Text
stringlengths
292
6.6k
labels
int64
0
19
Pac iwopseza boma pa bilo yachisankho Lisafike Lachitatu sabata ya mawa musanabweretse bilo yokhudza chisankho ndi maboma angono. Latero bungwe la amipingo la Public Affairs Committee (PAC) Lachinayi msabatayi. Izi zimanenedwa pamene bungweli lidayenda ulendo ku Nyumba ya Malamulo komwe limakapereka mfundozi. Bungweli lati ngati sizitheka, boma liyembekezere zionetsero zokwiya ndi boma. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Atavala mikanjo, ena makolala, akuluakulu amipingowa motsogozedwa ndi mkulu wa PAC Mbusa Felix Chingota, adayenda ndawala kuchokera ku Area 18 mumzinda wa Lilongwe mpaka kukafika ku Nyumba ya Malamulo komwe adakapereka mfundo zawo kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika ndi sipikala wa nyumbayo. Izitu zikuchitika pamene PAC, akuluakulu a malamulo komanso amabungwe akhala akufunsira nzeru pa biloyi. Nayo nduna ya zamalamulo Samuel Tembenu adalonjeza Amalawi pamene amalankhula Mnyumbayi kuti biloyi ikambidwa ndi aphungu a Nyumba ya Malamulo. Koma chilankhulireni, boma lapinda manja pamene silikulankhulapo. Mfundo zomwe PAC yalemba zati pamene biloyi ikubwera ku Nyumba ya Malamulo, boma lionetsetse kuti aphungu akambiranenso zokhudza lamulo loti opambana pachisankho cha mtsogoleri wa dziko lino, azipeza mavoti oposa 50 pa 100 alionse. Ngati izi sizikambidwa mpaka pa 29 November, 2017, ife sitichitira mwina koma kuchita zionetsero dziko lonse, idatero mbali ya kalatayo. Polandira kalatayo mmalo mwa Mutharika, mkulu wa khonsolo ya mzinda wa Lilongwe Charles Makanga adalonjeza PAC kuti nkhaniyi saikhalira ndipo ikamupeza Mutharika komanso onse ofunikira.
11
Escom, ganizirani Amalawi Utsi sufuka popanda moto. Mwambiwu umatanthauza kuti kalikonse kamveka sikatero pachabe. Zamveka kuti bungwe la Escom likufuna kukweza magetsi, tikukhulupirira kuti izi sizidangolankhulidwa, kenakake bungweri likukonza. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Escom idziwe kuti Amalawi amafuna zinthu zotsika mtengo komanso zoyenerera. Nthawi zonse pamene akukweza magetsi amanena kuti akufuna kukonza zinthu kuti magetsi asamazimezime yomwe imangokhala nyimbo. Tikulankhulamu magetsi akungozimazima pena mpaka kumatha tsiku lonse magetsi osayaka. Pamene azimitsa magetsi kodi amaganiza kuti anthu akugwiritsira ntchito chiyani? Makalanso ndi oletsedwa ndiye anthu agwire mtengo uti? Bungwe la Escom liganize lisadabwere ndi chiganizo. Tikukamba kuti kuchokera mu May chaka chatha akweza magetsi katatu. Ngakhale adakweza Amalawi sadaone kusintha kulikonse chifukwa kuzimba kwa magetsi ndiyo yakhala nyimbo yomwe aliyense akuyimba. Chonsecho tikumva kuti kampaniyi yagula galimoto zodula zedi masiku apitawa. Amalawi akufuna magetsi tsiku lonse komanso nthawi zonse. Magetsi akenso akhale otsika mtengo osati akwere ngati akakwera asintha kanthu. Zinthu zidakwera inde koma mMalawi aliyense akulira si inu nokha a Escom amene mukumva kuwawaku. Kondani Amalawi osati kukweza zinthu.
2
Ankadziwana ndi mayi anga Kale makolo amachita kusankhira ana awo munthu wokwatirana naye, koma pano zinthu zidasintha ngakhale kuti makolowo akhoza kungokhala muni wowalitsa kuti ana aonane nkukondana. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Anthu ambiri apezapo mabanja chifukwa chakuti makolo awo kapena abale awo ena amachezera limodzi ndipo kudzera mukucheza kwawoko ana awo adaonana ndi kukondana mpaka lero ndi banja. Lucky ndi Sheira patsiku la chinkhowe Njira ngati iyi ndimo lidayambira banja la Lucky Madaika wochokera kwa Chipyali mboma la Balaka ndi Sheira Kachitseko wa kwa Bubua, T/A Makwangwala ku Ntcheu. Awiriwa kuti akumane nchifukwa chakuti Lucky ankapitapita kunyumba kwa Shiera malingana ndi bizinesi yake ya zamakompyuta kukaonana ndi mayi a Sheira ngati kasitomala wake. Ukutu akuti kudali kumayambiriro a chaka cha 2015 ndipo atapita kangapo kunyumbako, adalephera kuugwira mtima mpaka adapempha nambala ya lamya kuti aziimbirana nkumacheza koma kenako chibwenzi chidayambika. Tidakhala pachibwenzi kwa miyezi ingapo kenako tidaganiza zopanga chinkhoswe ndipo zonse zoyenera monga kukaonekera kumakolo ndi zina zitachitika, chinkhoswecho chidachitikadi ku Area 47 mumzinda wa Lilongwe, adatero Sheira. Iye adati mmiyezi 7 ikudzayi awiriwa adzakhala akuvekana mphete, makamaka pa 9 July, 2016 mumzinda womwewu wa Lilongwe. Lucky adati aiwiriwa amakhulupirira kuti powalenga, Mulungu adakonza kuti adzakhala limodzi poona chikondi chomwe amapatsana komanso akuti pali zambiri zomwe onse amakonda kapena kudana nazo.
15
JB watukula amayi, koma ntchito ikadali Pamene dziko la Malawi lagwirana manja ndi maiko ena padziko lapansi pokukumbukira tsiku la amayi, Amalawi ena athirapo ndemanga ndi momwe mtsogoleri wa dziko lino, Joyce Banda, wagwirira ntchito. Ena akuti wayesetsa kutukula amayi mdziko muno, pomwe ena sakukhutitsidwabe kuti wakwaniritsa chiyembekezo chawo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Woyendetsa bungwe loona zomenyera ufulu wa amayi (national coordinator) la Women and Law in South Africa (WLSA) kuchigawo cha kummwera kwa Africa, Seodi White, komanso mkulu wa bungwe la Malawi Communications Regulatory Authority (Macra), Martha Kwataine, ati maudindo ena omwe amayi asenza lero sadayambe akhalapo nkale lomwe, zomwe zikusonyeza kuti Banda wachitapo cholozeka pa miyezi 11 yomwe wakhala akulamulira. White wati udindo wa mlembi wamkulu mboma, Hawa Ndilowe, komanso maudinso ena monga amene wasenza Kwataine ku Macra, ndi chitsimikizo kuti Banda wasinthako moyo wa amayi mdziko muno. Ukakhala pulezidenti anthu amayangana zambiri pa iwe. Komabe izi zili apo, a Pulezidentiwa pena zimakhala ngati zikuwalaka ndipo potero samaonetsa chitsanzo chabwino. Izi zimachititsa ena kulankhula kuti amayiwa ndi obalalika; amakhala ngati akubwerera mmbuyo, akutero White. Iye akupemphanso kuti Banda achilimike kuika amayi mmaudindo omwe sadakhalemo. Sitikufuna kuti anthu aziti amayi gemu yawakanika. Mmawu ake, Kwataine wati mwachaje satafuna, Pulezidenti Banda wachitapo zolozeka nthawi imeneyi, maka kwa amayi, zomwe zikuwalitsa amayi mdziko muno. Taona amayi akukhala nduna, amayi akusenza maudindo [onona], zomwe zikutinyaditsa. Mafuta agalimoto akupezeka kusiyana ndi nthawi [ya DPP], ichi ndi chonyaditsa. Pakalakwika timalankhula komanso pena pakakoma tisabise. Amayi tisachite nsanje mnzathu akachita bwino, komanso tisanyengerere zikakhota, adatero Kwataine. Tsiku la amayi timalikumbukira pa 8 March koma chaka chino mdziko muno alikumbukira Loweruka lino ndipo mutu wake ndi Lonjezo ndi lonjezo: Nthawi yochitapo kanthu pothana ndi nkhaza kwa amayi.
11
MBS Ichlimika Poteteza Miyoyo ya Anthu Bungwe la Malawi Bureau of Standards lati likudzipereka pa ntchito zoonetsetsa kuti anthu mdziko muno akudya ndi kugwilitsa ntchito zinthu zoyenera ndi cholinga choti miyoyo yawo idzikhala ndi chitetedzo chabwino nthawi zonse. Mkulu wa bungwe-li mdziko muno a Symon Mandala wanena izi ku Mangochi pomwe bungweli limazindikilitsa atolankhani ntchito za bungweli. Iwo ati bungweli likuyesetsa pa ntchito zake ngakhale pali anthu ena kufikira pano zakudziwabe za momwe bungweli limagwilira ntchitozi. Kumbari ya madandaulo omwe anthu ena akhala akupereka ponena kuti bungweli limachedwa kuvomeleza pa katundu wawo kuti ayambe kupezeka pa msika, a MANDALA anati zimenezi zimachitika kamba koti anthuwo amalephera kutsatira zomwe bungweli limafuna kuti klivomeleze izi.
