Text
stringlengths
292
6.6k
labels
int64
0
19
Dziko la Bahamas Lilonjeza Kuthandiza Mzika Zake Zokhudziwa ndi Ngozi ya Mphepo Wolemba: Sylvester Kasitomu "http://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/09/BAHAMAS-300x168.jpg" alt="" width="837" height="469" /> Dziko la Bahamas lati likuyesetsa kuchitapo kanthu pofuna kuthandiza anthu omwe akhudzidwa ndi mphepo ya mphanvu yomwe inaomba sabata yathayi. Malipoti a wailesi ya BBC ati zadza kutsatira madandaulo omwe anthu okhala pa chilumba cha Abaco akhala akunena kuti boma la dzikolo likulephera kuthandiza anthu omwe akhudzidwawa. Padakali pano anthu 43 ndi omwe afa chiyambireni mphepoyi ndipo pali chiyembekezo choti chiwerengero cha anthu omwe afa mdzikolo chitha kukwera kaamba koti nthito yopumutsa anthu omwe akhudzidwa idakali nkati. Polankhulapo nduna ya zofalitsa nkhani mdziko la Bahamas, Carl Smith anati boma la dzikolo likuchita chothekera pofuna kuthandiza anthu omwe akhudzidwa ndi mphepoyi kudzera ku ndondomeko yoona za ngozi zogwa madzidzidzi ya National Emergency Management Agency (NEMA) Tikuyesetsa kuti tifikire anthu onse omwe akhudzidwawa ndi cholinga choti apeze malo okhala komanso chakudya ndi zina kudzera mu ndondomekoyi, anatero Smith. Chiwerengero cha nyumba zomwe zagwa pa chilumba cha abaco chafika pa 90 Percent zomwe zikuchititsa kuti anthu mazanamazana asowe pokhala kaamba ka vutoli. Dziko la Bahamas lakhudzidwa ndi mphepo yamphanvu ngati izi kwa maulendo okwana asanu kuchokera mu chaka cha 2016 zomwe zakhala zikudzetsa imfa za anthu ochuluka kwambiri komanso kuonongeka kwa katundu ndi nyumba.
18
Lekani kulozanalozana, nyengo yasinthaMET Nthambi yoona za kusintha kwa nyengo ya Malawi Meteorological Services (MET) yati anthu adziwe kuti nyengo ikusintha ndipo aleke kulozana zala chifukwa palibe akuchititsa izi. Mkulu wa nthambiyi Jolamu Nkhokwe adalankhula izi Lachitatu pamene nthambiyi imakumbukira tsiku la zanyengo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Zikavuta choncho mmunda ena amaloza chala anzawo Nkhokwe adati nthambi yawo nthawi zonse imapereka uthenga wa momwe nyengo ikuyendera, koma akudabwa kuti ena akukhalabe moyo wachikale womaloza ena zizindikiro za kusintha kwa nyengo zikaoneka. Ambiri sakudziwabe kuti pali kusintha kwa nyengo, dziwani kuti nyengo yasintha ndipo izi zikuoneka kudzera mnjira zambiri monga kusowa kwa mvula ndi kusefukira kwa madzi. Anthu agwiritsire ntchito uthenga womwe tikuwapatsa kuti atsatizire bwino za kusintha kwa nyengo. Tsiku lililonse tikumatulutsa uthenga wa momwe nyengo ilili koma tikudabwa kuti ena akukhala moyo wachikale, adatero Nkhokwe. Kulankhula kwa Nkhokwe kukudza pamene mdziko muno anthu okalamba akukwapulidwa, ena kuwapha kumene powaganizira kuti akutseka mvula. Ku Chiradzulu mwezi wathawu ndiye anthu 7 adaothetsedwa moto masanasana ndipo adawasiya atalonjeza kuti mvula ibwera. Nkhoswe adati izi ndi zachisoni chifukwa palibe amene angatseke kapena kumasula mvula ndipo wapempha anthu kuti azitsatira zomwe nthambi yawo ikutulutsa kukhudzana ndi momwe nyengo ikhalire. Malawi ndi limodzi mwa maiko amene akhudzidwa ndi kusintha kwa nyengo moti mvula chaka chino yagwa mwanjomba kupangitsa kuti ena asaphulemo kanthu mminda yawo.
18
Anthu Ayamba Kuponya Voti Mdziko la Botswana Wolemba: Thokozani Chapola /2019/10/BOTSWANA-VOTING-300x168.jpg" alt="" width="521" height="292" />Anthu a mdziko la Botswana kuyipa pamzere kukaponya voti yawo Anthu a mdziko la Botswana ayamba lero kuponya voti yosankha mtsogoleri wa dziko komanso a phungu akunyumba ya malamulo. Malinga ndi malipoti a BBC aka ndikoyamba kuti anthu a mdzikomo achite chisankhochi chilandilireni ufulu odzilamulira mchaka cha 1966. Anthu pafupifupi 900, 000 ndi omwe akuyembekezeka kuti aponye nawo voti-yi. Zipani ziwiri za Botswana Democratic Party (BDP) chomwe ndi cholamula ndi chipani chotsutsa cha Umbrella for Democratic Change (UDC) ndi zomwe zikupikitsana pa chisankhochi. Mwa zina chipani chotsutsa cha UDC chati chili ndi chikhulupiliro chonse kuti chipambana pa chisankhochi, kaamba koti Manifesto ake akukamba zodzapereka mwayi wa ntchito kwa anthu 100, 000 chikapambana pa chisankhochi. Malipoti amasonyeza kuti mwa anthu 2.2 Million omwe ali mdziko-mo 20% ndi anthu omwe sali pa ntchito. Dziko la Botswana ndi limodzi mwa maiko ochita bwino mmayiko a muno mu Africa kaamba ka malonda a mnyanga ya njovu, kudzaso miyala ya mtengo wapatali ya mtundu wa Diamond.
11
Aphungu akumana komaliza Nthawi yatha. Aphungu a Nyumba ya Malamulo amene adasankhidwa mu 2014 akumana komaliza kuyambira Lachiwiri likudzali Amalawi asanavote pachisankho cha patatu pa 21 May chaka chino. Mwa zina, aphunguwo akakambirana za momwe ndondomeko ya zachuma ikuyendera kuchokera pomwe adaikhazikitsa chaka chatha komanso kumanso kukambirana mabilo ena. Izi zikutanthauza kuti nyumbayi akamaitseka, aphungu ena sadzabwereranso mnyumbayo ngati atalephera pachisankhocho. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Aphungu mNyumba ya Malamulo mmbuyomu Izi zili apo, akadaulo pa zachitetezo, ndale ndi maufulu ati msonkhano womaliza wa aphunguwo sukhala wa phindu ngati aphungu sakambirana za kubedwa ndi kuphedwa kwa anthu achialubino komwe kwayala nthenje mdziko muno. Akadaulowa ati izi zikhoza kutheka ngati aphunguwa atagwiritsa ntchito msonkhanowu popeza njira zokhwimitsira chitetezo cha anthu omwe ali ndi khungu la chialubino omwe chitetezo chawo chagwedezeka. Mmodzi mwa akadaulo pa zachitetezo, Brigadier General Marcel Chirwa yemwe adakhalapo msilikali komanso Kazembe wa dziko lino adatanthauzira chitetezo cha munthu ngati kukhala mosaopa ndi kusaphwanyiridwa ufulu uliwonse. Chitetezo cha munthu ndi pomwe munthuyo akukhala mwaufulu wosaopsezedwa mwanjira iliyonse monga kuphedwa, njala kapena matenda. Mwachidule, chitetezo ndi pomwe munthu akukhala mosatokosedwa kunyumba, kuntchito kapena mmudzi, adatero Chirwa. Iye wati aphungu akamakumana akuyenera kuunika momwe anthu akukhalira mdziko muno makamaka omwe ali ndi khungu la chialubino nkupeza njira zothetsera mavuto omwe anthuwa akukumana nawo makamaka pa nkhanza zobedwa ndi kuphedwa. Nzachidziwikire kuti anthu achialubino alibe chitetezo chifukwa akukhala mwa mantha ndi nkhanza zomwe akukumana nazo. Aphungu atakonza apa pamsonkhano wawowu, akhoza kuonetsa kukhwima nzeru kwawo, watero Chirwa. Katswiri pa ndale George Phiri wa ku University of Livingstonia (Unilia) wati dziko lonse lili maso pa Malawi kuti njira yothetsera nkhanza zomwe akukumananazo anthu achialubino ichokera pati moti yemwe angabweretse njirayo adzalandira ulemu waukulu. Phiri wati aphungu a ku Nyumba ya Malamulo asenza chiyembekezo cha dziko lonse kuti mwina muzokambirana zawo zomalizazi mukhoza kutuluka njira yosowayi. Aphungu ali nkuthekera kowongola zinthu pankhani ya maalubinoyi. Msonkhano uwu ndi womaliza ali pampando koma ndiokwanira kukambirana njira yotetezera maalubino moti akamakumana akuyenera kugwiritsa ntchito mpata umenewu, watero Phiri. Wapampando wa mgwirizano wa mabungwe olimbikitsa zaufulu Timothy Mtambo wati mabungwe ayesetsa kukankhirira kuti aphungu asalephele kukambirana zachitetezo cha maalubino mpaka njira ipezeke. Ngati mumatitsatira, muyikira umboni kuti takhala tikulimbana ndi boma pa zachitetezo cha maalubino koma tsopano taona mpata wina mumsonkhano wa aphungu womwe ukudzawu. Tiyesetsa kuti msonkhano umenewu usathe asadakambirane nkhaniyi, watero Mtambo. Nyumba ya Malamulo idasintha lamulo lokhudza kupezeka ndi ziwalo za munthu mchaka cha 2016 pofuna kukhwimitsa chitetezo cha anthu achialubino omwe nkhani ya kuzunzika kwawo idayamba kutchuka mchaka cha 2014. Lamuloli limati ndi mlandu kupezeka ndi ziwalo za munthu ndipo chilango chake ndi moyo wonse kundende ukugwira ntchito yakalavula gaga popanda mwayi wolipira chindapusa. Wapampando wa komiti yoona za malamulo mNyumba ya Malamulo Maxwell Thyolera wati cholinga china cha lamuloli nkuunikira kuti milandu yotere izikambidwa mkhothi lalikulu osati mmakhothi angonoangono a majisitileti. Nkhawa yathu ndi yoti apolisi ndi makhothi sakugwiritsa ntchito lamuloli mokwanira chifukwa tinkayembekezera kuti nkhani zotere zichepa kapena kutheratu ndi lamuloli, watero Thyolera. Pano, makomiti atatu; ya zamalamulo, chitetezo ndi makhalidwe a anthu mmadera akhazikitsa komiti imodzi yoti ifufuze chomwe chikuchitika pa nkhani zozembetsa ndikupha maalubino ndipo ati zotsatira zakafukufukuyu zidzaperekedwa mNyumba ya Malamulo.
11
Gulewamkulu ndi mankhwala Matenda akagwa pakhomo, makolo amakhala ndi njira zochuluka zothetsera matendawo malinga ndi zikhulupiriro zawo. Ena okhulupirira gulewamkulu akuti ngati mthupi mwabaya, akangovina wodwala amachira pomwepo. Mmudzi mwa Siledi kwa Senior Chief Kanduku mboma la Mwanza muli mayi wina amene ati adachira gulewamkulu atapalasa. BOBBY KABANGO akucheza ndi mkulu wa dambwe kumeneko, Maxwell Kondwerani. Gulewamkulu akuti ndi mankhwala Tidziwane maudindo wawa Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndili ndi maudindo angapo, ndine nduna ya mfumu mdera lino. Ndimamemeza anthu ammudzi muno ngati pali zina kuti zichitike kapena mfumu yaitana. Ngati anthu ammudzi muno ali ndi zochita zina monga mwa zikhulupiriro zawo amandifikira kuti ndipereke uthenga kwa mfumu yathu yomwe imaloleza zochitikazo komanso kudambwe ndili ndi gawo langa. Tikambe nkhani ya gulewamkulu Mufuna ndikambe nkhani iti kumeneku? Pajatu zakudabwe saulula, mumadziwa zimenezo? Inde koma, nzabwinobwino, osati zofwala gule. Chabwino, nkhani yake ndi yotani yomwe mufuna ticheze? Tikumva kuti guleyu ndi mankhwala, ndi zoona? Ndi zoona. Ife Achewa timakhulupirira zimenezi. Izi kuno zimachitika ngati mizimu yalamula kuti tichite. Zimakhala bwanji kuti mpaka zifike poitana gule? Timakhala talamulidwa ndi mizimu kuti gulewamkulu avine ndi cholinga chochotsa matendawa. Izi sizitheka popanda kulamulidwa ndi mizimu. Talongosolani chiyambi chake chimakhala chotani kuti mizimu ilamule? Munthu ngati akudwala, timayenda naye mwa asinganga momwe timakaombeza za chiyambi cha matendawo. Kumeneko nkomwe amanena ngati matendawo akufunika kuvinira gule kapena angomwa mankhwala. Apa ndikutanthauza kuti sizingatheke kuti mungoyamba kuvinira matenda ngati mizimu sidanene. Akati gule akavine zimakhala bwanji? Amanena kuti mukatenge chikho cha msunje ndipo tikaikemo ufa ndi kukanda. Apa mumayamba kumuzungulitsa chikho chija. Pomwe mukuzunguliza chikho chija mumaimba nyimbo. Tikatha amati tikataye patsinde pa mtengo. Pomwe tikuchita izi ngoma zimakhala zikusweka komanso zilombo zikuvina. Taimbani nyimboyo ndimve Timati.Tidzutsire wathuyu bwino, ngati ndi mizimu wathuyu adzuke. Mizimu mudzutse wathu pofika mawa Kodi matendawa amakhala atafika pothiphwa kwambiri? Eee! Matenda amakhala afika povuta ndipo tikamati tidzutsire wathuyu ndiye kuti amakhala salinso mwakanthu. Akamati mukavine gulewamkuluyo amakupatsani mankhwala alionse? Palibe mankhwala alionse omwe amatipatsa ndipo machiritso amagona pamenepo. Mukavina ndi kutsata zomwe akunenazo matenda amathera pomwepo. Ndani amayenera kupezeka pamwambo ngati umenewo? Akuluakulu a gule amapezeka pamalopo komanso mwini mbumbayo. Pomwe tikusankha mwini mbumba timayenera kusankha yemwe adalowa gule wamkulu osangotenga aliyense. Kodi zimatheka kuti gule avine chikhalirecho sindiwe wolowa? Sizingatheke. Kuno zimachitika chifukwa aliyense adameta kapena kuti kugula njira.
19
Zochitika ku mwambo wa kulamba Loweruka lapitalo kudali chaka ku likulu la mfumu yaikulu ya Achewa mmaiko a Malawi, Zambia ndi Mozambique Kalonga Gawa Undi ku Mkaika mboma la Katete ku Zambia. Khamu la anthu ochokera mmaikowa lidapita kumeneko kukachita nawo mwambo wa Kulamba. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Malinga ndi kufotokoza kwa mkulu wa bungwe la Chewa Heritage Foundation (Chefo) Dr Justin Malewezi, mwambowu umayanjanitsa Achewa ochokera mmaiko atatuwa. Dziko la Malawi ndilo lili ndi mafumu a Chichewa ambiri kuposa maiko enawa. Malawi ili ndi mafumu 136 a Achewa, pomwe ku Zambia aliko 36 pomwe ku Mozambique aliko 42. Malewezi adati mmaboma onse a dziko la Malawi muli mafumu a Achewa, kupatula maboma a Balaka, Rumphi, Mzimba ndi Karonga. Mmaiko atatuwa muli Achewa 14 miliyoni, omwe 9 miliyoni mwa iwo akuchokera ku Malawi. Nanga nchifukwa chiyani mwambowu umachitikira ku Zambia osati ku Malawi komwe kuli mafumu komanso Achewa ochuluka? Malewezi adayankha: Mwambowu umachitikira komwe kuli likulu la Kalonga Gawa Undi. Pochokera ku Zaire kalekalelo, likulu la Achewa lidali ku Mankhamba ku Mtakataka mboma la Dedza. Kenako lidasamukira ku Mozambique, koma kumeneko Apwitikizi amadana ndi mafumu ndipo Kalonga wanthawiyo adamangidwa kwa zaka 20. Atatulutsidwa, adasamukira ku Zambia komwe mpaka lero mwambowu umachitikira. Iye adafotokoza kuti Kalonga Gawa Undi ali ndi tanthauzo lakuya. Kalonga, akuchoka ku liwu lakuti kulonga chifukwa ali ndi mphamvu zolonga ufumu. Akutchedwa Gawa chifukwa ali ndi mphamvu yogawa malo; ndipo Undi chifukwa amateteza anthu ake. Nanga chimachitika pamwambowu nchiyani? Mwambowu umakhala ukuchitika kwa sabata zingapo, koma umafika pachimake Loweruka lomaliza la mwezi wa Ogasiti. Patsikulo pamakhala magule osiyanasiyana ndipo mafumu a Chichewa amapereka mphatso kwa Kalongayo, kuthokoza. Apa ndipo pachokera mawu akuti kulamba. Mwambowu umachitika anthu atamaliza kukolola komanso akukonzekera mvula yotsatira. Mafumuwo amapereka mphatso kwa mfumuyo mothokoza. Komanso amaifotokozera momwe zinthu zilili mmaiko mwawo pankhani ya chakudya, matenda ndi zina zotero, adatero Malewezi. Chochititsanso chidwi patsikulo ndichakuti Kalonga Gawa Undi amakapereka moni kwa mayi ake Nyangu. Chinanso chochititsa chidwi udali mpando wachifumu umene Kalonga Gawa Undi adakhalapo, mozungulilidwa ndi asilikali ake komanso makhansala ake. Mmbali mwa mpandowu mumayalidwa minyanga ya njovu. Ndipo kutsogolo kwake, mbali ya kumanzere kuli mutu wa kambuku, pomwe kumanja kuli mutu wa mkango. Izi zikusonyeza mphamvu ya mfumuyo poteteza anthu ake. Mwambowu udathetsedwa ndi atsamunda kwa zaka zambiri, kufikira mchaka cha 1981 pomwe udayambikanso. Iyi ndi nthawi imene Achewa a mmaiko atatuwa amayanjana ndikusangalala za chikhalidwe chawo, adatero Malewezi. Pambali pa magule komanso mchezo, anthu adakhwasula nyama zosiyanasiyana za kuthengo kuphatikizapo njati. Gule wamkulu adaliko mitundu yambiri, kuphatikizapo maria, makanja, nyolonyo, gologolo komanso chilembwe. Kudalinso magule ena monga manganje ndi soopa, utse komanso chisamba.
1
MRA Imema Mafumu Alimbikitse Anthu Kudula Msonkho Wolemba: Thokozani Chapola uploads/2019/09/kapoloma.jpg 312w" sizes="(max-width: 300px) 100vw, 300px" />Kapoloma: Mafumu ndi anthu ofunikira pa nkhani yotolera misonkho Mafumu a mboma la MANGOCHI awapempha akuti adzidzipereka pa ntchito zothandiza kuzindillitsa anthu za ubwino wopereka ndalama za misonkho molingana ndi phindu lomwe amapeza pa busness zawo. Mkulu wa bungwe lotolera ndalama za misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA) a STEVE KAPOLOMA ndi yemwe wanena izi lero ku MPONDAS mbomalo, pomwe bungwe-li limazindikilitsa mafumu za udindo umene ali nawo pogwira ntchito limodzi ndi bungwe-li. Iwo ati ndalama zamisonkho ndi ndalama zomwe zimathandizira pa ntchito zotukula dziko lino, kotero ngati mafumu ali ndi udindo waukulu woonetsetsa kuti anthu opezeka mmadera mwawo sakuchita zachinyengo koma akutha kupereke misonkho pa za malonda awo. Boma la Mangochi linachita malire ndi dziko la Mozambique ndiye ena amathawa kudula msonkho podutsa njira zamadulira. Ife tawona kuti anthu amenewa njira zachiudule amadutsazo ndi madera a mafumu choncho ndi kofunika kuwalimbikitsa mafumu kuti azitenga gawo pothandiza anthu kupereka msonkho mosathawathawa, anatewro a Kapoloma. Ena mwa mafumu a mdera la mfumu yayikulu MPONDA mbomalo omwe anafika pa msonkhano-woati agwirana manja ndi bungweli polimbikitsa anthu kupereka msonkho moyenera.
2
Chipani cha DPP Chilimbikitsa Bata Pambuyo pa Chigamulo Mmodzi mwa akuluakulu a chipani cha Democratic Progressive (DPP) Mwayi Kamuyambeni wapempha anthu otsatira chipanichi kuti adzavomereze chigamulo cha bwalo la milandu pa nkhani yokhudza chisankho cha mtsogoleri wa dziko. Apemphedwa kuti adzasunge bata-otsatira chipani cha DPP Kamuyambeni yemwenso ndi phungu wa dera la kumadzulo kwa boma la Ntcheu amalankhula izi lachisanu mmudzi mwa Eneya mdera la mfumu yaikulu Kwataine pa mwambo wokondwelera komanso kutsanzikana ndi chaka cha 2019. Iye wati ndi pempho lake kuti anthu adzagwirizane ndi chigamulochi kuti dziko la Malawi lipitilire kukhala la bata ndi mtendere. Polankhulaponso koma mosiyana mkulu wa achinyamata mchipani cha Democratic Progressive (DPP) mchigawo chakumvuma kwa dziko lino, a Steven Bamusi apempha achinyamata onse mchigawochi kuti adzalemekeze malamulo komanso kupewa ziwawa pa nthawi yomwe bwalo la milandu lidzapereke chigamulo chake pa nkhani yokhudza zotsatira za chisankho cha president. A Bamusi omwenso ndi khansala wa dera la Mbedza mu mzinda wa Zomba ati zimenezi ndi zomwe akuluakulu oyanganira achinyamata mchipanichi mzigawo zonse za dziko lino, agwirizana. Raphael Likaka analankhula ndi a Bamusi.
11
Utsi ku Nam pamene ma Queens anyamuka Utsi ukufukabe ku bungwe loyendetsa masewero a ntchemberembaye la Netball Association of Malawi (NAM) kaamba kosemphana zochita pakati pa mphunzitsi wa timuyi Peace Chawinga-Kalua ndi bungweli. Timu ya ntchemberembaye yomwe imangodziwika kuti Malawi Queens idanyamuka mdziko muno Lachitatu msabatayi ulendo ku Sydney mdziko la Australia komwe ikukapikisananawo mchikho chapadziko lonse. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Kugwebana kudayambika pamene zidadziwika kuti NAM idatumiza kale maina a atsikana amene apita ku Australia mosadziwitsa Kalua. Malinga ndi Kalua, NAM idatumiza maina a osewerawo pamene iye asadawaitane kukampu kuti akachite zokonzekera. Ineyo ndi amene ndimayenera ndisankhe osewera amene achita bwino kukampuko. Koma zomwe zachitika nkuti NAM yasankha kale osewera ine ndisakudziwa. Nditatulutsa mndandanda wa osewera anga amene ndikuwafuna, iwo akana osewera ena amene ndawapatsa ndipo aika amene akuwafuna, adatero Kalua. Queens captured on departure at Chileka Airport in Blantyre. Koma pamene amanyamuka pa bwalo la ndege la Chileka Lachitatu, nkhope za akuluakulu a NAM ndi mphunzitsiyu zimaoneka kuti sizikumvana zochita. Chitsanzo, titamufunsa mphunzitsiyu zomwe akonzekera kukabweretsa kuchokera ku mpikisanowo, iye adati, funsani amene akonzekera kukabweretsa zotsatira zomwe mukufunsazo. Ine sindingayankhe zimenezo, adatero mphunzitsiyu uko akusonya a NAM kuti atifotokozere. Koma titamufunsa pulezidenti wa NAM Rose Chinunda, iye adati sakuonapo vuto chifukwa ganizolo lidachitika atakambirana ndi wachiwiri kwa Kalua yemwe ndi Mary Waya komanso Griffin Saenda yemwe ndi wothandizira aphunzitsiwa kagwiridwe ka ntchito yawo. Tidafunsa anthu amenewa koma mphunzitsi yekha ndiye sitidamufunse. Ganizo lochotsa wosewera wina ndikubwereretsapo wina lidabwera titamva kwa awiriwa, ndiye palibe vuto komanso dziwani kuti majority rules [timamvera anthu ambiri popanga ganizo] adatero Chinunda. Komabe izi zakhumudwitsa kampani ya Airtel Malawi yomwe imathandiza atsikanawa. Mneneri wa kampaniyi Edith Tsilizani adapempha mbalizi kuti zikambirane ndikuthetsa kusamvanaku. Ndizodandaulitsa kuti pali chimkulirano chotere, koma ife tikupempha kuti akambirane ngati akufuna kuti tikabwere ndi zotsatira zabwino kuchokera ku ulendowo, adatero Tsilizani yemwe kampani yake idapereka K7 miliyoni pa ulendowu. Kalua amafuna atenge Ellen Chiboko wa Tigresses koma mmalo mwake NAM idachotsa dzina lake ndikuikapo Jean Chimaliro zomwe zadabwitsa. Uwu ndi mndandanda wa osewera amene anyamuka ulendo ku Sydney; Mwawi Kumwenda, Joyce Mvula, Towera Vinkhumbo, Carol Ngwira, Sindi Simtowe, Takondwa Lwazi, Chimaliro, Grace Mhango, Lauren Ngwira, Thandi Galeta, Bridget Kumwenda ndi Martha Dambo. Atsikanawa adatsimikiza kuti ngakhale pali kusamvana komabe ulendo wa ku Sydney akukamenya nkhondo.
16
Papa Wapempha Anthu Aleke Manyazi pa Nkhani za Mulungu Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco, wapempha a khristu kuti asamachite manyazi kuwonetsa kukondwa kwawo pa nkhani za Mulungu. Papa wanena izi pa nsembe ya ukalistia yomwe anatsogolera lero ku tchalitchi la Casa Santa Marta. Iye anati kufalitsa uthenga wa mulungu kutha kukhala kosavuta ngati a khristu azifalitsa uthengawu ndi mtima wokondwa. Papa anapitiriza kunena kuti kupatula mawu a mulungu, akhristu ayenera kugawira wina ndi nzake madalitso omwe ali nawo ndi anthu ena monga momwe Davide anachitira. Mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu anapitiriza kunena kuti a khristu akuyenera kuchita izi mokondwa, koma kukondwa kwake kosapitilira muyezo.
13
Okakamira milongoti zawo izo! Lachitatu likubwelali lidzakhala tsiku lowawa kwa iwo amaonera kanema ya mlongoti (aerial). Makanema ambiri adzazima ndipo kudzakhala mdima wadzaoneni. Patsikulo ena adzayesa kuzimitsa makanema awo nkuyatsanso koma sadzayaka ndipo ena adzawatengera kwa okonzetsa koma chithunzi osaoneka. Koma awa si mathero a dziko. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Okhawo omwe ali ndi zowayenereza kuonera kanema wawo munjira yatsopano ya dijito adzaona kuwala. Awa ndi mathero a zithunzi zamchengamchenga ndinso zooneka ngati mvula ikuwaza pakanema. Mchaka cha 2006 bungwe la United Nations (UN) lidagwirizana kuti maiko onse asiye kugwiritsa ntchito zithunzi zamchengamchenga nkupita kudijito. Bungweli lidati ndi dijito zithunzi za kanema zizioneka zopanda mchengamchega komanso mawu azimveka bwino opanda manzenene. Koma kodi ndi angati akudziwa za kusinthaku? Mwa anthu khumi omwe tidawapeza mmzinda wa Mzuzu, atatu ndi amene akudziwa za kusinthaku. A bungwe loona za ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) ati boma lilibe nazo ntchito kwenikweni za kusinthaku. Ndi zoonetseratu kuti boma silikukhudzidwa ndi kusinthaku chifukwa silikudziwa chomwe likuchita, ndi anthu omwe silidawadziwitse mokwanira za kusinthaku, adatero John Kapito, mkulu wa bungweli. Nayo nduna ya zofalitsa nkhani, Kondwani Nankhumwa, mmbuyomu idavomereza kuti boma lalephera kudziwitsa anthu mokwanira za kusinthaku. Koma mkulu wa bungwe loyanganira za kusinthaku la Malawi Digital Broadcasting Network Limited (MDBNL), Dennis Chirwa, adati bungwe lake layesetsa kuchita zomwe lingathe. Iye adati bungwe lake lagula ma decoder omwe akugulitsidwa mmapositi ofesi onse mdziko muno pamtengo wa K20 000.
0
Papa Watsiriza Ulendo Wake Wa Mdziko la Romania Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wamaliza ulendo wake wocheza mdziko la Romania. Papa ali mdziko la Romania Polankhula pakutha pa ulendowu Papa Francisco walimbikitsa akhristuwo za ubwino wolimbikitsa moyo wokhululuka. Papa Francis wati ngati akhristuwo atalimbikira kuchita izi ndiye kuti adzathandiza pa ntchito zolimbikitsa umodzi ndi chiyanjano pakati pawo. Papa Francis wakhala ali mdziko la Romania kuyambira kumapeto a mwezi wa May ndipo wamaliza ulendo wake pa 3 June.
13
Bungwe la MANEPO Lapempha Boma Liganizire Anthu Achikulire pa Mliri wa Coronavirus Bungwe loyanganira anthu achikulire la Malawi Network of Older Persons Organisation (MANEPO) lapempha boma kuti liganizire anthu achikulire pomwe likuyika ndondomeko zokhudza nthenda ya COVID-19. Kudzera mu kalata yomwe bungwe la Manepo latulutsa, mkulu wa bungweli Andrew Kavala wati kusowa kwa malamulo okhazikika oteteza anthu achikulire kukupitilira kuyika anthuwa pa chiopsyezo cha nkhanza zosiyanasiyana. Iye wapemphanso boma ndi mabungwe kuti pakhale njira zabwino zofalitsira mauthenga a COVID-19 kuti nawo anthu achikulire afikiridwe ndi mauthenga okhudza njira zabwino zopewera mliriwu. Mfundo za kuno ku Malawi zimasala anthu achikulire ndipo ichi ndi chiopsezo chachikulu ku matenda a COVID-19 kwa anthu amenewa, anatero a Kavala. Iwo apempha boma kuti liyike malamulo amphamvu oteteza anthu achikulire kwa anthu omwe amawaphwanyira ufulu.
