oyimbira komanso oyendetsa mpira azilandira ndalama zambiri. Pakalipano zikuonetsa kuti Nyamilandu atha kutenganso mpandowu kaamba koti mwa nthambi zisanu ndi zinayi za bungwe la FAM, zisanu ndi ziwiri zidalengezetsa kuti zili pambuyo pake. Ali momo: Yabwanya Phiri: Nthambi imodzi yokha ya Super League of Malawi ndi yomwe ikuti ili pambuyo pa Mijiga pomwe ya National Referees Committee ndi yomwe ikuti ili pambuyo pa Yabwanya. Koma zioneka komweko chifukwa voti ikhala yachinsinsi. Omwe akupikisana pampando wa wachiwiri kwa pulezidenti ndi Tiya Somba-Banda ndi James Mwenda. Mpikisano pampando wa wachiwiri kwa wachiwiri kwa pulezidenti uli pakati pa Pikao Ngalamila ndi Othaniel Hara.
16
Papa Wati Atsogoleri Athandize Anthu Awo Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Fransisco wapempha atsogoleri a mayiko kuti ayike ndondomeko zabwino zothandiza anthu awo. Papa Francisko Papa Francisco walankhula izi lolemba pa misa yomwe anatsogolera ku likulu la mpingo ku Vatican. Iye wati atsogoleri a mayiko ndi onse ochita ndale akuyenera kumachita zinthu zokhazo zomwe zingathandize pa ntchito zotetedza komanso kutukula anthu awo osati kuchita zinthu zongokomera iwo eni ndi zipani zawo.
14
Lutepo wakundende Bwalo lalikulu la milandu ku Zomba (High Court) Lachisanu lapitali lalamula Auswald Lutepo, yemwe ndi mmodzi mwa anthu omwe akuyankha milandu yokhudza kusolola ndalama za boma wotchedwa kuti Cashgate, kuti akakhale mndende kwa zaka 11 popezeka wolakwa pamlanduwu. Popereka chilango, jaji Redson Kapindu adati pamlandu woyamba wopanga upo pofuna kubera boma, Lutepo akaseweze zaka zitatu ndipo wachiwiri, wosolola ndalama zokwana K4.2 biliyoni, akaseweze zaka 8. Zilango zonsezi ziyendera limodzi kuyambira pa 11 June pomwe iye adapezeka wolakwa pamilandu yonse iwiri. Jajiyu adati wamumverako chisoni pamplandu wachiwiri kaamba koti adabwezako ndalama zokwana K370 miliyoni.
11
Sitalaka yatha, yaika amalawi pamoto Pomwe ogwira ntchito mboma ali pa sitalaka kufuna kuti malipiro awo akwere ndi K67 pa K100 iliyonse, anthu omwe amafuna thandizo la ogwira ntchito mbomawa tsopano ndiwo ali pamavuto adzaoneni. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Pomwe limafika Lachitatu nkuti maofesi ambiri aboma ali otseka. Kuchipatala kokha ndiko kudali kosatseka. Anamwino amene adakumana ndi mtsogoleri wa dziko lino Lolemba adati ngati madandaulo awo, kuphatikiza kukwezedwa kwa malipiro awo, sakwaniritsidwa pofika pa 26 February, nawonso achita sitalaka. Wophunzira wina pasukulu ya sekondale ya Nyambadwe adati kumeneko aphunzitsi a pulaimale ndi sekondale adayamba kunyanyala Lachiwiri sabata yatha. Mnyamatayu, yemwe ali fomu 3 ndipo ali ndi zaka 24, amagwira ntchito ya mnyumba ku Mbayani ndipo amalandira K5 000 pamwezi. Pandalamapo amachotsapo K4 700 kuti alipirire sukuluyo pateremu. Ndidachoka kwathu ku Mangochi chifukwa bambo anga adamwalira ndipo mayi anga ndiwo ankandilipirira sukulu. Iwo ankagulitsa tiyi. Koma zitawasokonekera, kusukulu adandithamangitsa. Nditapata ntchitoyi ndipomwe ndabwerera kusukulu. Ndimalimbikira kuti ntchitoyo ilipo ndikhale ndamaliza sukulu. Kunyanyala kwa aphunzitsi kukundiwawa chifukwa ntchitoyi mwina itha kutha zomwe zidzandivute kuti ndibwererenso kusukulu posowa ndalama, adadandaula mnyamatayu. Wophunzira wina yemwe ali sitandade 8 pa sukulu ya pulaimale ya Mbayani wati boma liwaganizire chifukwa mayeso ayamba posachedwapa. Sitidaphunzire mokwana, ndipo kwangotsala miyezi itatu kuti tilembe mayeso. Boma litiganizire zimenezi, adatero msungwanayo. Ndipo mnyamata wina pasukulu ya Nkolokoti ndipo ali sitandade 7 wati mayeso a aphunzitsi ayamba sabata ya mawayi kotero boma liwaganizire. Omwe akuchititsa izi adaphunzira kale ndipo ana awo ali msukulu za pulaiveti ndiye iyi si nkhani kwa iwo. Chonde boma liganizire, adatero mnyamata wa zaka 11. Mphunzitsi wina pa Mbayani adati mwana sakuyenera asemphe kanthu pano chifukwa mayeso ali pafupi. Chitsanzo a 8 ali ndi miyezi itatu yokha pomwe silabasi sadamalize, nanenso ndine kholo zikundimvetsa chisoni koma nanga nditani, adatero mphunzitsiyo. Ndipo Lachitatu, ana a sukulu zina mumzinda wa Blantyre adapita kusukulu ya Joyce Banda Foundation, yomwe ndi ya mtsogoleri wa dziko lino. Anawo adati akasokoneze maphunziro ati chifukwa ana kusukuluyo amaphunzirabe. Nawo maofesi a Road Traffic Lachitatu adali kotseka. Mkulu wina yemwe tidamupeza ku ofesiyi ndipo amafuna thandizo adati zamukhudza. COF ya galimotoyi yatha dzulo pa 19, ngati ndingayendebe pamsewu ndiye kuti andigwira. Akangondigwira ndiyenera kulipira K3 500. Ndachita changu kudzakonzetsa koma apa pali potseka. Boma lidziwe kuti omwe tikuvutika ndife osati iwo, adatero mkuluyo. Koma mkulu wa bungwe la ogwira ntchito mboma la Civil Service Trade Union Eliah Kamphinda wati anthu omwe akuvutikawa akuyenera kufunsa omwe achititsa kuti mavutowa adze. Pali ena achititsa izi, afunse azamaphunziro omwe adzetsa zonsezi, adatero Kamphinda. Iye adati ku Lilongwe apereka kalata yachidandaulo ndipo kuyambira Lachinayi amayembekezeka kumakumana malo amodzi mpaka boma litayankha. Nduna ya zachuma Dr Ken Lipenga Lachiwiri lomwelo adati sizingatheke kuti boma likweze malipiro a ogqira ntchito mboma chifukwa kuti boma litero, ndiye kuti ndalama zimene boma limalipira a ntchito ake zidzakwera kuchoka pa K92 biliyoni kufika pa K276 biliyoni chaka chilichonse. Iye adanena izi pamsonkhano wa atolankhani omwe adaitanitsa a bungwe la International Monetary Fund (IMF). Izi zingatanthauze kuti ndalama za boma zonse zithera kulipira ogwira ntchito mboma. Mankhwala mzipatala tidzagulira chiyani? adazizwa Lipenga. Mkulu wa IMF kuno ku Malawi Tsidi Tsikata adati adapempha boma la Malawi kuti lichepetse ndalama zomwe limagwiritsa ntchito. Boma likuyenera kuonetsetsa kuti likugwiritsa bwino ntchito ndalama zomwe zilipo. Mmalo motaya nthawi ndi zazingono, bwenzi boma likuikapo mtima pogwiritsa ntchito bwino ndalamazo, adatero Tsikata.
11
Blessings Cheleuka wa pa JOY FM Amalawi ambiri kuyamba Lolemba mpaka Lachisanu nthawi ya 2 koloko kufika 4 koloko masana amatsegula wailesi ya Joy FM kuti amvere nyimbo zothyakuka zoimbidwa ndi Amalawi anzawo. Namandwa wophulitsa nyimbo zimenezi ndi Blessings Cheleuka, yemweso wachitapo mbali yaikulu kutukula alakatuli mdziko muno. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Cheleuka: Chilichonse nchotheka pamoyo wa munthu Dzifotokoze mkulu wanga. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Blessings Cheleuka, ndimachokera mmudzi mwa Mothiwa kwa T/A Likoswe mboma la Chiradzulu. Ndine muulutsi wa pawayilesi komanso ndimakonda ndakatulo kwambiri. Ntchito yakoyi udayamba liti? Ndakhala ndikugwira ntchitoyi kwa zaka 12 ndipo ndagwira mnthambi zosiyanasiyana monga wolemba nkhani, mkonzi, muulutsi ndi zina. China choti mungadziwe nchakuti ndagwirako ntchitoyi kunyuzipepala ndi kuwayilesi komwe ndiye ndili ndi ukadaulo kwambiri. Akadaulo ambiri amakhala ndi komwe adaphunzirira ntchito, iwe udaphunzirira kuti? Choyamba, ndidaphunzira zautolankhani kusukulu yaukachenjede ya Polytechnic, nthambi imodzi ya University of Malawi. Kumeneku ndidaphunzira zomwe zimatenga kuti munthu ukhale mtolankhani mbali zonse. Kuchoka apo mmalo momwe ndakhala ndi kugwira ntchito monga Power 101 FM komwe ndidayambira ntchito; ndidaphunzirako za kuulutsa mapologalamu osanjenjemera chifukwatu kunena zoona ndi luso lapadera limenelija. Ndimayamikaso Mulungu ponditsogolera ndi kundiunikira. Nanga umaulutsa mapologalamu anji pawailesi? Ndimaulutsa mapologalamu ambiri monga Dimba Music yomwe imauluka kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu nthawi ya 2 koloko masana mpaka 4 koloko madzulo; Zina Ukamva yomwe imauluka 8 koloko madzulo Loweluka; pologalamu ya ndakatulo yotchedwa Patsinde yomwe imayamba 8 koloko mmawa mpaka 10 koloko; Mfuwu Wa Chimwemwe kuyamba 6 koloko mpaka 9 koloko mmawa Lamulungu; ndi Gospel Top 20 ya nyimbo za uzimu komanso ndine ndimayanganira za uwulutsi kuwailesi ndi kanema za Joy. Ukutinso uli ndi chidwi pa zaulakatuli, umatengapo gawo lanji? Ndapanga zambiri monga kudzera mu pologalamu yanga ya Patsinde. Ndimafukula alakatuli omwe sadayambe kudziwika. Ndimakonzaso zochitika za alakatuli ndipo anthu ambiri amazikonda. Ukafatsa umakonda kutani? Ndimakonda kuonerera mapologalamu a pakanema ndi zauzimu basi. Mwina okutsata amangoti ndiwe muulutsi, ungawauzenji za iwe? Ine ndine Blessings Cheleuka odziwika kuti Bule wanu pazausangalatsi ndipo cholinga changa nkusangalatsa Amalawi basi.