14
Boma, mafumu salabadira mavuto a Amalawi Kusapezeka kwa boma komanso mafumu ku zokambirana zomwe adaitanitsa a bungwe la amipingo la Public Affairs Committee (PAC) sabata yatha kwaonetsa kusalabadira zoombola Amalawi kumavuto omwe akula mdziko muno. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mkulu wa bungwe lomwe silaboma lolimbikitsa chilungamo la Justice Link, Justine Dzonzi, kudzanso mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wachibadwidwe la Malawi Watch, Billy Banda, anena izi msabatayi. Awiriwa ati ngati boma silokonzeka kukambirana zoombola Amalawi ku mavuto omwe ayala mphasa mdziko muno ndibwino mtsogoleri wadziko lino, Bingu wa Mutharika, akapume mopanda kukankhana. Koma mneneri wa boma, Patricia Kaliati wati uwu ndi mtopola komanso mabodza chifukwa aboma sadaitanidwe kuzokambiranazo. Iye wati sakukhulupiriranso kuti msonkhanowo udatsekulidwa kwa aliyense chifukwa bungweri lidathamangitsa atolankhani ena kumsonkhanoko. Ngati amathamangitsa atolankhani ndiye ife achikhala tidapita sibwezi atatithamangitsa? Ngati amatitukwana oti sitidapiteko ndiye zikadatha bwanji achikhala tidali komweko? Chifukwa chiyani amaloza dzala ena kuti achokera kuboma chikhalirecho amati aitana aboma? Zamtopola ndi mabodza ife sitifuna, adatero Kaliati. PAC idachititsa msonkhanowo ku holo ya mpingo wa Katolika ku Limbe Cathedral mu mzinda wa Blantyre kuyambira Lachitatu mpaka Lachinayi sabata yatha komwe idaitana amipingo, aboma, mafumu, atolankhani, azipani, akatswiri azamalamulo, komanso oona zamaufulu a anthu. Mbali zonse, kupatula mafumu ndi aboma zinafika. Koma wapampando wa bungwe la PAC, Robert Phiri wati bungwe lawo lidatumizira kalata mafumu atatu kuti adzakhale nawo pa zokambiranazo koma mfumu imodzi yokha ndiyo idabwera. Iye wati adadabwitsidwa ndi mfumu idabwerayo kuti idangokhala kanthawi kochepa ndipo idabwerera mosadadziwa chifukwa chake. Phiri wati aboma adawatumiziranso kalata kuti adzakhale nawo pazokambiranazo koma palibe nkhope ndi imodzi yomwe idabwera. Kupatula mafumu atatuwo tidatsekula msonkhanowo kuti yemwe akufuna atha kubwera, adatero Phiri. Pomaliza msonkhanowo, zina mwa mbali zoitanidwazi zidamanga mfundo kuti Mutharika atule pansi udindo wake mmasiku 60 kapena aitanitse riferendamu mmasiku 90. Apa Dzonzi, Banda ndi ena ati agwirizana kwathunthu ndi ganizoli ati chifukwa ngati Mutharika sangatule pansi udindo, chonsecho mbali ya boma osamapezekanso kuzokambirana, mavuto omwe akufinya anthu mdziko muno sangathe. Banda wati kusapezeka kwa boma kukusonyezeratu kuti lidadzipeza lokha lolakwa pazomwe zimakambidwa kumsonkhanowo. Dzonzi, yemwenso ndi katswiri wa zamalamulo, wati dongosolo la malamulo a dziko lino limalongosola nthawi yoyenera yomwe pangachitikire riferendamu komanso kumupempha mtsogoleri kuti atule pansi udindo. Iye wati riferendamu ingatheke ngati dziko likufuna kusintha malamulo ena kapena kuona ngati pulezidenti akukondedwabe ndi anthu. Iye wati nkothekanso kukhala ndi kukhalanso ndi zomwe maiko ena amatcha masankho apakatikati. Apa iye wati sikulakwira malamulo kumupempha pulezidenti kuti atule pansi udindo chifukwa naye amakhala ndi liwu pa ganizolo. Iye wati Pulezidenti atha kuchoka potula pansi udindo mwa iye yekha kapena ngati achotsedwa potsatira malamulo oikika. Mwa zina iye adati malamulo amapereka mpati wokakamiza Pulezidenti kusintha zingapo. Iye adatinso kuchita zionetsero zokakamiza kuti Pulezidenti atule pansi udindo nkololedwa mmalamulo adziko lino. Victor Sangula wa mmudzi mwa Kasitoma kwa T/A Liwonde mboma la Machinga wati boma silifuna kuvomereza kuti mavuto omwe adza mdziko muno abwera kaamba kosafuna kukambirana. Iye wati nkutheka boma limaganiza kuti msonkhanowo ungalephereke ngati ilo silipezeka. Sangula wati Mutharika atule pansi udindo chifukwa ngati satero mavuto mdziko muno apitirirabe. Assam Banda wa mmudzi mwa Manjeza kwa T/A Kadewere mboma la Chiradzulu wati kusapezeka kwa mbalizi kungaunikireponso za udani omwe ulipo pakati paboma ndi amabungwe. Iye wati mavuto a zachuma ndi ndale omwe ali mdziko muno ndiwo angakakamize Mutharika kuti akapume. Mfumu ina yaikulu ya mboma la Zombayomwe yapempha tisaitchule dzina kuti imasuke polankhulayati ngati mnyumba muli kusamvana pamafunika kukambirana, osati kuchotsa bambo wa mnyumbamo. Iyo yati boma lidaphonya mwayi posapezeka kuzokambiranako komwe ati kukadapezeka mayankho a mavuto omwe achuluka mdziko muno. Boma lidalakwa; apa zikutanthauza kuti mavuto omwe ali mdziko muno sangathe chifukwa boma likukana zokambirana, idatero mfumuyi. T/A Nthache ya mboma la Mwanza yati bungwe la PAC lidawalambalala kuzokambiranazo kotero apempha bungweli lichititse msonkhano wina omwe udzaitanitse Mutharika ndi Mafumuwa. Mfumuyi yati atsogoleri a midzi akaitanidwa kuzokambirana, eni msonkhanowo amayenera akonze mayendedwe ndipo a PAC sachite izi. Iyo yati mafumu amakhulupirira kukambirana ndipo adali chile kukakhala nawo pazokambiranazo. Nthache wati sakupeza chifukwa choti Mutharika atulire pansi udindo chifukwa zimenezi zingayambitse ziwawa zomwe zingathere mnkhondo. Nkhondo ya ku Mozambique idayambika motere pomwe padalibe kumvana kwa ena ndi boma; adzavutike ndi anthu a kumudzi, akutero Nthache. Iye wati PAC ichititse msonkhano wina womwe udzameme mafumu ndi Mutharika.
10
Msika wa ziwala, mbewa Tidali pamalo aja timakonda pa Wenela, mnyamata uja Bonny Wasawaliya Kanindo atafika ku nyumba ya ulemu ku Nyumba ya Malamulo komwe adakakwanitsa kupereka chikalata chodzudzula zophana. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndinakaperekera chikalatacho mchimbudzi chifukwa ndimafuna ndikapereke ndili chinochino. Zatheka, adatero Kanindo. Koma ayi ndithu mwaitha, uthenga wamveka ndipo tikudziwa amene amakonza zionetsero nkumayenda okhaokha atangerapo phunziro, adatero Abiti Patuma. Kanindo adati tisachedwe pamalopo, koma titsagane naye kupita ku Limbuli komwe amafuna akakhale limodzi ndi Moya Pete amene amati akakambe za chimanga chimene chimapezeka kwambiri. Mwayi wathu ndi womwewu, tikaguleko chimanga chifukwa pa Wenela chimanga ndiye chadula. Mwati pofika December sichikwana K25 000? Chongofika pa Limbuli, tidapeza atate, akazi awo ndi ana awo akudikira Moya Pete yemwe nthawiyo akumwa tiyi pamwala uja ankawerengera Chilembwe ku PIM mboma la Chiradzulo. Anthu adamupatsa molalo Kanindo. Koma tidaona akuluakulu ena akulozerana zala. Atafika Moya Pete, kudaterera. Ndidamuona akunongoneza mmodzi mwa asirikali ake. Kenako adamuloza Kanindo. Ndidangoona asirikali aja akukhamukira kwa Kanindo, kodi kapena dzina lake ndi Kawindo? Iwe uchoke pano. Moya Pete akuti akufuna achite zisudzo aseketse anthu chikhakhali. Zisudzo unachita iwe zabunobuno zija akuti wachepa nazo, adamuuza. Padalibe zaulemu, adamukoka kumutengera kugalimoto yake yolemba Wikoni 1. Moya Pete adaimirira. Kumanja kwawo kudali nsalu ya mtundu wa thambo. Inu! Inu! Mumadziwa za dirama kwambiri inu? Inetu ndidali wadirama kalelo. Zisudzo si nkhani. Mr Bean, Trevor Noah, Anne Kansiime mukutamayu, Teacher Mpami what? Onsewo ndaphunzitsa ndekha, adayamba motero. Anthu onse adafa nalo phwete! Sindikudziwa ngati amaseka zimene amanena Moya Pete kapena amawaseka! Ndikuuzeni kwambiri! Tiyeni tizidya utakafumbi! Tiyeni zithuli zagundikazi tisazilekerere. Tasekani kwambiri, adatero. Anthu adaseka. Ha! Ha! Ha! Abiti Patuma amvekere: Ki! Ki! Ki! Lol! Moya Pete adamezera malovu. Inutu mukudziwa kwambiri. Chimanga chikupezeka kwambiri kuno ku Limbuli kokha kuno. Choncho, tiyeni tizingotafuna akapuko.amkokamadzi. Mukapezanso makoswe mukhoza kuchita nawo, samapha konse. Sekani kwambiri anthu inu! adapitiriza. Anthu adaseka chikhakhali. Sindinaone munthu wodziwa kuseketsa ngati Moya Pete! Choncho! Ndachotsa chimanga chija adaika mkulu uja Mfumu Mose chifukwa pano chikusowa. Mbewa ndi zithuli ndizo tiziike apa! Muzidya zimenezi. Mwamva kwambiri? adafunsa. Pomwe amatero nkuti akutambasula nsalu yatsopano ija. Ndikumbuka bwino lomwe gogo uja adandipeza ndikulima osavala ankakonda kunena kuti safuna anthu ake azigona mnyumba zothonya mvula ikamagwa, azidya ndi kuvala bwino; ndidakumbukanso Mpando Wamkulu akunena kuti mukamva njala kaya minkhaka zitafunani. Kodi tsono enatu sadya mbewa ndiye azidyanji? ndidafunsa.
15
Mutharika Wauza Nyumba ya Malamulo Iwunike Ngati Nkoyenera Kuchita Chisankho Mkatikati mwa COVID-19 Mtsogoleri wa dziko lino Professor Peter Mutharika lero watsekulira nyumba ya malamulo kudzera mu uthenga omwe unali ojambulidwa. Sanapiteko ku nyumba ya malamulo Mutharika Komatu izi sizidasangalatse aphungu ena maka a mbali yotsutsa omwe anafunsa kuti boma lifotokoze momveka bwino chifukwa chomwe a Mutharika analankhula pa momwe zinthu zilili mdziko ,muno kapena kuti State of the Nation Address pachingerzi, kudzera mu uthenga ojambula osati kufika ku nyumbayi. Malipoti akuti a Mutharika anachita izi kamba ka chiopsezo cha mliri wa Covid-19 kuti mwina ku nyumbayi kukadafika anthu ochuluka zomwe ndi zosemphana ndi ndondomeko zomwe zilipo. Mwazina, a president wa dziko linoyu anakambako pa momwe chuma chikuyendera pakadali pano, ndondomeko zopewera mliri wa Covid-19, kudzudzula zipolowe za ndale komanso ndondomeko zomwe boma likutsata pofuna kuthandiza anthu mu nthawi ya mliriwu. Lowe: Zikumvetsa chisoni kuti akunyozabe ma judge Kumbali ya zisankho, a Mutharika wati nyumba ya malamulo ikambirane mozama ngati kuli koyenera kuti dziko lino lichite chisankho posachedwa kapena kudikira kaye kuti mliriwu uchepe. Iye pamenepa wadzudzulanso oweruza milandu kamba ka chigamulo chomwe adapeleka choti dziko lino lichitenso chisankhochi ndipo anati awa ndi maganizo ake osati kusalemekeza mabwalo amilanduwa. Koma poyankhapo pa izi, mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma a Robin Lowe ati ndi osakondwa ndi momwe mtsogoleri wa dziko linoyu akulankhulira pa nkhani zokhudza ma bwalo a milandu. Zikungokhala zomvetsa chisoni kuti mmene tayendera naye president sakulora kuti khothi lili padera, parliament ili padera komanso executive ili padera ndiye iwo atenga mphamvu za tonse afuna ayendetse, anatero a Lowe. Iwo apempha olangiza mtsogoleri wa dziko linoyu kuti amuthandize mtsogoleriyu kumvetsa chigamulo chomwe khothi linapereka.