6
Kwaya ya St. James Chilomoni Yakwanitsa Zaka 40 Wolemba: Sylvester Kasitomu wp-content/uploads/2019/09/chilomoni.jpg" alt="" width="427" height="391" />Tchalitchi la St. James Chilomoni ku Blantyre Kwaya ya St. James ya m`parish ya Chilomoni mu arkdayosizi ya Blantyre yayamikira mamembala ake omwe akhala akutumikira mu kwayayi kwa nthawi yaitali kamba ka kakudzipereka kwao potukula maimbidwe mu kwayayi. Wapampando wa kwayayi a Ezekiel Lokote ndiwo alankhula izi pa mwambo wa msembe ya ukaristia yothokoza mulungu kuti kwayayi yakwanitsa zaka makumi anayi (40) chiyikhazikitsireni. Iwo ati mamembalawa achita zazikulu mu kwayayi kwa nthawi yaitali zomwe ati zathandiza kwambiri potuluka mayimbidwe a kwayayi. Ifeyo tinachiona cha nzeru kuti tikonze mwambowu pofuna kuwathokoza mamemba athu kaamba ka ntchito yomwe agwira poonetsetsa kuti mayimbidwe mukwayayi akhalepo kwa zaka 40 zapitazi ena mwa mamembalawa akwanitsa zaka 30 akuimbira mulungu mukwayayi zomwe ndizonyaditsa Polankhulapo mmodzi mwa omwe atumikira kwayayi kwa zaka zochuluka mayi Betti Banda anati iwo anayamba kwayayi ali ndi zaka zochepa mpaka pano zomwe zachititsa kuti moyo wawo wamapempero usinthike. Ndinayamba kwaya imeneyi ndiri ndi zaka 10 ndipo ndaimba kwayayi kwa zaka makumi atatu zomwe ndizopindulitsa mu moyo wanga wa uzimu kaamba koti pamene kwayayi ikukula inenso ndikukula muuzimu, anatero mayi Banda. Kwaya St. James yomwe inayimbira misa yolandira mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse papa yohane Paulo wachiwiri yemwe anayendera dziko lino mu chaka cha 1989 inakhazikitsidwa mu chaka cha 1979.
13
YODEP Yalonjeza Kuthandiza Achinyamata Kukhala Odzidalira Bungwe la Youth Development YODEP lati lipitilira kuthandiza achinyamata kuti akhale ndi upangiri oyenera pa nkhani za chuma ndi cholinga choti azitha kumadzithandiza okha pa mavuto omwe amakumana nawo mdziko muno. Mkulu wa bungwe-li Mac-Blessings Buda wayankhula izi pambuyo pa mwambo wopereka mbuzi ku makalabu asanu ndi imodzi a achinyamata opezeka mmidzi ya mdera la mfumu yayikulu Chowe mboma la Mangochi. Iwo ati bungwe lawo lachita izi ndi cholinga chofuna kuti achinyamata azipeza thandizo la ndalama akagulitsa ziwetozi. Polankhulapo mfumu Nkata yochekera mderali inati ndiyokondwa kaamba ka thandizo lomwe bungweli lapereka kwa anthu zomwe iwo ati zithandiza achinyamatawa pa nkhani za maphunziro ndi zosoweka pa moyo wawo wa tsiku ndi tsiku. Ife tiri othokoza kwambiri a bungwe limeneli la YODEP kaamba kobwera mmudzi muno kudzapereka thandizo la ziweto zomwe zithandize anawa kupezako mathandizo a zomwe amasowa. Makope, zolembera, school uniform ndi zina azizipeza akagulitsa mbuzizi, anatero a group a Nkata. Bungweli lapereka mbuzi zokwana 60 kwa achinyamata ochokera mmakalabu 6 mmidzi yozungulira Group Village Nkata mfumu yayikulu Chowe mboma la Mangochi.
2
2017 yatilandira ndi zigumula Pangotha sabata chilowereni chaka cha 2017, koma malipoti a ngozi zakudza ndi mvula mmaboma osiyanasiyana atopetsa kale. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nyumba, sukulu, misewu, katundu ndi zakudya za anthu ena zaonongeka ndipo Amalawi ena ali pamavuto kaamba ka ngozizo. Lachitatu lapitali, nyumba 32 zidasasuka kudzanso zipupa zina kugwa kaamba ka mvula ya mphepo ya mkuntho yomwe idagwa kwa mfumu yaikulu Mkukula mboma la Dowa komwe idaononga katundu ndi chakudya. Mlatho wa pa Jalawe ku Rumphi udaguvukira mvula itakokolola zoulimbitsa Agulupu aakulu a Mengwe omwe dera lawo lidakhudzidwa kwambiri adati mvula ndi mphepozo zidayamba mma 3 Koloko masana a tsikulo ndipo mmudzimo mudali kokakoka anthu kusowa kolowera ndi pogwira. Chakudya chathu monga ufa, pogona ndi zofunda komanso katundu wina ofunika zidaonongeka pangoziyo moti ndi mwayi kuti palibe yemwe adavulala, adatero Mengwe. Mkulu wapolisi mbomalo Felix Phiri adakafotokozera ofesi ya DC momwe zinthu zilili apolisi atakayendera madera okhudzidwawo kuti athandizane zochita. Lachitatu lomwelo, anthu 7 adavulala pamalo okwerera basi a Mibawa mumzinda wa Blantyre mvula yamphamvu itazula chimtengo chomwe chidali pafupi ndi malowo nkuwugwetsera pa maminibasi 7. Lachiwiri, mvula ina ya mphamvu idakokolola mlatho wa Jalawe omwe umalumikiza maboma a Rumphi ndi Karonga pa msewu wa M1. Malingana ndi DC wa mboma la Rumphi Lusizi Nhlane, mvula yamphamvu idagwa usiku wa Lachiwiri zomwe zidapangitsa kuti madzi aziyenda mwamphamvu mpakana kufowola mizati ya mlathowo omwe udakokoloka. Ngozi zina zokhudzana ndi mvula yamkuntho zidachitika tsiku loyembekeza kulandira chaka cha tsopano pa 31 December, 2016 mdera la mfumu yaikulu Nanseta mboma la Thyolo komwe nyumba 114 zidaonongeka. Kauni yemwe khonsolo ya boma la Thyolo adachita wasonyeza kuti chiyambire mvula ya chaka chino, nyumba 1 000 ndizo zakhudzidwa ndipo izi zapangitsa kuti mavuto a malo okhalapo akule mbomali. Pa 31 December, 2016 pomwepo, nyumba 96 zidaonongeka ndi mvula yamkuntho yomwe idagwa mboma la Karonga ndipo a komiti ya zachitetezo ya District Civil Protection (DCPC) adati izi zidafikitsa chiwerengero cha nyumba zokhudzidwa pa 424 mbomali. Komitiyo idati midzi ya Mwamutawali, Mponera ndi Mwandovi ndi ina mwa midzi yomwe yakhudzidwa ndi mvula zolusazi mbomali ndipo zina mwa zomwe zaonongekeratu ndi sukulu ya pulaimale ya Chisumbu ndi msika wa Jetty. Nthambi yoona zanyengo mdziko muno idalengeza kumayambiriro a Mvula kuti chaka chino dziko lino liyembekezere mvula yamkuntho chifukwa cha mphepo ya La Nina yomwe nthawi zambiri imabweretsa mvula yamtunduwu. Pankhaniyi, mneneri wa nthambi yoona ngozi za dzidzidzi Jeremiah Mphande adati ndilokonzeka kulimbana ndi zotsatira za Mvula ya mtunduwu itati yabwera chifukwa ilo mothandizana ndi maiko ena komanso mabungwe adakhazikitsa kale ndondomeko zoyenera.
5
Chimulirenji apempha nduna zipewe katangale By Thokozani Chapola ent/uploads/2019/07/chimu.jpg" alt="" width="481" height="318" />Wachenjeza nduna za boma Chimulirenji Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Everton Chimulirenji walangiza nduna komanso achiwiri kwa nduna za boma kuti apewe katangale ndi ziphuphu. Chimulirenji walankhula izi pamene amatsegulira maphunziro a nduna za boma ku Sunbird Nkopola Lodge mboma la Mangochi. Iye walangizanso ndunazi kuti zikhale ndi chidwi pa maphunzirowa kaamba koti ndi omwe awathandize kugwira ntchito yawo moyenera. Ngati nduna mugwire ntchito yanu modzipereka komanso mupewe kuchita katangale mu ntchito yanu chifukwa katangale ndi mdani wa chitukuko, anatero Chimulirenji. Polankhulapo nduna yowona za maboma aangono ndi chitukuko cha kumudzi Ben Phiri wati aliyense amene apezeke kuti akukhudzidwa ndi katangale, lamulo ligwira ntchito pa iye. Nkhani yothetsa katangale si president yekha ayi koma ifeyo amene iye watikhulupilira kuti tiyendetse naye limodzi dziko lino. Amene apezeke akukhudzidwa ndi katangale lamulo ligwire ntchito pa iye ndipo panopa pakufunika munthu akakhudzidwa ndi katangale azichotsedwa ntchito osati kungomusintha malo ogwira ntchito, anatero a Phiri. Kumbali yake nduna yoona za ntchito mayi Martha Lunji Mhone Chanjo wati maphunzirowa awathandiza kudzindikira bwino ntchito yawo. ngati nduna timakhala patsogolo kupanga ziganizo mmalo mwa anthu choncho maphunzirowa atithandiza kuzama mmaganizidwe, kudziwa bwino ntchito yathu kuti titumikire anthu moyenera, anatero mayi Chanjo. Maphunzirowa omwe ndi a masiku awiri anayamba lolemba pa 15 July ndipo anatha lachiwiri pa 16 July, 2019.
14
Abwenzi a ku Phalombe athandiza Radio Maria Wolemba: Glory Kondowe 02/homepage-5.jpg 2000w" sizes="(max-width: 635px) 100vw, 635px" /> Abwenzi a Radio Maria Malawi ku parishi ya Phalombe mu Arkdayosizi ya Blantyre, lachisanu ati mkofunika Click to Tweet Leo Bwanaisa yemwe ndi Katekisiti wa parishiyi wanena izi loweruka pomwe abwenzi a mparishiyo, amapereka thandizo lawo ku wailesiyi. Bwanaisa wati abwenziwa, aperekathandizoli, atazindikira kuti ndi njira yokhayi yomwe angatsate pofuna kufikira anthu ambiri ndi uthenga wa Mulungu, kaamba koti pawokha sangakwanitse kufikira munthu aliyense ndi uthenga wa Mulungu. Tachita izi ngati njira imodzi yotenga nawo mbali pofalitsa uthenga wabwino, anatero a Bwanaisa. Mwazina, abwenziwa apereka thumba limodzi la mpunga ndi ndalama zokwana 62 sauzande kwacha.
14
Asanu anjatidwa atakana kupeleka magazi Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Govt to review Genset deal Abambo asanu a mboma la Mangochi anjatidwa powaganizira kuti adalephera kupereka magazi kwa mwana wa zaka 7 kaamba ka zikhulupiriro za mpingo wawo. Malinga ndi mneneri wapolisi ya Mangochi, Rodrick Maida, abambowa adatengera mwana kuchipatala cha Koche Health Centre komwe adakamugoneka akudwala malungo. Koma anamwino atamupima akuti adaona kuti mwanayo ankasowa magazi kotero adapempha mmodzi mwa abambowo amene ndi bambo ake kuti apereke magazi. Akufuna kwabwino ngati anthu awa akupulumutsa miyoyo. Bamboyo Saimoni Kamwendo wa zaka 44 ndipo yemwe amachokera mmudzi mwa Mapata kwa T/A Mponda ku Mangochi komweko, adakana kuti sangapereke magaziwo. Maida adati bamboyo atakana, anamwinowo adapempha amalume a mwanayo omwe adalipo atatu kuchipatalako kuti apereke magazi koma nawonso adakana. Achipatalawo adapempha agogo a mwanayu, Bernard Kamwendo, kuti apereke magaziwo koma nawonso adakana kupereka magaziwo ponena kuti ndi ampingo wa Mboni za Yehova ndipo samaloledwa kupereka magazi, adatero Maida. Iye adati nthawiyo mwanayo amasowa magazi kuti akhale moyo ndipo adamutengera kuchipatala chachikulu cha Mangochi pamene sisitere yemwe amayanganira chipatala cha Koche, Elizabeth Kamuikeni, adati apereka magaziwo. Kamuikeni adapereka magaziwo ndipo mwanayo adayamba kupeza bwino mpaka amutulutsa mchipatala. Ngakhale iyi idali nkhani yabwino koma kwa amunawa idali yowawa chifukwa kulandira kapena kupereka mankhwala kwa wodwala si ziloledwa ndi zikhulupiriro za mpingo wawo. Amunawa adayamba kuopseza kuti amutengera kubwalo la milandu sisitereyo popereka magaziwo. Achipatala adatidziwitsa tidathamanga ndi kudzamanga amunawa. Tawatsegulira mlandu wolephera kupereka thandizo kwa mwana zomwe zikusemphana ndi gawo 242 la malamulo ndi zilango zake ndipo chilango chake ndi zaka zitatu mndende ukugwira ntchito ya kalavula gaga, adatero Maida. Koma mmodzi mwa amene amapemphera chipembedzochi ndipo sadafune kutchulidwa dzina adati ndi zoona kuti kulandira kapena kupereka magazi sikololedwa ndi chikhulupiriro chawo. Iye adati izi samangochita koma pali malembo a mbaibulo amene amatsimikizira mfundoyi. Iye adatsindika kuti ndi bwino kuchita mosangalatsa Mulungu kulekana ndi kusangalatsa munthu. Komabe mpingowu uli ndi nthambi yomwe imafotokozera bwino nkhani zotere. Ndikhulupirira kanthawi kena mudzacheza nawo kuti adzatambasule bwino chomwe malembo amanena pa nkhaniyi, adatero. Nkhani ya amunawa idalowa mbwalo la milandu pa 24 April ndipo ikuyembekezerekanso kulowanso pa 27 May pamene mbali ya boma ibweretse mboni zina ziwiri omwe ndi ogwira ntchito pachipatala cha Koche. Amalume a mwanayu ndi Solomon Mwabwino wa zaka 29, Diverson Wabwino wa zaka 21 komanso Baison Chindanda wa zaka 40.
15
Ine ayi, Dausi wakana Chaponda Zomwe zachitika ku bwalo la mirandu ku Lilongwe msabatayi zalephera kupherezera mwambi woti khoswe akakhala pa mkhate sapheka. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Khwimbi la anthu lidapita kubwaloli Lachiwiri kukamvera mlandu wa nduna yakale ya zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi George Chaponda koma adachokako akupukusa mitu. Dausi: Anangotenthedwa Zomwe aliyense samayembekezera zidachitika nduna yazofalitsa nkhani Nicholas Dausi itanena mmaso muli gwaa kuti siikudziwapo kanthu pa ndalama zomwe zidapezeka mnyumba mwa Chaponda, mlandu omwe akuyankha pakali pano. Chaponda akuyankha mlandu wopezeka ndi ndalama zankhaninkhani za mMalawi komanso zakunja mnyumba popanda chilolezo cha Reserve Bank of Malawi monga momwe zimayenera kukhalira. Podziteteza ku mlanduwu, Chaponda adauza bwalo la milandu kuti K95 miliyoni pa ndalamazo zidali za chipani cholamula cha Democratic Progressive (DPP) ndipo kuti Dausi ndiye amayenera kukatenga ndalamazo nkukapereka kuchipani. Poperekera umboni wake, Dausi adauza bwalolo kuti zoti ndalamazo zidali za DPP nzabodza komanso kuti dzina lake lidangotchulidwamo nkhaniyi iye sakudziwapo kanthu. Zoti ine ndikudziwapo kanthu nzabodza. Mwina [Chaponda] adangosokonekera ponditchula chifukwa munthu akakhala pampanipani oterewu, kaya ndi phungu kapena nduna, mphamvu zimatheratu, adatero Dausi. Chaponda adali mmodzi mwa nduna zikuluzikulu za boma ndipo zake zidatembenuka chaka cha 2017 ali nduna ya zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi pomwe adayamba kufufuzidwa poganiziridwa kuti amakhudzidwa ndi kusokonekera kwa kagulidwe ka chimanga ku Zambia. Chaponda adamangidwa limodzi ndi mkulu wa kampani ya Transglobe Produce Export Limited Rashid Tayub ndi Grace Mijiga Mhango wa bizinesi yemwenso ndi wa pampando wa bungwe la makampani ogula ndi kugulitsa mbewu. Mmwezi wa February, nthambi yolimbana ndi katangale idakachita chipikisheni ku nyumba ndi ku ofesi ya Chaponda komanso ku mawofesi a Admarc komwe kudapezekanso zododometsa zina. Kuofesi ya Admarc, nthambiyi idalanda makina a kompyuta pomwe kunyumba kwa Chaponda idapezako ndalama zankhaninkhani za dziko lino ndi maiko ena monga za ku Amereka zomwe zidapangitsa kuti nkhaniyi yomwe poyamba imakhala ngati ingawakomere a Chaponda, itembenuke.
11
Boma ndi anthu a ku Cape Maclear Sakumvana pa Nkhani ya Malo a Hotela Wolemba: Thokozani Chapola Kusamvana kwabuka pakati pa boma ndi anthu a mmudzi wa Chembe mdera la Cape Maclear mboma la Mangochi pa nkhani ya malo amene pamangidwe hotela ya pamwamba (5-star hotel). Izi zadziwika pa mkumano omwe akuluakulu a ku unduna wa zokopa anthu komanso khonsolo ya boma la Mangochi anachititsa pokumana ndi anthu a mderali ndi kuwafotokozera za chitukukochi. Anthuwa anayankhula poyera kuti sakufuna kuchoka pa malowa kaamba koti pa umoyo wawo wa tsiku ndi tsiku amadalira mu nyanjayi ndipo apempha boma kuti ngati likufuna kumanga hotelayi liwonetsetse kuti isakhudze malo amene anthuwa akukhala. Ifeyo tili ngati nsomba kungotichotsa kumadzi kuno kukatisiya ku mtunda basi pompo tifa. Ife sitikukana chitukuko chifukwa ndi chinthu chabwino ndipo chizapindulira ife tomwe koma chomwe tikupempha ndi chakuti asatisamutse kuno. Iwowo ngati akufuna kumanga hotel yo amange koma awonetsetse kuti isakhudze anthu ammudzife, anatero Richard Zatha yemwe ndi mmodzi mwa mzika za derali. Pamenepa iwo apempha akuluakuluwa kuti abweretse chitsanzo cha maonekedwe a hotelayi (Sketch map) komanso mulingo wa malo amene itenge. Tawauza kuti atiuze kukula kwa malo amene akufuna akanika kutero ndiye chimene tawapempha ndi chakuti akamazabweranso ulendo wina azabweretse maonekedwe a hotela imeneyi kuti idzakahala yowoneka bwanji komanso kuti izafuna malo aakulu bwanji kuti tidziwiretu ngati itakhudze anthu a mdera lino, anatero Zatha. Koma polankhulapo pakutha pa msonkhanowu, bwanamkubwa wa boma la Mangochi, mbusa Moses Chimphepo wati ndi okondwa kuti anthu a mderali atulutsa madandaulo awo ndipo awonetsetsa kuti achite monga momwe anthuwa akufunira. Chimene chandisangalatsa ndi chakuti anthu a kuno chitukukochi sakuchikana koma sakufuna kuti project imeneyi iwachotse ku dera kuno. Pamene tisanamvetsaetsane ndi pa kukula kwa malo omwe akufunidwawo ndiye zimenezo tidikira akatswiri abwere azayeze malo amene afunidwewo ndipo ndi pamene tizawadziwitsenso, anatero mbusa Chimphepo. Ntchito ya ngati yomweyi inakanikanso mzaka za pakati pa 2013 ndi 2015 pamene kampani ya MotaEngil imkafuna kumanga hotela yapamwamba ku Monkeybay mdera la Masasa kaamba koti sanamvane maganizo ndi eni derali.
14
Kulambira Kalonga Gawa Undi Tamvapo zambiri za mwambo wa Kulamba. Mongokumbutsana, Kulamba ndi mwambo womwe mafumu Achichewa mmaiko a Malawi, Mozambique ndi Zambia amapezerapo danga lokapereka uthenga wa mmene zinthu zikuyendera mmadera awo kwa mfumu yawo yaikulu, Kalonga Gawa Undi. Lero tati tisanthule zina ndi zina zomwe zimaloledwa kuchita ndi kusachita pamaso pa mfumu ya Achewayi. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu kumwambo wa Kulamba wa chaka chino motere: Ndikudziweni mfumu. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ine ndine Senior Chief Lukwa, mmodzi mwa mafumu akuluakulu pakati pa Achewa a ku Malawi ndipo ndimachokera mboma la Kasungu. Tandifotokozerani zokhudza ulemu wa Kalonga Gawa Undi kuyambira mmene mumaperekera moni. Kalonga Gawa Undi ndi mfumu yaikulu kwambiri pakati pa Achewa kotero kuti ulemu wonse womalizira pakati pa Achewa umayenera kupita kwa Kalonga Gawa Undi. Pachifukwa ichi, palibe munthu aliyense yemwe amaloledwa kugwirana chanza ndi Kalonga Gawa Undi pokhapokha kalongayo atayamba yekha kupereka mkono koma sayenera kukhudzidwa mwanjira iliyonse. Nanga popereka mphatso kwa Kalonga Gawa Undi zimakhala bwanji? Uwu ndi mwambo wina wapadera womwe umafunika kusamala kwambiri. Popereka mphatso kwa Kalonga Gawa Undi munthu amayenera kuika mphatsoyo pansi kapena pagome lomwe lakhazikitsidwa mwini wake akuona. Akatero, imodzi mwa nduna zake za kalongayo amakatenga mphatsoyo nkukaika pamalo oyenera, osati kumupatsira mmanja, ayi. Nthawi zonse kumakumbuka kuti kalonga ndi munthu wamkulu. Nanga pokumana ndi Kalonga Gawa Undi, munthu amayenera kutani? Pokumana ndi Kalonga Gawa Undi, munthu amayenera kukhala pansi chotambalala osati chokhwinyata, ayi. Ngakhale mipando itakhalapo yambiri motani munthu amayenera kukhala pansi pokhapokhapo ngati mwini wake kalongayo wakukakamiza kuti ukhale pampando. Ngati uli Mchewa weniweni, ngakhale Kalonga atakukakamiza chotani, umayenerabe kukana ndi kukhala pansi basi, koma nkofunika kukumbukira kutambalala, osapinda miyendo pamaso pa Kalonga Gawa Undi. Nanga ungatani kuti Kalonga Gawa Undi akupatse mpata wolankhula naye? Funso limeneli limavuta nthawi zambiri chifukwa anthu amaona ngati Kalonga Gawa Undi amangolankhula chisawawa. Pomwe Kalonga waperekera mpata wolankhulana naye si pano ndipo ngati ukufuna kulankhula naye umayenera kuomba mmanja ndi kulankhula mokwenza mawu akuti: Yooh, Gawa! katatu ndipo ngati ali ndi mpata akhoza kukupatsa mwayi wolankhulana naye. Nanga ngati mfumu yaikulu ya Achewa, ubale wake ndi wotani ndi gulewamkulu? Choyamba, gulewamkulu alibe mphamvu iliyonse kwa Kalonga Gawa Unidi, chimodzimodzinso naye, ngati kalonga, alibe nthawi yopanga za gulewamkulu. Ntchito imeneyi amalekera mafumu ake kuti aziyendetsa. Kalonga akamayenda amayenera kuzunguliridwa ndi mbumba zake (amai oimba nyimbo). Nchifukwa chiyani mbumba, osati nduna? Pamwambo wa Achewa amayi ndiwo amakhala ndi mphamvu zosankha mfumu. Pachifukwachi, amayi amapatsidwa ulemu wapadera chifukwa popanda iwo kasankhidwe ka mfumu kamasokonekera. Kalonga Gawa Undi amadziwa zonsezi ndiye pofuna kulemekeza udindo womwe amayi ali nawo, nchifukwa amafuna kuti mbumba ndizo zizimuperekeza.
1
Arch-dayosizi ya Lilongwe Yatsekula Parish Yatsopano Arch-dayosizi ya Lilongwe yawonjezera ma parish ake kutsatira kukhazikitsidwa kwa parish yatsopano ku Mchinji boma. Walengeza za nkhaniyi-Ziyaye Kudzera mu kalata yomwe yasayinidwa ndi Arch Episkop a Arch-dayosizi yi ambuye Tarsiziyo Ziyaye ati mwambo wapadera okhazikitsa parish yi uchitika masiku akudzawa. Izi zikutanthauza kuti tsopano Arch-dayosiziyi ili ndi ma parish okwana 41. Kalatayi yafotokozanso kuti bambo Audifansio Kapinga ndiwo asankhidwa kukhala Bambo mfumu ku parish yatsopanoyi. Mwazina kalatayi yafotokozanso ma udindo ena omwe ambuye Ziyaye asankha komanso ena kuwatumiza kukatumikira kwina. Bambo Francisco Bisai awasankha kukhala Bambo mfumuku parish ya Kachebere mboma la Mchinji, Bambo Andrew Kholowa awasankha kukhala bambo mfumu ku parish ya Mkanda mbomalomweli la Mchinji, Bambo John Kaliwamba awasankha kukhala mlembi wa Arch Episkop a Arch-dayosiziyi ya Lilongwe, Bambo Alberto Elifala awasankha kukhala bambo mthandizi ku parish ya Mtima Woyera ku Lilongwe, Bambo Geoffrey Chikapa awasankha kukhala bambo mthandizi ku parish ya Nambuma mboma la Dowa, Ndipo Bambo Demetrio Banda awasankha kukhala owona zachuma ku St. Pauls Minor Seminary ku Mlale. Pamenepa, Ambuye Ziyaye ati ma udindowa ayamba kugwira ntchito pano ndipo afunira zabwino ansembewa pomwe akhale akugwira ntchito yawo.
13
Anjata wopezeka ndi mitengo ya tsanya Apolisi ku Lilongwe Lachitatu adanjata nzika ya ku China chifukwa chomuganizira kuti adapezeka ndi mitengo ya tsanya yomwe nzikayo imafuna kutumiza kwawo kuti ikasake misika. Nzikayi adaigwira pabwalo la ndege la Kamuzu International Airport dzuwa lili paliwombo pamalo ochitira chipikisheni pabwalo la ndegelo ndipo akuti katunduyo amafuna kumukwenza ndege yopita kwawo kudzera ku Ethiopia. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Apolisi a pabwalo la ndegelo adati mkuluyo, Lin Jie, adavomera mlanduwo ndipo adati mitengo yomwe amafuna kutumiza kwawoko idali yokafufuzira msika chabe kuti msikawo ukapezeka, ayambe bizinesi yotumiza mitengoyi kwawo. Yemwe amatanthauzira pakati pa apolisi ndi mkuluyo, Shi Qi Bine, adanena mosapsatira kuti iye amafuna kuyamba bizinesi yogulitsa mitengoyi kunja ndipo yomwe amatumizayo idali yokangoonetsa chabe, adatero Sapulani Chitonde, mneneri wa polisi pabwalo. Iye adati Lin Jie adauza apolisiwo kuti dziko la Malawi likufunika anthu ngati iye amasomphenya ofuna kupeza njira zina zopezera ndalama osati kudalira njira zamgonagona. Mkuluyu adabwera mdziko muno mwezi wa May chaka chino ndipo amakhala mumzinda wa Lilongwe. Malingana ndi malamulo a dziko lino, ndi mlandu kupezeka ndi zamnkhalango popanda chilolezo chilichonse ndipo apolisi ati adzathana ndi aliyense wopezeka ndi katundu wamnkhalango mwachinyengo kapena wofuna kutulutsa katundu woletsedwa kudzera pabwalo la ndegeli. Kumapeto a mwezi watha, apolisi adagwira nzika inanso ya ku China aipeza ikufuna kuzembetsa minyanga ya njovu yoduladula mapisi nkuibisa mchikwama ndi cholinga choti apite nayo kwawo.
19
Chonona chifumira kudzira Tikamakamba za kufunika kuti pasamakhale kusiyana pa mwayi womwe amayi ndi abambo akupatsidwa, titamakumbuka za mwambi uwu wakuti chonona chifumira kudzira. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Izitu zikutanthauza kuti kusintha kwenikweni pakhalidwe la anthu kwagona pa momwe anthu akuleredwera mmakomo mwawo, mmadera momwe tikukhala, mmipingo komanso kusukulu. Chimodzimodzinso nkhani ya kuthetsa nkhanza mmabanja komanso nkhanza zina zomwe anthu amakumana nazo kaamba koti ndi aakazi kapena aamuna, tikumbuke ndithu kuti nthawi youmba khalidwe la munthu ndi nthawi yomwe akukula. Mwachitsanzo, anthu ambiri-abambo ngakhalenso amayi-amene amakhala ndi mtima woderera amayi, amakhala kuti adakula pakati pa chikhalidwe chomwe chimaonera amayi pansi. Anthu oterewa amavuta kuti akhale pansi pautsogoleri wa mzimayi chifukwa amangoona kuti munthu amene akuwalamula sakuyenera kutero. Chikhalidwe cholakwikachi chimakhala chokhazikika mmitu mwawo ndipo kukonza kwake akakula kumakhala kovuta. Tsono udindo wambiri wokonza makhalidwe olakwikawa uli mmanja mwa makolo poonetsetsa kuti nzika zomwe mukulera zikhale ndi zikhulupiriro komanso makhalidwe oyenerera osapondereza, kuzunza kapena kuderera anthu ena kaamba ka momwe adabadwira. Amayi amene azunzika mmabanja ndipo ali ndi ana aamuna, akhoza kuonetsetsa kuti mwana amene akulera uja asadzakhale ngati bambo ake kuti adzazunzenso mkazi wake akakula. Ana aamuna aphuzitsidwe kulemekeza munthu wamayi. Adziwe kuti kusiyana kwawo ndi munthu wamkazi kwagona pa kaumbidwe ka ziwalo zawo pakabadwidwe. Zikakhala nzeru ndi machitachita ena palibe kusiyana. Auzidwe ana aamuna kuti mzimayi ndi muthu ngati iwo. Si chida chongoti wina akafuna agone nacho kapena kumamunyozetsa kumamuimbira miluzi akamayenda mmisewumu. Chimodzimodzinso ana akazi tiwaphunzitse kuti ali ndi kuthekera kofikira komanso kukhala chilichonse chomwe angafune pamoyo wawo. Tiwaphunzitse atsikana kuti asadalire thumba la munthu wammuna chifukwa chomwe bambo akuchita kuti apeze ndalama pakhomo iwonso akhoza kupanga. Mtsikana asalunjike nzeru zake pa thupi lake. Pali luso, nzeru ndi zinthu zina zomwe anadalitsidwa nazo kuti zipindulire iye komanso dziko. Aphunzitsidwenso mwana wamkazi kuti asalole munthu aliyense kumukokera pansi kapena kumuchitira nkhanza-angakhale mbale kaya mwamuna wake. Mwanayo auzidwe akali wamngono kukana ndi kusapirira mtundu uliwonse wa nkhanza.
15
UTM Idakalingalira za Mgwirizano Chipani cha UTM chati chilengazabe ngati chikhale pa mgwilizano ndi chipani china pokonzekera chisankho cha President chomwe chikuyembekezeka kuchitikanso mdziko muno. Zonse zikakonzeka tikudziwitsani-Chilima Mtsogoleri wachipanichi Dr. Saulos Chilima wati padakali pano sanganepo pankhani ya mgwirizano ndi zipani zina pofuna kukwaniritsa 50+1. Iye wanena izi pa msonkhano umene wachititsa loweruka pa bwalo la Masintha mu mzinda wa Lilongwe. Tikuyenera kukambirana bwino zimene tigwirizane mu mgwirizanomo si nkhani yongothamangira ayi chifukwa nthawi idakalipobe ndipo tikuuzani tikakonzeka kutero, anatero Dr. Chilima. Iye wati ndi zothekanso chipanichi kuyenda chokha pa chisankhochi osagwirizana ndi chipani chilichonse ndipo ndi kukwanitsa kudzapeza mavoti oposa theka la anthu ovotawo ponena kuti Dr. Bakili Muluzi komanso Dr. Bingu wa Mutharika anakwanitsapo kutero. Mwazina Chilima wapempha President Peter Mutharika kuti athandize pothetsa mavuto amene dziko lino likukumana nawo monga njala kusowa kwa mankhwala mzipatala mwazina ponena kuti dzina la Mutharika ndi lomwe likuyipa osati la anthu omwe amuzungulira omwe akumamuuza zabodza. Uwu ndi msonkhano wake oyamba pambuyo pa chigamulo cha khoti pa nkhani ya chisankho chomwe chinachitika pa 21 May chaka chatha.
