Text
stringlengths
292
6.6k
labels
int64
0
19
Amayi Okhudzidwa Akuyembekezeka Kuchita Ziwonetsero Poteteza Ansah By Thokozani Chapola Amayi omwe akuti ndi okudzidwa ndi ziwonetsero zokakamiza wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) mayi Jane Ansah kuti atule pansi udindo wake, alengeza kuti achita ziwonetsero mu mzinda wa Blantyre mawa lino. White kulira pa msonkhano wa atolankhani pomwe amalengeza za ziwonetserozi Iwo alengeza izi pa msonkhano wa atolankhani womwe anachititsa lolemba mu mzinda wa Blantyre. Mmodzi mwa amayiwa yemwenso ndi wapampando wa bungwe lomwe akulitcha Concerned Women a Seodi White wati ndi zokhumudwitsa kuti mayi Jane Ansah akutonzedwa ndi kunyazitsidwa mu njira zosiyanasiyana kaamba koti anali wapampando wa bungwe lomwe limayendetsa chisankho chapatatu. Iye wati akukhulupilira kuti anthu akuchita izi powona kuti mayi Ansah ndi munthu wamayi. Kuyenda kumeneku tikufuna kusonyeza kuti ife tili pambuyo pa mayi Ansah. Chisankho cha 2014 munthu mpaka anafa koma anthu sanapange ziwonetsero chifukwa anali munthu wammuna pano ndiye palibe munthu amene wafapo pa chisankhochi koma ena akupanga ziwonetsero. Ife tikuwona kuti anthu akupanga zimenezi chifukwa ndi mzimayi, anatero mayi White. Padakali pano nduna yowona za kusasiyana pakati pa amayi ndi abambo mayi Mary Navitcha ati akachita nawo ziwonetserozi Koma polankhulapo mmodzi mwa akatswiri pa nkhani za ndale mdziko muno a Enerst Thindwa ati ndi zodabwitsa kuti anthu omwe ali patsogolo kuchita izi ndi a chipani cha DPP komanso ena ali ndi maudindo mu nthambi za boma komanso ena ndi omwe anali patsogolo kunyoza ulamuliro wa mtsogoleri wakale wa dziko lino mayi Joyce Banda yemwenso ndi munthu wa mayi zomwe ati zikusonyezeratu kuti anthuwa akupanga zofuna zawo osati za a Malawi. Gulu limeneli ambiri ndi achipani cha DPP ndiye zikudabwitsa kuti dpp ndi nkhani ya chisankho zikugwirizana bwanji. Enanso mwa amenewa ndi amene amakhala patsogolo kunyoza amayi anzawo. Kumbukirani nthawi ya Joyce Banda mmodzi mwa amayi amenewa ndi amene anali patsogolo kunyoza mayi Banda ndiye lero zikudabwitsa kuti abwera ndi ganizoli, anatero a Thindwa Komabe a Thindwa ati ndi koyenera kuti amayiwa apatsidwe mpata wochita ziwonetserozo kaamba koti ndi ufulu wawo kutero malinga ndi malamulo a dziko lino.
11
Njala yavuta, mafumu achenjeza Mafumu ena mdziko muno apempha boma kuti liwathandize kuthana ndi njala yomwe yayamba kale kusautsa maboma angapo ndipo madera ena ayamba kale kupulumukira zikhawo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mafumuwa ndi T/A Kachindamoto ku Dedza, Tengani ku Nsanje ndi Mlauli ku Neno. Izi zikudza patangodutsa sabata ziwiri a bungwe lounikira ndi kuchenjeza za njala la Famine and Early Warning Systems Network (Fewsnet) litachenjeza kuti pafupifupi anthu 1.7 miliyoni asowa chakudya mdziko muno chaka chino. Lipoti la bungweli linaunikira za kapezekedwe ka chakudya mdziko muno kuyambira mwezi wa Ogasiti chaka chino mpaka Malichi chaka cha mawa. Kuunikiraku kunatinso ntchito zolimbana ndi njalayi zikuoneka kuti nzosakwanira kwenikweni ndipo zingakhale zitagugiratu pofika Novembala kapena Disembala chaka chino. Poonjezera, zounikirazi zinati mwa maboma okhudzidwa ndi Nsanje, Chikhwawa, Balaka, Blantyre, Phalombe, Machinga, Zomba, Thyolo, Mulanje, Neno, Mwanza, komanso Mangochi ku chigwawo cha kummwera, Salima ndi Ntcheu pakati komanso mbali zina mdera la kumpoto mboma la Karonga kumpoto. T/A Kachindamoto wati kumeneko midzi 300 yomwe muli anthu pafupifupi 70 000 yakhudzidwa ndi njalayo. Tidali ndi msonkhano ndi a bungwe la zaulimi ndipo tidapeza kuti tikufunika [thandizo la] matani 1 000 a chimanga. Tidayesera ulimi wa mthirira koma zakanika chifukwa mitsinje yaphwa. Ngati sitingalandire thandizo mpaka Disembala, chiyembekezo chilipo kuti anthu ataya miyoyo, yatero mfumuyo. Kachindamoto wati njalayi yagwa kaamba kosowekera mvula mmadera angapo komanso kuchuluka kwa mvula mmadera ena. Tidabzala kawiri kaamba ka vuto la mvula koma sizidaphule kanthu.Kumapeto nkomwe kudabwera mvula yambiri mpaka madzi kusefukira, adatero Kachindamoto. T/A Tengani wati galu wakuda sadasiye malo pomwe anthu 20 000 pansi pake akhudzidwa ndi njalayi. Vuto kumeneko akuti lidali lakusowa kwa mvula. Tidafika potopa kulankhula za njala kuno.Boma litithandize ndi zipangizo kuti tiyambe ulimi wa mthirira chifukwa pafupifupi dera lililonse kuno lakhudzidwa ndi njala, idatero mfumuyi yomwe yati dera lake lili ndi anthu pafupifupi 35 000. Iye wati posakhalitsapa ena ayamba kudya nyika chifukwa chosowa pogwira. Tengani adati madera ena kumeneko ayamba kale kulandira ufa ndi thandizo lachimanga. T/A Mlauli wati ku Neno mvula siidagwe bwino ndipo njala yakhudza pafupifupi boma lonse.Mlauli wati mmudzi mwake muli anthu 25 903 ndipo pafupifupi onse akhudzidwa ndi njalayo. Tikufuna thandizo mwachangu, adatero Mlauli. Mkulu wa bungwe loona za ndondomeko za ulimi lomwe si laboma la Civil Society Agriculture Network (Cisanet), Tamani Nkhono-Mvula, wati alandilapo malipoti kuti mabomawa akhudzidwa ndi njala. Iye wati kotero boma likuyenera kuvomereza kuti mdziko muno muli njala ncholinga choti mabungwe ayambe kuthandiza. Iye adati mabungwe ali chile kuthandiza anthu koma pena amadikira boma livomereze za vuto lomwe lagwalo. Pena atsogoleri amatha kuvomereza kapena kukana kuti kulibe njala pazifukwa za ndale ndipo mabungwe amakhala omangika kuyamba kuthandizapo. Chakudya mdziko muno chilipo. Chiyembekezo chilipo kuti anthuwa apulumutsidwa, adatero mkuluyu. Koma mneneri wa boma, Moses Kunkuyu, wati boma layamba kale kugawa chakudya mmadera ena omwe akhudzidwa ndi njalayi kotero madera omwe sadalandire thandizoli akuyenera kudziwitsa boma. Iye wati msabatayi madera ena okhudzidwa ndi njalayi mboma la Blantyre ndi amene amalandira thandizoli. Malinga ndi unduna wa zamalimidwe, dziko lino lidakolola matani 3.6 miliyoni a chimanga pomwe dziko lino limafunika matani 2.8. Chiyambire malipoti a njalawa, bola lakhala likutsutsa, ati dziko lino lili ndi chakudya chokwanira. Mmbuyomu, Nduna ya Mapulani a Chuma ndi Chitukuko, Atupele Muluzi, inati kuunikira kwa Fewsnet kunali kosadalirika, ati mdziko muno muli ndondomeko yomwe ingadziwe bwino za chiwerengero chomwe chili pa chiopsezo cha njala. Mu Julaye chaka chino, ndondomekoyo inati anthu 1.63 miliyoni ndi omwe anali pa chiopsezo. Chiopsezochi chikudza pomwe dziko lino likukumbukira tsiku lachakudya padziko lapansi, tsiku lomwe limakumbukukiridwa ndi mayiko oposa 150. Tsikuli lomwe limakumbukiridwa pa 16 Okutobala likukumbukiridwa pamutu woti Mgwirizano wa mabungwe azaulimi; ngodya yodyetsera dziko.
8
Mavuto a UDF angaphe demokalase Chipasupasu cha mchipani chakale cholamula cha United Democratic Front (UDF) chingaopseze ulamuliro wa demokalase mdziko muno womwe umalira kuti pakhale zipani zotsutsa zamphamvu zothandiza kuongolera pomwe chipani cholamula chikulakwitsa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Katswiri wa phunziro la ndale kudzanso otumikiridwa pandale aikira ndemangayi potsatira mgwedegwede womwe wakula mu chipani cha UDF. Iwo ati kufooka kwa UDFchimodzimodzi mikangano ya mchipani china chotsutsa chachikulu cha MCPkupereka mwayi kwa chipani cholamula cha DPP kuyenda moyera, mosatsutsidwa pa maganizo a kayendetsedwe ka boma. Katswiri pa maphunziro a ndale yemwenso ndi mphunzitsi pa sukulu ya ukachenjede ya Mzuzu, Noel Mbowela, wati chipani cha UDF chidali cha mphamvu polingalira kuti chidalamulapo koma awa ndi malecheleche ngati sichikonza zolakwikazi. Iye adati ngati zipani zotsutsa zili za mphamvu, zimakakamiza chipani cholamula kuti chidzilabadira zofuna za anthu ndipo izi zimapindulira dziko. Kuunikiraku kwadza pomwe tsopano mamulumuzana a UDF, omwe ena mwa iwo ndi a komiti yaikulu yachipanichi, agawikana ndipo kuli mbali ziwiri zomwe sizionana ndi diso labwino. Mbali imodzi kuli Gorge nga Ntafu, mlembi wamkulu Kennedy Makwangala, Lilian Patel, Atupele Muluzi komanso aphungu onse 15 a chipanichi ku Nyumba ya Malamulo. Mbali ina kuli Friday Jumbe yemwe adapatsidwa ulamuliro wachipani ndi wapampando wakale Bakili Muluzi, Hophmally Makande, Sam Mpasu, Humphrey Mvula komanso Ken Nsonda. Pano mbali ya Jumbe yalengeza kuti yachotsa Makwangwala komanso Atupele pomwe ati awiriwa adalephera kukaonekera ku komiti yosungitsa mwambo yachipanichi. Koma Msonda wati anthu asadandaule chifukwa zomwe zikuchitikazi pochotsa ena ndi njira imodzi yokonzera chipanichi. Iye wati mavuto onse omwe ali kuchipanichi adadza ndi Bakili chifukwa chodzitengera mwa yekha zochitika mchipanimo. Mgwedegwede mchipanichi udakula mwezi wa Okutobala 2011 pomwe Atupele Muluzi adabwera poyera ndikulengeza khumbo lake lodzaima nawo pa mpando wa pulezidenti mchaka cha 2014. Izi sizidakomere komiti yaikulu mchipanichi yomwe idati izi ndizosemphana ndi malamulo achipanichi. Apa chipanichi chidaitanitsa Atupele kuti akaonekere ku komiti yosungitsa mwambo yachipanichi koma iye adakana ndipo komitiyi idalengeza kuti yamuchotsa mchipani. Msonda wati aphungu onse akunyumba ya malamulo ali mbali ya Atupele, yemwenso ndi phungu wa dera la kumpoto cha kummawa kwa Machinga. Kugwedezekaku kudakulanso pa 21 Disembala 2011 pomwe Makwangwala adatulutsa kalata yomwe Msonda wati nkutheka idalembedwa atanamizidwa ndi Bakili Muluzi. Kalatayo idati: Maudindo onse a mchipanichi abwerera momwe adaliri pa 16 Julaye 2009 pomwe wapampando wachipanichi, Bakili Muluzi adanyamuka kupita kuchipatala ku UK ndikusiya zonse mmanja mwa mlembi wa mkulu wachipanichi. Ngodya zomwe zakonzedwa kuchoka pa 16 Julaye 2009 zonse zamasulidwa ndipo mamembala onse achipanichi omwe adakakamizidwa kuchoka mchipanichi abwezeretsedwa pamaudindo awo. Msonkhano wa komiti yaikulu yachipani udzachitika ku likulu la chipanichi ku Limbe pa 28 Disembala 2011 nthawi ya 9 koloko mmawa. Apa mamulumuzana ena achipanichi komanso Msonda adati kalatayo yalembedwa mosafunsa akuluakulu achipanichi. Iwo adati Makwangwala alibe mphamvu zoterezi chifukwa komiti yomwe ikugwira ntchito ndiyo idayenera kubweretsa poyera mfundozi ku komiti yaikulu ya chipani zisanatuluke. Msonda wati mfundo zomwe zidalembedwa mkalatayo, zikutanthauza kuti Bakili Muluzi ndiye adabweretsa mfundozi kuti Makwangwala alembe. Pa 16 pomwe akunenapo, Muluzi adatula maudindo kwa komiti yomwe ikugwira ntchito ndipo maudindowa adawatenganso atabwera kuchoka kuchipatala. Mu Disembala 2009, Muluzi adatulira udindo Jumbe pomwe adalengezanso kuti akusiya ndale. Lero wina akamati maudindo onse abwerera mwakale, akutanthauza kuti Muluzi wayambiranso ndale? Apa ife tikutsimikizirika kuti zonsezi akuchita ndi Muluzi, adatero Msonda. Kalatayi itangotuluka, akuluakulu achipanichi pamodzi ndi Msonda adakatenga chiletso choletsa msonkhano wa pa 28 Disembala. Chipanichi chidaitanitsa Makwangwala komanso Atupele ku komiti yosungitsa mwambo, koma awiriwa sadatuyukire. Apa awiriwa adachotsedwa mchipanimo nkusankha Hophmally Makande kuti akhale wogwirizira mpando wa mlembi wachipanichi. Chipanichi pa 27 Disembala chidaitanitsa Bakili Muluzi kuti akaonekere ku komiti yosungitsa mwambo pa 11 Januwale 2012 koma Muluzi, pobwera kuchokera ku Zambia, adati izi nzamkutu. Kalata yomwe idalembedwa ndi Makande idati Muluzi akuyenera kukayankha milandu itatu. Iyi ndiyo kusowetsa K125 miliyoni yachipanichi, kutenga katundu wachipani ndikukamulembetsa mdzina lake komanso kuitanitsa mamembala achipanichi pamodzi ndi Makwangwala pa 21 Disembala ku zokambirana chikhalilecho alibe mphamvu zotere malinga ndi gawo 12 (b)(vi), 12(b)(vii) ndi 12(b)(ix) a malamulo achipanichi. Mbowela wati zonsezi zikuonetsa kuti chipanichi komanso ulamuliro wa zipani zambiri ukulowera kuchiwonongeko. Sam Banda wa mmudzi mwa Chipoka kwa T/A Mponda mboma la Mangochi wati chipasupasuchi chikusokoneza anthu: Nditsate ziti? Sitikudziwa kuti tidzavotera ndani. Akuyenera kugwirizana zochita, adatero Banda. Sanudi Tambula wa mmudzi mwa Kalembo kwa T/A Kalembo mboma la Balaka wati chidwi ndi chipanichi chikuchoka. Msonda waloza chala Bakili Muluzi ndipo wakumbutsira zomwe adachita Muluzi ati potenga munthu wakunja kwa chipaniBingu wa Mutharikandikumupatsa ulamuliro wa UDF pa chisankho cha 2004. Iye adati pano Muluzi wayamba kugwiritsa ntchito ena monga Makwangwala kuti azibweretsa zachilendo mchipanichi, zomwe komiti yaikulu ikukana. Mchaka cha 1994 pomwe chipanichi chidalowa mboma, chipanichi chidali ndi aphungu 92 mnyumba ya malamulo ndipo pofika 1999 nkuti chili ndi aphungu oposa 100 chifukwa aphungu a chipani cha Alliance for Democracy (AFORD) adagwirizana ndi chipanichi. Mchaka cha 1999 mpaka 2004 chipanichi chidali ndi aphungu 55 ndipo panthawiyi chipani cha MCP ndicho chidatenga aphungu ambiri. Pano chipanichi chili ndi aphungu 15 okha kunyumba ya malamulo.
11
Amatsutsanabe zamakumanidwe awo Ambiri akapezana nkukondana nkugwirizana za banja amakhala ndi chikumbumtima cha komwe ndi mmene adakumanirana, koma ndi nkhani yochititsa chidwi kumva za Chiyembekezo Focus Maganga ndi Lydia Kalonde. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Awiriwa akuti mpaka lero sagwirizanabe za malo ndi tsiku lomwe adakumana koyamba ndipo chomwe amakumbukirako nchakuti mudali mchaka cha 2013 ndipo adapanga chinkhoswe pa 7 June 2013. Chomwe ndimakumbuka ine nchakuti ndidakamupeza kuofesi yake nditapita ndi mnzanga Dickson Kashoti pomwe iye amakakamira kuti tidakumana koyamba mminibasi koma kwa ine uku kudali kukumana kwachiwiri, adatero Focus. Focus ndi Linda pachinkhoswe chawo Panthawiyo nkuti Focus akugwira ntchito ya utolankhani pomwe Lydia adali wothandizira mkulu wa zofalitsa mawu kuunduna wa zofalitsa mawu komwe ali mpaka pano. Focus adati poti awiriwa alibe tsiku lokhazikika lomwe angati adakumana koyamba, chomwe amakumbukira nchakuti atakumana kuofesi ya Lydia adangopatsana moni polingalira kuti idali nthawi ya ntchito. Kwinaku akuti amakumbukira kuti atakumana mminibasi Lydia adali ndi chidwi ndi momwe iye adavalira, suti yapamwamba koma tsitsi losapesa ndipo mmaganizo mwake amangoti mwina wadzuka ndi mowa mmutu. Ngakhale adali ndi maganizo oterewa, macheza adayenda bwino mpaka posiyana tidapatsana nambala za foni nkumaimbirana mwakathithi mpaka chibwenzi chidayamba, adatero Focus. Iye adati chitachitika chinkhoswe iwo adalowana asadapange ukwati pofuna kukonzekera mofatsa ndipo akuti ukwatiwo ukhalako kumapeto kwa chaka chino. Focus akuti amakonda kwambiri Lydia chifukwa ndi wooneka bwino, wanzeru, wachikondi, woopa Mulungu komanso amamuthandiza nzeru ndi kumulimbikitsa akamafooka. Naye Lydia akuti amamukonda kwambiri Focus kaamba ka zochitika zake komanso masomphenya ndi kulimbikira pochita zinthu. Amapanga zondisangalatsa komanso ali ndi khama ndi luntha pochita zinthu. Tidapezana okonda kupemphera tokhatokha komanso ansangala, adatero Lydia.
15
Bwanji nkhuku yoweta sagula pamsika? Achewa ali ndi njira zosiyanasiyana zoperekera malango pakati pawo. Njira zina ndi monga nthano, magule, ndakatulo, chinamwali ndi miyambi ndi zininga. Lero nkhani yathu yagona pa miyambi ndipo tifukula mwambi wakuti nkhuku yoweta sagula pamsika. STEVEN PEMABMOYO adacheza ndi mfumu yaikulu Njewa ya ku Lilongwe, yomwe ikutambasula za mwambiwu. Choyamba, mfumu, tafotokozani za momwe nkhani ya chikhalidwe cha makolo ilili kuno. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kwathu kuno ndi dera limodzi lomwe anthu sataya chikhalidwe cha makolo ndipo kuti mukhale pakati pathu kwa masiku angapo mukhoza kuona kusintha poyerekeza ndi zomwe mudazolowera kuona. Anthu a kuno adamva mwambo ndipo adausunga. Njewa kufotokoza za tanthauzo la mwambiwo Tsono mukati adamva mwambo mukufuna kunena kuti adaumva bwanji? Pakati pa Achewa, mwambo ndi chuma chosiyirana. Makolo kalero adasiyira ana awo omwe adasiyiranso ana awo chonchoo mpakana lero timangosiyirana kuti mpakana kalekale mtundu wathu usadzasokonekere ayi. Ndikufuna kudziwa kusiyiranako mumachita kupatsana pamanja? Ayi, mwambo si chithu choti mungachione kapena kuchigwira. Imakwana nthawi yoti makolo amadziwa kuti mwana uyu akufunika kudziwa zakuti ndiye amakonza njira yomupatsira mwambo womwe ukufunikawo. Pali njira zingapo monga kutengera mwana kutsimba, kudambwe, kumuitanira anamkungwi kapena kudzera mmiyambi yomwe amatolamo tanthauzo. Eya pamenepo, pali mwambi uja amati nkhuku yoweta sagula pamsika. Mwambi umenewu uli ndi tanthauzo ndithu? Kwabasi, mwambi umene uja uli ndi tanthauzo lozama kwambiri ndipo mwachita bwino kusankha mwambi umenewu chifukwa umakhudzana ndi moyo wa munthu, makamaka akakula, kuti akukalowa mbanja nkukayamba moyo wina. Ndikufuna mumasule bwinobwino kuti nkhuku ikubweramo bwanji. Chabwino, ndiyambe ndi kumasulira motere: munthu ukafuna nkhuku yoti uwete, supita pamsika chifukwa akhoza kukugulitsa yodzimwera mazira kapena yoti idatopa kale kuikira ndiye kuti palibe chomwe wachitapo. Pokagula nkhuku yoweta umafika pakhomo pomwe pali khola ndipo umafunsa umboni woti nkhukuyo ikadaikira kapena isadayambe nkomwe ndipo kuti mtundu wake umaikira motani. Apa zimatanthauza kuti munthu akafuna banja sangangopita pamsewu nkutengana ndi mkazi kapena mwamuna osadziwa mbiri yake, komwe amachokera ndi mtima wake. Koma amayenera kutani? Munthu wanzeru amayenera kupita kwa makolo kapena abale a munthu yemwe wamukonda kukaonako ndi kuphunzira khalidwe lawo. Akhozanso kufufuza kudzera kwa anthu adera omwe amakhala kufupi ndi munthuyo, akakhutira akhoza kuyambapo dongosolo. Izi ndi zomwe makolo amatanthauza mmwambiwu. Paliso pena pomwe mwambiwu ungagwire ntchito? Kwinako zikhoza kutengera kuti pali nkhani yanji koma bola tanthauzo lake likhale loti pakufunika kusamala, makamaka kuchita kafukufuku osangophwanyirira pochita zinthu. Koma gwero lenileni makolowo poyambitsa mwambiwu adayambitsira nkhani ya maukwati.
10
Kuli ziii! Pa za mthandizi Kwangoti zii! Nkhawa yagunda ngati ntchito za mthandizi zomwe anthu amalandira kangachepe akalima msewu ichitike popeza nthawi yake yadutsa osamvapo kanthu. Iyi ndi ndondomeko yomwe anthu amalima misewu ndi kulandira ndalama yomwe imathandiza nthawi ya njala. Chaka chilichonse ntchitoyi imachitika mu January ndi February. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Koma pano miyezi itatu yatha mwachinunu, osamva kanthu kuchokera kuboma. Izi zadabwitsa mafumu amene amakhudzidwa ndi ntchitoyi pomemeza anthu a mmidzi yawo kuti akalambule misewu. Mfumu Kabunduli ya mboma la Nkhata Bay yati njala ikukuta anthu a mdera lake amene amapindula ndi ntchitozo. February ndi mwezi wa njala, chaka chino anthu akutuwa ndi njala chifukwa cha ngamba. Timadalira kuti tipezako mpumulo tikayamba kulima misewu koma mpaka lero, idatero mfumuyo. Koma mkulu woona momwe ntchito zachitukuko zikuyendera kunthambi ya Local Development Fund (LDF), Booker Matemvu, wati ntchitoyi yasintha kusiyana ndi zaka zonse. Ntchitoyi iyamba mu September ndipo idzatha November chaka chino. Iyi ndi nthawi yomwe takonza kuti anthu adzayambe kulima misewu, adatero Matemvu. Ganizoli likudabwitsa Kabunduli. Asinthiranji? Kapena zalowa ndale? Chifukwa mwezi wa njala ndi February mpaka March. Apapa ndiye kuti asokonezeratu cholinga cha ndondomekoyi, adatero iye. Tili ndi anthu kumudzi amene alibe chilichonse, ganyu ndi wovuta kumupeza ndipo amadalira kulima misewu kuti apeze thandizo. Popezera ndalama ndi ntchito yomweyi, ndiye akusinthanso? Matemvu wati kusinthaku kwachitika chifukwa zimatenga nthawi yaitali kuti anthu alandire ndalama zawo akalima misewu mu February. Pena zimafika April anthu asadalandire, nchifukwa chake tasintha. Komanso dziwani kuti mmidzimo tayambitsa ntchito zina zomwe anthu akugwira polandirapo ndalama monga kubwezeretsa zachilengedwe, adatero Matemvu. Iye adati akukambirana ndi boma kuti ndondomekoyi ichitike monga imachitikira zaka zonse chifukwa cha anthu amene akutuwa ndi njala. Talandira madandaulo kwa anthu, maka a mmadera amene akhudzidwa ndi njala. Ngati zonse zingathe bwino ndiye kuti ntchitoyi itha kuyamba nthawi iliyonse September asadafike, adatero Matemvu. Ngakhale ntchitoyi idzayambe mu September monga momwe Matemvu akunenera, madera ambiri misewu ndi yoonongeka chifukwa cha mvula pamene ina ndi yosalambulidwa. Ndalama zolimitsira misewuyi zachoka ku World Bank. Nthambi ya LDF yomwe imayendetsa ndondomekoyi idalandira kale K97 biliyoni (132 miliyoni dollars) kuti zigwire ntchito mpaka chaka chamawa. Njala yakhudza maboma a Neno, Nsanje, Chikwawa, Balaka, Mwanza, Phalombwe, Ntcheu, Blantyre, Karonga ndi ena.
15
Matenda Osapatsirana Akuchuluka-Boma Wolemba: Sylvester Kasitomu Boma kudzera muunduna wa zaumoyo lati pofika mchaka cha 2025 anthu ambiri mdziko muno azakhala atakhudzidwa ndi matenda monga kuthamanga kwa magazi ndi shuga kuposa matenda opatsirana monga a Edzi. Mkulu othandizira kuyendetsa zipatala ku matenda asapatsirana mdziko muno ku undunawu a Hestings Chigalu Chiumia ndiwo ayankhula izi mboma la zomba pomwe amafotokozera akuluakulu aboma la zomba za matenda amgonagona osapatsirana-wa. Mwazina a Chiumia alangiza anthu kuti apewe kusuta fodya ndi kuledzara alimbikitse kudya zakudya zamagulu komanso kuchita masewera olimbitsa thupi zomwe ndizothandiza kuti asadwale matendawa. Mwazina iwo anati anthu ambiri ngati sasata njira zoyenera pakayendetsedwe kwa moyo wawo azadwala matendawa kuposa amene azapezeke ndi matenda opatsilana monga edzi malungo ndi zina. Tikamafika mu chaka cha 2025 anthu ambili azakhala atadwala matendawa kaamba koti anthu masiku ano akukonda kudya zakudya za nyama chipisi cha pachiwaya ndi zina zomwe zingapangitse kuti chiwerengero cha mafuta amthupi chikwere ndikuamba kudwala matendawa, anatero a Chiumia. Mwazina iye wapepha anthu kuti apewe kudya zakudya zomwe zingakoledzere kukwera kwa chiwerengero cha mafuta mthupi komanso kukonda kuchita masewera kafukufuku anasonyeza kuti muchaka cha 2009 anthu odwala matendawa anali 33 pa hundred aliwonse odwala matenda a bp ndipo 6 pa hundred aliwonse odwala matensda a shuga ndipo mu chaka cha 2016 chinafika kufika pa 19 pa hundred aliwonse odwala bp ndipo atatu pa hundred aliwonse odwala shuga.
6
Anjata anthu 21 Kamba Kotentha Polisi ya Malomo Apolisi mboma la Ntchisi amanga anthu 21 powaganizira kuti akukhudzidwa ndi kuwotchedwa kwa polisi ya Malomo mbomalo. Wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sub Inspector Richard Kaponda watsimikiza za nkhaniyi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Iye wati mwa anthuwa, asanu ndi amayi pamene 16 ndi abambo, ndipo onsewa akuyembekezeka kukayankha mlandu wotentha nyumba ya boma zomwe ndi zotsutsana ndi gawo 337 la malamulo oyendetsera dziko lino. Sabata ziwiri zapitazo, anthuwa anagwira munthu wina yemwe amamuganizira kuti ndi opopa magazi ndipo mmene apolisi amafuna kulesetsa mkuluyo pamene amafuna kutenthedwa ndi gululo, ndi pomwe anthuwo anayamba kugenda ndi kutentha polisiyo. Kaponda wachenjezanso anthu omwe akufalitsa mbiri yoti mdziko muno muli opopa magazi kuti akapezeka adzayimbidwa mlandu Kamba koti limeneli ndi bodza la mkunkhuniza.
7
NASME Yapempha Amayi Achilimike Pamalonda Bungwe la business zingono-zingono la National Association of Small Business and Medium Enterprises NASME lachinayi lalimbikitsa amayi kuti achilimike komanso kutsata njira zovomerezeka zochitira malonda awo. Mmodzi mwa akuluakulu ku bungweli a Charles Nyekanyeka ndi omwe anena izi lachinayi ku Maula Cathedral mu mzinda wa Lilongwe pa maphunziro a tsiku limodzi okhudza momwe amayi angapititsire patsogolo malonda awo. Iwo ati ochita business zingono-zingono akuyenera kutsatira bwino njira zoyenera zovomerezeka ngati akufuna kugulitsa katundu wawo ku maiko akunja ngati njira imodzi yopititsira patsogolo malonda awo. Kwakukulu bungwe lathu likugwira ntchito ndi amayi omwe amachita ma bizinezi osiyanasiyana kuti abwewre pamodzi ndikuphunzitsana ma upangiri amene angachitire mabizinezi awo antero nyekanyeka. Polankhulapo mmodzi mwa amayi ochita malondawa, mayi Doreen Mtawi ati kudzera mu bungwe la nasme amayi wa apeza maupangiri abwino omwe angachitire mabizinezi awo monga kudziwa misika yoyenera ya zokolora zawo komanso kugulitsa zokolorazi pa mitengo yabwino zomwe zawapezetsa phindu lokwanira. Kukhala mmaguru ndi kothandiza kwambiri kaamba koti umapeza zinthu zoti pa iwe wekha siungazipeze monga kupeza misika ya zokolora ndi zina zambiri antero mayi Mtawi. Bungwe la NASME linakhazikitsidwa ndi cholinga chofuna kuti liziyanganira mabungwe angonoangono pomwe mwazina limathandiza amayi ochita malonda kuwapezera misika ya malonda awo yovomerezeka.
2
Zipani zigonjera chiletso cha Escom Chipani cha MCP chati chichotsa mbendera pamapolo Zipani za ndale mdziko muno zagwirizana ndi chiletso cha bungwe loyendetsa ntchito za magetsi mdziko muno la Escom choti zipani zandale zisamapachike mbendera zawo pazipangizo zake monga mapolo a magetsi. Mneneri wa chipani cha MCP Jessie Kabwila wati bungwe la Escom ndi lolandiridwa paganizo lakeli, koma wapempha kuti bungweli litsate njira zabwino pochotsa mbenderazo kuopa kuononga. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC A Escom sakulakwitsa chifukwa akuganizira za chitetezo cha anthu, koma tingopempha kuti pakhale kulumikizana kwabwino kuti katundu wathuyu asaonongeke poti ndi wodula, adatero Kabwila. Mlembi wamkulu wa chipani cha PP Wakuda Kamanga naye wati palibe cholakwika bungwe la Escom kuchita izi chifukwa ngozi za magetsi zimaopsa, makamaka ngati anthu akuseweretsa zida za magetsi. Iyi ndi njira imodzi yomwe bungwe la Escom laona kuti ikhoza kuthandiza kuchepetsa ngozi komanso kuteteza katundu wawo, choncho ife tikambirana ndi achinyamata athu kuti akachotse mbendera zomwe zili pamapolo a magetsi, adatero Kamanga. Koma mneneri wa chipani cha DPP Nicholas Dausi adati chipani chawo sichipachika mbendera zawo mmapolo a magetsi. Zimenezo mukafunse a PP, ife sitiika mbendera pamapolo a magetsi, adatero Dausi Tamvani itamufunsa za maganizo a chipani chake pa chiletso cha bungwe la Escom. Wachiwiri kwa mneneri wa bungwe la Escom George Mituka wati bungweli lidayamba kuganiza za nkhaniyi kalekale ndipo lakhala likukambirana ndi makampani ndi makhonsolo pa chimene angachite. Mituka adati aganiza zochita izi pano poona mmene mchitidwewu wakulira ndi momwe ngozi zokhudza magetsi zikuchitikira. Nkhaniyi tidaiyamba kalekale koma pano taona kuti zanyanya ndiye palibe kuchitira mwina moti pano tayamba kale kuthothola, adatero weachiwiri kwa mneneri wa bungweli. Mneneri wa bungwe loyendetsa zisankho mdziko muno la Malawi Electoral Commission (MEC), Sangwani Mwafulirwa, wati ndi mlandu kupachika mbendera za chipani mmalo osaloledwa ngakhale kuti malamulo a MEC sanena chilango chomwe wopezeka akutero angalandire. Bungwe la Escom lidaletsa zipani kupachika mbendera zawo pazipangizo zake maka mapolo a magetsi ndipo lidati lidzathothola mbendera ndi zipangizo zina za kampeni zomwe zidapachikidwa kale. Bungweli lati kupatula kuti mchitidwewu ndi woopsa, zipangizo zawo zimawonongeka ndipo izi zimasokoneza ntchito zawo. Escom sidzakhudzidwa ndi ngozi iliyonse yomwe ingaoneke pomwe anthu akupachika mbendera pamapolo a magetsi, komanso idzaimba mlandu yemwe adzapezeke akupachika mbenderazi pamapolo ake. Ndipo pomaliza Escom ithothola mbendera zonse zomwe zidapachikidwa kale, chatero chikalata cha Escom. Koma ngakhale bungwe la Escom lanena kuti layamba kale kuchotsa mbendera ndi zipangizo zina za kampeni mmapolo a magetsi , mbenderazi zidajali petupetu mmizinda, mmatauni ndi mmaboma pamene kwatsala mwezi umodzi ndendende kuti chisankho chapatatu chichitike pa 20 May.