11
Kota yatha, JC yabwerera Unduna wa za maphunziro wathetsa njira yosankhira ophunzira msukulu zaukachenjede yotchedwa kota, komanso yabwezeretsa mayeso a JC msukulu za sekondale. Kudzera mu njira ya kota, yomwe yakhala ikudzetsa mpungwepungwe mdziko muno, ophunzira amasankhidwa potengera boma lomwe amachokera osati momwe akhonzera. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ophunzira azisankhidwa msukulu zaukachenjede potengera kukhoza kwawo Anthu ndi akatswiri azamaphunziro ayamikira boma chifukwa cha kusinthaku, koma achenjeza kuti boma lisachite izi pofuna kukopa anthu kudzavotera chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP) pa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino chomwe chidzachitike pa May 19 chaka chino. Polengeza nkhaniyi pa msonkhano wa atolankhani mu mzinda wa Lilongwe Lachinayi, nduna ya maphunziro William Susuwere Banda idati boma lamvera maganizo a anthu, komanso malo msukulu zaukachenjede za boma achuluka poyerekeza ndi momwe zidaliri mmbuyomu. Monga mukudziwa boma lawonjezera malo msukulu zake. Kupatula apo, sukulu zina zomwe zidali pansi pa University of Malawi zaima pazokha zomwe zachititsa kuti malo achuluke msukuluzo. Boma lamvera Amalawi kaamba koti akhala akudandaula ndi njira ya kota, komanso kuchotsedwa kwa mayeso a JC, adatero Banda. Zipani zotsutsa boma zakhala zikugwiritsa ntchito kota pa kampeni ya chisankho cha pa May 19 2020. Mwachitsanzo, Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM akhala akuuza Amalawi kuti adzathetsa kota zikadzalowa mboma. Sinodi ya Livingstonia ya mpingo wa CCAP, yomwenso yakhala ikudzudzula boma chifukwa cha kota, yati siikambapo kanthu pokhapokha itaona kuti zinthu zasinthadi. Tamva koma sitinenapo zambiri chifukwa ilo ndi lonjezo chabe. Tiyambe kaye taona zikuchitika ndiye tidzalankhulapo, adatero mlembi wamkulu wa sinodiyo Mbusa Levi Nyondo. Wapampando wa gulu lina lotchedwa Quota Must Fall, lomwe lakhala likutsutsana ndi njirayi Dr Bina Shaba adati sakufuna malonjezo koma kuchotseratu kota. Tidzaomba mmanja tikadzaona zinthu zitasintha, koma padakali pano sitisiya kulankhula zotsutsana ndi kota, adatero Shaba. Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe loona zaufulu wa anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC), Charles Kajoloweka, adati akhala akulondola ngati boma likuchitadi zomwe lalonjezazo. Lonjezo limakhala la phindu likakwaniritsidwa. Tamva koma tikhala tikulondolo ncholinga chofuna kudziwa ngati boma likuchita zomwe lalonjezazo, adatero Kajoloweka. Mkulu wa bungwe Civic Society Education Coalition (Csec) Benedicto Kondowe adati nkhaniyi ndi yabwino, koma boma lisakhale likusewera ndi maganizo a Amalawi pogwiritsa ntchito kota ngati nyambo yokolera mavoti. Kuthetsa kota ndi ganizo labwino, koma tisalankhule zambiri chifukwa itha kukhala kampeni chabe. Nthawi zina boma limalankhula zinthu mongofuna kukopa anthu. Takhala tikulira za nkhanizi kwa nthawi yayitali ndiye lero lokha kwatani? adafunsa Kondowe. Mtsogoleri wa bungwe la sukulu zomwe si zaboma la Independent Schools Association of Malawi (Isama) Peter Patel wayamikira boma pobwezeretsa mayeso a JC. Patel adati kuchotsa kwa JC kumalowetsa pansi maphunziro. Chomwe chimachitika nchoti ophunzira amangosewera kuyambira Folomu 1 mpaka Folomu 3 nkudzadzidzimuka ali Folomu 4 chaka chawo cha mayeso ndiye amakhala kakasi chifukwa ntchito imachuluka zotsatira zake, ophunzira ambiri amalephera, adatero Patel. Pakati pa 2015 pomwe boma limathetsa JCE ndi 2019, ana 58 pa 100 aliwonse ndiwo amakhoza mayeso a MSCE pomwe pakati pa 2011 ndi 2014 JCE isadathe, ana 53 pa 100 aliwonse ndiwo amakhoza MSCE. Koma Kondowe adati izo zilibe ntchito chifukwa kupanda kuthetsa JCE, bwenzi ana akukhoza kwambiri kuposa 58 pa 100 aliwonse potengera ndi momwe ndondomeko ya maphunziro idasinthira. Makhozedwe pa zaka 8 adali motere: 2011 (51.8%), 2012 (51.8%), 2013 (52.48%), 2014 (54.08%), 2016 (58.32%), 2017 (61.66%), 2018 (63.00%) ndipo 2019 (50.36%). Boma lidalengeza kuti lathetsa mayeso a JC mu September 2015 ndipo izi zidatanthauza kuti ophunzira akapita ku sekondale, azingokhulula mpaka Folomu 4 komwe amalemba mayeso aboma a MSCE. Poteteza ganizolo, boma lidati iyi ndi njira imodzi yotetezera ndalama za boma chifukwa zimatanthauza kuti kuyambira Sitandade 1 ku pulayimale mpaka Folomu 4 ku sekondale, ophunzira azilemba mayeso aboma awiri basi a Sitandade 8 (PSLC) ndi pa MSCE. Njira ya kota idayamba mchaka cha 1987, koma anthu akhala akuikana koma boma limakakamirabe kuigwiritsa ntchito.
11
Tetezani kukokoloka kwa nthaka ndi biyo Njira zotetezera nthaka kumadzi othamanga zili mbwee, koma katswiri wa zanthaka kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College, Dr Jimmy Namangale, wati kuika biyo mmalo momwe mumadutsa madzi ndi njira yabwino yopewera ngalande mmunda. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Polongosolera Uchikumbe sabata ino, katswiriyu adati mmalo momwe mumadutsa madzi, makamaka mmunda, zaka zikamapita mumasanduka ngalande kutanthauza kuti nthaka yomwe idali pamenepo idanka kwina ndi madziwo. Iye adati mlimi akalekelera osachitapo kanthu, zotsatira zake munda umaonongeka komanso zimachititsa kuti mitsinje ndi madambo omwe amasunga madzi omwe akadagwira ntchito ya mthirira zikwiririke. Biyo wopangidwa ndi miyala amateteza nthaka ku madzi othamanga Ili ndi limodzi mwa mavuto omwe alimi ambiri amalekerera koma ndi chifukwa chimodzi mwa zifukwa zomwe zabwezeretsa ulimi mmbuyo. Zimaoneka ngati palibe chomwe chikuchitika chifukwa chaka chilichonse gawo lochepa lokha la nthaka ndilo limapita. Izi zimakhala zikuchitika chaka ndi chaka ndipo podzazindikira, mmunda mumakhala mutadzadza ngalande ngati mitsinje, adatero Namangale. Katswiriyu adati njira yodalirika yopewera zoterezi nkuyika biyo mmalo momwe mumadutsa madzi kuti liwiro la madzi oyendawo lizichepa komanso biyo amathandiza kuwakha nthaka yomwe imayenda ndi madzi. Paupangiri wake, iye adati biyo savuta kukonza kwake, koma nzoyenerera kufunsa upangiri wa alangizi pogwira ntchitoyi chifukwa pamakhalanso ukadaulo wapadera kuti miyala yopangirayo ilimbe, isadzakokoloke. Biyo amateteza nthaka ku madzi oyenda, makamaka othamanga, monga mudziwa kuti masiku ano mvula ikangogwa pangono madzi amathamanga kwambiri chifukwa chosowa poimira malingana nkuti mitengo ndi chilengedwe zidatha, adatero Namangale. Mkuluyu adati pokhapokha mavuto ngati awa atathetsedwa, ngozi zina ngati kusefukira kwa madzi ndi kukokoloka kwa mbewu zisanduka nyimbo ya chaka chilichonse komanso nthaka idzafika potheratu kutsala thanthwe basi. Mogwirizana ndi zimene adanena Namangale, katswiri wina wa zanthaka ku Bunda, Dr Patson Nalivata, adati pomwe alimi akuyesayesa njira zosiyanasiyana zobwezeretsera chonde mnthaka, mpofunikanso kuti azitsatira njira zoteteza kukokoloka kwa nthakayo. Iye adati palibe tanthauzo lililonse kuti chaka ndi chaka alimi azikhala ndi ntchito yokokera chonde mmanyowa koma osachiteteza kuti chisakokolokenso.
4
Dayosizi Ya Karonga Iyamba Kukakamiza Akhristu Kuvala Face Mask Ku Tchalitchi Dayosizi ya mpingo wakatolika ya Karonga yakhazikitsa dongosolo loti akhristu adzivala Face Mask mu tchalitchi pofuna kupewa matenda a COVID-19. Malinga ndi kalata yomwe diyosiziyi yalembera akhristu ake, dongosolori liyamba mwezi uno pa 18 July kumapita mtsogolo. Ndi mkulu wa dayosiziyo-Ambuye Mtumbuka Kalatayi yati, palibe mkhristu yemwe adzaloredwe kulowa mu chalitchi ngati adzakhale asanavale face mask. Malinga ndi mlembi wa diocese yi bambo Joseph Moloka Sikwese, dongosolori akhristu akulidziwa kale ndipo ati sakukhulupilira kuti papezeka mkhristu onyalanyaza. Ife ngati mpingo wa dayosizi ya Karonga tikukhulupirira kuti sipakhala mkhristu onyalanyaza kuvala ma face mask chifukwa choti takhala tikupereka maphunziro ophunzitsa akhritsu onse kuwopsa kwa matenda a COVID-19, ndipo tikhulupirira kuti akhristuwa azindikira kuti iyi ndi njira imodzi yopewera matendawa, anatero bamboo Sikwesi. Iwo atinso dayosiziyi ili ndikuthekera kochita izi kamba koti parish iliyonse inaphunzitsa atelala omwe iwo ngati dayosizi inawapasa nsalu kuti asoke ma mask-wa omwe akugulitsidwa pa mtengo wa 250 kwacha.
6
Apolisi ku Ntcheu Ayamikira Mpingo wa Katolika Wolemba: Thokozani Chapola Apolisi mboma la Ntcheu ayamikira mpingo wa katolika mu dayosizi ya Ntcheu potengapo gawo pothandiza kukweza ntchito za apolisi mbomalo. Mneneri wa apolisi mbomalo Sub Inspector Hestings Chigalu wanena izi pomwe bungwe la amayi a mu parish ya Ntcheu mu diocese ya Dedza linayitanitsa apolisi komanso achipatala ngati njira yophunzilira zina mwa zomwe akuyenera kuchita posamalira mabanja awo. Chigalu: Tiyamikire mpingo wa katolika ku Ntcheu parish Sub Inspector Chigalu ati mkumanowu wathandiza apolisiwa kufalitsa kwa anthu ntchito zomwe amagwira ndipo zithandizira kuchepetsa umbava, nkhanza komanso maukwati a ana achichepere mbomalo. Tiyamikire mpingo wa katolika ku parishi imeneyi ya Ntcheu. Pa tsiku limeneli tawaphunzitsa za mayendedwe abwino apansewu, kukakamiza ana kulowa mbanja, nkhanza kwa ana mbanja ndi zina zambiri powauza za udindo wawo pa zinthu zosiyanasiyana ngati mpingo, anatero a Chigalu. Mmodzi mwa apolisi kulankhula ndi amayi a ku parishi ya Ntcheu Iwo apempha mipingo ina kuti itengerepo chitsanza pa zomwe mpingowu mu parishiyi wachita ponena kuti ndi khumbo lawo kugwira ntchito ndi mipingo yonse mdziko muno. Wapampando wa bungwe la amayi ku parishi ya Ntcheu mu dayosizi ya Dedza, mayi Milliam Chikafa ati mkumanowu unali wopambana. Tinawaitana kuti azatithandize pa nkhani za nkhanza za mbanja komanso maufulu a ana, anatero mayi Chikafa. Iwo ati patsikulinso anayitana azachipatala kuti azathandize amayiwa za matenda monga khansa ya khomo la chiberekero, fistula komanso edzi.