11
Kuvulaza namfedwa Ndinali pa maliro ena masiku apitawa komwe amfumu adaganiza zokhutula nkhawa zawo za anamfedwa tili kumanda. Amfumuwo adati sadakondwe ndi momwe bambo wa malemu ankathamangira thamangira pamaliro mmalo mosiira ena kuti amuthandize. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polankhula, amfumuwa adadzudzula bamboyo akuti chifukwa ali ndi chizolowezi chochita zinthu mwayekha posafuna kuthandizidwa ndi ena. Aka sikanali koyamba kumva anamfedwa akudzudzulidwa mokhadzula mokhudzana khalidwe lawo pamudzi. Ena amadzudzulidwa kaamba kosapezeka maliro akagwera anthu ena. Ena amadzudzulidwa chifukwa chophonya ndondomeko kapena miyambo ina yokhudza maliro. Ndaonaponso anamfedwa ena ataphikiridwa nsima pamaliro nkuwasiira kuti adye okha ati chifukwa iwo akapita kumaliro a ena sadya chakudya. Pamene anthu tikukhala mmagulu, sipangalephere wina kulakwitsa kapena kulakwira ena. Nthawi zina pa zifukwa zomwe sitidziwa ena sachita nawo zoyembekezeka pagulu ngati kudya nsima pamaliro. Osakhala kuti akudana ndi nsimayo koma anthufe timayenda ndi matenda osiyanasiyana omwe nthawi zina salola ena kumangodyapo chisawawa. Ena kungodya za mchere kaya mafuta ndiye kuti aputa zosaputa mthupi. Sangakwanitse kulengeza za matenda awo kwa aliyense kuti awamvetsetse, nthawi zina kachetechete amangopewa zakudya zomwe sizinaphikidwe mwa dongosolo lomwe adapatsidwa kuchipatala. Yakhota pangono nkhaniyi, apa pagona nkhani lero ndi pa funso ili kuti nchi chifukwa chiyani amfumu ngakhalenso atsogoleri a mmadera ndi midzi yomwe tikukhala amafuna kumudzudzula namfedwa panthawi imene akumva kale kupweteka kotaya mbale wake? Amene mwaferedwapo mukudziwa kuwawa kwa imfa.
15
Alangiza Apolisi Akhale Oyera Mitima Apolisi mdziko muno awapempha kuti agwilitse bwino ntchito nyengo ya kubadwa kwa ambuye yesu pakukhala anthu oyera mitima. Senior Assistant Commissioner Ackis Muwanga ndiye wayankhula izi lachisanu ku Police College mu mzinda wa Zomba pa mwambo wa nyimbo mphwambo la nyimbo za uzimu la mu nyengo ya kubadwa kwa ambuye yesu lomwe limatchedwa Christmas Carols lomwe anakoznera apolisi onse ochokera mchigawo cha ku mmawa kwa dziko lino. Apemphedwa kukhala odziyeretsa Commissioner Muwanga yemwe anali mlendo wolemekedzeka kuyimilira mkulu wa apolisi mchigawochi chaku Commissioner Arlen Baluwa anati mwambowu umatandiza kulimbikitsa umodzi pakati pawo pokonzekera kubadwa kwa ambuye yesu. Zimatithandiza kukhalira limodzi ngatib anthu a zipembedzo zosiyanasiyana kudziyeretsa kuti nyengo ya Christmas ikamafika tikhale tili oyera, anatero Commissioner Muwanga. Poyankhula mmalo mwama choir omwe Aanafika ku mwambowu mayi Martha Perera omwe amayimba choir ya Police College anayamikira ofesi ya apolisiwa mchigawochi kamba kowakonzera mphando lamayimbidweli. Ena mwa ma kwaya anafika ku mwambo wamayimbidwe-wu ndi monga Police College Roman Catholic Choir, Balaka Seventh Day Choir, Zambezi Evangelical Lutheran Women Choir, Police College Mvano Choir, Sadzi Ccap Women Choir, St Gregory Holy Trinity Matawale Parish Choir ndi ena ambiri.
13
Papa Apemphelera Mtendere Wolemba: Thokozani Chapola .jpg 308w" sizes="(max-width: 300px) 100vw, 300px" />Papa: Zidani zimadzetsa nkhondo Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha anthu kuti apemphelere mtendere mmaiko kuti zidani zomwe zimadzetsa nkhondo, zisamakhalepo. Papa amalankhula izi lachitatu kwa anthu omwe anasonkhana pa bwalo la St. Peters Square ku likulu la mpingowu ku Vatican. Papa wapereka pempholi pamene dziko lapansi, lamulungu likudzali pa 1 September, lidzakhala likukumbukira kuti patha zaka 80 tsopano, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse chichitikireni mchaka cha 1939. Iye wati zidani zimadzetsa nkhondo, ndipo zotsatira zake zimakhala zoipa kwambiri monga imfa komanso kuwonongeka kwa zinthu. Mchaka cha 1939, dziko la Germany linayamba nkhondo ndi dziko la Poland, zomwe zinachititsa kuti maiko a Britain ndi France alowelerepo polimbana ndi dziko la Germany, zomwenso zinayambitsa nkhondo ya padziko lonse, pambuyo pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse yomwe inatha mchaka cha 1919.
13
Papa Walimbikitsa Akhritsu Asamakhale Ndi Mantha Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse, Papa Francisco wati mantha sakuyenera kupeza gawo mmoyo wa akhristu. Malinga ndi malipoti a Vatican Radio Papa Francisco walankhula izi lamulungu ku likulu la mpingowu ku Vatican. Iye wati Mulungu amakhala pafupi ndipo amasamalira anthu ake kotero ngati anthu okhulupirira akhristu sakuyenera kuchita mantha ngakhale pa nthawi ya mavuto osaneneka. Papa Francisco wapereka uthenga wa chilimbikitsowu pano pomwe maiko ambiri akudutsa mu nyengo yovuta chifukwa cha mavuto a mliri wa Coronavirus, nkhondo, kusowa ntchito kwa anthu, tsankho, pongotchula pangono ena mwa mavutowa. Polankhula laMulungu kwa anthu omwe anasonkhana pa bwalo la Saint Peters Square komanso kwa anthu ena kudzera pa wayilesi ya kanema ndi makina a intaneti Papayu wati anthu sakuyenera kuchita mantha angakhale akumane ndi zokhoma pa moyo wao monga ma udani kapena kuzunzidwa. Papa Francisco wati akhristu akuyenera kukumbukira nthawi zonse kuti Mulungu ndi wa chikondi, saiwala anthu ake ndipo amakhala nawo pafupi. Iye wati Yesu Khristu anali kuuza ophunzira ake kuti asachite mantha. Papa Francisco wati uwu ndi uthenga umene Yesu Khristu akupitirira kulankhula kwa akhristu masiku ano pomwe anthu pa dziko la pansi akudutsa mmavuto osiyana-siyana. Kwa alaliki a uthenga wa chipulumutso iye wati polalika uthengawu adzapezeka ena outembenuza kuti uwakomere. Pamenepa iye wati izi sizikuyenera kuwadandaulitsa kapena kuwafooketsa koma mmalo mwake zikuyenera kupereka mangolomera olalika uthengawu mwa mphamvu komanso chimwemwe. Pa mwambowo Papa Francisco anakumbutsa anthu zakufunika kosamala chilengedwe. Iye wati pa nthawi ya mliri wa Coronavirus chilengedwe mmaiko ambiri chakhala chosamalika bwino chifukwa cha kuchepa kwa ma ulendo a ndege ndi galimoto omwe amaononga chilengedwe ndi mpweya woipa. Iye wati pano pomwe ma ulendowa ayambika pangonopangono ndi bwino kuti anthu akhale a chidwi posamalira chilengedwe.
13
Masiku 100 a Mutharika sanakome Mtsogoleriwa dziko lino Peter Mutharika sabata yatha adakwanitsa masiku 100 pampando wa pulezidenti koma panyengoyi sadamwe wa mkaka.. ChiulutsirenikupambanakwaMutharika, Amalawi ataponya voti pa 21 May 2019, dziko la Malawi layendammikwingwirimayokhayokhapomweAmalawienaakhalaakuchitazionetserozosonyezakusakondwandimomwechisankhochichidayendera. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mutharika kulandira lupanga la ulemu atapambana chisankho Ngakhalemalamulo a dziko lino amaperekampatawochitazionetserozamtendere, zionetserozaulendounozaonetsaAmalawizambiripomwekatundu, bizinesi, galimotozaanthukomansozabomazawonongedwa. Izizafikapovutakwambirimpakabwalolailandusabatayathalidagamulakutipasachitikensozionetserokwamasiku 14 kutimbalizotsutsanazikambiranekutizionetserozozidzaayendabwanjimwabata. Katswiri pa ndale Ernest Thindwawatimmasiku 100 oyambirira a utsogoleriwaMutharikaAmalawiaonambwadza. Iyewatikwanthawiyoyambachiyambireniulamulirowazipanizambiri, AmalawiaonakugawanamitundundipoPulezidentiangoyanganira. Ngakhalemlanduukadalikukhoti, Mutharikandimtsogolerimpakakhotilidzagamulemwanjiraina. AkadakhalawinaakadagwiritsantchitomphamvuzakekulunzitsaAmalawindipoanthuakadamukonda, wateroThindwa. Iyewatikutikulunzanitsakokutheke, Mutharika, ndunazabomakomansoatsogoleri a zipanizotsutsabomaakuyenerakusankhamawuolankhula pa misonkhano. Ndipokadaulo pa pakayendetsedwekazinthumdzikoMakhumboMunthaliwatiboma la Mutharikalisadzilimbitsemtimakutizinthuzilibwinopomwezayipiratu. Mdzikomulizipolowezokhazokha, anthuakuotcherananyumba, galimotongakhalensomaofesindiyenkumatizilibwino? Ayi, wateroMunthali. Iyewatingatiboma la Mutharikalikufunaanthualikhulupilire, liwapangirezomweakufuna. Komandunayofalitsankhaniyomwensoimalankhuliraboma Mark BotomaniwatiMutharikawayendamofewa. Sitikuonapochipsinjochilichonse. Mutharikawayendetsabwinodzikondipoakukwaniritsazomweadalonjeza, wateroBotomani. Iyewatimmasiku 100 apitawa, boma la Mutharikalabzala kale zitukukomongamisewu, damu la madzikuDedza, kuonjezeramphamvuzaasilikalipowagulirasitimazankhondokomansokusainiramaubaleaukazembeosiyanasiyana. Amenesakufunaakhale, komaMutharikawatiuzakutiakufunachitukukopaliponsendipoifendunazaketikupangachitukukochomwakathithi, wateroBotomani. Amalawiakufunamkuluwabungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansahatulepansiudindokomapolankhulandiwayilesiya BBC, MutharikaadamenyetsankhwangwapamwalakutiAnsahsachoka pa pandowo.
11
Likodzo limatha magazi mthupi Likodzo ndi matenda amodzi amene akapanda kuzindikiridwa msanga akhoza kupha munthu chifukwa amayamwa magazi. Michael Luhanga amene ndi katswiri pa matenda a likodzo kuofesi ya zaumoyo ku Zomba adati likodzo limafala ngati munthu amene ali ndi likodzolo wakodzera mmadzi ndipo nkhono zimene zimanyamula tizilombo ta nthendayi tikhudzanso munthu wina amene alibe likodzo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndi bwino kupewa kukodzera mmadzi kapena kuchita chimbudzi patchire chifukwa madzi a mvula akakokolola zimenezi ndi kukathira mumtsinje ndiye kuti anthu onse amene akugwiritsa ntchito madziwo ali pachiopsezo chotenga likodzo, adatero Luhanga. Luhanga: Nthawi ya mvula ndi yofunika kusamala Malinga ndi Luhanga likodzo lilipo la mitundu iwiri: la mmatumbo komanso la mchikhodzodzo. Zizindikiro zooneka ndi maso kuti munthu ali ndi likodzi ndi kukodza timadontho ta magazi makamaka akamamaliza kukodza, adatero Luhanga. Kupatula kutha magazi mthupi, likodzo limachititsanso kuti ana azikula monyentchera, ana amakula opanda nzeru, kusabereka kwa amayi, khansa ya khomo la chiberekero, kutupa kwa kapamba ndi chiwindi komanso kudzadza kwa madzi mmimba. Ndi bwino kuti anthu akaona kuti akukodza magazi azithamangira kwa alangizi a zaumoyo kudera lawo kapena kuchipatala matendawo asanayale maziko mthupi mwawo, adatero Luhanga. Katswiriyu adati anthu amene ali pachiopsezo chachikulu chotenga likodzo ndi ana chifukwa amakonda kusewera mmadzi akuda a mvula komanso anthu amene amalima mpunga kumadambo ndi mbewu zina ndi amene ali pachiopsezo chotenga likodzo. Tikulangiza anthu kuti azigwiritsa ntchito zimbudzi akafuna kudzithandiza chifukwa kukodza kapena kuchita chimbudzi paliponse ndi koopsa masiku ano a mvula, adalangiza Luhanga. Iye walangizanso kuti likodzo ndi lochizika chifukwa wodwala amapatsidwa mankhwala a praziquantel amene amathaniratu ndi likodzo mthupi.
6
Aphungu aunguza njira zokhaulitsira auve Uve wanyanya mdziko muno koma pano zafika poti wina akalowa nazo kundende! Nyumba ya Malamulo yati nyansi zamgonagona zomwe zili mmakhonsolo osiyanasiyana zikubweretsa fungo loipa komanso zikuika moyo wa anthu pachiwopsezo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Pachifukwa ichi, aphungu a ku Nyumbayi agwirizana zoti akambirane zokhazikitsa malamulo omwe azipereka mphamvu zonjata munthu wopezeka akuchita utchisi. Nkhaniyi idalandiridwa ndi manja awiri ndi aphungu osiyanasiyana phungu wa pakati mboma la Lilongwe Lobin Lowe ataiyambitsa Lachinayi mNyumbayi. Lowe adati nzokhumudwitsa kuti fungo loipa lili ponseponse mmakhonsolo kaamba koti akuluakulu ake amalephera kuchotsa zinyalala komanso zoipa zochoka mmakampani ndi mmafakitale zikumathera mmitsinje. Iye adati izi zikuchitika kaamba koti palibe lamulo loletsa anthu kuchita uve monga momwe zimakhalira mmaiko ena. Vuto ndi loti tilibe malamulo ngati mmaiko a anzathu nchifukwa chake anthu amangotaya zinyalala chisawawa ngakhale kukodza kumene anthu amangokodza momwe afunira chifukwa palibe chilango chilichonse chomwe angalandire, adatero Lowe. Phungu wa ku Mpoto cha ku Madzulo kwa boma la Salima, Jessie Kabwila, adavomereza izi ponena kuti chomvetsa chisoni kwambiri nchakuti akuluakulu ena amaphunziro awo akuchita nawo uve woterewu. Iye adati uve wotere kuulekerera ukhoza kusokoneza ntchito zokopa alendo kaamba koti anthu obwera amafuna malo ndi zinthu zaukhondo kuopa woyandikana nawo nyumba. Lipoti loyamba likusonyeza kuti iye adayamba kugonana ndi ana akewo mchaka cha 2014 kutanthauza kuti wina ali ndi zaka 6 pomwe wina adali ndi zaka 4, Namwaza adatero. Chiyambireni zolaulazi, mkuluyo akuti wakhala akuopseza ana akewo kuti asadzayerekeze kutsina khutu aliyense za nkhaniyi. Koma poti amati tsoka chimanga chilinda moto, anawo adatopa ndi uvewo. Namwaza adati aka si koyamba kuti mkuluyo amveke ndi mbiri yomwa mazira akewo. Akuti mayi wa anawo, yemwe ndi mkazi wake, adawapezapo mwezi wa October chaka chino akuluwo ali ndi mwana wa zaka 7 akupanga naye zadama, koma banjalo lidakambirana za nkhaniyo ndipo idangofera mmazira. Akutitu atakambirana, bamboyo adapepesa komanso adaopseza mayiyo kuti akadzangoyerekeza kuulula adzamukhaulitsa ndiye chifukwa cha mantha, adakhaladi chete, adatero Namwaza. Iye adati koma pa November 22 ndi pomwe oyandikana nawo nyumba adalimbikitsa mayiyo kukanena nkhaniyi kupolisi. Namwaza adati anawo adapita nawo kuchipatala cha Kasungu komwe adakawayesa ndi kuti akalandire thandizo ngati nkoyenera ndipo apolisi akuyembekezera zotsatira. Tsiku lomwe mwanayo adakaulula za khalidwe la bamboo akewo ndi lomwe bwalo la milandu la magisitireti mumzinda wa Blantyre lidagamula Eric Aniva, fisi wa ku Nsanje, kuti akagwire ndende zaka ziwiri. Magulu osiyanasiyana, makamaka omenyera ufulu anthu, sadakondwe ndi chigamulochi ponena kuti ndi chochepa ndipo chosakwanira kuthetsa khalidwe lophwanya ufulu wa amayi ndi asungwana. Mmodzi mwa omwe adadzudzula chigamulochi ndi mkulu wa bungwe la Malawi Human Rights Resource Centre (MHRRC) Emma Kaliya yemwe adati chigamulochi nchosaopsa kwa abambo akhalidweli. Mkuluyu amachokera mmudzi mwa Chiswe, mfumu yaikulu Chikumbu mboma la Mulanje ndipo apolisi ati adzaonekera kukhothi kafukufuku akatha.
11
Milandu ya kashigeti yayamba kusongola Nkhani zakubedwa kwa ndalama mboma ya kachigeti tsopano yayamba koneka mutu wake. Padakali ano, anthu atatu apezeka olakwa pamlandu owaganizira kuti akukhudzidwa ndi kusolola kwa ndalama za boma. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Msabatayi, bwalo la milandu la majisitireti ku Lilongwe lidagamula Victor Sithole kuti akaseweze kundende zaka 9 atamupeza wolakwa pamlandu wopezeka ndi ndalama zakunja popanda chilolezo, kupezeka ndi katundu wobedwa komanso kuyeretsa kusungunula ndalama zobedwa kuti zisadziwike. Sithole adali wachiwiri kutumizidwa kujere kutsatira yemwe anali mlembi wa unduna wa zokopa alendo Tressa Namathanga Senzani yemwe bwalo lomnwelo lidamulamula kuti akaseweze zaka zitatu popezeka ndi K63 yomwe adasolola kuboma. Sithole adapezeka wolakwa pamlandu woti adali ndi K112 miliyoni yosadziwika bwino, US$31 850 (zoposa K16.6 miliyoni) komanso marand122 000 (K5.7 miliyoni) zomwe zabwezedwa ku boma. Ngakhale oimira mlandu Sithole adapempha bwalolo kuti lisamutumize kundende chifukwa kadali koyamba kuti apalamule, woweruza Patrick Chirwa adati akaseweze chaka chimodzi chifukwa chopezeka ndi ndalama zakunjazo popanda chilolezo, chaka chimodzi popezeka ndi ndalama zakuba komanso zaka 7 pofuna kuzimbaitsa kuti ndalama zakuba zisadziwike. Ndipo bwalolo, lapezanso Wyson Zinyemba Soko wolakwa pamlandu wakuti adalandira K40.9 miliyoni kuchokera ku unduna wa zokopa alendo ngakhale palibe ntchito imene adagwirira undunawu kupyolera mukampani yake ya zomangamanga ya Watipaso General Dealers. Soko, wachipani cha MCP, ndi mmodzi mwa anthu 9 amene adaimira zipani zosiyanasiyana pachisankho cha pa 20 May amene akukhudzidwa ndi nkhani yosolola chuma cha bomako. Poweruza mlanduwo, majisitileti Patrick Chirwa adakana kumva kudziteteza kwa Soko yemwe ankanena kuti munthu wina wotchedwa Godfrey Banda yemwe adagwiritsa ntchito kampani yake posolola ndalamazo. Ndikudabwa nazo mukunenazo chifukwa sizikumveka konse, adatero Chirwa. Malinga ndi ripoti la osanthula momwe chuma chagwiritsidwira ntchito a Baker Tilly amene adapemphedwa ndi nthambi ya chitukuko mdziko la Britain, lomwe lidapempha akadaulowo, K24 biliyoni idasololedwa kuboma pamene ena amalipidwa ndalama pomwe sanagwire ntchito zaboma, enanso amalandira ndalama asanagulitse kalikonse kuboma.
7
BAMBO ATHOTHA MWANA Bambo wina mmudzi mwa Nchada kwa T/A Nthondo ku Ntchisi amulamula kuti alipe mkazi wake ndi mwana wake wamkazi wa zaka 17, chipepeso cha K2 000 aliyense chifukwa chomuganizira kuti ankafuna kugonana ndi mwanayo mwezi wathawu. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Zamvekanso kuti msungwanayo sakuoneka komwe ali kaamba koti bamboyo wamumasula kuti si mwana wakenso kaamba koti adakana kugonana naye. Koma bamboyo wakana kuti izi ndi zoona ponena kuti abale a mkazi wake ndiwo akumupekera nkhaniyi pofuna kumuipitsira mbiri. Mayi a mtsikanayu (omwe sitiwatchula pofuna kuti anthu asamuzindikire msungwanayu) atsimikiza za nkhaniyi ndipo ati mwana wawoyo adasowa mwezi watha pa 21 May koma ati pochoka adauza mnzake yemwe amacheza naye kuti bambo ake amuuza kuti achoke pankhomopo chifukwa amakana kuchita nawo zachisembwere. Mayiyo wati mu March mwanayo adawadandaulirapo kuti bambo akewo amamupempha kuti azigonana nawo ndipo kuti adzamukwatira mtsogolo koma atafotokozera mchemwali wawo wamkulu adawawuza kuti nkhaniyo asaipupulumire. Iye wati mwezi wa April msungwanayo adakadandauliranso mayi ake aakuluwo kuti bambowo adamulondola kubafa komwe amasamba nkumuuza kuti agonane koma mwanayo adawaopseza kuti akuwa ngati satuluka kubafako. Ulendo wachiwiriwu udatiopsa ndipo tidakatula nkhaniyi kwa amfumu omwe adatiitanitsa kukakamba nkhani ndipo amuna anga adawalamula kuti apepese mwanayo komanso ineyo ndi K2 000 aliyense, adatero mayi a msungwanayo. Iye adati sakudziwa chomwe amafuna pamwanayo koma ambiri akuganiza kuti amafuna kupanga chizimba. Takhala mbanja kwa zaka 27 ndipo tili ndi ana anayi, atatu aamuna ndipo wamkazi ndi yekhayu. Panopa anali mu fomu 4 pasukulu ina kuno ndipo akaweruka amagulitsa mugolosale kumsika. Ngati sindiwasangalatsa akanangondiuza kuti akufuna akwatire mkazi wina. Mwanayo adakakhala chitsiru bwenzi akumagona naye ine osadziwa, adatero mayiyo. Mkulu wawo mayiyo adavomereza kuti mu April mwanayo adawapezadi kunyumba kwawo kuwadandaulira kuti bambo akewo adamutsatira kubafa akusamba ndi kumuuza kuti akalola kugona nawo athetsa banja ndi mayi ake kuti amukwatire. Ulendo woyamba atandiuza mayi ake ndimaona ngati zamasewera koma ulendo uwu ndidadziwa kuti nkhani yake inali yaikulu ndipo ndidawafotokozera mayi ake kuti tikadandaule kwa mfumu, adatero mayiyo. Mfumu Pitala Kangoma yomwe idaweruza nkhaniyi, yatsimikiza kuti izi zidachitikadi ndipo mpaka pano msungwanayo sakuoneka mmudzimo. Iye wati nkhaniyi panopa ili mmanja mwa apolisi omwe akuthandiza kufufuza komwe kuli mtsikanayo. Koma bamboyo adati ili ndi bodza lamkunkhuniza. Nkhani imeneyi ndinaimva koma sindikufuna kuyaluka nchifukwa chake ndinangokhala chete. Ndikudziwa zonsezi zikuchokera kwawo kwa akazi anga chifukwa sitigwirizana nawo, adatero mkuluyu pouza mtolankhani wa Msangulutso aamfunsa kuti amve mbali yake palamya. Adatinso abale a mkazi wakewo amusemeranso chinyau china ponena kuti adatukwana apongozi ake. Apolisi ku Ntchisiko akuti afufuze kaye za nkhaniyi asanaperekepo ndemanga iliyonse..
15
Kenya Ikudikira South Africa Kuti Ipulumutse Anthu Omira Mu Indian Ocean Wolemba: Sylvester Kasitomu Dziko la Kenya lati likudikira akatswiri osambira pamadzi a mdziko la South Africa omwe afike mdzikolo Lolemba kuzathandiza pa ntchito yosaka matupi a anthu awiri omwe afa atamira pa nyanja yaikulu ya Indian Ocean. Anthuwa ndi mayi komanso mwana wake wankazi ndipo anamira muyanjayi masiku apitawa galimoto yomwe anakwera itaphonya nseu ndi kulowa mu nyanjayi. Kanema oonetsa mmene ngoziyi yachitikira wakhala akuonetsedwa pa masamba a internet ndipo nthambi yoona za ngozi zogwa mwadzidzidzi mdziko la Kenya yati inalephera kupulumutsa komanso kupeza matupi a anthuwa kaamba kosowa zipangizo zokwanira zoti agwirire ntchitoyi. Nduna yofalitsa nkhani mdziko la Kenya Cyrus Oguna yati akatswiriwa alipo magulu awiri ena anafika mdzikolo lamulungu ndipo otsiriza akuyenera kufika mdzikolo lolemba kuti ayambe ntchito yosaka matupi a anthuwa. Tikuyesesa kuchitapo kanthu kuti anthuwa apezeke ndipo akatswiriwa afika mdziko muno lero kuti ayambe ntchito yawo, anatero a Oguna. Malipoti awilesi ya BBC ati nduna yoona za mayendedwe James Micharia yatsimikiza za nkhaniyi ndipo akatswiriwa ena afika kale mdzikolo ndipo ena akhala akufika posachedwapa mdzikolo.
14
Akayidi Atatu Adzodzedwa Ubusa Wolemba: Thokozani Chapola oads/2019/09/dausi.jpg" alt="" width="489" height="275" />Dausi: Ku ndende si malo olangira Akayidi atatu a ndende yaikulu ya Zomba lachitatu, adzodzedwa kukhala abusa. Pa mwambo-wu mbusa DR. KI SUNG KIM wa mdziko la KOREA wapereka ma CERTIFICATE kwa AKAIDI 98 omwe amachita maphunziro a za uzimu ndi kasinthidwe kamaganizo omwe amachititsa ndi a MAHANAIMA BIBLE COLLEGE ochokera mdziko la KOREA. Boma lati ndende za mdziko muno simalo olangira anthu opalamula milandu koma ndimalo osinthira munthu kuti akatuluka akhale mdzika yothandiza ya dziko lino. Polankhulapo nduna yowona zachitetezo cha mdziko a NICHOLAS DAUSI ati ndende za mdziko muno simalo olangira anthu opalamula milandu koma ndimalo osinthira munthu kuti akatuluka akhale mdzika yothandiza ya dziko lino. Anthu ambiri amati munthu akapita ku ndende amawona ngati ndi malo olangirako anthu ochimwa zomwe sizoona. Boma likufuna liphunzitse anthu kuti ku ndende ndi malo osainthirako makhalidwe ndi kaganizidwe ka anthu osati kuwazunza. Anthu akasinthika ndi kutuluka ku ndende atha kukakhala mzika zodalillika za dziko lino, anatero a Dausi. Poyankhulapo mmodzi mwa akaidi omwe alandira ma CERTIFICATE a uzimuwa (THEOLOGY) ku ndendeyi TONNEY CHIPHWANYA wapempha boma kuti lidzikhululukira akaidi omwe atsintha powopa kuti akakhalitsa mu ndendemo athanso kumaphunzira zoyipa kwa Akaidi osokonekera mu ndende-yi. munthu amatha kusintha koma akapitilira kukhala mu ndende muno chifukwa chakuti akukhala pafupi ndi anthu omwe ndi osokonekera zimapezeka kuti nayenso amasokonekera makhalidwe, anatero Chiphwanya. Pamwambo mkulu wa ndende mdziko muno mayi WANDIKA PHIRI wati maphunzirowa achepetsa milandu ya Upandu chifukwa akaidiwa akatuluka akakhala anthu otsinthika mu Uzimu komanso mukaganizidwe.
13
Red Cross imangira nyumba mabanja 600 Mabanja 600 mwa mabanja omwe adakhudzidwa ndi kusefukira kwa madzi achita mphumi bungwe la Red Cross litalonjeza kuti lithandizapo ndi zipangizo zomangira nyumba kwa mabanja ena. Woyanganira ntchito zothandiza anthu okhudzidwa ndi ngozi zodza mwadzidzidzi kubungweli ku Malawi, Joseph Moyo, ndiye adanena izi ndipo wati thandizolo liyamba kuperekedwa kunja kukayera. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Madzi osefukira adagumula nyumba zambiri Nyengo yothandiza ndi zinthu monga zakudya, zovala ndi mankhwala ikupita kumapeto tsopano ndiye tili mkati mokonzekera gawo lina lomwe ndi kuthandiza mabanja ena okwana 600 ndi zipangizo zomangira nyumba zamakono, adatero Moyo. Iye adati bungweli likufuna kuthandiza anthu makamaka a mmaboma momwe mudagwa vuto la kusefukira kwa madzi kumanga nyumba zomwe zingapirire ku chigumula cha madzi kuti mtsogolo muno vutoli likachitika lisamakhudze anthu ochuluka. Mwa zina Moyo adati bungweli lidzapereka mwaulele malata, misomali, simenti ndi kuthandiza popanga mapulani a nyumba zomwe akatswiri a zomangamanga adzatsimikize ngati zingapiriredi chigumula. Tikuyangana madera monga Nsanje, Chikwawa ndi Phalombe komwe vutoli limagwa chaka ndi chaka. Cholinga chathu nchakuti mtsogolo muno tisadzaonenso zomwe zawoneka chaka chino kuti anthu komanso maanja ochuluka chonchi nkumasowa pokhala ayi, adatero Moyo. Iye adati polingalira vuto lomwe limakhalapo mmidzi, thandizo ngati limeneli likamabwera, bungweli silidzatengapo mbali posankha mabanjawo koma mafumu ndi eni mudzi adzasankhana okhaokha ndipo iwo adzangobweretsa thandizolo. Moyo adati bungweli lidzapitirizabe kuthandiza anthu okhudzidwawo mnjira zina monga mankhwala ndi chakudya makamaka kwa anthu omwe minda ndi mbeu zawo zidakokolokeratu ndi madzi ndipo ali pachiopsezo chakuti akhudzidwa ndi njala. Katundu wambiri, kuphatikizapo ziweto ndi nyumba zidakokoloka ndi madzi osefukira ndipo anthu okhudzidwa akusungidwa mmisasa momwe mavuto ena ndi ena monga matenda adayamba kale kuvuta ndipo ambiri akuti adzasowa pogwira akamadzawachotsa kumisasako. Wachiwiri kwa woyendetsa ntchito zothana ndi mavuto ogwa mwadzidzidzi mu nthambi yolimbana ndi mavuto amtunduwu, Gift Mafuleka, adati anthu oposa 900 000 ndiwo adakhudzidwa ndi madzi osefukira kuyambira mwezi wa January. Iye adapempha anthu akufuna kwabwino kuti asatope kupereka thandizo lopita kwa anthuwa omwe ena ndi ana asukulu omwe pano adayamba aima kuphunzira.