9
Tinkapita kumpira wa Silver Ena akangomva za masewero ampira amalingalira zogenda, kuvala ziyangoyango kapena kuimba nyimbo basi komatu monga zochitika zina zilizonse, iyi ndi nthawi yokumana ndi anthu osiyanasiyana okonda zinthu ndi zochita zosiyanasiyananso. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Onse amakonda timu ya Silver: Daniel Kudzera mumtendere woterewu, ena amachita mwayi waukulu pamoyo wawo mwina mpaka kupeza nthiti yawo monga momwe zidakhalira ndi Daniel Nthala wa mmudzi mwa Yesaya, kwa mfumu yaikulu Kalumbu ku Kamphata mboma la Lilongwe ndi Mary Kaliati. Awiriwa akuti adakumana ali pasukulu ya Nkhoma pomwe onse ankaphunzira ndipo apa adali paulendo wopita kukaonerera masewero a timu ya Silver Strikers ndipo mwamwayi zidachitika kuti onse ankasapota timu yomweyo. Ine ndinkapita kukaonerera mpira ndiye patsogolo panga ndidaona munthu akulowera njira yomweyo. Pokhala munthu woti ndinkamuona pasukulu, ndidamuthamangira ndipo nditamufunsa komwe ankapita adandiyankha kuti adali paulendo wa kumpira, adatero Daniel. Iye adati apo awiriwo adayendera limodzi ndipo ali mnjira atazindikira kuti onse amakonda timu imodzi ubale udayambika pomwepo moti ankatengana nthawi zonse kukakhala mpira kukaonerera limodzi. Nditaona chidwi chake pampira komanso nditakhutira kuti zokonda zake ndi zanga ndi zofanana ndidaona chanzeru kuti tidzasungane ndipo nditamuuza, adagwirizana ndi maganizo anga,adatero Daniel. Mary adati iye ataona zomwe Daniel amakonda sadachotsere kuti adakumana ndi munthu yemwe angadzasungane naye popanda mavuto ndipo mwamaganizo akewo zidayendadi choncho mpaka pano akukhala limodzi ngati banja mokondwa. Zidangokhala ngati kuti ndife mapasa chifukwa zambiri zomwe ndimakonda, nayenso amakonda zomwezo monga kuleza ntima, khama pa zinthu ndi kukonda masewero ampira komanso timu yathu kukhala imodzi ndi chinthu chondisangalatsa kwambiri, adatero Mary. Awiriwa adamaliza zilinganizo zonse zoti anthu nkutengana ngati bambo ndi mayi ndipo pano ndi banja la ana atatu ndipo akuti anawonso akuyenda mmapazi mwa makolo kukonda timu ya Silver Strikers. Chikondi chomwe awiriwa ali nacho pa timu yomwe amasapotayi nchodabwitsa chifukwa akuti timuyi ikapanda kuchita bwino ngakhale chakudya onse awiri sachifuna mpaka kumatheka kugona nayo chakudya akuchiona.
16
Papa Wapereka Zipangizo Za Mchipatala Mdziko La Ecuador Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wapereka thandizo la zipangizo za mchipatala ku dziko la Ecuador. Malinga ndi malipoti a Vatican Radio, Papa wapereka thandizoli ngati njira imodzi yofuna kuchepetsa mavuto omwe dziko la Ecuador likukumana nao maka chifukwa cha mliri wa Coronavirus. Thandizoli ndi la zipangizo zothandiza anthu omwe akuvutika kupuma bwino kuti athe kupuma mosavutika. Bungwe la ma episkopi a Mpingo wa Katolika mdziko la Ecuador atsimikiza za nkhaniyi kazembe wa dziko la Ecuador kulikulu la Mpingo ku Vatican Jos Luis lvarez Palacio atalengeza kuti thandizoli latumizidwa kale ndipo kuti lifika mdzikolo masiku ochepa akubwerawa. Anthu 47,000 agwidwa ndi nthenda ya Covid 19 ndipo anthu 4,000 amwalira ndi nthendayi mdziko la Ecuador lomwe liri ndi chiwerengero cha anthu chokwana 17 million malinga ndi malipoti a unduna wa za umoyo mdzikolo. Thandizo la Papa Francisco ku dziko la Ecuador ndi limodzi mwa zithandize zomwe iye wakhala akupereka ku maiko osiyana-siyana omwe akhudzidwa ndi mliri wa Coronavirus. Mmbuyomu iye wapereka thandizo la zipangizo za mchipatala ku maiko a Italy, Romania, Spain, Syria, Israel, Zambia pongotchula ochepa.
6
T/A Kaphuka Alonjeza Kuthana ndi Miyambo Yokolezera Edzi Chipatala cha mpingo wa katolika cha Kasina mu dayosizi ya Dedza chinachita nawo mwambo wokumbukira matenda a Edzi pa dziko lonse wa chaka chino. Mwambo-wu wachitika lolemba pa bwalo la zamasewero la Nampala lomwe lili mdera la mfumu yaikulu Kaphuka. Mmau ake mkulu woyanganira zoyeza magazi pa chipatala cha Mission cha Kasina Mai Dorothy Chikafa ati nkoyenera kuti munthu aliyense adzidziwa momwe mthupi mwake mulili poyezetsa magazi. Tikupempha kwambiri abambo ambiri kuti azibwera kudzayezetsa magazi kaamba koti ngakhale anthu ali banja amatha kuthala ndi zotsatira zosiyana anatero mayi chikafa. Polankhulanso mfumu yaikulu Kaphuka ya mbomalo yomwe inali nawo ku mwambowu yati iyesetsa kulimbana ndi miyambo ina yomwe ikupitilira kukolezera kufala kwa kachilombo koyambitsa matenda a edzi ka HIV ndipo kuti aliyense yemwe apezeka akulimbikitsa miyambo yoyipayi mmudzi mwawo azilandila chilango chokhwima kuti wena atengerepo phunziro.
6
Kufumuka si kulakwa, olemekezeka! Nkhani ili mkamwamkamwa panopa ndi yoti nduna ya zaulimi, mthirira ndi chitukuko cha madzi, George Chaponda, kudzanso mkulu wa bungwe la Admarc, Foster Mulumbe, atule pansi maudindo awo kuti komiti yomwe Pulezidenti Peter Mutharika wakhazikitsa kuti ifufuze za nkhani ya chimanga chomwe boma lidagula kudziko la Zambia igwire bwino ntchito yake. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Chaponda wanenetsa kuti satula pansi udindo wake monga nduna. Nayenso Mulumbe wati sanenapo kanthu pankhaniyi. Chaponda wati sakuonapo chomwe adalakwa ngakhale kuti akukhudzidwa ndi nkhani yogula chimanga kuchokera kudziko la Zambia kuti chipulumutse anthu kunjala yomwe yagwa mdziko muno. Zomwe zikumveka nzakuti pakukhala ngati padalowa chinyengo malinga ndi mmene malonda a chimangawo adayendera. Izi zili choncho chifukwa mmalo mongogula chimangacho motchipa ku Zambia Cooperative Federation (ZCF) ogulitsa chimanga ku Zambia, boma la Malawi, kudzera ku bungwe la Admarc, lidaganiza zogula chimangacho pamtengo wodula pogwiritsa ntchito kampani yomwe si ya boma la Zambia yotchedwa Kaloswe Commuter and Courier Limited ngati mkhalapakati. Chifukwa chogwiritsa ntchito kampaniyo pogula chimanga chokwana matani 100 000, boma la Malawi lidasakaza ndalama zokwana K26 biliyoni zomwe lidakongola kubanki ya Eastern and Southern African and Development, lomwe limadziwikanso ngati PTA Bank. Achikhala kuti adangogula chimangacho ku ZCF, boma likadagwiritsa ndalama zokwana pafupifupi K15 biliyoni basi. Izi zikutanthauza kuti boma la Malawi lidasakaza ndalama zokwana pafupifupi K9.5 biliyoni zapamwamba pogula chimangacho kudzera kukampani ya Kaloswe Commuter and Courier Limited. Ho, zichulukirenji ndalama! Funso nkumati: Padali chifukwa chanji chosankhira njira yogula chimanga pamtengo wokwera chomwechi pomwe njira idalipo yopezera chimangacho pamtengo wotsika? Apa mpamene pakhota nyani mchira, nchifukwa chake Amalawi ambiri, kuphatikizapo a mabungwe osiyanasiyana akuganiza kuti pena pake payenera kuti padalowa chinyengowina ayenera kuti adanyambitapo kena kake! Ndikukumbukira nthawi ina yake Joe Manduwa, yemwe adali wachiwiri kwa nduna ya zaulimi nthawi ya Bakili Muluzi, ankayankha mlandundaiwala pangono kuti udali mlandu wanji poti ndi kale limene lija. Manduwa, mwa iye yekha, adatula pansi mpando wake wonona ponena kuti ankafuna kuti chilungamo chioneke bwinobwino pamlandu wake posatengera kuti wavala ministerial jacket (jekete ya uminisitala). Mwina a Chaponda ndi a Mulumbe, akadatengerapo phunziro pa zomwe adachita Manduwa potula pansi udindo kuti zofufuza ziyende myaa popanda zokayikitsa kapena zopingapinga. Ngati ofufuzawo sawapeza kulakwa pa zomwe zidachitikazo, sindikukayika kuti Pulezidenti Mutharika adzawabwezera pantchito zawo zofufuzazo zikadzatha.
10
Papa Wakhazikitsa Chaka cha Faustina pa Kalendala ya Mpingo Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wakhazikitsa chaka Faustina Woyera pa kalendala ya mpingo. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican izi zadziwika kudzera mu kalata yomwe bungwe lowona za chipembedzo ndi ma sakramenti ku likulu la mpingo ku Vatican latulutsa tsiku lolemba pa 18 May. Chithunzithunzi cha Faustina Woyera Kalatayo yati Papa Francisco wakhazikitsa tsiku la 5 October pa kalendala ya mpingo wa katolika kuti likhale chaka cha Faustina Woyera. Bungwe loona za Chipembedzo ndi ma Sakramenti kulikulu la Mpingo ku Vatican (Congregation for Divine Worship and the Discipline of the Sacraments) lomwe limatsogoleredwa ndi Cardinal Robert Sarah lolemba pa 18 May lalengeza kuti Papa Francisco wakhazikitsa chaka cha Maria Faustina Kowalska pa kalendala ya Mpingo (Liturgical calendar). Malinga ndi kalata ya bungweli Papa Francisco wakhazikitsa tsiku la 5 October chaka chilichonse kukhala chaka cha Faustina Woyera. Chochititsa chidwi pa nkhaniyi nchakuti nkhaniyi yadziwika pa 18 May tsiku lomwe Mpingo umakumbukira kuti papita zaka 100 pamene Papa Yohane Paulo Wachiwiri Woyera anabadwa ku Poland ndipo ndi Papa Yohane Paulo Wachiwiriyu yemwe adakhazikitsa Faustina kukhala Woyera mchaka cha 2000. Faustina adabadwa mchaka cha 1905 ku Poland ndipo anamwalira mchaka cha 1938.Iye adali kukhala ndi asisitere a chipani cha Amayi Maria a Chifundo (Sisters of Our Lady of Mercy) Faustina adali kusinkhasinkha za chifundo cha Mulungu chotumphuka kudzera mwa Ambuye Yesu. Mapemphero osiyana-siyana a Chifundo cha Mulungu komanso laMulungu la Chifundo cha Mulungu (Divine Mercy Sunday) ndi zipatso za moyo wa Faustina Woyera yemwe anali Virgo.
13
Anthu ku Liwawadzi Aponya Voti Anthu a ku ward ya Liwawadzi mdera la kumpoto kwa boma la Balaka aponya voti yofuna kusankha khansala wa deralo. Chisankho cha chibwerezachi chikudza kutsatira imfa ya yemwe anasankhidwa kukhala khansala wa derali pa chisankho chomwe chinachitika mdziko muno pa 21 May 2019. Malinga ndi mtolankhani wathu amene ali ku derali, anthu ochepa ndi omwe akupita kukaponya voti yawo pa chisankhochi zomwe zikupereka chikayiko chakuti anthu ochepa ndi omwe atenge nawo gawo poponya voti pa chisankhochi. Anthu amene akupikisana pa chisankhochi alipo asanu ndi mmodzi (6) omwe ndi a Precious chimtengo omwe ndi oyima powokha, a Falao Kambiri omwe akuyimira chipani cha Democratic Progressive (DPP), a Mervin Makwinja akuyimira chipani cha Freedom, a Harris Mhere omwe akuyimira chipani cha Mbakuwaku Movement for Development (MMD), a Ronald Mphepo omwe akuyimira chipani cha Peoples (PP) komanso a Obert Peter omwe akuyima pawokha. Malinga ndi dongosolo la bungwe loyendetsa chisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC), kuponya voti kwayamba 6 koloko mmawa ndipo kukuyembekezekanso kutsekedwa nthawi ikakwana 6 koloko madzulo ndipo pambuyo pake payambe ntchito yowerengera mavotiwo. Anthu okwana 2482 ndi omwe analembetsa mu kaundula wa voti pa chisankhochi.