11
Ulangizi wabala mwana ku Mulanje Njala yomwe yakhudza madera ambiri ikuvutanso mboma la Mulanje komwe anthu akuyembekezereka kutuwa chifukwa cha mvula yanjomba yomwe adalandira nyengo ya mvula yapitayi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ngakhale njalayi yapereka mantha kwa ambiri, anthu a ku Mulanje West kwa T/A Juma, galu wakudayu wayamba kulambalala chifukwa cha ulimi wamthirira omwe wabonga kumeneko. Mlimi kupatutsa madzi mmunda wa chimanga Monga akufotokozera Esther Makweya wa mmudzi mwa Mlapa, langizo la alangizi awo ndilo labala zotsatira zabwino kumeneko. Alangiziwo akuti adawauza kuti akumbe zitsime ndi kuyamba ulimi wa mthirira zomwe zabereka mwana. Pano kuderali chimanga chili mbwee pamene ena akubzala, ena akukolola ndipo enanso atangwanika pamsika kukagulitsa chachiwisi. Aggrey Kamanga ndiye wachiwiri kwa wokonza za mapulogalamu ku nthambi ya zamalimidwe ya Blantyre Agriculture Development Division (Bladd). Iye adati nkhawa apachika kuti anthuwa angatuwe ndi njala chifukwa chomvera malangizo abwino. Tidawalangiza kuti ayambepo ulimi wa mthirira pokumba zitsime komanso pafupi ndi iwo pali mtsinje womwe suphwerapo. Pano aliyense ali kalikiliki ndi ulimi pamene ena tawalangiza kuti ayambiretu kupanga manyowa, adatero Kamanga.
15
Achitira zadama mu basi Anthu ena okhala mumzinda wa Mzuzu akhala akuchitira za dama mmabasi omwe adaimikidwa kumsika wa Zigwagwa pafupifupi miyezi inayi yapitayi. Mabasiwa, salinso mmanja mwa kampani ya Axa chifukwa banki ya FDH idawagulitsa kwa mkulu wina wa bizinesi yemwe adawaimika ku Zigwagwako poyembekezera kuwagulitsa ndi kuwaphwasula ena mwa iwo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Imodzi mwa basi amachitiramo zadamayo Komatu anthu ena apezerapo mwayi wochitiramo za chiwerewere maka yomwe idali ndi magalasi osaonekera mkati, tintedi. Msangulutso udatsinidwa khutu kuti izi zakhala zikuchitika madzulo komanso usiku ndipo kuti anthuwa amalipira kangachepe kuti apeze mwayi wodzithandiza mbasimo. Komatu si anthu a zadama okhawa omwe amapumira mmabasiwo, ngakhalenso ena osowa kogona, adatenga mabasiwo ngati nyumba zogona alendo. Pomwe Msangulutso udakazungulira pamalopo udapeza mlonda Chimwemwe Kachali yemwe adavomereza kuti wakhala akupezerera anthu akuchita chiwerewere mu imodzi mwa mabasiwo makamaka usiku. Anthu amatengerapo mwayi chifukwa ndi yosaonekera mkati ndiye zomwe amachitazo sizimaoneka kunja. Chifukwa choti chitseko chake sichitsekeka, anthu ankangolowamo, adatero Kachali. Iye adakanitsitsa zoti adalandirapo ndalama kuchokera kwa anthuwa. Mwina popeza miyezi yapitayo tidalipo awiri ndi mnzanga, ndiye kuti mwina ndi yemwe amalandira ndalama; koma ine sindidalandireko kanthu chifukwa ambiri mwa anthu omwe amachitira zadama mmenemo adali anthu woti timawadziwa ndithu, adatero Kachali. Iye adaonjezera kuti zikuoneka kuti ngakhale komwe mabasiwo adali asadagulidwe ndi bwana wake mchitidwewu umachitika chifukwa adabwera ali ndi makondomu ogwiritsidwa ntchito mwa zina. Apa adatinso masiku ena amapezanso makondomu ogwiritsidwa kale ntchito omwe anthuwo amawataya akamaliza zadamazo. Idafika nthawi yoti anthu amakuwa akamadutsa pano kuti mmabasimu mutuluka mwana ndipo ena amati aphwasulidwe kapena kugulitsidwa mwachangu, adalongosola Kachali. Iye adati zitafikapo abwana ake adayesa kuitseka ndi mawaya kuti anthu asamalowe koma sizidathandize chifukwa anthuwo adadula mawayawo. Nthawi zina ndikati ndikayendere basi pakati pausiku ndimapeza mwagona anyamata achilendo. Zikatero ndimawathamangitsa. Ambiri mwa iwo amakhala oti athamangitsidwa mnkhalango ndipo alibe kolowera, adatero Kachali. Pocheza ndi tsamba lino, mwini ma basiwo George Biyeni adati adagula mabasi asanu omwe adali a kampani ya Axa kuchokera kubanki ya FDH ndipo adalemba alonda ake awiri oyanganira mabasiwo koma mmodzi adasiya ntchito. Biyeni adati mphekesera yoti mmabasiwo makamaka ya tintediyo mumachitika za dama idamupeza ndipo adangoganiza zoyitseka ndi mawaya kuti anthuwo asamalowemo. Ndimati ndikalowa mbasimo, mumaoneka kuti anthu amachitamo zawo ndithu, koma ndikafunsa sindimayankhidwa bwinobwino, adatero Biyeni. Iye adati basi yomwe izi zimachitika kwambiriyo waiphwasula tsopano ndipo yomwe yatsala pamalopo ndi yoti omwe adawagulitsawo aikhonza kukonzekera kupita nayo ku Blantyre. Biyeni adaonjezera kuti nzovuta anthu a zadamawa kugwiritsa ntchito basi inayo chifukwa mwini wake adaikamo anthu ake angapo omwe akugona momwemo poilondera kwinaku akuikhonza. Ndipo polankhulapo mneneri wa polisi mchigawo cha ku mpoto Peter Kalaya adati ofesi yake sidalandirepo dandaulo pa nkhaniyi. Tikadauzidwa tikadafufuza ndipo ochita zadamawo akadaimbidwa mlandu wa idle and disorderlykuchita zadama malo osayenera, Kalaya adatero.
15
HRDC Yati Ichititsa Ziwonetsero Zatsopano Zokakamiza Ansah Kutula Pansi Udindo Bungwe lomenyera ufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) lati lichititsanso ziwonetsero zokakamiza wapampando wa bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC), Justice Dr. Jane Ansah komanso makomishonala onse kuti atule pansi maudindo awo. Trapence ndi Tembo (kumanja) Izi zanenedwa pa msonkhano wa atolankhani omwe bungweli linachititsa lolemba mu mzinda wa Lilongwe ndipo ati zionetserozi azikonza kuti zidzachitike pa 28 mwezi uno. Akulu-akulu a bungweli ati ndi odabwa kuti mpaka lero Dr Ansah sakutulabe udindo wawo ngakhale adanenetsa kuti adzatero ngati bwalo la milandu la Apilo litapezadi kuti sadayendetse bwino chisankho cha mtsogoleri wa dziko cha chaka chatha. Masiku apitawa akhala akunena kuti amadikira khoti ligamule ndipo khoti lagamula kuti sanayendetse bwino zisankho ndipo tikudabwa kuti mpaka pano sakusiya udindowu ndiye ife tikufuna tingowachotsapo tokha ndikuika munthu oti ayendetse bwino chisankho, anatero Tembo. Iwo ati ngakhale kuli nthenda ya COVID-19 ziwonetserozi zichitikabe ndipo akhala akutsata ndondomeko zomwe a unduna wa zaumoyo akhazikitsa.
11
CMST iyambanso kugawa mankhwala Nkhokwe ya mankhwala ya Central Medical Stores Trust (CMST) yatsiriza kukambirana ndi mabungwe omwe amathandiza dziko lino pa nkhani ya zaumoyo kuti udindo wosunga ndi kugawa mankhwala ubwerere mmanja mwake. Mkulu woyendetsa ntchito zaumoyo mdziko muno, Dr Charles Mwansambo, komanso mkulu wa CMST, Feston Kaupa, atsimikiza za nkhaniyi. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ngoma: Ana ndi amayi amavutika Akuluakulu awiriwa ati izi zikutanthauza kuti mabungwe ndi maiko othandiza dziko lino pa zaumoyo akhutira ndi kusintha kwa ndondomeko zoyendetsera ntchito za ku nkhokweko makamaka pa chitetezo cha mankhwalawo. Apa ndiye kuti mabungwe ali ndi chikhulupiliro mu nkhokwe yathu ya mankhwala chifukwa adayamba kupereka okha mankhwala mzipatala kusolola mankhwala kutavuta mzaka za mu 2002, watero Mwansambo. Kaupa wati, mwa zina, mabungwe adatuluka mu ndondomeko yakale yodzera ku nkhokwe pogawa mankhwala pofuna kuti zinthu zina zisinthidwe ku nkhokweko ndipo zonse zatheka tsopano. Tidasintha zambiri monga chitetezo cha mankhwala mu nkhokwe, komanso pakagawidwe kake. Nkhokwe zathu nzamakono, nzovomerezeka kusungamo mankhwala, komanso tili ndi galimoto zapamwamba zokhala ndi zipangizo zoilondola kuti mankhwala asabedwe, watero Kaupa. Koma kadaulo wina pa zaumoyo Dorothy Ngoma wati ngakhale nkhaniyi ikumveka yokoma, akuluakulu aku nkhokweyo akuyenera kuganizira mozama amayi ndi ana pa ntchito yawo. Apa zikutanthauza kuti mphamvu zikubwera mmanja mwawo ndiye sitikufuna kuti posachedwapa tiyambenso kumva nkhani zogonthetsa mkhutu kuti mankhwala ena sakupezeka kapena ndiwoonongeka ayi. Zimenezi zimazunzitsa amayi ndi ana, watero Ngoma. Kadauloyu wati pomwe mabungwe ankaganiza zotuluka mndondomekoyi adaona kuti amayi ndi ana ndiwo amavutika. Choncho akhoza kukhala akuyesa ngati utsogoleri wa ku nkhokweyo wasinthadi. Chomwe chimavuta nchoti amakhalapo ena ofunadi kusintha zinthu, koma mkati momwemo mukhalanso ena atambwali ndiye tiyeni tiona kuti aziyendetsa motani, koma langizo langa ndiloti tichepetse mtima wodzikonda, watero Ngoma. Mwansambo wati mabungwe atakhumudwa ndi kubedwa kwa mankhwala, adanyanyala nkuyamba kupereka okha mankhwala mzipatala moti kuchoka 2002, kudali magulu oposa 12 osunga ndi kugawa mankhwala okha. Chomwe chimachitika nchoti padali ena osunga ndikugawa mankhwala okhudzana ndi matenda a edzi, ena amapanga za mankhwala achifuwa chachikulu, ena zauchembere ndi zina zosiyanasiyana, koma tsopano zonsezi zibwera pamodzi pansi pa nkhokwe yathu, watero Mwansambo. Iye wati izi zithandiza kuchepetsa ndalama zonyamulira mankhwala kupita mzipatala za boma chifukwa ofesi ya zaumoyo ikayitanitsa mankhwala, onse azinyamulidwa pakamodzi mmalo moti ena apititse pa wokha, enanso pa wokha.
6
Moyo pachiswe: Ambiri akuzemba mankhwala otalikitsa moyo Amati phukusi la moyo umadzisungira wekha, koma kumene zikuloweraku, zikuonetsa kuti Amalawi ambiri omwe ali pamndandanda wolandira mankhwala otalikitsa moyo (ma ARV) akukwirira phukusi lawo pachulu cha aganga pozemba kulandira ndi kumwa mankhwalawa. Malingana ndi zomwe Tamvani yapeza kuchokera kumgwirizano wa mabungwe olimbana ndi kufala kwa kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi, anthu 20 mwa anthu 100 alionse oyenera kulandira mankhwalawa akuchita ukamberembere. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mankhwala otalikitsa moyo ngati awa safuna kudukiza munthu akayamba kumwa Wapampando wa mgwirizanowu, Maziko Matemba, wati ukamberemberewu ndi chiphe kaamba koti anthu otere sachedwa kugwidwa ndi chipwirikiti cha matenda chifukwa chitetezo cha mthupi mwawo chimatsika msanga. Matemba adati kupatula kutsika kwa chitetezo cha mthupi, anthu omwe amati kuyamba kumwa mankhwalawa nkudukiza thupi lawo limapima kotero kuti silimvanso mankhwala alionse omwe angalandire akamva. Tili ndi nkhawa yaikulu kwambiri chifukwa anthu otere ndiwo amabwezeretsa chitukuko cha dziko mmbuyo. Boma likuyesetsa kugula mankhwala kuti anthu ake azikhala nthawi yaitali ali ndi thanzi, koma iwo nkumathawanso, komwe kuli kusayamika, adatero Matemba. Iye adati abambo ambiri komanso omwe amakhala mmatauni ndiwo akuchulukira kuzemba mankhwalawa kaamba ka manyazi, kuiwala kuti ali ndi udindo pamabanja awo ndi dziko lomwe. Mafigala a bungwe la Malawi Network of Aids Organisations (Manaso) amasonyeza kuti mdziko muno muli anthu pafupifupi 850 000 omwe akuyenera kumalandira mankhwala otalikitsa moyo koma mwa anthuwa, mmadera akumidzi ndimo anthu ambiri amatsatira ndondomeko. Mkulu wa Manaso, Abigail Dzimadzi, adati gulu lina lomwe likuchulutsa ukamberembere ndi achinyamata omwe safuna kuonekera kuti ali ndi kachilombo poopa kuti angadzasowe mabanja mtsogolo. Chiopsezo chachikulu chili poti munthu yemwe sakulandira mankhwala ndiye ali nkuthekera kwakukulu kofalitsa kachilombo ndiye ngati achinyamata akuzemba, zikutanthauza kuti tikulimbana ndi nkhondo yomwe tikumenyananso tokhatokha, adatero Dzimadzi. Nduna ya zaumoyo, Dr Peter Kumpalume, akuti nkhaniyi ndi yomvetsa chisoni kaamba kakuti boma limafunitsitsa vutoli litatheratu mdziko muno poti ena mwa anthu omwe dziko limataya chifukwa cha vutoli ndi ofunika mipando yautsogoleri. Anthu ena auza Tamvani kuti nthawi zina anthu amazemba kukalandira mankhwala kaamba ka momwe amalandiridwira kuchipatala, koma unduna wa zaumoyo ndi bungwe la Manaso ati chifukwa ichi nchozizira polingalira za moyo wa munthu. Mpofunika kuunika nkhani ya chinsinsi cha odwala chifukwa ena safuna kuonekera koma ali ndi mtima wofuna kumalandira thandizo. China ndi malankhulidwe a ogwira ntchito kuchipatala omwe amagwetsa anthu ulesi, adatero Lucy Banda, wapampando wa gulu lophunzitsa ndi kuyendera anthu omwe ali ndi kachilombo ka HIV ku Senga Bay, komwe akuti abambo ambiri amazemba kulandira mankhwalawa nkumatangwanika ndi usodzi. Woyanganira nkhani za umoyo muunduna wa zaumoyo, Dr Charles Mwansambo, wati ichi nchimodzi mwa zifukwa zomwe boma, kudzera muundunawu, lidakhazikitsa pologalamu yoti kuchipatala kuzikhala malo apadera oti anthu azikalandirirako uphungu pankhani za Edzi ndi mankhwala otalikitsa moyo. Panopa mzipatala zambiri muli malo apadera omwe anthu amakalandirirako uphungu, kuyezetsa magazi ndi kulandira mankhwala otalikitsa moyo. Ndiye nkhani ya chisinsiyo idakonzedwa, adatero Mwansambo. Iye adatinso boma lidakhazikitsa pologalamu ya ma 90 atatu (90 90 90) kufuna kuti anthu athe kuzindikira kufunika kwa kutsatira ndondomeko ya mankhwala a ARV. Ndondomekoyi imatanthauza kuti anthu 90 alionse pa anthu 100 akudziwa momwe alili mthupi mwawo; mwa anthu 90, 90 a iwo akulandira mankhwala otalikitsa moyo moyenerera; ndipo anthu ena 90 atetezedwa kukutenga kachilomboka. Potsindika kufunika kolimbana ndi matendawa, naye sipikala wa Nyumba ya Malamulo, Richard Msowoya, adapempha aphungu a nyumbayi kuti kupatula kudalira bajeti ya boma, azikhala ndi mapologalamu opezera zipangizo zomenyera nkhondoyi. Pempholi adaliperekanso kwa akuluakulu a mabungwe pamisonkhano yomwe nyumbayi idachititsa mwezi wa August wa aphungu ndi amabungwe pankhani yolimbana ndi matendawa mchigawo cha maiko a kummwera kwa Africa, yomwe imadziwika kuti Sadc-PF.
6
Papa Wapempha Akhristu Amenye Nkhondo Yolimbana ndi COVID-19 Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha mayiko omwe ali pa nkhondo ya pachweniweni kuti aleke kuchita izi mmalo mwake atanganidwe ndi nkhondo yolimbana ndi mliri wa Coronavirus. Papa kupemphelera anthu okhudzidwa ndi Coronavirus Iye walankhula izi ku likulu la mpingowu ku Vatican pomwe wati akugwirizana kwathunthu ndi pempho la mlembi wa mkulu wa bungwe la United Nations, Antonio Gutterez lopempha mayiko ndi magulu osiyanasiyana kuti ayambe asiya kuchita nkhondo, pofuna kuyamba nkhondo yolimbana ndi nthenda ya COVID-19, yomwe yavutitsa dziko la pansi. Pamenepa Papa wati nkhondo yolimbana ndi mliri wa Coronavirus ingayende bwino ngati pali ubale wabwino pakati pa anthu a mitundu yosiyana. Mwazina Papa Francisco wapempha anthu omwe akumachitirana zamtopola kuti kuchita izi sikungabweretse kusintha kulikonse pokhapokha atakhala pansi ndi kukambirana, zonse zingatheretu.
6
Mafumu akusunga zitupa za ena Pamene gawo lachitatu la kalembera wa chisankho cha pa 21 May 2019 akuyembekezeka kutha mawa mboma la Lilongwe, anthu ena adandaula kuti akulephera kulembetsa chifukwa mafumu akusunga ziphaso zawo. Mmadera ena omwe Tamvani adazunguliramo, ena adandaula kuti mafumu adawalanda ziphaso za unzika ndipo akupereka ndalama kuti awabwezere zitupazo popita kokalembetsa pomwe mmadera ena akuti anthu akulephera kukalembetsa chifukwa cha miyambo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Zopingazi zaululika pomwe zipsinjo zimene zidalipo mgawo loyamba ndi lachiwiri makamaka zokhudza kuvutavuta kwa zipangizo ndi kamemedwe ka anthu zikuoneka kuti zakonzedwa. Anthu pamalo olembetsera a Malembo kwa T/A Khongoni mbomali Lolemba adati akulephera kukalembetsa chifukwa zitupa zawo za unzika zili ndi mafumu omwe akufuna ndalama kuti awabwenzere zitupazo. Mndondomeko ya kalembera wa ulendo uno, bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) likugwiritsa ntchito chitupa cha unzika chokha ngati umboni woti munthu alembetse mkaundula ndipo popanda chitupachi, munthu sakuloledwa kulembetsa. Mmodzi mwa anthuwo, Moses Phiri, wa mmudzi mwa Salamba adati mafumu adatenga zitupazo ati pofuna kulongosola za kaundula wa sabuside. Mafumu ndi a zamalimidwe adatenga kuti apangire kaundula wa makuponi a sabuside koma akuti pali chikonzero choti mudzi ulionse upereke ndalama yopangira kaundulayo ndiye tikupereka ndalama kwa amfumu kuti akulembe kenako nkukubwezera chitupa chako, adatero Phiri ataombola chitupa chake ndi K500. Woyanganira malo olembetserawo Ezala Nacford adatsimikiza kuti zitupa za anthu ambiri zili ndi mafumu zomwe zikupangitsa kuti anthuwo azilephera kulembetsa. Tabweza mafumu angapo atabwera ndi zitupa zambirimbiri kuti adzalembetsere anthu. Malamulo salola izo. Titafufuza, tapeza kuti eni zitupazo akulephera kukazitenga chifukwa sakupereka ndalama, adatero Nacford. Woyanganira za zisankho ku bungwe la MEC Sammy Alfandika Lachiwiri adati kusunga chitupa cha wina ndi mlandu ndipo adachenjeza kuti aliyense yemwe ali ndi chitupa cha mnzake akuyenera kubweza. Aliyense ayenera kusunga yekha chitupa chake chifukwa chingafunike nthawi iliyonse osati ya kalembera yokha, adatero Alfandika. T/A Khongoni adadabwa atamva nkhaniyi ndipo adati aitanitsa mafumu onse a mdera lake kuti awafunse nkhaniyo ndipo akatsimikiza aona momwe athanirane ndi mafumu omwe akukhudzidwa ndi mchitidwewu. Mmalo ena monga Sonkhwe, Tsachiti, Kasemba ndi Kamphata kwa T/A Kalumbu, ogwira ntchito adadandaula kuti anthu sakufika mwaunyinji kukalembetsa chifukwa cha miyambo. Pa Sonkhwe, anthu 1 698 ndiwo akuyembekezeka kulembetsa koma pofika Lolemba lapitalo, anthu 866 ndiwo adali atalembetsa ndipo woyanganira pamalowo, Lemson Solomon, adati zinthu sizikuyenda chifukwa cha miyambo. Kukuoneka kuti ino ndi nyengo ya ziliza ndi maukwati koamnso chiyambireni kalembera, kwachitika maliro akuluakulu angapo zomwe zachititsa kuti anthu azitanganidwa mmidzi, adatero Solomon. Pamalo olembetsera a Tsachiti, anthu 2 120 akuyenera kulembetsa koma pofika lolemba, anthu 1 115 ndiwo adali atalembetsa ndipo woyanganira malowo David Chikumba adati mmasiku 6 oyambirira, kudagwa maliro anayi mmidzi yozungulira. Kupatula maliro, woyanganira malo olembetsera a Kasemba, Laika Palikena, adati mderalo mudali miyambo ya ufumu iwiri ndi ziliza zomwe zidatangwanitsa anthu. Poyamba kudali mwambo okwenza amfumu a Chimbalame ndipo pano mwambo olonga umfumu wa a Ndunga uli mkati. Kupatula apo kudali maliro atatu komanso ziliza ndiye zinthu sizikuyenda ayi, adatero Palikena. Mkulu wa bungwe la MEC Jane Ansah adati zopinga zokhudza miyambo nzokulira bungwelo koma nzongofunika kukambirana bwino ndi mafumu kuti awone momwe angakonzere zinthu kuti kalembera asasokonekere. Miyambo ngati imeneyi komanso maliro ndi zinthu zomwe zimakhalako nthawi zonse chaka chonse kaya kuli kalembera kapena ayi ndiye nzotikulira koma tiyesetsa kukambirana ndi mafumu, adatero Ansah. Ngakhale zili chonchi, bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) Trust lati akukhulupilira kuti akwanitsa chiwerengero cha anthu omwe akuyembekezera kulemba mgawoli.
8
Sakundikwatira Agogo, Ndithandizeni. Ndili paubwenzi ndi mwamuna yemwe adakwatirapo koma banja lake lidatha ndi mkaziyo ndipo kuli mwana mmodzi. Inenso ndili ndi mwana mmodzi. Titatha chaka tili pachibwenzi adandiuza kuti andikwatira koma mpaka lero padutsa zaka 4 palibe chimene chkuchitika. Foninso adasiya kundiimbira, komanso pan chikondi chachepa. Nditani? BH Zikomo BH, Mwamunayo si wachilungamo ndipo akungokunamiza, za banja alibe nazo ntchito. Ngati ukuti pano zaka 4 zatha chikuuzireni kuti akufuna akukwatire ndipo olo foni sakukuimbiranso, ufuniranji umboni wina woti alibe nawe chikondi? Usataye naye nthawi ameneyo, udzangodikirapo madzi a mphutsi apa. Palibe chako. Akadakhala kuti ali ndi chidwi nawe pano atakaonekera kwa makolo ako ndipo pano bwenzi tikukamba kuti muli pabanja. Ndidalirebe? Agogo, Ndifunse nawo. Ine kwathu ndi ku Rumphi ndipo ndakhala ndili pachibwenzi ndi mnyamata wa ku Mzimba kwa zaka ziwiri tsopano. Sitinagonanepo ndipo tinagwirizana zotengana koma mpaka pano chaka chikuthanso. Ndikamufunsa akuti akonzeke kaye. Kodi ndipange bwanji? Ndidalirebe? Zikomo pondilembera kuchoka ku Rumphiko. Funso lovuta kuyankha mwana wangakodi udalirebe? Inde ndikuti eee, usataye mtima poti kuona maso a nkhono nkudekha. Ngati mnyamatayo akuti akonzeke kaye, mwina akunena chilungamo. Ndi anyamata ochepa amene amatha kukhala pachibwenzi ndi mtsikana kwa zaka ziwiri osagonana naye. Sindidziwa, paja amati mtima wa mnzako ndi tsidya lina, koma mmene ndikuonera fatsa, zoona zake zioneka zokha. Iwe ukuthamangira banja chifukwa chiyani? Mwamunayo ngwanzeru nchifukwa chake akuti akonzekere kaye za ukwati, osangoti lero ndi lero basi tikwatirane uku alibe chilichonse. Ndikudziwa bwino lomwe kuti ku Mzimba ndi ku Rumphi miyambo yokhudza ukwati imafanana, mwamuna akafuna kukwatira amayenera kupereka malobolo, si choncho? Ndiye mwina akusakasaka kaye kuti akamatuma thenga kwa asewere akhale ndi kenakake mmanja, osati kungopita chimanjamanja. Chachikulu nchoti simudagonanepo ndipo ngati ukuona kuti akukunamiza ukhoza kumusiya nkupeza wina amene watsimikiza za ukwati. Nthawi zambiri atsikana ena zikawavuta, tiyese kuti mwatsoka achimwitsidwa ndi wina pamene ali pachibwenzi ndi winanso, amakakamira wachikondiyo kuti akwatirane msangamsanga ncholinga choti azikati pathupi mpamwamunayo! Ndikhulupirira sizili chonchi ndi iwe. Ofuna Mabanja Ndine mayi wa mwana mmodzi ndipo ndikufuna mwamuna wodziwa mavuto, wachikondi, woopa Mulungu koma wopanda banja. 0884 437 604 Ndili ndi zaka 23 ndipo ndifuna mwamuna woti ndimange naye banja. Akhale woti akufunadi banja osati zoyesana ayi. Wofuna aimbe pa: 0992 673 004 Ndine mayi wa ana awiri ndipo ndifuna mwamuna womanga naye banja. Akhale wachilungamo komanso woopa Mulungu.0992 728 276
15
Mnyamata asiya sukulu chifukwa cha mantha A makhumbira atakhala msirikali, koma popanda moyo ntchitoyi singatheke. Lero Christopher Robert, mnyamata wachialubino, wasankha kaye moyo posiya sukulu yomwe ati ikadamuphetsa. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Zochitika pa 6 May 2016, pamene mnyamata wina wosamudziwa adafika pasukulu pawo kudzamutenga ndi zomwe zachititsa kuti thupi la Christopher lichite tsembwe ndi mantha kuti moyo wake ukhoza kukhala pachiswe ndipo walembera aphunzitsi ake kuti wasiya sukulu. Mphunzitsi wamkulu pasukulu ya Mwatonga, kwa T/A Kasumbu mboma la Dedza, wauza Msangulutso kuti patsikulo mnyamata wina adafika pasukulupo nkunena kuti watumidwa kudzamutenga Christopher, wa zaka 18, yemwe ali kalasi 6, chifukwa akumufuna kupolisi ya Dedza. Amati watumidwa, koma nditaimba kupolisi, adandiuza kuti ndimumange, ndipo ndidaterodi, adatero mphunzitsiyu, Felix Mussa. Akuti moyo wake uli pachiopsezo: Christopher Adatsagana ndi mayi ake a Christopher ndi achitetezo cha mmudzi ulendo kupolisi komwe ati adakadzidzimuka akuuzidwa kuti amupepese mnyamatayo chifukwa chomunjata popanda chifukwa. Ine limodzi ndi mayi a Christopher komanso achitetezo tidamupepesa ndipo adamumasula pomwepo, adatero Mussa. Mnyamatayo, yemwe ndi wabisinesi, adauza Msangulutso kuti: Adati ndikatenge amfumu, makolo a mwana ndi mwanayo kuti abwere kupolisi adzafunse zina ndi zina chifukwa amati kunyumba kwawo kudapitako anthu amene ankafuna akamube, adatero iye. Mathedwe a nkhaniyi adatutumutsa Christopher ndipo mantha adayanga thupi lake nchifukwa adaganiza zolembera mphunzitsi wamkuluyu kuti sukulu waisiya. Zikomo Ahedi. Muli kudziwitsidwa kuti ndayamba ndasiya sukulu chifukwa cha nkhani yomwe inachitika Lachisanu. Ndiye ndaona kuti sindingathe kuphunzira chifukwa ndingathe kumakhala ndi maganizo komanso poweruka ndimakhala ndekha ndiye njira ndiyaitali chosadziwika chondichitikra munjiramu pamene ndili ndekha paja poyamba ndinafotokoza kale ndiye panopa ndili pankhawa ngati pangakhale kusamvetsa pazomwe ndanenazi munene tsiku kuti ndibwere kuti tidzakhambirane. Zimene ndinafuna kudziwitsani ndi zomwezi. Ndine Christopher, ikutero kalaya yomwe adalemba Christopher. Mtolankhani wa Msangulutso atamupeza kunyumbako, kudali kovuta kuti alankhulane naye. Adadzitsekera mnyumba, ngakhale ahedi a Mussa, amfumu komanso achibale ena adamuuza kuti asaope, iye adakanitsitsa poganiza kuti mtolankhaniyu wabwera kudzamuba. Padatha mphindi 30, ndipo Christopher adatuluka, mayi ake atakambira naye. Nkhope yakugwa, iye adakhala patali ndi mtolankhaniyu. Ndili wachisoni kuti ndasiya sukulu. Ndimakhumbira nditakhala msirikali, koma basi sindidzakhalanso msirikali chifukwa sukulu ndasiya, adayamba kufotokoza Christopher, amene adakhala nambala 4 mkalasi teremu yatha. Iye adati sakuganizanso atabwerera kusukulu chifukwa chilungamo sichidayende pankhani yake. Ndi bwino andiphere pakhomo pano kusiyana kuti akandiphere kusukulu. Izi zidandipatsa mantha ndipo ndidaganiza zolemba kalatayo kuti ndasiya sukulu. Nakonso kukwaya sindikupita ndipo ndikungodzitsekera mnyumbamu, adatero Christopher, amene bambo ake banja lidatha ndi mayi ake. Wachiwiri kwa mneneri wa polisi ya Dedza, Cassim Manda, adavomera kuti mnyamata amene adapita kusukulu ya Christopher adamutulutsa chifukwa adamangidwa mlandu wosaudziwa. Tikufuna tifufuze kaye ndiye tamutulutsa. Kungoti pali zomwe zidachitika ndiye tikufufuza, adatero Manda, ponena kuti sangayankhe mafunso ambiri pafoni koma pamaso. Ngakhale mutu weniweni wa nkhaniyi sukudziwika bwinobwino, Christopher akuti sabwereranso kusukulu, komwe amayenda makilomita 7 kuchoka kunyumba kwawo. Padakalipano mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wapempha amipingo kuti athandizepo kuti mchitidwe wopha ndi kusowetsa achialubino otheretu.
3
Andale agundika misonkhano, osapewa Covid-19 Msabatayi, anthu ena 5 adapezeka ndi kachirombo ka coronavirus mdziko muno, kuchititsa kuti chiwerengero cha anthuwo chifike pa 63. Chiopsezo cha nthendayi chikukulirakulira. Koma zikuoneka kuti andale sakusamala za izi, pomwe akuchititsa misonkhano mosalabadira kuti nkhani ya gulu ndi chinyezi chofalitsa matendawa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Atangopereka zikalata zawo kwa wapampando wa bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) Jane Ansah, Lazarus Chakwera yemwe akutsatizana ndi Saulos Chilima mumgwirizano wa zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party adazungulira mumzinda wa Blantyre komwe chikhamu chimasonkhana, osapereka mpata wokhala mita imodzi. Ndipo atapereka zikalata zawo, mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika yemwe akuimira zipani za Democratic Progressive Party (DPP) ndi womutsatira wake Atupele Muluzi wa United Democratic Front (UDF) nawo adazungulira mumzindawo mosalabadira za khamu lofikako. Ndipo Lamulungu, Chakwera ndi Chilima adachititsa msonkhano kubwalo la Mzuzu Upper Stadium, pomwe Muluzi adali pamisonkhano yoimaima kuchoka ku chigawo cha kumwera mpaka pakati. Monsemo, kudalibe kutsata ndondomeko yotalikana. Koma akadaulo ena pa zaumoyo ndi ndale ati zipanizi zikuika miyoyo ya anthu pachiswe chifukwa matenda a Covid-19 ndi oopsa. Kadaulo pa zaumoyo Maziko Matemba wati ndale zili apo, atsogoleri a zipani akuyenera kutsatidwa. Kampeni imayenera kutha pa 30 June koma chifukwa choti tsiku la chisankho silinaikidwe, onse okhudzidwa ayenera kudziwa kuti kapmeni iyenera kutha masiku kuchokera tsiku la chisankho, adatero iye. Koma kadaulo wa malamulo Sunduzwayo Madise adati MEC ili ndi udindo wosankha tsiku la chisankho, monga lichitira posankha tsiku la chisankho chapadera. Nyumba ya Malamulo idakhazikitsa tsiku pofuna kutsata malamulo a chisankho kuti psakhale chisokonezo chifukwa nkhani ya chisankho cha patatu chiyenera kutsatidwa. Koma MEC ili ndi mphamvu yokhazikitsa masiku atsopano, monga imachitira pakakhala chisankho chapadera cha aphungu kapena makhansala, adatero Madise. Wapampando wa komiti ya zamalamulo ku Nyumba ya Malamulo Kezzie Msukwa adati adzidzimuka ndi nkhaniyi. Nzodabwitsa kuti MEC ikufuna kuti chisankho chidzakhaleko pa 23 June, adatero Msukwa. Ndipo msabatayi, akachenjede a zamalamulo apempha Mutharika kuti alemekeze chisankhocho pochotsa makomishona a MEC omwe bwalo lamilandu lidawapeza kuti sadayendetse bwino chisankho cha pa 21 May 2019. Mmodzi mwa akachenjedewa, Garton Kamchedzera wa ku Chancellor College adati anthu ali tcheru kuyembekeza tsiku lomwe Mutharika adzachotse makomishonala nkusankha ena. Nchifukwa chiyani sakufuna kutula pansi maudindo? Ndikuona kuti zikanakhala bwino akanatula maudindo awo pa okha. Kupanda kutero, anthu okhanza kupanga chiganizo pazosatira za chisankho chomwe chikubwerachi ndipo kupitirira kukhalabe maofesi sikovomerezeka mmalamulo. Ndipo Mutharika akuyenera kuchitapo kanthu pogwiritsa ntchito section 75 ya malamulo. Gawo 75 ndime 4 imaperka mphamvu kwa mtsogoleri wa dzko kudzera kubungwe la Public Appointment Committee (PAC) ya ku Nyumba ya Malamulo ikapeza kuti komishoniyo ilibe kuthekera koyendetsa masankho. Mipando ya makomishonayo itha pa 5 June pomwe iwo akwaniritse ndime yawo.