14
Milandu, Ngozi Zakwera Mboma la Ntcheu Apolisi mboma la Ntcheu adandaula ndi kukwera kwa milandu komanso ngozi za pansewu mmiyezi isanu ndi umodzi ya chaka chino, poyerekeza ndi miyezi ngati yomweyi chaka chatha. Chigalu: Ngozi zachuluka kwambiri Wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sub-Inspector Hastings Chigalu wati mu lipoti la chaka chino, zasonyeza kuti mu miyezi 6 yapitayi, bomali lalembetsa ngozi zochuluka kuyerekeza ndi miyezi yomweyi chaka chatha. Lipotili lasonyezanso kuti milandu yophana komanso kugwilirira yakweranso kuyerekeza ndi chaka chatha. Lipotilo lati miyezi yoyambilira ngati yomweyi chaka chatha ngozi za pansewu zinali 19 ndipo chaka chino zakwana 44 ndipo milandu yophana chaka chino yapezeka 16 pomwe chaka chatha inalipo 11 komanso milandu yogwililira chaka chino yapezeka 30 pomwe chaka chatha inalipo 15.
14
Akagawira Ukayidi Zaka 10 Kamba Kogwililira Bwalo loyamba la milandu mboma la Mangochi lalamula a Maxwell Jiya a zaka 53 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka khumi (10) kamba komupeza olakwa pa mlandu wogwilira msungwana wa zaka 10 zakubadwa yemwe ndi mwana wa ku banja la akazi ake. Bwalolo linamva kuchokera kwa oyimira boma pa mlandu Sub-Inspector Skeva Munyapa kuti bamboyu ndi mkazi wake akhala akulephera kupeza mphatso ya mwana, ndipo anakatenga msungwayo ku banja la akazi awo kuti azikhala naye pa khomopo. Pa 2 April, 2020 mmawa akazi a bambo-wa anapita kotunga madzi ndi kusiya msungwanayo ali pakhomo ndipo bamboyu anapezerapo mwayi wokokera msungwayu ku chipinda komwe anakamugwilira ndipo akazi awo atafika pa khomopo anadabwa ndi ululu umene mwanayo anali kuumva ndipo atamufunsa anaulula za nkhaniyi. Woyimira boma pa mulanduyu Sub Inspector Munyapa anati zomwe anachita mkuluyi zinali zosayenera kotero akuyenera kulandira chilango chokhwima. Ndipo popereka chigamulo First Grade Magistrate Roy Kakutu anagwilizana ndi zomwe analankhula oyimira boma pa mulandu-wu ndi kupereka chigamulo cha mtunduwu kuti ena atengero phunziro. A Maxwell Jiya amachokera mmudzi mwa Ngumela mdera la mfumu yayikulu Juma mboma la Mulanje.
7
Alimi samalani thonje, kwagwa kachilombo koononga Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Kwatulukira kachilombo kotchedwa kodikodi kapena kuti mealybug kamene kakuononga thonje, watero mlembi wamkulu wa unduna wa malimidwe Erica Maganga. Maganga wati kachilomboka kakuumitsa mitengo ya thonje komanso nkhunje za thonje zikumaphulika zisanakhwime zomwe zikuchepetsa zokolola. Madera ambiri kunsi kwa mtsinje wa Shire monga ku Magoti EPA mboma la Nsanje komanso ku Lisungwi EPA mboma la Neno ndi komwe tizilomboni tagwa ndipo thonje lambiri lauma. Malinga ndi Maganga, thonje la mtundu wa Chureza lomwe lili ndi maluwa komanso lopanda maluwa ndi lomwe lagwidwa kwambiri ndi tizilomboti. Maganga wati tizilomboti tikumabisala mmingalu komanso mmauna kapena mopindika mwa mbewu zomwe zikuchititsa kuti alimi alephere kutiona. Mlimi kusamalira thonje lake Mlembiyu akuti kupha kwa tizilomboti ndi kovuta chifukwa cha momwe tidabadwira. Timakhala ndi mafuta pa khungu lake komanso taufaufa zomwe zimateteza tizilomboti ku mankhwala ndi ku nyengo ina iliyonse yobweretsa chiopsezo ku tizilomboti, adatero Maganga. Malinga ndi mlembiyu, sizikudziwika kuti kachiromboka kachecheta ndime yaikulu bwanji chifukwa undunawu ukadafufuza chionongekocho. Komabe Maganga wati alimi apopere minda yawo mankhwala a Acephate, 75 SP 1gm/L kapena Malathion 50 EC 2ml/L pa mlingo wa mamilimita 250 pa hekitala kapena maekala awiri ndi theka pogwiritsa ntchito mlingo wa 17.5l wa mankwhalawa mumalita 14 a madzi. Iye wati tizilomboti timafala kudzera mumbewu ya thonje, mphepo, madzi omwe amagwiritsira ntchito, madzi a mvula, mbalame, anthu komanso ziweto. Mkalata yomwe undunawu watulutsa, tizilomboti timapezeka mmitengo ya maluwa, zipatso, mbewu zakudimba ndi kumunda komanso mtchire.
4
MEC ikufunakusinthatsiku la chisankho Pavuta kuti chisankho chichoke mwezi wa May kupita September monga bungwe loyendetsa chisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) lidapemphera komitiya Nyumbaya Malamulo yoona zamalamulo. Mkulu wa MEC, Jane Ansah sabata yatha adapempha komitiyo kuti ilingalire za ganizoli. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Iye adati izi zikudza chifukwa mwezi wa May ndiwozizira komanso usiku umatalika kuposa tsiku, zimene zingachititse ena kulephera kuvota. Malinga ndi malamulo, chisankho chiyenera kuchitika sabata yachitatu mwezi wa May ndipo ngati kusinthako kungachitike pachisankho cha 2019, ndiye kuti mtsogoleri wadziko lino Peter Mutharika akhala pampandowo miyezi 4 yoonjezera. Koma mneneri wachipani chotsutsa cha Malawi Congress Party (MCP) Ezekiel Chingoma komanso mkulu wabungwe losanthula zandale la Institute for Policy Interaction (IPI), Rafiq Hajat ati izonzosatheka. Chingoma Lachinayi adati a Malawi atopa ndiboma la DPP ndipo sadakonzeke kuti mpaka akhalebe ndinthawi yaitali asadachotse chipanicho mboma. Ndizachilendo kumva kuti masiku akufuna asinthidwe. Mwezi wa May sidziko lonse limakhala ndi nyengo yozizira. Akufuna achitenji? Ife a MCP takana zimenezo, adatero iye. Hajat adamema zipani ndi mabungwe kuti akane ganizo la MEC ponena kuti ntchito yosintha tsiku siyophweka. Popanga tsiku padali nthawi komanso mbali zonse zofunikira zimene zidapezeka kuti apange lamulo. Kutanthauza kuti pali ndime kuti tsikuli lisinthe. Komanso sindikuona kufunika kwake. Amabungwe ndi zipani akane, adatero Hajati. Koma kadaulo pa malamulo Edge Kanyongolo akuti ganizo la MEC losintha tsikuli ndilochitika. Ndizotheka palibe chovuta, adatero Kanyongolo. Chofunika nkhaniyo ipite ku Nyumba ya Malamulo kuti ikakambidwe ndi aphungu. Apo ayi, phungu wina athakukaiyambitsa kumeneko kuti aikambirane. Iye adati aka sikoyamba nkhaniyi kuchitika. Ngati sindikulakwitsa mu 1999 zotere zidachitika. Nachonso chipani cha Republican Party [RP] chidatengera MEC kubwalo lamilandu pankhani ngati yomweyi. Palibe chachilendo ndiponso palibe chosatheka. Ndizotheka ngati atafuna, adaonjeza Kanyongolo. Iye adati maiko ena amangotchu latsiku la chisankho osati mpaka kukhala ndi tsiku lenileni lochititsa chisankho. Kodi patsiku lachisankho kutachitika chivomerezi mungapite kukavota? Nchifukwa anzathu sakhala ndi tsiku lenileni, adatero iye. Mneneri wa chipani cha UDF Ken Ndanga adati sadalondoloze bwino zokambirana zomwe zimachitika pakati pa MEC ndi azipani kotero sangaike mlomo. Komabe Ndanga adati tilankhule ndi mlembi wa chipanichi Kandi Padambo amene foni yake samayankha. Nakonso ku DPP sikudachokere mawu pamene Francis Kasaila yemwe ndi wolankhulira chipanichi samayankha foni yake. Malinga ndi mkulu wamgwirizano wa mabungwe okhudzidwa ndikuyendetsa zachisankho la Malawi Electoral Support Netwrok (Mesn) Steve Duwa adati ganizo losinthalo lidadza atakambirana ndi MEC.
11
Papa Wati Chaka Chino Akacheza ku Iraq Mtsogoleri wa Mpingo wa Katolika pa dziko lonse Papa Francisko wati akacheza mdziko la Iraq chaka chino. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa Francisko walankhula izi lachitatu polandira gulu la akhristu a Katolika ochokera mdziko la Iraq kulikulu la Mpingo ku Vatican. Papa pa umodzi mwa maulendo ake a utumiki Mmawu ake, Papa Francisko wati amakhala pafupi ndi anthu a mdziko la Iraq tsiku ndi tsiku kudzera mmapemphero chifukwa cha nkhondo komanso mavuto omwe anthu mdzikolo akukumana nao ndipo wati ndicholinga chake kuti akacheza mdzikolo chaka chino. Lachitatu Papa Francisko watsimikizira gulu la akhristu a Katolika ochokera mdziko la Iraq za mapemphero ake malinga ndi nkhondo komanso mavuto osiyanasiyana omwe anthu a mdziko la Iraq akukumana nao. Iye wauzanso gulu la a Katolikawo kuti ndi cholinga chake kuti akacheza mdzikolo chaka chino. Kwa nthawi yaitali Papa Francisko wakhala akufunitsitsa kukacheza mdziko la Iraq ngakhale kuti mpaka pano likulu la Mpingo ku Vatican silidatsimikizebe za ulendowu ngati ungachitike. Mmwezi wa December mchaka cha 2018 mlembi wa mkulu wa likulu la Mpingo ku Vatican (Secretary of State), Cardinal Pietro Parolin adakacheza mdziko la Iraq. Ngati ulendo wa Papa Francisko wa mdziko la Iraq ungatheke adzakhala Papa woyamba kukacheza mdzikolo.
14
NICE Trust Ilimbikitsa za Bata Pambuyo pa Chigamulo Bungwe la National Initiative for Civic Education Nice Trust lapempha atsogoleri a zipani zandale pamodzi ndi anthu omwe amawatsatira kuti asunge bata ndi kudzavomereza chigamulo cha bwalo lamilandu pa zotsatira za mlandu wa chisankho cha mtsogoleri wa dziko lino. Mmodzi mwa akuluakulu a bungweli a Grey Kalindekafe anena izi ku Zomba pa maphunziro a tsiku limodzi olimbikitsa zamtendere omwe bungweli linakonzera mafumu, akuluakulu a zipani zandale, makhansala komanso aphungu a kunyumba ya malamulo a mboma la Zomba. Iwo ati atsogoleri a ndale ali ndi udindo wozindikiritsa anthu omwe amawatsatira za momwe zotsatira za chisankho zimakhalira ndi cholinga chakuti zotsatira zikadzabwera mosemphana ndi momwe amaganizira, pasadzakhale mchitidwe wa ziwawa. Polankhula woyimilira zipani zandale zomwe zinabwera pankumanowu mkulu wa achinyamata mu chipani cha UTM mchigawo chakummawa a Henderson Waya ati zomwe bungweli lachita pobweretsa maphunziro zithandiza anthu kukhala ndi chinthunzithunzi chabwino pa momwe angalandilire zotsatira za chisankhochi.