11
Veteran hymnist Nyathole buried Victoria Nqabile Thole, celebrated locally for her hymn writing skills, was buried last week in Mzimba. Coincidentally, Nyathole, as she was fondly called, was the mother of the late singer and composer Griffin Mhango, who founded Kalimba Band. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Her touch on murals Nyatholes coffin Nyathole was the daughter of Reverand PZ Thole, whose compositions appear in the Tumbuka Hymn Book. She composed numerous spiritual songs, some of which have made it into the newer edition of Tumbuka Hymns. According to her grandson, current Kalimba Band leader Vita Chirwa, Nyathole was born in 1924. She initially worked for Malawi Young Pioneers (MYP) in Mzuzu, then was transferred to Nansawa Training Base where she worked as matron under former president Bakili Muluzi who was then principal of the base. She eventually went to Ghana and later, Germany for technical training and when she returned, she helped to shape various Malawi women into productive citizens, he said. According to Chirwa, Nyathole was later transferred to MYP Headquarters in Kanjedza where she continued with her noble work until her retirement in 1975. She later became one of president Kamuzu Bandas nominated MPs for Mzimba and served two successive terms after which she quit politics and devoted her time to serving the Lord through singing and preaching, he said. She came from Elangeni Village in Mzimba where she was laid to rest.
15
Mgwedegwede mzipani wakula Mgwedegwede womwe wayanga chipani cholamula cha DPP ndi zina zotsutsa boma monga UDF ndi MCP ungabale zisankho zabwino mu 2014, waunikira katswiri pandale yemwenso ndi mphunzitsi wa zandale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkuluyu, Blessings Chinsinga, wati umu ndi mmene zimayenera kukhalira maka zisankho pulezidenti komanso a phungu zikayandikira. Apa Chinsinga wati ichi ndichiyambi chabe ndipo pena zidzifika pa alindi mwana agwiritse, koma anthu adekhe mpaka madzi atadikha kuopa kumwa matope. Iye wati misamuko ikuchitika mzipani ndi imene itamangenso zipani mwatsopano, kuzisanduliza zolimba. Sabata yatha, aphungu anayi a chipani cholamula cha DPP adauza nyuzipepala ya Weekend Nation kuti akhazikitsa gulu lomwe lidziunikira pomwe pakhota nyani mchira mchipanichi. Gululi lomwe woliyankhulira ndi phungu wa dera la kumwera kwa kwa mzinda kwa Blantyre, Moses Kunkuyu, lati pali aphungu 30 ndipo lidziuza mtsogoleri wa dziko lino Bingu wa Mutharika chindunji, osati phula lomwe ena omuzungulira akhala akukumata. Ku UDF matatalazi sakutha pomwe chipanichi chagawika pawiri. Akatakwe monga Humphrey Mvula ndi Sam Mpasu mwa ena ali pambuyo pa Friday Jumbe yemwe akugwiriziza udindo wa pulezidenti wa chipanichi kuchokera pomwe mtsogoleri wakale Bakili Muluzi adalengeza kuti wasiya ndale. Ndipo gulu lina kuli zikanthawe monga mlembi wachipanichi, Kennedy Makwangwala, Geroge Nga Ntafu, Ibrahim Matola kudzanso aphungu 15 a chipanichi ku Nyumba ya Malamulo ali pambuyo pa mwana wa Atcheya Atupele Muluzi. Pomwe ena akadziotche monga yemwe adali wachiwiri kwa mneneri wachipanichi, Ken Msonda, wasamuka mu UDF ndipo walowa chipani cha wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda cha Peoples Party [PP]. Henry Phoya, yemwe adachotsedwa mchipani cha DPP mmbuyomu nayenso waumanga ndipo walowa MCP. Phoya adakhalapo nduna mmaboma a UDF ndi DPP. Chinsinga wati zonsezi ndizosadabwitsa chifukwa zisankho zikayandikira andale amasinkhasinkha kolowera kuti adzachite bwino. Apa aliyense amayangana mazira omwe angamubalire kanthu akawafungatira. Pofika mu Juni zikhala zambiri zikuchitika pandale. Izi zikuyenera kuchitika pano chifukwa zitati zizichitika mu 2013 woponya voti angasokonekere koopsa. Pounikira pa andale angapo omwe akwawira kuzipani zina, iye wati kuyenda kwa anthuwa kungakhale ndi tanthauzo, mwinanso ayi. A Msonda adatsanzika kuti akukalera zidzukulu, koma pano akuti alowa kuchipani cha PP. Izi sizingapatse anthu chikhulupiriro mwa mkuluyu. Zomwe achita a Phoya zadabwitsa ambiri, ngakhale inenso. Koma izi mwina zingasinthe zingapo pandale malinga ndi momwe anthu amachionera chipani ca MCP. Nkutheka a Phoya abweretsa zingapo ku MCP chifukwa cha kulimba mtima kwawo komwe adaonetsa potsutsa mabilo oipa mnyumba ya malamulo, akutero Chinsinga. Baziliyo Kajani wa mmudzi mwa Chaponya kwa T/A Mzukuzuku mboma la Mzimba wati, sakuganiza kuti mpungwepungwewu ungakonze masankho a mu 2014 kaamba koti nthawi ino ndiyoyenera kuti zipani zotsutsa zizichita ntchito yachitukuko. Pandale pamafunika kukhala mgwirizano ncholinga chotukula dziko, osati zikuchitikazi zomwe sizingatipindulire. Zipani zotsutsa zikuyenera kupereka thandizo kuchipani cholamula, maka pankhani ya chitukuko, zomwe sizikuchitika. Izi zingadzabale ziwawa mu 2014, adatero Kajani. Frank Mpuno wa mmudzi mwa Yoyola kwa T/A Masasa mboma la Ntcheu wati masankho abwino mu 2014 angadze ngati akuluakulu a zipani akudziwitsa anthu za zomwe zikuchitikazo. Amatifuna panthawi ya kampeni basi. Mukadzamva kuti sitikavota osamadabwa, akutero Mpuyo. Mgwedegwede mu UDF udayamba mmwezi wa Okutobala 2011 pomwe Atupele Muluzi adabwera poyera ndikulengeza kuti iye adzaima nawo pa mpando wa pulezidenti mchaka cha 2014. Izi sizidakomere komiti yaikulu mchipanichi ndipo akuluakulu mmenemo adati izi nzosemphana ndi malamulo achipani. Apa chipanichi chidaitanitsa Atupele kuti akaonekere ku komiti yosungitsa mwambo yachipanichi koma iye adakana ndipo chidamuchotsa. Kugwedezekaku kudabukanso pa 21 Disembala 2011 pomwe mlembi wachipanichi Kennedy Makwangwala adalemba kalata yothetsa maudindo onse. Kulumana ku MCP kuli pakati pa mlembi wa chipanichi, Chris Daza, ndi mtsogoleri wachipani, John Tembo. Daza wakhala akulankhula poyera kuti Tembo akuyenera kusiira utsogoleri wachipanichi mmanja mwa achinyamata, zomwe zakhala zikutsutsula Tembo. Mmwezi wa Sepitembala chaka chatha, komiti yaikulu ya chipanichi idachotsa Daza kuti sindiyenso mlembi wachipanichi koma bwalo lamilandu lalikulu ku Lilongwe mmwezi wa Okutobala lidabwezeretsa Daza pa mpandowo. Pano chipanichi chalandira Phoya. Ku DPP kwachoka aphungu angapo monga Jennifer Chilunga wa ku Zomba Nsondole yemwe adalowa chipani cha PP komanso Grace Maseko wa ku Zomba Changalume.
11
Anatchereza Kodi nditani? Gogo Natchereza Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 25 ndipo ndakhala pa chibwenzi ndi mnyamata wina kwa zaka zinayi. Mnyamatayu ali ndi nyumba yake ndipo akugwira ntchito yabwino pa kampani ina yopanga mafuta wophikira mu mzinda wa Lilongwe. Tidagwirizana kuti tidzakwatirana, koma mnzanga ndikamufunsa za banja amangozengereza. Kumuuza kuti apite kwathu akaonekere amangoti ndidzapitabe mpaka zaka nkumatha. Gogo, kodi pamenepa nditani popeza mnyamatayu ndimamukonda ndi mtima wanga wonse? JPJ Lilongwe JPJ Nkhaniyi siyachilendo. Atsikana ambiri amadandaula kuti anyamata adawauza kuti adzawakwatira, koma akuchulutsa njomba. Mnyamata wofuna banja sasowa. Sazengereza mwayi wokaonekera kwa makolo a mtsikana ukapezeka. Anyamata ambiri safuna banja. Amangofuna kugona ndi atsikana moti chakumtima kwawo chikapwa amawasiya nkupeza ena kumene kuli kulakwa. Muunikeni bwino bwenzi lanu kuopa kudzanongoneza bondo mtsogolo. Paja amati mtsinje wa tinkanena udakathera msiizi. Gogo Natchereza Makolo ake akukana Ndine mtsikana wa zaka 23 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Mnyamata wina adandiuza kuti akundifuna chibwenzi ndi cholinga choti adzandikwatire mtsogolo ndipo ndidalola. Koma makolo ndi abale ake amamukaniza kuti asakwatiwe ndi mtsikana wa mwana moti panopa zochita za bwenzi langa sindikuziona bwino. Ndikamuimbira foni nthawi zina sayankha. Ndikamutumizira uthenga pa WhatsApp umaonetsa kuti waona, koma sayankha. Gogo, mutu wanga wazungulira nditani? APA APA Usadandaule, ungozivomereza. Makolo ena amaletsa ana awo kukwatiwa ndi atsikana oti adaberekapo kumene kuli kulakwa. Anthu awiri akakondana zenizeni saona zoti wina ali ndi mwana kapena ayi. Apa zikuonetsa kuti mnyamatayo wamvera zonena za makolo ake. Choncho kutha kukhala kovuta kuti chibwenzi chanu chipitirire. Limba mtima, mudzapeza mnyamata wokukondani posatengere kuti mudaberekapo. Usada nkhawa. Chachikulu ndi kudekha. Sunga khosi mkanda woyera udzavale.
12
Tauni ya Mangochi Idakali ndi Misewu ya Fumbi Wolemba: Thokozani Chapola Phungu wa kunyumba ya malamulo wadera la pakati mboma la Mangochi, Victoria Kingstone wadandaula kaamba ka kuipa kwa misewu yozungulira tawuni ya Mangochi. Kingstone: Ndapempha kale ku boma ndipo a nduna alonjeza kuti akonza misewuyi Padakali pano misewuyi ndi ya fumbi ndipo nthawi ya mvula imakhala ndi matope kaamba koti ilibe phula zomwe malinga ndi iye sizoyenera mu tawuni yomwe posachedwapa ikhale mzinda. Pamenepa iye wati wakambirana ndi a unduna woona za maboma aangono ndi chitukuko chakumidzi kuti misewuyi ikonzedwe poyika phula. Nditapita ku nyumba ya malamulo ndinapempha ndipo olemekezeka a Ben Phiri omwe ndi a nduna a za maboma aangono andiyankha kale kuti mzaka zikubwerazi misewu yonse ya pa boma ikhala ndi tala, anatero Kingstone Kingstone amalankhula izi pa msonkhano womwe anachititsa pa sukulu ya pulaimale ya Milambe womwe cholinga chake chinali kuthokoza anthu omwe anamusankha pa udindowu. Iye wati zimenezi zithandizanso popititsa patsogolo ntchito zokopa alendo mbomalo polingaliranso kuti boma lili ndi malingaliro omanga hotela yapamwamba komanso bwalo la ndege mbomalo. Izi zikudza patapita pafupifupi chaka pomwe anthu ochita bizinesi ya kabaza mbomalo anachita ziwonetsero pofuna kukakamiza akuluakulu a khonsoloyo kuti akonze misewu yozungulira tauniyi zomwe sizinachitikebe mpakana padakalipano. Pa za tsikuli iye wati anawona kuti ndi koyenera kuti apite ku dera kwake ndi kukathokoza anthu omwe anamusankha pa udindowu ndi kudya komanso kusangalala nawo limodzi. Iye anati achita miyambo ya ngati imeneyi mmalo onse oponyera voti a mu dera lake omwe alipo okwana 25. Patsikuli mwazina iye anakumbutsanso anthuwa za malonjezo ake omwe anali akuchita mu nyengo yokopa anthu kuti azamuvotere zomwe anawatsimikizira kuti zichitikadi. Chimodzi mwa icho ndinawalonjeza amayi kuti theka la malipiro anga lizipita kwa iwowo. Pano ndikuwatsimikizira kuti ndalama zomwe zikubwera mwezi uno theka lake ndiwapatsa kuti azichitira bizinesi, anatero Kingstone.