11
Akagwira Ukayidi Kaamba Kodyetsa Mwana Chimbudzi Bwalo loyamba la milandu mboma la Kasungu lalamula a Hickson Banda a zaka 26 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavulagaga kwa zaka zitatu kamba kowapeza olakwa pa mlandu odyetsa chimbuzi mwana wake omupeza. Wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sergeant Miracle Mkozi waudza Radio Maria Malawi kuti a Banda adapalamula mulanduwu pa 22 April ndipo mayi a mwanayu atakatula nkhaniyi ku polisi ndi pomwe anamangidwa tsiku lomwelo. Popereka chigamulo chake First Grade Magistrate Damiano Banda adati zomwe adachita a Banda podyetsa mwana chimbudzi ndi zosemphana ndi gawo 240 la malamulo a dziko lino, choncho akuyenera kuti akagwira ukayidi kwa zaka zitatu kuti anthu ena atengerepo phunziro. Panali pa22 April pomwe a Hickson Banda a zaka 26 anasiyiridwa mwana ndi akazi awo omwe anapita kuchigayo ndipo pobwera anapeza kuti mwanayo wadyesedwa bibi ndipo akaziwo anabwera kuzanena ku polisi, anater Mkozi.
7
2019 MSCE Results Out By Thokozani Chapola ele.jpg" alt="" width="452" height="320" />Has released the results-Susuwele Banda The Malawi National Examinations Board (MANEB) has released the 2019 MSCE examination results. According to the annouced results, a total of 98,332 candidates had registered for the examination but 92,867 sat for the examination. The results have been announced by Minister of Education, William Susuwele Banda through a statement. Out of the 92,867 candidates who sat for the examination, 46,771 have passed. This represents 50.36 % pass rate. Out of the 41,708 female candidates who sat for this examination 17,887 have passed. This represents 42.89% pass rate. Out of the 51,159 male candidates who sat for this examination 28,884 have passed. This represents 56.46% pass rate. Out of 573 Special Needs candidates who sat for this examination 302 have passed. This represents 52.71% pass rate. The results of 6 candidates have been withheld pending investigations for contravening MANEB regulations, reads the staterment. The MANEB has also released a list of ten best performing schools in this years MSCE examinations are as follows: Loyola Jesuit Secondary School of Kasungu Marist Secondary School of Dedza Mlare Secondary School of Lilongwe East Lilongwe Islamic (Pvt) Secondary School of Lilongwe West Pius X11 Seminary of Chiradzulu Ludzi Girls Secondary School of Mchinji Zomba Catholic Secondary School of Zomba Urban St Marys Secondary School of Zomba Urban Marymount Catholic Girls Secondary School of Mzuzu City Johns ( Pvt ) Secondary School of Lilongwe City According to the same MANEB, The ten best candidates in this years MSCE examinations are as follows: Ranking Candidate Name Sex Centre Name Aggregate points 1 Arthur Promise Chibondo M Zomba Catholic Secondary School 6 2 Lusako Mwaisango M Chaminade Secondary School 7 3 Misheck A. Masamba M Blantyre Secondary School 7 4 Ruth Paul Bizeck F St. Marys Secondary School 7 5 Yamikani Watson M Zomba Catholic Secondary School 7 6 Bland Benson Mtchona M Maranatha (Pvt) Secondary School 7 7 Harris Ecrem Majamanda M Robert Blake Secondary School 7 8 Gowokani Mkandawire M Chaminade Secondary School 8 9 Wilned Kanyimbo M Marist (Pvt) Secondary School 8 10 Leonard Kadzamira M Marist (Pvt) Secondary School 8 The minister has however congratulated MANEB for releasing free, fair and credible examination results.
3
Gwamba wochokera kubanja loimba Mdziko muno muli oimba osiyanasiyana. koma kukamba za oimba nyimbo zauzimu, Gwamba ndi mmodzi mwa oimba amene akusintha miyoyo ya anthu pa Malawi pano. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Gwamba: Ndi nyimbo zokoma kwambiri Gwamba, ndimasule kuti ndikudziwe bwinobwino mmachezawa. Dzina langa lonse ndi Duncan Gwamba Zgambo omaliza mbanja la ana anayi ndipo kwathu ndi mboma la Rumphi ku mpoto kwa dziko la Malawi. Anthu ambiri amangoti Gwamba, tawauze kuti kodi Gwambayo ndi wotani ndipo amakonda chiyani. Zikomo kwambiri, Gwamba ndi dzina lomwe ndimatchukadi nalo ngati oyimba koma munthune ndimapanga zambiri monga mabizinesi ndi zina. Kuimbaku ndi chimodzi mwa zochita zomwe ndimapanga pamphepete pa mabizinesi. Kodi iweyo zoimbazi udayamba bwanji? Funso labwino ndipo anthu ambiri amandifunsa zimenezi moti ndikayankha iweyo ndiye kuti ndayankha anthu ambiri nthawi imodzi. Munthune ndimachokera ku banja la zoimbaimba. Malume anga, Bright Nkhata, adali munthu waluso kwambiri pa zoimba moti ambiri amamudziwa bwino. Kupatula apo, malume anga ena, Bernard Kwilimbe, nawonso ndiwokonda zoimba kwambiri moti oimba ena mMalawi muno adaphunzira kwa anthu awiri amenewa. Mwachidule, zoyimbazi ndi za mmagazi osati kuchita kuphunzira kapena kukakamiza ayi. Watulutsa chimbale posachedwapa, kodi udachitulutsa liti ndipo chimatchedwanji? Chimbale chimenechi chikutchedwa Jesus is my Boss kutanthauza kuti Ambuye Yesu ndi bwana wanga. Ndi nyimbo ya uzimu yokoma kwambiri ndipo ili ndi tanthauzo ndi chiphunzitso chapamwamba kwa okhulupilira. Chimbale chimenechi chidakhazikitsidwa pa 24 December 2016 ku Bingu International Convention Centre (BICC) ija ena amati 5 Star Hotel. Chimbalechi chili ndi nyimbo zingati ndipo zina mwa izo ndi ziti? Chimbalechi chili ndi nyimbo 11 ndipo papita luso ndikudzipereka kuti chituluke ndi kumveka momwe chimamvekeramu. Kudatengera kudzipereka kwa anthu angapo monga oimba, ojambula ndi azipangizo omwe. Muli nyimbo monga Anabwera Yesu yomwe ndimayikonda kwambiri komanso ndiyo yoyambirira. Mulinso nyimbo yotchedwa Bwana yomwe adathandizira Lulu ndipo nayonso ndi nyimbo yokoma kwambiri. Mwachidule, nyimbo zomwe zili mchimbalechi nzokoma zokhazokha.
9
Radio Maria Itsekera Nyengo ya Mariatona Wolemba: Richard Makombe A Director a Radio Maria Malawi Bambo Joseph Kimu ati wayilesiyi ikukwanitsa kufalitsa uthenga wabwino wa yesu khristu ngakhale ili ndi ngongole zoposa 50 million kwacha. Bambo Joseph Kimu amayankhula izi pa mwambo wa nsembe ya ukaristia otsekera nyengo ya Mariatona omwe unachitikira ku Mtendere Parish mu dayosizi ya Dedza. Bambo Kimu ati ndiokondwa kuti anthu ambiri amamvera wayilesiyi kuphatikizapo anthu omwe si a mpingo wa katolika zomwe anati ndi chisonyezo kuti zikulimbikitsa anthu kukonda kupemphera. Anali mlendo wolemekezeka pa mwambowo- a Bonga ndi akazi awo Pali anthu ena ambiri omwe amathandiza wayilesiyi omwe ndi a mipingo ina ndipo izi zapangitsa kuti Radio Maria ikhale ikufalitsa uthenga wabwino wa yesu khristu kuyambira pomwe inatsegulidwa zaka 20 zapitazoanatero Bambo Kimu. Bambo Kimu anapitiliza kupemph anthu onse akufuna kwabwino komanso akhristu kuti apitilize kuthandiza komanso kuyikonda wayilesiyi kuti izikwaniritsa cholinga chake chofalitsa uthenga wabwino kwa anthu ambiri. Ndikupempheni kuti mupitilize kupemphelera Radio Maria komanso muzikonda kugwiritsa ntchito wayilesiyi mu zochitika zanu kuti uthenga wa mulungu upilire kufalikira ponseponseanapitiliza motero Bambo Kimu. Bambo Kimu anati Ndikudziwa kuti muli ndi mavuto a zachuma pano pa Parish komanso mmanyumba mwanu koma munaona kuti nkofunika kuti muthandize Radio Maria ndithokoze kuti mwaonetsa chikondi chomwe muli nacho ku wayilesiyi Mmawu awo Monsignor John Chithonje anati akuthokoza a Director a wayilesiyi kamba kosankha kudzachitira mwambo otsekera Mariatona ku dayosizi ya Dedza zomwe ati zikusonyeza ubale wabwino omwe ulipo pakati pa dayosiyi yi ndi Radio Maria Malawi. Dayosizi ino ndiyokonzeka kuthandiza Radio Maria nthawi ina iliyonse ndipo timayesetsa kuthandiza kuti ntchito zake zipitilire kupita patsogolo anateroMonsignor Chithonje. Monsignor Chithonje anathokoza kwambiri akhristu a Parishi yi kamba kotenga gawo pothandiza wayilesiyi zomwe anati zaonetsa ubale omwe ulipo ndi wayilesiyi komanso kuti amayikonda Radio Maria. Ntchito yomwe Radio Maria ikugwira yathandiziranso kuti ubale wathu ndi akhristu a mdziko la Mozambique ukhale opambana komanso wamphamvundipo zaonetseratu kuti akhristuwa amakonda kumvera wayilesiyianatero Monsignor Chithonje Nyengo ya Mariatona inatsegulidwa ku Sacred Heart Zomba Cathedral ku Zomba dayosizi pa 4 May ndipo yatsekedwa pa 27 July 2019 ku Mtendere Parish mu dayosizi ya Dedza. Pa mwambowu ndalama zokwana 1 million six hundred and fifty 9 hundred forty kwacha ndi zomwe zinapezeka ndipo mlendo olemekezeka pa mwambowu anali a Mike Bonga omwe anapereka cheke cha ndalama zokwana 5 hundred thousad kwacha.
13
Youth Week ibwereredi Achinyamata, mafumu Mtsogoleri wa achinyamata pa ndale wa bungwe la Young Politicians Union Clement Mukuwa wati ndi wosangalala ndi ganizo la boma lofuna kukhazikitsanso sabata ya achinyamata (Youth Week) chifukwa likugwirizana ndi zomwe achinyata adaika pamndandanda wa zolinga zawo. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Tili ndi mndandanda wa zomwe tikufuna achinyamata atamachita ndipo chimodzi mwa izo ndi kugwira ntchito modzipereka ndiye tikakumbuka zomwe Youth Week inkachita, zikugwirizana ndi mfundo imeneyi, adatero Mukuwa. Kudikira kuti boma likonze: Munthu kuoloka movutikira paulalo woonongeka Phungu wa kumpoto cha kummawa kwa boma la Mchinji, Alex Chitete, ndiye adayambitsa nkhaniyi mNyumba ya Malamulo pomwe aphungu amaunika momwe chuma cha dziko chayendera pamiyezi isanu ndi umodzo (6). Phunguyu adapempha boma kuti likhazikitsenso sabata ya achinyamata monga zidalili mnthawi ya ulamuliro wa malemu Dr. Hastings Kamuzu Banda pomwe achinyamata mdziko muno adali ndi sabata yogwira ntchito zachitukuko mmadera awo pofuna kuwaphunzitsa za ubwino wogwira ntchito modzipereka potukula dziko lawo. Iye adati panthawi ya ulamuliro wa chipani chimodzi achinyamata ankatenga gawo lalikulu pachitukuko kusiyana ndi masiku ano pomwe kuli ntchito zogwira ndi chiyembekezo cholandira dipo yomwe akugwira ndi anthu akukuluakulu. Poyankhapo, nduna ya zantchito Henry Mussa adati ganizoli si loipa koma silokakamiza ndipo mmapulani a boma muli kale ndondomeko zomwe akuti achinyamata azipatsidwa mpata kutenga nawo mbali pantchito zina. Iye adati mundondomekoyi, ntchito zina zomwe zizigwiridwa ndi zachitukuko monga momwe zinkakhalira mnyengo ya Youth Week kalelo. Tidayankha kale pankhani imeneyo kuti si zokakamiza koma ndondomeko ilipo kale moti pompanopompano ziyambika, adatero Mussa. Mukuwa adati ngati mtsogoleri wa achinyamata pandale akhoza kukhala wokondwa anthu atadziwitsidwa ubwino wa Youth Week ndi zolinga zake kuti mtima wogwira ntchito wodzithandiza posayembekezera malipiro ubwerere mwa Amalawi. Katswiri pa mbiri ya dziko lino, Desmond Dudwa Phiri (DD Phiri), ndi mafumu angapo akuluakulu ati ganizo lokhazikitsanso sabata ya achinyamatali ndi lofunika kwambiri pachitukuko cha dziko la Malawi. DD Phiri adati Youth Week ndi nyengo yomwe achinyamata ankatengapo mbali pachitukuko chosiyanasiyana ngati nzika za dziko mwaulere ndipo izi zinkathandiza kutula midzi ndi madera omwe ankakhala. Nthawi imeneyi achinyamata ankakhala otangwanika kwambiri pantchito zachitukuko monga kukonza misewu, milatho, zipatala, sukulu ndi zina mmadera mwawo mwaulere ndipo zinthu zinkayenda, adatero mkhalakaleyu. Iye adati ntchito ngati zomwezi, pano zimalira bajeti yaikulu kuti anthu agwire, mapeto ake ndalama zikasowa, zitukukozi zimayamba zaima kwa nthawi yaitali, zinthu nkumapitirira kuonongeka. Youth Week inkakhalako chaka chilichonse nyengo ngati ino ya Pasaka ndipo tinkadziwiratu kuti misewu yonse yoonongeka, milatho, zipatala, sukulu ndi nyumba za aphunzitsi zomwe zikuonongeka zikonzedwa. Pano ntchito ngati zimenezi zimalinda ndalama za mbajeti kuti anthu kapena makontirakitala azigwire. Ngati ndalamazo palibe, ndiye kuti zinthuzo zizingopitirira kuonongeka mpaka ndalama zidzapezeke, adatero DD Phiri. Mkuluyu adati Youth Week idatha mdziko muno mutabwera ulamuliro wa zipani zambiri poganiza kuti idali nkhanza kwa anthu (thangata) ndipo mmalo mwake boma lidasenza lokha udindo wogwira ntchito zachitukuko. Iye adati koma anthu sankaona Youth Week ngati thangata ndipo ankagwira ntchito modzipereka ndi umodzi mpaka pomwe adauzidwa kuti ndi thangata. Mkulu wodziwa za mbiri yakaleyu adati maiko ambiri omwe ndi otukuka pano adayamba ndi eni ake kudzithandiza ndipo boma linkangobwera pambuyo kudzawonjezera pomwe paperewera. Mfumu yaikulu (T/A) Maseya wa ku Chikwawa akugwirizananso ndi ganizoli ponena kuti achinyamata amaphunzira ntchito zosiyanasiyana panyengoyi chifukwa amasakanikirana ndipo omwe adali ndi luso amagawira anzawo pogwira ntchitozo. Iye adati kudzera mnjira imeneyi, achinyamata amakula ndi mtima wokonda ntchito ndiposo zimawathandiza kukhwima mmaganizo kuti paokha akhoza kupanga chinthu chooneka popanda kuyanganiridwa. Zidali zokoma kwambiri moti zitati zayambiranso zikhoza kukhala bwino kungoti nzofunika kuti poyambitsapo aunike bwinobwino kuti ntchitozo angazigawe motani potengera zaka kuti zisakolane ndi nkhani yogwiritsa ana ntchito yoposa msinkhu wawo, adatero Maseya. Inkosi Chindi ya ku Mzimba idasangalalanso ndi ganizoli ponena kuti nyumba zambiri zophunziriramo, zokhalamo aphunzitsi, milatho ndi misewu zomwe pano zili ngati bwinja zikhoza kukonzedwa mosavuta. Chitukuko cha kudera ndi udindo wa anthu okhala kudera limenelo ndiye anthu atafotokozeredwa bwinobwino phindu lomwe angapeze kuchoka muntchito zachitukuko cha Youth Week, sindikukhulupirira kuti angawiringule, adatero Chindi. Iye adati munyengoyi, achinyamata amagwira ntchito zosiyanasiyana monga kulambula misewu, kukonza milatho, nyumba za aphunzitsi ndi zitukuko zina uku akutayitsa nthawi ndi macheza. Naye T/A Mkanda ya mboma la Mchinji idati ana ambiri masiku ano amalephera kupita kusukulu nyengo ya mvula kaamba kolephera kuoloka mitsinje chifukwa chodikirira kuti boma likonze milatho.
10
Tigwirane manja pothana ndi chisaka cha Nthochi Mkulu woona za mbewu za mgulu la zipatso ku dipatimenti ya za kafukufukuku mu unduna wa zamalimidwe Felix Chipojola akuti nkhondo yolimbana ndi matenda a chisaka cha nthochi mdziko muno siingaphule kanthu pokhapoka anthu atagwirana manja. Iye adafotokoza kuti njira yokhayo yothana ndi chisaka ndikuchotsa nthochi zonse zakale ndikubzala zina. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kukakamira nthochi zakale kukuchititsa kuti chisaka chizipitirira Chipojola adati mzomvetsa chisoni kuti alimi ena sakufuna kudzula nthochi zawo zakale zomwe zikuchititsa kuti matendawa asathe msanga mdziko muno. Tidakagwirana manja ndikuonetsetsa kuti nthochi zonse zakale zachotsedwa, matendawa akadatha ndipo mdziko muno bwenzi mukupezeka ntchochi zochuluka, iye adatero. Malingana ndi mkuluyu, ngakhale alimi omwe adachotsa nthochi zakale ndikubzala zopanda matenda ali pachiopsezo cha matendawa chifukwa amzawo sakufuna kudzula nthochi zawo zakale zomwe zikhoza kuchititsa za tsopanozo kuti ziyambenso kugwidwa ndi matendawa. Chipojola adati matenda a chisaka cha ntchochi amafala ndi nsabwe zomwe zimatha kuulukira mminda ina. Ena akumaputsitsika akaona nthochi zawo zikuoneka za thanzi koma akuyenera kudziwa kuti matendawa amabisala ndipo tsiku lina amadzavumbuluka, iye adatero. Woona za ulimi wa mbewu za mtunduwu kwa Bvumbwe Harold Katondo adati adayendera mmaboma momwe mumalimidwa kwambiri nthochi mdziko muno ndicholinga chofuna kupeza zomwe zikuchititsa kuti alimi azikakamirabe mbewu zakale. Pocheza nawo alimiwa amafotokoza kuti mbewu zawo zakale nzokoma kwambiri komanso amatha kuzigwiritsa ntchito kuphikira zinthu zosiyanasiyana. Chodabwitsa nchoti ngakhale amayankhula zoterezi, sadayetserepo kulima kapena kudya nthochi zatsopanozi, iye adatero. Katondo adati izi zachititsa kuti ayambe kutolera mbewu zakalezi mmadera osiyanasiyana a mdziko muno ndikuzikonza kuti zikhale zopanda matenda. Iye adati akazikonza ndikuzichulukitsa adzazibwezera kwa alimi kuti azidzabzala. Mkulu wa za ulimi mboma la Thyolo Jackson Mkombezi adati alangizi mbomali adayesetsa kuwafotokozera alimi za njirayi koma ntchito ya kalavula gaga yomwe imakhalapo pochotsa ntchochi ndiyomwe ikuchititsa kuti mbewu zakale zizipezekabe. Ntchitoyi ikadakhala yosavuta ikadayenda mwachangu ndipo nthochi zambiri zikadachotsedwa ndikubzalidwa zina zopanda matenda, iye adatero. Mkuluyu adati alimi omwe adabzala mbewu zopanda matenda mu 2015 pano akutsimba lokoma ndipo ambiri akupeza zokolola zamnanu. Mulanje ndi limodzi mwa maboma omwe ulimiwu umachitika kwambiri moti mkulu wa za ulimi mbomalo Evelyn Chima akuti kuchepa kwa mbewu ndi ena mwa mavuto omwe amachititsa kuti azikakamirabe mbewu zakale. Poyambirira tidalandira mbewu yochepa moti alimi omwe adavomereza kubzala mbewu zopanda matenda sadalandire onse. Chaka chino talandira mbewu yochuluka komanso alimi ena tawaphunzitsa kuti azitha kuchulukitsa ndikumagaira anzawo. izi zithandizira kuti anthu ochuluka apeze mbewu, iye adatero. Chima adati alangizi a mbomali akuyesetsa kugwira ntchitoyi ndi atsogoleri a mipingo, mabungwe komanso zipani ndi cholinga chofuna kupititsa patsogolo ulimiwu.
4
Sitima Ya Papa Francisko Ikupulumutsa Miyoyo Sitima ya pa madzi yotchedwa Papa Francisco ikupereka thandizo la chipatala ku madera a mtsinje wa Amazon mdziko la Brazil. Malinga ndi malipoti a Vatican Radio sitimayi ikupereka chithandizo cha zipangizo za mchipatala kumidzi ya pafupi ndi mtsinje wa Amazon kwa anthu omwe akuvutika chifukwa cha mliri wa Coronavirus. Sitimayi akuti yapulumutsa miyoyo komanso kubweretsa chiyembekezo pakati a anthu a ku deralo. Pamene mliri wa Coronavirus ukupitilira kuvutitsa maiko ambiri anthu a ku dera la mtsinje wa Amazon mdziko la Brazil ndi oyamika kaamba ka sitima ina ya pa madzi yotchedwa Papa Francisco yomwe ikuthandiza anthu ku deralo ndi zipangizo za mchipatala pa nthawi iyi ya mliri wa Coronavirus. Sitimayi ili pa ntchito yolimbana ndi mliri wa Coronavirus pothandiza omwe akudwala komanso kuteteza awo omwe sanagwide ndi nthendayi. Malinga ndi Joel Sousa bulazala wa chipani cha Francisco Woyera wa ku Assisi, sitimayi akuti yabweretsa chiyembekezo komanso yapulumutsa miyoyo ya anthu ambiri ku deralo. Sitimayi yakhala ikuthandiza anthu ku deralo kuyambira mwezi wa July mchaka cha 2019 ndi chithandizo cha chipatala koma kuti panopa ogwira ntchito mu sitimayi ali pa ntchito yolimbana ndi mliri wa Coronavirus. A bulazala komanso ansembe a chipani cha Francisco Woyera wa ku Assisi ndiwo eni ake a sitimayi ndipo iwo akuti analimbikitsidwa pa ntchito yopereka chithandizo cha chipatala kwa anthu mderalo ndi Papa Francisco pomwe anali ku Brazil pa chaka cha achinyamata (World Youth Day) mchaka cha 2013. Sitima yotchedwa Papa Francisco yi ili ndi anthu 23 odziwa ntchito za chipatala, zipinda momwe anthu amalandira thandizo, chipinda chopangira ma opareshoni, chipinda chopimira anthu mmene aliri mthupi mwao pongotchula zochepa chabe. Dziko la Brazil ndi limodzi mwa maiko omwe akhudzidwa kwambiri ndi mliri wa Coronavirus pokhala pa nambala 2 pa mndandanda wa maiko omwe chiwerengero cha anthu omwe agwidwa ndi nthenda ya Covid 19 ndi chokwera kwambiri. Anthu pafupi 1.9 million agwidwa ndi nthenda ya Covid 19 mdziko la Brazil kutsatira dziko la United States of America lomwe lili pa nambala 1 pa chiwerengero cha anthu omwe agwidwa ndi nthenda ya Covid 19. Malinga ndi malipoti a pa 14 July 2020 a sukulu ya ukachenjede ya John Hopkins anthu 72,833 amwalira ndi nthenda ya Covid 19 mdzikolo. Ndipo ndi pa tsiku lomweli la 14 July 2020 pomwe likulu la Mpingo wa Katolika pa dziko lonse linalengeza kuti Papa Francisco watumiza thandizo ku dzikolo la zipangizo zothandiza anthu omwe akuvutika kupuma bwino kuti athe kupuma mosavutika (ventilators).
14
Papa Wadzudzula Mchitidwe wa Tsankho Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco walimbikitsa anthu pa dziko lonse kuti akuyenera kumachita zinthu mosakondera kamba koti izi ndi zomwe zimasangalatsa Mulungu. Papa Francisko Iye wanena izi pakutha pa mwambo wa mapemphero a lero mmawa ku likulu la mpingo-wu ku Vatican. Iye wati pofuna kupereka thandizo la mtundu wina uliwonse anthu akuyenera kuti azipewa kuchita tsankho kamba koti izi ndi zosayenera pa maso pa Mulungu. Iye wati Mulungu akamapereka thandizo ndi chisamaliro chake samayanganira khalidwe la munthu kaamba koti chikondi chake ndi chopanda malire.
14
Dziko la Ghana Latsekula Malo Opemphelera President wa dziko la Ghana Nana Akufo-Adodo watsekula malo opempherera omwe anatsekedwa pofuna kupewa kupatsirana kwa kachilombo koyambitsa nthenda ya COVID-19 mdzikolo. Walengeza za nkhaniyi- Akufo-Addo Malipoti a wailesi ya BBC ati malowa ndi monga matchalitchi komanso mizikiti ndipo anthu osaposa 100 ndi omwe akuloredwa kumasonkhana mu nthawi yosapitilira ola limodzi. Anthu omwe akusonkhana mmalo opemphelerawa apemphedwa kupitiliza kutsatira njira zopewera kupatsirana matendawa monga kukhala motalikirana komanso kuvala chotchinga kukamwa ndi mphuno (Mask) pomwe akupemphera. Mwazina presidenti-yu wati kuwonjezera apo ophunzira a mchaka chomaliza ayambanso kupitiriza maphunziro awo ndipo mzipata zolowera mdzikolo zikhalabe zotseka. Ganizoli ladza pomwe chiwerengero cha anthu opezeka ndi nthendayi chaima pa 8,060 omwe ndi kuphatikizapo 36 omwe amwalira ndi nthendayi.
13
Khama lipindula paulimiPhungu Nthawi zambiri chomwe chimasowa paulimi ndimasomphenya. Alimi ambiri amangolingalira zoti ndikakolola chaka chino ndidzalimanso chaka cha mawa mmalo moti azilingalira kuti chaka chino ndalima ndipo chaka chamawa ndidzakhale pena. Phungu wa kunyumba yamalamulo wa ku mpoto kwa boma la Mangochi Benedicto Nsomba ndichitsanzo chabwino pankhaniyi. Iye adayamba ngati mlimi ochulukitsa mbeu nkusuntha kufika pogulitsa mbeu ndipo pano ali ndi kampani yakeyake yopanga mbeu. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere: Nsomba: Mbewu zanga nzovomerezeka ndi boma Ndikudziweni olemekezeka. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Benedicto Chambo ndipo, monga mwanena kale, ndine phungu wa ku Nyumba ya Malamulo woimira anthu a kumpoto kwa boma la Mangochi. Kunyumba ya Malamuloko ndilinso mukomiti ya zaulimi komanso pandekha ndimalima kwambiri. Inu mulinso ndi kampani yopanga mbewu, kodi mbiri yanu ndi yotani? Za inetu anthu ambiri sakhulupirira ayi. Ndidayamba zaulimi ngati mlimi wochulukitsa mbewu pansi pa gulu la Association of Smallholder Seed Multipliers Action Group mchaka cha 2005. Nditachitapo ulimiwu ndidasuntha nkuyamba kugulitsa mbewu nditatsegula Chambo Agro- Dealers ku Mangochi komweko. Ndagulitsa mbewu mpaka kufika pomwe ndimatsegula kampani yanga yopanga mbewu ya Pindulani Seed Company. Chiyambi chake nchotani? Mchaka cha 2010 ndidaona kuperewera kwa mbewu za gulu la nyemba pamsika ndiye ndidaganiza zoyamba kupanga mbeuzi. Ndapangapo mbewu za mgulu la nyemba kwa zaka ziwiri mpaka kufikira mchaka cha 2013 pomwe ndidaonjezera nkuyamba kupanganso mbewu ya chimanga kufikira pano. Muli ndi msika wa mbewu zanu? Kwambiri ndipo mbewu zanga ndi zimodzi mwa mbewu zomwe alimi ambiri akukonda chifukwa zimamera ndi kubereka mwapamwamba kwambiri. Mwinanso ndikuuzeni pano kuti boma lidavomereza mbewu zanga moti pano zili mupologalamu ya zipangizo zotsika mtengo ya sabuside. Apa ndikutanthauza kuti mbewu ina yomwe alimi alime kuchokera musabuside ya mgulu la nyemba komanso chimanga ndi yopangidwa ndi kampani yanga ya Pindulani. Mumapanga mbewu yochuluka bwanji pachaka? Poyamba penipeni ndidayamba ndi matani 10 okha ndipo ndimanka ndikukwera pangonopangono mpaka pano ndidakula ndithu. Chaka chino ndapanga matani 340 a mbewu zosiyanasiyana za mgulu la nyemba ndinso matani 150 a chimanga chamakono chopirira ku ngamba chomwe boma ndi akatswiri akulimbikitsa. Ndili wokondwa kuti mbewu zonsezi zidatengedwa mupologalamu ya sabuside. Inu mbewu zanu mumazitenga kuti? Si njere iliyonse yomwe ili mbewu. Nzoona, si njere iliyonse ungabzale nkumati ndi mbewu. Ine ndili ndi alimi anga ochokera kudera langa omwe ndimagwira nawo ntchito. Ndimawapatsa mbewu kuti achulukitse ndipo ndimawagula pamtengo wabwino ngati njira imodzi yowatukulira. Alimi ambiri panopa kudera kwanga adatukuka moti amangamanga nyumba zamakono za malata kumeneko kuchokera mu ntchito imeneyi. Tinene kuti mudaima pambewu zamitundu iwiriyi basi? Ayi, ndiye kuti mutu wasiya kuganiza. Lingalirani komwe ndikuchokera kudzafika pano ndiye ndiimire pano? Pakalipano tikuchita kafukufuku wa mbewu za mtedza ndi nyemba zoyenera mthirira zomwe zotsatira zake zikatuluka tikhala tikulimbikitsa alimi kuti azichita ulimi wamthirira wa mbewuzi. Kupatula apo, tikuchitanso katupe wa mbewu zamakono za chinangwa ndi mbatata zamthirira moti ntchito imeneyi yakhala pangono kutha kuti tiyambe kugulitsa mbewu yake. Eni makampani opanga ndi kugulitsa mbewu amadandaula za akamberembere omwe amakopera mbewu zawo nkumaononga mbiri yawo, kaya inu mudakumanapo nazo zotere? Zimenezo nzoona, akamberembere alipodi koma chimachititsa kwambiri ndi ogwira ntchito kumakampaniko omwe ali osakhulupirika chifukwa ndiwo amatenga mapaketi nkumakagulitsa kwa akamberemberewo kuti aziikamo mbewu yachinyengo. Komabe pobwerera kufunso lanu, ife zimenezi sitidakumanepo nazo chifukwa tidapanga njira yoti mapepala a umboni aja amati seal oika mkati mwa paketi, timapanga tokha ndiye olo atapeza mapaketi athu, seal ikhoza kuwasowa. Alimi ambiri amakakamira pamodzimodzi zaka nkumapita, inu mungawauzenji? Nkhani yaikulu ndi kukhala ndi masomphenya basi. Kumaona patali kuti kodi ineyo lero ndili pano nanga mawa ndidzakhale pati? Mlimi akakhala ndi maganizo otere, zinthu zimayenda chifukwa amayesetsa kuti maloto ake aja akwaniritsidwe, asafere mmalere. China, pamafunika kulimba mtima pochita zinthu chifukwa ukakhala ndi mantha ndiye sizingakuyendere mpangono pomwe. Kupatula kuyendetsa kampani ya mbewu, pali china chokhudza ulimi chomwe mumapanga? Ndili ndi sikimu zingapo ku Mangochi komwe ndimachitirako ulimi wamthirira wa mbewu zosiyanasiyana. Ndidalemba alimi oposa 1 500 nkuwagawira malo musikimumo kuti azilima. Akakolola, ndimawagula mbewuzo pamtengo wabwino komanso zina zimakhala zawo zakudya pakhomo. Mwezi wa October alimi adakolola nyemba zambiri ndipo ndidawagula zonse pamtengo wa K600 pakilogalamu moti pano ambiri ali ndi ndalama, savutika nyengo yachisangalaloyi.
4
Mayi amwalira kokafuna golide Mayi wa zaka 36 wamwalira ku Salima pamene dothi la mumtapo wa golide yemwe amafunafuna litamugwera iye ndi mwamuna wake. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Mneneri wa apolisi ku Salima Gift Chitowe watsimikiza za nkhaniyi pouza Msangulutso Lolemba lapitali kuti nkhaniyi idachitika pa 8 January chaka chino pamene mayi womwalirayu, Elinati Mkaundu, pamodzi ndi mwamuna wake adanyamuka kumudzi kwawo kupita kumudzi wa Sadzu komwe ankafuna kukayesera mwayi wawo kokafuna miyala yamtengo wapatali yotchedwa galanayiti. Chitowe adati atafika kumalo komwe kunali mtapoko mayiyo ndi mwamuna wake adafikira kulowa mdzenje la mtapolo ndi kuyamba kufunafuna miyala ija koma mwatsoka dothi lomwe lidali mudzenjemo lidawagwera ndipo mayiyu adamwalira pomwepo pamene mwamuna wake adavulala thupi lonse ponyukanyuka.
6
Chiwerengero Chamatenda Opatsirana Chakwera Kwambiri Mmaiko a mu Africa-WHO By Glory Kondowe .radiomaria.mw/wp-content/uploads/2019/07/who-300x150.jpg" alt="" width="452" height="226" /> Bungwe lowona za umoyo pa dziko lonse la World Health Organisation (WHO) lati chiwerengero cha anthu omwe akugwidwa ndi matenda a chikuku ndinso matenda ena opatsirana chakwera kwambiri chaka chino mmaiko ambiri a mu Africa. Malinga ndi malipoti a news24, bungwe la WHO lati chiwerengero cha anthu opezeka ndi matendawa, chakwera ndi 700% mchaka chino chokha cha 2019. Bungweri lati izi zikuchitika chifukwa maikowa sakupereka katemera wa matendawa mokwanira kwa anthu awo kuti chiwerengero chamatendawa chitsike.