15
Wonyozedwa ali moyo Alemekezedwa atamwalira Gogo wina ku Ntcheu, yemwe amagona pachisakasa chonga pogulitsira tomato abale ake akukana kuti agone mnyumba yabwino, adalemekezedwa atamwalira ndipo siwa idali nyumba ya makono ya mmodzi mwa abale amamukana ali moyowo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Batameyu James, wa zaka 67 wakhala akugona panjapo, samapatsidwa chakudya, amangodzionongera, ndipo mvula idakhala ikumuthera pathupi abale ake atatemetsa nkhwangwa pamwala kuti sangayerekeze kumuthandiza. James mchisakasa chomwe ankagona Gogoyu asadamwalire, adauza Msangulutso pa 25 December 2015 kuti ankagwira ntchito yaulonda ku Lirangwe mboma la Blantyre koma pamene adabwerera kumudzi kwawo anthu sadamulandire. Ndinkagwira ntchito yolondera. Ndidapita kale ndipo sindingakumbuke kuti ndi liti. Mkazi wanga adamwalira komweko, ndipo ndidaganiza zobwerera kumudzi kuno komanso nthawi yomwe ndimabwera nkuti ndikudwala, adatero gogoyu nthawiyo. Koma ganizo lobwerera kumudzi kwawo kwa Howa, T/A Phambala silidakomere mchemwali wa gogoyu, Felisita James. Gogoyo adafikira pamtengo, amagona pomwepo ndipo sabata isadathe akuti matenda adakula ndipo samayenda. Chimbudzi ndikupangira pomwepa chifukwa sindingakwanitse kupita kuthengo. Miyendo yafa komanso ndikuzizidwa kwambiri chifukwa zofundazinso zikumanyowa kukabwera mvula, adatero akali moyo. Titamufunsa Felesita chomwe sadamulandirire mbale wake, iye adati sakufuna kulankhula zambiri. Koma titamupempha kuti amulole gogoyu azigona mnyumba mwake, iye adati: Ngati alowe mnyumbamu ndiye ine ndituluka. Kodi pali chifukwa chiyani chomwe akulangira mbale wawo? Muwafunse kuti adachoka liti pakhomo pano. Ndiye andifune lero? nanensotu ndine wokalamba chifukwa iwowo ndi ine wamkulu ndi ine, adatero iye. Matenda atakula, gogoyu akuti adakomoka ndiye patsikuli adatengedwa ndi ena oyandikana nyumba kuti agone mnyumba mwawo. Chisakasa cha Jemusi ndipo kumbuyoko ndi nyumba ya siwa28 Apa ndi pamene mudziwo udagwirizana kuti umumangire nyumba gogoyu koma malinga ndi nyakwawa Howa, izi sizidatheke. Timafuna tipeze kaye udzu koma mpaka amwalira anthu tisadakumanebe kuti timumangire nyumba gogoyu. Mbale wawo mmodzi wotchedwa Mkwaso ndiye adadzazika timitengoti, idatero mfumuyo. Pa 13 February akuti kudayamba mvula yosalekeza mpaka pa 15 ndipo mvulayinso akuti idamuthera pathupi gogoyu. Gogoyo akuti adazizidwa kwambiri ndipo mmawa wa pa 15 adapeza kuti wamwalira. Koma abale adasonkhana ndi kuyamba mwambo wa maliro. Koma chodabwitsa, thupilo akuti adalirowetsa mnyumba ya Felesita kuti anthu ayambe bwino kukhuza. Nsima yomwe wakhala akuisowa akuti idaphikidwa ndipo achibale adalira mosaleka. Gulupu Mpochela idati anthu ena adakwiya kuona kuti banjali lidaganiza zolemekeza maliro kusiyana ndi munthu wamoyo. Gogogyu wakhala akuvutika kwa nthawi yaitali. Adabwera kuno mu October mpaka wamwalira akugona panja opanda chakudya. Lero wamwalira ndiye amulowetsa mnyumba ya malata komanso paphikidwa chakudya, adatero iye. Mpochela wati izi zakumukhumudwitsa ndipo aitanitsa banjali likamalira kulira malirowo. Uku ndi kulakwa, kuzuza munthu wamoyo choncho komanso wokalamba ngati uyo sibwino. Ndawaitanitsa ku bwalo langa, adatsimikiza Mpochela. Gogoyu ali moyo adauza Msangulutso kuti ali ndi ana ku Lirangwe, koma pazolengeza za pamalirowo, abanja adati malemuwo sadasiye mwana ndipo mkazi wawo adamwalira. Malinga ndi wachibale wina amene adakana kumutchula ndipo akukhala mumzinda wa Blantyre, malemuwa sadabereke mwana ndipo ana awiri amene amakhala nawo adali owapeza ndipo sadziwanso komwe anawo ali. Nkhani zozuza anthu okalamba si zachilendo mdziko muno. Posakhalitsapa, anthu ena ku Neno adapha anthu anayi okalamba powaganizira ufiti.
15
CFM Ipempha Mabanja Akhale Ogwirizana Wolemba: Glory Kondowe Mabanja achikhristu mdziko muno awapempha kuti azikhala ogwilizana pofuna kumanga maziko abwino abanja. Bungwe la mabanja a chikhristu la Christian Family Movement ku Limbe parish mu arch-dayosizi ya Blantyre lanena izi pa mkumano wa bungweli ku Limbe Cathedral. Polankhula ndi mtolankhani wathu wapampando wa bungwe-li ku Parish ya Limbe, banja la mayi ndi bambo Chinganda linati mchitidwe ozembelana mbanja ndi umene ukusokoneza mmanja ambiri a chikhristu mdziko muno. Mwazina banja la Chingamba anati mwamuna ndi mkazi ayenera kukhala wokhulupilika kwawina ndidzake ndipo anatinso maanja tiyenera kumayika pansogolo mlungu pachina chilichonse. Powonjezerapo anatinso azimayi amene amachita makhalindwe oyipawa ayenera kusintha mchitidwewu ndipo ayenera kumapemphera kuopa kusokoneza ma banja awo.
13
Ambuye Ziyaye Apempha Achinyamata Amasuke Posankha Utumiki Wawo Arkiepiskopi wa arkidayosizi ya Lilongwe, Ambuye Tarcizio Ziyaye wapempha achinyamata mu mpingo wa katolika kuti akhale ndi ufulu wosankha utumiki wa kumtima kwawo. Ambuye Ziyaye anena izi ku Maula Cathedral pa mwambo wa malumbiro a ku nthawi zonse a Sister Mary Umukonde Madeya a chipani cha Poor Clares. Ziyaye: Pali kuyitanidwa kosiyanasiyana Iwo ati arkidayosizi yawo yakhazikitsa njira zosiyanasiyana zomwe zingathandizire kukopa achinyamata ambiri kuyamba moyo wa utumiki mu mpingo. Sindingayembekezere kuti onse abwere kuno. Pali kuyitanidwa kosiyanasiyana tsono kuno ku nyumba ya mapemphero tikufuna atsikana kuti abwere kuzathandiza kupitisa mpingo patsogolo, anatero Ambuye Ziyaye. Iwo ati akugwiritsa ntchito njira zosiyana-zoyinana zokopera achinyamata monga nsembe za misa pa wailesi kuti achinyamatawa azisirira kapempheredwe kawo.
13
Chatsalira wa Silver Strikers Kwa onse otsatira mpira wa miyendo, dzina la Ndaziona Chatsalira si lachilendo chifukwa mnyamatayu zitchito zake zimaonekera pakati pa timu mbwalo la masewero. Mnyamatayu padakalipano akusewera mu Silver Strikers ndipo ndi mmodzi mwa osewera omwe amakayimirira dziko lino pamasewero a pakati pa maiko a kumwera kwa Africa sabata yapitayo. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye kuti amve za mbiri yake ndipo machezawo adali motere: Chatsalira: Ankafuna wotseka pakati Kodi Ndaziona Chatsalira ndani? Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndaziona Chatsalira ndi mnyamata wosewera mpira yemwe adabadwa mbanja la ana 5, amuna okhaokha, ndipo ndi wachiwiri kubadwa. Kumudzi kwathu ndi ku Dowa kwa T/A Chiwere. Tafotokoza, mpira udayamba liti? Mpira ndidayamba ndili Sitandade 4 komwe ku Dowa ndipo pomwe ndimafika Sitandade 8 ndimasewera mmakalabu angonoangono a kwathu komweko mpakana ndimasewera mmipikisano yodziwika kumeneko. Nanga kuti upezeke ukusewera mu Super League zidayenda bwanji? Nditalemba mayeso a Sitandade 8 adandisankhira kusukulu ya sekondale ya Madisi komwe ndidakapitiriza mpira. Nditayamba Fomu 1 choyamba ndidapeza malo mutimu ya pasukulu. Ndili kalasi yomweyo kudabwera mkulu wina yemwe adachokera ku Lilongwe ndipo adandiona ndikusewera. Ndidacheza naye pangono ndipo adatenga nambala yanga kenako adadzandiimbira foni kuti timu ya Pakeeza ku Lilongwe imandifuna. Kenako zitatero? Ndidapita kukakumana ndi akuluakulu a timuyo ku Lilongwe ndipo tidamvana mpaka ndidayamba kusewera mutimu ya Pakeeza mchaka cha 2005 kenako ndidapita kutimu ya Escom United mchaka cha 2007. Mwayi umenewu udakupeza bwanji? Mchaka cha 2007, timu ya Escom United idabwera ku Lilongwe kudzasewera mpira ndi timu ya Silver Strikers ndiye poti adali atandiona kale ndikusewera mtimu ya Pakeeza adandiitana kuti ndikayese mwayi wanga kumeneko. Mchaka cha 2008 ndidakayesa mwayiwo nkukhoza. Umu ndimo ndidapezekera ku Escom United nkuyamba kusewera mwakathithi mu Super League. Pano dzina lako limamveka ku timu ya Silver Strikers, udankako bwanji? Nditasewera ku Escom United kwa kanthawi, timu ya Silver Strikers imafuna osewera angapo oti azikatseka pakati, kumbuyo komanso kumwetsa zigoli ndipo mchaka cha 2011 ndidali mmodzi mwa osewera omwe timuyo idatenga ndipo malo anga adali pakati kuthandizira otseka kumbuyo ndi omwetsa zigoli omwe. Umaseweransotu mtimu ya Flames, tafotokoza udahonga ndani? Amwene, munthu ukakhala wakutha ndiwe wakutha chifukwa kudalira kuhonga munthu suchedwa kutha.
16
Apempha Anthu Asamalire Zitukuko Zotsala Bambo mthandizi wa parish ya Domasi mu dayosizi ya Zomba bambo Peter Mlomole apempha akhristu aku Zomba Cathedral komanso madera ena a boma la Zomba kuti asamalire bwino zitukuko zomwe malemu Peter Zakiresiki akhala akulimbikitsa mdelaro. Anatsogolera misayo-Bambo Mlomole (pakati) Bambo Mlomole amayankhula idzi lachisanu mmudzi mwa a Group Village Headman Ntogolo mdera la Senior Chief Malemia pa mwambo wa Nsembe ya Ukalistia umene unakonzedwa bungwe la Partners In Action For Sustainable Development (PASD) ngati njira imodzi yokumbukira mzimu ndi moyo wa Peter Zakiresiki yemwe adamwalira pa 5 February mdziko la kwao ku Canada ndipo ayikidwa mmanda lachisanu pa 14 February kwawo komweko ku Canada. Iwo ati Mpingo wa katolika ku Zomba Cathedral udzakumbukiranso mkulu-yi kamba ka zitukuko zomwe analimbikitsa pomangira mpingowu matchalichi awiri, nyumba zopangitsa rent, komanso kugula mipando ku school ya Primary ya Namikhate, komanso kugulira ma uniform a choir ndi zina zambiri. Bambo Mlomole atinso kupatula kuthandidza mpingo wa katolika a Zakiresiki amathandidzanso bungwe la Partners In Action For Sustainable Development (PASD) mmadera a mafumu a akulu Malemia ndi Mlumbe mboma la Zomba. Poyankhulanso pakutha pamwambo wansembe ya ukalistia-yo mkulu wa bungwe la Partners in Action for Sustainable Development a Amos Chiyenda anati nawo adzawakumbikira malemuwa kamba ka chikondi chomwe chali nacho kwa munthu wina aliyense.
14
Msoliza, Kayuni share spoils Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ernest Msoliza and Osgood Kayuni fought to a draw in an eight-round welterweight bout at Obrigado Leisure Centre in Mzuzu on Saturday. The Mzuzu-based boxer Msoliza failed to make use of home advantage against Kayuni who had an upper hand in the first three rounds. Osgood Kayuni Backed by home support, Msoliza upped the tempo in the fourth round with a flurry of punches, but his seasoned opponent held. Following Saturdays bout, Kayuni now has a record of 30 fights with 22 wins, lost five and three draws. On the other hand, Msoliza has 11 fights with seven wins, two losses and two draws. Speaking after the bout, Msoliza claimed he was robbed of victory The bout was good, but I am not happy with the results, I dominated most of the rounds, but I am surprised that the judges have settled for a draw. I have been robbed of victory, said Msosliza. Msoliza Surprisingly, Kayuni also claimed to have been robbed. I have been hearing that judges here favour Mzuzu-based boxers and I have proved it today. I just cant understand how they settled for a draw, this is not good for the sport, lamented Kayuni. In supporting bouts, Laston Kayira beat Alexander Likande while Lomelu Mwakhwawa beat Wilfred Nyambose. Ruth Chisale defeated Violet Nyambose. Joe Nyirongo who promoted the fights, said he was impressed with the performance and pledged to continue organising bouts in the city. The fights went on well. I am happy with the results. I feel judges have the mandate to rule who has carried the day. I promise to continue supporting boxing. I am here to stay. I want to make sure that I assist the government in putting Malawian boxers on the global map, said Nyirongo. Mzuzu district sports officer Olga Mshali said her office will make sure that boxing is supported just like any other sporting activity in the city. She then appealed to the corporate world to emulate what Nyirongo is doing in supporting boxing.
15
Apempha Makwaya Athandize Radio Maria Mmodzi mwa atsogoleri a kwaya ya St. Benadetta Masanjala ya mu arkidayosizi ya Blantyre a Felix Khonje ati makwaya a mpingo wa katolika ali ndi udindo waukulu wothandiza Radio Maria Malawi. Imodzi mwa kwaya zomwe zinatenga nawo gawo pa festival ya Radio Maria A Khonje anena izi pofotokozera Radio Maria pa zazikulu zomwe wailesiyi yachitira makwaya a mpingowu mdziko muno zomwe makwayawa ayenera kuyithokoza. Iwo ati ngakhale anthu ena samaonetsabe kufunika kothandiza Radio Maria Malawi kamba ka zifukwa zawo koma akuyenera kudziwa kuti wailesiyi ndi chida cha mphamvu chothandizira kufalitsa uthenga wabwino kudzera mu mpingo wakatolika mdziko muno. Radio Maria ikuthandiza kwambiri makwaya mdziko muno nde njira yokhayo yobwezera ulemu ndi kupereka thandizo lathu ku wailesiyi, anatero a Khonje. Kwaya ya St. Benadeta Masanjala ndi yomwenso inakhala katswiri pa chiphwando cha mayimbidwe chomwe wailesiyi inachititsa mchaka cha 2019.
13
Msonkhano wa YCW Uli Mkati ku Karonga Msonkhano waukulu wa pa chaka wa bungwe la achinyama a mpingo wachikatolika la Young Christian Workers kuno kumalawi uli mkati mu dayosizi ya Karonga. Polankhula ndi Radio Maria Malawi lero pulezidenti wa bungweri Light Balton wati msoknanowu ukuchitikira ku sukulu ya atsikana ya St. Mary ndipo usokhanitsa ma membala onse a bungeri ochokera mmadiosizi onse asanu ndi atatu a mpingo wakatolika a mdziko lino. Msonkhano umenewu chaka chinochi nkhani yayikulu yomwe tikukapanga, ndikupereka malipoti a momwe YCW yagwirira ntchito chaka chimenechi, kuonjezera apo kukachita ntchito ya chifundo ku sukulu ya ana osamva ndi osayankhula. Komanso loweruka kudzakha kulumbira kwa membala amene alowa kumene bungeri anatero a Balton. Mwazina iye wati mawa kukhala mwambo wa misa yotsegulira msonkhanowu ndipo omwe adzatsogolere ndi ambuye Peter Musikuwa a Chikwawa Diosizi ndipo mwambo wa misa omwe udzachike loweruka pamene mamembala atsopano adzalumbire adzatsogolere ndi ambuye Musikuwa komso ambuye MStumbuka. Ndipo msokhanowu awuchita motsogoleredwa ndi mutu wakuti Kubatizidwa Ndi Kutumidwa ndi cholinga chofuna kuyendera limodzi ndi mpingo mu dongosolo lake.
13
Chilala chavuta maboma ambiri Nduna ya zamalimidwe ndi chitukuko cha madzi, Dr Allan Chiyembekeza, wati pakhala msonkhano wounikira momwe ngamba yakhudzira anthu makamaka mchigawo cha kummwera. Chiyembekeza adanena izi msabatayi atayendera madera omwe ngamba yavuta mmaboma ena a dziko lino. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ulendo wa Chiyembekeza udali wachisoni chifukwa maboma ena alimi sadabzale, ena chimanga chafota pamene madera ena sichidamere. Gojo: Chimanga chikamasula popanda mvula sichingabereke Malinga ndi malipoti a mmaboma amene aperekedwa ku unduna wa zamalimidwe, mmaboma a Phalombe, Chiradzulu, Nsanje, Chikwawa, Neno ndi Mwanza ndi komwe kwavuta kwambiri chifukwa cha kusowa kwa mvula. Mwachitsanzo, boma la Phalombe lalandira mvula masiku 8 okha. Malinga ndi lipotilo, pofika Lolemba pa 25 January nkuti mvula yozama ndi mamilimita 130.6 okha itagwa. Nthawi ngati yomweyo chaka chatha nkuti bomalo litalandira mvula kwa masiku 27 ndipo idali itazama ndi mamilimita 663. Mkulu wa zamalimidwe mbomalo, Osmund Chapotoka, wati chifukwa cha kuchepa kwa mvula, alimi amene adabzala koyambirira, chimanga chawo chafota pamene amene adabzala kumapeto, chimanga chawo sichidamere. Ngakhale mvula itagwa lero chimanga chimenechi sichingapulumuke. Apa ndiye kuti alimi ayambiranso kubzala, adatero Chapotoka. Tili ndi madera amene kumavuta mvula chaka chilichonse monga ku Kasongo, koma pano ndi madera omwe kumagwa bwino mvulawo kuli gwaaa! Alimi onse akulira. Nako ku Thyolo, ndiye angolandira mvula kwa masiku 14 yochuluka ndi mamilimita 199.9 basi. Nthawi ngati yomweyi chaka chatha nkuti bomali litalandira kale mvula kwa masiku 22 yomwe idali yozama ndi mamilimita 558.2. Kumenekonso, malinga ndi mkulu wa zamalimidwe, Raphael Mkisi, zinthu zasokonekera. Chiyembekeza: Tikumana Mvula idasiya chimanga chitangoyamba kupota. Yadula kwa sabata ziwiri ndiye ngakhale yayambiranso pano, sichingabereke ndipo alimi akuyenera abzalenso, adatero Mkisi. Ku Mulanje mvula yangogwa masiku 15 yozama mamilimita 284.8. Nthawi yonga yomweyi chaka chatha nkuti atalandira mvula kwa masiku 32 yozama ndi mamilimita 934.9. Ku Neno ndiye angolandira mvula ya mamilimita 150.5 yomwe yagwa kwa masiku 8. Nthawi ngati yomweyi chaka chatha, bomali lidali litalandira mvula ya mamilimita 806.5 kwa masiku 24. Chiyembekeza akuti maboma a Balaka, Nsanje, Chikwawa, Ntcheu, Machinga, Chiradzulu ndi ena ali mmavuto onga omwewa ndipo zikuchititsa mantha. Ili si vuto la munthu, Namalenga ndiye akudziwa zonse ndipo sitikudziwa kuti watikonzera zotani chifukwa palibe boma lomwe lili ndi nkhani yabwino, adatero Chiyembekeza. Kuchigawo cha kumpoto lipoti lofotokoza momwe zinthu zilili silidaperekedwe kuboma koma ndunayi yati posakhalitsapa lipotilo lituluka pamene iyo ipitenso kukayendera mmaboma ena. Tilibe komwe tikulandira mvula mokhazikika, chaka chino tikuyenera kusamala kwambiri chifukwa tilibe chiyembekezo kuti tipeza chakudya chokwanira malinga ndi momwe mvulayi ikugwera, adatero Chiyembekeza. Komabe ndunayi yati kupatula kuti boma likhala pansi kukambirana za chomwe achite, alimi akuyenera ayambe kubzala mbewu zina zosalira mvula yambiri. Ngati mvula itabwera, tisalimbanenso ndi kuthira feteleza chimanga chomwe sitikololapo. Ndi bwino timusunge fetelezayo kuti tikagwiritsire ntchito paulimi wamthirira. Alimi akonzeke kubzala mbewu zina monga chinangwa, mapira, mchewere, mbatata ndi mbewu zina zosafuna madzi ambiri ngati mvula yagwa kudera kwawo, adatero Chiyembekeza. Iye adati si dziko lokha la Malawi lomwe lakumana ndi chilalachi komanso maiko monga a South Africa, Lesotho kudzanso Zambia nawo ali pamoto monga zilili kuno. Chiyembekeza adati boma liyesa kupeza njira zoti lithandizire anthu. Si vuto la mvula lokha, maboma a Phalombe ndi Mulanje ntchemberezandonda nazo zikuteketa mmera womwe wangomera. Undunawu ukuyembekezera kutulutsa lipoti lomwe lifotokoze momwe zinthu zilili mdziko muno ukamaliza kuyendera maboma onse. Pamenepo ndipo padziwikenso momwe chaka chino anthu akololere ngakhale Chiyembekeza wataya chiyembekezo chokolola dzambiri. Anthu oposa 3 miliyoni mdziko muno ndiwo akutuwa ndi njala ndipo boma layamba kale kugawa chakudya mmaboma ena. Koma monga akulirira Nyakwawa Gojo ya mboma la Mulanje, chaka chino kulira kulipo chifukwa anthu alibe chakudya pamenenso chiyembekezo chokolola chachoka. Onani mmunda mwanga muno, chimanga chonse chamasula pamene mvula kulibe. Ngakhale itabwera lero palibe chomwe chingachitike. Mulungu amve kulira kwathu, adalira Gojo.
2
Kuwonongeka kwa Nkhalango ya Amazon Kutha Kubweretsa Chiwopsezo pa Dziko Lonse Wolemba: Glory Kondowe Malinga ndi Kafukufuku yemwe akatswiri ena azasayansi achita wasonyeza kuti kusakazika kwa za chilengedwe mu nkhalango ya Amazon yomwe ikupezeka mdziko la Brazil kutha kudzetsa mavuto aakulu pa miyoyo ya anthu pa dziko lonse lapansi. Kafukufuku-yi wachitika potsatira kukwera kwa nambala ya ngozi zosiyana siyana monga ngozi za moto zome zakhala zikusakaza mitengo ndi zina zachilengedwe mu mkhalangozi kwathawi yayitali. Malingana ndi malipoti a BBC zikusonyeza kuti ngozi za moto mu mkhalango-yi zakwera ndi 83 Percent mchakachi, zomwe zikupereka chiopsezo chakuti ngati zinenezi zipitilire ndiye kuti mitengo yambiri yomwe imathandiza kuchepetsa kutentha kwa mpweya woyipa , ndinso kuthandizira pakangidwe ka mvula ndi zina zambiri zitha kusokonekera chifukwa chatchitidwewu. Mwazina president wa dzikolo a Jair Bolosonaro wati pakadari pano ndi wokhudzidwa kwambiri ndi ngozi za moto zomwe zikupitilira kuchitika mu mkhalango-yi kotero wati boma lake liyesetsa kuti lidzipereke pa ntchito zotetedza mkhalango-yi. Mkhalango ya Amazon ndi imodzi mwa mkhalango zikulu-zikulu zomwe zimathandiza kuteteza dziko lonse ku mpweya wotenthandipo kusakazika kwa mkhalango-yi akuti kutha kudzetsa mavuto a akulu a pa miyoyo ya anthu pa dziko lonse.
18
Njala yafikapo, ena akugonera mango Pali chiopsezo kuti anthu ena angafe ndi njala yomwe yagwa mmadera awo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Anthuwa ati ngakhale boma likugawa chimanga mmaboma omwe akhudzidwa, chimangachi ati ndichochepa kuyerekeza anthu omwe akhudzidwa pomwe ena akuti sadalandirebe chimangachi ngakhale madera awo njala yafika posauzana. Maderawa ndi monga Neno, Dedza, Mwanza, Chiradzulu, komwe anthu akugonera mipama ndi mango. Mayi Esther Chibwana wa mmudzi mwa Mithiko kwa T/A Mpama mboma la Chiradzulu ali ndi ana anayi ndipo amuna ake sagwira ntchito. Mayiyu wati adakolola matumba atatu achimanga koma chimangacho chidatha mu Julaye. Apa moyo udayamba kulimba pomwe adayamba kukhalira maganyu ndipo akadya bwino ndiye kuti agonera gaga yemwe walimitsa. Timalowa mtaunimu [Chiradzulu boma] komwe timapeza maganyu olima mmunda ndipo timalimitsa gaga koma pano gagayonso akusowa ndiye tikumalimitsa mango omwe tikumakagonera. Ngati sitipeza chakudya ndiye timagonera mango apo ayi kukangogona koma ndi ana kumakhala kovuta, watero mayiyo, yemwe ndi wa zaka 30 ndipo akuti chimanga ngakhale ufa sizidagawidwe kumeneko. Iye wati kumudziko mavuto akusowa kwa chakudya afikapo ndipo chiyembekezo chotaya miyoyo chakula. Nyakwawa Benito ya kwa T/A Mlauli mboma la Neno yati anthu 290 ndiwo akufunika thandizo lachimanga koma mudzi wake udalandira matumba 100. Tangogawana ndipo ena amapita ndi makilogalamu atatu nanga tikadatani? watero Benito. Naye Gulupu Mlauli wati mwa anthu 360 omwe akufuna thandizo, mudziwo walandira matumba 110 zomwe zayika ena pamavuto. Anthu onse adzagwada kwa ine kufuna thandizo chifukwa njala yagwira aliyense kuno chifukwa sitidakolole kaamba ka vuto la mvula, watero Mlauli. T/A Kachindamoto ya mboma la Dedza yati anthu 70 000 ndiwo akufunika thandizo koma kumeneko adalandira matumba 500 achimanga. Pena ukuchita kukanika kutuluka mnyumba kuopa anthu chifukwa akuwona ngati vuto ndi ine. Tithokoze boma chifukwa talidandaulira za vutoli ndipo chiyembekezo chilipo kuti litithandizanso, watero Kachindamoto. T/A Nthache ya mboma la Mwanza yati kumeneko chimanga sichidafike ndipo sakudziwa kuti chifika liti. Iye wati anthu kumeneko akugonera mango pomwe ena mipama kaamba ka njalayi. Mfumuyi yati pa 17 Novembala chaka chino mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda adakapereka ufa koma amagawa matumba 10 mmudzi uliwonse. Pano zinthu zikupitirira kuvuta, miyoyo ya anthu ili pamoto. Kuno ku Mwanza njala ikukhudza aliyense chifukwa palibe yemwe adakolola. Chonde boma litikumbuke ndi chimanga chomwe anzathu akulandira, adatero Nthache yemwe adati thandizo likachedwa anthu atha kutaya miyoyo. Koma mneneri wa boma, Moses Kunkuyu wati sakudziwa kuti mmadera ena mudafika chimanga chosakwana kotero ayambe wafufuza kaye. Sindikudziwa kuti zili choncho komabe ndifufuza. Ku Dedza mukunenako ndikadzimvera ndeka chifukwa lero [pa 21 Novembala] ndikupita komweko. Komabe ndithokoze kuti anthu akubwera poyera ndikunena zomwe akukumana nazo ndipo izi zitithandiza, adatero Kunkuyu. Ngakhale malipoti amawonetsa kuti chaka chino tili ndi chakudya choposera pa mlingo wake komabe njala yatenga malo. Pulezidenti wa dziko lino adavomereza kuti ngakhale malipoti amasonyeza kuti anthu oposa 1.7 miliyoni ndiwo akhudzidwe ndi njala koma chiwerengerochi chitha kuposa pa 2 miliyoni.
6
Chikho cha Carlsberg chafika pachimake Osewera ndi okonda Kamuzu Barracks Kusangalala mmbuyomu Thambo lagwa, chikho cha Carlsberg chaka chino chabwera ndi zake pamene anyamata ovala jombo atenga malo kugwedula matimu omwe amakula mtima. Chikhochi tsopano chafika mndime ya semifayinolo pamene dzulo Evirom imakumana ndi Red Lions pa Kamuzu mumzinda wa Blantyre. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Lachitatu Big Bullets idatulutsidwa ndi Kamuzu Barracks ku Dedza 1-0 Bullets itapha Silver Strikers ku Kamuzu. Patsikuli ku Chitowe Mafco idapondedwa ndi asilikali anzawo Moyale 3-1 mpira umene udathera mmapenote. Lachinayi masewero adaliponso ku Silver Strikers kumene Blantyre United idaumbudza Mponela United 1-0. Pofika dzulo masana nkuti mndime ya semifayinolo mutalowa Blantyre United, Moyale ndi Kamuzu Barracks. Moyale imangodikira timu imene ipambane pakati pa Red Lions ndi Evirom, pamene Kamuzu Barracks imene idatulutsa amene amateteza chikhochi a Blue Eagles ikumana ndi Blantyre United. Koma malinga ndi mphunzitsi wa Kamuzu Barracks Billy Phambala, timu ya chisilikali ndiyo itenge chikhochi. Iya adalankhula izi atakomola Bullets. Tidali bwino kuposa Bullets, chokhumba chathu kuti titenge chikhochi, adatero Phambala. Pamene mphunzitsi wa Mafco Stereo Gondwe polankhula atatuluka, adati timu ya chisilikali ndiyo itenge chikhochi. Tatenga chikho cha apulezidenti, pano tatuluka koma tikukhulupirira kuti chikhochinso chipita kwa asilikali. Matimu akuluakulu monga Mighty Wanderers, Civo ndi Silver adatsanzika mmawa omwe.