11
Boma latipaka mafuta pakamwa Ogwira ntchito mboma ena ati boma lawapaka mafuta pakamwa powalonjeza kuti malipiro awo akwera ndi K61 pa K100 iliyonse kuyambira mwezi wa March chifukwa malipirowo sanakwere monga boma lidalonjezera. Iwo auzaTamvanimsabatayi kuti ena malipiro awo akwera pomwe ena sadakwere. Iwo atinso ngakhale magiledi afanana koma kakwezedwe kakusiyana pomwe ena adakaphulabe njerwa zamoto. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Boma ndi anthu ogwira ntchito mbomawa adagwirizana za malipirowa mmwezi wa February chaka chino pomwe antchitowa adachita zionetsero sabata ziwiri pokakamiza boma kuti lisunthe malipiro awo. Iwo amati bomali likweze ndi K67 pa K100 iliyonse koma boma lidati likwanitsa kukweza ndi K61. Mgwirizanowo udati omwe amalandira ndalama zochepetsetsa ndiwo alandire K61 ndipo nambalayo izichepa mpaka kufika pa K5 kwa bwana kwambiri mboma. Mphunzitsi wina yemwe ali mgiledi L-4 kusukulu ina mboma la Ntcheu wati kumeneko aphunzitsi adakhalirana pansi kuti aone momwe alandirira malipiro. Amene talandira bwino ndi ife a giledi L-4. Giledi imeneyi ndiyo yotsikitsitsa kwa aphunzitsi. Malipiro athu akwera ndi K2 000 pomwe ena asintha ndi K500 ena sadawawonjezere kalikonse. Omwe talandira bwinofe ndi amene tikulimba ndi ntchito chifukwa tikutengedwa kuti tikulandira bwino kusiyana ndi anzathu. Maphunziro asokonekera kale, nthawi zonse tikungokambirana zimenezi kusiya kuphunzitsa, adatero mphunzitsiyo yemwe ankalandira K29 000. Ogwira ntchito kuchipatala akuti malipiro a ena akwera pomwe ena adakali pakale. Mu giledi yathu timalandira K26 000 koma pano ena zawayendera pomwe alandira K34 000 koma ine palibe chasintha. Tikusowa kuti tifunsa ndani, adatero wina. Malinga ndi wapolisi wina, wapolisi yemwe amalandira ndalama zotsikitsitsa ndiconstableyomwe ndi K32 000. Malinga ndi kusintha kwa malipiro maconstableena awakwezera ndi K1 000. Zikuvuta kuzimvetsa, palibe akwezapo apa chifukwa momwe zinthu zakwerelamu sangakweze malipiro ndi K1000. Moyo wamavuto ukupitiriza ndipo izi sizichepetsabe mchitidwe wa ziphuphu pakati pa apolisi, adatero wapolisiyo akuvomerezana ndi wapolisi wina yemwe amati malipiro ake sadasinthe. Koma kwa mamesenjala zinthu akuti zili bwino pomwe aona ulemerero ndi kukwera mtengo kwa malipiro awo. Ena omwe tidacheza nawo ku depatimenti yoona zolowa ndi kutuluka ya Immigration adati malipiro akwera kuchoka pa K19 000 akadulidwa msonkho kufika pa K31 000. Ayi bolani kusiyana ndi poyamba, adatero mesenjala wina akugula mandasi kumeneko. Koma mkulu wa bungwe loona ufulu wa anthu ogwira ntchito mboma la Civil Servants Trade Union (MCTU), Elijah Kamphinda Banda sadakane kapena kuvomereza za nkhaniyi ponena kuti mgwirizano omwe anthuwa ndi boma adapanga ukuwonedwabe. Bvutoli litha kukhala loona poti makonzedwe ake anali othamanga kwambiri poganizira za ntchito zomwe zidaima [pomwe timakakamiza boma kuti likweze malipiro]. Komabe pokambirana mbali zonse zidagwirizana kuti wolandira K18 000 adutse pa K29 000 ndipo izi zidachikadi. Panopa zokambirana zili mkati malingana ndi mgwirizano wa mbali ziwirizi kuti pofunuka kuthetsa zolakwika za malipirowa kuti mu July adzakhale atsopano, adatero Kamphinda. Iye adafotokozapo momwe kuwonjezerako kudachitikira. Mwachitsanzo wolandira zochepa adaonjezeredwa ndi K11 000 kutanthauza kuti mwa ndalama zimenezi K3 300 yapita ku msonkho ndipo munthuyu watsala ndi K7 700 basi. Ndi chifukwa timanena kuti ndife akapolo a msonkho. Iye adatinso bungwe lawo lidzanena chomwe lingachite ngati zokambiranazi sizingathe bwino potsindika kuti pofika July zonse zikhala zitayera. Mneneri wa boma, Moses Kunkuyu wati oimira anthu ogwira mbomawa omwe amakambirana ndi boma amayenera kufotokozera anthu awo za momwe malipirowo akhalire asadayambe kusangalala kuti malipiro akwera. Omwe amayenera kulandira K61 ndi omwe akulandira ndalama zochepetsetsa. Malipirowo amanka nasintha malinga ndi giledi yomwe munthu ali. Ngati anthu aona kuti malipiro asintha asadabwe ndizo tidagwirizana, adatero Kunkuyu. Koma pankhani yoti ena akulandira malipiro osiyana koma giledi imodzi iye adati: Imeneyo ndiye yoyenera kukhalira pansi ndikuona kuti pavuta ndi pati. Anthu omwe amaimira anthuwa bwezi atabwera ndi nkhaniyi ndikupeza pomwe padakhota kuti zotere zichitike.
11
Anatchezera: Akukana kunditsata Agogo, Ndine mnyamata wa zaka 20 ndipo ndili pachibwenzi ndi mtsikana wa zaka 22 ndipo timakondana kwambiri koma vuto ndi loti akukana kunditsata kuchipembedzo changa. Ndiye ndithetse chibwenzichi kapena ndipitirize? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu RM Zikomo RM, Choyamba ndikanakonda nditadziwa kuti cholinga cha chibwenzi chanu ndi chiyani, komabe poti ukufuna maganizo anga ndikuuza. Ndikhulupirira kuti cholinga cha chibwenzi chanu ndi kudzamanga banja mtsogolo, ngati sindikulakwa, ndipo ngati anthu muli ndi cholinga chodzakhala thupi limodzi ndi bwino kwambiri kuti muzigwirizana muzonse. Inde, pali mabanja ena oti mwamuma amapemphera mpingo wina ndipo mkazi nayenso amapita kwina, nkumakhala bwinobwino mwansangala. Koma kunena zoona mukasiyana zipembedzo pamakhalabe kenakake kosonyeza kuti pali kusagwirizana mbanjamo. Ndiye ndi bwino kugwirizana chimodzi musanalowe mbanja. Munayamba mwakhala pansi nkukambirana kuti chifukwa chake nchiyani akukanira kukutsatira kuchipembedzo chako? Nanga iweyo sungamugonjere wachikondi wakoyo kuti umutsate kumpingo kwake? Nchifukwa chake nthawi zambiri kumakhala bwino inu achinyamata mukamafuna mnzanu wachikondi muzidyerera maso kwa anyamata kapena atsikana omwe mumapemphera nawo mumpingo umodzi. Nanga chokafunira wachikondi kwina nchiyani? Ndiye wafunsa kuti kodi uthetse chibwenzichi kapena ayi? Ine ndikuti zili ndi iwe mwini mmene ukumvera mumtima mwako. Ndipange bwanji? Agogo, Ndine mnyamata wa zaka 20 ndipo ndinakwatira mwangozi nditapereka mimba kwa mtsikana wina. Ndimafuna nditapitiriza sukulu koma zikukanika chifukwa mkaziyu akukana kuti nditero. Ndipange bwanji? JK Zikomo JK, Ndakhala ndikulangiza anyamata ndi atsikana ambiri kuti mfulumiza adadya gaga, lero si izi waziona, mwana wanga? Ndakondwa kuti waona wekha kufunika kwa sukulu ndi kuipa koyamba kugonana ndi atsikana, komanso mosadziteteza, udakali pasukulu. Udakali msinkhu wopita kusukulu ndipo ndi bwino kwambiri utatero. Ngati mkazi wakoyo umamukonda ndipo iyenso amakukonda chimodzimodzi, ayenera kumvetsa cholinga chako choti upitirize maphunziro ako kuti kutsogolo mudzakhale moyo wabwino, wodzidalira nokha, osati mmene zilili panopa chifukwa mmene ndikuonera banja lanu lidalira makolo-chakudya, zovala, sopo amene ndi zina zotere. Umutsimikizire mkaziyo kuti kupitiriza sukulu sikutanthauza kuti banja lanu latha, koma kuti ukuganiza za tsogolo lanu ngati banja. Umuuze kuti sukulu simatha-akuluakulu amene mukuwaona mmaofesiwa ambiri afika pamene ali chifukwa chopitiriza sukulu ali mbanjabe. Tsono chovuta kuti iwe upitirize sukulu nchiyani? Ngati iye safuna sukulu, zake izo, iwe chita zomwe ukufuna. Ndikhulupirira ngakhale makolo ako adzasangalala kwambiri kumva kuti ukufuna kupitiriza sukulu. Ndinalapa Anatchereza, Ndinali mchikondi kwambiri ndi mwamuna wa kwa Jali koma atandipatsa pathupi samandiuza nzeru iliyonse yothandiza pa umoyo wa mwana wodzabadwayo, mapeto ake anandipatsa ndalama zokachotsera pathupipo kuchipatala. Zotsatira zake ndinadwala kwambiri koma nditapeza bwino anayamba kundipepesa koma ine ndinamenyetsa nkhwanga pamwala kuti sindidzayambiranso. Kodi mwamuna wotsogolera zolakwa ndi wabwino? Koma ineyo ndinalapa, amama, ndipo ndinasiyana naye. ML Zikomo ML, Ine ambiri ndilibe koma ndingoti khokhokho! Kumeneko ndiye timati kukula. Akulu akale adati mmphechepeche mwa njovu sadutsamo kawiri. Munthu ukachimwa ndi bwino kulapa monga wachitira iweyomu. Ndithudi mwamunayo sadakufunire zabwino ndipo chikondi chake chidali cha chiphamaso, basi; amangofuna zogonana koma osalabadira za zotsatira zake. Wachita bwino kumusiya ameneyo ndipo yamba moyo wina watsopano. Mwamuna wina akakufunsira mulole, koma osamulola kuti muyambe mwagonana musanalowe mbanja. Amuna ambiri akangowavulira musanalowe mbanja, sakhalanso ndi chidwi chifukwa amati ngati wandilola, nkutheka kuti adalolanso amuna ena.