6
Adatuma nthenga kudzandifunsira Kudali ku Dedza, mwezi wa October mchaka cha 2017 pomwe Lucy Mvula adalandira uthenga kuchokera kwa mzake wa Geoffrey Kishombe. Uthengowo umati Kishombe akulephera kugona kotero akumufuna chibwenzi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Koma Lucy sadaugwiritse ntchito uthengawo chifukwa choti wobweretsa nthengayo adali ankakonda kuledzera ndipo pomwe ankapereka uthengawo patsikulo nkuti atalawa pangono. Koma nthengayo adabweranso tsiku lina maso ali gwaa kudzatsindika za khumbo la Kishombe. Ndipo adandipatsa nambala ya phone ya nzawoyo ndipo ine ndidapereka yanga, adatero Lucy. Lero ndi thupi limodzi: Banja la a Kishombe Apatu awiriwo adakhala masiku ndithu osayankhulana mpaka pomwe tsiku lina Kishombe adamuimbira Lucy ndipo ichi chidasanduka chizolowezi kufikira tsiku lomwe adagwirizana zoti akumane. Tsiku lokumana litafika, Kishombe, pamodzi ndi anzake ena awiri adapita kunyumba kwa Lucy kukacheza, zomwe zidachititsa kuti macheza awo agwire moto. Mosakhalitsa, Kishombe adafunsira ndipo naye Lucy sadazengereze koma kulola. Ndidatengeka kwambiri chifukwa cha momwe ankandizondera. Ankakonda kuimba foni kungofuna kudziwa za moyo wanga, adatero Lucy. Awiriwo adakhala pa ubwenzi kwa zaka ziwiri kufikira pa November 19 2019 pomwe adalowa mbanja ndipo madyerero adachitikira pa Greek Orthodox Garden, mu mzinda wa Blantyre. Awiriwo ati mavuto awo amathana nawo poyangana kwa Mulungu. Lucy amagwira ntchito yaunamwino ndi uzamba pomwe Kishombe amagwira ntchito ku bungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS). Pakadali pano awiriwo akukhalira ku Chigumula mu mzinda womwewu wa Blantyre koma Lucy amachokera ku Euthini, mfumu Chindi mboma la Mzimba ndipo Kishombe amachokera mmudzi mwa Mwafilaso, mfumu Kyungu mboma la Karonga.
15
Chiyembekezo pa ntchito zakunja Ofuna ntchito ku Lilongwe ngati awa akufuna boma likonze zolakwika Pamene boma lalengeza kuti likulingalira zoyambanso kutumiza achinyamata kukagwira ntchito kumaiko ena, osowa ntchito ena ati ngakhale ndondomekoyi ndi yabwino, akukayika ndi momwe amasankhira okagwira ntchito kunjako. Mneneri wa unduna wa za ntchito, Joyce Maganga, adati ntchito yotumiza achinyamata kunja imene idayamba muulamuliro wa Joyce Banda ipitirira. Iye adatsutsa kuti chipani cha DPP chidaimika ntchitoyi, imene achinyamata 100 000 amayenera kupeza mwayi wa ntchito ku South Korea, Quatar ndi Dubai. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chifukwa choti ntchitoyi idayamba ndi mtsogoleri wakale wa dziko lino, sizikutanthauza kuti ikuyenera kuimitsidwa kapena kutayidwa. Mtsogoleri wa dziko lino [Peter Mutharika] ali ndi ndondomeko zatsopano zopitirizira pologalamuyi, adatero Maganga. Malinga ndi nduna yakale ya achinyamata, Enoch Chihana, boma limafuna kuti achinyamata 2 000 atumizidwe kunja koma lidangokwanitsa kutumiza 800 okha, makamaka ku Dubai. Achinyamata 15 000 adayesa mwayi wawo pachilinganizo choyamba koma adapeza mwayi sadapose 1 000. Koma achinyamata ena, ati akukayika ngati osauka apindule pachilinganizochi. Alfred Limbani wa zaka 29 ndipo amakhala ku Area 36 mumzinda wa Lilongwe adati adakondwera pomwe adamva kuti boma la Joyce Banda liyambitsa ndondomekoyi. Koma mvula ya masautso ake a ulova sidakate momwe amayembekezera. Ndidakondwa nditamva kuti kukudza mwayi wa ntchito. Koma sindidamve bwinobwino kuti opitawo amawasankha bwanji. Adatenga achinyamata. Zoti chilinganizochi chipitirira ndi nkhani yabwino koma tipemphe boma latsopanoli kuti libweretse poyera ndondomeko zotengera achinyamata ena ulendo uno komanso enafe tipindule nawo, adatero Limbani. Sibongile Manda, wa zaka 26, adati boma likuyeneranso kubwera poyera malinga ndi malipoti ena oti achinyamata ena amene adapeza mwayiwo amazunzika. Boma liyenera kukayendera kaye malo antchitowo kuti lionetsetse kuti achinyamata sakukumana ndi mavuto kumeneko. Komanso litenge ambiri kuti nafenso tipeze chochita, adatero Manda. Izi zidapherezera lipoti la Amnesty International limene mmbuyomu lidasonyeza kuti maiko monga South Korea ndi Qatar amazunza ogwira ntchito awo, makamaka amene akugwira ntchito zammunsi komanso ochokera kumaiko akunja. Komatu chiyembekezochi sichili ndi achinyamata okha. Nawo akuluakulu monga Cydric Brazilo wa zaka 35, ali maso kunjira. Koma iye adati zachinyengo zimene zimachitika pandondomeko ya mmbuyomu zisakhaleko. Pologalamuyi tidaimva koma anthu timafooka nayo chifukwa choti kasankhidwe ka achinyamata okagwira ntchitoyi kamaoneka ngati kachinsinsi. Tikuona ngati adapita abale awo a akuluakulu a boma okha basi. Mnzanthu wina adapereka K15 000 nkulembedwa dzina kuti apita koma adamuyenda pansi. Pano akadali lova kwawo ku Kasiya, adatero iye. Kulipira ndalama kotere, malinga ndi Patrick Bvumbwe wa zaka 44, nkusupula amphawi amene akufuna ntchito. Mmbuyomu zimamveka kuti wofuna ntchito apereke ndalama, tsono amphawife tizipeza kuti ndalamazo? adatero iye. Malinga ndi Maganga, ntchitoyi idakumana ndi mikwingwirima ku South Korea kokha. Ngakhale boma linkati lidagwirizana ndi boma la South Korea kuti litumizako achinyamata, mmodzi mwa akuluakulu oona za kunja kwa dzikolo Moon Sung Hwan adati padalibe mgwirizano ulionse pakati pa maboma awiriwo. Vuto tinali nalo ndi lokhudza dziko la South Korea. Kumeneku kokha ndiye ntchitoyi tidaimitsa kaye. Koma kumaiko a Dubai ndi Kuwait ikupitirira, adatero mneneriyo. Mlembi wamkulu wa ungano wa mabungwe oyanganira apantchito wa Malawi Congress of Trade Union (MCTU), Elijah Kalichero, adati bungwelo lakhala likutsutsana ndi ndondomekoyi chifukwa achinyamata ambiri amakumana ndi zokhoma kumaiko achilendoko. Takhala tikulandira malipoti oti achinyamata ambiri amazunzidwa ndi kugwira ntchito zakalavulagaga kumaiko kumene amapitako. Komanso ambiri akugwira ntchito zosiyana ndi zimene adalonjezedwa. Ena akufunitsitsa atabwerera kuno kumudzi, adatero Kalichero. Tidalephera kulankhula ndi nduna ya zantchito Henry Mussa kuti timve ndondomeko zimene boma lakonza kuti mavuto amene adalipo mmbuyomu athe chifukwa samayankha foni yake.
15
Tidakhulupirirana tsiku loyamba Chikondi chidayambira kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College komwe Dennis Lupenga akuti atakumana ndi Sheila Chimphamba mchaka cha 2013 pomwe onse amachita maphunziro, adakhulupirirana tsiku lomwelo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Awiriwa adamaliza maphunziro awo ndipo Sheila amagwira ntchito muofesi ya mapolojekiti komanso ndi mkonzi wa mapologalamu kuwayilesi ya Zodiak pomwe Dennis ali ndi kampani yake ya zamakina a Internet. Dennis akuti ubale wa awiriwa udayamba pa 9 April chaka chokumanacho Awiriwa tsopano ndi thupi limodzi cha 2013 iye atauza njoyelo mwachindunji kuti akufuna kumukwatira osati za chibwenzi monga momwe anthu ambiri amayambira. Ndidalibe nthawi yotaya nkumati ndili pachibwenzi chifukwa Sheila adandigwiriratu mtima ndipo ndidalibeso nthawi yoti ndimuone kaye ayi, adatero Dennis. Iwo akuti ngakhale uku kudali kusukulu, mmaganizo mwawo mudalibe za chibwenzi koma kuti akungoyembekezera tsiku lodzalowa mbanja ndipo panthawi yonseyi sadasiye makolo ndi abale awo mumdima pozindikira kuti ubale wawo sudali wachibwana. Titakambirana, tidadziwitsa abale ndi makolo kuti azidziwa chifukwa timazindikira kuti pokangopita nthawi pangono tiwafuna kuti atimangire chinkhoswe ndi kutigwira dzanja pomwe tikukalowa mbanja, adatero Dennis. Iye akuti adakhala choncho mpaka chaka cha 2014 pa 9 August pomwe adamanga chinkhoswe nkuyamba kukonzekera ukwati omwe udachitika pa 2 April ku tchalitchi cha Katolika cha Maula ndipo madyerero adali ku Peak Gardens mumzinda wa Lilongwe. Sheila ndi mkazi wanzeru, wokongola, wachilungamo, wodzisamala ndi woopa Mulungu. Adandiwonetsa chikondi chenicheni monga momwe makolo anga adandionetsera, adatero Dennis. Dennis ndi mwamuna wolimbikira, wodzichepetsa ndi wachikondi komanso wachilungamo. Amandilimbikitsa ndikakhala ndi chofooka ndipo amandiphunzitsa kuthana ndi zokhoma, adatero Sheila.
15
Papa Afunira Zabwino Atolankhani Akatolika Omwe Akuchita Maphunziro Wolemba: Glory Kondowe Aku-likulu la mpingo wakatolika ku Vatican afunira zabwino atolankhani a mpingowu omwe akuchita maphunziro awo mdziko la Ivory Coast. Mmodzi mwa akulu-akulu a ku ofesi ya zofalitsa nkhani ku likulu la mpingo-wu ku Vatican, Paolo Ruffin, ndi amene wapereka uthenga-wu kuyimira mtsogoleri wa mpingo-wu pa dziko lonse. Papa Franscico Mwazina uthenga womwe akulu ampingo wakatolika ku Vatican anatumizira atolankhaniwo ndi wolimbikitsa kuti akuyenera kugwira ntchito zawo mwa ukatswiri ndi kuwonetsetsa kuti akuthandiza kulimbikitsa ntchito zachilungamo ndi zina zambiri. Maphunziro omwe akonzedwa ndi bungwe la ngwilizano watolankhani achikatolika ACJ mogwirizana ndi ndinthambi yofalitsa nkhani mumpingo mudzikomo mothandizana ndi mkulu ofalitsa mawuthenga muzikomo abuye Raymond Ahowa.
3
Chitetezo chibwerera mchimake Mkulu wapolisi mdziko muno Lot Dzonzi wati uchifwamba omwe anthu ambiri akudandaula kuti wafika povuta tsopano utha chifukwa cha njira zina zomwe apolisiwa akonza. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Dzonzi adanena izi pomwe amatsegulira msonkhano wolimbikitsa mgwirizano wa apolisi ndi anthu popititsa patsogolo chitetezo omwe unachitikira kulikulu la polisi ku Lilongwe Lolemba. Iye adati a polisi omwe agwira bwino ntchito aziwapatsa mphoto zikuluzikulu monga kukwenzedwa pa ntchito nyengo ya Khirisimasi komanso zina za ndalama. Dzonzi adati likulu la polisi lakonzanso ndondomeko yotumiza apolisi ambiri mmatauni ndi mmadera omwe azikakhalira komweko kuti azigwira bwino ntchito yawoyo ndipo aziwayendera kuona mmene ntchitoyi ikuyendera. Titumiza a polisi ambiri mmadera onse ndipo tiziwayendera pafupipafupi kuti tiziona mmene ntchito ikuyendera. Pambali potumiza a polisi ambiri, kumapeto kwa chaka chilichonse tizikhala ndi mwambo wopereka mphoto zikuluzikulu monga kukweza apolisi omwe agwira ntchito bwino komanso kuwapatsa ena ndalama kutengera ndi mmene agwirira ntchito yawo, adatero Dzonzi. Iye adaonjeza kuti akudziwa za mavuto amene apolisi amakumana nawo mmadera momwe akukhala ndipo adatsimikizira apolisiwa kuti zinthu zisintha posachedwa chifukwa awakhazikitsira maofesi pafupipafupi. Pamsoknhanowo, apolisi ena komanso maofesi a mmaboma adalandira mphoto chifukwa chogwira bwino ntchito ndipo Dzonzi adapempha apolisi onse makamaka a pansewu kuti azikhala a ulemu ndiomvetsetsa. Timvetsetsane apa. Sikuti kugwira bwino ntchito ndikumanga anthu kokhakokha koma kuwaunikira pomwe akuoneka kuti akusochera. Komabe pochita izi, tikuyenera kuonetsetsa kuti tikuteteza anthu olakwiridwa, adatero Dzonzi. Yunus Lambat yemwe anali wapampando wa bungwe loyendetsa za mgwirizano wa apolisi ndi anthu adati pazaka ziwiri zokha, bungweli lakhazikitsa maofesi okwana 27 000 mdziko muno omwe amayanganira ntchito za chitetezo ndipo adapempha komiti yatsopano kuti ipitirize ntchitoyi. Mkulu wa bungwe loona za ufulu wa anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation, Undule Mwakasungula, adati apolisi achita bwino kuganiza zokhazikitsa njirazi chifukwa anthu akuzunzika ndi uchifwamba. Mwakasungula adati nkofunika kuti a polisi aganize zokhazikitsa njira zambiri zoti anthu azidziwitsira apolisi pamene akumana ndi zovuta kapena aona anthu okayikitsa.
7
MET Yachenjeza za Mvula Yamphamvu Nthambi yowona za nyengo ndi kusintha kwa nyengo yati mvula yamphamvu ikuyembekezeka kugwa mmadera ambiri mdziko muno kuyambira lero mpaka lachisanu pa 14 February 2020. Malinga ndi chikalata chomwe chasayinidwa ndi mkulu wa nthambiyi Jolam Nkhokwe, mvulayi yomwe ikhale yosakanikirana ndi mphepo yamphamvu, komanso ziphaliwali ikuyembekezeka kugwa mmadera a kumwera, pakati komanso madera a mbali mwa nyanja. Mvulayi akuti ikuyembekezeka kudzetsa kusefukira kwa madzi mmadera otsika komanso momwe mumachitika-chitika ngozi za mtunduwu kaamba koti padakalipano dothi lidakali lonyowa mmadera ambiri mdziko muno. Mwazina mphepo yamphamvuyi komanso ziphaliwali, zili ndi kuthekera kowononga zinthu, kuvulaza komanso kupha anthu. Pamenepa nthambiyi yapempha anthu kuti asamuke mmadera omwe ndi angozi, apewe kuwoloka mitsinje pamene yadzadza komanso kupewa kubisala pansi pa mitengo ndi nyumba zina zosalimba, pofuna kupewa ngozi zomwe zingadze kaamba ka nyengoyi.
18
Bungwe la TC Lachititsa Maphunziro Ozindikiritsa Adindo za Malamulo Mchitidwe ogwiritsa ntchito ana mminda ya fodya akuti ungachepe ngati adindo atatsatira moyenera malamulo omwe adakhazikitsidwa oyendetsera ulimi wa fodya mdziko muno. Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe lowona za ulimi ndi malonda a fodya mdziko muno la Tobacco Commission (TC) a Hellings Nason ndi omwe anena izi pambuyo pa maphunziro ozindikiritsa adindo, ena mwa malamulowa. A Nason anati mchitidwewu ukukula mchigawo chapakati cha dziko lino ndipo adindo akuyenera kuchitapo kanthu kuti izi zithe. Mfundo zina zomwe zili mmmalamulo amenewa zinafunikira kuti tizifotokozere kwa iwo amene akhoza kuthandizira kuti lamulo liyambe kugwira ntchito moyenera monga mafumu amene amakhala kumidzi ndi anthu ndi amene angakwanitse kuwafotokozera anthu, anatero a Nason. Poyankhulapo komishonala owona za milandu a Samawat Chisale anadandaula kuti milandu yochepa yokha ndi yomwe imafika ku polisi ndipo anati maphunzirowa athandizira kuti anthu adziwe za malamulo.
4
Mwambo wopha mudzi poika mfumu Anthu ena amakhulupirira kuti akamwalira amayenera akaikidwe chatsonga kapena kuti chokhala. Izi zimachitika kwambiri pakati pa mafumu Achingoni maka a kwa Maseko. Umu ndi momwe zidakhalira ndi maliro a T/A Bvumbwe wa ku Thyolo mwezi wathawu, yemwe adaikidwa chatsonga. Anthu otere akamwalira, pamakhala mwambo wopha mudzi. Izi zimachitika pokumba nyumba yoti igone mfumuyo. BOBBY KABANGO akutsata momwe zimakhalira. Pepani wawa ndi zovutazi. Koma ndimati tichezepo pangono za miyambo ina yokhudza maikidwe a mfumu Yachingoni. Koma poyamba tidziwane. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ndine Opesi Mangombo ndipo kwathu ndi mommuno mwa Bvumbwe. Ndinu wa mtundu wanji? Mukadzaona nsalu ya Gomani chonchi komanso mthini pamutu, musadzafunse, dziwani kuti amenewo ndi Angoni ankhondo aja amene adachoka ku Mozambique ku Domwe. Moti ine ndi Mngoni, ndili kumtundu wa Bvumbwe. Ndamva kuti inu ndiye mumatsogolera adzukulu okumba manda a mfumu Mwamva zoona koma si kuti ndi manda onse, koma kuti ndinatsogolera adzukulu amene akumba manda amene tiike thupi la mfumu yathu Bvumbwe. Timamva za mawu oti kupha mudzi pamene mukukumba manda ogona mfumu, zimatanthauzanji? Choyamba dziwani kaye kuti mfumu yathu igona chatsonga, kupha mudzi kumachitika ngati mukukumba manda a munthu amene akaikidwe chatsonga. Kwa iwo okaikidwa chogona ndiye sikukhalanso kupha mudzi. Mudzi ndi malo kapena kuti phanga lomwe mfumuyo imaikidwako. Choyamba mumakumba dzenje lotalika ndi mamita atatu ndi theka. Limakhala dzenje lozungulira, osati lamakona anayi monga zikhalira ndi ena. Mukamaliza kukumbako ndiye mumakhala pansi kupanga mudziwo. Fotokozaninso, mwati mudzi nchiyani? Mudzi ndi malo kapena kuti phanga lomwe mfumu igoneko. Pamene mwakumba ndi kumaliza manda, ndiye mumayamba kupanga phanga. Kukula kwake kufanane ndi kukula kwa bokosilo. Koma nthawi zambiri mudziwo umakula ndi mamita awiri mlitali ndi mlifupi. Ndiye mukati kupha mudzi mumatanthauza chiyani? Timatanthauza ntchito yomwe mumachita kuti muyambe kupanga phangalo lomwe kulowe mfumu yathu. Zimatheka bwanji kuti mupange phanga loti muli kale mdzenje? Timaonetsetsa kuti dzenjelo likhale lokula bwino kuti mukathe kukhala pansi ndi kumagoba mudziwo. Timapangira khasu lomweli koma timaligulula ndi kulizika ngati nkhwangwa. Mukamaliza mumatani? Tikafikira mlingo womwe tikufuna, timatenga timitengo ndi kukhoma pakhomo pa mudziwo chifukwa bokosi likalowa, timayenera titseke pakhomopa kuti dothi lisalowe. Simungapange mudzi musadayeze kukula kwa bokosi lomwe mfumu yathu igonemo. Dothi lakenso liti? Pajatu dzenjeli timalikwirira pamene taika mfumu yathu, ndiye pakhomo pa mudzi timatsekapo kuti dothi lisamupeze. Koma cholinga chopangira mudziwu nchiyani? Mfumu siyenera kuthiridwa dothi pamutu. Mudziwu umapangidwa dala kuti ipeze kobisala pamene tikuthira dothi. Ndi manda ngati awa, chiliza chake chimakhala chotani? Chimamangidwa mozunguliranso (akuloza ziliza za mafumu ena pamandapo) osati chogona monga zina zimakhalira. Malo ano ndi a mafumu okhaokha komanso akazi awo. Mwana wa mfumu sagona pano pokhapokha ngati wavekedwa ufumu. Kodi uku sikungovutika chabe? Mwatero ndi inuyo koma ife sitiona kuvutika koma kukwaniritsa chikhalidwe chathu ndi ulemu kwa mafumu athu monga Angoni.
1
St. Augustine Parish Yati Ipilira Kuthandiza Achinyamata Mmasewero Achinyamata ku parish ya Augustine woyera mu dayosizi ya mpingo wakotolika ya Mzuzu awalimbikitsa kuti azikhala otanganidwa ndi nkhani zotukula mpingo-wu mdziko muno. Bambo mlangizi wa achinyamata mu parish-yi bambo Samuel Nawasha anena izi loweruka pa bwalo la za masewero la St. Augustine pomwe achinyamata kuchokera mma zoni onse anayi a mparishi-yi anakumana malo amodzi ndi kuchita masewero olimbitsa thupi monga mpira ndi zina zambiri. Iwo anati ndondomekoyi inakhazikitsidwa ndi ambuye John Ryan omwe ndi episkopi wa dayosiziyi ndi cholinga chofuna kulimbikitsa achinyamata kuti azikhala otanganidwa ndi zinthu zina pofuna kupewa makhalidwe oyipa omwe angamachite kaamba kosowa zochita. Program imeneyi muyambitsi weniweni ndi ambuye Ryan omwe ndi mwini wake wa dayosizi ino pofuna kuwapatsa chisamaliro chapadera pa moyo wawo wauzimu komanso wa wa thupi, anatero bambo Nawasha. Mmau ake mmodzi mwa achinyamata omwe anachita bwino pa zamasewerowo Jonas Muhango anayamikira dayosiziyo kamba ka chikonzerochi zomwe iye wati zithandiza achinyamatawa kukhala ozipereka mu mpingo komanso kudziwana ndi anthu ena omwe ndi a dayosizi yomweyi koma amakhala maparish ena. Mpikisanowu uyambira mmadinale onse kenako omwe achite bwino mmadinale azakafika mpaka pa dayosizi kuti akapikisane ndi achinyamata a madinale ena.
16
Alangiza boma pa kayendetsedwe ka chuma Adadza ndi ndondomeko: Gondwe Zipani zotsutsa boma ndi akatswiri pa kayendetsedwe kabwino ka boma ati boma lisamale kwambiri mmene liyendetsere ndalama zapadera zomwe aphungu a Nyumba ya Malamulo adavomereza boma kugwiritsa ntchito kwa 4 ikudzayi. Nyumba ya malamulo idavomereza boma kugwiritsa ntchito ndalama zokwana K210 biliyoni Lachisanu sabata yatha koma otsutsa ndi akatswiri ati kusowa kwa ndondomeko yeniyeni ya mmene ndalamazi zigwirire ntchito ndi nyambo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Wolankhulira chipani cha Malawi Congress Party (MCP) pankhani za chuma mNyumba ya Malamulo Joseph Njobvuyalema adati kunena kuti boma igwiritsa ntchito ndalamazi si ndondomeko ya chuma cha dziko choncho nkofunika kusamala mmene zigwiritsidwire ntchito. Ndondomeko yeniyeni ya chuma cha dziko imafotokoza bwinobwino mmene ndalama iliyonse igwirire ntchito kotero kumakhala kosavuta kulondoloza pomwe ndalama izi nzongofuna kukokera boma pomwe ndondomeko yeniyeni ikubwera, adatero Njobvuyalema. Iye adati pachifukwachi boma likufunika kuonetsetsa kuti ndalamazi zagwira ntchito moyenerera makamaka mnthambi zofunika kwambiri za boma. Wolankhulira chipani cha Peoples Party (PP) Ralph Jooma adati nduna ya zachuma Goodal Gondwe amayenera kulongosola mmene nthambi za boma zipindulire ku ndalamazi kuopa mchitidwe osakaza. Akatswiri pa zakayendetsedwe kabwino ka boma ayamikira Nyumba ya Malamulo povomereza ndalama zapaderazi koma ati zonse zili mmanja mwa boma kuonetsetsa kuti ndalamazi zapindulira Amalawi. Mkulu wa bungwe la mpingo wa Chikatolika lowona kuti boma likuyendetsedwa mwachilungamo ndi mtendere la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP), Chris Chisoni, wati K210 biliyoni ndi yokwana kupindulira boma ngati zitagwiritsidwa bwino ntchito. Malamulo a dziko lino amapereka mphamvu kuboma kupempha ndalama zapadera ngati mboma mulibe ndalama koma chofunika ndi chilungamo kuti eni ndalamazo, omwe ndi Amalawi, apindule nazo, adatero Chisoni. Gondwe adauza Nyumba ya Malamulo Lachisanu sabata yatha kuti boma la DPP lidapeza mboma mulibe ndalama pomwe limatenga boma ndipo kuti boma lapitalo lidasiya ngongole zankhaninkhani zofunika kubweza. Nkhawa ya zipani zotsutsa ndi akatswiri ndi mchitidwe osolola ndalama za boma omwe udachititsa kuti maiko omwe amathandiza dziko la Malawi anyanyale ndi kuimika thandizo lawo. Mkulu wa bungwe la Institute for Policy Interaction (IPI) Rafiq Hajat adati kuima kwa thandizo lochoka kunja kumaimitsa ntchito zina zaboma ndipo anthu amavutika.
2
Njala ikhaulitsa a Malawi Ma Admarc ena kuli gwagwagwa! Zafika pena. Ngati wina samwalira ndi njala ungokhala mwayi chabe koma zinthu zaipa mdziko muno moti anthu ena akugona kumimba kuli pululu. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika akunenetsa kuti palibe amene amwalire ndi njala, koma ngati sipachitika china chake mmisika ya Admarc mdziko muno ena amwalira nayo. Mzere wa ofuna kugula chimanga ku Admarc Ulendo wa Tamvani mmaboma a chigawo cha kummwera, pakati komanso kumpoto, wapeza kuti madera ena patha miyezi ingapo chimanga chikusowa mmisika ya Admarc. Ma Admarc a Chikomwe, Ngwerero, Nasawa, Mayaka, Sunuzi, Jenala, Zaone ndi Buleya mboma la Zomba kwa T/A Mbiza akuti atha miyezi iwiri kulibe chimanga. Gulupu Belo wati malinga ndi kusowa kwa chimangacho, anthu amagonera deya amene amagula pamtengo wa K240 pa kilogalamu. Panopa amene wapeza gaga ndi munthu. Chakudya chasowa, moti ndatumiza anthu 8 kuchipatala amene amaonetsa zizindikiro zachilendo chifukwa chosadya, adatero Belo. Ku Mwanza malinga ndi T/A Kanduku, miyezi iwiri yatha chimanga kulibe. Iye wati poyamba anthu amagonera mango koma lero ndiye kolowera kwasowa. Ndi nkhani yosabisa, njala yavuta kuno ndipo chimanga chatenga nthawi chisadafike ku Admarc, adatero Kanduku. Ku Balaka patha miyezi iwiri chimanga chisadafike pa Admarc ya Phalula pamene kwa Sosola ndiye patha mwezi. Sabata yatha tidapeza anthu ammudzimo akupita kukadandaula kwa DC wa bomalo chifukwa akhala akuuzidwa kuti chimanga chibwera koma kuli chuuu. Admarc ya Misuku ku Chitipa ikumalandira chimanga mwezi ulionse kamodzi koma chimangacho chikuchokera kubungwe la World Vision. Admarc ya Chikwera mbomalo ilibiletu chimanga, pamene Admarc ya paboma yangolandira kumene matumba 300. Mabanja 2 000 ndiwo amadalira Admarc ya pabomayo koma ikugulitsa makilogalamu osaposa 15 kwa aliyense. Admarc ya pa Karonga boma ili ndi chimanga koma pamene timafikapo Lachiwiri msabatayi nkuti pali mnzere wotalika ndi mamita 280. Anthu akumagona pomwepo kuti agule chimanga. Ma Admarc a boma la Nkhata Bay akuti akumalandira chimanga pafupipafupi koma chikumatha tsiku lomwelo chifukwa chikumafika chochepa kuyerekeza ndi anthu amene akufuna chakudyacho. Mkulu wa bungwe la Admarc Foster Mulumbe wati chiyambireni September chaka chatha agulitsa matani 26 000 a chimanga. Iye watinso kufika pano, Admarc yatsala ndi matani ochepa. Chimanga chidakalipo koma chochepera, ndipo tikupitiriza kupereka mmisika yathu. Ngati chimanga chatha mmisika yathu, ndi bwino kutidziwitsa msanga kuti titumize china, adatero Mulumbe. Miyezi ingapo yapitayo, boma lidagula matani 30 000 a chimanga mdziko la Zambia. Woyendetsa ntchito wamkulu mu unduna wa malimidwe Bright Kumwembe wati chimanga chonsecho chidapita kumisika ya Admarc. Chimanga chonsecho chidafika mdziko muno ndipo chili mmisika ya Admarc. Likulu losamala chakudya la National Food Reserve Ageency [NFRA] likugula chimanga china mdziko momwe muno, adetro Kumwembe. Nkhani ya njala si yachilendonso mdziko muno. Bungwe la World Food Programme (WFP) lati lakwanitsa kufikira anthu 1.6 miliyoni mmaboma 15 amene ali pamoto wa njala. WFP Lolemba lidatulutsanso lipoti lina lomwe limati anthu 14 miliyoni ali pachiopsezo chokukutika ndi njala kummawa kwa Africa. Dziko la Malawi ndi limodzi mwa maiko okhudzidwa chifukwa cha mavuto a kusowa kwa mvula.
2
Mwana wa Dos Santos Anathawa Mlandu-Boma Mkulu woyimira boma pa mlandu mdziko la Angola wati akufuna mwana wa mtsogoleri wakale wa dzikolo Isabel Dos Santos abwelerenso mdzikolo. Malipoti awailesi ya BBC ati Santos yemwe ndi mmodzi mwa amayi olemera kwambiri kuno ku Africa, anakhazikika ku London bambo ake atangochoka pa udindo wa utsogoleri wa dzikolo. Akuti akukhudzidwa ndi katangale ku dziko la kwawo-Santos Mayiyu ati akukhudzidwa ndi nkhani za katangale zomwe zimachitika mdzikolo nthawi yomwe bombo ake anali mtsogoleri wa dziko. Polankhuklapo, Santos wati zomwe apolisiwa akunena ndi zabodza ndipo ndi ndale chabe. Mmodzi mwa apolisi azofufufzafufuza-wa Helder Pitra wauza wailesi ya dzikolo kuti ndi thandizo lochokera ku maiko a Portugal, Dubai ndi maiko ena, achita chothekera kumubweretsa Santos kumudzi kuti azayimbidwe mlandu wokhudza za katangale zomwe anachita mdzikolo. Mwazina, nkhaniyi inafika kale ku bwalo lamilandu la mdzikolo pomwe zinaululika kuti mayiyu amagwiritsa ntchito makalata achinyengo pochita malonda ake mdzikolo.
7
Kucheza ndi Ibu Mphanje: Gaba wochemerera Bullets Anthu otsata masewero a mpira wa miyendo alipo ambiri koma ena amaonjeza kukonda kwake. Ena adachita kufika popereka maina achilendo kumatimu omwe amachemerera ati pofuna kuwopseza anzawo. Ibu Mpanje ndi mmodzi mwa ochemerera timu ya Big Bullets yomwe eni ake amati Timu ya Fuko kapena Ma Palestina. Ndidacheza naye motere: Mphanje: Masapota tionjezera mphamvu Moni wawa komanso ndikudziweni? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ine ndine Ibu Mpanje kwathu nku Nathenje koma ndikukhala mtauni ya Lilongwe. Ndimakonda kwambiri masewero a mpira wa miyendo moti timu yanga ndi Big Bullets. Anthu ambiri amandidziwa ndi dzina lakuti Gabadinho, osati osewera mpira uja, ayi, koma wochemerera. Tsono dzina la Gabadinho lidabwera bwanji? Basi kumpira anthu ambiri amandipatsa ulemu pa nkhani yochemerera ndiye nthawi ija kudadzatulukira Gabadinho wa mpira ija anthu amatengera momwe adagwedezera iye nkumandiitana ndi dzina lomwelo. Anthu ambiritu amakonda kudzitcha okha maina a anthu otchuka, sizili choncho ndi iwe? Ayi, nokhaso mudaona momwe zidalili kuja kokhala anthu ochemerera momwe ndidagwedezera ochemerera matimu ena omwe samafunira Bullets zabwino. Zimakhala mommuja nthawi zonse kukakhala mpira, makamaka wa Big Bullets, timu yanga kuyambira kalekale. Umangokonda mpira basi kapena uli ndi mbiri iliyonse pamasewerowa? Mpira ndinkasewera kalekale kuyambira kupulayimale mpaka mmakalabu ena ndi ena moti kusiya ndidasiyira pa timu ya KIA. Ndasewerako malo osiyanasiyana mgalaundi koma malo omwe ndidasewera kwambiri ndi kutsogolo. Kuvulala ndiko kudandichititsa kuti ndisiye kusewera mpira. Ndidavulala kamodzi ndiye kuyambira pomwepo ndinkati ndikasewera mpira ndimadzutsa vutolo. Malingaliro ako adali otani panthawiyo? Panthawiyo ndinkafunitsitsa kudzasewera mmatimu akuluakulu makamaka ya Big Bullets moti sindikaika kuti chipanda kuvulalako, nkadafika pomwe ndimafunapo. Anthu omwe adandionererako nthawi imeneyo akhoza kufotokoza bwino za luso lomwe ndidali nalo moti pano ndimadandaula kwambiri chifukwa ndidasiya mpira ndisadasewereko mutimu ya Flames. Chifundo chosechi pa timu ya Bullets bwanji supikisana nawo pamaudindo kuti uzitumikira nawo? Ayi, zinthu zimafunika kupatsana mpata. Ngati pali ena omwe aonetsa kale mtima wofuna kutumikira, ena mumafunika kuthandiza amenewo kuti pakhale umodzi chifukwa nonse mukamalimbirana, mkangano suchedwa kuyamba, ayi. Sabata yathayi mwasewera masewero awiri omwe simudapambaneko. Zikutanthauzanji kwa iwe ngati wochemerera? Poti awo adali masewero ongopimana mphamvu ndiye sindingazitengere kwenikweni, koma tikudikira ligi ikayamba ndiye anthu adzaone Bullets yeniyeni. Mudaona nokha ligi yathayo momwe Bullets idavutira, chaka chino tiposa pamenepo ndipo ifenso ochemerera tionjezera mphamvu kuti anyamata osewera nawo adzadzipereke kotheratu.