11
DPP madzi afika mkhosiMuntali Zipani zotsutsa zati nzodabwa kuti boma lagundika kukweza anthu ogwira ntchito mboma, komanso kulipira mafumu nthawi ino ya kampeni pamene mmbuyo monsemu akhala akudandaula koma samathandizidwa. Mwezi umodzi wokha boma lakweza apunzitsi 20 000, apolisi 7 000 moti padakali pano lili mkati molipira mafumu 42 000 ndalama za miyezi 6 zomwe zidatsalira chaka chatha. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Otsutsa akuti chipani cha DPP chikunyengerera mafumu kuti adzachivotere Boma ligwiritsa ntchito K832 miliyoni polipira mafumuwo. Zipani zotsutsa zati zikuona kuti chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) chikungofuna kugwiritsa ntchito ndondomeko zaboma pochita kampeni. Koma mneneri wa boma Henry Musa adati sakuonapo vuto lililonse chifukwa palibe lamulo lomwe limafotokoza nthawi yokwezera anthu pantchito kapena kulipira mafumu. Anthu ogwira ntchito mboma akhala akukwezedwa, komanso mafumu akhala akulipidwa mmaulamuliro onse omwe akhalapo. Choseketsa nchoti palibe lamulo lomwe lifotokoza nthawi yokwezera ogwira ntchito kapena kulipilira mafumu, adatero Mussa. Mfumu Chindi ya ku Mzimba, Chadza ya ku Lilongwe ndi Dambe ya ku Neno yatsimikizira Tamvani kuti mafumu alandira mswahara wa June mpaka December 2018. Mneneri wa unduna wa maboma angonoangono ndi chitukuko cha mmidzi Muhlabase Mughogho adati ndalamazi nzomwe boma limayenera kuonjezera pa mswahara wa mafumuwo kuchokera pomwe Nyumba ya Malamulo idakweza mswaharawo. Nyumba ya Malamulo idavomereza kuti mswahara wa mafumu ukwere ndi K100 pa K1 000 iliyonse koma kuyambira mwezi wa June mpaka December 2018, mafumu samalandira ndalama yoonjezerayo ndiye akupatsidwa pano, adatero Mughogho. Mlembi wamkulu wa chipani cha UTM Patricia Kaliati adati ndiwodabwa kuti kuonjezera mswahara wa mafumu kutavomerezedwa, aphungu adaika mbajeti ndiye nchifukwa chiyani samapatsidwa ndalama zonse? Apatu ndikuona kuti boma limazunza dala mafumu kuti pambuyo pake adzawatseke mmaso nthawi ya kampeni. Uku nkulakwa chifukwa panthawiyo akadatha kupanga ndondomeko zina, adatero Kaliati. Koma iye adati ndiwokondwa kuti mafumuwo alandira ndalama zawo zomwe adagwirira ntchito ngakhale azilandira nthawi yolakwika. Kaliati adati ndalamazo nzofunika kuonjezeranso chifukwa nzochepa poyerekeza ndi ntchito yomwe mafumu amagwira. Mawuwa akugwirizana ndi omwe adalankhula mtsogoleri wa chipani cha Malawi Congress (MCP) Lazarus Chakwera pa msonkhano wake wa ku Kasiya kuti mswahara wa mafumu ndiwofunika kuganiziridwa, komanso azipatsidwa mu nthawi yake. Mneneri wa MCP Maurice Munthali adati zomwe zikuchitikazi zikusonyeza kuti chipani cha DPP chapanikizika chifukwa cholephera kuchita zinthu mu nthawi yake. Kodi aphunzitsi amayenera kukwezedwa liti? Nanga mafumu amayenera kulandira liti ndalamazo? Panopa madzi ali mkhosi ndiye akufuna awanamize? Ayi sititero, adatero Munthali. Iye adati aphunzitsi ndi apolisi omwe akwezedwawo awonetsetse kuti zofunikira zonse zatheka kuti wina asadzawakanire mawa, komanso mafumu alandire ndalama zawo koma zisawasokoneze pokavota, adatero Munthali. Mlembi wamkulu wa chipani cha United Democratic Front (UDF) Kandi Padambo adati boma lifotokozere bwino mafumu ndi anthu komwe kwachokera ndalamazo chifukwa ena akhoza kumaona ngati DPP ndiyo yapereka. Katswiri pa ndale George Phiri adati Mussa akunena zoona kuti palibe lamulo lofotokoza nthawi yokwezera munthu kapena kumulipira malipiro ake, koma pali ndondomeko zina zomwe zimayenera kutsatidwa zomwe akuona kuti sizidatsatidwe. Choyamba munthu amakwenzedwa akagwira bwino ntchito. Nzowona kuti aphunzitsi ndi apolisi onsewa akugwira bwino ntchito yawo? Chachiwiri adziwa liti kuti akuyenera kukwenzedwa pa ntchito? adatero Phiri. Iye adati nkhaniyi ikapanda kuunikidwa bwino, idzabweretsa mavuto aakulu patsogolo makamaka ngati sipakhala makalata a umboni oti anthu akukwezedwadi pa ntchito.
11
Atumiki a Dayosizi ya Dedza Asulidwa za Chibalalitso Wolemba: Thokozani Chapola Mkulu owona za utumiki mu dayosizi ya DEDZA bambo Peter White, lachisanu lapitali ati ati msulo wowakonzekeretsa ansembe ndi a sisiteri za chaka cha chibalalitso cha mpingo umathandiza kuzindikiritsa atumikiwa ntchito yomwe ali nayo mu mpingowu. Bambo WHITE omwe ndi mkulu oyanganira za utumiki mu dayosiziyi amalankhula izi pa maphunziro a tsiku limodzi omwe anakonzedwa ndi office yoona za mabungwe a utumiki wa apapa mu dayosiziyi. Tinawona kuti ndi kofunika kuwasula atumikiwa chifukwa iwo ndi amene amakhala patsogolo kutsogelera ma parishi awo choncho akamvetsa bwino za chibalalitso cha mpingo zikathandizanso pomema akhristu kuti apereke molowa manja pa tsikuli, anatero bambo White. Mmawu ake mkulu wa mabungwe a utumiki wa apapa mu dayosizi ya DEDZA, bambo PETER MADEYA ati office yawo inakonza maphunzirowa kuti ansembe athe kuzindikira bwino za chibalalitso cha mpingo komanso athe kuzindikiritsa akhristu zimene a Papa akufuna mu uthenga wawo wa chaka chino. Zithandizanso atumikiwa kumvetsa zambiri za mabungwe a utumiki wa a Papa, anatero bambo Madeya. Mwambo waukulu wa chaka cha chibalalitso mu mpingo wa katolika mdziko muno uchitikira ku St. Pius Parish mu arkidayosizi ya Blantyre pa 13 October 2019.
13
Anjatidwa Kamba Kogona ndi Galu Apolisi mboma la Mchinji amanga mamuna wina wa zaka 20 zakubadwa Glandisoni Feliyala kaamba komuganidzira kuti anachita zadama ndi galu. Wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo, Inspector Kaitano Lubrino wati mkuluyu anapezeleredwa ndi mkazi wake akuchita zadama ndi galu usiku wapa 27 December 2019. Mkazi wake atamuuza kuti akagone anakana ndipo mayiyo anakalowa yekha mnyumba koma atawona kuchedwa anaganiza zotuluka kuti awone chomwe chachitika kwa mamuna wakeyo ndipo ndi pomwe anamupeza akugona ndi galu. Anayitana Anthu ena oyandikana nawo ndipo anthuwa anamugwira mkuluyu ndi kumupititsa ku polisi, anatero Inspecto Lubrino. Inspector Lubrino wati a Feliyala anauza apolisi kuti iwo adawudzidwa ndi nsinganga wina wa ku Karonga kuti ngati akufuna kulemera agone ndi galu ngati chizimba. A Glandisoni Feliyala ali ndi zaka 20 ndipo amachokera mmudzi mwa Malewa, T/A Gumba mboma la Mchinji ndipo akuyembekedzereka kukawonekera ku bwalo la milandu posachedwapa.
14
Papa Wati Akhristu Apemphelere Atsogoleri Wolemba: Glory Kondowe 9/08/francis.jpg 308w" sizes="(max-width: 512px) 100vw, 512px" />Wapempha anthu apemphelere atsogoleri-Papa Francisko Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko lero wati ndi kofunika kumapempherera atsogoleri a boma komanso a ndale. Iye walankhura izi pamwambo wa misa yomwe anatsogolera ku likulu la mpingowu ku Vatican. Malinga ndi Papa Francisko koyenera kumawapemphelera atsogoleriwa nthawi zonse ndi cholinga choti atumikire anthu awo moyenera poyanganira za udindo omwe amasenza. Mwazina mtsogoleriyu anagwira mau a mkalata yoyamba ya Paulo Woyera kwa Timoteyo 2 ndime ya 1 mpaka 8 onena za kufunika kopemphelera mafumu ndi onse olamulira. Iye wati nthawi zina atsogoleri amayamikiridwa komanso kunyozedwa ndipo Papa wati zimenezi sizinasiye malo popeza ngakhale atsogoleri a mpingo monga ansembe, a episikopi komaso asiteri amayamikilidwa komanso kunyozedwa choncho ndi kofunika kuwapemphelera nthawi ndi nthawi kuti apitilize ntchito zawo ndikukhala atsogoleri abwino nthawi zonse.
13
Milandu Yogwililira Yakwera Mboma la Zomba Mkulu wa apolisi chigawo chaku mmawa kwa dziko lino Commissioner Arlene Baluwa wapempha anthu mdziko muno kuti athandizane ndi polisi pa ntchito yothana ndi mchitidwe wogwilira ana mdziko muno. Wati milandu yogwililira yakwera kwambiri-Baluwa Commissioner Baluwa amayankhula izi kwa Group Village Headman Chingondo, mdera la mfumu yayikulu Mwambo mboma la Zomba pa msonkhano womwe apolisi anakonza okambirana ndi anthu za momwe angathetsere nkhanza zogwilira ndi kuzunza anthu okalamba kuphatikizapo anthu a khungu la chi-albino. Commissioner Baluwa wati nkhanza zogwilira zikuchulukira mboma la Zomba kamba koti mchaka cha 2019 milandu yokwana 97 idalembetsedwa kusiyana ndi milandu 68 yomwe idalembetsedwa chaka cha 2018. Choncho Iwo apempha anthu kuti adzikanena ku polisi za nkhadza zogwililira zomwe zikuchitika pakati pa magulu okhudzidwawa. Pa nkhani ya belo ya polisi Commissioner Baluwa wati anthu akuyenera kudziwa kuti beloyi ndi yaulele kotero sakumayenera kupereka ndalama ina iliyonso kwa apolisi pomwe apempha belo.