16
Apolisi adalakwa pomanga aphungu Katswiri wina wa za malamulo ndi anthu ena othirapo ndemanga agwirizana ndi bungwe la Malawi Law Society (MLS) ponena kuti kumanga phungu wa Nyumba ya Malamulo pomwe mkhumano wa Nyumbayo uli mkati ndi kulakwira malamulo a dziko lino. Mphunzitsi wa zamalamulo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College, Edge Kanyongolo, wanenanso kuti kumanga anthu pogwiritsa ntchito mauthenga a pafoni nkuwaphwanyira ufulu wawo wokhala ndi chinsinsi. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kanyongolo adanena izi msambatayi apolisi atagwira aphungu awiri ena a Nyumba ya Malamulo a chipani cha MCP, Peter Chakhwantha ndi Jessie Kabwila, ndi mkulu wina wa chipanichi, Ulemu Msungama powaganizira kuti amakambirana zogwetsa boma la Peter Mutharika pamauthenga a palamya otchedwa WhatsApp. Izi zitangochitika, bungwe la maloya la Malawi Law Society (MLS) lidati apolisi adaphwanya lamulo pomanga aphunguwo masiku a zokambirana zawo asanathe. Gawo 21 la malamulo oyendetsera dziko lino limati aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi chinsinsi. Lamuloli limaletsa kusechedwa opanda chikalata cha boma, kulandidwa katundu ngakhalenso kuwerengeredwa kalata komanso nkhani zonse zokhudza mafoni, adatero Kanyongolo. Iye adati umboni wotengedwa popanda chilolezo wotere suloledwa kukhoti ndipo ngati wina angapereke umboni wotere, akhoza kusumiridwa. Koma zikhoza kuvuta ngati mmodzi mwa amene amakambirana nawo izi ndiye adakapereka mauthengawo kupolisi, adatero Kanyongolo. Mpungwepungwe udayamba Lamulungu pomwe apolisi adamanga Msungama pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyo pomwe Chakhwantha ndi Kabwila samadziwika komwe adali. Koma Lolemba pamene msonkhano wa aphunguwo udayamba, apolisi adatchinga zipata zotulukira ku Nyumbayo koma sadathe kugwira aphungu awiriwo. Kabwila adamugwira akuti azithawira kumaofesi a kazembe wa dziko la Germany pomwe Chakhwantha adakadzipereka yekha kupolisi Lachiwiri. Kanyongolo adati malamulo a dziko lino salola kumanga phungu pomwe mkhumano wa Nyumba ya Malamulo uli mkati. Ndime 60(1) ya malamulo imanena kuti phungu ali ndi chitetezo choti sangamangidwe panthawi yomwe akupita, kuchokera kapena pomwe ali ku Nyumba ya Malamulo, adatero Kanyongolo. Naye mphunzitsi wotchuka wa za malamulo ku Cape Town mdziko la South Africa, Danwood Chirwa, adapherapo mphongo ponena kuti aphungu akangoyamba kukumana amakhala otetezedwa pankhani yomangidwa ngakhale kuti sali mNyumbamo. Malamulo amati aphungu sayenera kumangidwa zokambirana zikatsegulidwa chifukwa amakhala otetezedwa. Zokambirana zingatenge nthawi yaitali bwanji chitetezochi chimakhalapo koma akhoza kudzamangidwa zokambirana zikatsekedwa, adatero Chirwa. Mpungwepungwe wa Lachiwiriwo udachititsa sipikala wa Nyumba ya Malamulo Richard Msowoya kuimitsa msonkhano wa aphungu atamasulira kumangidwa kwa aphunguwo ngati kuchepetsa mphamvu za Nyumbayi. Zokambirana ziyamba zaima mpaka boma lititsimikizire za chitetezo chathu ngati aphungu a Nyumba ya Malamulo, adatero Msowoya. Koma mkulu wa apolisi Lexton Kachama adati apolisi sadalakwe pomanga atatuwo ndipo adati akadafufuza nkhaniyi. Sitidachite kutumidwa ndi andale. Anthuwo sitidawazenge mlandu wofuna kuukira boma chifukwa tidangofuna kumva mbali yawo. Ntchito yathu ngati apolisi nkusungitsa bata ndipo izi timachita mwa ukadaulo wathu, adatero Kachama ngakhale sadafune kunena momwe adapezera mauthenga a foni za eni ake. Mpungwepungwewu udayamba sabata yatha kumkhumano wa komiti yoona za mmene zinthu zikuyendera mdziko ya Public Affairs Committee (PAC) mumzinda wa Blantyre komwe nthumwi za boma ndi zotsutsa boma zidasemphana Chichewa pankhani yoti Mutharika ayenera kutula pansi udindo wake ngati mtsogoleri wa dziko lino ati kaamba kolephera kupeza mayankho a mavuto a zachuma ndi kusowa kwa chimanga mmisika ya Admarc. Kusemphanako kudabuka nthumwi zotsutsa boma zitatemetsa nkhwangwa pamwala kuti Mutharika atule pansi udindo kaamba kolephera kuyendetsa bwino zinthu. Nkhani yomwe idavuta kwambiri ndi ya kayendetsedwe ka chuma ndi njala yomwe yasanduka mutu wa nkhani pafupifupi paliponse mdziko muno maka pakusowa kwa chimanga mmisika ya Admarc. Zipanizi zidapereka malire a masiku 30 kuti boma litumize chimanga mmisika ya Admarc kapena litule pansi udindo kuti ena omwe angakhale ndi njira zothetsera vutoli atenge phamvu zoyendetsa boma. Pamkhumanowu, aphungu akuyembekezeka kukambirana za momwe chuma chikuyendera, nkhani ya njala, nkhani yokhudza ufulu wolemba ndi kufalitsa nkhani ndi mitu ina yomwe idatsalira pazokambirana za ndondomeko ya chuma cha 2015/16. Nkhani yokhudza ufulu wa atolankhani yakhala ikuvuta ndipo ndi imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zidabwerera pamkhumano wa ndondomeko ya chuma womwe wapitawo ndipo bungwe la atolankhani ndi maiko ena kudzera mwa akazembe awo adadzudzula kuponderedzedwa kwa nkhaniyi.
7
Chilima adzapikitsana nawo chaka cha mawa Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Chilima, wati adzaima nawo pa zisankho za chaka cha mawa dongosolo lonse loyenera posankha mtsogoleri likadzatsatidwa. Chilima adalankhula izi pa pologalamu ya padera pa wailesi ya Zodiak Broadcasting Station (ZBS). Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Zidali chonchi Mutharika ndi Chilima asadasemphane Pa June 6 Chilima adalengeza kuti atuluka Democratic Progressive Party (DPP) kaamba ka za mtopola zomwe achinyamata achipanicho amachitira anthu amufuna kuti adzapikitsane ndi mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, pa msonkhano wosankha atsogoleri a chipanicho. Koma Chilima adakana kudzalimbana ndi eni ake a chipani cha DPP ndipo mmalo mwake adaganiza zotulukamo. Kusagwirizana kudabuka mchipanicho kuchokera pomwe mkazi wa mtsogoleri wakale wa dziko lino, Callista Mutharika, adapempha mlamu wake, Peter Mutharika, kuti apereke mpando wake kwa Chilima kaamba koti wakula, komanso sangadzapambane pa zisankhozo. Peter Mutharika adakana kutula pansi udindowo ndpo adati aliyense yemwe sakufuna kuti adzaimenso ndi Yudase Isikariote wosafunira DPP zabwino. Koma polankhula ndi wailesi ya ZBS, Chilima adatsimikizira Amalawi kuti ndi wokonzeka kudzapikitsana nawo pa zisankho za chaka cha mawa dongosolo loyenera posankhira atsogoleri likatsatidwa kaamba koti sakufuna kukakamiza anthu kuti adzawaimire. Iye adati anthu ambiri akhala akulimbikitsa kuti adzapikitsane nawo. Koma sadafotokoze kuti adzaima payekha, alowa chipani kapena ayambitsa chake. Tikukuma ndi mabungwe, komanso zipani ndipo dongosolo lonse likatha tilengeza zotsatira zake. Kuima pa wekha nkwabwino, koma uyenera kukuganizira bwino chifukwa utha kumalimbikira mtunda wopanga madzi, adatero mtsogoleri yemwe walongeza Amalawi kuti tsogolo la Chilima Movement lisongola pasanathe masiku 10. Mtsogoleriyu waonetsa ubwino wa mgwirizano pakati pa zipani ngati womwe udachitika mu 2004. Iye watsutsa zoti Mpingo wa Katolika ndiwo ukumulimbikitsa kuti adzaima. Mpingo wa Katolika umalimbikitsa kuti Akhristu ake kuti azitenga nawo mbali pa ndale, koma sulodzera anthu mtsogoleri woti adzamuvotere. Chilima wakhala akupezeka, komanso kulankhula misonkhano yisiyanasiyana ya mpingo wa Katolika komwe ansembe ena akhala akumulimbikitsa kuti asakane maitanidwe wodzaima nawo pa zisankho za chaka cha mawa. Mtsogoleriyu wakhala akudzudzula mchitidwe wa ziphuphu mboma zomwe zakhala zikudabwitsa anthu kaamba koti iyeyo ndi wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino. Chilima wapempha anthu kuti akalembetse mwaunyinji wawo kuti adzaponye nawo mavoti pa zisankhozo. Kulumpha dzenje nkuliwonera patali. Ndipemphe anthu kuti akalembetse chifukwa Mulungu adzawapatsa atsogoleri womwe akufuna, adatero mtsogoleriyu. Chilima walimbikitsanso achinyamata omwe akufuna kudzapikitsana nawo pa zisankhozo kuti asagwe mpwayi ndipo adapereka zitsanzo za andale odziwika bwino monga Aleke Banda, Gwanda Chakuamba ndi ena omwe adalowa ndale ali achinyamata.
11
Atsekera wogwiririra Gogo wa zaka 80 Bambo wa zaka 54 yemwe adagwirira gogo wa zaka 80 ku Dowa amulamula kuti akaseweze zaka ziwiri ndi theka atamupeza wolakwa pamlanduwu. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Khoti la Msongandewu, lomwe lili ku Mvera mbomalo lidapereka chilangocho kwa mkuluyo, Biwi Ephraim wa zaka 54, koma anthu ozingwa ndi zimene adachitazo ati chigamulocho nchofooka. Anthu a mmudzi mwa Nyemba kwa Mfumu Yaikulu Chiwere mbomalo adaima mitu ndi zomwe Ephraim adachita pogwiririra gogoyo potengera danga kuti gogoyo adaledzera. Chomwe chaimika mitu anthuwa nchakuti bamboyu ali pabanja ndipo ali ndi ana 7. Anthu a mmudzimo ati sakumvetsa chomwe chidamukopa bamboyu kunyazitsa gogoyo. Mmodzi mwa anthuwo, Joel Machira, adati: Izi zikachitika, timaganizira masilamusi kapena kukhwima chifukwa munthuyu ali ndi banja ndipo ngati mthupi munatentha akadatha kupeza mpumulo kunyumba kwake. Kaponda: Gogoyo adapita kokamwa Ndipo Rose Thodwa adati mkuluyo adayenera kulandira chilango chokhwimirapo. Uku nkuvula mtundu chifukwa gogo wa zaka 80 ndi mtsitsi wa anthu ambiri ndiye kumupanga chipongwe nzosamveka, adatero Thodwa. Mneneri wa polisi mbomalo, Richard Kaponda adati patsiku la chipongwelo, gogoyo adapita kukamwa mowa mmudzi mwa Chiponda mdera lomwelo ndipo pobwerera, bambo wachipongweyo amamuzemberera. Atafika mmudzi mwa Chifisi, adambwandira gogoyo nkumukokera patchire pomwe adamuchita chipongwecho ndipo achipatala cha mishoni cha Mvera adatsimikiza kuti adagwiriridwa, adatero Kaponda. Ephraim amamuzenga mlandu wogwiririra zomwe zimatsutsana ndi ndime 132 yamalamulo ndipo iye adakana mlanduwo koma woyimira boma Sergeant Benedicto Mathambo adabweretsa mboni zitatu mkhothimo. Iye adati chilango chokhwimitsitsa chimene akadalandira nkukhala kundende moyo wake onse. Wolakwayo adapempha ogamula mlanduwo majisitileti Amulani Phiri kuti amuganizire pogamulapo chifukwa ali ndi banja lofunika chisamaliro komanso ndi wamkulu. Popereka chigamulocho, Phiri adati zomwe adanena Mathambo nzomveka komanso potengera umboni omwe udaperekedwa mkhotimo, Ephraim akuyenera kukakhala kundende zaka ziwiri ndi theka akugwira ntchito yakalavulagaga.
7
Dzombe Zavuta Kwambiri Kumvuma Kwa Africa Bungwe la United Nations lapempha maiko kuti athandize pa ntchito yothana ndi dzombe zomwe zavuta kwambiri mmaiko a chigawo chakumvuma kwa Africa. Mneneri wa nthambi yoona za chakudya komanso ulimi ku bungweli wati thandizoli likufunika msanga chifukwa dzombezi zayika pachiwopsezo nkhani ya zokolora komanso kadyedwe kabwino. Maiko a Ethiopia, Kenya komanso Somalia ndi amene akhudzidwa kwambiri ndi vutoli. Malipoti a wailesi ya BBC ati maiko a Ethiopia komanso Somalia sanakhudzidwepo ndi vutoli kwa zaka makumi awiri ndi zisanu 25 pomwe dziko la Kenya linakhudzidwapo ndi vutoli zaka 70 zapitazo. Malinga ndi mneneri wa United Nations-yu, njira yokhayo yothana ndi dzombezi ndi yopopera pogwiritsa ntchito ndege. Malipoti akusonyeza kuti dzombezi zachokera mdziko la Yemen ndipo zadza kaamba ka mvula yamphamvu yomwe inagwa mdzikomo kumapeto a chaka chatha yomwe inachititsa kuti mbozizi ziswane.
18
Amuna Awiri Anjatidwa Kamba Kogwililira Msungwana Mmodzi Amuna awiri ali mchitolokosi cha apolisi mboma la Nkhotakota powaganizira kuti agwililira msungwana wa zaka 15. Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sergeant Paul Malimwe wati amunawa ndi David Francis wa zaka 26 komanso Uzeni Banda wa zaka 18, onse a mmudzi wa Muyanja, mfumu yaikulu Nkhanga mbomalo. Iye wati pa 27 June chaka chino, msungwanayu anatumidwa kukagula mchere pa kamtini ina mderalo ndipo pobwelera ndi pomwe anakumana ndi awiriwa omwe anamukokera pa tchire ndi kumugwililira mosinthana-sinthana. Msungwanayu akuti anayesetsa kukuwa koma palibe anamumva kaamba koti panali patali ndi nyumba za wanthu ndipo pambuyo pomugwililira amunawa anamusiya msungwanayu akumva ululu kwambiri. Atakafika kwawo iye anakafotokozera makolo ake za nkhaniyi omwe anakatula nkhaniyi ku polisi yaingono ya Mkaika ndipo zotsatira za ku chipatala cha Malowa zinatsimikiza kuti msungwanayu wagwiliridwa. Awiriwa anjatidwa ndi apolisi lachitatu ndipo akuyembekezeka kukawonekera ku bwalo la milandu ndi kukayankha mlandu wogwililira zomwe ndi zotsutsana ndi gawo 138 ya buku loweruzira milandu mdziko muno.
7
Mbusa wa CCAP Alimbikitsa Akhristu Kuthandiza Radio Maria Wolemba: Thokozani Chapola Mbusa Joseph Maganga wa mpingo wa CCAP mboma la Zomba, loweruka wapempha anthu kuti akonde kuthandiza Radio Maria Malawi. Mbusa Maganga (wavala jekete lofiira) ndi ena mwa amayi omwe anali nawo pa ulendowu Mbusa Maganga walankhula izi pa ulendo womwe amayi a mpingowu ku tchalitchi la Mpsyupsyu anali nawo pomwe anakayendera likulu la wailesiyi ku Mangochi. Iye wati ngakhale mpingo wawo uli ndi wailesi ina koma amawona kuti mkofunika kuthandiza Radio Maria ponena kuti ntchito ya utumiki ndi imodzi. Anthu apitirize kuthandiza Radio Maria posatengera kuti ndi a mpingo waniji. Tili nayo wailesi yathu ya Blantyre Synod koma ndimawona kuti mkofunika kumathandiza Radio Maria chifukwa ntchito yomwe tikugwira ya utumiki ndi imodzi, anatero mbusa Maganga. Iwo ati anawona kuti amayi ambiri amakonda kumvera Radio Maria choncho akufuna kudzala mtima wokonda kuthandiza wailesiyi mwa amayiwa. Chaka ndi chaka ndimabweretsa amayi a mpingo wathu wa CCAP chifukwa Mulungu ndi mmodzi, tonse tikutumikira iyeyo. Ndimafuna aziyamikira ntchito za Radio Maria kutinso akhale ndi chidwi choyithandiza, anatero abusawo. Iwo ati akufunitsitsa kuti utumiki wa Radio Maria upite patsogolo kuti uthenga wake umveke pa dziko lonse.
13
Achenjeza zobzala chinangwa cha matenda Katswiri oona za tizilombo toononga komanso toyambitsa matenda ku mbewu wa kunthambi ya kafukufuku ya Bvumbwe Research Station, Dr Donald Kachigamba, wati alimi apewe kubzala mbewu ya chinangwa chomwe chikuonetsa zizindikiro za matenda. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pamene mvula ikugwa ndipo Madera ena imagwa mocheperako, alimi ena padakalipano ali pa kalikiliki kubzala mbewuyi kuti adzapeze chakudya ngakhalenso kugulitsa. Kachigamba adati matenda a chinangwa omwe azunguza kwambiri mmaiko ambiri a mu Africa kuphatikizapo Malawi ndi a khate (cassava mosaic) komanso oola (cassava brown streak). Matenda a khate amapangitsa masamba a chinangwa kukwinyana pomwe matenda a kuola amapangitsa mtengo wa chinangwa kuoneka okandikakandika komanso chinangwa chenichenicho chimaola mkati mwake, adatero katswiriyu. Khate la chinangwa limachititsa masamba kukwinyika Iye adalangizanso kuti ngati mbewu zina zayamba kuonetsa zizindikirozi pamene zili mmunda, mlimi akuyenera kuzizula ndi kuzitaya zikadali zazingono kuti zisakhale gwero la matendawa ku mbewu zina. Katswiriyu adaonjeza kuti kachilombo kotchedwa gulugufe oyera ndi komwe kamafalitsa matendawa mmunda wa chinangwa. Gulugufeyu payekha sioopsa koma kuipa kwake ndi kwakuti amafalitsa matendawa mmunda wa chinangwa choncho chofunika ndi kungoonesetsa kuti mmunda mulibe matenda, adatero katswiriyu. Mkulu oona za mbewu za gulu la chinangwa ndi mbatata kunthambiyo, Miswell Chitete, adati matendawa ndi ofunika kuwapewa chifukwa kupanda kutero, mlimi akhonza kupeza zokolola zochepa kwambiri. Alimi akuyenera kupewa matenda a chinangwa chifukwa ena mwa matendawa, mwachitsanzo khate, limatha kupangitsa chinangwa kuti chisabereke nkomwe kotero mlimi akhonza kungotaya mphamvu zake pachabe, adatero mkuluyo. Mphatso Jalasi, yemwe amachita bizinesi yolima ndi kugulitsa mbewu ya chinangwa mboma la Zomba wati matendawa akupangitsa kuti mbewu ya chinangwa ikhale yoperewera. Iye adati kuperewera kwa mbewuyi ndi komwe kunamupangitsa kuti ayambe kulima ndi kugulitsa mbewu ya chinangwa. Iye adati akuvutika kuti achulukitse mbewu ya chinangwa yopirira ku matendawa chifukwa siichita bwino kuchigawo cha kummwera. Ngakhale pali mbewu yopirira ku matendawa, mbewuyi ndiyosankha madera komanso ndi yowawa kotero pakufunika mbewu yosawawa komanso yosasankha Madera, adatero Jalasi.
4
Mayor Apempha Red Cross Iphunzitse Anthu First Aid Wolemba: Sylvester Kasitomu /wp-content/uploads/2019/09/kapombosola.jpg" alt="" width="388" height="470" />Wavomereza za kufunika kwa first aid-Kapombosola Banda Meya wa mzinda wa Zomba, khansala Benson Bulla lachiwiri wapempha bungwe la Malawi Red Cross Society kuti liphunzitse anthu mmadera ambiri za First Aid kuti anthuwa adzithandidza anzawo akamvulala asanawatengere kuchipatala. Iye wayankhula izi kwa Jali mboma la Zomba pamwambo womwe bungwe la Malawi Red Society lidakonza wa First Aid Day. Khansala Bulla yemwe anali mlendo wolemekezeka pa mwambowo wapemphanso bungwe la Malawi Red Society kuti liphunzitse akaidi mndende za dziko lino pa zamomwe angathandizilane pomwe wina wavulala mu ndendezi. Monga tikudziwa kuti zipatala zathu ndi zamutalimutali komanso kusowa kwa makhwala mzipatalazi kwakula. Ndi khumbo lathu kuti pakhomo pali ponse pakhale muthu modzi yekha yemwe aphunzitsidwe mmene ngathandizire muthu akavulala asanapite ku chipatala, anatero a Bula. Poyankhulapo pamwambo-wu mkulu wa zaumoyo ku bungwe la Malawi Red Society mdziko muno a Dan Kapombosola Banda anavomeleza zakufunika kwa maphunziro okhudza kaperekedwe ka thandizo loyambilira kwa anthu omwe avulala. Kutengera ndikufunika kwa chithandizo choyambirira ndi koti timapewa kuluza moyo wa muthu kaamba kotalikira chipatala, zimatha kutheka kuti muthu wakomoka athu amalephera kumpatsa chithandizo kaamba kosowa upangiri wa mmene angamuthandizire, antero Kapombosola Banda. Bungwe la Malawi Red Cross limathandiza popereka maphunziro kwa anthu kuti adziwe njira zomwe angamuthandizire munthu amene wadwala mwadzidzidzi kapena wachita ngodzi kuti apewe infa zodza kaamba kaamba kosowa chisamaliro chokwanira.
6
Dayosizi ya Dedza Iyamikira Akhristu Ake Dayosizi ya mpingo wa katolika ya Dedza yayamikira akhristu ake kamba kothandiza pa mwambo wa Dinner And Dance omwe dayosiziyi inakonza ndipo unachitikira ku sukulu ya New Era mboma la Ntcheu. Ndi yemwe akuyendetsa dayosizi ya Dedza padakalipano-Monsignor Chithonje Malinga ndi mkulu wa kuofesi yofalitsa nkhani mu dayosiziyo bambo Joseph Billiat, cholinga cha mwambowo chinali chofuna kupeza 5 million kwacha yomangira malo ogona atsikana ku parishi ya Mtendere mu dayosiziyo. Padakalipano ndalama zomwe zapezeka patsikuli sizinadziwike koma akuganiza kuti ndalamyo yakwana monga anayerekezera. Patsikuli panachitikanso mayere omwe pamapeto pake a Horris Kasudze ogwira ntchito ku bungwe la Chilungamo ndi mtendere anapeza mphotho ya Plasma Screen ndipo anthu ena apezanso mphotho zosiyanasiyana.
13
Man Sentenced 18 Years IHL for Sleeping With Niece Mangochi Senior Resident Magistrate Court on Friday has convicted and sentenced a 41-year-old man to 18 years imprisonment with hard labour for an offence of sleeping with his niece. State prosecutor Elias Chitsulo told the court that Edwin was staying with his elder brother in one compound but in different houses at village Muonda in Capemaclear Traditional Authority Namkumba in Mangochi district. In October 2019, the convicts elder brother left his 15 year old daughter in his house with her step mother for fishing. This angered the wife who instead snatched the girls beddings as punishment for her fathers sins. In the night the girl sought refuge in her uncles house which was just a few metres away from her house. On first night the girl shared the same bed with her uncle who is single untill morning without being defiled. From the second to eighth night the convict defiled the girl several times each night. Upon arrival on ninth day her father stopped the girl from spending nights with her uncle. Thereafter the step mother noticed some changes in the body of the girl that prompted her to invite elder women for questioning. The girl was taken to monkey-bay community hospital for check up where it was revealed that the girl is pregnant. Appearing before court Edwin pleaded not guilty to charges levelled against him that prompted the state to parade five witnesses who testified beyond any reasonable doubt that made court to find him guilty. In mitigation Edwin asked court for leniency citing the girl tempted him by spending nights on his bed. In submission the state prayed for stiff penalty citing that as an uncle, convict had an obligation of protecting the girl but he choose otherwise and he indicated that what the convict did is contrary to section 138(1) of the penal code. Passing the sentence senior resident magistrate Joshua Nkhono concurred with the state hence he was slapped the convict with 18 years imprisonment with hard labour as a deterrent to other would be offenders. Edwin (41) comes from village Muonda in traditional authority Nankumba in Mangochi.
7
Escom isayerekeze kukweza magetsiBanda Makina amagetsi a Escom Kutsatira zomwe mkulu wa zachuma kukampani ya magetsi mdziko muno ya Escom Delano Ulanje adauza wailesi ya MBC kuti bungweli likweza magetsi posakhalitsa, mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu la Malawi Watch Billy Banda wati kampaniyi losayesere zokweza magetsi. Lachinayi Ulanje adakanira The Nation kuti sangabwerezenso mawu amene adalankhula pa MBC kotero tilankhule ndi mneneri wa bungweri. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma mneneri wa bungweli George Mituka adati sizoona kuti pali chikonzero chokweza magetsi. Ngakhale pali kukanirana kotero komabe Banda wati ndi chipongwe kuti bungweri likweze magetsi pamene anthu akuvutika ndi nkhani zachuma. Chuma sichidapole, ngati bungweli lingakweze magetsi ndiye kuti zonse zikwera mtengo. Boma likuyesetsa kuti zinthu ziziyenda bwino pamene iwo akufuna kukweza magetsi. Ndiye kuyenda bwino kwake kuti? Ngati atero ndiye kuti akusemphana ndi zomwe boma likuchita kuti anthu azisangalala ndi momwe zinthu zikuyendera. Ife ngati amabungwe tikuti ayi, adatero Banda. Banda adati sanganeneretu chomwe bungwe lake lichite ngati Escom ikweze magetsi koma wati adzawona chomwe angachite. Kuyambira May chaka chatha magetsi akwera katatu zomwe zachititsa kuti zinthu zikwere mitengo. Izi zikuchitika pamene magetsi akungozima mdziko muno. Sabata zingapo zapitazo, ena adadzudzula kampaniyo kuti ikuononga ndalama pogula galimoto za K1.4 biliyoni ndipo ena akhala akudandaula ndi kuzimazima kwa magetsi.
2
HRDC Yati Ipitilira ndi Ziwonetsero Zokhudza kwa Nsundwe Wachiwiri kwa mkulu wa apolisi mdziko muno a John Nyondo anenetsa kuti onse omwe angapezeke olakwa pa nkhani yokhudza kuchitira nkhanza amayi ndi atsikana kwa Nsundwe adzayimbidwa mlandu molingana ndi malamulo. Iwo amalankhula izi lero pa msonkhano wa atolankhani ku likulu la apolisi ku Area 30 mu mzinda wa Lilongwe. Iwo ati cholinga cha apolisi sikufuna kuzizilitsa nkhaniyi koma akuyesetsa kuti ndondomeko zonse zitsatidwe pasanafike poyimba milandu anthu omwe angapezeke olakwa. John Nyondo kuloza chala Timothy Mtambo pa zionetsero zammbuyomu Polankhulapo mkulu wa bungwe la NGO Gender Coordination Network a Babra Banda ari akhala akudikira mwachete zotsatira za lipoti lomwe apolisiwa atulutse. Pakadalipano, bungwe la HRDC lati lipitilirabe ndi ganizo lake lochititsa ziwonetsero za dziko lonse pa nkhaniyi, lachinayi lino. Nkhani yokhudza kugwililira si nkhani ya chibwana. Ife sitikuona chifukwa choti achitirenso kafukufuku wina pomwe a MHRC anapereka kale zotsatira choncho ife tipitilira kuchita ziwonetsero zathu lachinayi likudzali, anatero Luke Tembo yemwe ndi mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la Human Right Defenders Coalition (HRDC).
11
Kunjatidwa kwa Kasambara kunganyanyule mavuto Kusamvera mabwalo a milandu komwe boma laonetsa kwasonyeza kulephera kwa chipani cha Democratic Progressive (DPP) pa kulemekeza ufulu wachibadwe, zomwe ati zingakhale ndi zotsatira zoipa. Azipani zotsutsa boma, amabungwe oona za ufulu wachibadwidwe, mfumu ina kudzanso anthu mmadera osiyanasiyana aunikira izi pomwe apolisi adakakamira kusunga mmodzi mwa akatswiri woimira anthu pamilandu, chonsecho bwalo lamilandu litampatsa belo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ralph Kasambara-yemwe wakhala akudzudzula boma mzambiri komanso kuimira pamilandu odzudzula boma-adamangidwa Lolemba pa 13 Febuluwale poganiziridwa kuvulaza anthu omwe ati amafuna kumupha komanso kuphulitsa nyumba yake ndi bomba la petulo. Ngakhale womuimira pamilandu adatenga belo ya bwalo lamilandu kuti Kasambara atulutsidwe, apolisi sadamulole kutuluka, kufikira Lachiwiri pa 21 Febuluwale pomwe adatulutsidwa pa belo. Apa omwe aikirapo ndemanga ati izi zingapereke chithunzithunzi choti boma silikulabadira za ufulu wachibadwidwe ndipo likutseka pakamwa Amalawi otsutsana ndi ulamuliro wa DPP komanso mtsogoleri wa dziko lino, Bingu wa Mutharika. Ndemangazi zati mwa zina maiko ndi mabungwe akunja angapitirize kumana dziko lino thandizo chifukwa boma silikulemekeza ufulu wachibadwidwe. Dziwani Tuwanje wa mmudzi mwa Chiwalo kwa T/A Chiwalo ku Phalombe wati izi zikungosonyeza kuti ufulu wobadwa nawo uli pachiopsezo. Ife timadalira anthu omenyera ufulu ngati amenewa; ngati akumangidwa pazifukwa zonsamveka bwino ndiye kuti ifenso tili pachiopsezo, akutero Tuwanje. Samuel Luangwa wa mmudzi mwa Maulabo kwa T/A Maulabo mboma la Mzimba wati moyo wa anthu uli pachiwopsezo, maka ngati zizifika pokanzidwa belo chonsecho bwalo lamilandu litaloleza. Mfumu ina yaikulu ku Mwanza yomwe siidafune kutchulidwa dzina yati sikumvetsa chomwe Kasambara amakaniziridwa belo. Monga mfumu, ndikuti ndikulakwa kukaniza Kasambara kutuluka pa belo. Ufulu wathu uli pachiopsezo chachikulu. Apa boma likuchita kuonetseratu nkhanza zonse. Izi zikutipatsa uthenga woipa kumudzi kuno kuti ngati ena atalankhula zosakhala bwino ndiye kuti azingomutumizira anthu achipani ndikumukhapa, mwina kumuotchera nyumba kumene, ikutero mfumuyi. Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wachibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda wati mawanga aboma pankhani ya Kasambara akuonetsa kuti boma la DPP silikuimira mzika za Malawi chifukwa likapemphedwa kuti likonze likuganiza kuti akunenayo akufuna kulanda boma. Maiko akunja akhoza kudula thandizo dziko chifukwa chilichonse chikuchitika mokomera munthu mmodzi, akutero Banda. Mtsogoleri wachipani cha Petra, Kamuzu Chibambo, wati maso a dziko akuyenera kumakhala kwa anthu a kumudzi chifukwa amazunzika ngati awanenera zamavuto awo alibe mwayi odzudzula boma. Iye adanenetsa kuti anthu akumudzi asadandaule kwambiri pa nkhani ya Kasambara chifukwa azipani ayesetsa kuti chilungamo chioneke. Kasambara-yemwe kale adali mlangizi woyambirira wa boma pazamalamulo mboma la Bingu wa Mutharika-wakhala akudzudzula boma pa zokhudza ulamuliro wabwino. Iye damangidwa pamodzi ndi Arthur Chikankheni, Mayamiko Kadango, Brian Magoya, Patrick Gadama ndi Ali Kaka ndipo adatulutsidwa pa belo ya bwalo lamilandu Lachitatu pa 15. Koma mwa onsewa, Kasambara yekha adamangidwanso patangotha maola awiri, ati ndondomeko zotulutsira amunawa sizidatsatidwe. Koma mneneri wa mtsogoleri wa dziko lino, Hetherwick Ntaba, wati anthuwa akuyenera kumvetsa nkhanza zomwe adachita Kasambara pootcha anthu osalakwa kumaliseche ndi moto wa magetsi, uko atawamanga. Iye wati izi sindale ndipo palibe chisonyezo chilichonse kuti boma lachipani cha DPP lasiya kulemekeza ufulu wachibadwidwe. Lachinayi pa 16 Febuluwale, Kasambara adatengeredwa ku ndende ya Zomba komwe adasungidwa pamodzi ndi akaidi wodikira kuphedwa kapena kuseweza moyo wawo wonse. Lachisanu, Kasambara adamutengera kuchipatala cha Mwaiwathu mumzinda wa Blantyre kuti akalandire chithandizo chachipatala, ati malinga ndi vuto lake la mtima. Koma Ntaba wati mwina anthu sakumvetsetsa, ati apolisi sangangomanga munthu popanda chifukwa. Nokha mwamva kuti belo yomwe adapatsidwa idali yosasayinidwa ndi apolisi ndiye kumumanganso sikuti pali zifukwa za ndale apa. Kasambara wakhala akulankhula chipongwe mmbuyo monsemu koma bwanji samamangidwa ngati zili zifukwa za ndale? akutero Ntaba. Malinga woimira Kasambara pamilandu, Wapona Kita, ngakhale Kasambara watulutsidwa pa belo sizikudziwika kuti adzikaonekera masiku ati. Pomwe timasindikiza nkhaniyi nkuti Kasambara ali kuchipatala cha Mwaiwathu mumzinda wa Blantyre, kuyembekezera kupita kunja ku chipatala Lachinayi.