16
Njovu ziwiri zitengetsana pa 19 May Zadziwika tsopano kuti njovu ziwiri zomwe ndi mgwirizano wa Democratic Progressive Party (DPP) ndi United Democratic Front (UDF) komanso Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party ndizo zidzalimbane pachisankho cha pa 19 May. Izi, zidatsimikizika Lachitatu zipani za MCP ndi UTM zitabwera poyera nkunena kuti mgwirizano wawo womwe wakhala mphekesera chabe kwa nthawi yaitali tsopano watheka. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zikutanthauza kuti tsopano zipani zinayi zomwe zidali zikuluzikulu pachisankho cha pa 21 May chaka chatha tsopano zapanga mbali ziwiri zomwe zidzapikisane pachisankho chomwe chikubwerachi. Zipani za DPP ndi UDF zidalengeza mgwirizano wawo pa 25 February pomwe MCP ndi UTM ati mgwirizano wawo wangopsa kumene ndipo adzasainira pa 19 March ku Bingu International Convention Centre (BICC) ku Lilongwe. Polengeza mgwirizano wawo, DPP ndi UDF onse adati adaona kuti mfundo zawo zachitukuko ndi zolinga zawo nzofanana ndipo MCP ndi UTM nawo akunena zomwezo. Migwirizanoyi yapangidwa pokonzekera chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chobwereza potsatira chigamulo cha Constitutional Court choti chisankho cha pa 21 May sichidayende bwino ndipo chibwerezedwe. Khothilo lidagamula kuti chisankhocho chichitike mmasiku 150 kuchokera pa 3 February 2020 pomwe lidapereka chigamulo chake chomwe chidakomera Lazarus Chakwera wa MCP ndi Saulos Chilima wa UTM Party. Awiriwa adakamangala kukhoti kuti bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidapotoza zotsatira zachisankhocho chomwe lidapambanitsa Peter Mutharika wa DPP. Koma zokonzekera chisankhocho ziyembekeza kuti mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika asainire mabilo a zachisankho amene aphungu a Nyumba ya Malamulo adapereka kwa iye. Mwa zina, mabilowo akuti chisankho cha aphungu ndi makhansala chotsatira chidzachitike mu 2025 kuti chidzalingane ndi cha mtsogoleri wa dziko lino. Aphunguwo adapemphanso Mutharika kuti achotse makomishona a MEC amene bwalo lidawapeza kuti sadayendetse bwino chisankho cha pa 21 May chaka chatha. Oimira ufulu wa anthu Timothy Mtambo, Gift Trapence ndi MacDonald Sembereka adamangidwa pokonza zionetsero zokakamiza Mutharika kuchotsa makomishonawo. Wotambasula za ndale Humphreys Mvula wati polingalira za nthawi yomwe yatsala kuti chisankho chichitike, nkoyenera kuti Pulezidenti asadikire masiku 21 kuti asayinire mabiluwo. Nzoona malamulowo akutero koma apapa tikuyangana nthawi yomwe ilipo kuti chisankho chichitike, adatero iye.
11
Bambo Stanislaus Chinguwo Amwalira Mwambo woyika mmanda thupi la malemu bambo Stanislaus Chinguwo, uchitika loweruka likudzali pa 30 May, 2020 ku Limbe Cathedral mu arkidayosizi ya Blantyre. Malemu bambo Chinguwo Bambo Chinguwo amwalira mbandakucha wa lero lachinayi pa 28 May, 2020 ku chipatala cha Mwaiwathu mu mzinda wa Blantyre. Mwambo wa maliro ukuyembekezeka kudzayamba 10 koloko mmawa, motsogozedwa ndi arkiepiskopi wa arkidayosiziyo Ambuye Thomas Luke Msusa, omwenso ndi wapampando wa bungwe la maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko muno la Episcopal Conference of Malawi (ECM). Chikalata chomwe likulu la mpingo wa katolika latulutsa chati mawa sikukhala kusonkhana ndi kuchita mapemphero ndipo mmalo mwake ansembe komanso akhristu akupemphedwa kuti adzipemphelera malemu bambo Chinguwo mmakomo mwawo kuti mzimu wawo uwuse mu mtendere. Malemu bambo Stanislaus Chinguwo anabadwa pa 19 January mchaka cha 1969 ndipo amachokera ku Namlenga parish mu arkidayosiziyo.
14
Akulipitsa kulembetsa khadi Anthu ena amene sadalembetse nambala zawo akulirira kuutsi pamene ma agenti ena akuwauza kuti alipire ngati akufuna nambala yawo ilembetsedwe. Izi zikudza pamene makampani a foni za mmanja a Airtel ndi TNM adachotsa nambala zimene sizidalembetse pofika pa 30 September chaka chino. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kulembetsa makadi ndi kwa ulere Ngakhale kampanizi zidachotsa nambala zina, eni nambalawo ali ndi mwayi wokalembetsa nthawi iliyonse mwaulere. Koma izi zikusiyana ndi zimene anthu ena akukumananazo pamene akupemphedwa kulipira kuti nambala yawo ilembetsedwe. Mboma la Mulanje ndi Thyolo anthu ena akulipira kuti alembetse nambala zawo. Mtolankhaniyu atayendera malo ena ku Chirimba mafupi ndi sitolo ya Macsteel adauzidwa kuti alipire K300 kuti nambala yake ya Airtel ilembetsedwe. Tikuyenera tigule mayunitsi a K300 omwe timalowera mu system ya Airtel kuti nambala yanu ilembetsedwe. Koma nambala yanuyo idadulidwa mwezi wapitawo zomwe zimapangitsa kuti ntchito yathu ikhale yovuta, adatero agentiyo. Titamuuza kuti tili ndi K100, iye adakananso kuti ndalamayo yachepa chifuwa polingalira kukula kwa ntchito yolumikizira nambalayo. Mneneri wa kampani ya Airtel Norah Chavula-Chirwa adati ndi wodzidzimuka kuti anthu ena apezerapo mwayi kumabera makasitomala awo pamene akulembetsa nambala zawo. Iye adati kampani yawo iyesetsa kuyenda mmidzi kulangiza anthu kuti sakuyenera kulipira polembetsa nambala. Tikulangiza makasitomala athu kuti aimbe 121 ngati wina wawauza kuti alipire polembetsa nambala yawo. Ngatinso mderalo kuli ofesi yathu, athamangireko kuwamuneneza agent amene akulipiritsayo. Apo ayi athamangire kupolisi kukanena. Pamene akuimba 121, ayenera adziwe code ya agent-yo kuti tichotse nambala yake, adatero Chirwa. Naye mneneri wa kampani ya TNM, Daniel Makata adati alandira nkhani zotere mboma la Mulanje komwe agent akufuna ndalama kuti alembe nambala. Makata adati kampani yawo idalemba ntchito ma agent oposa 2500 mmadera onse a dziko lino kuti alembe onse amene ali panetiweki ya TNM. Ifeyo tidawalemba ntchito, ndi kulakwa kuti nawonso ayambe kulipiritsa makasitomala athu. Anthu adziwe kuti kulembetsa nambala ndi kwaulerere, sakuyenera kulipira kanthu pa ntchito imeneyi. Ngati wina wakupemphani ndalama chonde tidziwitseni apo ayi pitani kupolisi, adatero Makata. Makata adati pofika pa 30 September, kampani yawo nkuti italemba makasitomala 75 pa 100 alionse.
11
Papa Wasankha Mkulu Woona Zachuma ku Vatican Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wasankha mkulu wa bungwe loyangana momwe chuma chiyendera ku likulu la mpingo ku Vatican. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican Papa Francisco wasankha Giuseppe Schlitzer kulowa mmalo mwa Tommaso Di Russa yemwe nthawi yake yokhalira pa udindowu inatha mwezi wa January chaka chonchino. Likulu la Mpingo wa Katolika ku Vatican lalengeza za kusankhidwa kwa akuluakulu awiri oyanganira bungwe la Mpingowu loona momwe chuma chiyendera. Mkulu wa bungweli lomwe limadziwika pa chingerezi kuti Financial Intelligence Authority ndi Giuseppe Schlitzer ndipo womutsatira wake ndi Federico Antellini Russo. Awiriwa akulowa mmalo mwa Tommaso Di Russa yemwe adatsiriza ntchito yake pa 20 January chaka chonchino atakhala pa udindowu kwa zaka zisanu. Mwa zina bungweli limalimbana ndi machitidwe wozembetsa ndalama (money laundering). Papa Benedicto wa 16 ndiyemwe adakhazikitsa bungwe la Financial Intelligence Authority mchaka cha 2010 kuti liziona momwe ndalama zimagwiritsidwira ntchito ku likulu la Mpingo ku Vatican komanso kuti ndondomeko za chuma zomwe likulu la Mpingo wa Katolika limatsata nzogwirizana ndi momwe mabungwe komanso maiko achitira.
14
Anthu 50 000 akutenga HIV chaka chilichonse Pamene nkhondo yolimbana ndi matenda a Edzi ikupitirira, zadziwika kuti chaka chilichonse anthu 50 000 akutenga kachirombo ka HIV kamene kamayambitsa matendawa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Polankhula pamwambo woganizira anthu amene adataya miyoyo yawo kaamba ka nthendayi komanso amene ali ndi kachirombo koyambitsa nthendayi, wachiwiri kwa pulezidenti wa dziko lino Khumbo Kachali adati aliyense ayenera kutengapo gawo kuti chiwerengerochi chitsike. Ndi udindo wa tonse kulimbana ndi matenda a Edzi ndipo tonse tiyenera kuyezetsa, adatero Kachali, yemwenso ndi nduna ya zaumoyo. Mkulu wa bungwe la UNAIDS ku Malawi Patrick Brenny adati Malawi ikuchita bwino pankhondo yolimbana ndi matendawa. Malawi akuchita bwino makamaka makamaka pankhani ya kadyedwe, kuchepetsa kupatsirana kwa nthendayi pakati pa mayi ndi mwana komanso ma ARV, adatero iye. Koma Brenny adati nkofunika kuti Amalawi agwirane manja ndipo asatope popewa matendawa. Pamwambowo, wogwira ntchito kuwailesi Wesely Kumwenda adati atolankhani amene adapezeka ndi HIV ayenera kubwera poyera. Iye adati ngakhale adamupeza ndi HIV zaka 10 zapitazo, alibe nkhawa, ndipo wabereka ana awiri pakatipa.
6
Kuweta ngombe zamkaka nkokoma, koma. Alimi ndi akadaulo ena pa zaulimi abwekera ubwino ndi phindu la ulimi wa ngombe, koma ati pali zina zoyenera kuchita kuti ulimiwu ufikepo. Mwa zina, ngakhale alimi ambiri amene adacheza ndi Uchikumbe mzigawo zonse za dziko lino adati akusimba lokoma paulimiwu pali zina zoyenera kukonza kuti phindulo libwere pambalambanda. Kadaulo pa nkhani ya ziweto kusukulu ya ukachenjede ya Lilongwe University of Agriculture and Natural Resources (Luanar) pulofesa Timothy Gondwe komanso mkulu wa mgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndi ulimi la Civil Society Agriculture Network (CisaNet) a Tamani Nkhono-Mvula adaphera mphongo zonena za alimiwo. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu A Gondwe adati pakadalipano alimi a ngombe zamkaka akuchuluka koma chiwerengero cha ngombe nchochepa. Pali zina zoyenera kusintha kuti alimi a mkaka apindule kwambiri Iye adati izi zili choncho chifukwa ambiri mwa iwo ndi angonoangono ndipo amakhala ndi ngombe imodzi kapena ziwiri. Alimi akuluakulu sakuonetsa chidwi ndi ulimiwu. Alimi aangono ambiri alibe zipangizo komanso akusowa ulangizi pa kadyetsedwe, kasamalidwe ka ngombe komanso momwe angasamalire mkaka wawo kuti ukapeze msika wabwino, adatero Gondwe. Adapereka chitsanzo cha ngombe ya mkaka ya mtundu wa Fresian imene itadyetsedwa bwino ikhoza kutulutsa malita 40 pa tsiku koma alimi ambiri amakama malita 10 kapena 12 okha patsiku. Iwo adatinso vuto lina ndi ndondomeko zoyendetsera msika wa mkaka. Pophera mphongo, Nkhono-Mvula adati imodzi mwa ndondomeko zimene zimathimba alimiwa pakhosi ndi Gawo 36 ya malamulo a bizinesi ya mkaka. Malingana ndi lamuloli, alimi angonoangono sangagulitse mkaka wawo momasuka pokhapokha atakhala ndi njira zowiritsira yomwe ndi ntchito ina yapadera chifukwa afuna kudutsa mndondomeko zambiri kuti avomerezedwe kutero. Pachifukwa ichi, alimiwa amakakamizidwa kukagulitsa mkaka wawo kumakampani omwe ali ndi zipangizo pamtengo wozizira, adatero iwo. Malinga ndi mkuluyo, alimi a mkaka ali pachipsinjo cha misonkho kusiyana ndi alimi ena poti iwo amadulidwa msonkho pa ndalama zilizonse zomwe angapate pa malonda awo pomwe pamalamulo a msonkho, munthu amayenera kudulidwa msonkho ngati wapeza ndalama zoposa K50 000 pa mwezi. Mawu a akadaulowa akungopherezera zimene alimi ena mzigawo zonse zitatu adauza Uchikumbe. Wapampando wa gulu la Lusangazi Dairy Farmers Cooperative ku Mzimba, Hesco Banda, adati vuto la kusowa kwa zakudya likuchititsa miyoyo ya alimiwa kukhala yowawa. Iye adati ngakhale alimi ali ndi kuthekera kogula chakudya cha ngombezo pamtengo wa K10 000 thumba la makilogalamu 50, chikusowa. Zakudya zikusowa, moti tikungogwiritsa ntchito deya. Vuto lake, deyayu tikulimbirananso ndi anzathu a ku Tanzania amene akulolera kugula deyayo pamtengo wa K500 pa kilo mmalo mwa mtengo wake wa K200, adandaula Banda. Vuto lina, iye adati, ndi kusowa kwa msika chifukwa kumpoto kulibe kampani zogula mkaka monga momwe zilili mzigawo zina. Kampani za Lilongwe Dairy, Suncrest Creameries komanso Dairibord zimagula mkaka kumwera ndi pakati. Adaonjeza kuti izi zachititsa kuti mavenda alowererepo, pomagula mkaka pamtengo wolira. Ngakhale msika ulipo, alimi ena, monga Thomson Jumbe wa mmudzi mwa Waruna, T/A Chimaliro ku Thyolo mitengo ndiyotsika. Malingana ndi unduna wa malimidwe, mtengo wotsikitsitsa umene mkaka uyenera kugulitsidwira ndi K155 pa lita. Timagulitsa mkaka pa mtengo wa K150 pa lita pomwe kuti titulutse lita imodzi zimalowa ndi zambiri, makamaka tikawerengera zakudya monga deya komanso mankhwala, adatero Jumbe. Poyankhapo pamadandaulowa, nduna ya zamalimidwe ulimi wothirira ndi chitukuko cha madzi Dr George Chaponda adati unduna wake uunika madandaulowa nkuwona kuti ungathandizane bwanji ndi alimiwa kuti ulimiwu upite patsogolo.
4
Chipatala cha Kamuzu Central Chayika Ndondomeko Zatsopano Zopewera COVID-19 Akuluakulu a chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe ayika ndondomeko zatsopano ngati njira imodzi yofuna kuteteza anthu odwala ku mliri wa COVID-19 pa chipatalachi. Anthu akamalowa apa aziyamba ayezedwa Izi zadziwika kudzera mu chikalata chomwe akuluakulu a pa chipatalachi atulutsa chomwe chikufotokoza ndondomeko zatsopano zomwe akhazikitsa zopewera mliri-wu. Mwazina chipatalachi chati chiziwonetsetsa kuti aliyense wolowa mzipata za pa chipatalachi akuyezedwa ku nthendayi. Tikufuna tichepetse kuchuluka kwa anthu omwe amabwera kuzaona odwala, kudzadikilira odwala. Tichepetsanso magulu amene amabwera kuzachita za tchalitichi ndi mapemphero mu ward zomwenso zimachititsa kuti anthu achulukane ndi kufalitsa matendawa, anatero a Kambeni omwe ndi mmodzi mwa akuluakulu a pa chipatalachi. Kudzera mu kalatayi chipatalachi chati anthu opita ku chipatalachi adzivala face mask, adzisamba mmanja komanso aziyezedwa mu zipata zolowera ku chipatalachi.
6
A khonsolo ndi ankhanzaAmalonda Ena mwa ochita malonda (mavenda) mmisewu ya mumzinda wa Blantyre alira ndi khalidwe la akhonsolo ya mzindawu kuti akuwachitira nkhanza ngati Malawi si dziko lawo. Pocheza ndi Msangulutso mavendawa akuti akupempha khonsoloyi kuti iwaganizire, maka iwo amene akuchita mabizinesi angonoangono. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Koma mneneri wa khonsoloyi, Anthony Kasunda, akuti sadalandirepo dandaulo lililonse kuchokera kwa anthuwa. Iye wati zomwe akudziwa nzoti akhonsolowa akumamenyedwa ndi mavenda akamagwira ntchito yawo yoletsa malonda mmalo amene si oyenera kuchitiramo bizinesi. Tikudziwa kuti nthawi zambiri ma rangers (othamangitsa anthu mmalo oletsedwa) athu akhala akugendedwa ndi mavenda ndipo umboni ulipo chifukwa timapita nawo kuchipatala. Galimoto zathunso zagendedwapo kambirimbiri. Mukumbukira kuti ranger wathu wachikazi adamenyedwa mu Limbe ndi ochita malonda koma anthu anaona ngati kuti wamenyedwa ndi venda, adatero Kasunda. Komabe amalondawa akuti akhala akudandaulira khonsoloyi koma sichitapo kanthu. Francis James, amene amagulitsa mkaka wamadzi wa mmapaketi) adati adamenyedwapo ndi akhonsolowa komanso kumulipitsa K5 000 kaamba kochita malonda mumzindawu. Adandigwira madzulo ndikupita kunyumba. Mmanja mwanga ndidali ndi machubu awiri a mkaka. Adandigwira ndi kundimenya ndi zitsulo mmiyendomu ndipo adandilipiritsa K5 000, adatero James. Iye akuti akukumbukiranso za mnzake wina amene ankagulitsa nsapato. Adamulanda nsapato zonse ndipo patadutsa sabata, tidakumana ndi mmodzi mwa amene adamulandawo atavala imodzi mwa nsapatozo. Mnzanga wina wogulitsa maheu adamumenyanso ndi zitsulo komanso adamumwera maheuwo, adatero James. Naye mayi wina, yemwe adati ndi Alinafe, akuti adamugwira ndipo adakamutsitsa ku Chileka kuti akayende wapansi kuchokera kumeneko atamugwira ndi malonda a nthochi. Koma Kasunda akuti katundu aliyense akuyenera kugulitsidwa mmalo ovomerezedwa ndi khonsolo kukhala msika. Malo oyenera kuchita malonda ndi okhawo omwe khonsolo idakhazikitsa ngati msika, komanso malo amene avomerezedwa ndi khonsolo potsatira pempho lochokera kwa ofuna kuchita malonda. Dziwani kuti aliyense wochita malonda malo amene khonsolo lavomereza amakhala ndi chiphaso, adatero Kasunda.
2
Ndale zogawanitsa miyambo zanyanya Si zachilendonso kumva kuti andale adzetsa ziwawa pamwambo wachikhalidwe. Lamulungu, kudali gwiragwira kokhazikitsa mwambo wag ulu la Ayao lomwe likutchedwa Chiwanja Cha Ayao. Pamwambowo, wothandizira wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino Saulos Chilima adamunjata pomuganizira kuti amachita zokaikitsa. CSOs in Pay Back Our Money campaign Govt to review Genset deal Govt moves to audit firearms Othandizira Chilima (pakati) adamangidwa pochita zokaikitsa Anthuwo ati adali ndi mphatso yochoka kwa Chilima koma adalephera kupereka chifukwa cha zovuta zina. Izi zimachitika patangotha mwezi, patabukanso chisokonezo pamaliro a Themba la Mathemba Chikulamayembe mboma la Rumphi. Mpungwepungwe udadza pamene ampingo adalandidwa chimkuzamawu pamene amapereka mpata kwa Chilima ndi mtsogoleri wa zipani zotsutsa Lazarus Chakwera kuti alankhule. Nakonso ku mwambo wa Gonapamuhanya wa Atumbuka kwakhala kukuchitika zisokonezo zodza ndi andale kwa zaka ziwiri zotsatizana. Mmalo mopitira zomwe ayitanidwira, andalewo amafuna kupikisana ku miyamboyo ndipo salola kugonjerana. Polankhulapo pa mchitidwewo, kadaulo wa ndale pa sukulu ya ukachenjede ya University of Livingstonia George Phiri adati vuto lalikulu limabwera chifukwa okonza miyamboyo amapereka gawo lalikulu kwa andale. Phiri adapereka chitsanzo cha mwambo wa kulamba omwe Achewa amakonza mdziko la Zambia komwe ngakhale kumapita andale, sapatsidwa mphanvu. Iye adati izi zimathandiza kuti kumaloko kusakhale mpikisano ndi kudzionetsera pakati pa zipani. Achikhalidwe azionetsetsa kuti mwambowo uli mmanja mwawo osati kuwapatsa andale, adalongosola Phiri. Iye adatinso vuto lina limadza maka andalewo akatenga gawo lalikulu popereka thandizo lokonzera mwambo wa mtunduwo. Tiyeni tisiye zomachita ndale paliponse chifukwa zikuononga chikhalidwe. Tizilekanitsa zinthuzi, adatero Phiri. Naye mbusa Macdonald Sembereka yemwe ndi mmodzi wa akuluakulu omwe adakonza mwambo wa Chiwanja cha Ayao adati vuto la andale ndi loti amafuna kudzionetsa kuti wa mkulu mndani ku miyambo yachikhalidwe. Sembereka adati andalewo amaphangira ku zochitikazo mpaka kuononga miyambo ya chikhalidwe. Khalidwe ili silikuthandiza chikhalidwe chathu. Tikuwapempha kuti asamapezerepo mpata wotsatsa malonda awo pa miyamboyo, adatero Sembereka. Iye adatinso andalewo ngofunika kulolerana pa nthawi ngati imeneyo ndipo adapereka chitsanzo cha mtsogoleri wopuma wa dziko lino Joyce Banda yemwe ngakhale ali wa mtundu wa Chiyao sadakhale nawo. Anthufe tikungoyenera kudziwa kuti chikhalidwe nchachikulu kuposa ndale ndipo ndale zikufunika kulamulilidwa ndi chikhalidwe, adatero Sembereka. Wapampando wa gulu losunga chikhalidwe cha Achewa, Kanyama Phiri adati gululo limakana kutengapo gawo pa ndale chifukwa malamulo awo ochokera kwa Gawa Undi sawavomereza kutero. Phiri adati popewa andale kuwasokonezera zachikhalidwe chawo, gululo amakakumana kwa Gawa Undi basi. Palibe cholakwika kuwaitana andalewo koma mpofunika kukhazikitsa ndondomeko zoti azitsatira akafika pamalowo, adatero Phiri. Naye Gogo Chikalamba Gondwe yemwe amakonza mwambo wa Atumbuka wa Gonapamuhanya omwe wakhala ukukumana ndi mazangazime chifukwa cha andale, adati gulu lawo tsopano lidaika ndondomeko zomwe andalewo amatsatira popewa chisokonezo. Komabe tinene kuti nthawi zambiri tikayandikira nthawi yosankha atsogoleri, andalewo amalowerera ndithu cholinga choti anthu awadziwe, adatero Gondwe. Iye adati gulu lake lidawauza andalewo kuti akamapita ku mwambo wa Gonapamuhanya, azikangoonera osati kuchitapo ndale.
11
Amayi omwe ali ndi kachilombo akufuna mudzi wawo Amayi omwe ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka HIV kwa T/A Kalolo ku Lilongwe apempha boma kuti liwapatse mudzi wawo kuti azipindula nawo pa ndondomeko ya zipangizo za ulimi zotsika mtengo ya sabuside. Amayiwa ati mafumu a mmidzi yomwe akukhala amawasala mnjira zambiri kuphatikizapo pa kagawidwe ka makuponi ogulira zipangizozi zomwe zimapangitsa kuti mabanja awo azikhala ndi njala chaka ndi chaka. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Iwo adapereka pempholi pamsonkhano omwe bungwe lowona za maufulu a anthu la Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR) lidakonza kumudzi wa Kalolo ku Lilongweko kuti amaiwa akumane ndi akuluakulu osiyanasiyana kuti apereke madandaulo awo pazovuta zomwe amakumana nazo. Mkulu wa gulu lina la amayi omwe ali ndi kachilombo la Kalolo Community Aids Coordinating Committee Tisauke Nazoni wati amaiwa amaphonya kamwedwe ka mankhwala obwezeretsa chitetezo mthupi, ma ARV, chifukwa chosowa chakudya zomwe zimaika miyoyo yawo pachiopsezo. Nzokhumudwitsa kuona kuti makuponi akuperekedwa kwa anthu oti ali ndi mphamvu oti akhoza kudzipezera zipangizo mosavuta koma tikati tiyesere kudandaula amati tipalamula. Ma ARV amafunika chakudya chokwanira koma nthawi zina timalephera kumwa chifukwa palibe chakudya. Timatha kukhala ndi njala kuyambira mmawa mpaka madzulo, adatero Nazoni. Koma woyendetsa ntchito zaulimi ku Chileka EPA komwe amaiwa amachokera Chrissie Chiusiwa wati pempho la amaiwo silingatheke chifukwa midzi yolandira zipangizozi imatengera malire a ma T/A omwe amapereka ndondomeko kuboma. Iye adapempha amaiwo kuti akadandaule kuofesi yoyendetsa za ulimi kapena kuofesi ya bwanamkubwa wa Lilongwe kuti akawathandize. Mfumu yaikulu Sakuzamutu idavomereza kuti mafumu angonoangono ena amachita za chinyengo, kupondereza anthu. Iye adati aitanitsa mafumu onse kuti akhale nawo pansi ndi kukambirana nawo kuti mchitidwewu uthe. Ndizachisoni chifukwa anthu ngati amenewa ndiamene boma limaganizira mmapologalamu ngati awa a sabuside tsono ngati mafumu akutenga zinthuzi ndikumagawira anthu amphamvu kale ndiye kuti tikuchitapo chiyani? Tikhala nawo pasi kuti tikonze zonse, adatero Sakuzamutu.
6
MBTS Ipempha Anthu Apitilize Kupereka Magazi Wolemba: Glory Kondowe uploads/2019/09/blood-donors.jpg" alt="" width="530" height="450" />Ena mwa anthu akupereka magazi nthawi ya mbuyomu Bungwe lotolera magazi mdziko muno la Malawi Blood Transfusion Services (MBTS) lapempha anthu mdziko muno kuti apitirize kupereka magazi ndi cholinga chofuna kupulumutsa miyoyo ya anthu ochuluka mu zipatala zosiyanasiyana. Wofalitsa nkhani za bungweli mdziko muno a Allen Kaombe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi. Iwo ati udindo wopereka magazi ndi wa wina aliyese ndipo anatsutsa zimene anthu ena amaganiza kuti kupereka magazi ndi ntchito ya ophunzira okhawokha a msukulu zosiyanasiyana. Mwa zina a Kaombe ayamikira anthu omwe amadzipereka popereka magazi ku ma ofesi awo zomwe ati ndi zofunika kwambiri. Iwo akumbutsa a Malawi kuti anthu omwe akuyenera kupereka magazi ndi aliyense oyambira zaka 15 zakubadwa kulekeza 65 ndipo ndi anthanzi. Sizoti ndi ana a sukulu wokha ayi ndipo ndikupempha a Malawi onse kuti ndi udindo wawo kupereka magazi ku bungweri, anatero a kaombe. Iwo ati magazi omwe amafunikira mdziko muno ndi 120 thousand litres pa chaka ndipo amene latolera ndi 58 thousand yomwe ndi 50 percent yokha basi.
6
Kwaya ya Masiphumelere Ichita Ubale ndi Abwenzi a Tchalitchi la Kankhomba Kwaya yopangidwa ndi akhristu a mpingo wakatolika a kuno ku Malawi koma akukhalira ku Capetown mdziko la South Africa ya Fishhoek Masiphumelere yayamikira ubale wabwino umene ulipo pakati pa kwayayi ndi bungwe la abwenzi a tchalichi la Kankhomba mu parish ya Thunga mu arch-dayosizi ya Blantyre, koma akukhalira mdziko lomwelo la South Africa. Wapampando wa kwaya-yi a Mosses Lusale ndi omwe anena izi pakutha pa mwambo wa Paper Sunday yomwe kwayayi inachita ngati njira imodzi yofuna kupeza thandizo la ndalama zojambulira chimbale chawo. Iwo ayamikira mamembala bungwe la abwenzi a tchalichi la Kankhomba omwe akukhalira ku Capetown mdziko-mo kaamba kofika ndi kudzawathandiza pa mwambo-wu. Pamenepa a Lusale ati zomwe zachitikazi zasonyeza umodzi umene ulipo pakati pa magulu awiri-wa. Polankhulanso mmodzi mwa mamembala a bungwe la abwenzi atchalichi la Kankhomba mu parish ya Thunga mu arch-dayosizi ya Blantyre okhalira mdziko la South Africa-wa a Velonica Makawa, ati ndi wokondwa ndi ubale-wu.
13
Kusamvetsetsana kwabuka ku Mwanza Kusamvetsetsana kwabuka pakati pa anthu a ku Mphete mboma la Mwanza ndi ofesi ya DC wa bomali chifukwa cha nyumba ya mphunzitsi pasukulu ya Mphete imene kampani yokonza njani ya Vale Logistics idagwetsa. Malinga ndi mlembi wakomiti yoyendetsa ntchito za pasukulu ya Mphete, Allan Gaviyawo , mchaka cha 2012 a kampani ya Vale Logistics adagwetsa nyumba ya mphunzitsi imodzi pasukulu ya Mphete chifukwa inali pamalo pomwe payenera kudutsa njanji yomwe ikudutsa mdziko muno kuchokera ku Mozambique. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Gaviyawo adati kampaniyi idalonjeza kuwapatsa anthu a mderali ndalama zokwana K1.5 miliyoni kuti amangire nyumba ina pamalo ena zomwe anthu a mderali adakana ponena kuti ndalamayi siinali yokwana kumangira nyumba ina yamakono ngati yomwe inagwetsedwayo yomwe inali mphatso kwa anthu a mderali kuchokera kubungwe la European Union. Zitachitika izo, kampaniyo idalonjeza kupereka K12.7 miliyoni yoti nyumba ina imangidwe zomwe anthuwa adagwirizana nazo popeza amayembekezera kuti ndalamayi ikanakwanira kumanga nyumba ziwiri zamakono za amphuzitsi mmalo mwa imodzi. Anthu a mderali anadabwitsika poona kuti ndalamazi zinakapelekedwa kuofesi ya DC yomwe idabwera kudzamanga nyumbayo ndipo anthu aku Mphete sakukhutisidwa ndi nyumba yomwe ofesi ya DC wa boma la Mwanza yamanga pasukulu ya Mphete pakuyerekeza ndi ndalama yomwe idaperekedwa yomangira nyumbayi, adatero iye. Wapampando wa khonsolo ya Mwanza Moses Walota adati iye ndi makhansala anzake mbomali atakayendera nyumbayo adakhumudwa ndi momwe nyumbayo ayimangira ndipo sadakhutisidwe ndimamangidwewo. Walota wanena kuti ataona izi analembela kalata bwanankubwa wa boma la mwanza yomuunikira zolakwika zomwe mankhansalawa anapeza panyumbayi zoti zikonzedwe nyumbayi isanaperekedwe kwa anthu aku mphete mmboma la Mwanza. Koma mpaka lero kalatayo siinayankhidwe ndipo zolakwika pa nyumbayo sizinakonzedwebe. Poyankhapo pankhaniyi DC wa boma la Mwanza Gift Lappozo wavomereza kuti nzoona kuti kontilakitala yemwe adapatsidwa ntchitoyi wayithawa atagwira ntchito yosasangalatsa kumapeto kwenikweni kwantchitoyi koma bwanankubwayu adati padakalipano ofesi yake ikuunikanso bwinobwino mgwirizano omwe anagwirizana ndi kontilakitayu asanapeze wina oti amalizitse ntchitoyi Koma iye wakana kuti kontilakitayu adapatsidwa ndalama zonse zokhudza ntchitoyi koma kuti amalipidwa mzigawo akamaliza chigawo chilichonse chantchitoyi moyenerera. Lapozo adati kusamvetsetsana komwe kulipo pakati pa ofesi yake ndi anthu aku Mphete kwadza chifukwa cha kusadziwa momwe ofesi ya bwanankubwa imachitira pogwira ntchito ngati zimenezi komwe anthuwa alinako ndiponso chifukwa chokuti anthuwosakufuna kumva kufotokoza komwe akhala akufotokzeredwa ndi ofesi ya DC pazankhaniyi.
7
Samalani maso popewa khungu Khungu ndi amodzi mwa matenda a maso opeweka. Katswiri wa maso pa chipatala cha Chiradzlu Frank Mwamadi wati izi zimachitika munthu akasamalira bwino maso ake. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Iye adati munthu wakhungu ndi amene maso ake onse sakuona. Mwamadi: Khungu ndi lopeweka Khungu limadza mwadzidzidzi kapena pangonopangono, adatero mkuluyu. Mwamadi adati khungu ndi amodzi mwa matenda omwe amabwezera mmbuyo chitukuku cha munthu. Munthu wakhungu amakanika kugwira ntchito, kupanga maphunziro, kuyenda, komanso kusonkhana ndi anzake pa zochitika zosiyanasiyana, adatero katswiriyu. Ngakhale khungu ndi loopsa, katswiriyu watsindika kuti pali kuthekera kothana nalo kuti asayale maziko pa moyo wa munthu. Iye adapereka chitsanzo monga kuyezetsa maso pafupipafupi ku chipatala, kupereka zakudya za Vitamini A kwa ana, komanso kuchita ukhondo. Pamene ana akupatsidwa Vitamini A wokwanira anthu akuluakulu akuyenera kuchititsa opaleshoni diso kapena maso awo akapanga ngala chifukwa imaika maso pa chiopsezo cha khungu, adatero katswiriyu. Mwamadi adalangiza anthu kuti pamene akukumana ndi vuto la maso azithamangira ku chipatala osati kugwiritsa ntchito mankhwala azitsamba.