14
Titsirika nkhalango zonseNganga Gulu lina la asinganga ku Dedza ladzithemba kuti likhoza kuteteza nkhalango za dziko lino ndi chambu koma akuluakulu a boma ati zonse zili mmanja mwa asingangawo kuti awakhutitse kuti njirayo idzayenda. Mkulu woyanganira za nkhalango mdziko muno Clement Chilima adati nthambiyo ndi yokonzeka kupereka mpata kwa asingangawo kugwira ntchito ndi asingangawo poteteza nkhalangozo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kodi nsupa ndi zitsamba zingathandize kuteteza nkhalango? Iye adati chomwe asingangawa angachite nkulembera kalata nthambiyo kuti ifunse upangiri pena ndi pena koma ganizo lawolo ndi lolandiridwa ngati silikuphwanya malamulo. Mmagwiridwe a ntchito yathu, timalandira aliyense yemwe ali ndi njira yothandiza. Ngati asingangawa akunena zoona ndipo njira yawoyo siyikuphwanya malamulo, abwere tiwapatsa mpata, adatero Chilima. Mkulu wa nthambi yoteteza nyama za kutchire Brighton Kumchedwa adati sanganeneretu mwa ndithendithe kuti chambu ndiye yankho koma adati gulu la asingangalo ndilolandiridwa ngati likudziwadi njira yomwe ingathandize kuteteza nkhalango. Ntchito yathu ndi yogwira ndi anthu ndiye ngati papezeka ena omwe akuti ali ndi njira yomwe ingathandize, chowaletsera nchiyani? Atatipeza nkutifotokozera bwinobwino, ndipo titamvetsa, tikhoza kuona kuti tingagwire nawo bwanji ntchito, adatero Kumchedwa. Iye adati mdziko muno muli nkhalango 84 zomwe zimafunika chitetezo chifukwa mitengo ndi nyama zopezeka mmenemo zikutha mosakhala bwino chifukwa cha mbala. Gulu la asingangali ndi lochokera mboma la Dedza ndipo lanenetsa kuti chambu chikhoza kugwira ntchito yoteteza nkhalango kuposa ntchito ya alonda ndi asilikali. Nthambi ya za nkhalango ndi nyama zopezeka mmenemo, itaima mutu ndi mchitidwe opha nyama komanso kudula mitengo mozemba, idalemba alonda omwe amathandizana ndi asilikali kuteteza nkhalango ndi nyama. Woyanganira ndi kulangiza asinganga pantchito yawo mboma la Dedza, Gulupu Ntambeni Chinyamula adati kupatula chidima, ophotchola mnkhalango akhoza kukakamiraa mpaka kugwidwa momwemo. Chambu nchamphamvu zedi chikhoza kugwira munthu yemwe amafuna kukasokoneza mnkhalango mpaka kugwidwa momwemo nkulandira chilango choyenera, adatero Chinyamula. Pulezidenti wa asinganga a mdziko muno Frank Manyowa adati nzotheka kuteteza nkhalangozi potsirika nkhalangozo ndi chambu mmalo modalira alonda ndi asilikali. Ndi chambu, tikhoza kuteteza nkhalango zonse zomwe zikusowa chitetezo kuti owonongawo asamazione powakantha ndi chidima ndipo akhoza kulephera kupanga upandu omwe adakonzawo, adatero Manyowa. Iye adati asinganga ali ndi njira zambiri zomwe akhonza kulangira anthu oononga nkhalango ndipo zilangozo zikhoza kuwapatsa mantha moti sangalakelake kubwerera kunkhalango. Manyowa adati asinganga zimawapweteka nkhalango zikamaonongeka chifukwa kasupe wa ntchito yawo wagona mmenemo. Timalimbikitsa kuteteza nkhalango chifukwa ndiko timapeza mankhwala athu. Boma lakhala likuyesetsa kuteteza nkhalango koma zikuwoneka kuti zikuvuta koma asinganga akhoza kukwanitsa ndi chambu, iye adatero.
19
Mkazi wansanje achekacheka mnzake Bwalo la milandu la majisitireti ku Mchinji masiku apitawa lidalamula kuti mayi wansanje amene adachekacheka mayi mnzake ndi mpeni pakhosi ndi kunkhope akagwire jere la miyezi 12 koma lidamumasula ponena kuti asadzapezekenso ndi mlandu wina kwa chaka chimodzi ndi theka. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Woimira boma pamilandu, Thom Waya, adauza bwalolo kuti mkazi wansanjeyo, Chimwemwe Fanizo, wa zaka 21, adafuna kuvulaza mwana wa mkazi mnzake wa miyezi 7 ndi mpeni ati popeza mwamuna wake ankapereka thandizo kwa mwanayo. Wasiya kuonetsa mabala ake mchipatala Waya adati mpeniwo udasempha mwanayo yemwe adali kumsana ndi kulunjika pakhosi la mayi ake. Mbereko yomwe adaberekera mwanayo idamasuka moti adagwa pansi ndipo achisoni adamutola ndi kuthawa naye. Izi sizidakondweretse Fanizo, yemwe adalikumba liwiro kuthamangitsa munthu amene adathawitsa mwanayo, mpeni uli mmanja. Komatu apa nkuti mkaziyo atamuchekacheka mnzakeyo malo anayi. Anthu adamugwira ndipo adapita naye kupolisi pamodzi ndi wovulazidwayo. Izi zidachitika mmawa wa pa 6 January pa Mkanda Trading Centre. Apolisi adamutsekulira mlandu wovulaza munthu, womwe womangidwayo adauvomera pamaso pa woweruza, majisitireti Rodwell Meja. Malinga ndi Waya, bwalolo silidachedwe kugamula mlanduwo chifukwa woimbidwa mlandu sadatayitse khotilo nthawi povomera kulakwa. Podandaulira bwalolo kuti limuganizire popereka chilango, Fanizo adati adapalamula mlanduwo chifukwa adachita kuputidwa ndi wodandaulayo, Tsala Wasiya, pokhala pachibwenzi ndi mwamuna wake. Pogamula mlanduwo, Meja adati bwalo lake lidamupeza ndi mlandu wovulaza ndipo ayenera kulangidwa molingana ndi malamulo a dziko lino, koma adapereka chilango chosakhwimacho poganizira kuti adachita kuputidwa komanso poti sadatayitse bwalolo nthawi povomereza kulakwa kwake. Meja adapereka chilango choti Fanizo akaseweze chaka chimodzi kundende koma adati kundendeko sapitako bola asapezekenso ndi mlandu kwa miyezi 18. Adamulola kuti azipita kwawo, mlandu watha. Adatinso ngati sakukhutira chi chigamulocho ali ndi ufulu kuchita apilo. Msangulutso udacheza ndi Wasiya, yemwe ali ndi zaka 20, kuti umve mbali yake ndi mmene zidakhalira kuti zifike mpakana kuvulazidwa chonchi. Iye adati adalidi paubwenzi ndi Daniel Nkhomo ndipo ubwenziwu utafumbira adapezeka ndi pakati. Iye adati ngakhale awiriwa sadalowane, Nkhomo adali kupereka chisamaliro chonse chomwe munthu oyembekezera amafuna mpaka mwana adabadwa. Koma ndidadabwa kuti pomwe mwana wanga adakwanitsa sabata zitatu, abambowa adakatenga mkazi wina kwa Msundwe ndipo adasiya kupereka chithandizo, iye adatero. Wasiya adati koma patadutsa miyezi iwiri bamboyu adayambiranso kuthandiza mwana wakeyu ndipo awiriwa amatchayirana lamya mwanayu akadwala zomwe sizimamkomera mkazi mnzakeyo. Tsiku lina ndidatumiza uthenga palamya kuti andiimbire kaamba koti mwana adali atadwala matenda otsekula mmimba. Mkazi wakeyu ndiye adandiimbira ndi kunditukwana, Wasiya adatero. Iye adati mphuno salota sadadziwe kuti Fanizo adali ndi mangawa ndipo adakagula mpeni ndi kukanoletsa kumatchini ndi cholinga chofuna kuthana naye. Wasiya adati patsikuli adali akuchokera kumsika ndipo Fanizo adamutchingira kutsogolo. Adandifunsa kuti bwanji ndimaimba lamya ya mwamuna wake? Bwanji adandisiya ine nkutenga iyeyo ngati ndili naye mwana wake? Nkudzati ndipanga za iwe, pompo mpeni sololu kuti abaye mwana kumsana. Mpeniwu udafikira pakhosi panga, adalongosola Wasiya Iye adati koma adali wodabwa kuti ngakhale adavulazidwa chomwechi Fanizo ndi mfulu ndipo adampititsa kwawo. Msangulutso udachezanso ndi Wasiya Titus, bambo wa mayi wovulazidwayu. Iye adati sakudziwa kuti mlanduwu uli pati kaamba koti atafufuza kupolisi ya Mchinji adauzidwa kuti Fanizo adamasulidwa ndi abwalo la milandu. Abwalo la milandu sadamve mbali ya mwana wanga yemwe sakupezabe bwino, kodi adamtulutsa bwanji ife okhudzidwa kulibe? Komabe ndipita konko kuti ndikamve umo zidayendera, adatero Titus. Pakalipano Wasiya wanenetsa kuti zivute motani akufuna mwamunayu amukwatire basi. Ine ndikufuna mwamunayu andikwatire chifukwa wandipatsitsa mabala, moti amuna ena sadzandisiriranso ayi. Ndipo mkazi wakeyu achita bwanji nsanje ndi ine, popeza ine ndiye ndidali woyamba ndipo ndimafunika kuchita nsanjezo ndineyo osati iyeyo wachiwiri ayi, adalankhula motsindika Wasiya. Pomwe Msangulutso udacheza ndi mwamunayo Lachinayi lapitali palamya, iye adati Wasiya adali mkazi wachibwenzi pomwe Fanizo adali wapanyumba.
7
Radio Maria Yalimbikitsa Omvera Ake Kuti Asatope Kuithandiza Mnyengo ya Coronavirus Radio Maria Malawi yalimbikitsa omvera ake, kuti asasiye kuthandiza wayilesiyi ndi thandizo lililonse lomwe angakhale nalo, kuti ntchito zake, zipitilire kuyenda bwino pomwe matenda a COVID -19 ayimitsa ntchito zambiri mdziko muno. Phiri: Coronavirus wayimitsa zokonzekera zonse Mkulu oyendetsa ntchito za wayilesiyi Louis Phiri, ndiyemwe wanena izi pomwe amalankhulapo pa momwe matendawa asokonezera zokonzekera za nyengo ya Mariatona yomwe imayenera kuyamba la Mulungu likudzali pa 3 May. Iye wati zokonzekera za nyengoyi zidayima kaye mpaka mtsogolomu, ndipo pano akhristu komanso ena onse akufuna kwabwino omwe amakonda kumvera wayilesiyi, akuyenera kuti atenge udindo waukulu othandiza wailesiyi kuti ntchito zake zipite patsogolo. Kuno ku Radio Maria tinali ndi malingaliro oti tikatsegulire Mariatona ku Lutchenza koma chifukwa cha mliri wa Coronavirus wu takanika kutero, anatero Phiri.
13
Papa Walengeza Zakusintha kwa Tsiku la Chaka cha Achinyamata Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco walengeza kuti chaka cha achinyamata (World Youth Day) chidzachitike kutsogoloku osati mmene adakonzera poyamba. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa Francisco wavomereza kuti Chaka Cha Achinyamata (World Youth Day) komanso Chaka Cha Mabanja (World Meeting of Families) zisachitike mmene adakonzera poyamba malinga ndi nthenda ya COVID-19. Uthengawo wati malinga ndi mmene zinthu ziliri padakali pano, Chaka Cha Mabanja chomwe chimayenera kudzachitika mwezi wa June 2021 ku Rome, chidzachitike mwezi wa June mchaka cha 2022 ku Rome komweko ndipo kuti Chaka Cha a Chinyamata chomwe chimayenera kudzakhalapo chaka cha 2022 ku Lisbon mdziko la Portugal chidzachitika mu August mchaka cha 2023 ku Portugal komweko. Malinga ndi uthengawo, mliri wa Coronavirus mwa zina wasokoneza zokonzekera zomwe zimayenera kukhala zitayamba kuchitika mma Diocese a Mpingo wa Katolika pa dziko lonse komanso zokonzekera zomwe zimayenera kukhala zitayamba kuchitika padakali pano kulikulu la Mpingo ku Vatican. Chaka Cha Mabanja chimasonkhanitsa pamodzi mabanja a chikatolika kuchokera mbali zonse za dziko la pansi ndi cholinga chofuna kukondwerera moyo wa banja pakati pa mamuna ndi mkazi ndipo izi zinayamba mchaka cha 1994 pamene Chaka Cha a Chinyamata chimasonkhanitsa a chinyamata a Mpingo wa Katolika kuchokera mbali zonse za dziko la pansi pofuna kulimbikitsa a chinyamatawa pa moyo wao wa chikhristu. Papa Yohane Paulo Wachiwiri Woyera ndiye adayambitsa Chaka Cha a Chinyamata mchaka cha 1985.