12
Muva: Kutsitsimutsa anthu mukuimba Lero Lamulungu akuyembekezeka kukakhazikitsa chimbale chake cha Messiah 1 ku Mzuzu pa Boma Park. Kumeneko kukakhala oimba osiyanasiyana odziwika mMalawi muno. DAILES BANDA adacheza ndi Donnex Muva kuti amudziwitsitse mkuluyu, yemwe akuti cholinga chake nkutsitsimutsa anthu kudzera mu nyimbo. Adacheza naye motere: Akhazikitsa chimbale chake lero: Muva Tikudziweni achimwene. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndine Donnex Muva ndipo ndimachokera mmudzi mwa Kajani kwa Inkosi Kampingo Sibande mboma la Mzimba. Ndili ndi zaka 32 zakubadwa, ndili pabanja ndipo ndili ndi ana atatu. Mbiri ya maphunziro anu njotani? Ndayenda sukulu zambiri kaamba ka bambo anga omwe ndi abusa, koma mayeso anga a Sitandade 8 ndidalembera ku Chihami mboma la Nkhata Bay ndipo sekondale ndidaphunzira ku Chintheche mboma lomwelo. Nditamaliza sekondale ndidachita mwayi woyamba ntchito ku Chipiku koma pakadalipano ndikugwira ntchito kubungwe la Solar Aid Malawi. Mudayamba bwanji kuimba? Kuimba ndidayamba ndili wachichepere kwambiri, makamaka kaamba ka ubusa wa bambo anga. Panthawiyo ndinkaimba mukwaya ya kumpingo kwathu. Kuimba kwenikweni ndidayamba mchaka cha 2009 pomwe ndidatulutsa chimbale choti Nthawi ya Manna Inatha. Chaka chino ndikuyembekezeka kukakhazikitsa chimbale changa cha Messiah 1 ku Mzuzu ku Boma park pa 30 August. Kumeneko kukhalanso oimba osiyanasiyana odziwika mMalawi muno. Zomwe mwakwaniritsa pamoyo wanu ndi ziti? Chachikulu chomwe ndakwaniritsa ndi kubweretsa anthu kwa Mulungu kudzera mu nyimbo komanso kukhala ndi zimbale ziwiri si chinthu chapafupi chifukwa kupanga chimbale pamalowa ndalama zambiri. Pali zopinga zotani zomwe mwakumanapo nazo? Zopinga ndiye zilipo, choyamba ndi mchitidwe woba nyimbo moti ndikunena pano anthu ayamba kale kubena nyimbo zanga. Mchitidwewu umabwezeretsa kwambiri mmbuyo anthu oimbafe. Chachiwiri ndi kusowa kwa chithandizo popanga chimbale. Monga ndanena kale, ndalama zimalowa zambiri pantchito yapanga chimbale, zomwe oimba ambiri sitingakwanitse patokha ndipo timafuna chithandizo kuchokera kwa makampani akuluakulu monga zimakhalira kumaiko ena. Oimba anzanu muwauza zotani? Pakhale chikondi pakati pathu osati kuponderezana. Ndi mtima wofuna kukhala pamwamba nthawi zonse womwe ukuononga oimba ambiri mdziko muno.
9
Kusolola mboma kudayamba kale Ingakhale sukulu iyi? Chitukuko kumidzi chikulephera kupita patsogolo chifukwa ena akuba ndalama za boma Zayamba kuululika. Kafukukufuku yemwe adapangidwa pakati pa 2009 ndi 2012 waulula kuti boma lotsogozedwa ndi chipani cha DPP, chomwe mtsogoleri wake adali Bingu wa Mutharika, lidasowetsa ndalama zoposa K90 biliyoni mnjira zopanda dongosolo. Kafukufuku wowunika njira yoyendetsera chuma cha boma ya Integrated Financial Management and Information System (Ifmis) yemwe ofesi yolondoloza chuma cha boma ya National Audit Office (NAO) idachita mwezi wa November 2011 kufikira 2012, wasonyeza kuti kusololaku kudayamba kale, makamaka muulamuliro wa demokalase. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Zotsatira za kafukufukuyu zikusonyeza kuti boma la DPP lidasokoneza ndalama zankhanikhani mnjira zosiyanasiyana makamaka kugula katundu wa boma popanda dongosolo komanso kulipira makampani omwe sadagwire ntchito iliyonse. Kafukufukuyu wasonyezanso kuti kusololaku sikudaonekere poyera msanga kaamba koti boma la DPP lidayimika kafukufuku yemwe unduna wa zachuma udakhazikitsa utakayikira chinyengo ndi njira ya Ifmis. Boma la DPP lidaimika kafukufukuyu nthambi 14 za boma zisadaunikidwe, zomwe zidachititsa kuti chinyengo cha kunthambizi chisaonekere poyera. Ofesi ya NAO idakanika kufufuza ofesi ya mtsogoleri ndi nduna zake chifukwa ochita kafukufukuwo adabwezedwa, pomwe unduna wa zachuma sudafufuzidwe chifukwa adakonza kuti udzakhale womalizira kufufuzidwa ndipo nthambi zina 12 sizidafufuzidwe chifukwa cha mavuto a ndalama zogwirira ntchitoyi. Kumapeto kwa chaka cha 2011, kafukufukuyu ali mkati, kalaliki wogwira ntchito ku ofesi ya mkulu wowerengera ndalama za boma adapezeka ndi ndalama zokwana K400 miliyoni kubanki. Panopa kukankhizirana kuli mkati pakati pa chipani cha DPP ndi chipani cholamula cha PP pankhani yosakaza chuma cha boma yomwe aphungu akukambirana ku Nyumba ya Malamulo. Koma anthu ndi katswiri wina wa zachuma mdziko muno ati mfundo za otsutsa boma mNyumba ya Malamulo pankhani yokhudza ndalama zomwe zidabedwa kulikulu la boma ku Lilongwe zingathandize kupeza anthu omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi. Anthuwa ati nzomvetsa chisoni kuti kafukufukuyu wakhwimitsidwa kwambiri kwa makalaliki ndi anthu amaudindo angonoangono mboma kulikululi pomwe pali malipoti ena osatsimikizidwa oti akuluakulu ena akukhudzidwa ndi kusokonekera kwa chumachi. Tikukamba pano, bungwe lothana ndi katangale ndi ziphuphu la Anti-Corruotion Bureau (ACB) lamangapo kale mkulu woyendetsa unduna wa zokopa alendo ndi zankhalango Tressa Namathanga Senzani. Iyeyu akumuganizira kuti adalamula unduna wake kuti ulipire kampani yake yotchedwa Visual Impact ndalama zankhaninkhani chikhalirecho kampaniyo sidagwire ntchito yotumidwa ndi boma. Otsutsa boma aganiza bwino kwambiri pamenepa polimbikitsa kuti akuluakulu a mboma afufuzidwenso pankhaniyi osati azibisala kumbuyo kwa mipando yawo ayi. Nthambi zomwe zikufufuza nkhaniyi zimve mawu amenewa ndipo zichitepo kanthu, Joana Nkhwazi, mphunzitsi pasukulu ya pulaimale ya Kaufulu mumzinda wa Lilongwe, wauza Tamvani. Naye Martin Mpiringidza, yemwe amayendetsa lole yonyamula katundu mumzindawu, adati kufufuzako kusangothera pa ogwira ntchito mboma koma kuchitikenso ndi makampani omwe akuganiziridwa kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyi. Mpiringidza adanena izi potsatira zomwe adanena mtsogoleri wa chipani cha DPP mNyumba ya Malamulo, George Chaponda, kuti makampani oterewa eni ake ndi akuluakulu a boma omwe amatumiza ndalama zambiri kumakampaniwa ngati akulipira ndalama za katundu yemwe sadaperekedwe nkomwe. Mabvuto Bamusi, yemwe amalondoloza bwino nkhani za chuma ndi zaumoyo, wayamikira zipani zotsutsazi polimbikitsa kuti kafukufukuyu afikenso kumabanki komwe ndalamazi zimalowera ndi kutulukira. Otsutsa anena zanzeru kwambiri chifukwa mulimonse mmene kafukufukuyu angathere, ndalama zosowazo zimalowera ndi kutulukira kumabanki ndiye nkutheka kuti mmabankimo muli anthu ena omwe akukhudzidwa ofunika kufufuzidwa, watero Bamusi. Zipani zotsutsa zidadandaula kuti boma silidauze Nyumba ya Malamulo mfundo zogwira mtima Lolemba pomwe wachiwiri kwa pulezidenti wa dziko lino Khumbo Kachali amatsegulira msonkhano wadzidzidzi wa aphungu womwe cholinga chake ndi kukambirana za ndalama zobedwazo ndi nkhani zina zikuluzikulu. John Tembo wa MCP, Clement Chiwaya wa UDF ndi George Chaponda wa DPP, ati boma lidangobwereza zomwe anthu ndi aphungu amadziwa kale mmalo monena mfundo za momwe boma likuyendetsera nkhaniyi. Tembo, yemweso ndi mtsogoleli wa zipani zotsutsa boma mNyumba ya Malamulo, adati zipani zotsutsa zimayembekeza kuti boma lilongosola bwino chifukwa chenicheni chomwe mtsogoleri wa dziko lino adachotsera nduna zake zonse pa October 10 ndiponso chomwe nduna zina zikuluzikulu sadazibwezere pamaudindo awo potsatira nkhaniyi. Nkhani imeneyi itangochitika mtsogoleri wa dziko adachotsa pamipando nduna zonse ndipo posankha nduna zatsopano nduna zina adazibwezera mmipando yawo koma nduna zina zikuluzikulu ngati Ken Lipenga ndi Ralph Kasambara adazichotseratu pamipando yawo. Izi zikutanthauzanji, chifukwa ndi zinthu zomwe Amalawi amayembekezera kumva kuchokera kuboma, osati kubwereza zinthu zomwe anthu akudziwa kale, adatero Tembo. Lipenga adali nduna ya zachuma, unduna womwe ukukhudzidwa kwambiri ndi chisokonezochi, ndipo katswiri wa zachuma Maxwell Mkwezalamba ndiye watenga mpandowu. Mpando wa nduna ya zachilungamo ndi malamulo womwe udali wa Kasambara, waperekedwa kwa katswiri wa zamalamulo Fahad Assani.
2
Trump Wayamba Kuthothola Akazitape Mtsogoleri wa dziko la America, Donald Trump wachota mmaudindo akuluakulu ena a mboma kaamba koti amachitira umboni oti iye achotsedwe pa u president. Wathamangitsa ena mwa ogwira ntchito mboma-Trump Malipoti a wailesi ya BBC ati kazembe wa dzikolo ku bungwe la European Union, Gordon Sondland wauzidwa kuti achoke ku bungwelo. Ndipo Leftenant Colonel Alexander Vindman mmodzi mwa alangizi ake pa za ubale wa dzikolo ndi Ukraine wayimitsidwanso ntchito. Malipoti akusonyeza kuti President Trump akuyembekezeka kuchotsa ntchito anthu ena, pamene akuluakulu adzikolo lachitatu lapitali alengeza kuti president Trump sakuyenera kuchotsedwa pa udindowu. Anthu ena mdzikolo kuphatikizapo aphungu akunyumba ya malamulo anavomereza kuti President Trump achotsedwe pa udindo wake kutsatira nkhani zokhudza ubale wake ndi dziko la Ukraine.