11
Malawi Ili ndi Kuthekera Kochita Bwino pa Ulimi-FAO Wolemba: Sylvester Kasitomu Nthambi ya bungwe la United Nations yoona zaulimi ndi chakudya ya Food and Agriculture Organisation FAO yati dziko la Malawi lili ndi kuthekera kochita bwino pa nkhani za ulimi ngati litayikanso chidwi pa ulimi wa ziweto. Mkulu wa bungweli mdziko muno a Zijun Chen ati ngakhale dziko lino likuyesetsa pa ntchito yolimbana ndi umphawi polimbikitsa ntchito za ulimi, kuchilimika pa ulimi wa ziweto kuthanso kuthandiza anthu kuti azipeza ndalama pomwe agulitsa ziweto zawo. Iwo amalankhula izi pamwambo okhazikitsa ndondomeko yolimbikitsa kuzindikilitsa alimi mwansanga zamatenda omwe amagwira ziweto. Mmawuake, mkulu oyanganira ntchito za ulimi ku unduna wa zaulimi Dr. Tanira Mtupanyama anati mkumanowu wafika mu nthawi yabwino ndipo akuyembekezera kuti mfundo zomwe zimangidwe zithandiza alimi kukhala ndi njira zamakono zochitira ulimi wa ziweto kuti azipeza phindu lochuluka pa ulimi wawo. Ngati boma taika kale njira zosysanasiysana pofuna kuteteza nyama zathu pomwe zagwidwa ndi matenda kuti zisapatsilane komanso kuwaphuzitsa anthu kuti akapha nyama yoto imadwala matendawa asagawe kwa anthu omwe ali ndi ziweto anatero Mtupanyama. Mwazina iwo ati akugwira ntchitoyi mboma la mchinji kaamba koti ndi limodzi mwa boma omwe ali mmalire adziko lino zomwe zingachititse kuti kugawana kwa matenda kukhale kochuluka kwa nyama za mdziko muno.
4
Parishi ya Magomero Ayiyamikira Polimbikitsa Mpingo Odzidalira Wolemba: Sylvester Kasitomu Akhristu a mparish ya Magomero mu Dayosizi ya Zomba awayamikira kamba konetsa chidwi pa ntchito zotukula mpingowu modzidalira. Mmodzi mwa amsembe otumikira mu parishi-yi bambo Alfred Chilenga ndi omwe anena izi polankhula ndi mtolankhani wathu. Iwo ati ndi momwe akhristu akudziperekera pogwira ntchito zotukula parishi-yo zikuonetseratu poyera kuti tsopano ayamba kudziwa za udindo wawo pothandiza mpingo modzidalira. Kuno ku St. Pius toikuyetsera kachita kuthekersa pantchito zozamitsa moyo wa uzimu monga kupereka masacrament, kupereka nsembe za ukalistia komanso mibindikiro zomwe tikuchita pa parishi pano, anatero bambo Chilenga. Mwazina iwo ayamika akhristu amparishiyi kaamba kodzipereka pa ntchito yotukula mpingo posadalira thandizo lochokera kwina monga kumanga ma tchalitchi komanso kugula njinga zamoto zothandizira mayendedwe kwa aketichisti ndi zina zambiri.
2
Aonjezera masiku a katemera Mkulu wa oyanganira zaumoyo mu unduna wa zaumoyo Dr Charles Mwansambo wati ngakhale ntchito yopereka katemera wa chikuku wa Rubella idayenda bwino, padali mavuto ena amene adachititsa kuti aonjezera masiku opereka katemerayo. Kuyambira pa 12 mpaka 16 June, boma lidapereka katemerayu ndipo ngakhale padali mavuto ena, ntchitoyo idayenda bwino. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ntchito iliyonse imakhala ndi zokolakola moti padali mavuto ena amene adachititsa kuti ana ena asabaidwe. Izi zidachititsa kuti tionjezere ndalama ndi nthawi ya katemerayu, adatero Mwansambo. Iye adaonjeza kuti katemerayo ndi wofunika kwambiri. Mkulu wa bungwe la zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe adati ndiwokhutira ndi momwe ntchitoyo idayendera. Iye adati: Ntchito idayenda bwino kwambiri moti tiyamike magulu onse omwe adatengapo mbali kuti adagwira ntchito yotamandika chifukwa ameneyu ndi katemera ofunika kwambiri. Malingana ndi mneneri wa unduna wa zaumoyo, Adrian Chikumbe, sitalaka ya aphunzitsi imene idaliko sabata yatha idapereka mpata kwa ana omwe amangokhala kuti apite kukalandira katemerayu mwaunyinji. Zidachitika ngati kutulo. Chikonzero chathu chidali chopereka katemera kwa ana pafupifupi 8 miliyoni ndipo pofika Lachitatu sabata ya katemerayo, ana 80 pa 100 aliwonse adali atabayitsa, adatero Chikumbe. Potengera chiwerengero chomwe adapereka Chikumbe, zikutanthauza kuti mmasiku atatu okha a katemerayu, ana 6.4 miliyoni mwa ana 8 miliyoniwo adali atalandira kale katemerayo ndipo ana 1.8 miliyoni ndiwo amayenera kulandira katemera mmasiku awiri otsalira. Chikuku (Rubella) ndi nthenda yomwe imagwira yopumira ndipo imatulutsa zidzolo mthupi lonse ndi zizindikiro za chimfine monga kutentha thupi, kuchucha mamina ndi kutsokomola ndipo imafala popatsirana kudzera mumpweya. Malingana ndi tsamba la zaumoyo la pa internet, chikuku (Rubella) chimayamba ndi kachilombo ka mtundu wa virus komwe nkovuta kuthana nako kwake kotero, mwana akadwala, amayenera kupatsidwa mpata wokwanira wopuma kuti asamasewere ndi anzake. Tsambali likusonyezanso kuti ana 90 mwa 100 omwe sadalandire katemera amakhala pachiopsezo chotenga matendawa. Izi zimachititsa unduna wa zaumoyo kukhazikitsa nyengo ya katemerayu.
6
Othawa nkhondo ku Mozambique asamukira ku Neno Bungwe lothandiza anthu othawa kwawo pazifukwa zosiyanasiyana la UNCHR layamba kusamutsa anthu othawa nkhondo ku Mozambique kupita ku Luwani mboma la Neno. Anthuwa, omwe akuthawa nkhondo yapachiweneweni, amafikira kumisasa yongoyembekezera mmaboma a ku Nsanje, Chikwawa, Mwanza komanso Neno omwe achita malire ndi dziko la Mozambique. Escom in free-for-all fuel scam Wait gets longer Secrecy over party funders Bungwe la UNHCR lidayamba kusamutsa othawa nkhondowa sabata ziwiri zapitazi pamene anthu 81 adawapititsa ku Luwani mboma la Neno kuchokera kumalo omwe amangodikirirapo ku Nsanje. Ena mwa othawa nkhondo ku Mozambique ulendo wa ku Luwani Mkulu wofalitsa nkhani kubungweli mMalawi muno, Kelvin Shimoh, adati cholinga chawo ndi kuti othawa nkhondowa akhale malo amodzi komwe angakalandire thandizo lokwanira. Iye adati pali pafupifupi anthu okwana 11 000 omwe athawa nkhondo kuchokera ku Mozambique ndipo chiwerengerochi chikuyemebezeka kukwera kwambiri. Ku Kapise mboma la Chikwawa kuli anthu pafupifupi 10 000 ndipo akuyembekezeranso kusamutsidwa kupita ku Luwani komwe kuli malo abwino okhala, olandirira thandizo la mankhwala komanso sukulu zoti ana omwe ndi ambiri azikaphunzirako. Mkulu wina wa bungwe lomweli la UNHCR woona za chitetezo cha othawa kwawo, Elsie Bertha Mills-Tettey, wapemphanso dziko la Malawi ndi anthu onse kuti asawasale anthuwa powaganizira kuti ndi achiwembu. Kafukufuku wathu wapeza kuti anthu othawa nkhondowa ali pachipsinjo choopsa chifukwa ataya katundu wawo, abale awo ena aphedwa akuona, komanso ena mwa iwo apulumuka atazunzidwa, adatero Mills-Tettey. Iye wayamikiranso bungwe la Unicef pachithandizo chomwe likupereka kwa anthuwa nkhondowa, makamaka ana, pankhani zowambikitsa kuti apitirizebe maphunziro awo.
11
Abwenzi Alonjeza Kuthandiza Radio Maria mu Nthawi ya Mariatona Wolemba Richard Makombe Abwenzi a Radio Maria mu Akidayosizi ya Blantyre ati ndiokonzeka kuthandiza wayilesiyi mu nthawi ino ya Mariatona kuti ikwanitse kupeza ndalama zomangira studio yayingono mu mzinda wa Mzuzu. Wapa mpando wa Abwenzi a Radio Maria mu Akidayosizi ya Blantyre a James Ngomba awuza Radio Maria kuti gulu lawo ndilokonzeka kuonesetsa kuti mu nthawin ya Mariatona wa October Radio Maria ipeze ndalama zokwanira kuti cholinga cha wayilesiyi chikwaniritsidwe. Radio Maria imadalira thandizo kuchokera kwa anthu komanso akhristu eni ake choncho ife ngati abwenzi tikuyenera kukhala patsogolo kuthamanga ndi amayi Maria pofuna kupeza thandizo loyenera kuti lithandize wayilesiyianatero a Ngomba. A Ngomba ati ayesetsa kufikira anthu ambiri kuti atahandize wayilesiyi komanso kuonesetsa kuti katundu monga ma booklet a Radio Maria afika kwa anthu ochuluka kuti akwanitse kuthandiza mu nyengo ya Mariatona. Mariatona inayamba pa 13 October ndipo ikuyembekezeka kufika kumapeto pa 8 December 2019,ndipo wayilesiyi ikuyembekezeka kupeza ndalama zokwana 15 million kwacha.
13
Banja Lafa Polimbirana Thumba la Chimanga Anthu okwiya apha bambo wina mboma la Ntcheu kamba komenya ndi kupha mkazi wake atasemphana maganizo kamba ka thumba la chimanga. Chigalu: Aphedwa mmachitidwe osiyana Wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sub-Inspector Hestings Chigalu, watsimikiza zankhaniyi ndipo wati bamboyu yemwe ndi Aubrey James wa zaka 41 zakubadwa anasemphana maganizo ndi mkazi wake Lyness Million wazaka 33 zakubadwa kamba kofuna kugulitsa thumba la chimanga ndi cholinga choti abwenze ngongole, Kutsatira kusamvanaku, bamboyu anayamba kumenya mkazi wakeyu ndi chitsulo mpaka kukomoka, ndipo anthu anamutengera ku chipatala chachingono cha Nsipe komwe anamwalira asanalandire thandizo la mankhwala. Anthuwo anabwerera kumudzi ndi kukafunafuna bamboyu, ndipo atamupeza, anamumenya mpaka kupha. Anthuwa aphedwa mu machitidwe osiyana pomwe anthuwa anasemphana ndipo bamboyu analedzera ndipo anayamba kumenya mkaziyo mpaka kukomoka kutsatira kumwalira kwa mayiyo ku chipatala cha Nsipe, anthu okwiya anamenya ndi kuphanso bamboyo, anatero a Chigalu. Iwo ati akufufuzabe zankhaniyi ndipo anthu omwe achita iziwa akuyenera kumangidwa kamba kotengera lamulo mmanja mwawo. Lyness Million amachokera mmudzi mwa Zidana mfumu yaikulu Kwataine ndipo Aubrey James amachokera kwa mfumu yaikulu Makwangwala onsewa ndi a mboma la Ntcheu.
14
Boma Lilangiza Alimi Kulima Mbewu Zakasakaniza Wolemba: Sylvester Kasitomu Boma lalangiza alimi kuti ayambe kuchita ulimi wa kasanikaniza pofuna kuthana ndi mavuto odza kamba ka kusintha kwa nyengo. Nankhumwa: Alimi asamangodalira kulima chimanga basi Nduna ya zaulimi, ulimi wa mthilira ndi chitukuko cha madzi a Kondwani Nankhumwa amayankhula lachitatu pa mwambo wa chaka chino okumbukira chakudya pa dziko lonse amwe unachitikira kwa Bvumbwe mboma la Thyolo. Iwo ati unduna wawo waika ndondomeko zapadera zowafikira alimi pa mbeu zoyenera zomwe akuyenera kulima potengera ndi madera awo padakalipano pomwe mvula ikugwa mwa njomba kaamba ka kusintha kwa nyengo. Choyambirira tikulimbikitsa alimi kuti asamngodalira mbewu monga ngati chimanga chokha zithanso kulima mbewu zina monga chinangwa kapena ntedza zomwe zimabereka ngakhale mvula yochepa, anatero Nankhumwa. Polankhulapo mthumwi ya bungwe la food and agriculture organization mdziko lino ku bungwe la mmaiko onse Dr. Zijune Cheign wati wokhutira momwe boma lamalawi likuchitira pankhani za chakudya. Mwazina iwo ati ngakhale izi ziri chomwechi pakufunika kuchitapo kanthu maka pakasungidwe ka chakuya komanso kulimbikitsa zakudya za magulu. Mwambo wakumbukira chakudya wa chaka chino umachitika pa mutu woti machitidwe athu, tsogolo lathu, zakudya zopatsa nthanzi, fuko lopanda njala.
4
Achikulire asowa thandizo madzi atavuta Limodzi mwa mabungwe omenyera ufulu wa anthu achikulire mdziko muno lati ena mwa achikulire amene adakhudzidwa ndi madzi osefukira sabata ziwiri zapitazo sakulandira thandizo loyenera kuchokera ku boma. Madzi osefukirawa akhudza maboma 15 mwa 28 mdziko muno, ndipo anthu 868 895 ndiwo akusowa pokhala chifukwa cha vutoli. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mwa anthuwa, 672 ndiwo adavulala pomwe 56 adaphedwa, malinga ndi kalata yomwe bungwe la Unicef idatulutsa Lachitatu. Kazembe adagonekedwa kuchipatala Pakadalipano anthu 90 000 akukhala mmisasa yomwe yakhazikitsidwa mmaboma ena monga Chikwawa ndi Nsanje. Komatu anthuwa akulandira thandizo loperewera lomwenso likumafika mochedwa malinga ndi kalata yochokera ku bungwe la European Commissions Joint Research Centre(JRC). Koma mwa anthuwa achikulire ndiwo akuvutika kwambiri chifukwa akungodalira thandizolo chifukwa cha ukalamba. Bungwe la Friends for the Elderly lati kafukufuku wake akuonetsa kuti anthu achikulire ena sadalandirebe thandizo mpaka lero ngakhale ngozi ya madzi osefukirawa idagwa sabata zitatu zapitazo kuchokera pa 5 March. Malinga ndi kalata yomwe bungwelo latulutsa yosainidwa ndi mmodzi mwa oyendetsa bungwelo Mike Magelegele, bungwe lake lidapeza kuti vutoli lakhudza achikulire omwe amakhala okha opanda owasamalira komanso mmalo ena kufikamo. Bungwelo lati mmodzi mwa nkhalambazi, Gogo Naphiri yemwe amakhala mmudzi mwa Namboya kwa T/A Machinjiri mboma la Blantyre adamupeza ali yekhayekha opanda thandizo ndipo kuti anthu a mmudzi mwake sangamuthandize chifukwa ati ndi mfiti. Naye gogo Fanny Kazembe wa zakat 56 yemwe ndi Nyakwawa Nnunkha ya kwa T/A Mpama mboma la Chiradzulu yemwe nyumba yake idamugwera pa March 7 ndipo adavulala phazi, kumsana ndi mmapewa mpaka kugonekedwa pachipatala cha Nguludi thandizo lochokera kuboma monga chakudya ndi zina silinamupeze.
15
Cama, ma Rasta asemphana pa za zionetsero Chetechete sautsa nyama zabvumbulukadi kuti pali mangawa aakulu pakati pagulu lotsatira chikhulupiriro cha Chirasta ndi mabungwe omenyera maufulu a anthu mdziko muno. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zavumbuluka kuyambira pomwe bungwe loyanganira za ufulu wa anthu ogula malonda la Consumers Association of Malawi (CAMA) lidalengeza kuti padzakhala ziwonetsero pa 17 Januwale zosonyeza mkwiyo umene Amalawi ali nawo pa mfundo za chuma za boma la Joyce Banda. Gulu la ma Rasta lotchedwa Rastafari for Unity in Malawi motsogozedwa ndi mkulu wawo Charles Liwomba yemwe amadziwika kuti Ras Judah I lati a mabungwe amakonda kuwafuna akakhala ndi vuto loti awathandize koma iwo akapeleka madandaulo awo kumabungwe salandira thandizo lililonse. Judah I anauza atolankhani sabata yatha ku Lilongwe kuti gulu lawo lakana pempho la CAMA loti ma Rasta adzachite nawo zionetserozo chifukwa gulu lawo likuwona ngati amabungwewo amangofuna kuwagwiritsa ntchito nkuwataya zinthu zikayenda komanso sakufuna kuti anthu adzavutikenso ngati momwe zinaliri pa 20 Julaye 2011. Iye adati gulu lawo linapereka kalata yopempha kuti boma liwaganizire pa zinthu zina zomwe zimawavuta pamoyo wawo kudzera ku bungwe loona za maufulu a anthu la Malawi Human Rights Commission (MHRC) nthawi yomwe wapampando wa bungwe la CAMA a John Kapito amatsogolera bungwelo koma sanathandizidwe. Mwa zina zomwe ma Rasta ankafuna kuti boma liwapangire ndi kulola kuti ana a gulu lawo okhala ndi tsitsi litalilitali lopotana kuti aziloledwa kuphunzira limodzi ndi anzawo msukulu za boma komanso kuti boma livomereze kulima ndikuchita malonda a fodya wamkulu wa chamba. Vuto lomwe lilipo ndilakuti anthu amaona ngati ma Rasta ndi anthu otsalira kwambiri koma sichoncho nafenso ndianthu ofunika tsono tisamaoneke ngati anthu pokhapokha pakakhala vuto. Takhala tikupempha kuti boma liunikeko ena mwa mavuto omwe ife timakumana nawo koma mabungwe omwewo satithandiza ndiye ife tiwathandiza bwanji? anatero Judah I. Koma Kapito wauza nyuzipepala ya The Nation kuti zomwe ma Rasta anenazo ndizabodza ndipo wati bungweli silinapemphe munthu kapena bungwe lililonse kuti lidzatengepo mbali pazionetsero koma anthu omwe ndiogula malonda ndipo akumva nawo kuwawa ndimomwe zinthu zikuyendera. Adatsutsanso zomwe Judah I adanena kuti bungwe la Cama lidati ma Rasta achite nawo zionetsero ndipo adzapatsidwa K400 000. Bungwe lathu silinapempheko munthu kapena bungwe lililonse kuti lidzachite nawo zionetsero. Ngati sitinapemphe a bungwe loyanganira za maufulu aanthu ogwira ntchito la Malawi Congress of Trade Union (MCTU) ndiye iwo ndi ndani? anatero Kapito.
10
Papa Wasankha Episkopi Watsopano Mdziko la Zambia Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wasankha episkopi watsopano wa dayosizi ya Ndola mdziko la Zambia. Malinga ndi malipoti a Vatican Radio, Papa lachisanu wasankha Ambuye Benjamin Phiri kukhala episkopi wa dayosiziyo. Episkopi watsopanoyo-Ambuye Phiri Ambuye Phiri akhala ali episkopi wothandizira wa dayosizi ya Chipata mdzikolo kuyambira mchaka cha 2011. Lachisanu pa 3 July 2020 nthawi ya 12 koloko masana ku Rome likulu la mpingo wa katolika, Vatican, ndi pamene lalengeza kuti Papa Francisco wasankha Ambuye Benjamin Phiri kukhala episkopi wa dayosisi ya Ndola. Ambuye ongosankhidwawa omwe adabadwa pa 14 June 1959 ku Chipata adadzodzedwa unsembe pa 14 September 1986 ku dayosisi ya Chipata. Ngati wansembe, iwo atumikira ma parish osiyana-siyana komanso anali woyanganira za chiyitanidwe, anakhalapo woyanganira sukulu yosula ma catechist komanso anakhalapo mlembi wa Ambuye Medardo Mazombwe. Kuyambira mchaka cha 1997 mpaka 2002 adakachita maphunziro a malamulo a mpingo (Canon Law) ku sukulu ya ukachenjede yotchedwa Pontifical Urban University ku Rome. Pambali pokhala episkopi wothandiza kapena kuti Auxiliary Bishop wa Diocese ya Chipata kuyambira mchaka cha 2011 iwo analinso mkulu woyanganira kapena kuti Rector wa Seminary yaikulu ya Saint Dominic ku Lusaka mdzikolo, ntchito yomwe ayigwira kuyambira mchaka cha 2004. Mpingo wa katolika ku Malawi nawo ukudikira mwa chidwi komanso modekha kuti Papa Francisco asankhe episkopi wa dayosizi ya Dedza.
11
HRDC Yauza A Malawi Akhale Tcheru pa Chisankho Bungwe lomenyera ufulu wa anthu mdziko muno la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lapempha anthu mdziko muno kuti akhale tcheru pa mchitidwe uliwonse omwe ungakhale okayikitsa pa chisankho chomwe chikudzachi. Mkulu wa bungweli Gift Trapence wanena izi pa msonkhano wa atolankhani omwe bungweli linachititsa lero mu mzinda wa Lilongwe. Ena mwa mamembala a bungwe la HRDC Trapence wati pali mphekesera zakuti pali ena omwe akufuna kubera chisankho choncho ndi kofunika kukhala tcheru mu nyengoyi ndi kuwonetsetsa chilichonse chomwe chikuchitika mdziko muno. Iwo apempha athu kuti akhale tcheru ndi mmalire mwa dziko lino komanso mmabwalo a ndege pamene pakumveka mphekesera kuti ena afuna alowetse mapepala oponyera voti mwachinyengo. Pamenepa iwo atsimikizira a Malawi kuti aliyense obera chisankhochi azayankha mlandu payekha-payekha ati popeza apeza kale owaimira mlandu pakazachitika chisokonezo chilichonse. Trapence anatinso kutsatira kukanidwa kwa bungwe lawo kuti liyanganire nawo chisankhochi, iwo agwira ntchito ndi mabungwe ena omwe achita nawo ubale omwe anapatsidwa kale chaka chatha chilolezo chochita izi kuti azipeza mauthenga okhudza chisankhochi.
11
Kampani ya Terras Yati Itenga Gawo Pothana ndi Coronavirus Kampani yopanga mankhwala a za chilengedwe ya Terras yati ikufuna kutenga nawo gawo pothandiza anthu omwe apezekeka ndi kachirombo koyambitsa nthenda ya COVID-19 ngati njira imodzi yolimbana ndi nthendayi mdziko muno. Akuti ali ndi kuthekera kothandiza COVID-19 Izi zayankhulidwa pa msonkhano wa olemba nkhani omwe kampaniyi inachititsa loweruka pa 9 May mu mzinda wa Blantyre pamene yati ikufuna kugwira ntchito ndi boma maka kuti ifikire anthu omwe apezeka ndi nthenda-yi yomwe ilibe mankhwala ovomerezeka kufikira pano.
6
Lamulo latsopano la zipani alikambirana Dziko lino lili ndi zipani zoposa 40. Komatu mwa zipanizi zisanu zokha ndi zomwe zimakangalika pomwe zina zili ziii ngati madzi a mfiliji kudikira nthawi ya zisankho. Komatu mchitidwewu ukhala mbiri yakale malinga ndi lamulo latsopano la zipani lomwe aphungu a Nyumba ya Malamulo akuyembekezera kukambirana akakumananso mwezi wa May. Malinga ndi mtsogoleri wa Nyumba ya Malamulo, Kondwani Nankhumwa, aphungu adzakambirana za lamuloli mwezi wa May chifukwa pamene aphungu akukumana panopa, nthawi ndi yochepa. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kupereka ndalama, zinthu zina kwa ovota kudzaletsedwa Tikadakonda tikadakambirana za lamuloli koma nthawi yangochita njiru. Imeneyi ilowanso pamndandanda wa zokambirana za mwezi wa May, adatero Nankhumwa. Ndi lamuloli, zipani zizikakamizika kuonetsa kuti zikugwira ntchito yake, monga kupanga nawo zisankho, komanso kupanga misonkhano yaikulu ya mamembala mchipani ndi cholinga choonetsa kuti zikugwiradi ntchito zotumikira anthu. Zikapanda kukwaniritsa izi, mpamene mkulu woyanganira zipani azizichotsa mkaundula. Lamulo latsopanolo lidzachotsa lamulo lakale la zipani lomwe limaona kulembetsa kwa chipani ndi ndondomeko zotsatira. Mwa zina, lamulo latsopanolo lomwe lili ndi magawo 8 likuunikira zingapo, monga kukhazikitsa ofesi ya wolembetsa ndi kuthetsa zipani, zipani kulongosola bwino momwe zimapezera ndalama komanso kuti mamembala azidziwa momwe ndalama za chipani zikuyendera. Lamulolo likutambasulanso za kayendetsedwe ka zisankho monga kuthana ndi mchitidwe wopereka ndalama ndi zinthu zina kwa ovota nthawi ya chisankho komanso kukhala membala wa zipani zingapo. Polankhulapo za kufunika kwa lamuloli, mkulu wa bungwe limene muli zipani zosiyanasiyana la Centre for Multiparty Democracy (CMD), Kizito Tenthani adati adati padakalipano mamembala a zipani alibe mphamvu zenizeni mzipani mwawo, zimene lamulolo likufuna kusintha. Bungwelo ndi lomwe lakhala likukambirana ndi mbali zonse zokhudzidwa momwe lamulolo lidzathandizire zipani kukwaniritsa ntchito yoimirira anthu komanso kupereka umwini wa chipani kwa mamembala. Zimaoneka ngati atsogoleri ndi amene amakhala ndi mphamvu zambiri mchipani. Lamololi lithandiza kusintha zimenezi. Kuonjezera apo, ndale zathu Mmalawi muno zakhala kwambiri zodalira ndalama. Panthawi ya chisankho, zipani, komanso amene akufuna kuimira zipani pamipando yosiyanasiyana amakhala akupereka ndalama ndi zinthu zina ncholinga chokopa anthu kuti awavotere, adatero Tenthani. Iye adati mchitidwewu umapangitsa ndale kukhala zodula, komanso anthu omwe ali ndi ndalama kukhala ndi mwayi wolowa mmaudindo ngakhale nthawi zina anthu oterowo amakhala opanda masomphenya a mmene angathandizire anthu kudera kwawo. Lamuloli lithandiza kuthetsa mchitidwe umenewu. Likufunanso zipani zandale zizinena komwe zimapeza ndalama ncholinga chothetsa mchitidwe wa katangale, adaonjezera Tenthani. Koma mmodzi mwa akadaulo pa ndale mdziko muno Rafiq Hajat adati palibe chaphindu chomwe lamulo latsopanolo liphule chifukwa lamulo lomwe lilipo lakanika kugwiritsidwa ntchito bwino. Hajat adati mwachitsanzo lamulo lakaleli limati chipani chilichonse chizipereka kwa mkulu wakalembera wa zipani momwe achitira pa chuma chaka chikamatha ndipo kuti ngati satero chipanicho chizithetsedwa. Komatu izi sizili choncho. Ngati tikukanika kukwaniritsa zinthu ngati izi, ndiye lamulo latsopanoli tidzaligwiritsa ntchito bwanji? adadabwa Hajat. Iye adati aphungu ayenera kutenga nthawi yaitali kukambirana zinthu monga za kuba ndalama mboma (cashgate), njala ndi zina osati za lamulo la zipanili. Tiyeni tiyangane njira zogwiritsa ntchito lamulo lakale lomweli, adatero Hajat. Komatu Tenthani adatsutsa izi polongosola kuti lamuloli ndi losiyana kwambiri ndi lakaleli chifukwa layesera kukonza zimenezi ndipo akukhulupilira kuti lidzagwiritsidwa ntchito bwino. Choti anthu adziwe nchakuti lamulo lilipo pano lidapangidwa mwachangu kwambiri ncholinga choti mchaka cha 1993 anthu athe kulembetsa zipani kuti zikapange nawo chisankho cha 1994. Mmalo ambiri, lamulo lili panoli silinaunike bwino maka pankhani ya kayendetsedwe ka zipani, komanso kuumiriza kuti zipanizo zitsatire malamulowo, adalongosola Tenthani.