14
Ayamba kugawa makuponi Nduna ya malimidwe Joseph Mwanamvekha yapempha alimi kuti asagulitse makuponi awo amene boma lidayamba kupereka Lachinayi. Ndunayo idakhazikitsa ntchito yopereka makuponi 4 miliyoni kwa alimi 1 miliyoni ogulira mbewu ndi feteleza pasukulu ya Mtaya mboma la Balaka. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Nduna ya malimidwe Joseph Mwanamvekha adalangizanso mafumu ndi ena okhudzidwa ndi kugawa makuponi kuti apewe kuba ndi chinyengo pantchitoyi monga zakhala zikukhalira mmbuyomu. Ndikunena pano, anthu 58 amene adagwidwa pamilandu ya makuponi chaka chatha. Amene ayerekeze kuba makuponi, lamulo lidzagwira ntchito, adatero Mwanamvekha. Iye adapempha alimi kuti ayambe kukonza mminda yawo kuti azabzale ndi mvula yoyamba chifukwa feteleza afika kumadera mnthawi yake. Chaka chino, makampani amene akugulitsa mbewu ndi feteleza mmaboma onse atitsimikizira kuti afika mnthawi yake mmadera onse. Tikufuna anthu akangolandira makuponi, nthawi yomweyo agule zipangizo, adatero Mwanamvekha. Mmbuyomu, alimi akhala akudandaula chifukwa makuponi amawaolera mmanja kaamba kosowa kokagula zipangizo zotsika mtengo. Phungu wa dera la kummawa cha pakati mbomalo Yaumi Mpaweni adapempha alimi kuti agwiritse ntchito makuponi amene alandire. Si bwino kugulitsa makuponi anu chifukwa uko ndi kudzipha. Kuti mukolole zokwanira, ndi bwino kuwagwiritsa bwino ntchito, adatero Mpaweni. Mwa zina, chaka chino kuponi iliyonse izikhala ndi nkhope ya woyenera kulandira ndi cholinga choti munthu wina asagwiritse ntchito. Makuponi 4 miliyoni ogulira zipangizo zotsika mtengo adafika mdziko muno mwezi watha ndipo aperekedwa kwa alimi 1 miliyoni mchilinganizochi chaka chino. Mndondomeko ya zachuma ya chaka chino mpaka chaka chamawa, boma lidapereka K151 biliyoni ku unduna wa malimidwe ndipo K42 biliyoni ipita ku ntchito ya makuponi.
4
Apolisi mbweee! ku PAC Kwa munthu wongofika kumene mumzinda wa Blantyre, ngakhale nzika za mzindawu, sabata imene yangothayi kudali chitetezo chokhwima zedi pomwe apolisi adali ponseponse. Kuyambira mmawa, apolisi adali ndi ma rodibuloku adzidzidzi mmadera ena. Mmodzi mwa anthu okhala ku Machinjiri, Leston Kampira, Lachitatu adati adadabwa ndi mndandanda wa galimoto umene udalipo pa Wenela. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Tidayenda pangonopang;ono mpaka kukafika pa Wenela kuchoka pa HHI. Tidapeza kuti apolisi amaimitsa galimoto iliyonse ndikuchita chipikisheni kubuti. Ati apolisi amaopa kuti anthu ena apita ndi zida kumsonkhano wa PAC [Public Affairs Committee], adatero iye. Msonkhano wa bungwe lounikira momwe dziko lino likuyendera la PAC udali kuchitika ku Sunbird Mount Soche ndipo usanayambe mlangizi wa pulezidenti pa zochitika mdziko muno Hetherwick Ntaba adati boma limadziwa kuti pali anthu 300 amene amakonza zipolowe msonkhano wa PAC ukangotha. Msonkhanowo udaliko Lachitatu ndi Lachinayi. Ndipo Kumbukani Mhlanga wa ku Chinyonga adati adadabwa kuona apolisi akuimika galimoto iliyonse yolowa mtauni. Zidatichedwetsa ku ntchito. Ndipo ndimadabwa kuti chikuchitika nchiyani ndisanamve kuti kuli msonkhano wa PAC, adatero iye. Kuchuluka kwa apolisi sikudali mmisewu mokha, ngakhalenso kuhotelayo, apolisi adali mbweee, ena atanyamula mfuti zawo. Pa gulu la apolisi omwe anali ku msonkhanowo, oitanidwa ndi PAC adali 6 okha, malinga ndi mkulu wabungwelo Robert Phiri. Koma Phiri adati kuonjezereka kwa apolisiwo sikunasokoneze dongosolo lawo chifukwa adakonzekera. Tidadziwa kuti apolisi abwera ochuluka potengera nkhani zomwe zidamveka za chisokonezo. Mwina nthumwi zina zidasokonezeka, koma ife tachita mmene tidakonzera, adatero Phiri. Mmodzi mwa nthumwi ku msonkhanowo, mkulu wa bungwe la Peoples Land Organisation (PLO) Vincent Wandale adati anthu adadabwa ndi gululi, koma adamasuka kukamba zotukula dziko. Zidali ngati dziko likulamulidwa ndi apolisi. Nthumwi zaboma zidabwera zambiri, sitikudziwa kuti amaopa chiyani. Ubwino wake aliyense adapereka mfundo zimene adakonza. Zoopa apolisi zidali kale ndipo sitidanjenjemere kupezeka kwawo, adatero Wandale. Mneneri wa polisi mdziko muno James Kadadzera adati kuchuluka kwa apolisi sikudali kuopseza anthu koma kupereka chitetezo. Ndife osangalala kuti msonkhano watha popanda zovuta zili zonse. Timapezeka pofunika chitetezo kuti aliyense agwire ntchito yake mosaphwanya lamulo osati kuopseza. Ndipo okonda dziko lake sanganene kuti apolisi adalakwitsa, adatero Kadadzera. Chitetezo chapolisi chokhwimachi chidaonekeranso pamene apolisi mogwirizana ndi khonsolo ya mzinda wa Blantyre adaphwanya ndi kulanda makontena amene anthu amachitiramo bizinesi mumzindawo. Izi zidachitika usiku wa Lolemba ndi Lachiwiri.
11
Mwambo odzodza ansembe uchitika ku Blantyre, Zomba By Richard Makombe _0449-1-1024x683.jpg 1024w" sizes="(max-width: 662px) 100vw, 662px" />Mwambo wa malumbiro ngati umenewu uchitika ku Zomba komanso Blantyre Mwambo odzodza madikoni anayi kukhala ansembe mu arkidayosizi ya Blantyre uchitika loweruka ku Limbe Cathedral mu akidayosizi ya Blantyre. Malinga ndi Bambo Alfred Chaima omwe ndi mkulu wa muofesi yoona za utumiki mu arkidayosiziyi ati zonse zokonzekera kudzodza adikoni atatu achibadwiri komanso mmodzi wa chipani cha mzimu woyera tsopano zafika kumapeto. Bambo Chaima ati Ambuye Thomas Luke Msusa ndi omwe adzatsogolere mwambowu. Padakalipano nawo akhristu eni ake ati zokonzekera zizafika kumapeto pomwe magulu omwe akutsogolera miyambo yosiyanasiyana alimbikitsa kukonzekera zochitikazi ngati njira imodzi yokometsa mwambowu. Mmodzi mwa omwe ali mu komiti ya zochitika chitika pa tsikuli Patrick Kombe wati ali ndi chiyembekezo choti akhristu komanso alendo omwe ayitanidwa pa tsikuli azasangalala komanso kuthandiza archdiocese yao pamene ikulandira atumiki atsopanowa. Zonse zili mchimake ndipo pofika tsiku loweruka aliyense yemwe waitanidwa kuti adzabwere mwaunyinji chifukwa mmodzi wa ana awo mu dayosiziyi adzadzodwa pa tsikuli,anatero a Kombe. A Kombe anati ndi kofunika kuti akhristu wa adzaonetse umodzi wawo potenga nawo gawo pa zochitika pa tsikuli pomwe nso dayosizi tsopano yakula ndipo ili ma ma Parish 43. Mu dayosizi ya Zomba mwambo odzodza ma deacon atatu kukhala ansembe uchitikanso loweruka pa pomwenso kukakhale chikondwelero choti ansembe atatu akwanitsa zaka 25 akutumikira mulungu mu diocese ya Zomba. Malinga ndi Bambo Innocent Chiwanda yemwe ndi Pastoral Secretary wa Diocese ya Zomba, Ambuye George Desmond Tambala ndi omwe akatsogolere mwambowu. Ma Deacon atatu wa ndi a Peter Chiopsa, Petro Chilumpha ndi Fortune Gondwe, ndipo ansembe atatu omwe akukondwelera kuti atha zaka 25 akutumikira Mulungu ndi Bambo Daniel Beneti, Bambo Ignancio Bokosi ndi Bambo Charles Namalitha.