11
Eni Minibus Ati Ali ndi Ufulu Wokweza Mitengo Mmodzi mwa anthu amene amatsatira bwino nkhani za pa nsewu mdziko muno, Coxley Kamange wati unduna wa za mtengamtenga ukuyenera kutsatira njira zabwino pofuna kukamiza eni minibus kuti atsitse mitengo yokwelera minibus mdziko muno kaamba ka kutsika kwa mafuta a galimoto. Kamange: Tili ndi ufulu wokwezabe A Kamange anena izi pamene amathilira ndemanga pa chikalata chomwe undunawu unatulutsa chonena kuti kuyambira pa 15 June, undunawu uyamba kugwira ma minibus onse omwe sakutsitsa mitengo yawo chifukwa zikuphinja ufulu wa anthu okwera, mu nyengo ino ya Coronavirus. Iwo ati minibus kuti iyende sifuna mafuta okha komanso pali zinthu zina zofunika monga ishulansi choncho ndi kwabwino kuti undunawu uwunikenso mitengo yolipilira ishulansi maka mu nyengo ino yomwe dziko lino laphinjika ndi mliri wa Coronavirus. Ngakhale mitengo ya mafuta yatsika tili ndi ufulube opitiriza kugwiritsa ntchito mitengo yokwera chifukwa minibus simayendera mafuta okha komanso minibus yoti imanyamula anthu 16 ikunyamula 8, pa anthu 8pa sakutichoseranso inshulansi, anatero a Kamange. Iwo apempha boma kuti likambirane ndi makampani a ishuransi kuti litsitse mitengo ya misonkho mu nyengo ya COVID-19. Padakalipano unduna wa za mtengatenga ndi zomangamanga sunayankhepo kanthu pa nkhaniyi.
17
Mwambo woliza mfuti pamaliro Achingoni Mfumu Yachingoni ikagona, pamaliropo amaomba mfuti thupi la mfumuyo lilowe mmanda. Mwezi wathawu, kudachitika maliro a T/A Bvumbwe mboma la Thyolo. ku malirokonso kudalizidwa mfuti, chomwe anthu ena amene adali kumwambowo adadabwa nacho. BOBBY KABANGO adacheza ndi mkulu amene amaomba mfutiyo kuti amve zambiri za mwambowu motere: Wawa Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Fikani ndithu musaope. Ndikudziweni bwanji? Choyamba dzina langa ndine Moses Chikoko. Mungandidziwe monga mbali ya mbumba kwa T/A Bvumbwe. Ngati mudamvapo za Gomani Chikuse amene adadulidwa khosi, ameneyo ndiye adabereka mayi anga. Mkazi wachinayi wa Gomani Chikuse ndi amene adabereka mayi angawo. Ndiye mudapezeka bwanji kuti mukukhala ku Thyolo kuno? Pajatu Angoni adali ankhondo, ndiye gulu la mayi anga ndi lomwe lidabwera kuno pamene Angoni ena ankafikira madera ena. Mayi anga adali wa mtundu wa Maseko koma bambo anga adali a kwa Mulauzi. T/A Bvumbwe wagonayu adali ndani wanu? Wagonayu ndi mwana wanga, koma sindikutanthauza kuti ine ndi amene ndidabereka iyeyu, koma kuti bambo ake adayenda limodzi ndi ine kusukulu, amenewo adali a Steven Bvumbwe. Mfuti mwatengayi mufuna mugwiritsire ntchito yanji? Ngati mukumva kulira mfuti pamalo pano ndikuliza ndineyo, ntchito yake nkuti ilire pamene tikugoneka mfumu yathu. Dziwani kuti pamaliro a mfumu Yachingoni pamalira mfuti mpaka mfumuyo itatsikira mmanda. Mumaliza kangati? Mfuti imalira kanayi. Koyamba imalira kusonyeza kuti mfumu yamwalira. Apa amakhala kuti amene alowe mmalo mwake wabwera kudzaona nkhope ndi kutsimikizadi kuti mfumuyo yamwalira. Imalira kachiwiri pamene tikutulutsa thupi la mfumuyo mnyumba. Timalizanso kachitatu pamene tanyamula thupi ulendo kumanda. Pamenepa timaomba kusonyeza kuti akutsanzika. Timadzaombanso komaliza pamene bokosi latsitsiridwa mmanda kusonyeza kuti wafika. Chifukwa chiyani mumaomba mfuti? Kusonyeza kuti Mngoni ndi wankhondo. Ndiye ngati Mngoni, yemwe timamudziwa bwino kuti ndi wankhondo, wamwalira zotere zimayenera zichitike. Bvumbwe adamenya kuti nkhondo yake? Bvumbwe adali Mngoni ndipo Angoni amadziwika kuti ndi ankhondo ngakhale sadamenye nkhondoyo. Sindingakuyankheni kuti adamenya kuti koma dziwani kuti Bvumbwe adali Mngoni yemwe ndi wankhondo. Nkhondo yake iti kodi? Mukudziwa kuti Angoni adachita kumenya nkhondo mpaka kudutsa ku Domwe. Akafika pamalo amayamba amenya nkhondo ndi kukhazikika bwino. Nkhondo yake ndi imeneyo. Kodi ndimayesa nkhondoyo idatha kalekale? Nanga inu mukuchitabe izi bwanji? Eya, koma nkhondo yathu ndi ya mmagazi, kusonyeza kuti simatha. Mwambo umenewu udayamba kalekale ndi makolo athuwo. Mfuti zisadayambe kupangidwa mumaliza chiyani? Aaah, mwaiwala? Kudali mfuti zagogodera zomwe tinkagwiritsa ntchito nthawi ngati ino. Mwapeza bwanji chilolezo choliza mfuti? Choyamba dziwani kuti ndine msirikali, mfuti ndimaidziwa chifukwa cha ntchito. Ndilinso ndi mfuti komanso ndidali Wapayoniya. Ndiye mnyumba mwanga mfuti si yachilendo. Anthu enatu amadzidzimuka, mumakhala ndi chilolezo kuti muombe mfuti? Nchifukwa chake mwandiona kuti ndakhala kutchire ndekhandekha podziwa kuti pali anthu odwala mtima amene angathe kukomoka mfuti ikalira. Ndiyetu tailozetsani kumbali kuopa kuti chipolopolo chingafwanthuke Ndikudziwa chomwe ndikuchita, apapa olo zitachita kuvuta kotani singalire.
1
Chikondwerero cha Amalitiri aku Uganda Chayimitsidwa Chikondwelero cha chaka chino cha Amalitiri a ku Uganda ati sichichitika mwansanga monga momwe zimakhalira zaka zonse mdzikomo. Izi zili chomwechi kaamba ka ziletso zomwe boma la dzikolo lidayika poletsa mikumano ya anthu ochuluka komanso maulendo a pa ndenge ndi a pamadzi ngati mbali imodzi yoteteza kufala kwa kachilombo ka Coronavirus. Chikondwelero cha Amalitiri aku Uganda cha zaka zammbuyomu Malinga ndi chikalata chomwe likulu lampingo wadzikolo yatulusa yati kukonzekera chikondwererocho kumafunika kukumana ndi anthu ochuluka pafupi pafupi. Kutha kukhala kovuta kuyamba kukonzekera mwambowu lero lino kamba koti nthawi ndi yochepa, chatero chikalatachi. Abwenzi a Amalitiri aku Uganda ku Malawi ati achita chikondwelero chawo mdziko mommuno Malinga ndi mlembi ofalitsa nkhani mu bungwe abwenzi a Amalitiri aku Uganda kuno ku Malawi a Isaac Mphweya, iwo achita chikondwelerochi mdziko momwe muno zones zikayenda bwino. Izi zatikhumudwitsa kwambiri kamba koti abwenzi ambiri anakonzekera ulendowu koma tamvetsetsa kamba ka vutoli ndipo ife kuno ku Malawi tizakondwerera konkuno pa 4 October ku Bvumbwe Parish mu arkidayosizi ya Blantyre, anatero aMphweya.
13
Awiri Afa Pochokera Ku Interview Ya Zaumoyo Anthu awiri afa ndipo mmodzi wavulala modetsa nkhawa njinga ya moto yomwe anakwera itaphonya msewu ndi kukagwera ku phompho ku Changalume Barracks mboma la la Zomba. Omwalirawo anali gulu limodzi ndi awa-Achinyamata osaka ntchito mMalawi Malingana ndi mmodzi mwa anthu okhudzidwa ndi ngoziyi mayi Sellina Bomani omwe ndi mkulu wa bungwe la Tikondane Positive Living Support Organisation (TIPOLISO) mbomalo, mmodzi mwa anthu omwe afa pa ngoziyi ndi yemwe amayendetsa ndi njingayi Benson Machira, ndipo winayi ndi Mirriam Ganizani mmodzi mwa atsikana awiri omwe anakwera njingayi, ndipo amene wavulala pa ngoziyi ndi Ellen Samson. Mayi Bomani atsikana awiriwa akuti amachokera kochita mayeso olowera ntchito (interview) omwe a ku unduna wa za umoyo amachititsa ku malo a sukulu ya sekondale ya Zomba Urban mbomalo.
14
Papa Wayamikira Mabungwe Red Cross, Red Cresent Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wayamikira bungwe la Red Cross komanso Red Crescent chifukwa cha ntchito yotamandika yomwe mabungwewa amagwira. Papa Francisco walankhula izi lachisanu pa Misa yomwe anatsogolera kulikulu la Mpingo ku Vatican. Iye wayamika mabungwe awiriwa chifukwa chothandiza anthu pa nthawi ya mavuto osiyana-siyana. Papa wati Mulungu awatsitsire mabungwe amenewa madalitso chifukwa chogwira ntchito mwa toto moyo komanso walimbikitsa anthu kuti akhulupirire Mulungu popeza amakhala nawo pamene ali mmavuto.
6
Mavolontiya Achita Mbindikiro wa Advent Anthu omwe amatumikira ku Radio Maria Malawi ati akuyenera kuzindikira ubwino wokhala moyo wodziyeretsa ndi cholinga choti azipindula ndi uthenga wachipulumutso umene amafalitsa kudzera pa wailesiyi. Mavolontiya kumvetsera maphunzitso a bambo Chimbalanga Bambo mfumu a parish ya utale II mu dayosizi ya Mangochi bambo Saulos Chimbalanga anena izi loweruka mboma la Balaka pambuyo pa mbindikiro wa otumikira omwe amatumikira wailesiyi mzigawo zonse za dziko lino. Iwo ati ngati atumiki a mthenga wabwino akuyenera kuti azikhala oyambilira popindula ndi uthenga wabwino umene amafalitsa. Mavolontiya ali ndi udindo waukulu wofalitsa uthenga wa Mulungu yemwe ndi Oyera choncho nawonso akhale oyeretsedwa, anatero bambo Chimbalanga. Polankhulapo bambo Joseph Kimu a Director a wailesiyi ati ndi okondwa ndi momwe mbindikirowu wayendera. Atilimbikitsa kukonda kupemphera komanso kuti tizichita zomwe timawauza anthu kuti achite, anatero bambo Kimu. Mbindikirowu unayitanitsa mavolontiya onse a wailesiyi ku ntambi zake zonse zisanu ndi imodzi za mdziko muno.