6
Mawu a JB ndi loto Akuluakulu a mabungwe ena ati mawu a mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda potsegulira msonkhano wa aphungu Lachisanu lapitalo ndi loto la chumba chifukwa ngakhale adapereka chiyembekezo kwa Amalawi, zinthu zikupitirira kuthina. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zadza chifukwa patangotha maola ochepa Banda atangopereka uthenga wa chikhulupiriro ndi chiyembekezo kuti zonse ziyenda, mtengo wamafuta udakwera pomwe bungwe loona za mafuta la Malawi Energy Regulatory Authority (Mera) lidalengeza kuti petulo wakwera kuchoka pa K606.30 kufika pa K704.30 pomwe dizilo adafika pa K683.60 kuchoka pa K597.40. Malinga ndi mkulu wa bungwe la ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito kukwerako kukutanthauza kuti zinthu zikweranso mitengo ndipo Amalawi afinyika, kuphwetseratu chiyembekezo chimene Banda adapereka. Iye adati Amalawi akuyenera kudikira zaka 15 kapena 20 zikubwerazo kuti mfundo zomwe Banda adalankhula zidzayambe kupindulira anthu. Adangochekenira chifukwa izi ndizo akhala akuzinena. Zangosonyezeratu manthu wamavuto. Akungonena loto chabe koma osati Amalawi angayembekezerepo kanthu. Zambiri akukamba monga za Kayerekera sizingapindulire munthu wakumudzi panopa. Chiyembekezo chingabwere ngati pali njira zopindulira Amalawi monga za ntchito zomwe anthu amagwira kumudzi komanso mfundo zotukulira anthuwo koma zomwe zilipo ndikungosangalatsa omvera, adatero Kapito yemwe adati uthengawo udali wa ndale chabe. T/A Mphuka wa mboma la Thyolo adati padakali pano anthu mdera lake komanso madera ambiri mdziko muno akupanidwa malinga ndi mavuto ambiri, kuphatikizapo kukwera mtengo kwa mafuta kwa posachedwapa. Padakali pano zinthu zina zayamba kale kukwera mtengo. Koma pa mawu a Banda, sindinganenepo kanthu chifukwa ndikudziwa kuti monga mtsogoleri wa dziko lino amaona zapatali choncho mavuto amene alipo panopa akhoza kutha monga akunenera, adatero Mphuka. Ndipo mkulu wa bungwe loona kuti nkhani zachuma zikuyenda mokomera onse la Malawi Economic Justice Network (Mejn) Dalitso Kubalasa wati zomwe Banda adalankhula zakhala zikukambidwa ndi bomali ndipo wati ndibwino kulankhulaku kuthe ndipo ayambe kukwaniritsa. Uthengawu ukungofuna kuthunzitsa anthu mtima. Adanenapo kuti nduna ziziunikidwa momwe zikugwirira ntchito. Sitikudziwa ngatinso izi zili pa ndondomeko yofuna kubwezeretsa chuma cha dziko lino. Zalankhulidwa zambiri koma Amalawi akufuna zooneka kuti akhale pa mpumulo osati kungolankhula, adatero Kubalasa. Koma kadaulo wa ndale, Blessings Chinsinga adati zikukaikitsa ngati Amalawi angatonthole monga Banda adanenera muuthenga wake ponena kuti pakufunika ntchito ichitike. Iye adadzudzulanso Banda kuti palibe chomwe akuchita pofuna kukwaniritsa mfundo zokonzanso chuma cha dziko lino zomwe zili mu Economic Recovery Plan (ERP). Akuyenera kuyanganira zambiri. Sitikudziwabe yemwe akuyanganira ndondomeko ya ERP, nanga tikuchitanji kuti tifikire mlingo omwe tikufuna? Tikumvanso kuti mabilu a foni akuchita kufika mamiliyoni osaneneka. Izi zititengera nthawi kufi tifikire pachomwe tikufuna ngati dziko. Ndikaona uthengawu wangochuluka kulankhula zina zomwe akhala kale akulankhula koma chiyembekezo mulibe chifukwa anthu amadikira ntchito osati mawu, adatero Chinsinga. Masiku apitawa, kudamveka kuti nyumba ya boma kudali mabilu a foni okwana K98 miliyoni, mmiyezi 9 ndipo kampani ya mafoni ya MTL imafuna kukadula mafoni kunyumba ya bomayo. Ndipo nkhani ya mavuto a za chuma ili mkamwa, ogwira ntchito mboma Lachiwiri adayamba sitalaka yosonyeza kukwiya kwawo ndi malipiro ochepa, pamene mitengo ya zinthu ikupitirira kukwera. Iwo adatchinga zipata za kumaofesi a likulu la nthambi za boma ku Lilongwe ndipo atanyamula nthambi za mitengo adali kuimba kuti: Akulemera tikuona! Akunenepa tikuona. Malinga ndi mkulu wa bungwe la ogwira ntchito mboma la Civil Service Trade Union (CSTU) Eliah Kamphinda Banda akufuna malipiro akwere molingana ndi ogwira ntchito mmakampani. Ogwira ntchito mboma tatopa ndi kudya bonya. Sitibwerera kuntchito malire ake boma litiganizire. Boma likuchedwa dala kuti lionjezere malipiro athu ndipo tikumva kuti akweza malipiro mu Julaye ndi 5 peresenti. Sitingalole, adatero Banda. Ndipo dzulo lidali tsiku lomaliza limene bungwe la Cama lidapereka ku boma kuti likonze mfundo zina zimene amati zikulakwika mchikalata chomwe adachipereka pakutha pa zionetsero za pa 17 January. Pomwe timasindikiza, mneneri wa boma Moses Kunkuyu adati aitanitsa akuluakulu a Cama kuti akambirane.
11
Ogwira Ntchito Mboma Ayamba Kunyanyala Ntchito Lolemba Bungwe loyanganira anthu ogwira ntchito mboma la Civil Servants Trade Union (CSTU) lauza anthu onse ogwira ntchito mboma kuti ayambe kunyanyala ntchito kuyambira lolemba likudzali. Njolomole: Tikufuna kulikumbutsa boma zomwe tinagwirizana Mlembi wa bungweli Madalitso Njolomole wauza Radio Maria Malawi kuti iwo aganiza zochita izi kutsatira kutha kwa masiku 21 omwe anapereka ku boma kuti likhale litakweza pa ntchito anthu onse omwe agwira ntchito mboma kwa zaka zoposera zisanu ndi chimodzi (6). Iye wati kusachitapo kanthu kwa boma pa nkhaniyi kukusonyeza chibwana chachikulu ndipo ati kunyanyala ntchitoku kuchitika mpaka pa 12 June pomwe adzabwerenso ndi ganizo lina ngati boma silichitapobe kanthu. Tikungofuna kulikumbutsa boma kuti lipange zomwe tinalipempha kuti likweze ma a Civil Servants onse omwe akhala pa malo omwewomwewo kwa zaka 6 kupita mtsogolo, anatero a Njolomole. Iwo ati kwa omwe padakali pano sakugwira ntchito apitirize kukhala mmene akukhalira koma kwa omwe amapita ku ntchito atha kumapitabe koma ati asamakakhalitseko monga momwe amachitira kale.
14
Afuna chitukuko chofanana mmadera a aphungu Ntchito za chitukuko mmadera oyimiriridwa ndi aphungu a ku Nyumba ya Malamulo chiyamba kufanana tsopano ntchito yodulanso malire ikachitika. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Bungwe loyanganira zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lati ntchitoyi tsopano ikungodikira katswiri wochokera kunja yemwe adzaigwire. Zonse zatheka tsopano tikungodikira katswiri yemwe achokere kunja kudzagwira ntchito yodulanso malirewa. Katswiriyu sitikumudziwa koma atumizidwa ndi akuluakulu a bungwe la Commonwealth, chidatero chikalata chomwe bungweli lidatulutsa. Mneneri wa bungwe la sisankho mdziko muno, Sangwani Mwafulirwa, adati kudulanso malirewa kuthandiza kuti aphungu onse 193 azikhala ndi madera ofanana komanso chiwerengero chofanana cha anthu. Madera ena pakalipano ndi aakulu kwambiri pomwe ena ndi aangono kwambiri ndiye poti aphungu amagwira ntchito imodzi, tikufuna kuti madera awo akhale ofanana kuti ntchito ikhalenso chimodzimodzi, adatero Mwafulirwa. Iye adati mwachitsanzo dera la chigawo cha pakati mboma la Lilongwe ndicho chili chachikulu kwambiri ndi anthu oponya voti 126 115 pomwe dera la chilumba cha Likoma ndicho chochepetsetsa ndi anthu ovota 6 933 basi. Ngakhale pali kusiyana kotereku ndalama za chitukuko zomwe aphungu amalandira zotukulira madera awo zimakhala chimodzimodzi kutanthauza kuti ndalama zomwezo kwina zikuthandiza anthu ochuluka kuposa kwina. Ngakhale zinthu zili choncho, palinso nkhani yosintha ndondomeko ya kayendetsedwe ka chisankho yomwe kauniuni wa malamulo akale adachitika ndipo komiti yomwe imachita kauniuniyu idatulutsa kale zotsatira zake. Imodzi mwa mfundo zikuluzikulu mndondomeko yatsopanoyi ndi yakuti aphungu asamakhale ndi malire koma kuti boma lililonse lizikhala ndi chiwerengero cha aphungu potengera chiwerengero cha anthu mbomalo. Mwafulirwa adati bungwe la MEC silinganenepo kanthu pa za tsogolo la ntchito yodulanso madera a aphungu potengera malamulo atsopanowa pokhapokha nthambi ya zamalamulo idzanene mfundo yomaliza. Nzoonadi, ndondomeko yatsopanoyi idapangidwa koma sidaperekedwe kunthambi ya zamalamulo (Law Commission). Zonse zidzidziwika nthambiyi ikadzanena maganizo ake. Panopa tiyeni tibatsata zomwe zilipo, adatero Mwafulirwa.
11
Anatchezera Ndimufunsirebe? Ndine mnyamata wa mu Lilongwe ndipo ndidagwa mchikondi ndi msungwana wina. Ndakhala ndikuponya mawu kwa iye koma iyeyo amayankha moti savomera kapena kundikana. Kodi ndipitirizebe kumufunsira? Ndithndizeni ndazunzika maganizo. B, Lilongwe. Zikomo B, Ndikuyankha molingana ndi kuti siunandiuze kuti wakhala nthawi yaitali bwanji ukuyesa mwayi wako. Zikuoneka kuti msungwanayo sanapange chiganizo chokulola kapena kukukana. Nthawi zambiri msungwana akakhala mmalingaliro otero nchifukwa chakuti akukukayikira. Chikaikochi chikudza chifukwa pali zina zimene adamva za iwe ndiye akadali kulingalira kuti apange chisankho payekha. Komanso iweyo mwina chidwi chako ukungoonetsa kuti ukumufuna. Tsono akalola, chotsatira chidzakhala chiyani? Mwinatu msungwanayo malingaliro ake ndi akuti akufuna kupeza mwamuna wa banja pamene iwe ukungoonetsa zizindikiro za chibwenzi basi. Pomaliza ndiyenera kukuuza kuti ngati wayesa kumufunsira koma siukulandira yankho loyenera, bwanji osayamba wakhala mnzake nkumacheza zina ndi zina? Akuyenera kukumvetsetsa kaye kuti umaganiza chiyani, nanga umafuna chiyani asanakulole. Izo ndiye udziwe. Mbali inayi, ungodziwanso kuti fupa lokakamoza limaswa mphika choncho ngati watha nthawi yaitali ukuyendera, ndi bwino kuyangana kwina. Nthawi siyibwerera. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Wokwatira wandipatsa mimba Zikomo Gogo, Ndinapanga chibwenzi ndi mwamuna wina amene ankaonetsa Chikondi kwambiri pa ine. Izi zili choncho, mwamunayo sanandiuze kuti ndiwokwatuira koma nditamva kwa ena ndidamufunsa adayankha kuti akufuna kumusiya ndipo andikwatira ineyo. Inetu ndili pasukulu ndipo zisanatheke zoti andikwatirezo, wandipatsa mimba pano akuti ndizikhala kwathu ndipo azingondithandiza. Kodi ndipange bwanji pamenepa. VD, Chiradzulu. VD, Ndi ambiri asungwana ndi amayi amene ali ndi nkhani zotere. Zagwa zatha, ukuyenera kuyangana kutsogolo. Pali zinthu ziwiri zimene ndingakulangize. Choyamba, udziwe kuti ngati wakupatsa mimba, nkhaniyi ukuyenera kuitengera kukhoti la majisitileti. Malamulo atsopano a ukwati akusonyezeratu kuti wopereka mimba nkuthawa akuyenera kubweretsedwa pamaso pa oweruza. Kukhotiko nkomwe akatambasule kuti akuyenera kukuthandiza motani. Chachiwiri chimene ndinganena nchakuti usataye mtima kulekeza sukulu panjira chifukwa uli ndi pathupi. Osataya pathupipo monga ena angaganizire. Ukuyenera kukabereka ndipo ukalera ndi kuyamwitsa mwana wakoyo mwakathithi, udzabwerere kusukulu. Sukulu ndi tsogolo lako lowala ndipo udziwe kuti udzatha kuthandiza bwino mwana wakoyo moti bamboyo adzachita manyazi. Koma osaiwala kutengera nkhaniyi kukhoti. Andipatse mimba? Agogo, Ndinali ndi chibwenzi chimene ndakhala nacho zaka 4 ndipo takhala tikugwirizana za ukwati. Koma posakhalitsapa anangosintha nkumanena kuti akufuna andipatse mimba koma adzandikwatira zaka ziwiri zikubwerazi. Kodi pamenepo pali chikondi? Chonde ndithandizeni. RC, Mzuzu. RC, Apa palibepo chikondi. Akupatse mimba ya chiyani? Adzakukwatira zaka ziwiri zikatha chifukwa chiyani? Zaka 4 zonse zapitazo asanakukwatire akufuna chiyani? Udabwe nazo. Kodi anatu amayenera kukhala mphatso ya mbanja ngakhale ena angathe kukhala ndi chisankho chokhala ndi ana a mwamuna kapena mkazi amene sanakwatirane naye. Choti udziwe, amuna ena amangofuna kukupusitsa. Uyu akhoza kukhala mmodzi mwa amuna otere. Nanga mpaka kukuuza kuti akufuna kukupatsa mimba? Nkutheka iyeyo akuuzanso akazi ena atatu chimodzimodzi. Tsono udzatani nonse mukalolera kutenga mimba kuchoka kwa iye? Khala pansi, sunthapo phanzi asakutaire nthawi.
12
Mpoya Akhazikitsa Thumba la Ndalama Zolipilira Ana Sukulu Phungu wa m`dera la Mtonya m`boma la zomba a Nedson Mpoya wati komiti yomwe isankhidwe kuti iyendetse thumba ia ndalama zolipilira ana osowa sukulu fizi m`sukulu Bursary m`derali iwonetsetse kuti yalemba ana oyenera. A Mpoya omwe amayimira chipani cha UDF m`delaro wati ndalama zimenezi ndi Constituency Development Fund (CDF) choncho oyang`anira thummali ndi phungu waku nyumba ya malamulo choncho anthu-wa akuyenera kuonetsetsa kuti pasankhale kukondera kapena katangale posankha ana ovutikawa omwe azilipilipiridwa sukulu ndi komitiyi. Mwazina iye wachenjezanso anthu omwe akumagulitsa ma form ogwilitsira ntchito yolembera ophunzirawa kuti akkapezeka alandila chilango popeza ma form-wa ndi aulele. Chomwe ndikufuna kutanthauza kwambiri tidagozindikira ma form atabwera ku ma constituency kwanthu kuno ndiye timafusa kuti maform-wa abwera bwanji, anatero a Mpoya. A Mpoya ati ndondomekoyi si momwe adakonzera poyamba koma ati zakhala chomwechi chifukwa choti zinthuzi zangochitika mwadzidzidzi.
3
Milandu yachepa ku Blantyre Milandu yosiyanasiyana mu mzindawa Blantyre yatsika kuchoka pa 328 mu February chaka chatha kufika pa 204 mwezi omwewo chaka chino, atero apolisi. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wachiwiri kwa mneneri wa polisi mu mzindawo, Dorrah Chathyoka adati iyi ndi nkhani yosangalatsa. Kutanthauza kuti milandu yomwe anthu amapalamula yatsika ndi 37.8 pa 100 iliyonse. Iyi ndi nkhani yabwino kutsimikizira ntchito yomwe apolisi a Blantyre akugwira usiku ndi usana, adatero Chathyoka. Iye adati polisi yawo idakhazikitsa ndondomeko zothana ndiupandu zomwe zayamba kubala zipatso. Mwazina ndikuyendayenda komwe apolisi akuchita mmadera onse. Ena akumavala zovala za polisi ndi ena zovala zawamba kuti tithane ndi upandu, adatero iye. Izitu zikumachitika usiku ndi usana pamene tikumayenda pa galimoto, njinga komanso ena kuyenda wapansi. Takhazikitsanso zipata mmisewu, tikumatola onse amene akuyenda nthawi yosaloledwa popanda chifukwa chenicheni, adaonjeza Chathyoka. Iye adati zinanso zomwe achita ndikupanga ubale wabwino pakati pa apolisi ndi anthu okhala mumzinda wa Blantyre. Tidakhazikitsa polisi yammadera, tikulankhulana bwino ndi anthu. Komanso kugawana maganizo ngati pafunika kutero. Chathyoka adati kudzera mnjira zotere, apolisi akumanjata owaganizira kupalamula mlandu mosavuta pamene anthu akumawatsina khutu. Anthu akupemphedwa kuti apitirize kupanga ubale wabwino ndi a polisiwa kuti nkhani yabwinoyi ichitika kwa nthawi yotalikirapo. Cholinga ndi kupanga Blantyre wokomera aliyense, adatero.
7
Bungwe La Amayi Ku Mphakati Wa St. Clara Lalimbikitsa Amayi Kuthandiza Radio Maria Bungwe la amayi ku mphakati wa St. Clara omwe uli pansi pa St. Dennis parish mu Arch-Diocese ya Lilongwe, lalimbikitsa amayi kuti adzitenga nawo mbali pothandiza Radio Maria Malawi. Wapampando wa bungweli ku mphakatiwu mayi Idah Nkhoma ndi omwe anena izi lolemba pambuyo pa mkumano omwe mphakatiwu unali nawo pomwenso anapezerako mwayi othandiza wailesiyi pa nthawi ino pomwe wailesiyi ikuchita Mariatona. Iwo anati kuthandiza Radio Maria kumathandiza kuti ntchito za wailesiyi zipite patsogolo. Tinawona kuti tikamakumana ngati azimayi, kakangono kamene tilin ako tikuyenera kuthandiza wailesi yathu yomwe imatidalitsa kuti ikathandizenso anthu ena, anatero mayi Nkhoma. Mmodzi mwa amayi omwe anachita nawo mkumanowu mayi Patricia Mwapasa anati ndi okondwa popeza athandiza wailesiyi mu nyengo ino ya Coronavirus pomwe ntchito zambiri zikuoneka kuti zakhudzidwa kwambiri ndipo sizikuyenda bwino.
13
Abusa ku HIH ndi zina Tsikulo ndidali pa Wenela kuitanira minibasi monga mwanthawi zonse. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndirande iyi! Machinjiri iyo! A Lilongwe achamba atatu iyo yopita! Ndati achangu atatu a Lilongwe iyi! Mukudziwa kale. Nthawi imeneyo nkuti ndikumveratu nyimbo zatsopano zokhazokha, ma headphone ali kukhutu. Pamaphulikatu nyimbo zongomasula kumene: Namadingo adabwera ndi Msati Mseke, Wambali amvekere Asungwana a kwa Chitedze, anyamata a ku Chileka akuti Mr Bossman ndipo Lucius akuti Walema. Osaiwala munthu wamkulu Nkasa akufwamphula Anenere. Ndidachotsa ma headphone mkulu wina atandikodola. Iyetu adali atangotsika basi ndipo ndidadziwiratu kuti ndi mbusa. Musandifunse kuti ndidadziwa bwanji chifukwa sindikuyankhani. Ndipo nkakuuzani kuti ndidaonera mwinjiro wake wakuda, ndi kolala yoyera muchitapo chiyani? Nanga nkakuuzaninso kuti simukudziwa kolala yoyerayi idabwera bwanji mulephera kuyankha. Ndangokhala muno muliyenda kuchoka kwathu kwa Kanduku komwe ndidasiya mkazi wanga wokondeka, Nambe, koma ndimadziwa kuti nthawi imeneyo abusa ankaphedwa pochekedwa makosi. Iyitu idali nthawi yowawitsa pamene kukhala mbusa chidali chinthu choopsa zedi. Komatu abusa anthawiyo adali olimba mtima ndipo adayamba kuika kolala yoyera pakhosi kuti langa ndi limeneli liduleni koma sindisiya kufalitsa uthenga wabwino, kuthandiza kuti ochimwa asinthe ndipo iwo ali olungama apitirize kutero. Ameni? Atsogoleri, inetu wanga ndi wa ku HIH, ndikwere ya chiyani? adandifunsa. Ya Ndirande, kapena ya Machinjiri. Kwerani iyi abusa. Ya Machinjiri ndi K200, ya Ndirande K100. Simufuna bodyguard? Ndikumvatu kwaterera, ndidatero. Adangoseka, uku akukwera minibasi ya Ndirande. Akukwera, ndidaona chisenga chikusuzumira. Madzulo a tsikulo, tili malo aja timakonda pa Wenela, adatulukira Abiti Patuma ali wefuwefu. Mkulu wina wandilipirira kuti ndipeze chitupa choyendetsera galimoto. Koma eeeh! Abale ku Ginnery Corner uku kuli gahena ndithu. Kudikira tsiku lonse uli chiimirire koma chitupa osatuluka, adalira. Bwanjinso nanga? ndidafunsa. Kuli mazunzo. Ena akundiuza ayendera masiku 8 nkhani yomweyi. Ukapolotu uwu. Tsono nthawi yotakata mtaunimu ikhalapo? Ndalama zopereka ndiye simasewera. Akatolera ndalamazo ndiye basi kususa kukhalepo. Osololawo aiwala kuti lero Adona Hilida athawa pano pa Wenela kuopa kukwizingidwa poti ena akuti akukhudzidwa ndi kusolola mopanda manyazi kudagundika ku Kapitolo, adatero Abiti Patuma. Palibe icho ndidatolapo. Mwati chiyani? adafunsa wapamalopo, Gervazzio. Kodi simunamve kuti Mani Rich alembera akatalangwe ena kuti Adona Hilida akusautsidwa mmaganizo ndi anthu amene akusaka moyo wawo? Nanga simunamvenso kuti uja wa mabasi Leo wachita muja adachitira Pitapo, kunena kuti Adona Hilida ndiwo adawatuma kusolola khobidi? adayankha Abiti Patuma. Tonse tidangoti kukamwa yasaa! Man Rich amafatsa! Atatsegula wailesi Gervazzio, tidangomva mkulu uja adawerenga kwambiri vesi yaifupi mbaibulo akulankhula. Mwamuiwala kale mkuluyu? Nanga ndichite kukuuzani za vesi ija imati Yesu analira? Kapena mwamuiwala mkulu woyanganira maula adalira pomwe adanena kuti Moya Pete ndi Dizilo Petulo Palibe ndiwo akadaulo pobera maula? Amene apambana ndi Dizilo Petulo Palibe, Ukafuna Dilu Fatsa komanso Male Chauvinist Pigs, adatero mkuluyo. Posakhalitsa adatulukira Kenny Foot Soldier Nsongo. Atiberanso maula. Panalibe chilungamo pamaula amenewa. Pali kukondera, adali kutero. Shhhhh! Tikumvera nkhani. Mipingo ina idzatha ngati makatani, adatero Abiti Patuma.
13
Akufuna fisi alangidwe koopsa Magulu omwe amalimbikitsa maufulu a amayi ati mpofunika mkulu woimira boma pa milandu Director of Public Prosecutions (DPP) Mary Kachale atengere nkhani ya Eric Aniva kubwalo lalikulu. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Aniva, yemwe adanjatidwa zaka ziwiri kukagwira ntchito ya kalavulagaga kundende atapezeka wolakwa pamlandu wotenga mbali pa miyambo yoopsa pokhala fisi wochotsa fumbi ndi kulowa kufa mboma la Nsanje. Adampatsa zaka ziwiri: Aniva Nkhani ya Aniva idagwedeza dziko atabwera poyera nkuulula kuti wakhala akugwira ntchito ya ufisi kwa nthawi yaitali ndipo adagonana ndi amayi ndi atsikana oposa 100. Koma magulu a amayi, motsogozedwa ndi mabungwe a Malawi Human Rights Resource Centre (MHRRC), NGO Gender Co-ordination Network (NGO-GCN) ndi African Womens Development and Communications Network (Femnet), ati chigamulo chomwe Aniva adalandira lachiwiri lapitali nchochepa. Maguluwa ati potengera mlandu wa Aniva, ufulu wa amayi sudalemekezedwe kotero amayenera kulandira chilango chokhwima osati zaka ziwiri basi. Ndife okhudzidwa kuti munthu yemwe ali ndi kachilombo ka HIV komwe kamayambitsa matenda a Edzi ndipo amapitiriza kugona ndi amayi ndi ana achichepere mpaka zaka 12 angalandire chilango chochepa chonchi. Ndi uthenga wanji omwe tikupereka kwa abambo ena akhalidwe longa lomweli? Zaka ziwiri basi mlandu wonsewu? Uku nkunyoza amayi ndipo bwalo la milandu likuyenera kuunikapo bwino nkusintha chigamulochi, adatero mkulu wa bungwe la MHRRC Emma Kaliya. Mabungwewa adati ngati nkhani yoyamba ya mtunduwu yoweruzidwa pogwiritsa ntchito lamulo latsopano la za ufulu wa anthu, Aniva amayenera kulandira chilango choletsa khalidweli. Naye mkulu wa zophunzitsa anthu kubungwe la Femnet, Hellen Apila, adati apa dziko la Malawi waphonya mwayi waukulu wopera chenjezo kwa anthu omwe salemekeza ufulu wa amayi potsatila miyambo. Bwalo la Magistrate ku Blantyre lidagamula Aniva lachiwiri lapitali kuti akagwire ntchito yakalavulagaga kundende atavomera kuti amachita mwambo wa fisi akudziwa kuti ali ndi kachilombo ka HIV.
7
Papa Wati Ali Limodzi Mmapemphero ndi Mzika za ku America Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco watsimikizira a Katolika ndi anthu onse ku United States of America kuti ali nawo limodzi mmapemphero. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa walankhula izi lachinayi kudzera mu uthenga wake wa pa lamya kwa President wa bungwe la ma episkopi a mpingo wa katolika mdziko la America, Archbishop Jose Gomez wa archdiocese ya Los Angeles. Iye wayamikira maepiskopi a mpingo wa katolika mdziko la United States of America chifukwa chosonyeza utsogoleri wabwino pomwe mdzikolo mukuchitika ziwawa chifukwa cha imfa ya nzika ya dzikolo, George Floyd. Kudzera mu uthenga wa pa lamya-wo Papa Francisco wati ali pafupi ndi anthu mdzikolo pa nthawiyi ndipo akuwapempherera. Papayu wayamikiranso maepiskopi a Mpingo wa Katolika podzudzula mchitidwe wa tsankho mdzikolo womwe wachititsa kuti George Floyd aphedwe. Papa Francisco wauza Archbishop Gomez pa lamyayo kuti mwapadera waikiza mmapemphero Archbishop Bernard Hebda ndi Mpingo wonse ku Minneapolis mdzikolo komwe Floyd adaphedwera. Lachitatu pa 3 June 2020 Papa Francisco adadzudzula kuphedwa kwa nzika ya chikudayi mdzikolo. George Floyd adaphedwa ndi wapolisi wina pa 25 May, 2020 ndipo padakali pano anthu ena asanu aphedwanso pa zionetsero ndi zipolowe zomwe anthu akuchita powonetsa kusakondwa kwawo.
13
Boma Lilonjeza Kumanga Ubale ndi Mpinga wa Katolika Wolemba: Thokozani Chapola Boma lati liyesetsa kumanga ubale wabwino ndi mpingo wakatolika mdziko muno. A Ralph Jooma omwe ndi nduna ya za mtengatenga ndi zomangamanga, kudzanso a Bright Msaka omwe ndi nduna ya zamalamulo anena izi pa mwambo wokhadzikitsa chimbale cha nyimbo zomvera ndi kuonera za kwaya ya mpingo-wu ya St. Annie ku St. Louis Montfort Parish ku Balaka mu dayosizi ya Mangochi. Iwo ati boma limadziwa zakufunika komanga ubale wabwino ndi mpingowu. Polankhulanso mmodzi mwa aphungu a chizimayi mboma la Balaka, mayi Bertha Mackenzie Ndebele anayamikira ntchito yotamandika yomwe mamembala a kwayi akugwira pofalitsa uthenga wabwino kudzera mu mayimbidwe. Kumwambowu kunafikanso a ndale ena monga olemekezeka a Chifundo Makande MP, kudzanso a Shadrick Namalomba MP. Mutu wa chimbale cha nyimbo zomvera ndi kuonera zomwe kwayayi yakhazikitsa ndi Ndanyamuka.
14
Dziko la DRC Latulutsa Akayidi 1200 Kaamba ka Coronavirus Unduna wa zachilungamo mdziko la Democratic Republic of Congo, watulutsa akayidi okwana 1,200 pofuna kuchepetsa kuchulukana kwa akayidi mndendezi ngati mbali imodzi yolimbana ndi kufala kwa kachilombo ka Coronavirus. Malingana ndi nduna mu undunawu Celestine Tunda, ena mwa omwe amasulidwa ndi omwe anali ndi milandu ingoingono. Ndende ya Makala yomwe ili mu mzinda wa Kinshasa ndi imodzi mwa ndendezi ndipo yamasula akayidi okwana 700. Ndunayi yati akayidi enanso akhala akumasulidwa posachedwapa ndipo yapempha oweruza milandu kuti azimanga okhawo omwe apalamula milandu ikuluikulu monga ya kupha ndi yogwirira. Mdziko la Democratic Republic of Congo mwapezeka anthu okwana 180 omwe ali ndi matendawa ndipo ena 18 amwalira. Padakalipano boma la dzikolo layimitsa zochitika zonse za mdera la Gombe mu mzinda wa Kinshasa kwa sabata ziwiri kaamba ka vutoli.
6
Bullets, manoma akunthana lero Kumakhala fumbi nthawi zonse Bullets (zifiira) ndi Wanderers akamakumana Tsoka mtunda ndi nyanja popeza woipayo watsikira pa Civo Stadium masanawa. Ligi ya TNM Super League tsopano yafika pa gwiritse. Nkhawa ili biii! Kwa osapotera timu ya Big Bullets ndi Mighty Wanderers pamene matimuwa akhale akuphananso masanawa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Iyi ikhala nkhondo yeniyeni chifukwa ngati Nyerere zipambane masewero asanu amene yatsala nawo ndiye kuti zikhala ndi mapointsi 55 kutanthauza kuti iposa matimu onse. Apa ndiye kuti zili ndi mwayi wophulanso ligiyi patangodutsa mwezi zitanyamula chikho cha Standard Bank. Koma mwina loto la Wanderers lingakhale lovuta chifukwa mphunzitsi watsopano wa Bullets, Gerald Phiri, akuti akulotanso atapambana masewero asanu amene timuyi yatsala nawo kuti mwina angathere pabwino kapena kutenga ligi. Bullets ikuchokera kolepherana mphamvu ndi Blantyre United. Iyo ili pa nambala 6 ndi mapointsi 36. Pamene Nyerere zikuchokera koboola jombo ya Moyale ku Balaka ndi zigoli ziwiri kwa duuu! Izo zili pa nambala yachiwiri ndi mapointsi 40 kutsogozedwa ndi Red Lions yomwe ili ndi mapointsi 41 koma yatsala ndi magemu anayi. Masewero a Wanderers ndi Bullets ali pa Civo pamene pakhale pakhomo pa Nyerere. Timuyi ndiyo yasankha bwaloli chifukwa pa Kamuzu idathamangitsidwa patachitika ziwawa ndipo siidamalize chilango. Koma mlembi wa Nyerere David Kanyenda akukhulupirira kuti lero Maule aona mbonaona. Mukaonetsetsa takhala tikuchita bwino, sitikuchinyitsa zigoli. Tikuchokera kopambana ndi Moyale, ndipo dziwani kuti Bullets ndi akazi athu, akutero Kanyenda. Matimuwa akumanapo kawiri posakhalitsapa. Mndime yoyamba ya ligiyi, matimuwa adalepherana mphamvu pochinyana chigoli chimodzi kwa chimodzi. Matimuwa adakumananso ku Lilongwe mubonanza ya Luso TV pomwe Bullets idapambana kudzera mmapenote. Matimu ena akhalenso akuphana mchikhochi masanawa. Mzuzu United ikhomana ndi Civo United pa Mzuzu Stadium. Evirom ithyolana ndi Blue Eagles pa Kamuzu. Jombo ya Red Lions ili pakhomo ndi Kamuzu Barracks ku Zomba. Mawa, Blantyre United iphwanyana ndi Blue Eagles pa Kalulu Stadium. Epac F.C ikwapulana ndi Silver Strikers pa Civo Stadium. Moyale ikumana ndi Civo United pa Mzuzu Stadium. Azam Tigers igogodana ndi Kamuzu Barracks ku Balaka Stadium. Evirom ikumananso ndi Mafco FC pa Kamuzu Stadium.
16
DPP, UDF Asayinira Mgwirizano Zipani za United Democratic Front (UDF) ndi Democratic Progressive (DPP) zati ndi zokonzeka kugwilira ntchito limodzi potukula dziko la Malawi. Muluzi (kumanzere) ndi Mutharika kusonyeza mgwirizano wawo Zipanizi zanena izi lachiwiri kunyumba yachifumu ku Lilongwe pomwe zimasayinirana mgwirizano kuti zigwilira ntchito limodzi pamene akukonzekera chisankho cha Pulezident chomwe chichitike pa 19 May chaka chino. Atsogoleri a zipani ziwirizi a Peter Mutharika komanso a Atupele Muluzi ati ndi okonzeka kugwilira ntchito limodzi kamba koti zipani zawo zimatsatira mfundo zofanana. Amayi a DPP komanso UDF kuvinira limodzi Pa 3 February chaka chino bwalo la milandu ya zamalamulo linalamula kuti chisankho chomwe chinachitika mdziko muno pa 21 May chaka chatha ndi chosavomerezeka ndipo chichitikenso pasanathe masiku 150 kuchokera patsikuli. Ndipo kutsatira izi nyumba ya malamulo yagwirizana kuti chisankhochi chichitike pa 19 May 2020.