13
Chakwera angadze ndi kalumo kakuthwa Chakwera (wachiwiri kuchokera ku manja) limodzi ndi mkazi wake Monica komanso akuluakulu ena kumsonkhanowo Mlendo ndiye adza ndi kalumo kakuthwa. Akadaulo pandale ati kusankhidwa kwa mbusa Dr Lazarus Chakwera kukhala mtsogoleri wa chipani chachikulu chotsutsa boma cha MCP kungadzetse kuwala mchipanimo pamene chisankho cha 2014 chili pamphuno. Chakwera adasankhidwa kumsonkhano waukulu wa chipanichi ku Natural Resources College mumzinda wa Lilongwe sabata yatha ndipo ndiye adzaimire chipanichi pa chisankho cha 2014, maso ndi maso ndi mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda yemwe adzaimire chipani cha PP, Peter Mutharika wa DPP komanso Atupele Muluzi wa UDF. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Malinga ndi pulezidenti wa bungwe la akatswiri potambasula za ndale la Political Science Association of Malawi (Psam) Joseph Chunga, kusankhidwa kwa Chakwera kungachititse kuti chithunzithunzi chimene anthu anali nacho pa MCP chisinthe. Iye adanena izi polingalira kuti mbiri ya chipanichi idali ya nkhanza, makamaka paulamuliro wake wa zaka 31 kuchokera mu 1964 pomwe chidathetsa ulamuliro wa atsamunda. Ambiri akukumbukirabe nkhanza za ulamuliro wa MCP umene udachotsedwa mu 1994. Komanso, pakatipa chipanichi chinagawanika chifukwa cha mkangano wa atsogoleri a chipanichi makamaka John Tembo ndi Gwanda Chakuamba. Atangochoka mchipanichi Chakuamba, otsatira ena a chipanichi mchigawo chakumwera adazitulukanso, adatero Chunga. Chakuamba adatenga mpando wa utsogoleri wa chipanichi mu 1997, mtsgoleri wakale wa dziko lino Dr Hastings Kamuzu Banda atausiya chifukwa adali atakula. Iye adaimira chipanichi mu 1999. Koma Tembo adagonjetsa Chakuamba kukovenshoni yokonzekera chisankho cha 2004, ndipo adaimira chipanichi mu 2004 ndi 2009. Chakuamba adatuluka MCP atangogonja kwa Tembo ndipo atsogoleri ena adamutsatira pomwe ena adayambitsa zipani zawo. Chunga adati kudza kwa Chakwera kungachititse kuti kukhale kovuta kuti zipani zina zigonjetse chipanichi chifukwa zipani zambiri zomwe zilipo sizikuonetsa utsogoleri weniweni, makamaka chifukwa anthu amene akutsogolera zipanizo ayesedwa ndipo aunikidwa momwe akuyendetsera ndale. Pajatu kafukufuku wa 2012 Afrobarometer adasonyeza kuti Amalawi 40 mwa 100 alibe chipani makamaka chifukwa chosowa chikhulupiriro mwa atsogoleri andale. Ndiye MCP ikhoza kutolera gawo la anthu amenewa. Koma Chakwera ali ndi ntchito yaikulu yoyanjanitsa komanso kuluzanitsa atsogoleri amene adalephera kupeza mipando, adatero Chunga. Katswiri wa ndale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Blessings Chinsinga, wati ngakhale Chakwera ndi mlendo pandale ali ndi mphamvu zodzatengera chipanichi mboma. Iye wati Chakwera atapambana pa chisankhochi, zochitika za mchipanichi ndi zomwe zingamupangitse kuyendetsa bwino dziko kapena kulephera chifukwa cha chilendo chakecho. Ndale ndi zosiyana ndi kayendetsedwe ka bungwe, mpingo kapenanso kampani chifukwa ndale zimafuna kwambiri luso lolimbikitsa maubale lomwe munthu woyamba kumene ndale angavutike kukwaniritsa. Zikutengera zochitika mchipanichi kuti ngati Chakwera atapambana adzalamule dziko bwino kapena ayi. Kumbali imodzi chilendo chake chikhoza kumupangitsa kuti azipanga mfundo zokhwima bwino ndi kuzikwaniritsa posawerengera ndale komanso ngati atamusokoneza ngakhale atapanga nfundo zolimbazo zikhoza kuvuta kuzikwaniritsa kwake, adatero Chinsinga. Chinsinga wati tsopano anthu anayi akuluakulu odzapikisana nawo pampando wa mtsogoleli pa chisankho cha 2014 adziwika ndipo zikuonetsa kuti misonkhano yokopa alendo chaka chino mpakana cha mawa ikhala yovuta kwambiri. Iye wati kutengera anthu anayiwa, zipani zikuyenera kupanga nfundo zamphamvu zodzagulitsira munthu odzaimirirayo chifukwa mpikisano wake udzakhala wa mphamvu. Zikuoneka kuti mpikisano wa chaka cha mawa udzakhala oopsa ndiye mpofunika kupanga mfundo zenizeni osati kutaya nthawi ndi kukamba za munthu kapena zipani zina. Chitukuko chimatengera nfundo zomwe zamangidwa osati kudziwa kulankhula basi, watelo Chinsinga. Katswiriyu wati pamene nyengo ya misonkhano yokopa anthu odzavota yayandikira anthu ayiwale za mipingo, mitundu, ndi malo ochokela koma kumvetsetsa mfundo zomwe zipani zakonzela dziko lino. Ndipo Senior Chief Kaomba ku Kasungu yati kusankhidwa kwa Chakwera ndi chitsimikizo kuti ndale zayamba kukhwima mdziko muno. Iye adati ngakhale Chakwera sadatchukepo mumbiri ya ndale palibe chomuletsa kutsogolera chipani ngati mwini wake akudzidalira komanso ngati wasankhidwa ndi anthu. Timanena za mphanvu ku anthu zimenezi ndiye mphanvu kuanthuzo. Iye ndi munthu wamkulu akudziwa zomwe akuchita chofunika ndi chakuti akuluakulu ena omwe ndi a mkhalakale pandale mchipanimo azimugwira dzanja zonse ziyenda bwino, adatero Kaomba. Chakwera wati kuchokera tsiku lomwe adasankhidwa maso ake ali patsogolo kuwunika mofooka monse kuti adzakonze bwino ngati MCP ingalowe mboma chaka cha mawa. Iye wati ali ndi chikhulupiliro kuti anthu a mchipani cha MCP amuthandiza kuyala mfundo zokomera Amalawi. Chipani cha MCP ndi chachikulu kwambiri ndipo chili ndi ochitsatira ambiri omwe akufuna chitukuko. Kuchipani chathu tikhala pansi bwinobwino ngati anthu okhwima nzeru kuti tione zimene dziko lino likusowa ndikupeza podzayambira kukonza tikadzapambana, adatero Chakwera. Pa zolola amuna kapena akazi kukwatirana okhaokha, iye adauza wailesi ya Zodiak Lachinayi kuti atasankhidwa kutsogolera dziko lino kuti achite zimene Amalawi sakufuna. Ndipo pa za mkangano wa nyanja ya Malawi, iye adati kukambirana ndiye kofunika pakati pa maiko a Malawi ndi Tanzania.
11
NRB ionjezera masiku otengera zitupa Ntchito yopereka zitupa za unzika kwa anthu a mmaboma 15 mdziko muno, imene imayenera kutha dzulo ayionjezera mboma la Blantyre, mneneri wa bungwe limene likuyendetsa ntchitoyi watero. Maboma onse a chigawo chapakati komanso Blantyre, Mwanza, Neno, Nsanje ndi Chiradzulu ndiwo akulandira zitupazo mgawo Lachiwiri ndipo malinga ndi mneneri wa bungwe la National Registration Bureau (NRB) Norman Fulatira adati bungwelo laonjezera sabata imodzi kuti anthuwo atenge zitupa zawo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Fulatira Lachinayi adati: Tionjezera sabata imodzi kuti anthu alandire ziphaso zawo ndipo ngati ena akhalebe asadatenge, zitupa zawo akatengera ziphaso zawo ku ofesi ya DC. Fulatira wati amene satenga zitupazo pakutha kwa kuonjezerako azikatengera zitupazo kuofesi ya DC wa boma lawo. Kafukufuku wa Tamvani mumzinda wa Blantyre Lachinayi adavumbulutsa unyinji wa anthu akulimbirana kutenga zitupa ndipo anthu ena amene tidacheza nawo adati ndi bwino ntchitoyi ayionjezere. Patrick Sandramu, yemwe adalembetsa kusukulu ya pulaimale ya Makata ku Ndirande mumzindawo, adati gulu likumakhala kotenga zitupako nchiletso. Kufika lero Lachinayi, anthu ambiri sanatenge zitupa zawo ndipo gulu lake ndi losanena. Ine ndidachita mwayi chifukwa ndimadziwana ndi mmodzi mwa amene akugawa ziphaso ndipo ndidamuuza kuti akachipeza changa andisungire, adatero mkuluyo. Maxwell Majawa Lachinayi adati iye adati adayendera masiku angapo kusukulu ya Zingwangwa kuti atenge chitupa chake. Mbali imene amayendetsa aphunzitsi sizimavuta, koma kumene kumakhala anthu wamba ndiye mavuto analipo. Zoti tizipita kukatenga zitupa motsatira maina athu nazo zidatipomboneza. Ine ndidayendera masiku atatu kuti ndipeze chitupa, adatero Majawa. Ndipo Roselyne Manjawira amene adalembetsa kusukulu ya pulaimale ya Katete ku Chirimba adati pofika Lachinayi adali asanatenge chitupa chake chifukwa cha khamu, komanso chifukwa ameyenera kupita kuntchito. Akadaonjezera masiku chifukwa akanena kuti tizikatengera kwa a DC kukakhala chipwilikiti choopsa kuposa momwe zilili mmaderamu, adatero iye. Izi zili choncho, Madera ena, makamaka amene kulibe anthu ambiri, amatenga mosavuta. Gawoli likatha, lisamukira mboma la Thyolo, Chiradzulu ndi Mulanje. Ndondomeko yopereka ziphasozi idayamba mu October chaka chatha ndipo ikuyembekezereka kutha mu March chaka chino.
7
Papa Wasankha Amayi Awiri Mmaudindo Akuluakulu ku Vatican Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wasankha amayi awiri mmaudindo akuluakulu a ku likulu la mpingowu ku Vatican. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa wasankha Dr. Rafaella Vincenti kukhala mkulu woyanganira nkhokwe yosungira mabuku yomwe imatchedwa kuti Vatican Apostolic Library ndipo wasankha Professor Antonella Alibrandi kukhala membala wa bungwe lothana ndi mchitidwe wozembetsa ndalama lotchedwa Vatican Financial Information Authority. Malinga ndi likulu la mpingo wa katolika Dr. Vincenti adakhalapo mlembi wa Vatican Apostolic Library pamene Professor Alibrandi ndi membala wa bungwe la maloya mdziko la Italy lotchedwa Milan Bar Association, iyenso ndi President wa bungwe la za chuma ndi aphunzitsi a za malamulo Association of Economics and Law Professors komanso ndi membala wa bungwe la chi Katolika la anthu a za malamulo Union of Catholic Jurists. Nkhokwe yosungira ma buku Vatican Apostolic Library idakhazikitsidwa mchaka cha 1475 ndi Papa Sixto wa 4 ndipo ndi imodzi mwa nkhokwe za kale kwambiri pa dziko la pansi komanso nkhokwe yochititsa chidwi yomwe ili ndi zolembalemba zambiri za mtengo wa patali za make dzana. Ndipobungwe lothana ndi mchitidwe wozembetsa ndalama la Vatican Financial Information Authority adalikhazikitsa ndi Papa Benedicto wa XVIpa 30 December mchaka cha 2010.
14
Akhristu Akutsidya La Nyanja Ya Chirwa Akusowa Thandizo Wolemba: Sylvester Kasitomu ent/uploads/2019/09/lake-chilwa.jpg 367w" sizes="(max-width: 822px) 100vw, 822px" /> Akhristu achikatolika ku tsidya kwa nyanja ya Chirwa mu dayosizi ya Zomba apempha anthu akufuna kwabwino kuti awathandize kumalizitsa chalitchi chawo chomwe akumanga. Wapampando wa chalitchi-lii a joseph zakariya ndiwo apereka pemphori pofotokonzera mtolankhani wathu mu mzinda wa Zomba. Malinga ndi a ZAKARIA, ntchito yomanga tchalitchichi yatha ndipo chikusoweka ndi Mbalawala, malata komanso matumba a cement. Kunoko zinthu zambiri ndi zovuta kaamba koti mayendedwe ndi odula timagwiritsa ntchito ku mtunda komanso panyanja kuti tipite kumalo kumene kuli zipangizo zomngira ndiyene anthu attithandiza ndi ndalama ntchito itha kupepukako anatero a zakaria Pamenepa a ZAKARIA ati, akhristu a ku tchalitchi chawo cha St. Peters Ngotakota, amadalira usodzi zomwe akuti ndi zovuta kuti amalizitse ntchito yabwino yomwe yayambika yomanga kachisi wa Ambuye.