11
MSE Ipereka Maphunziro apa Intaneti kwa Atolankhani Kampani yogulitsa ma share, ya Malawi Stock Exchange yati kudzera mwa atolankhani ndi kwapafupi kuti anthu amvetse momwe msika wa ma share umakhalira. Kanyangala: Atolankhani ndi ofunika kwambiri Mmodzi mwa akuluakulu a kampaniyi a Kelini Kanyangala awuza Radio Maria Malawi lolemba pakuyamba kwa maphunziro a sabata imodzi a pa internet, omwe kampaniyi yakonzera atolankhani ochokera mnyumba zofalitsa nkhani zosiyansiyana za mdziko muno. A Kanyangala ati maphunzirowa athandiza kwambiri kuzindikiritsa anthu ambiri za momwe angachitire ngati akufuna kugula ma share kamba koti atolankhaniwa adzatha kufotokozera bwino pambuyo pa maphunzirowa, zomwe ati ndi zothandiza kwambiri pa chitukuko cha dziko lino. Ife monga Malawi Stock Exchange (MSE) timazindikira gawo lofunikira lomwe atolankhani amatengapo maka potenga gawo pofalitsa nkhani zapa msika wama share ndipo talimbikitsa ubale umenewu pochita maphunziro apa intaneti, anatero a Kanyangala. Iwo ati maphunzirowa athandiza atolankhaniwa kumvetsa nkhani za malonda komanso anthu kuti akakhala ndi mafunso azidziwa kokafusa.
2
A Malawi adalimba nazo chaka chatha Ululu, kulavulagaga ndi kupala moto kudalipo mchaka chomwe changothachi monga momwe akadaulo mnthambi zosiyanasiyana akunenera kuti padalibe popumira koma kubanika kokhakokha. Malinga ndi akadaulo a zamaufulu, zaumoyo ndi oyimira anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana, Amalawi adawawulidwa, makamaka pa mmene ogulitsa zinthu amakwezera mitengo ndi mmene ntchito zina monga zaumoyo, ufulu wa anthu, magetsi ndi madzi zidayendera mchaka changothachi. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Madzi ndi moyo: Mnyamatayu sakadachitira mwina koma kupeza njira yomwera madzi ku Nkhotakota Za umoyo Chaka cha 2015 ndi chaka choyamba chomwe tidaona anthu odwala mchipatala akudya kamodzi patsiku osatengera mtundu ndi kuchuluka kwa makhwala omwe akulandira pavuto lawo. Chaka chomwechi ndicho kudali chionetsero cha anamwino ndi azamba pa nkhani yoti boma silikuwalemba ntchito ngakhale kuti adachita ndi kumaliza maphunziro awo a ntchitoyi panyengo yomwenso ogwira ntchito zachipatala ali operewera. Malingana ndi mkulu wa anamwino ndi azamba, Dorothy Ngoma, cholinga cha chionetserochi chidali kupempha boma kuti lilembe ntchito achipatala omwe adamaliza maphunziro komanso libweze ganizo loti anthu odwala azidya kamodzi patsiku. Iye adatinso nkhani ina yodandaulitsa idali kusowa kwa mankhwala mzipatala, zomwe zidachititsa kuti anthu osauka asakhale ndi mwayi wolandira thandizo loyenera akadwala. Chomwe ife tikufuna nchakuti anamwino ndi azamba onse omwe sadalembedwe ntchito alembedwe komanso chilinganizo choti anthu odwala azilandira chakudya kamodzi mzipatala chibwezedwe chifukwa munthu wodwala amafunika chakudya chokwanira kuti mankhwala agwire bwino ntchito mthupi, adatero Ngoma. Mkulu wa bungwe loyanganira za ufulu wa anthu pa nkhani za umoyo, Charles Nyirenda, adati kafukufuku yemwe bungweli lidachita mzipatala zingapo mdziko muno adaonetsa kuti mankhwala mzipatalazi mudalibe. zaumoyo Peter Kumpalume adati mankhwala adasowa mzipatala kaamba ka anthu ena oipa mtima omwe amaba mankhwala nkumakagulitsa posaganizira miyoyo ya anthu. Ndunayi idalonjeza akuti ithana ndi anthu onse omwe akukhudzidwa ndi zachinyengo cha mtundu uliwonse muundunawu. Za maufulu Nkhani ina yomwe idakhoma misomali yowawa pamitu pa Amalawi ndi ya maufulu omwe akatswiri akuti sadalemekezedwe monga momwe zimayenera kukhalira. Malingana ndi mmodzi mwa akuluakulu oyanganira za maufulu, Billy Mayaya, maufulu ambiri adaphwanyidwa, monga ufulu wa maalubino omwe akuti amaphedwa ndi kuchitidwa nkhanza za dzaoneni. Iye adatinso ufulu wina ndi wolandira nthandizo la mankhwala akadwala komanso chakudya. Mayaya adatinso mchakachi, boma lidaonetsa kusalabadira maganizo ndi zofuna za anthu makamaka pa mmene lidagulitsira banki ya boma ya Malawi Savings anthu ndi magulu osiyanasiyana atayesetsa kuletsa. Mkuluyu adatinso ufulu wa atolankhani udaponderedzedwa kwambiri mchakachi ngakhale kuti boma lidalonjeza kuti lidzapititsa patsogolo ufulu wa atolankhani kuti azidzatha kufufuza ndi kuulutsa nkhani popanda kusokonezedwa. Mwachitsanzo, wayilesi ya Zodiak idaletsedwa kulowa kunyumba ya boma kuli zochitika pomwe wailesi ndi nyuzipepala zina zidaloledwa, kumeneku nkuwaphwanyira ufulu wotola ndi kuulutsa nkhani, adatero Mayaya. Nduna yofalitsa nkhani za boma, Jappie Mhango, adati mpofunika kumpatsa nthawi yoti alingalire zonsezi asadayankhepo kalikonse kuti poyankha atsekeretu maenje onse. Magetsi ndi madzi Mawu oti madzi ndi moyo adasanduka nthano mchaka chimenechi polingalira mavuto omwe adalipo kuti mpaka anthu kufika pomamwa madzi a mzitsime ndi zithaphwi chifukwa mipopi imakhala youma nthawi zambiri. Malinga ndi akuluakulu a makampani opopa ndi kugawa madzi osiyanasiyana, vutoli lidakula kaamba ka vuto la magetsi omwenso adamvetsa kuwawa Amalawi. Madzi timachita kupopa ndi mphamvu ya magetsi ndiye ngati magetsi kulibe, simungayembekezere kuti tipopa madzi okwanira nchifukwa mumaona kuti madzi pena atuluka pena asiya, adatero mmodzi mwa akuluakulu a makampaniwa, Alfonso Chikuni, wa Lilongwe Water Board. Mkulu wa bungwe loyanganira za anthu ogula ndi kugwiritsa ntchito zinthu zosiyanasiyana, John Kapito, adati kulanda anthu madzi ndi magetsi ndi chilango chowawa kwambiri potengera ndalama zomwe anthuwa amapereka kumakampaniwa. Chodabwitsa nchakuti mabilu a madzi ndi magetsi mmene alili kukwera chonsecho nthawi zambiri kumakhala kulibe. Anthu amangokhalira mumdima ndi kumwa madzi osalongosoka, adatero Kapito. Anthu ambiri makamaka a mabizinesi adandandaula kuti kuthimathima kwa magetsiwa kudasokoneza bizinesi moti ena adataya katundu wambirimbiri yemwe adaonongeka panyengo yomwe kudalibe magetsi. Za makhalidwe Kapito adati moyo mchakachi udawawa zedi potengera momwe mitengo ya zinthu imakwerera pomwe mapezedwe a ndalama adali ovuta kwambiri. Iye adati kusakolola bwino kwa chaka chatha, kuvuta kwa malonda a fodya ndi mabala a Cashgate ndi zina mwa zomwe zidachititsa kuti mmatumba mwa anthu muume, koma izi sizidamange buleki ya kakwenzedwe ka mitengo ya katundu. Kunena zoona Amalawi adamva ululu mchaka chimenechi. Ndalama zimasowa koma si momwe zinthu zimakwerera mtengo. Kayendetsedwe ka chuma nako kadali kodwalitsa mutu; zimangokhala ngati palibe woyendetsa, adatero Kapito. Iye adati chodandaulitsa kwambiri nchakuti mayankho omwe ankaperekedwa pamavuto onsewa sadali ogwira mtima, mmalo mwake zimakhala ngati kunyogodola anthu omva kale kuwawa. Chiyembekezo mu 2016 Akuluakuluwa adati Amalawi akufunika zakupsa mchaka chomwe tayambachi cha 2016 monga kusintha momwe zinthu zimayendetsedwera chaka chatha komanso kupatula ndale ndi kayendetsedwe ka boma. Kapito adati ali ndi chiyembekezo kuti chaka chino, boma lichita chotheka kuchita kafukufuku wokwanira ndi kuweruza milandu ya Cashgate kuti maiko omwe adanyanyala kuthandiza dziko lino abwererenso. Mayaya naye adati boma likhwimitse ndondomeko zotetezera maufulu a anthu, makamaka maalubino, ana ndi amayi omwe nthawi zambiri amakhala kunsonga ya nkhanza zosiyanasiyana.
2
Lengwe National Park Idzetsa Mavuto a Malo Olima By Thokozani Chapola 2019/07/lengwe-np.jpg 367w" sizes="(max-width: 820px) 100vw, 820px" />Mbali imodzi ya Lengwe National Park Anthu a mmidzi ya Mtambawatherere komanso Njobvuyalema kwa mfumu yaikulu Ngabu mboma la Chikwawa ayamba kuthawira mdziko la Mozambique kaamba kosowa malo olima. Malinga ndi anthu a mderali lomwe ndi loyandikana ndi nkhalango yosungirako nyama zakutchire ya Lengwe, anthu amaletsedwa kulima mu nkhalangoyi momwe ndi mokhamo momwe muli malo olima ati kaamba koti ndi nkhalango yotetezedwa. Mfumu ya derali yati anthuwa kwa nthawi yaitali akhala akulima mu nkhalangoyi kufikira zaka ziwiri zapitazo pomwe oyanganira nkhalangoyi anayamba kugwira ndi kumanga aliyense wopezeka akulima mu nkhalangoyi. Malinga ndi mfumuyi anthuwa akagwidwa akumalipilitsidwa ndalama za nkhaninkhani akapezeka akulima mmalowa zopmwe ati zakwiyitsa kwambiri anthu a mdera lake. Abusa anapita kukadyetsa ngombe koma anagwidwako pomwe mbuyo monsemu timapitako bwinobwino. Abusa wa alipiritsidwa 80 sauzande aliyense kuti atuluke ku polisi. Zimenezi ndi zomwe zakwiyitsa anthu ndi kuyamba kupita mdziko la Mozambique kuti mwina mkukapezako malo olima ndi kudyesera ziweto, inatero mfumu Chagaka. Iwo apempha mabungwe omenyera ufulu wa anthu kuti athandize anthu a mderali kuti apezeko mtendere. Trapence: Boma lichitepo kanthu Polankhulapo wachiri kwa wapampando wa mgwirizano wa mabungwe omwenyera ufulu wa anthu mdziko muno Human Rights Defenders Coalition a Gift Trapence ati boma likuyenera kukambirana ndi anthuwa ndi kuwapezera malo olima. Ngati anthu akusowa polima ndiye kuti pali vuto ndiye bomalo liyenera kuti liyesetse kuti likambirane ndi anthu komanso mafumu a derali, kuti nawonso apeze malo okhala ndi kulimapo, anatero Trapence. Koma polankhulapo mneneri mu unduna wa zachilengedwe, mphamvu za magetsi ndi migodi a Sangwani Phiri ati anthu sayenera kulima ku malowa kaamba koti malowa ndi otetezedwa ndi boma kuti azisungirako nyama basi. Malo aliwonse omwe ndi otetezedwa aliyense akapezekamo ndi kulakwira malamulo a boma. Nyama zikawavulaza adzabweranso ku boma kuti liwapepese ngati kuti ifeyo tikulephera kusamalira nkhalangoyo choncho ife tikuteteza nyama komanso kuteteza miyoyo ya anthuwo, anatero a Phiri. Lengwe National Park inakhazikitsidwa mchaka cha 1970 ndipo kwa nthawi yaitali anthu akhala akulima mu nkhalangoyi yomwe ili ndi nyama zochuluka kuphatikizapo yotchuka kwambiri ya Nyala.
14
Amanga ogulitsa chamba Wolemba ndi JOSEPH MKANGO* Apolisi ku Zalewa mboma la Neno amanga abambo awiri atawapeza ndi chamba cholemera makilogalamu 10. Minda ya chamba ngati iyi njoletsedwa Malinga ndi wapolisi wofufuza nkhani zosiyanasiyana James Kancheka, awiriwo ndi John Tamani wa zaka 27 ndi James Chibani wa zaka 34 omwe ndiwochokera kwa mmudzi mwa Zalewa kwa T/A Symon mbomalo. Anthu ndiwo adatsina khutu apolisi ponena kuti awiriwa amagulitsa chamba. Mchitidwe wogulitsa chamba ukusokoneza ena mpaka kusiya sukulu panjira ndipo ena akupenga nacho kumene, adatero Kancheka. Iye adati nchifukwa chake apolisi akuchilimika kumanga opezeka ndi chamba kuti ena atengerepo phunziro. Padakalipano, chambacho achitengera kumalo ofufuzira zinthu a Bvumbwe Research Station kuti akachiyese. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi *a Mkango ndi mtolankhani wathu wapadera.
7
Ntchito Yomanga Tchalitchi la Mzimu Woyera Yayambika Wolemba: Glory Kondowe Akhristu a tchalitchi la Mzimu Woyera 1 nthambi ya parishi ya Mzama mu dayosizi ya Dedza ayamba ntchito yomanga tchalitchi latsopano. Malinga ndi wapampando wa tchalitchili a Edmond Kamwana, ganizoli ladza kutsatira kuchuluka kwa chiwerengero cha akhristu a tchalitchili. Iwo ati padakalipano pa tsiku la mapemphero, akhristu ena akumapemphelera panja kaamba ka kuchepa kwa tchalitchili. Powonjerapo mayi Gloria Kamwana omwe wapampando wa bungwe la amayi pa tchalitchili anati ndiwosangalara ndi kufika kwa Radio Maria Malawi ku derali. Ndikuthokodza chifukwa Radio Maria Malawi chifukwa imasisimutsa anthu osiyanasiyana woti ena si a mpingo wakatolika. Wailesi imeneyi ndi imodzi mwa ma wailesi omwe imatimvetsa kukoma chotcho tsiku lina mukadzafuna kubwera mudzatidziwe kuti tidzakonzekera kuti wailesiyi izipitiliza kuti mvetsa kukoma, anatero mayi Kamwana.
13
Ndime ya vakabu yapita, koma samalani Ena mwa anthu okhala mumzinda wa Mzuzu ati ngakhale bwalo lounika za malamulo oyendetsera dziko lino lidati lamulo la vakabu nlosayenera, apolisi ayenera kukhala tcheru pogwiritsa ntchito malamulo ena owapatsa mphamvu zomanga anthu opanda chilolezo cha bwalo la milandu(warrant of arrest)kuopa zigawenga kutengerapo mpata wozunguza anthu usiku. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Lachiwiri lapitali oweruza milandu atatu: Zione Ntaba, Micheal Mtambo ndi Sylvester Kalembera adalamula kuti gawo 184(1) (c) ya malamulo a dziko lino ngolakwika ndipo sakugwirizana ndi ulamuliro wa demokalase omwe uli mdziko lino. Venda wina wogulitsa majumbo Mayeso Gwanda ndiye adatengera nkhaniyi ku bwaloli mothandizidwa ndi woimira milandu Mandala Mambulasa. Kadadzera: Anthu asadere nkhawa Pomwe Msangulutso udacheza ndi ena mwa anthu okhala mzinda wa Mzuzu, mmodzi mwa anthuwa Chrissy Phiri yemwe amakhala ku Masasa mzindawu adati sadasangalale ndi kuchotsa kwa lamuloli ata kaamba koti zigawenga zipezerapo danga lozunguza anthu maka usiku. Phiri adati zigandanga zambiri zimaenda usiku ndipo ndi lamulo la vakabu, apolisi amatha kuzilonda mpaka kuzigwira. Ndili ndi mantha kuti zigawenga zikhonza kupezerapo mwai pakuchotsa kwa ndimeyi, adatero Phiri. Pomwe Frank Chisale adati vakabu imalakwika poti pena apolisi amanyamula aliyense ndi wosalakwa omwe. Nthawi zina amanyamula ndi opita kumapemphero ausiku omwe, adatero Chisale. Iye adati apolisi amayenera kunyamula okhawo omwe akuganiziridwa kuti ndi zigawenga kapena apalamula mlandu. Koma polankhulapo, mneneri wa ku likulu la polisi ku Lilongwe James Kadadzera adati anthu asadere nkhawa kaamba koti apolisi azikwidzingabe oganiziridwa kuti ndi zigawenga pogwiritsa ntchito malamulo ena. Kadadzera adati izi zithandiza kuchepetsa umbava ndi Umbanda ngakhale achotsa ndime ina ya ya gawo 184(1) ya malamulo yomwe imakamba za vakabu. Iye adati lamuloli lithandiza kutsatira ndi kutsekera mchitokosi oganiziridwawa ngakhale oyenda pansi koma alibe zida sazinjatidwa. Okha okhawo omwe apezeka ndi zida zowopsa ndiwo azikwidzingidwa ndi unyolo mpaka kuimbidwa mlandu poyesetsa kuteteza mzika za dziko lino, adatero Kadadzera. Ndime yachotsedwayi imapatsa mphamvu apolisi kugwira ndi kutsekera mchitokosi munthu aliyense wooneka kuti akhoza kudzetsa chisokonezo kapena ali ndi zolinga zochita zosemphana ndi malamulo kumene kaya ndi mu msewu kapena mmalo ena ndi ena. Bwaloli lidanenetsa kuti ndi kandime kokhaka komwe kali kosayenera ndipo ndime zina zonse mgawo lonselo zikhoza kugwiritsidwa ntchito.
7
Chipulula mu DPP Masankho a ndime ya chipulula (mapulaimale) ayamba ndi moto mchipani cha Democratic Progressive Party (DPP). Lolemba lapitali yemwe adali mkulu wa bungwe la fodya la Tobacco Control Commission (TCC) komanso adakhalako woyanganira nyumba yachifumu ya mtsogoleri wa dziko lino Bruce Munthali, adagwa Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Adazitaya: Munthali chagada kumpoto mboma la Mzimba. Iyeyu amapikisanana ndi Rosemary Mkandawire yemwe adali mkulu wa Toyota Malawi. Pomwe Mkandawire adapeza mavoti 407 pamalo wovotera oyamba a Elunyeni, Munthali adasiyidwa pa mphepo ndi voti yake yokha basi. Apa mpomwe adangozitaya, poona kuti ngakhale apitirire kumalo ena 7 otsalawo saphula kanthu. Munthali adati ngakhale padali zovuta zina zomwe sadafune kuzitchula iye wasankha kuvomereza kulephera. Ndalephea, ndipo ndavomereza kuti ndagwa pamasankho a chipulula. Ndigwira ntchito ndi mnzanga amene wapambanayu popititsa patsogolo mgwirizano mchipani chathu, adalongosola Munthali. Yemwe amayanganira masankhowa Songazaudzu Sajeni adati monga woyendetsa zisankhozo, zomwe zidachitikazo zidawapatsa mphepo. Nafe tidamera tsemwe titaona kuti anthu onse apita pambuyo pa mayi Mkandawire nkuwasiya a Munthali wokha, adalongosola Sajeni. Zisankhozi zidapitilira opanda Munthali ku madera monga Kamwe, Engucwini, Ezondweni, Enukweni, Luzi ndi Kacheche. Nako kumpoto mboma la Karonga, Mungasulwa Mwambande adadutsa wopanda wopikisana naye. Iyeyu amayenera kupikisana ndi yemwe ndi phungu pakadalipano Vincent Ghambi koma adalowa gulu la UTM. Ndipo Lachitatu, mapulaimale adaliko ku Nkhata Bay pomwe ofuna uphungu atatu Vuwa Kaunda kudera la pakati, Happy Chirwa mdera la kummwera komanso Etta Banda kummwera cha kummawa adadutsa popanda opikisana nawo. Mdera la kumpoto cha kumadzulo Julius Chione adagonjetsa David Kaweche, yemwe adakhalapo phungu wa deralo. Mchigawo cha kummwera, zisankho za ndime ya chipululazi ziyamba pa 15 ndi boma la Nsanje. Akadaulo ena koma ati njira yoimika anthu kumbuyo kwa yemwe akumufuna siyabwino chifukwa ena amaimira mantha. Katswiri pankhani za ndale, Nandini Patel adati kavotedweka nkopangitsa ena kuvotera munthu yemwe sakumufuna poopa kunenedwa komanso posangalatsa abale, anansi ndi atsogoleri a zipani. Pomwe Humphrey Mvula adati andale ambiriwa amakopa ovota ndi ndalama. Choncho akaluza, amawakwiyira anthu aja adawadyera aja powakhumudwitsa. Kunena chilungamo, nzowawa kuona munthu alibe aliyense pambuyo pake polingalira nyengo yaitali yomwe imatenga kupanga kampeni, adalongosola motero.
11
Papa Wakhazikitsa Thumba Lapadera Lothandizira Anthu Okhudzidwa Ndi Coronavirus Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisko wakhazikitsa thumba la ndalama zothandiza pa mliri wa Coronavirus. Papa kupemphelera anthu okhudzidwa ndi Coronavirus Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa Francisco wachita izi lolemba ndipo wapereka ku thumbali, ndalama zokwana 750,000 United States Dollars zomwe ndi zokwana 500million kwacha zoti zithandize anthu omwe akuvutika chifukwa cha mliri wa Coronavirus. Polankhula atakhazikitsa thumbali, Papa wapempha akatolika ndi anthu akufuna kwabwino kuti apereke thandizo lawo ku thumbali kudzera ku ma ofesi a mabungwe a Papa mmaiko awo omwe amatchedwa kuti Pontifical Mission Societies (PMS).
6
Maepiskopi Apitirizabe Kudzudzula Boma Mpingo wa katolika mdziko muno wati upitiriza kudzudzula mosakondera, pamene zinthu zisakuyenda bwino mdziko muno. Ena mwa maepiskopi a mpingo wa katolika ku Malawi Wapampando wa bungwe la maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM) Ambuye Thomas Luke Msusa alankhula izi pothilirapo ndemanga pa za kulumbilitsidwa kwa atsogoleri atsopano a dziko lino omwe ndi Dr. Lazarus Chakwera komanso wachiwiri wawo Dr. Saulosi Chilima. Iwo ati ntchito yawo ngati ma episkopi, si yokhala mbali ya boma koma kuthandizana ndi boma pa ntchito za chitukuko cha dziko lino komanso kulankhulapo ngati pena sizikuyenda bwino. Ife tipitiriza ntchito yathu ya upostoli yomwe ndi kulalikira komanso kulankhulira anthu pamene zinthu sizikuyenda bwino kuliwuza boma kuti likonze zimenezo ndipo ife sitisiya komanso sitidzasiya kudzudzula boma. Tipitirizabe kulemba ma pastoral letter ndi kudzudzula, anatero Ambuye Msusa. Mwazina Ambuye Msusa apempha atsogoleriwa kuti alimbikitse mgwirizano pakati pa amalawi komanso kupititsa patsogolo chitukuko cha dziko lino pokwaniritsa malonjezo omwe amapereka mu nyengo yokopa anthu.
14
Dayosizi Ya Mzuzu Yauza Akhristu, Atumiki Adzivala Zodzitetezera ku COVID-19 Dayosizi ya mpingo wa katolika ya Mzuzu yauza akhristu ake kuti adzivala zotchinga kukamwa ndi mphuno pamene akuchita mapemphero osiyanasiyana mmatchalitchi. Walemba kalatayo-Bishop Ryan Episkopi wa dayosiziyo ambuye John Ryan ndi omwe anena izi kudzera mu kalata yomwe alembera ansembe, abulazala komanso asistere, yomwe yatsindika za kuopsa kwa nthenda ya COVID-19. Iwo ati potengera ndi kukwera kwa chiwerengero cha anthu omwe apezeka ndi kachilombo ka Coronavirus mu dayosiziyo, ndi kofunika kuti anthuwa azitsatira njira zoyenera zopewera mliriwu. Malinga ndi kalata yomwe episkopi wa dayosizi ya Mzuzu ambuye JOHN RYAN walembera atumiki onse a dayosiziyo, kuvala kwa mask komwe kukuchitika kwambiri mmadera a matawuni a dayosiziyo kukuyenera kukhale ngati chikhalidwe ndipo kuzichitika mmadera onse kuphatikizapo mmadera omwe ndi a kumudzi. Ntchito yolandira ma sacrament a kulapa komanso ukaristia, akuti zikuyenera zizichitikira panja komanso motsata malamulo onse omwe a zaumoyo akulimbikitsa, ndipo nambala ya anyamata othandizira misa akuti yachepetsedwa. Kalatayi yati ana omwe akupita ku tchalitchi adziperekezedwa ndi akuluakulu komanso anawa asamakhale mmagulu ndi kumasewera kutchalitchiku zomwe zachititsanso kuti ayimitse maphunziro onse a katekisimu wa ana. Espiskopiyu kudzera mu kalatayi wayimitsa zochitika zosiyansiyana mu dayosiziyo. Iye wati kupereka kwa masacrament a ubatizo, ukaristia, ulimbitso komanso ukwati, kuyambe kwayima kaye. Iye wayimitsanso maulendo oyenderana pakati pa matchalitchi ndi maparishi komanso magulu ndi mabungwe onse mu dayosiziyo ndipo wati aliyense ogwira ntchito mu dayosiziyo azikatenga chilorezo ku ofesi ya epskopiyu ngati akufuna kuyenda ulendo wopita kunja kwa dayosiziyo. Mwazina Ambuye Ryan apempha akhristu a mu dayosiziyi kuti azikhala moyo wabwino kuphatikizapo kudya zakudya zabwino, kuchita masewero olimbitsa thupi, kuchepetsa kumwa mowa komanso kukhwimitsa moyo wawo wa uzimu popemphera nthawi ndi nthawi. Ndipo pamapeto pake episkopiyu walangiza atumikiwa kuti aziwonetsetsa kuti akutsatira malangizo onse a pansewu popewa kuyendetsa galimoto mosasamala komanso ataledzera ndipo wati atumikiwa apewenso kuyenda maulendo aatali nthawi ya usiku.
6
Boma Lati Litseka Sukulu Zophwanya Malamulo mu Nyengo ya COVID-19 Unduna wa zamaphunziro wachenjeza eni sukulu zomwe sizaboma kuti zisiye kupitiliza maphunziro, patamveka mphekesera zoti sukulu zina zikugwirabe ntchito zawo zophunzitsa ana mozemba, mkatikati mwa mliri wa nthenda ya COVID-19. Tilanda ziphaso zawo-Susuwele Banda Nduna ya zamaphunziro yomwenso ndi mmodzi mwa mamembala a komiti yapadera yowona za matendawa mdziko muno Dr. William Susuwele Banda, ndi omwe anena izi paulendo omwe anayendera chipatala cha Ntcheu ndi cholinga chofuna kukaona momwe chipatalachi chikukonzekelera polimbana ndi nthendayi. Ndunayi yati sukulu zopezeka zikuchita izi zilandira chilango cholandidwa ziphaso zawo zoyendetsera bizineziyi. Tamva kuti sukulu zina zikupitilira kuphunzitsa ana mozemba ndiye ife sitilimbana nawo kwambiri. Chimene tichite tingowalanda chiphaso chawo ndipo sadzatsegulanso sukulu zawozo, anatero Dr. Banda. Polankhulapo pa nkhani yokonzekera kulimbana ndi nthenda ya COVID-19, mkulu wa pachipatala cha Ntcheu Dr. Isaac Mbingwani wati iwo ayika ndondomeko zoyenera kuti athane ndi nthendayi. Padakalipano boma lati lidakalingalirabe momwe lingathandizire mzika za dziko lino zomwe zili mdziko la South Africa omwe akuti akufuna kubwera mdziko muno kamba ka mavuto omwe akukumana nawo mdzikomo.
6
Dziwani za matenda a mphere Kutsatira malipoti a kubuka kwa matenda a mphere kuchigwa cha mtsinje wa Shire, uyu ndi tsatanetsatane wa matendawa kuchokera pa zomwe bungwe loona za umoyo padziko lapansi la World Health Organization lidapeza. Matenda a mphere amakhudza khungu la munthu ndipo amayambika ndi kachilombo kakangono kamene kamapezeka muchakudya. Mchingerezi, Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC kachilomboka kamatchedwa mite ndipo asayansi amakatcha Sarcoptes scabiei. Kachilomboka sikaoneka chifukwa ndi kakangono kwambiri. Kakalowa pakhungu la munthu, amakanda mosalekeza. Malinga ndi World Health Organization, matenda a mphere amati ndi okhudzana ndi madzi. Ndi zosadabwitsa kuti lero tikukamba za mphere zomwe zafala kuchigwa cha mtsinje wa Shire komwenso madzi aononga katundu ndi kugwetsa nyumba. Matendawa amafala ngati kachilomboko kapita pakhungu la munthu wina koma amafala kwambiri pamene munthu amene wakhudzidwa ndi matendawa wakhudzana ndi mnzake monga pogonana mosadziteteza. Matendawa amafala kwambiri moti mu 2010 anthu oposera 100 miliyoni padziko lapansi ndiwo adakhudzidwa ndi matendawa. Matendawa mungawadziwe msanga chifukwa pamene akuyamba umangokanda mosalekeza ndipo khungu limatha kusupuka. Zizindikiro zokhala ngati walumidwa ndi udzudzu zimaoneka. Kukandaku kumafika palekaleka usiku pamene ukugona. Kuyabwakutu kumachitika chifukwa tizilombo tija timakhala tikuyendayenda mthupimo. Matendawa amafalanso posinthana zovala, zopukutira mukasamba, zofunda. Koma matendawa angathe kukhala pathupi la munthu kwa masiku atatu osapatsira munthu. Kugwiritsira ntchito mankhwala monga permethrin kapena ivemectin kumachepetsa kufala kwa matendawa koma mpaka lero palibe mankhwala amene amachiza matendawa. Kukhala munthu wa ukhondo kungathandize kuti usadwale matendawa. Izi ndi zomwe achipatala amalimbikitsa kuti muyenera kumasamba, zovala zizikhala zochapa ndipo malo ogona akhale okonzedwa bwino.