11
Atudzula ziwalo za mwamuna wake Pamene nkhanza zambiri zomwe zimachita zimakhakla zochokera kwa abambo kupita kwa amayi, Loveness Nakayuni wa mmudzi mwa Chapyoka, T/A Mwaulambia mboma la Chitipa, masiku apitawa adali mchitolokosi pomuganizira kuti adafinya mwamuna wake kumalo obisika mpaka kutudzula ziwalo. Mneneri wa polisi mchigawo cha kumpoto Maurice Chapola adatsimikiza za nkhaniyi pouza Msangulutso kuti mayiyo adali mmanja mwawo kaamba kovulaza mwamuna wake, Winis Kita, wa zaka 46, atamugwira kumoyo chifukwa akuti adaphwanya lonjezo logona kunyumba kwake. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Iye adati Kita, yemwe ndi wamitala, adanyamuka kupita kukamwa mowa komwe adabwerako madzulo. Iye adafikira kunyumba kwa mkazi wake woyamba, Nakayuni, koma sadakhalitse ndipo adapita kunyumba ya mkazi wake wamngono. Izi zidamuwawa Nakayuni, yemwe adamulondola mwamunayo kunyumba kwa mkazi wake wamngonoyo. Atafika adapeza mwamunayo atakhala pakhonde akusuta fodya. Nakayuni adangombwandira malo obisika a mwamuna wakeyo nkufinya mpaka kutudzula, adafotokoza Chapola. Iye adati Kita adamutengera kuchipatala cha boma komwe adalandira thandizo lobwezeretsa ziwalozo zake mchimake. Pano akuti akupezako bwino ndipo akuchita kuyendera kukalandira mankhwala kuchipatala. Funso nkumati kodi banja lilipobe apa? Tidalephera kuyankhula ndi Kita, koma wapolisi wa zofufuzafufuza, teketivu Yatamu Kasambara, adauza Msangulutso kuti mkuluyu adakatseketsa mlandu kupolisiko ponena kuti zidali zambanja ndipo mkazi wake pano ali kunyumba ati azikalera ana. Ku Chitipa komweko, mayi wina, Mawazo Nzunga, akumuganizira kuti wapha mlamu wake atamumenya ndi mpini wa khasu pamutu atalephera kumvetsetsana pankhani ya chakudya. Chapola adauza Msangulutso kuti wophedwayo, Willard Mwilenga, adapita komwa mowa ndipo pochoka kumowako adaganiza zokapempha chakudya kunyumba ya mbale wake komwe adauzidwa kuti chakudya chake kulibe. Yankho la mlamu wakeyo silidamusangalatse ndipo kaamba ka kuledzera adayamba kummenya. Nzunga pobwezera adatenga mpini wa khasu ndipo adamugogoda nawo pamutu nkumukomola nawo, adafotokoza Chapola. Mwilenga adathamangira naye kuchitapatala cha Kameme koma ataona kuti zawakulira adamutumiza kuchipatala chachikulu ku Chitipa komwe adakafera. Chapola adati Nzunga ali pa rimandi pandende ya Chitipa kudikira kuyankha mlandu wa kupha munthu. Pothirapo ndemanga pankhani za nkhanza, wapampando wa bungwe la NGO Gender Coordination Network, Emma Kaliya, wati nkhani kuti itengedwe kuti ndi ya nkhaza kwa amayi kapena abambo zimakhala bwino kuyangana chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga. Mboma la Chitipa amuna ndi azikazi awo ali ndi kachisimo kokamwa mowa ku chilabu limodzi, makamaka madera a kwa Kameme ndi Mwaulambia. Tikuyesetsa kuthana ndi mchitidwe womwa mowa ku chilabu chifukwa tikukhulupirira kuti umakolezera nkhaza pakati pa amayi ndi abambo, adatero Kaliya.
15
Ndidamuona koyamba mu Shoprite Kwangotsala mwezi umodzi kuti anthu adzathyole dansi paphwando la ukwati wa Evance Mwale ndi Tiwonge Nundwe pa 4 May. Evance amagwira ntchito ku Sinodi ya CCAP ya Livingstonia pomwe bwenzi lakelo ndi muulutsi pa wailesi ya Voice of Livingstonia. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Awiriwa akhala pa ubwenzi kwa zaka zitatu. Malinga ndi Mwale, adamuona koyamba Nundwe mu Shoprite ku Mzuzu, ndipo adamusangalatsa. Tidakumana koyamba mchaka cha 2015 mu Shoprite ndipo adandipatsa chidwi mpaka ndidayamba kumufufuza ndithu kuti ndimudziwe bwino lomwe monga kwawo komanso kudziwa zomwe amachita, adalongosola Mwale. Ndipo iye adati anthu akufuna kwabwino adamuuza zonse za namwaliyu. Komatu Mwale adali ndi mwayi chifukwa mchaka chomwecho adapeza danga lokagwira ntchito kuofesi ya Nundwe komwe sadachitenso za bo! bo!bo! koma kuyamba kucheza ndi mtsikanayo. Ndipo pofika chaka cha 2016, ubwenzi wa ponda-apa-nane-ndipondepo udayambika pakati pa awiriwa. Ndidamufunsira ndine chifukwa adalibe nane chidwi olo pangono kuti nkukhala nane paubwenzi wokathera mbanja. Zidanditengera miyezi isanu ndi umodzi kuti andipatse danga lokhala naye pa ubwenzi, adalongosola Mwale. Komatu monga zikhalira, ubwenzi uliwonse umakhala ndi zokhoma zake ndipo nawo awiriwa akumana nazo zokhoma zofuna kuwalekanitsa, koma Chauta waikapo dzanja kuti amange banja. Pomwe Mwale adamutsira diso Nundwe koyamba mu Shoprite, namwaliyo adamuona koyamba Mwale pomwe adakayamba kuphunzira ntchito kusinodiyi. Kumayambiliro timacheza monga munthu ndi mnzake, koma sindidaganizeko zoti awirife nkukhala paubwenzi, koma ndi nthawi, tidayamba kucheza kwambiri mpaka anthu kumaona ngati tili paubwenzi pa nthawiyo, pomwe sizidali chomwechi, adalongosola Nundwe. Iye adati chikondi cha awiriwa chidayambira pomwe ankapitira limodzi kokadya nkhomaliro mmalo odyera mumzinda wa Mzuzu.
15
Kukokana pa za amayi ovina Jameson: Mzimayi abise thupi Zusamvana komwe kudabuka pa zakayendetsedwe ka bungwe la Asilamu la Muslim Association of Malawi (MAM) kwayamba kufalikira mmaboma ambiri tsopano. Magulu a anthu osiyanasiyana omwe akumadzitcha kuti ndi Asilamu okhudzidwa ayamba kulankhulapo pankhani yofuna kuchotsa wapampando wa bungweli, Idrisa Muhammad, yemwe akuti akuphwanya ngodya za chiphunzitso cha chipembedzochi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Koma Muhammad watsutsa za nkhaniyi ndipo wati sakugwedezeka chifukwa palibe munthu kapena bungwe lomwe lingamuchotse pampandowo. Iye wati akuganiza kuti magulu omwe akuchita izi akutumidwa ndi akuluakulu ena mchipembedzochi omwe sakumufunira zabwino ndipo walonjeza kuti sagonjera anthu oterewa. Ndikudziwa kuti alipo ena ake omwe akuwatuma kuti azichita zimenezi koma saphulapo kanthu chifukwa ngakhale atachita bwanji palibe yemwe ali ndi mphamvu zondichotsa pampando komanso sindingalole kutula pansi udindo wotsogolera chipembedzochi, watero Muhammad. Magulu omwe akulimbikitsa kuti Muhammad atule pansi udindo wake akuti mkuluyu walephera kugwiritsa chiphunzitso cha Chisilamu polola amayi achipembedzochi kuvina pamisonkhano ya ndale ndi kugwiritsa ntchito nyimbo za Chisilamu zimene angozisintha potamanda andale. Limodzi mwa magulu omwe sakukondwa ndi mtsogoleriyu ndi bungwe loona kuti zinthu mChisilamu zikuyenda mwachilungamo la Muslim Commission on Social Justice. Mtsogoleri wa bungweli Abdul-Aziz Shouaib Jameson wati amayi a Chisilamu saloledwa kulankhula kapena kuvina pamalo omwe pali abambo. Jameson wati amayiwa ndi ololedwa kutenga nawo mbali pandale, koma osati kudzera mchipembedzo. Chiphunzitso chathu chimanena kuti mzimayi abise thupi lake komanso asalankhule pomwe pali abambo pokhapokha ngati ali awiri ndi mwamuna wake, watero Jameson. Kuyambira pomwe nkhaniyi idaphulika sabata zitatu zapitazo mumzinda wa Blantyre pomwe gulu lina limafuna kukatseka ofesi ya Muhammad, gulu lina lidachititsa msonkhano wa atolankhani mumzinda wa Lilongwe pankhani yomweyi. Lachisanu lapita gulu lina mboma la Salima lidachita zionetsero zoti sakusagwirizana ndi wapampando wa bungweli ndipo lidakapereka kalata kwa bwanamkubwa wa bomalo chosonyeza kusakondwa ndo mtsogoleriyo.
11
Papa Wati Akhristu Aphunzire Kukonda Anzawo Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wadzudzula khalidwe lodzikonda pakati pa anthu. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa walankhula izi lachiwiri pomwe amakumana ndi ana omwe akuchita masewero osiyanasiyana komanso mapemphero ku likulu la mpingowu ku Vatican. Iye wauza anawa kuti moyo umakoma ngati munthu ali ndi abwenzi ndipo ndi kofunika kuti iwo akhazikitse ma ubwenzi abwino ndi anzawo Atatha kulankhula kwa anawa, Papayu anachezanso ndi omwe akuyanganira anawa komanso kuthandizira pa zina ndi zina asanabwerere kunyumba yake yomwe amakhala ya Casa Santa Marta kapena kuti Nyumba ya Marita Woyera. Zochitikachitika za anawa zinayamba kumayambiriro a mwezi uno ndipo pali masewero osiyana-siyana, kuphunzira zina nzina komanso kuchita mapemphero. Ena mwa masewero omwe akuchitika ndi masewero a mpira wa miyendo (football), tennis, basketball, kusambira (swimming) pongotchula ochepa. Zonse zikuchitika motsata ndondomeko zoyikika pofuna kupewa nthenda ya Covid 19. Anawa omwe alipo pafupi 100 ndipo a zaka zoyambira zisanu (5) mpaka zaka khumi ndi zinayi (14) ndi ana a anthu omwe amagwira ntchito zosiyana-siyana ku Vatican.
14
Awanjata Kaamba Kobera Agent wa Mpamba Apolisi mboma la Chikwawa amanga amuna awiri kaamba kowaganizira kuti apalamula mualandu wakuba ndalama mu phone kudzera mu njira ya mpamba. Malinga ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani mbomalo Sergeant Dickson Matemba amunawa ndi Yamikani Mukhoya wazaka 29 komanso James Mbewe wazaka 21 zakubadwa. <noscript><img class="alignnone size-full wp-image-10387" src="http://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2020/01/mpamba-agent.jpg" alt="" width="183" height="275" /><noscript><img class="alignnone size-full wp-image-10387" src="http://www.radiomaria.mw/wp-content/uploads/2020/01/mpamba-agent.jpg" alt="" width="183" height="275" /> Amunawa anapalamula mulanduwu lachitatu pa 15 January 2020 pansika wa pa Dyeratu mbomalo pomwe ananamiza wothandiza anthu potumiza ndalama (Agent) kuti atumize ndalama kunambala ina yomwe amati ndi ya Mayi awo, pomwe anatumiza ndalamayi amunawa anathawa pamalopa atapereka jumbo ya mtundu wa black yomwe munali mapepala okhaokha malo mwa ndalama. Agent-yu ataona kuti mupepalali mulibe ndalama anapereka uthenga pansikawu woti aliyense awone muthu akutenga ndalama kumpamba zokwana K70, 000 amudziwitse agentiyu. Patangotha kanthawi pangono ananva zoti amunawa akutenga ndalamayi pamalo ena pafupi ndi nsikawu ndipo pomwepo anadziwitsa apolisi omwe anabwera ndikugwira amunawa. Amunawa akuyembekezeka kukaonekera kubwalo la milandu ndi kukayankha mlandu wakuba.
7
Obwereza MSCE adzionere njira Unduna wa zamaphunziro wati siungachite kulembetsa mayeso apadera ophunzira 72 542 omwe adalakwa mayeso a Malawi School Certificate of Education (MSCE) a 2018 monga momwe makolo ndi anawo amalingalirira. Makolo ena ndi ena mwa ana omwe adalephera mayesowo adauza Tamvani kuti zikadathandiza ana olephera akadalemba mayeso awoawo ogwirizana ndi silabasi yakale yomwe adaphunzira. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chide: Sizikusiyana kwambiri Koma mneneri wa undunawu Lindiwe Chide wati ophunzira onse adzalemba mayeso a silabasi yatsopano ndipo kwa omwe sadaphunzire nawo silabasiyi adziwiretu chochita kuti zidzawayendere. Palibe kusintha kwakukulu pakati pa silabasi yakale ndi yatsopano ndiye palibe chifukwa cholembetsera mayeso osiyana. Yemwe akuona kuti pali zina zomwe ali mmbuyo, akuyenera kupeza njira yoti azidziwe, watero Chide. Iye wati aphunzitsi ndi wokonzeka kusula ana onse obwereza ndi omwe adzalembe mayeso koyamba kuti adzakhonze koma mkulu wa mabungwe omwe siaboma pa za maphunziro Benedicto Kondowe watsutsa mfundoyi. Choyamba, aphunzitsi ambiri sadaphunzitsidwe za kaphunzitsidwe ka silabasi yatsopano komanso alibe mabukhu owatsogolera pophunzitsa. Kachiwiri, silabasi yatsopano ndiyodzadza ndi za sayansi zomwe ambiri obwereza sadaphunzirepo, watero Kondowe. Iye wati ophunzira ambiri obwereza ndi omwe akudzalemba mayeso koyamba adzakukuta mano mmayeso chifukwa adzakhala asadakonzekere mokwanira potengera momwe silabasi yatsopano idakhazikitsidwira. Mukakumbuka, mabukhu ambiri adachedwa kubwera, ndi nkhani ya sayansiyi, kumafunika zipangizo ngati malabotale omwe msukulu zambiri makamaka ma CDSS mulibe. Ndiye ngati akudetsa nkhawa mwana yemwe adaphunzirako zithuzo pangono, kuli bwanji yemwe sadaphunzirepo kalikonse, watelo Kondowe. Makolo ndi ana omwe alankhula ndi Tamvani ati akadakonda pakadakhala mayeso apadera ochokera mu silabasi yakale oti ana omwe akubwereza adzalembe kenako nkumapanga ndondomeko yophatikiza ndi ophunzira a silabasi yatsopano. Jennifer Ngwira wa ku Area 25 yemwe mwana wake adalakwa mayeso a MSCE adati kukakamiza anawo kulemba mayeso a silabasi yatsopano nkuwapha chifukwa palibe chomwe angadzaphulepo. Ngati mwana adalakwa zinthu zomwe adaphunzira, angadzakhonze bwanji zomwe sadaphunzirepo nkomwe? Uku ndiye kufuna kupha tsogolo la ana, adatero Ngwira. Mmodzi mwa ana omwe akuyembekezera kubwereza mayeso a MSCE ndipo sadafune kutchulidwa dzina adati sakuona tsogolo lililose mundondomeko yomwe undunawu wakonza. Poyamba tinkamva zoti tidzabwerera Fomu 1 zomwe tidakonzekera kale kutsutsa akadzalengeza tsono apa akuti tilemba silabasi yatsopano, si chimodzimodzi nkubwereza? adatero iye. Mwa ana 197 286 omwe adalemba mayeso a MSCE a 2018, ana 124 745 ndiwo adakhonza kutanthauza kuti 72, 542 adalakwa ndipo akuyenera kubwereza ngati ali ndi chidwi chopita patsogolo ndi maphunziro.
3
Chimanga chikololedwa chochepaUnduna Kauniuni woyamba wa zokolola wasonyeza kuti chaka chino Amalawi akolola chimanga chocheperako kusiyana ndi chaka chatha, chikalata chimene unduna wa malimidwe watulutsa chatero. Chaka chilichonse undunawu umachita kauniuni katatu pa mbewu, ziweto ndi nsomba pofuna kuunikira kuti zokolola zikhala zotani. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Kauniuni woyambayo wasonyeza kuti chaka chino mlingo wa chimanga utsika kuchoka pa matani 2 776 277 chaka chatha kufika pa 2 719 425, ndipo izi zikutanthauza kuti pa makilogalamu 100 alionse omwe tidapeza chaka chatha, chaka chino pazichoka makilogalamu awiri. Kauniyu wapezanso kuti fodya wa chaka chino achuluka kuchoka pa makilogalamu 192 967 541 chaka chatha kufika pa makilogalamu 211 083 000 chaka chino pomwe thonje atsika ndi makilogalamu 43.2 pa makilogalamu 100 alionse omwe adakololedwa chaka chatha. Undunawu wati mpunga uchuluka ndi makilogalamu 1.4 pa makilogalamu 100 omwe adakololedwa chaka chatha pomwe mtedza uchuluka ndi makilogalamu 4.5, nyemba 5.2 ndipo nandolo 3.1 pa makilogalamu 100 aliwonse omwe adakololedwa chaka chatha. Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi wa Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Tamani Mvula Nkhono adati kauniuni wa mtunduwu ndiwofunika chifukwa umapereka chithunzithunzi cha kakololedwe. Iye adati undunawu wachita bwino kutulutsa zotsatira zakauniuni woyambayu koma lipitirize kuunikanso kawiri kamene katsala.
18
Ampingo avula gule zigoba Madzi achita katondo kwa Kansonga mdera la mfumu Chilowoko, mboma la Ntchisi komwe Akhristu a mpingo wa CCAP wa Biwi adavula zigoba za gule wamkulu yemwe adakasononeza msonkhano wawo wachitsitsimutso. Sabata yapitayi, Akhristu a mpingo wa Kanjiwa adali ndi msonkhano wachitsitsimutso pampingo wa Biwi. Msonkhanowo udatenga masiku atatu, kuyambira Lachisanu kufikira Lamulungu. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Anthu ena amayerekeza gulewamkulu akafuna kuchita chiwembu Malinga ndi omwe atitsina khutu omwe amachita malonda pamsikawo, ulaliki umatsindika kwambiri za gule wamkulu zomwe sizidasangalatse akuluakulu a kumzinda. Ndipo pofika Lamulungu gule wokwana 7 adatulukira pamalo a chitsitsimutsowo kuti akasokoneze, koma Akhristuwo adagwirapo zirombo ziwiri ndi kuzivula zigoba ndipo zirombo zinazo, zitaona izi zidathawira kudambwe. Polankhulapo, Mfumu Chilowoko ya mbomalo yati ikufufuzabe za nkhaniyi kuti idziwe ngati mizimuyo idawedzedwa ndi mfumu ya mzinda. Nthawi zina anthu ena amangoyeserera gule wamkulu ndipo awa ndi omwe amangotuluka paokha opanda mfumu ya mzinda chifukwa kuti titsimikize kuti uyu adalidi gule, pafunika chitsimikizo chochoka kwa mfumuyi, adatero Chilowoko. Iye adatinso pali chikaiko choti guleyo adali wovomerezeka chifukwa mfumu yaikulu ya Achewa Kalonga Gawa Undi adaletsa kuwedza gule malinga ndi mlili wa Covid-19. Koma zikapezeka kuti nzoona kuti guleyu adali wa mzinda ndipo akapezeka wolakwa, timalipiritsa mbuzi kapena kuposera apo chifukwa ife ngati Achewa timafuna mabungwe onse azikhala mwamtendere opanda chiopsezo, adatero Chilowoko. Malinga ndi iye, nkhani yomwe wamvetsedwa ndi yoti nawo a mpingo pachitsitsimutso chawo amangokamba za gule wamkulu zomwe sizidakomere agulewo. Pakadalipano tingodikira kuti apolisi atiuze pomwe nkhaniyi ili chifukwa ndauzidwa kuti idakafika mmanja mwawo, monga mukudziwa anthu salowa mabwalo awiri, adalongosola Chilowoko. Koma iye adanenetsa kuti apolisiwo akathana nazo za mzinda alekere eni chikhalidwe omwe ndi mafumu omwe amakawedza gule kumanda. Koma mneneri wa polisi mboma la Ntchisi, Richard Kaponda adati nkhaniyo siyidafike kupolisi chifukwa mbali zonse zokhudzidwa zidangokambirana pazokha. Nawo a bungwe losungitsa chikhalidwe la Chewa Heritage Foundation (Chefo) adati atumiza ku maloko mkulu woyanganira nkhani za mafumu komanso chikhalidwe kuti akafufuze chidatsitsa dzaye kuti njovu itchoke mnyanga. Wapampando wa bungwelo George Kanyama Phiri adati mpungwepungwe pakati pa mpingo ndi a gulewamkulu wakhala ukusowetsa mtendere kwa kanthawi tsopano.
1
Katelele back in the studio Sensational musician Katelele Chingoma is back in the studios where he is recording a new album that is expected to hit the market in May. The musician, fondly known for composing reggae and Sena jive songs, has recorded nine of 10 songs to be roped into the album, Zanga Zatheka. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Her touch on murals Katelele: The songs have been recorded at a number of studios As usual, the artist has used his brother Petros, a versatile producer, on the consoles. I have used my brother again this time because he understands the type of music my fans like. The songs have been recorded at a number of studios in Lilongwe and South Africa and this will bring about a mixed blend. I deliberately did this to make sure that I come up with the best quality music that will soothe my fans, said the Blantyre-based musician. The musician, famed for the track Asowe Mlamu, said his trip to South Africa late last year has helped him to tap more skills from SA musicians. I went there and conducted live shows with Thomas Chibade and Moses Makawa. I utilised my trip to tap more talent from artists such as DJ Cleo, with whom I shared the stage. I hope the fusion of talent will help my album sell well locally and internationally, said the musician. Katelele released his album Ndili Nawo Mwayi in 2011 and says he has taken time preparing for the new album. I feel bad if fans dont welcome my music. That is why I dont rush in releasing albums. I want to stand to quality; hence, my four-year silence. I hope the album will sell well considering that I have taken a lot of time to prepare, said the musician. Katelele says he will work with reggae outfit Black Missionaries to promote the album once it gets on the market.
0
Malawi ipunthanandi Zimbabwe lero Mpikisano wa matimu a mu Africa wa Africa Cup of Nations (Afcon) wayamba lero pamene matimu osiyanasiyana akuthethetsana. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Matimu a mgulu L, momwe muli Malawi, Zimbabwe, Swaziland ndi Guinea, ayambanso kutuwitsana lero pamene Malawi ikulandira Zimbabwe pa Kamuzu Stadium masanawa. Zimbabwe, yomwe ili panambala 119 mdziko lapansi pamomwe matimu akuchitira pamndandanda wa Fifa, yakumana ndi zokhoma zosowa ndalama ndipo izi zidachititsa kuti timuyi itulutse mochedwa maina a osewera amene akubwera ku Malawi kuno. Lachiwiri usiku, kochi wa timuyi, Kalisto Pasuwa, adatulutsa mndandanda wa osewera 19 kuti abwere kudzazimitsa Flames. Malinga ndi nyuzipepala ya TheHerald ya ku Zimbabweko, timuyi idayamba zokonzekera zake Lachitatu koma ndalama zoti igwiritsire ntchito kubwera ku Malawi zidali zisadapezeke. Koma kumbali ya Malawi, zonse zili mchimake, malinga ndi kochi Young Chimodzi. Tidakasewera ndi Egypt, ngakhale tidagonja [2-1] komabe zatithandiza kuti tione anyamata amene tingawagwiritsire ntchito pamene tikumane ndi Zimbabwe. Tingathe kunena kuti chilichonse chatheka, adatero Chimodzi, amene timu yake yakhala mkampu kwa mwezi tsopano. Timuyi ili ndi osewera onse amene adakasewera nawo ku South Africa mumpikisano wa Cosafa komanso akatswiri ena amene amasewera mmaiko ena. Ku Egypt, John Banda ndiye adagoletsa chigoli cha Malawi. Lero maso akhale pa katswiriyu komanso Atusaye Nyondo ndi Esau Kanyenda kutsogolo kwa Malawi. Zimbabwe yaitana Nyasha Mushekwi amene amasewera ku Sweden. Mnyamatayu watchuka ndi kumwetsa zigoli kumeneko ndipo masanawa Flames iyenera kuchenjera naye ameneyu. Masewero omaliza pakati pa matimuwa amene adachitikiranso pabwalo lomweli pa 5 March chaka chatha, Malawi idagonja 1-4 ndipo Atusaye ndiye adachinya chigoli cha Malawi.
16
Malawi sisewera ndi Uganda Chiyembekezo chidalipo kuti Malawi iswana ndi Uganda kuti ikonzekere masewero a World Cup pa 7 October pamene ikunthane ndi Tanzania. Koma mlembi wa bungwe loyendetsa masewero mdziko muno la FAM, Suzgo Nyirenda, walengeza kuti izi sizithekanso chifukwa osewera a Flames amene amasewera mpira wawo kunja kwa dziko lino sakwanitsa kudzasewera masewerowo chifukwa makalabu awo akhala otangwanika. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Malinga ndi Nyirenda, Flames idzanyamuka mdziko muno ulendo ku Tanzania pa 4 October osachita zokonzekera ndi timu iliyonse. Koma kochi wa timuyi, Ernest Mtawali, pofuna kupima mphamvu za anyamata ake, adakonza masewero ndi FISD Wizards Lachitatu ndipo Flames idapambana 4-0. Flames idzakumananso ndi Tanzania pamasewero achibwereza pa 11 October pa Kamuzu Stadium mumzinda wa Blantyre.
16
George Nyirenda: Za Flames waiwalako Zambiri zakhala zikulankhulidwa za George Nyirenda amene akusewera mu Caps United mdziko la Zimbabwe kuti atengedwe ku Flames. Iye mwini wakhalanso akufunitsitsa ataitanidwa koma makochi a Flames amangomupatsa nkhongo. BOBBY KABANGO adacheza naye komanso pa za mphekesera yomwe yamveka kuti akubwera kudzasewerera Bullets: Nyirenda: Ndingasewere Bullets basi Moyo uli bwanji ku Caps? Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Zonse tayale madala koma nditangofika kumene ndiye zidatenga nthawi kuti ndizolowere momwe mpira wawo amasewerera. Kodi udapita liti kumeneko? Mudali mu May chaka chatha. Caps idandipeza pamene ndidali kukampu ya Flames ndipo ndidabwera kuno ngakhale padali kusamvana ndi Bullets, timu yomwe ndimasewerera kumudziko, malinga ndi utsogoleri womwe udalipo panthawiyo. Tikumva kuti akuchotsa kuti usamasewerenso kumbuyo ndipo wabwera pakati. Chachitika nchiyani? Zoona, panopa tili ndi kochi wina wochokera ku England ndiye wabwera ndi nzeru zake. Ndikusewera bwino moti ndachinya kale zigoli ziwiri. Osati chifukwa umadzibayanso kumbuyoko? Hahaha! Ayi si choncho, koma adangondikhulupirira kuti ndingachite zakupsa kusiyana ndi ena amene amasewera pakatiwo. Pali mphekesera ku Malawi kuno kuti ukubwera kudzasewera mtimu yako yakale, kodi izi ndi zoona? Mphekesera chabe, ine ndili kuno kaye ndipo zinthu zikuyendanso bwino. Koma nditakhala kuti ndabwera ku Malawiko ndiyedi palibe timu yomwe ndingasewere koma Bullets basi. Ndidzafa ndikusewerera timuyi, ndi yamagazi. Wakhala ukulankhulapo za kusiyidwa kwako ku Flames ndipo anthu amati ukuyenera kutengedwa koma sizili choncho. Kodi vuto lili pati? Sindikudziwa kuti vuto nchiyani koma ine ndilibe vuto kusewerera timuyi. Koma dziwani kuti za Flames panopa si mbali yanganso [kwabwino] ndizingopanga za kalabu basi koma za Flames panopa ayi. Kodi wakhumudwa? Ayi, koma ndangosankha kuti ndizichita za kalabu basi. Pomaliza, tikumudziwa George kuti ndi rasta wodya zamasamba, kumeneko mwasintha? Kulikonse Rasta ndi Rasta ndipo anandipatsa dzina kuti Jah Love chifukwa cholimba mtima ndi za Chirasta.
16
Anatchezera Amandikakamirabe Agogo, Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine mtsikana wa zaka 19 zakubadwa, vuto langa ndi lakuti pali mnyamata wina wake amene amandifuna koma ineyo sindimamufuna olo pangono. Iye samafuna kuti angondisiya moti pano miyezi iatatu yakwana akundifunabe. Nthawi zina ndimayesetsa kuti ndimuonetse nkhope yosangalala koma mtima wanga umakana. Ndiye nditani poti ine ndili naye kale amene ndimamukonda ndi mtima wanga wonse? Chonde ndithandizeni. Zikomo mtsikana, Ndikuthokoze kwambiri chifukwa cha maganizo ako abwino. Ndithudi akadakhalapo atsikana ambiri amaganizo ngati akowa bwenzi zinthu zikoma. Atsikana ambiri masiku ano amakonda kukhala ndi zibwenzi zambirimbiri ati kuti pamapeto adzasankhepo mmodzi. Chimenecho si chikondi ndipo mapeto ake ambiri amasokonezeka, mwinanso kutenga pathupi pa mnyamata amene samamukonda. Apa iwe waonetsa kale kuti ndiwe wokhwima mmaganizo ndipo ndikufuna kuti ndikulimbikitse kuti chikondi sakakamiza. Ngati uli kale ndi mnyamata amene umamukonda ndi mtima wako wonse palinso chifukwa chanji choti uzitaya nthawi ndi wina amene ulibe naye chidwi? Komabe nthawi zina chimachitika nchoti amene umamukonda kwambiri iye alibe chikondi, angofuna kukuseweretsa ndi kukometsa mawu a pakamwa ndipo amene sukumukonda ndi amene ali ndi chikondi chozama pa iwe. Ndiye apa chimene ungachite uyambe waona kuti bwenzi lakolo ndi munthu wotani? Ndi wamakhalaidwe otani? Ndi waulemu kapena ayi; ndi yo kapena wodzilemekeza; cholinga chanu ndi chiyani pa ubwenzi wanu? Chimodzimodzi amene ukuti akukukakamira chibwenziyo, kodi ndi munthu wotani? Cholinga chake ndi chiyani? Ndi wakhalidwe kapena mvundulamadzi chabe? Ukalingalira zonsezo bwinobwino mpamene ungasankhe chochita, chifukwatu nthawi zina umatha kukakamira mtunda wopanda madzi nkusiya munthu wachikondi weniweni. Gogo wanga, Ndithandizeni. Ine ndinapeza bwenzi chaka cha 2010 ndipo adapita ku Joni chaka chomwecho. Foni amaimba, inenso ndimaimba koma amangoti ndibwera pompanopompano koma kuli zii! Amandiuza zolimbitsa mtima ndipo ndili pano ndakana amuna ambiri mpakana ena kufika pomandinena kuti ndine chikwangwani. Agogo, ndizidikirabe? AK, Lilongwe.
12
Anatchezera Sakuthandiza mwana Agogo, Ndine mtsikana wa zaka 19 ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Ndidali pabanja koma litatha bambowo samatumiza chithandizo olo sopo. Ndiye nditani poti mwanayu ndimavutika naye ndekha? Pepa mtsikana, Ndi zimene ndakhala ndikulangiza atsikana nthawi zonse kuti limbikirani sukulu mudakali anthete, osati kuthamangira kukwatiwa! Tikamanena kuti si bwino kuthamangira banja timadziwa kuti nthawi zambiri zotsatira zake zimakhala ngati zimene wakumana nazo iwezi. Tsono nkovuta kukuthandiza zenizeni chifukwa sukulongosola kuti ukwati wanu udali wotani-wongolowana, wachinkhoswe kapena mudadalitsa kutchalitchi? Nanga zifukwa zomwe banja lako lidathera nzotani? Ukwatiwo udathera kuti-kukhoti kapena basi mwamuna adangoti zipita kwanu? Ngati ukwati wanu udali ndi ankhoswe, iwo akutipo chiyani pa kutha kwa ukwati wanu? Banja lenileni silimangotha lero ndi lero popanda zifukwa zenizeni; banja si masanje. Ndiye mmene zikuonekera inu mudangotenganapo popanda ndondomeko yeniyeni ndipo mwamuna adalola zokukwatira pothawa milandu atakupatsa pathupi, si choncho? Ndiye poti amati madzi akatayika saoleka, chomwe ungachite nchoti nkhaniyi upite nayo kwa ankhoswe kapena kubwalo la milandu kuti akakuthandize chifukwa bamboo wa mwana ali ndi udindo woti azithandiza mwana wake ngakhale kuti banja lanu latha. Mwana asavutike chifukwa cha kusemphana Chichewa kwa inu makolo. Kodi, sukulu udalekeza mukalasi yanji? Chonde, ngati pali mwayi woti nkubwerera kusukulu, chita zomwezo chifukwa udakali mwana wamngono. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndikhulupirire? Anatchereza, Ndidali ndi chibwenzi chomwe tinkakondana kwambiri ndipo tinkamvanadi koma titakhala zaka ziwiri osaonana kaamba ka zovuta zina popeza aliyense ankakhala ndi makolo ake. Koma panopa adakwatiwa ndipo ali ndi mwana mmodzi. Titakumana miyezi yammbuyomu adandiuza kuti amandikondabe. Kodi ndikhulupirire? Kapena ndipange bwanji? Ndithandizeni Anathereza. Godfrey Richard Sindima, Thyolo Okondeka a Sindima, Tisatayepo nthawi apa. Si mwati adakwatiwa ameneyo ndipo ali ndi mwana mmodzi? Ameneyo si wanunso ayi, ndi mwini wake! Akadakhala kuti amakukondani akadakudikirani, osati kukwatiwa ndi munthu wina, ayi. Kodi mukundiuza kuti kuti kumene adakwatiwako adachita kumukakamiza? Padali chikondi pakati pa mwamunayo ndi mkazi yemwe mukuti adali chibwenzi chanuyo. Tsono inu musapusitsidwe kuti akukukondanibe pamene ali pabanja ndi mwamuna wina. Apa ndiye kuti dzanja silidalembe kuti iye adzakhala nthiti yanu. Funani wina, achimwene, ameneyo ngodanitsa. Mkazi wapabanja amene amadyeranso maso amuna ena timati ndi wachimasomaso ameneyo ndipo si wofunika kutaya naye nthawi. Ndikhulupirira mwamvetsa. Amamumenya Zikomo Anatchereza, Ineyo ndili ndi chibwenzi ndipo timakondana kwambiri koma makolo ake amamumenya chifukwa cha ine. Ndiyeno ndikamuuza kuti chithe amakana, koma ineyo ndimaopa kuti adzamuvulaza. Nditani pamenepa? Ndimusiye? Pati bii pali munga! Makolo anzeru sangamamenye mwana wawo wamkazi popanda chifukwa. Zimene ukunena kuti amamumenya chifukwa ali mchikondi ndi iwe si zoona ayi, koma chilipo chifukwa chomwe amamumenyera. Mwina mwana wawoyo adakali pasukulu ndipo sakufuna kuti asokoneze maphunziro chifukwa chochita zibwenzi ali pasukulu; mwina nkutheka sakuvomereza chibwenzi chanu kaamba ka zifukwa zina ndi zina. Vuto ndi loti sukufotokoza bwinobwino za cholinga cha chibwenzi chanucho, msinkhu wako ndi zina zotero. Ngati chibwenzi chanucho cholinga chake nchoti mudzakhale pabanja, iwe wachitapo chiyani kuonetsa kuti si zachibwana ayi? Iwe udamaliza sukulu ndipo uli pantchito kapena ayi? Pali chitomero kapena ayi? Mwina utandiyankha mafunso amenewa ndingathe kuona kuti ndikuthandize bwanji.