14
Akati tonde azimveka fungo akutanthauzanji? Miyambi ilipo yosiyanasiyana ndipo ina ukaimva mutu umachita kuwira, kulephera kulumikiza mwambiwo ndi tanthauzo lake. Ena amangoti bola ndanenapo mwambi osalingalira kuti kodi omvera akutengapo phunziro lanji pamwambiwo. Mwambi watitengera pabwaloli lero ndi wakuti tonde azimveka fungo. STEVEN PEMBAMOYO adakumana ndi mfumu Thipwi ya ku Nkhotakota kwa T/A Kanyenda pamsonkhano wokhudza za katetezedwe ka chilengedwe pomwe padatuluka mwambi wozunguawu ndipo adacheza motere: Ndikudziweni, wawa. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ine ndine Village Headman Thipwi wa mdera la gogochalo Kanyenda mboma lino la Nkhotakota. Pamsonkhano walero mumabwerezabwereza mawu oti tonde azimveka fungo, mumatanthauzanji ndi mauwa? Choyamba mudziwe kuti mawu amene aja ndi mwambi chabe ndiye monga mudziwa mwambi umanenedwa ndi cholinga choti omvera atengepo phunziro kapena chenjezo malingana ndi zomwe zachitika kapena zikuchitika. Nanga poti pamsonkhano umeneuja padali anthu okhaokha padalibe mbuzi? Nchifukwa chake mawuwo akutchedwa kuti mwambi, kutanthauza kuti sakuimira munthu aliyense, ayi, koma kuti pali phunziro lomwe tikufuna kuti anthu atolepo. Mwachitsanzo, msonkhano udali wokhudza za katetezedwe ka chilengedwe pogwiritsa ntchito njira zosiyanasiyana ndiye mwambi umene uja udali woyenerera kuugwiritsa ntchito. Nanga mwambiwu umatanthauzanji? Chabwino, mwambi umenewu umatanthauza kuti ntchito zamanja za munthu ndizo zimamuchitira umboni. Ngati munthu ali wolimbikira, zotsatira za kulimbikira kwakeko zimafotokoza zambiri za iye popanda wina kuima pachulu nkumalalika. Mwachitsanzo, mlimi wolimbikira amadziwika kuti ngolimbikira potengera zokolola zake, chimodzimodzi katswiri wa mpira wosewera kutsogolo amadziwika kaamba komwetsa zigoli. Kutanthauza kuti mbuzi nchitsamba chabe chongobisalirako? Ndi momwemo ndithu, sikuti timatanthauza kuti munthu yemwe tikukambayo ndi tonde poti akumveka fungo la mbuzi, ayi. Iyi ndi njira chabe yoperekera phunziro kapena malangizo ndi chilimbikitso moti apo anthu omwe adali pamsonkhanowu adziwa kuti aliyense pamenepanja azilingidwa ndi zotsatira za ntchito zake, osati kungokamba pakamwa, ayi. Ndiye tonde zikumukhudza bwanji pamenepa, osasankha nyama zina bwanji? Tondeyo ali ndi mbali yake yomwe amagwiritsidwira ntchito. Nkhani yaikulu ndi yakuti mkhola la mbuzi mukamabadwa ana pafupipafupi, ulemu umanka kwa tonde chifukwa ndiye amagwira ntchito mmenemo. Tonde akakhala wolephera kapena kuti ofooka, khola limakhala pomwepomwepo asasuntha, ayi. Ndiye mlimi akaona kuti zaka zikutha mbuzi zake sizikuswana, amakabwerekera tonde wina, uja nkumuchotsamo mwina kumugulitsa kwa mabutchala. Apa ndiye kuti amene uja sadamveke fungo chifukwa tonde mnzakeyo akangolowa mkhola nkuyamba kubereketsa, amalandira matamando kuti ndiye tonde chifukwa zipatso zake zikuoneka. Ndiye kuti aja amati akamva fwemba la munthu nkumati tonde azimveka fungo amalakwitsa? Kwambiri, chifukwa potero paja sipayenera kugwiritsidwa ntchito mwambi umenewu. Atapeza mwambi wina bola monga mwambi wakuti wakumba kanyimbi chifukwa apo zikugwirizana poti kanyimbi naye ali ndi fungo vloboola mmphuno osati masewera, ndiye ngati munthu akumveka fungo losakhala bwino monga mwaneneramo kuti fwemba ndiye kuti akuononga mpweya ndipo anzake akuzunzika ngati momwe amazunzira kanyimbi.
1
Anthu Okwiya Apha Bambo Wina Kamba Koba Nyemba Zaziwisi Anthu okwiya mboma la Chikwawa apha bambo wina wa zaka 30 kaamba komuganizira kuti waba nyemba zaziwisi mu dimba la mkulu wina. Malinga ndi wachiwiri kwa mneneri wa apolisi mbomali Sergeant Dickson Matemba, malemuyu Feston Sulupi usiku wa pa 6 July, anapita mmundawu omwe uli mphephete mwa mtsinje wa Shire kukathyola nyembazi koma ali momwemo anthu ozungulira derali anamugwira ndi kuyamba kumumenya. Mbale wawo wa malemuwa anafotokoza kuti mchimwene wawo anapita kukaba nyemba ku madimba omwe ali mphepete mwa mtsinje wa shire ndipo ali kumeneko anthu anayamba kumumenya komwe anakomoka, anatero Matemba. Sergeant Matemba ati anthu ena atamutengera ku chipatala, ndi komwe anakatsimikiza kuti wamwalira. Pamenepa Sergeant Matemba achenjeza anthu kuti asiye kutengera lamulo mmanja mwawo ndipo ati aliyense yemwe wachita izi amangidwa.
14
Tsabola ndi waphindu, wophweka kulima Ulimi wa tsabola umaoneka opanda pake komanso ogwetsa mphwayi, koma Benison Kuziona, mkulu wa Bungwe la Zikometso Innovation and Productivity Centre akuti ulimiwu ndi waphindu komanso wophweka. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kuziona adati ndi ndalama yochepa, mlimi amatulutsa ndalama zochuluka. Chaka chathachi, mbewuyi idafika pamtengo wa K3 000 pa kilogalamu ndipo alimi omwe adalima, adachita nayo mphumi kwambiri, adatero mkuluyu. Iye adaonjezanso kuti ubwino wina wa tsabola ndi woti ukabzala chaka choyamba, chaka chachiwiri subzalanso chifukwa mvula ikangogwa mitengo ija imaphukiranso ndipo zokolola zake zimakhala zochuluka kuposa poyamba. Tsabola ndi mbewu imene alimi ena akupindula nayo kwambiri A bungwe la Malawi Fruits mogwirizana ndi Mzuzu Agriculture Development Division (Mzadd) adachita kafukufuku wa tsabola mzaka za mmbuyomu ndipo adapeza kuti kulima tsabola ndi kophweka komanso sikulira ndalama zochuluka poyerekeza ndi mbewu zina. Ngakhale izi zili chomwechi, president wa bungwe la Farmers Union of Malawi, Alfred Kapichira Banda, wati alimi ena atsabola mmadera ena mdziko muno amagulitsa kwa mavenda pamtengo wotsika kwambiri. Iye adati alimi ambiri sakudziwa misika yeniyeni ya tsabola kotero amangoberedwa ndi mavenda. Tikupempha misika yovomerezeka yomwe imagula tsabolayu kuti ibwere poyera, tikufuna alimiwa azitha kugulitsa pa mitengo yabwino, adatero Kapichira Banda. Iye adati chifukwa chakuti alimiwa akhala akugulitsa pa mitengo yotsika, ambiri akumangolima moyerekeza pomwe ena adalekeratu ulimiwu. Bungwe la Zikometso Innovation and Productivity Centre ndi limodzi mwa mabungwe omwe amalimbikitsa za ulimi wa tsabola. Zikometso, ndi nthambi ya bungwe la National Smallholder Farmers Association of Malawi (Nasfam). Ntchito zake ndi kugula tsabola kwa alimi, kuwagulitsa njere zabwino komanso kuwaphunzitsa momwe angalimire tsabolayu kuti azikolola ochuluka komanso wapamwamba. Bungweli lili ndi fakitale yomwe imapanga tsabola wa mmabotolo yemwe amagulitsidwa mMalawi ngakhalenso maiko akunja. Malinga ndi Kuziona, ulimi wa tsabola umayambira ku nazale ngati momwe anthu amachitira ndi ulimi wa mbewu za masamba monga tomato. Tsabola amayenera kufesedwa kumapeto kwa mwezi wa October ndipo akuyenera kuwokeredwa pamene mvula yayamba kugwa yochuluka, adatero Kuziona. Iye adafotokoza kuti mizere imayenera kutalikana masentimita 75 komanso pobzala, mapando amayenera kutalikirana ndi masentimita 45. Akayamba kuphukira, amayenera kudulidwa tisonga take kuti apange nthambi zochuluka. Izi zimathandiza kuti pamtengo uliwonse mlimi adzakolole tsabola ochuluka, adatero Kuziona. Iye adaonjezanso kuti mbewuyi imayenera kuthiridwa feteleza wa D Compound ikangobzalidwa kumene komanso CAN pakadutsa masiku 21. Kathiridwe kake ndi kofanana ndi momwe timathirira ku chimanga. Fetelezayu amathandiza tsabola kuti akule bwino komanso abereke mochuluka, adatero mkuluyu. Iye adaonjezanso kuti tsabolayu nthawi zina amatha kugwidwa ndi matenda komanso tizilombo. Tizilombo tomwe timasakaza mbewuyi ndi tofanana ndi tomwe timagwira mbewu za mtundu wa masamba monga tomato ndipo mankhwala ake ndi ofanana ndi omwe amapoperedwa kumbewuzi. Mlimi akhonza kupopera mankhwala koma chachikulu ndi kubzala mbewu zabwino komanso kumapalira kuti apewe matenda ndi tizilomboti, adatero Kuziona.
4
Kusefukira kwa madzi kupha anthu 21 Anthu 21 atsikira kuli chete, pamene ena 100 000 ali kakasi kusowa kopita kutsatira mvula ya mphamvu yomwe yasakaza katundu komanso kusamutsa anthu mdziko muno. Izitu zachitika kuyambira mwezi wa July chaka chatha mpaka mwezi uno wa January. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Malinga ndi nthambi ya boma yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma), maboma 24 ndi omwe akhudzidwa ndi mavutowo. Mwa mabomawo, maboma 12 ali mchigawo cha kummwera 8 chigawo chapakati pamene anayi ali mchigawo chakumpoto. Malinga ndi mneneri wa Dodma Chipiliro Khamula, pofika Lamulungu pa 13 January, ngoziyi nkuti itapha anthu 21. Mwa anthuwo, 12 adamwalira ataombedwa ndi mphenzi pamene anthu ovulala pangoziyo adalipo 38, adatero Khamula. Iye adati boma lakhala likuwapatsa anthu okhudzidwawo thandizo monga chakudya, zofunda ndowa ndi zina komanso malo okhala mongoyembekezera. Ntchitoyo ikupitilira ndipo tikadafikirabe madera omwe ma makhonsolo awo atidziwitsa za ngozi, adatero Khamula. Nthambi yoona zakusintha kwa nyengo ya Department of Climate Change and Meteorological Services (Met), yati kuliraku sikutha chifukwa sabata ino mvula yosefula madzi ikatamuka. Ena mwa maboma okhudzidwa ndi Nsanje, Karonga, Mulanje, Chikwawa, Balaka ndi Lilongwe. Polankhula ndi Tamvani, DC wa boma la Mulanje, Charles Makanga adati madzi osefukira ochokera mumtsinje wa Thuchira, Lolemba pa 14 adaononga minda ya anthu 520 ochokera mmidzi ya Kada ndi Nongwe kwa mfumu yaikulu Nkanda. Apapa ndiye kuti anthuwo akufunikira thandizo la mbewu ndi zofunikira zina chifukwa minda yawo yakokoloka, adalongosola Makanga. Iye adatinso anthu 680 mdera lina komweko ali kakasi mvula ya mphepo itasakaza nyumba zawo. Tikuyesetsa kupereka thandizo loyenera kwa anthuwo ngakhale tikudikirabe thandizo lofika kwa anthu omwe ali kakasi ochokera kumsika wa njala komwenso mvula ya mphepo idasakaza katundu, adalongosola Makanga. Sabata yathayo, anthu awiri adamwalira mboma la Balaka ndi wina mboma la Mangochi chipupa cha nyumba yawo chitawagwera kutsatira mvula yomwe idagwa mmabomawo. Ku Mzimba kwa Mberwa, Jalavikuwa, Ntwalo ndi Mabulabo mabanja pafupifupi 1000 akhudziwa ndi mvula ya matalala komanso madzi osefukira. DC wa bomalo, Thomas Chirwa adati chifukwa choti madera ambiri akhudzidwa pakamodzi, anthu ambiri sadalandirebe thandizo. Mzinda wa Lilongwe ndi malo enanso omwe madzi adazunguza sabata yatha. Anthu 176 adasamutsidwa ndi madzi ndipo katundu adaonongeka. Nduna ya zachitetezo mdziko muno yomwe yakhala ikuyendera anthu okhudzidwawo, Nicholus Dausi idati ngozizo zanyanya chaka chino ndipo mpofunika kuti anthu akhale osamalitsa kukamagwa mvula kapena mphepo.
5