6
Zokhudza mikangano ya ufumu Nkhani za ufumu zakhala zikuvuta kwa nthawi yaitali. Zina mwa nkhani zomwe zakhala zikupanga mitu ndi mikangano ya ufumu komanso pakati apo kudabuka ganizo loti mmatauni musamakhale mafumu STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi Gulupu Santhe imodzi mwa mafumu akale. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndikudziweni mfumu. Santhe: Makhoti asamalowererepo Ndine Aclas Chisoni koma la ufumu ndine nyakwawa Santhe wa mdera la T/A Kalolo ku Lilongwe. Tiziti a Santhe ake ndi a ku Kasunguwa? Chibale chilipo koma chakumizu. A ku Kasungu ndi a mbere la a Nkhoma pomwe ife a kuLilongwe ndife a mbere la a Mwale. Ufumu mudaulowa liti? Ndidalowa ufumu mchaka cha 1985 achimwene anga a Wilson Pwela omwe adali afumu atamwalira mchaka cha 1983. Panopa ndikutha zaka 21 ndili mfumu ndipo chaka chino ndikuyembekeza kukwenzedwa kufika pa Senior Group Santhe. Pa zaka zonsezi mwakhala mfumu, ndi mavuto anji omwe mungatiuze kuti amapezeka mu ufumu? Mavuto alipo ambiri osayiwala mikangano. Maufumu ambiri amatchuka ndi mikangano makamaka yemwe adali nfumu akamwalira ndiye kuti wina alowepo. Nthawi zina mpaka pamalowa za mankhwala kulimbirana ufumu. Vuto lina ndilakuti adani amachuluka chifukwa ukangoweruza mlandu, yemwe sizidamukomere basi chidani chimayamba pomwepo. Ndiye pakatipo kudabuka zoti maufumu a mtauni athe, maganizo anu ngotani? Sizowona ayi mafumu ndiwofunikabe paliponse. Chitukuko kuti chiyende ndi mafumu, pakagwa zovuta mafumu ndiwo amaongolera zonse. Palibe kanthu kuti ndi mtauni kapena kumudzi koma pomwe pali anthu pamayenera utsogoleri. Makhansala sangagwire ntchito ya mafumu? Inu tiyeni tiziganiza mozama. Mfumu amasankha munthu okhwima maganizo odziwa ndi kutsata mwambo ndi chikhalidwe tsono makhansala ambiri amasankhidwa kaamba ka maphunziro kapena kutha kulankhula basi. Utsogoleri wa ufumu sachita kampeni ayi anthu okha amaona kuti uyu atithandiza. Nanga nkhani za ufumu kupititsa mukhoti? Ukunso nkusokoneza chifukwa nkhani ya ufumu imayenera kukambidwa kumudzi apo ayi kwa DC ndipo zikavutitsitsa ku unduna wa zamaboma angonoangono ngati kholo la maufumu.
8
Lidali tsiku la Big Sunday Sangwani Mwafulirwa tsopano ndi bambo, si mnyamatanso monga ena akumudziwira chifukwa dzulo pa 4 June 2016 wamulonjeza Trufena Chiwaya, mwana wa mmudzi mwa Muleso kwa Senior Chief Somba mboma la Blantyre kuti sadzamusiya mpaka imfa. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Sangwani ndi mneneri wa bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission pamene Trufena akugwira ku Western University of Malawi. Kukwaya ya mpingo wa Living Waters ku Ndirande ndiko kudayambira kukumana kwa awiriwa. Sangwani, yemwe kwawo ndi ku Ndirande mumzinda wa Blantyre, akuti panthawiyo iye adalibe khumbo lothira Chichewa namwaliyu. Amangondisangalatsa khalidwe lake. Zachibwana ayi, zibwenzi ayi, nthawi zonse chidwi ndi Mulungu wake. Izi zidandipatsa chidwi, adatero mneneriyu. Sangwani ndi Trufena pano ndi thupi limodzi Ndimadziwa kuti makolo anga akwiya akamva zoti ndapanga chibwenzi, komanso ndimafuna ndikafike ku University, adaonjeza Sangwani. Nthawi idakwana kuti awiriwa asiye kucheza zamapemphero zokhazokha. Ngakhale Sangwani adalibe maganizo, komabe Mulungu adazikonza. Zonse zidayambika pamene mayi ake a Trufena adamwalira ku Ndirande, zomwe zidachititsa namwaliyu kuti abwerere kwawo kwa che Somba. Kuiwalana ndi Sangwani kudali komweko. Patatha masiku ndidayamba kumukumbukira. Kodi moyo wake uli bwanji? Kodi akulimbikirabe kupemphera? Khumbo lomuyendera lidalipo koma padalibe amene amadziwa komwe ankakhala, adatero Sangwani. Koma tsiku lidakwana kuti akumanenso. Uku tsopano kudali ku Big Sunday yomwe idachitikira ku Living Waters Church ku Chimwankhunda mumzinda wa Blantyre. Kumeneko ndiye kudali kufunsana zambiri ndipo Sangwani adadziwa komwe namwaliyu akukhala. Pakutha pa masiku angapo, Sangwani adakwawira kwa che Somba. Mofunsira njira, iye adakwanitsa kukakumana ndi namwaliyu. Apo padali pa 8 July 2001. Ndinenetse kuti ndinalibe maganizo ofunsira koma kukangomuona. Tikucheza, nkhani zidandithera, kenaka ndidatulutsa mawu achikondi, adatero Sangwani. Naye Trufena adati: Ndinadabwa akundiuza zachibwenzi. Ndinali ndisanapangepo chibwenzi, padalibenso zoganiza koma kumuyankha pomwepo kuti zimenezo sindimapanga. Adandikakamira ndipo ine ndinayamba kudabwa naye. Kenako maganizo adandifikira kuti ngati munthuyu wayenda mtunda wautali ndiye kuti watsimikiza. Moyo wanga udavomera, ndidamulola.
13
Koche Parishi Ilonjeza Kusamalira Ansembe Awo Atsopano Wolemba: Thokozani Chapola Akhristu a mpingo wakatolika ku parishi ya St. Magadalena wa Kanosa ku Koche mu dayosizi ya Mangochi alonjeza kuti adzipereka pothandiza amsembe atsopano omwe mpingo wakatolika mu dayosizi-yo waatumiza kuti adzitumikira mparishi-yo. Malingana ndi Montfort Mwale yemwe ndi mtolankhani wa dayosizi-yi, amsembe omwe awatumiza kuti adzitumikira mu parishi ya St. Magadalena wa Kanosa ku Koche mu dayosizi-yi ndi bambo Paul Rappozo, komanso bambo Medrick Mlava. Polankhula pa mwambo wolandira a msembe-wa wapampando wa parishi-yi a Bruno Chakhaza ati mpingo mu parishi-yo ndi wokondwa ndikufika kwa amsembe atsopano-wo. A Chakhadza ati ali ndi chikhulupiliro chakuti amsembe atsopano-wa athandiza pa ntchito zokweza mpingou mu njira zosiyanasiyana. Mmawu awo a bambo mfumu a parishi-yi bambo Clemence Pindulani athokoza akhristu a mparishi-yo kamba kolandira bwino amsembe-wa. Polankhula mmodzi mwa amsembe atsopano ku parishi-yi bambo Paul Rappozo ati ndi okhutira ndi momwe mpingo wakatolika wawalandilira mu parishi-yo.
13
Kupherera ngamba ndi Akalozera mmunda Alangizi a zaulimi apempha alimi mdziko muno kuti azipanga akalozera kuti ateteze nthaka, komanso kusunga chinyontho kwa nthawi yaitali mminda yawo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Madalitso Munthali, mlangizi wa mbewu ku Kaporo mboma la Karonga, wauza Uchikumbe kuti mavuto odza ndi kusintha kwa nyengo atha kuchepa alimi ambiri atayamba kupanga akalozera mminda mwawo. Mlangiziyu adati akalozera amathandiza alimi kukolola madzi a mvula, komanso kuteteza nthaka kuti isakokololoke mmunda mwawo. Alimi kupanga akalozera pogwiritsa ntchito chingwe Akalozera ndi muuni wa kayendedwe ka madzi mmunda ndipo alimi amayenera kuunga mizere. Umu ndi momwe mumalimidwa milambala, yoongoledwa bwino, yomwe imachengeta nthaka podekhetsa madzi mmizere. Kulima mwa chisawawa, opanda akalozera, zikuchititsa kuti nthaka izikokoloka ndi madzi a mvula. Zotsatira zake ndi njala chifukwa chajira chikukokoloka kusiya minda yoguga ndipo mbewu zikumauma posowa chinyezi popeza madzi amangothamangira ku mitsinje, adatero Munthali. Katswiriyu adalangiza alimi kupeza thandizo la alangizi a mmadera mwawo popanga akalozera. Osangokhala kumadikira mvula igwe mu October kapena November. Pakadalipano, mlimi wotsogola akupanga akalozera, manyowa ndi galauza, iye adatero. Mlangizi wina wa ku Chingale EPA mboma la Zomba, Limbani Thangata, akuti nthaka ndi yofunika kwambiri pa ulimi choncho iyenera kutetezedwa. Alimi asaiwale kuti kusintha kwa nyengo kukusokoneza ntchito yathu choncho tiyenera kupanga akalozera mmunda mwawo. Dongosololi limathandiza kusamalira chajira poimitsa madzi nkusunga chinyezi kwa nthawi yaitali chothandiza mbewu kuchita bwino ngakhale mvula idule, adatero Thangata. Mkuluyu adati kupanga akalozera ndi njira imodzi yothana ndi ngamba kaamba koti madzi samathamanga ndipo akhala ndi nthawi yolowa pansi mmunda makamaka alimi akapanga maswale, ulimi wa mmaenje, phimbira ndi ngonyeka (box ridges). Popanga akalozera, Thangata adati pamafunika anthu atatu, chingwe chotalika mamita 5, mitengo (ndodo) iwiri yoongoka bwino nkutalika mamita 1.6 mpaka 2.0, chikwanje, zikhomo, hamala ndi levuloija amagwiritsa ntchito amisili pomanga nyumba. Adafotokoza kachitidwe kake motere: Anthu awiri amaima ndi ndodo zomangidwa chigwecho ndipo mmodzi amakhala pakati ndi levulo ija kuyeza. Pomwe timadzi mu levuloyo tabwera pakatikati, wa kumapeto amakhoma chikhomo ndi kusunthira komwe kuli ndime. Amatero mpaka kumaliza munda wonse. Malingana ndi kutsika kwa malo, akalozera amatalikirana mamita 5 kapena 10. Umu ndi momwe timaungamo milambala ija. Mmodzi mwa alimi mminda mwawo muli akalozera mmudzi mwa Giliya kwa mfumu Mwaulambo mboma la Karonga, Jimmy Mwakila ndi mmodzi mwa alimi womwe amapanga akalozera munda mwake. Mwakila, wa mmudzi mwa Giliya mdera la mfumu Mwaulambo ku Karonga, adati dongosololi lamuthandiza kuti azikolola dzinthu zambiri.
4
Ziphuphu mkalembera Pamene kalembera wa unzika za dziko lino ali mkati, zadziwika kuti anthu ena apeza mpata wosolola mmatumba mwa Amalawi omwe akutenga nawo gawo lolembetsa mukalemberayu. Amalawi ena akumafunsidwa kupereka K500 kapena kuposera apo kuti apeze mwai wa fomu yolembapo mbiri yawo. Izi zikumachitika makamaka pamalo akalemberayu pakakhala khwimbi la anthu omwe akumauzidwa kuti mafomu atha ndipo apereke kangachepe kuti ziwayendere. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mwachitsanzo, Lachiwiri lapitali apolisi mboma la Dowa adatsekera ofesala wa bungwe lomwe likuyendetsa kalemberayu la National Registration Bureau(NRB) yemwe amayanganira ntchitoyu pa malo akalembera a Chuzu, kwa Traditional Authority(T/A) Nkukula mbomalo pomuganizira kuti amalandira ziphuphu. Ena mwa anthu omwe amalembetsa pamalopa amauzidwa kuti mafomuwa atha ndipo apitenso tsiku lotsatira ndi K500, ndipo mafomuwa akumatulukadi. T/A Nkukula adavomereza kuti apolisi atsekeranso munthu wina yemwe adapita pa malo a Chuzu ndi kutenga mafomu atatu ponena kuti ena ndi a abale ake kunyumba koma amatsatsa mafomuwo pa mtengo wa K500. Komanso masiku apitawo chifukwa cha mitambo makina a kalemberayu adalibe moto choncho anthu ena adasonkha ma K200 nkukagula maunitsi a magetsi omwe adatchajira makinawa kuti zinthu ziyende, adatero Nkukula. Komatu si ku Dowa kokha chifukwa nako ku Dedza ziphuphu zikuperekedwa kuti anthu ena apeze mwai olembetsa nawo mkalemberayu. Malinga ndi mzimai wina wochokera pa malo a kalembera a Katsekaminga yemwe adapempha kuti tisamutchule dzina lake, adapereka K500 kwa mfumu ina mderali kuti apeze mwai wa fomu yolembapo mbiri yake. Polankhulapo T/A Kamenyagwaza wa mboma la Dedza adati ngakhale kalemberayu wayenda bwino mmalo ena, vuto lalikulu lili pamalo a kalembera a Bembeke pomwe anthu akuvutika kuti apeze mafomu. Anthu ozungulira pa Bembeke akumauzidwa kuti mafomu atha ndipo akumakapempha pamalo ena a Liberito komwe mphekesera yandipeza yoti akumawatchaja kangachepe, adatero Kamenyagwaza. Ndipo mneneri wa bungwe loyanganira kalemberayu Norman Fulatira adavomereza zoti bungweli lalandira madandaulo a ziphuphu mmalo ena. Tikupempha Amalawi akufuna kwabwino kuti azititsina khutu za mchitidwewu ndipo ife mogwirizana ndi apolisi tidzachita kafukufuku, adatero Fulatira. Iye adatsimikizanso za kutsekeredwa kwa ofesala wawo wa pamalo a kalembera a Chuzu. Ntchito ya kalembera wa unzika idayamba mwezi wa May ndi cholinga chofuna kuti mwazina nzika za maiko ena zisamalandire nawo thandizo lopita kwa Amalawi monga mzipatala zomwe zili mmalire a dziko lino ndi maiko ena.
11
Chilima Wati Mafuta a Galimoto Akuyenera Atsikebe Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Dr. Saulos Chilima wati kutsika kwa mitengo ya mafuta a galimoto komwe kwachitika kawiri konse mdziko muno ndi kosakwanira poyerekeza ndi mmene zinthu zilili pakadali pano. Chilima: Musagulitse mafuta pa mtengo wokwera Dr. Chilima omwe akuyima ngati wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha MCP, Dr. Lazarus Chakwera pansi pa Tonse Alliance pa chisankho chomwe chikudzachi amalankhula izi loweruka pa msonkhano okopa anthu omwe unachitikira pa bwalo la zamasewero la Kasungu Community. Iye wati akudziwa kuti boma likupeleka ma contract kwa anthu osavomerezeka kuti azibweretsa mafutawa mdziko muno kuti phindu lina lizipita ku chipani cha DPP ndipo wati izi zikuyenera kutha kuti mitengo ya mafutayi itsikebe. Musagulitse mafuta pa mtengo odula, mutsitsebe anthu azisangalala chifukwa mukupatsana macontract ndi anthu amuchipata kuti akupatseni 4 million dollars kuti mupangire campaign, anatero Chilima. Pamenepa Dr. Chilima alimbikitsa anthu kuti akavotere mgwirizanowu pachisankhochi kuti miyoyo yawo isinthe kumbali ya ulimi, ntchito za umoyo, za maphunziro, mwayi wa ma business ndi ntchito.
2
Ndewu ya gule kudambwe Kudali fumbi koboo! Kudambwe la Phingo mboma la Chikwawa pamene gulewamkulu adaponyerana zibakera pokanganirana zovala zovinira. Mneneri wapolisi ya Chikwawa Foster Benjamin, gule wina adavulazidwa pamene adamutema pamutu ndi botolo ndipo adamutengera kuchipatala kuti akamusoke. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kudavuta ku Chikwawa, gulewamkulu kutola mwala Izitu zimachitika mmawa cha mma 7 Lamulungu pamene guleyu amafuna avale kuti atakase kudambweko. Benjamin adati kudambweko kudasonkhana anthu amene amafuna kuvala gulewamkulu. Mnyamata wina, Innocent Tayi akuti adapitako koma alibe zovinira. Izi zidachititsa kuti iye apemphe mnzake, Colless Tiwa kuti amubwereke zovala zake koma adakanizidwa. Tayi adakakamira mpaka ndewu idabuka pakati pa iye ndi Tiwa, adatero Benjamin. Podziwa kuti avulazidwa, Tayi, 17, adatola botolo lagalasi ndi kumenyera nalo Tiwa pamutu mpaka kutemeka. Malinga ndi Benjamin, anthu ammudzi ndiwo adathamangira kudambweko kukaleletsa ndewuyo. Dambwelo lili pafupi ndi mudzi ndiye pamene anthuwo amamva kulira adathamangirako kuti akaone chimene chimachitika. Kenaka adagwira Tiwa kubwera naye kupolisi komwe tidamutsekera Lamulungu pamlandu wovulaza komanso tidamutengera kuchipatala Tayi, adatero. Tiwa adamutsegulira mlandu wovulaza. Koma Lachiwiri Tayi atatulutsidwa kuchipatala, adapita kupolisiko kukathetsa mlandu. Paramount Lundu ya mbomalo yati izi zimachitika kuti anthu pena amasemphana Chichewa. Nanga pali nkhani pamenepo? Inu simusemphana ndi anzanu? idafunsa mfumuyo. Titafunsa ngati mbomali muli gulewamkulu, Lundu adati Chikwawa ndi kuchimake kwa gulewamkulu. Inu simudziwa kuti kuno ndi kwawo kwa gulewamkulu? Simukudziwa kuti mchaka cha 1969 Kamuzu Banda adadzafika kuno komwe ndi kudambwe langa? Kuno tili ndi gulewamkulu, adatero Lundu amene adati kudambweko aliyense amakhala ndi zovala zake. Koma mkulu wa bungwe la Achewa la Chewa Heritage Foundation (Chefo) George Kanyama Phiri adati zimene wapanga gulewamkulu ku Chikwawa ndi chisonyezo kuti amenewo si ometa. Tikamakamba za gulewamkulu timanena za chigawo chapakati ndi ku Blantyre pangono koma osati ku Chikwawa, adatero Kanyama. Komanso muyenera kudziwa kuti gulewamkulu ndi mizimu ndipo imachokera kumanda. Sibwino kusambira gulewamkulu. Masiku apitawa, gulewamkulu amavutitsa ku Mchesi mumzinda wa Lilongwe pamene amagenda galimoto ngati samupatsa ndalama.
15
Msika wa fodya wa okushoni ukuponderezedwa Kampani yoyendetsa malonda a fodya pamsika wa okoshoni ya AHL Group yauza alimi kuti akhale tcheru pogulitsa fodya wawo pa mgwirizano ati kaamba koti cholinga cha ogula fodyawa chokola alimi muukonde wa mgwirizano kuti mtsogolumu alimiwa adzakhale opanda liwu pafodya wawo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mkulu wa zamalonda kukampaniyi Moses Yakobe adauza alimi a fodya ku Lufita, mboma la Chitipa Lachiwiri kuti cholinga cha kampani zogula fodya nkuthetsa msika wa okushoni poika alimi onse pa mgwirizano. Msika wa fodya wa okushoni Tikasiyanitsa Malawi ndi maiko oyandikana nawo monga Mozambique komwe kulibe okushoni, alimi kumeneko akuvutika chifukwa ogula fodya ndi womwe ali ndi ulamuliro onse; osati olima fodya, Yakobe adatero. Iye adati izi zaonekera pamsika wa fodya wa bale chaka chino pomwe alimi omwe adatenga ngongole kukampani zogula adagulidwa pamtengo wabwino wa $1.79 (pafupifupi K700). Yakobe adati alimi omwe adali pa mgwirizano koma sadatenge ngongole adagulitsa pamtengo wa $1.64 ndipo zidavutiratu pa okushoni pomwe fodya adagulidwa pa mtengo wotsikitsitsa wa $1.46. Polongosola ogulawo adati alimi omwe adatenga ngongole adagulidwa fodya wawo pamtengo wokwererapo kuti apereke ngongole msanga. Apa chidakula ndikukondera popeza alimi enawanso adakatenga ngongole paokha ena adafufuza ndalama paokha. Koma pano akugulitsa fodya wawo pamtengo wotsika zedi chifukwa choti sadatenge ngongole ku kampani zogula fodya, Yakobe adatero. Izi zili chonchi, mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Alfred Kapichira-Banda wapempha boma kuti lithetse chilinganizochi chimene chidayamba mu 2012.
2
DPP yasankha atsogoleri atsopano Msonkhano wa masiku atatu wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) womwe umachitikira mu mzinda wa Blantyre wasankha mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti ndiye adzatsogoleri chipanicho pa zisankho zapatatu za chaka cha mawa. Wachiwiri kwa Mutharika mchigawo chakumpoto ndi Goodall Gondwe, chapakati ndi Uladi Mussa, chakummawa Bright Msaka pamene Kondwani Nankhumwa wa mchigawo chakummwera. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mutharika, Gondwe ndi Msaka adasankhidwa opanda opikitsana nawo pamene Mussa adagwetsa Dean Josaya Banda, Zelia Chakale, Hetherwick Ntaba ndi Samuel Tembenu pamene Nankhumwa adasosola nthenga Joseph Mwanamvekha ndi Henry Mussa. Mlembi wamkulu wa chipanichi ndi Greselder Jeffrey, mneneri ndi Nicholas Dausi, msungichuma Jappie Mhango, mkulu wokopa anthu Everton Chimulirenji, wa zochitikachitika Symon Vuwa Kaunda, woona za chuma Ralph Jooma, wa za malamulo Charles Mhango, woona za amayi Cecilia Chazama ndipo mkulu wa zokonzakonza ndi Chimwemwe Chipungu.
11
CCJP Yalimbikitsa Alimi Kugwiritsa Ntchito Manyowa Bungwe la chilungamo ndi mtendere mu mpingo wa katolika la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) mu akidayosizi ya Blantyre lati ulimu wogwiritsa nthito manyowa uli ndi kuthekela kobwezeretsa chonde mu nthaka ngati alimi atatsatira ndondomeko zoyenera pogwiritsa ntchito mayowa-wa. Mayi Chasowa kuphunzitsa alangizi Bungweli lanena izi mboma la Thyolo lolemba pa 24 February 2020, pambuyo pa maphunziro a alangizi a ulimu a bungweli mbomali wowunikira purojekiti ya bungweli yolimbikitsa alimi kugwiritsa ntchito mayowa komanso yowazindikilitsa zokhuza ufulu wawo pa nkhani za malo. Mau ake modzi mwa akulu akulu a bungweli ku akidiosizi ya Blantyre, a Joseph Kampango anati kupatulapo kuti manyowa ndi osavuta kupeza komanso safuna upangili ozama, komabe ndikofunika kuti anthu ayambe kuzindikila ndi kugwilitsa mayowa chifukwa iwo ali ndi umboni ngati bungwe pa ubwino wa manyowa. Kupatulapo kukolora zokolora zokwana ngati alimi akugwiritsa ntchito manyowa, kugwilitsa ntchito manyowa kuli ndi kuthekela kobwezeletsa chonde mu nthaka kusiyana ndi feteleza, anatero a Kampango. Alangizi a zaulimi a bungwe la CCJP mboma la Thyolo omwe anachita maphunzirowo A Kampango anapitiliza kunena kuti purojekitiyi yakwanitsa kupeza njira zina zopangira mayowa monga manyowa amadzi omwenso ndiosavuta kunyamula komanso kuthila mminda. Alimi amenenso akugwitsa ntchito mayowa amadziwa minda mwawo muli mmela wazaoneni, anawonjedzela motero a Kampango. Mmau ake modzi mwa alangidzi azaulimi wa boma mboma la Thyolo a Esinta Chasowa anati kutsatira kuti nthaka inaguga ndi china chimene chikupangisa kuti anthu azikhala ndi zokola zochepa chomcho alimi akuyenela kuzalanso mbeyu zomwe zimabwezeletsa chonde munthaka komanso azikolora zokolora zokwana. Mbewu ngati za guru la nyemba zimakwanitsa kubweretsa chonde mu nthaka, anatero a Chasowa. A Chasowa anapitiliza kunena kuti kuphuzitsa alimi njira zowathandiza kukolora chakudya chambiri sizikukukwanira opanda kuwaphuzitsanso momwe angasamalire chakudyacho. Alimi akhoza kukolora zambiri koma ngati saphunzitsidwa momwe angasamalire zokolorazi, zonse zili chabe chifukwa kuononga chakudya kumayambira ngakhale pokolora mpaka pakhomo, analankhula motero a Chasowa. Pothilirapo ndemanga, mmodzi mwa mlangizi wa alimi wa bungweli amene anatenga nawo gawo pa maphuzirowa a Joyce Gatoma anayamikira bungwe la CCJP kamba ka maphuzirowa ponena kuti awathandiza kuzindikira njira zina zotsogola zopangila manyowa komanso kasamalidwe ka chakudya. A Gatoma anapempha mabungwe omwe akukhuzidwa pophuzitsa alimi kuti agwirane manja kuti aziphunzitsa alimi zofanana. Ndizovuta kuti munthu usatilere ziti chifukwa mabungwewa amabwela ndizosiyana choncho ndikoyenela kuti mabungwe agwilane manja potiphunzitsa chimodzi kuti nafe tizikaphunzitsa zolondora kwa alimi, anadandaula motero a Gatoma Bungwe la CCJP likugwira ntchitoyi mboma la Thyolo kwa ma T/A asanu ndi modzi omwe ndi Ngolongoliwa, Nanseta, Bvumbwe, Chimaliro, Kapichi ndi Nchiramwela.
4
CMO ya Blantyre Ikhutira Ndi Ntchito Zake Zomwe Zagwiridwa Chaka cha 2019 Bungwe la Umodzi wa a bambo la Catholic Men Association mu arkdayosizi ya Blantyre lati ndilokhutira momwe lagwilira ntchito zake mchaka ichi cha 2019. Abambo a Mwanza parishi kujambulitsa limodzi ndi abambo a ku Nthawira parishi A Martin Chiwaya omwe ndi wapampando wa bungweli mu arkdayosizi ya Blantyre ndiwo alankhula izi kwa mtolankhani wathu yemwe amafuna kudziwa momwe bungweli lagwilira ntchito zake pomwe chakachi chikupita kumapeto A Chiwaya ati chakachi chakhala chopambana pomwe bungweli lakwanitsa kukhazikitsa mabungwe oterewa ku maparish osiyanasiyana a mu arkdayosiziyi zomwe anati akwanitsa kufikira maparish ochuluka opezeka mu arkdayosiziyi. Ndinene pano kuti chaka cha 2019 pomwe chikupita kumapeto ndine okondwa kulengeza kuti tafikira maparish ambiri ndipo mwa maparish 43 opezeka mu arkidayosiziyi tsopano tafikira maparish 35 ndipo tatsala ndi maparish asanu ndi atatu (8) omwe mchaka chatsopano cha 2020 tifikakonso kukakhazikitsa bungweli anatero a Chiwaya 5.jpg 300w, https://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/12/IMG-20191203-WA0019-1024x768.jpg 1024w, https://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/12/IMG-20191203-WA0019-768x576.jpg 768w, https://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/12/IMG-20191203-WA0019.jpg 1080w" sizes="(max-width: 479px) 100vw, 479px" />Nduna ya za mdziko a Nicholas Dausi alowa nawo mu bungweli mchakachi Iwo atinso mchakachi akhala ndi mwayi wosonkhana pamodzi abambo okhaokha amu arkdayosiziyi ndikukondwelera limodzi chaka cha nkhoswe yawo Yosefe mwamuna wake wa Maria pamwambo wa nsembe ya ukaristia womwe unachitikira ku Limbe Cathedral ndipo unatsogoleredwa ndi Ambuye arkepiskopi Thomas Luke Msusa womwe abambowa anatsogolera okha pachipembedzo monga kuyimba nyimbo, kuvinira komanso kuthandizira misa. A Chiwaya apitilizanso kuti akhalanso ndi mwayi wopanga maubale ndi mabungwe oterewa a madayosezi ena monga Zomba komanso arkdayosizi ya Lilongwe Tapanga ubale ndi abambo anzathu aku Lilongwe omwe anakhala nafe pamisa ya pa 1 May ndipo pa 15 December, 2019 tinali ku Zomba komwenso tinatsogolera mayimbidwe pamwambo wokhazikitsa bungwe lotereli ku parish ya Holy Trinity Matawale ndipo ndife okonzeka kupitanso ku madayosezi monga Chikwawa ndi Mangochi ngati angatiyitane anapitiliza a Chiwaya. Mchaka cha 2020 bungweli lipitilizanso ntchito yokhazikitsa mabungwe otere ku maparish 8 otsala komanso kukhazikitsa makomiti abungweli mma deanery onse osayiwalanso komiti yokhazikika ya pa dayosizi. Ndipo pali chikonzero choti bungweli lizakhazikitsidwa kwenikweni mu dayoseziyi mu mwezi wa October 2020.
13
Anthu 6.9 miliyoni alembetsa mavoti Zotsatira za kalembera wa mavoti zomwe bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) latulutsa zasonyeza kuti anthu 6 856 295 ndiwo alembetsa mdziko lonse kuti adzaponye nawo voti chaka cha mawa. Bungwe la MEC limayembekezera kulemba anthu 8 510 625 mmaboma onse mmagawo onse 8 koma chifukwa cha zovuta zina zomwe bungweli limakumana nazo mkati mwa ndime, anthu 1 654 330 sadalembetse. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Pachisankho cha 2014, anthu 7 520 816 ndiwo adalembetsa mkaundula kutanthauza kuti odzavota pachisankho cha ulendo uno akuchepera ndi anthu 664 521 kwa omwe adalembetsa kuti akavote mu 2014. Koma mneneri wa MEC Sangwani Mwafulirwa wanenetsa kuti chiwerengerochi chikhoza kusintha bungwe la MEC likayamba ntchito ya kalondolondo wa kalembera mmalo onse omwe anthu amalembetserako. Izi nzotsatira zomwe zili mkaundula potengera mapeto a kalembera koma tiyamba ntchito ya kauni. Mkauni, ena amapezeka kuti adalembetsa kawiri pa zolinga zawo ndiye mayina otero timachotsa kumodzi nkusiya kumodzi choncho anthu asadzadabwe kudzamva kuti ma figala asintha, watero Mwafulirwa. Mwa anthu omwe alembetsawa, 3 045 766 ndi abambo pomwe 3 810 625 ndi amayi ndipo Lilongwe ndiyo yalembetsa anthu ambiri 1 013 414 pomwe Likoma ndilo chimtseka khomo ndi anthu 6 946. Zina mwa zovuta zomwe bungwe la MEC lidakumana nazo mkati mwa kalembera ndi kuonongeka kwa makina opangira kalembera, kuvuta kwa mphamvu ya magetsi yoyatsira makina ndikunyanyala ntchito kwa ochita kalembera pofuna malipiro makamaka kumayambiriro. Mabungwe komanso zipani zotsutsa boma zidapereka nkhawa zawo ku bungwe la MEC zokhudza kutsika kwa chiwerengero cha anthu olembetsa ndipo adapempha kuti ngati nkotheka, kalembera akuyenera kudzabwerezedwa mmadera ena omwe zidanyanya. Zotsatira za kalembera sizikukhala zabwino koma si vuto la anthu chifukwa akupita mmalo molembetsera koma akubwerera. Bungwe la MEC likuyenera kuchitapo kanthu kuti kalembera adzabwerezedwe, adatero mneneri wa Malawi Congress Party (MCP) Reverend Maurice Munthali. Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu la Centyre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) Timothy Mtambo adati kupanda kupereka mpata wina wa kalembera nkuphwanya ufulu wa anthu. Mawu a Mtambo akutanthauza kuti ufulu wodzaponya voti wa anthu 1 654 330 omwe sadalembetse waphwanyidwa ndipo akuyenera kupatsidwa mpata wolembetsa kuti nawo adzakhale ndi danga loponya voti. Kalembera wa mkaundulayu ndi gawo limodzi la zokonzekera chisankho cha 2019 koma bungwe la MEC silidabwere poyera nkunena ngati liganizire pempho lobwereza kalembera kapena ayi potsatira pempho la mabungwe ndi zipani.
11