12
Ndidamuona koyamba mu Shoprite Kwangotsala sabata ziwiri zokha kuti anthu adzathyole dansi paphwando la ukwati wa Evance Mwale ndi Tiwonge Nundwe pa 4 May. Evance amagwira ntchito ku Sinodi ya CCAP ya Livingstonia pomwe bwenzi lakelo ndi muulutsi pa wailesi ya Voice of Livingstonia. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Awiriwa akhala pa ubwenzi kwa zaka zitatu. Chikondi cha Evans ndi Tiwonge chidazama kuntchito Malinga ndi Mwale, adamuona koyamba Nundwe mu Shoprite ku Mzuzu, ndipo adamusangalatsa. Tidakumana koyamba mchaka cha 2015 mu Shoprite ndipo adandipatsa chidwi mpaka ndidayamba kumufufuza ndithu kuti ndimudziwe bwino lomwe monga kwawo komanso kudziwa zomwe amachita, adalongosola Mwale. Ndipo iye adati anthu akufuna kwabwino adamuuza zonse za namwaliyu. Komatu Mwale adali ndi mwayi chifukwa mchaka chomwecho adapeza danga lokagwira ntchito kuofesi ya Nundwe komwe sadachitenso za bo! bo!bo! koma kuyamba kucheza ndi mtsikanayo. Ndipo pofika chaka cha 2016, ubwenzi wa ponda-apa-nane-ndipondepo udayambika pakati pa awiriwa. Ndidamufunsira ndine chifukwa adalibe nane chidwi olo pangono kuti nkukhala nane paubwenzi wokathera mbanja. Zidanditengera miyezi isanu ndi umodzi kuti andipatse danga lokhala naye pa ubwenzi, adalongosola Mwale. Komatu monga zikhalira, ubwenzi uliwonse umakhala ndi zokhoma zake ndipo nawo awiriwa akumana nazo zokhoma zofuna kuwalekanitsa, koma Chauta waikapo dzanja kuti amange banja. Pomwe Mwale adamutsira diso Nundwe koyamba mu Shoprite, namwaliyo adamuona koyamba Mwale pomwe adakayamba kuphunzira ntchito kusinodiyi. Kumayambiliro timacheza monga munthu ndi mnzake, koma sindidaganizeko zoti awirife nkukhala paubwenzi, koma ndi nthawi, tidayamba kucheza kwambiri mpaka anthu kumaona ngati tili paubwenzi pa nthawiyo, pomwe sizidali chomwechi, adalongosola Nundwe. Iye adati chikondi cha awiriwa chidayambira pomwe ankapitira limodzi kokadya nkhomaliro mmalo odyera mumzinda wa Mzuzu.
15
Dziko la Malawi Lapezeka Mmaiko 10 Amtendere mu Africa Dziko la Malawi lapezeka mu gulu la mayiko 10 a mtendere mmayiko a mu Africa. Nyanja ya Malawi-Chimodzi mwa zinthu zokopa alendo Malinga ndi kafulufuku amene bungwe lina lokhudzidwa ndi nkhani zochita kafukufuku mmaikowa linachita, ena mwa mayiko amene ali mguluri ndi monga a Equatorial Guinea, Tanzania, Namibia, Ghana, Sierra Leone, Zambia, Madagascar, Botswana komanso Mauritius. Malingana ndi kafukufukuyu, ambiri mwa maikowa akusonyezanso kuti amachita bwino pa nkhani zokopa alendo mchigawochi kamba ka mbiri yabwino yomwe ali nayo.
14
2019 Polisi Idaziona Mchaka changothachi cha 2019, nthambi ya chitetezo ya polisi idalibe mpata opumira chifukwa cha mpungwepungwe womwe udalipo ndikusukuluka kwa chikhulupiliro pakati pa apolisi ndi anthu. Ngakhale wogwirizira mpando wa mkulu wapolisi Duncan Mwapasa wavomereza izi muuthenga wake wotsanzikana ndi chaka cha 2019 chomwe Amalawi sadzayiwala mmbiri ya dziko lino. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mwapasa: Kudali mkokemkoke Mwapasa wati ngakhale nthambiyo yayesetsa mbali zina monga kuchepetsa ngozi za pamsewu ndi anthu omwalira pangozizo, nkhani yokhazikitsa bata ndi mtendere udali mtunda ovuta kukwera. Zonse zidayamba bwino mu January ife nkumati zili bwino koma atsogoleri awiri atangotsutsa zotsatira za chisankho cha mu May, 2019, kudali mkokemkoke ophwanya malamulo nkutengera zonse mmanja mwa anthu, adatero Mwapasa muuthenga wake womwe adaupereka pa 31 December 2019. Iye wati apolisi ambiri adavulazidwa ndi anthu ndipo ena mpaka adaphedwa chifukwa chakudzipeleka pantchito yawo ndi malingaliro oyipa aanthu omawona apolisi ngati zirombo zaboma zogwiritsa ntchito pofuna kuthana ndi anthu. Koma katswiri pandale Ernest Thindwa wati apolisi adadzipalira okha moto chifukwa cha momwe ankagwirira ntchito yawo mdzina loteteza anthu ndi chuma chawo. Iye adati kulephera kwa apolisi kudaonekera pomwe adakanika kukhazikitsa bata pakati pa anthu ochita zionetsero opanda zida zoopsa komanso mchitidwe wokondera pogwira ntchito. Zimachita kuonekeratu kuti a mbali yolamula akangokolana ndi anzawo, enawo ndiwo amalangidwa. Chonchi anthu nkumati chiyani? Nchifukwa chake ubale udasokonekera ndiye akupadziwa pomwe padalakwika tingopemphera kuti akonzepo mchaka chatsopanochi, adatero Thindwa. Mmodzi mwa akuluakulu a zamaufulu Timothy Mtambo watsutsa kuti Amalawi adali ndi mtopola mchaka cha 2019 ndipo wati Amalawiwo amafuna kuteteza ufulu wawo womwe boma pogwiritsa ntchito apolisi amafuna kupondereza. Zimenezo ndidakana ndipo ndidzakanabe. Amalawi alibe vuto koma boma pogwiritsa ntchito apolisi ndiwo adakolezera moto kuti dziko lidzadze utsi chonchija, adatero Mtambo. Mwa zowawa zina, Mwapasa adati apolisi ambiri adamenyedwa, nyumba zawo kutenthedwa komanso mawofesi ambiri a polisi adatenthedwa ndipo apolisi adasamuka mmalo ena momwe zinthu zidafika poyipitsitsa. Koma Mwapasa walonjeza kuti panyengo yomwe Amalawi akhale akudikirira chigamulo cha mlandu wa zisankho, nthawi yolengeza chigamulo ndi mmasiku otsatira, apolisi apereka chitetezo chokwanira. Nzachidziwikire kuti anthu mitima ili mmwamba ndipo chilichonse chikhoza kuchitika. Ife apolisi ndife okonzeka kuteteza anthu ndi katundu koma tikupempha atsogoleri ambali zonse zokhudzidwa pamlanduwo kuti mlandu uliwonse opambana amakhala mmodzi basi, adatero Mwapasa. Muuthenga wake wotsanzikana ndi 2019, Mwapasa adati polisi idachita bwino mbali zina monga kuchepetsa ngozi zapamsewu kuchoka pa 996 mu 2018 kufika pa 975 mu 2019. Pangozizo, iye wati chiwerengero cha anthu omwalira chidatsikanso kuchoka pa 1163 mu 2018 kufika pa 1141 mu 2019 ndipo adati zambiri mwangozizo zidachitika chifukwa chakusasamala kwa oyendetsa galimoto ndi ena ogwiritsa ntchito msewu.
11
Ambuye Msusa Alimbikitsa Chikondi Pakati pa Akhristu mu Nyengo ya Pasaka Akhristu a mpingo wakatolika mu arkidayosizi ya Blantyre awapempha kuti alimbikitse chikondi mu nyengo ino ya Pasaka. Arkiepiskopi wa arkidayosiziyi , Ambuye Thomas Luke Msusa, alankhula izi pambuyo pa misa ya chikondwelero cha Pasaka imene anatsogolera ku Limbe Cathedral mu arkidayosiziyi. Msusa: Tiwonjeze mapemphero Iwo atsindika ponena kuti maziko abwino a chikhristu agona mu chikondi, kotero kulimbikitsa izi ndi kumene kumakondweretsa Mulungu. Tiwonetse moyo wa chikhristu chathu pokondana, kugwirizana ndi kuthandiza ena amene ali ovutika. Tikuyenera tikhale anthu achifundo, anatero Ambuye Msusa. Mwazina Ambuye Msusa alimbitsa mtima akhristu kuti asawope nthenda ya COVID-19 koma alimbike mapemphero ponena kuti pameneYesu wagonjetsa imfa ndiye kuti agonjetsanso matendawa. Iwo apemphanso anthu kuti apitilire kutsatira malangizo omwe boma lapereka pa nkhani yokhudza nthendayi.
13
Kalembera wa mafoni aima Boma laimitsa kalembera wa lamya za mmanja yemwe nthambi yoyendetsa ntchito za mauthenga ya Malawi Communications Regulatory Authority (Macra) idakhazikitsa mwezi watha. Macra idalamula kuti aliyense yemwe ali ndi lamya ya mmanja alembetse nambala ya lamya yakeyo pasadafike pa 31 March 2018 apo biii nambalayo idzasiya kugwira ntchito. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Unduna wa zofalitsa nkhani wati boma laganiza zoimika kalemberayu potsatira maganizo a anthu omwe akhala akukhuthula nkhawa zosiyanasiyana zokhudza kalemberayu. Tikudziwa kuti kalemberayu ndi wofunika potsatira malamulo koma poti ili ndi boma lomva maganizo a anthu, tayamba taimitsa kaye kalemberayu mpaka tikonze zinthu zina, chidatero chikalata chochokera ku undunawu. Kuimika kwa ntchitoyi kwakwiyitsa mkulu wa bungwe loyimira ogula la Consumers Association of Malawi (Cama) Davis Kapito yemwe mmbuyomo adayamikira Macra kaamba kokhazikitsa ntchitoyi. Iye wati ganizoli ndi lolakwika chifukwa kalemberayu amatsatira lamulo lomwe lidakhazikitsidwa mNyumba ya Malamulo kotero kumuimika kumayenera kudzera ku nyumba yomweyo. Ngati padali nkhawa kaya mavuto amayenera kupititsa nkhawazo ndi mavutowo ku Nyumba ya Malamulo osati nduna kapena unduna kungodzuka mmawa nkuyimika kalembera ofunika ngati ameneyu, adatero Kapito. Nkhawa zambiri za anthu pa kalemberayu zidali mayendedwe kuchoka kumudzi kukafika komwe kuli malo olembetserakowo ndi nthawi polingalira kuti posachedwapa, anthu amaima pamizere italiitali kudikira kulembetsa zitupa za unzika. Kapito adati dziko la Malawi limakhalira mmbuyo pankhaniyi chifukwa maiko ena adayamba kale kuchita kalembera wamtunduwu. Mmaiko ena sungangogula khadi ya lamya pamsewu nkuyamba kugwiritsa ntchito osalowa mkaundula nchifukwa chake anthu amangogula khadi nkupangira zolakwika nkulitaya, adatero Kapito.
7
Chitukuko cha foni Ndati ndikuuzeni abale anzanga, mbale wina amene anatchona ku Jubeki ndipo anasungidwa ku Lindela kwa nthawi wafika pa Wenela. Chanzeru chimene wandibweretsera ndi foni yochonga. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Tsonotu lero nkhani si ya mtchona wamkulu Adona Hilida. Inde apa sindikambatu za kutha mphamvu kwa Kwacha chifukwa ngakhale Moya Pete alibe yankho lenileni! Sindinganene wamasiye wamkulu Shati Choyamba amene adathawa mkazi wake lero akutizunza ndi uthenga wakuti ndi wa masiye! Ndipo tili pankhani wa mkuluyu, ndidaona nyumba ina yozinga bwino msewu wa Fatima, tsono ndikudabwa kuti akukakamira mtauni bwanji? Sindinganene za Mpando Wamkulu chifukwa pano msana uja udapola ndipo wasiya zopita ndi mtsamiro kukhoti kukayankha zosolola ndi zina ndi zina. Abale, ndinganene chiyani za Lazalo Chatsika wa Male Chauvinist Pigs yemwe tsopano naye wayamba kuonetsa mawanga a gogo uja adandipeza nditavula polima kwathu kwa Kanduku ku Mwanza? Ngati simunamve, mfunseni Thursday Jumbo! Koma inu! Lero nkhani si ya Polisi Palibe, gulu limene likutha ngati makatani a China. Makatani ndi onse, koma pajatu belo siyinama! Nanga taonani Adona Hilida kutuma uja Ibula kuti achotse uyu wa chitaganya kenako Adona Hilidawo nkudzanena kuti ayi mkulu wa chitaganyayo asachotsedwe. Inde, sitikamba za Pitapo yemwe tsopano akusimba lokoma apoooo! Chifukwa sabata imeneyi ndakhala ndi kuunguza nawo pa Facebook ndati ndiyalule zina ndi zina zimene ndakhala ndikuona. Nkhani yaikulu ndi ya kuzimazima kwa magetsi! Abale inu, we are living in the dark ages ndipo bungwe loonetsetsa kuti mdima ukufikira aliyense pano pa Wenela likadakhala chakudya bwenzi ali manyumwa. Musandifunse kuti chipatso chimenechi nchiti chifukwa sindkuuzani. Kuzolowera zipwete eti? Tsono mmodzi mwa anthu amene anaponya nkhani yake pa buku la nkhope (kaya ndi nkhope ya buku, sindidziwa) adatambasula zomwe anakumana nazo chifukwa cha kuzima kwa magetsi. Mkazi wanga anandipeza ndi kucheza ndi mkazi woyendayenda. Anapita kunyumba kumene adakhutulira mafuta mpoto, nkuika pa cooker. Mkaziyo adayatsa cooker nkukagwira ntchito zina. Ntafika sanafunse kalikonse koma adaphula mafuta aja nkundikapiza. Samadziwa kuti nthawi amaika mafutawo pamoto, magetsi anazima ndipo mafuta sanawire. Zikomo Eeeeeeeishkom! Abale anzanga, ndikhulupirira madotolo a chipatala cha odwala misala aziyangana kaye zimene odwala awo akhala akulemba pomwe amayenda pamsewu ngati abwinobwino. Ndipo nditaunguza Gervazzio, wa pamalo aja timakonda pa Wenela, ndidapeza kuti ali mgulu lina lotchedwa Kupeza Mabanja ndi Zibwenzi Pa Wenela! Chodabwitsa nchakuti iyeyo ali pabanja! Kodi Facebook yaphweketsa chiwerewere chomwechi? Ndikumadabwanso kuti nkatsegula tsambali, akumandifunsa kuti What is on Your Mind! Akadziwa ndiye amafuna nditani? Nkhawa zanga si zotulira anthu osadziwa? Ndiye pali ena akuponya zithunzi zolaula pa Facebook. Akakhalakhala, umva akunena kuti wina wawalowera kutsamba lawo! Mukunamiza ndani? Ngakhale zandipeza mochedwa Abiti Patuma adandiuza kale kuti amene zithunzi zotere zikuoneka patsamba pawo ndiye kuti adatsegula zithunzi zotere patsamba la ena! Usawi, chichi? Kukamba za Abiti Patuma, sabata iyo adanditengera ku ukwati wina umene udali pamalo ena oyandikira pa Wenela. Kudali mwana wa munthu ku ukwati umenewo. Itafika nthawi yofupa akuchimuna, ndinadabwa aliyense ali pa foni yake. Nanenso ndidalowa nawo mgulumo, nkumaseweretsa foni yanga. Nkatere, kutola zithunzi za anthu ali kakaka ndi mafoni awo, popanda wofupa. Nkatero, ndaponya kale pa Facebook. Kungoponya kenako nkupanga like. Nthawi yomweyo nkudzaponya comment: Life is good#embarassed with lasanje! Akuchimunawo adapitiriza kuseweretsa mafoni awo, popanda wofupa olo mmodzi. Titabwerera kukakhala pansi ndidafunsa Abiti Patuma kuti akuchimuna kuumira kwanji kotere? Kungopita mbwalo kukavina mmalo mofupa! Anthu a nkhanza, satana ali bwino, ndidatero. Abiti Patuma adaseka ngati wakwatiwa kumene. Kikikiki! Tade mudzatsala. Anthuwatu akufupa kupyolera pa Mpamba, Airtel Money komanso achina Mo626 ndi njira zina zosamutsira ndalama pafoni, adanditsegula mmaso Abiti Patuma.
2
Sheikh Chabulika ayamikira Radio Maria Wolemba: Thokozani Chapola /uploads/2019/09/chabulika.jpg" alt="" width="293" height="165" /> Chabulika: Ndimakonda kumvera Radio Maria Mmodzi mwa atsogoleri a chipembedzo cha chisilamu mdziko muno Sheikh DINALA CHABULIKA wayamikira RADIO MARIA MALAWI kamba koulutsa nkhani zothandiza kulimbikitsa bata ndi mtendere. SHELK CHABULIKA yemwenso ndi mneneli wa bungwe la MUSLIM ASSOCIATION OF MALAWI (MAM) walankhula izi popereka uthenga wake wa mafuno abwino ku wailesi-yi imene LOWELUKA likudzali pa 28 SEPTEMBER 2019 ikhale ikuchita mwambo wokondwelera kuti yakwanitsa zaka 20 chifikireni mdziko muno. Sheikh CHABULIKA wati RADIO MARIA ndi wailesi imene ili ndi ukadaulo wabwino wa kaulutsidwe ka mawu mdziko muno. Ndimakonda kumvera Radio Maria chifukwa ndi wailesi imene imalimbikitsa bata ndi mtendere simatenga nawo mbali polimbikitsa ziwawa ngati momwe ma wailesi ena amachitira, anatero Sheikh Chabulika. Iwo apempha atolankhani a wailesi zina mdziko muno kuti atengere chitsanzo cha Radio Maria Malawi pomalemba nkhani zolimbikitsa mtendere mdziko muno.
13
Msika wa fodya utsekulidwa April Misika yaikulu ya fodya mdziko muno ikhoza kutsekulidwa sabata yachiwiri ya mwezi wa mawa, atero akuluakulu a bungwe lowona za fodya mdziko muno la Tobacco Control Commission (TCC). Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Fodya ndi mbewu yaikulu imene dziko lino limagulitsa kunja ndi kubweretsa ndalama zimene zimathandiza pa ntchito zina za boma. Msika wa fodya wa okushoni Polankhula pa lamya kuchokera ku Lilongwe Lachiwiri, mkulu wa TCC Albert Changaya adati masikuwa ndiwongoganizira chabe popeza zokambirana zili mkati. Apa Changaya adachenjeza alimi kuti misikayi ikatsekulidwa asamalitse ndi onyamula fodya ena omwe akumachita utambwali pobera alimi. Iye adati onyamula fodya achinyengowa adabera alimi pafupifupi K1.4 biliyoni chaka chatha. Ena mwa onyamula fodya amanama malo omwe atengako fodyayu ngati uli mtunda waufupi potchula dera lakutali ndi cholinga chofuna kuba. Kafukufuku yemwe adapanga akatswiri athu odziwa kulondoloza zachuma adapeza kuti mchaka chatha choka K1.4 biliyoni idapita, Changaya adatero. Apa adanenetsa kuti anthuwa adziwe kuti kwawo kwatha chifukwa bungweli lili pa kalikiliki wokhazikitsa ndondomeko zatsopano zothana ndi mchitidwewu. Tizigwiritsa ntchito nambala za zitupa za alimi zomwe pa Chingerezi timati zoning. Apa tizidziwa dera lomwe fodyayu akuchokera ndipo wonama aliyense azidziwika, Changaya adatero. Iye adati bungweli likukumana ndi onyamula fodyawa sabata yamawa kuti akambirane za ndondomeko zomwe zakhazikitsidwa pokonzanso zinthu. Changaya adati TCC laletsanso bungwe limodzi kukhala loyanganira alimi lomwelonso lonyamula fodya. Sabata zapitazi woyanganira kampani ya Auction Group mchigawo cha kumpoto, Joseph Kawinga adauza gulu la alimi akuluakulu a fodya ochokera mchigawocho kuti ena mwa onyamula fodya amatenga fodya kuchokera kwa alimi ndi kungomusiya mmalo osungira katundu mumzinda wa Mzuzu mmalo mokasiya kumsika wa fodya. Kawinga adati chifukwa cha kukhalitsa kwa fodyayu mnyumbazi anthuwa amaluza ziphaso zoperekera fodya ndipo amakonzanso ziphaso zawo za bodza. Mwamwayi ziphaso zabodzazi zomwe nambala zake sizigwirizana ndi nambala za pa zitupa zenizeni za kumsika wathu wa fodya, timazidziwa ndipo sitilola kuti fodyayu agulitsidwe popereka chiletso mpaka zonse zitalongosoka, adatero Kawinga. Iye adapempha alimi kuti chaka chino ayesetse kupeza owanyamulira fodya okhulupirika oti akafikitsa mabelo awo kumsika wa fodya. Mmodzi wa alimi akuluakulu a fodya mchigawochi Harry Mkandawire adati bungwe la TCC lichirimike pokonzanso ndondomekozi.
2
Miyambo ya ukwati Ukwati sangotengana ngati nkhuku, pali miyambo yake. Ukalakwitsa miyamboyi, mavuto ena akakugwera umasowa mtengo wogwira. Pakati pa Achewa miyambo ya ukwati nayo ilipo. KONDWANI KAMIYALA adacheza ndi Chikumbutso Funani wa mmudzi mwa Phulusa kwa T/A Kasumbu ku Dedza kuti atambasule zoyenera kutsata. Adacheza motere: Akulu zikuyenda? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Zikuyenda pangonopangono, mavuto a zachuma omwewa basi. Funani: Kukagwa maliro ungasowe mtengo wogwira Ndaona mukuchita izi za kabanza. Chiyambire ntchito ndiyomweyi? Ayi ndithu. Ndidakagwirako ntchito ku famu ina ku Ntchisi. Ndidagwira kwa chaka chimodzi ndipo nditalandira malipiro anga a pachaka, K47 000, ndidabwerera kumudzi kuno. Ndidagula njinga ndipo ndakhala ndikuchita izi kwa zaka ziwiri. Maphunziro mudapita nawo patali bwanji? Ndidalekeza sitandade 7 pasukulu ya Chipaluka. Mudziwa zovuta za kuno kumudzi. Zovuta zanji? Makolo ambiri amakakamiza ana awo kuti aleke sukulu azikawathandiza kumunda kapena kupita kuphiri kukasaka nkhuni. Pofuna kuti tisaone kuzunzika kotero, ambiri timasiya sukulu nkukakwatira kapena kukwatiwa kuti tizidzipangira tokha zapakhomo. Ana ena akukwatira ali ndi zaka 15! Tsono miyambo ya ukwati imayenda bwanji kuno? Kunotu kumakhala kupereka chapamudzi komanso ya chitengwa. Komanso kuli chiwongo, chamsana chimene madera ena amati malowolo komanso pamakhala nkhuku. Tafotokozani poyamba za chapamudzi ndi chamsana. Chapamudzi ndi ndalama zimene zimaperekedwa ngati mwamuna akufuna kukhala mkamwini mmudzi. Ndalamayi imapita kwa mfumu. Chitengwa ndiye umapereka kwa mfumu pamene ukutenga mkazi mmudzi kuti ukakhale naye kwanu. Kodi mitengo yake imasiyana? Eya imasiyana. Mwachitsanzo, padakali pano chapamudzi ndi K7 000 pomwe ya chitengwa ndi K5 000. Cholinga choperekera kwa amfumu nchiyani? Iwo chikuwakhudza nchiyani pamene anthu awiri akondana? Musatero. Kodi utangobwera nkukwatira mmudzi amfumu osadziwa powapatsa chapamudzi utamwalira mwambo wa maliro ungayende bwanji? Nanga utatenga mkazi kupita naye kwanu amfumu osadziwa chifukwa sunawapatse ya chitengwa, mkaziyo nkumwalira mwambo wa maliro ukhala wotani? Mfumu imakana kuti sitikudziwa kuti tili ndi mkamwini kapena mkazi wakuti ndi nthengwa mmudzi wina. Kodi mudachita kupita kwa mfumu kukapereka ndalamayo? Ayi. Mwa mwambo wake, tidapita kwa eni banja. Pamtundu wa chifumu amasankha munthu mmodzi amene amatchedwa mwini banja. Tikapereka kwa iwo ndiwo amakapereka kwa mfumu. Tsono munakamba za chiwongo, chamsana komanso nkhuku. Tatambasulani. Chiwongo chimaperekedwa ngati kuthokoza kuti mkazi adaleledwa mpaka kukula. Dziwani kuti liwu loti chiwongo limatanthauzanso mfunda umene amayi amakhala nawo. Mwachitsanzo, mwana wamkazi wa Obanda chiwongo chake ndi Nabanda. Tikakamba za chamsana kapena malowolo ndiye amaperekedwa kwa mayi a mkazi. Nkhuku ndiye ndi ija amagawana ankhoswe. Kodi anthu akuzitsatabe? Alipo ambiri amene akutsata. Koma nthawi zina ena satsatira izi chifukwa mitundu ya sakanikirana.
1
Ogwira Ntchito ku MACOHA Akunyanyala Ntchito Anthu ogwira ntchito ku factory ya bungwe la Malawi Council for the Handicaped (MACOHA) ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre akuchita mbindikiro pofuna kukakamiza mabwana awo kuti awapatse malipiro omwe anagwilira ntchito mu nthawi yowonjezera. Wofalitsa nkhani ku bungwe la MACOHA a Harriet Kachimanga atsimikiza zankhaniyi ndipo ati izi zachitika kamba ka mavuto ena omwe bungweli likukumana nawo. Mbali imodzi ya fakitaleyo Kachimanga wati bungweli lili mkati mokonza mavutowa ndipo ati posachedwapa anthuwa akhala akulandira malipiro awo. Ndizoonadi kuti ogwira ntchito ku factory ya MACOHA akuchita mbindikiro kamba kofuna kukakamiza mabwana kuti awapatse malipiro awo omwe akhala akugwira ntchito nthawi yowonjezera, anatsimikiza motero Kachimanga. Iwo ati izi zakhala chomwechi kamba koti kampaniyi ikukumana ndi mavuto osiyana siyayana koma padakali pano ikukonza mavutowa ndipo pofika mmawa aliyense akhala atalandira malipiro ake.
6
Ku Nsanje akukana zosamuka Ife zosamuka ayi, yanenetsa gulupu Karonga ya kwa mfumu yaikulu Mlolo mboma la Nsanje. Mawu a mfumuyo akudza pamene anthu 56 pofika Lachinayi sabata ino adatsimikizika kuti amwalira ndi mvula yosalekeza yomwe idazunguza dziko lino sabata yatha. Malinga ndi nthambi yoona za ngozi zogwa mwa dzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (Dodma), nyumba 184 589 omwe ndi anthu 922 945 akhudzidwa. Lachitatu Dodma idachenjeza anthu amene akukhala malo angozi kuti asamukire kumtunda chifukwa a zanyengo alosera kuti mvulayo itha kubweranso. Komabe izi sizikusuntha gulupu Karonga amene wati anthu aiwale zosamukazo chifukwa pali zambiri zomwe ataye ngati atasamuka. Lero ndine mfumu, kuti ndisamuke kupita dera lina ndiye kuti ndikakhala munthu wamba, mukupaona bwanji pamenepo, adatero Karonga, kulankhula mmalo mwa mafumu ake angonongono. Mfumuyo limodzi ndi anthu ake atsakamira pachilumba cha Makhanga. Ndi pakati pa madzi, sangapite madera ena pokhapokha akwere bwato lomwe ulendo umodzi ndi K5 000. Mfumuyo yatinso anthuwo atha kusamuka ngati atawapezera dera lomwe kulibe anthu kuti aliyense akakhale ndi udindo wake komanso malo okwanira. Koma mlembi wamkulu wa Dodma Wilson Moleni adati apita ku Nsanje kukawapemphabe anthuwo kuti asamuke. Akuti mvulayi ibweranso, kutanthauza kuti zinthu zifike polakwika kuposa apa, ndi bwino kusamukira malo okwera kuti tipewe, adatero Moleni. Ngozi ya mvulayi yakhudza maboma 14 mdziko muno koma boma lomwe lakhudzidwa kwambiri ndi Chikwawa chifukwa anthu 8 ndi amene afa. Mu 2015 dziko lino lidakhudzidwanso ndi ngozi ya madzi yomwe idadza chifukwa cha mvula yosaleka. Anthu 79 adafa ndi 153 adasowa. Anthu 638000 adakhudzidwa.
5
Ziweto zisasowe mtendere mkhola yengo ya mvula ino, ziweto monga ngombe, mbuzi, nkhosa ndi nkhumba zimasauka kaamba ka matope mkhola, zomwe zimachititsa kuti ziwetozi zizisowa mtendere. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Nthawi zambiri ziweto zomwe khola lake limadikha, zimakhala zofooka nthawi zonse poti zimalephera kupuma mokwanira kaamba kakuti zimagona choimirira chifukwa cha chidikhacho. Ngombe sizingapeze mtendere mkhola ngati ili. Ngakhale mkakawo ungakome? Mkulu woyanganira za ulimi wa ziweto ndi kuchulukitsa ziwetozo, Dr Ben Chimera, wati mchitidwe ngati umenewu umabwezeretsa ulimi wa ziweto mmbuyo chifukwa nthawi zina ziweto zimatha kugwidwa ndi matenda. Pocheza ndi Uchikumbe, Chimera adati zoterezi zimachititsanso kuti mmalo monenepa, chifukwa msipu wamera, ziweto zimayamba kunyentchera kaamba koti mmalo moti zizidya, zimakhalira kugona kubusa. Zimadabwitsa kuti mmalo moti ziweto zizinenepa poti msipu wamera, zikunyentchera. Chifukwa chake sichikhala china, ayi, usiku zimakhala kuti zachezera chiyimirire ndiye masana zimafuna kugona pamalo ouma mmalo momadya, adatero Chimera. Iye adati ulimi wabwino wa ziweto nkutsatira zomwe amanena a zamalimidwe pakakonzedwe ka khola la ziweto komwe kamathandiza kuti nthawi zonse mkhola muzikhala mouma ndi mwaukhondo. Pali njira zosiyanasiyana koma njira yosaboola mthumba ndi yomanga khola pamalo otsetsereka kuti madzi asamadekha mkhola. Ziweto zili ngati anthu, nazonso zimafuna malo abwino kuti zizitakasuka, adatero Chimera. Mkuluyu adati kwa alimi a ziweto monga mbuzi ndi nkhosa, khola labwino ndi lammwamba kuti ndowe zizigwera pansi komanso madzi asamakhale mkholamo. Chimera adati mlimi akhoza kumanga khola labwino pogwiritsa ntchito mitengo, luzi ndi tsekera ngati palibe ndalama zokwanira kugulira zitsulo ndi malata koma chachikulu nchakuti mkholamo muzikhala mouma. Apa mutha kuona chomwe timalimbikitsira kubzala mitengo mmunda ndi pakhomo chifukwa sungavutike kokapeza mitengo yomangira khola, kungofunika kugula pepala lofolerera, basi kwinaku nkugwiritsa ntchito luzi, adatero Chimera. Malingana ndi chimera, ziweto zokhala mkhola laukhondo zimadya mosangalala ndipo mpovuta kugwidwa ndi matenda ndipo zimaonekera bweya bwake kusalala kuti ndi zaukhondo.
4
Kupha nyani sayangana nkhope Kuyambira pomwe dziko lino lidayamba kukhala ndi ulamuliro wa demokalase (matipate) zinthu pangonopangno zidayamba kusokonekera, makamaka pakayendetsedwe ka chuma. Muulamuliro wa Bakili Muluzi, chuma cha dziko lino chidalowa pansi kotheratu moti njala idalowa; anthu amaswera kumisika ya Admarc koma chimanga kudalibe. Atatenga ulamuliro Bingu wa Mutharika, zaka 5 zoyambirira zinthu zidayamba kusonya ndipo chuma chidayamba kubwerera mchimake. Koma atasankhidwanso kachiwiri, mtsogoleriyu adatayirira ndipo dziko lidayambanso kulunjika kuphompho. Mmene ankatisiya nkuti mafuta akusowa mdziko muno; ndalama zakunja nazo zidasowa; mitengo ya zithu idakwera molapitsa. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Amalawi adaona ngati Chauta wayankha kulira kwawo pamene Mayi Joyce Banda adakhala mtsogoleri wa dziko lino kaamba ka imfa ya Bingu, koma haa! Lero suyu tikumva kuti anthu ogwira ntchito mboma akungosolola ndalama mmene angafunire, makalaliki akumapezeka ndi mamiliyoni mnyumba kapena mgalimoto! Mdziko muno chikuchitika nchiyani, abale? Zagwa zatha! Koma Amalawi tikuti tatopa ndi mchitidwe wotibera chifukwa ndalama zikubedwazi zikuchokera kwa anthu osauka amene akukhoma misonkho kuti apeze mankhwala mzipatala, misewu yabwino ndinso kuti ana awo azipita kusukulu zabwino.
11