13
Zipani zakonzeka kusankha makomishona Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wauza zipani za ndale komanso nthambi yoyanganira ogwira ntchito makhoti (Judicial Service Commission) kuti apereke maina a omwe akuona kuti akhonza kukhala makomishona a bungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) komanso wapampando wake. Izi zikutsatira kutula pansi mpando kwa yemwe adali wapampando wa bungwe la MEC Jane Ansah komanso polingalira kuti mphamvu za makomishona ena onse zikutha pa 5 June 2020. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Adalembera zipani: Mutharika Malingana ndi mneneri wa Mutharika, Mgeme Kalilani, mtsogoleri wa dziko linoyo wapanga izi pofuna kuti kubungwe la MEC kusakhale mphako mphamvu za makomishona enawo zikatha. Apulezidenti sadapereka nthawi yeniyeni yoti mainawo abwere koma polingalira kuti tikuthamangitsana ndi nthawi yachisankho cha Pulezidenti, tikuyembekeza kuti zipani komanso amakhoti apereka msanga mainawo, adatero Kalilani. Malingana ndi malamulo, wapampando wa MEC amasankhidwa ndi komiti ya makhotiyo ndipo mneneri wa nthambi ya makhoti Agness Patemba watsimikiza zoti nthambiyo yalandira kalata youzidwa kuti ipereke dzina. Kalata yatipeza ndipo komiti ya makhoti ikumana kuti iunike momwe zikhalire koma zikhala zachangu potengera kuti makomishona afunika pachisankho chikudzachi, adatero Patemba. Khothi lidagamula pa 3 February 2020 kuti chisankho cha Pulezidenti chichitikenso potsatira umboni omwe udaperekedwa pamlandu woti chisankhocho sichidayende bwino. Saulos Chilima wa UTM Party ndi Lazarus Chakwera wa MCP ndiwo adakasuma kuti bungwe la MEC lidasokoneza chisankho cha pa 21 May 2019 litalengeza kuti Peter Mutharika wa DPP ndiye adapambana. Khothilo lidaperekanso mphamvu ku Nyumba ya Malamulo kuti iunike makomishona ngati ali nkuthekera kopitiriza ntchito koma nyumbayo idapeza kuti makomishona onse adalakwa pantchito yawo ndipo idawunikira kuti achoke pabwere ena. Katswiri pa ndale George Phiri wati Mutharika wapanga bwino kupereka mpata kuzipani kuti zipereke maina a makomishona koma wati naye apange machawi akalandira mainawo. Iye wati uwu ukhonzanso kukhala mwayi poti aphungu a Nyumba ya Malamulo akhala akukumana posachedwa ndiye zikhonza kuchita ubwino kuti makomishonawo akawakambiranetu ku nyumbayo. Ngati zangochitika, zakhala bwino chifukwa zipani zikapereka maina pulezidenti nkuvomereza, Nyumba ya Malamulo ikhala ndi mpata owakambirana isadayalule. Tipha mbalame zingapo ndi mwala umodzi, adatero Phiri. Malamulo a zachisankho a 2018 amalola zipani zomwe zili ndi aphungu 10 mwa 100 aliwonse kutanthauza kuti pafupifupi aphungu 19 kupita mtsogolo mnyumbayo kupeleka maina a makomishona. Apa zikusonyeza kuti mnyumbayo, zipani za DPP ndi MCP ndizo zili nkutuekera kopeleka maina a makomishona a MEC. Mneneri wa DPP Nicholas Dausi watsimikiza kuti chipanicho chalandira kalata youzidwa kuti chipereke maina a makomishona atsopano. Talandira ndipo tipanga momwe a pulezidenti anenera. Tisankha anthu angapo nkuwaunika kenako nkusankhapo maina omwe akufunikawo nkupeleka, adatero Dausi. Mneneri wachipani cha MCP Maurice Munthali wati chipani cha MCP chidakonzeka kalekale kusankha makomishona atsopano chifukwa icho chimakanitsitsa kuti makomishona akalewa adzayendetsenso chisankho. Tipereka maina mosavuta chifukwa nzomwe takhala tikuyembekeza nthawi yonseyi, adatero Munthali.
11
Papa Wachenjeza Ogulitsa Nyuzipepala Mmisewu pa Nkhani ya Mliri wa Coronavirus Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wachenjedza anthu omwe amagulitsa nyuzipepala mmisewu kuti adzichita malondawa mosamala pofuna kupewa kutenga kachilombo ka Coronavirus. Papa Francisko Papa Francisco walankhula izi kudzera mu uthenga umene watumizira anthuwa. Iye wati akudziwa bwino momwe mliri wa Coronavirus wakhudzira ntchito za ogulitsa nyuzipepalawa mmalo osiyanasiyana pa dziko lonse. Mwazina mu uthengawo mtsogoleri wa mpingo wa katolikayu Papa Franciso wayamikira anthuwa chifukwa chothandiza pa ntchito zofalitsa mauthenga osiyanasiyana omwe akuchitika pa dzikoli.
6
Tetezani ana ku BP Chimodzimodzi akulu, ana nawo amakhala pachiopsezo cha matenda othamanga magazi choncho makolo akuyenera kuwateteza, watero mkulu wa pa chipatala cha Moyowathanzi mboma la Lilongwe Henry Ndhlovu akuti. Iye adafotokoza kuti ana omwe amakhala pa chiopsezo chodzadwala matendawa mtsogolo ndi oyambira zaka zitatu kulekezera 6 kapena 8. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kawirikawiri ana oterewa amakhala omwe adabadwa masiku asadakwane komanso ndi sikero yotsika. Matenda a imphyo ndi a mu mtima amakolezeranso vutoli ku ana, iye adatero. Masewero olimbitsa thupi ndi ofunika kwa ana Kwa ana omwe abadwa opanda mavutowa, Ndhlovu adati zinthu monga kunenepa kwambiri, kudya zakudya za mafuta, mchere ndi shuga wambiri kumaika ana pachiopsezo chodzadwala matendawa mtsogolo. Mkuluyu adaonjeza kuti kusachita masewero olimbitsa thupi ndi gwero lina la matenda othamanga magazi ku ana. Ana omwe adabadwa ndi mavuto ena mu impso kapena mtima, masiku awo asadakwane kapena ndi sikero yochepa, ziwalo zawo sidzigwira ntchito moyenera. Zotsatira zake, magazi sayenda bwino monga momwe amayenera kuchitira, iye adatero. Mkuluyu adafotokoza kuti makolo akuyenera kutenga gawo lalikulu mwachitsanzo kupewa zinthu zomwe zikhoza kuchititsa kuti mwana abadwe ndi mavutowa. Kuonjezera apo, iye adati makolo apewe kuwapatsa ana chakudya chokhala ndi shuga, mchere ndi mafuta ochuluka. Aziwalimbikitsa ana awo kuchita masewero olimbitsa thupi komanso azikawayezetsa matendawa, adakwangula motero.
6
Kwelepeta Adandaula ndi Kuchuka kwa Atsikana Osiya Sukulu Wolemba: Sylvester Kasitomu Wachiwiri kwa nduna yowoona zoti pasakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo, ana komanso olumala mayi, Grace Kwelepeta lolemba adandaula kaamba ka mchitidwe wosiyira sukulu panjira kwa atsikana ambiri mdziko muno. Mai Kwelepeta ayankhula izi pa mwambo wopereka njinga kwa Ophunzira pa sukulu ya secondary yoyendera ya Katsonga mboma la Zomba zomwe bungwe la World Bicycles Relief lapereka kwa ophunzirawa. Kwelepeta: Zimabwezera mbuyo chitukuko cha dziko Mwazina mayi Kwelepeta ayamika bungwe la World Bicycles Relief kaamba kopereka njingazi kwa ophunzirawa zomwe zithandize kuti ophunzirawa asamasiyire school panjira kaamba koyenda mtunda wautali kupita ku sukulu. Ndithokoze bungwe la World Bicycles Relief kaamba kopereka njingazi kwa ophunzirawa ndipezerepo mwayi olimbikitsa atsikana kuti apewe mchitidwe olekera sukulu panjira poti izi zimasokoneza chitukuko cha dziko, anatero mayi Kwelepeta. Polankhulapo pambuyo polandira njingazi mmodzi mwa ophunzira pasukuluwa Olive Meja wayamikira bungweli kaamba ka thandizo la njindazi kaamba koti izi zichititsa kuti ophunzira omwe amachokera madera akutali ndi sukulu kuti azifika nsanga. Kawiwrikawiri ndimakonda kuchedwa kusukulu kaamba koti ndimayenda ntunda wautali zomwe zimandipangitsa kugona nthawi yophunzira koma kutsatira kupatsidwa njingayi ndiyesa kufulumira kusukulu kuti ndizakhoze bwino mayeso anga, anatero Olive.
3
Ayamikira Chakwera Ponena Kuti Adzikayankha Mafunso ku Nyumba Ya Malamulo Mmodzi mwa akatswiri pa nkhani za ndale mdziko muno George Phiri wayamikira ganizo la mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera loti adzipita kunyumba ya malamulo kukayankha mafunso kuchokera kwa aphungu a kunyumba ya malamulo. A Phiri omwe ndi mphunzitsi wa phunziro la za ndale ku University ya Livingstonia wauza Radio Maria Malawi kuti ganizoli ndi labwino kwambiri ndipo lingathandize mtsogoleriyu kudziwa za mavuto omwe anthu ake akukumanan nawo. Phiri wati President adalembedwa ntchito ndi Amalawi choncho ndi kofunika kuti adzikayankha mafunso kunyumba yamalamulo chifukwa ndi mbali imodzi mwa ntchito yomwe adalembedwera. Mtsogoleri ndi wantchito wathu osati olamulira-Phiri Katswiriyu wati anthu akuyenera kuti achotse maganizo akuti mtsogoleri ndi olamulira ndipo akuyenera kudziwa kuti mtsogoleri ndi munthu amene amalembedwa ntchito ndi anthu ndipo akuyenera kuwatumikira moyenera. Iye wati pali zinthu zambiri zomwe anthu akuyenera kudziwa kuchoka kwa mtsogoleri wawo. Pankhani yakuti President adzikhalanso ndi nthawi yokumana ndi mtsogoleri wotsutsa boma kunyumba ya malamulo phiri wati ndi zinthu zabwino kwambiri ponena kuti kutsutsa boma sikutanthauza kufuna kugwetsa boma koma kuti kukonza zinthu zomwe zikuwonongeka. Katswiriyu wayamikiranso zomwe anayankhula mtsogoleri wa dziko linoyu kuti munthu ayenera kugwira ntchito molimbika kuti adzilipidwa ndalama osati kulipidwa kaamba kowomba mmanja kapena kuyimba nyimbo pa misonkhano ya chipani. Iwo ati ndi koyenera kuti anthu akhale olimbika pa ntchito komanso business zomwe akuchita ponena kuti zimenezi ndi zothandiza pokweza chitukuko cha dziko lino. Anthu ambiri mdziko muno ayamikira zomwe anayankhula Dr. Chakwera pomwe amalandira lupanga la nkhondo losonyeza ukulu wa asilikali a nkhondo mdziko muno pomwenso dziko lino limakondwelera zaka 56 za ufulu odzilamulira.
11
Sister Adora Magaleta Likwethu Alowa Mmanda By Glory Kondowe Thupi la Sister Adora Magaleta Likwethu a chipani cha atumiki a Maria Virgo Oyera cha Servants of the Blessed Virgin Mary (SBVM) lalowa mmanda ku Mary-View ku Nguludi mboma la Chiradzulu. Amwalira ali ndi zaka 95-Sister Adora Likwethu Malingana ndi mlembi wa mkulu mu chipanichi Sister Georgina Kapangwa wati Sister Adora anamwalira loweruka pa 15th June 2019 ku nyumba yosungira asisitere achikulire ndi odwala ya Mary View ku Nguludi mbomalo. Malemu sister Adora anabadwa pa 5 June mchaka cha 1924, mmudzi mwa Nachamba mdera la mfumu yayikulu Machinjiri mboma la Blantyre. Iwo amwalira ali ndi zaka 95 zakubadwa komanso 75 zotumikira mu chipani cha asistere cha SBVM. Pa mwambo woyika malemuwa, ambuye Thomas Luke Msusa a mu arkidayoyosizi ya Blantyre omwe anatsogolera mwambowu apempha akhristu ndi abale a atumiki a mu mpingo kuti azikhala ndi chidwi chothandiza atumikiwa adakali moyo komanso kusamalira manda awo akamwalira.
14
Nsewu wa Kachulu Uyamba Ndondomeko Yachuma Ikadutsa Botomani Boma latsimikizira anthu a mdera la Zomba Chisi kuti nsewu wopita ku Kachulu ku Nyanja ya Chilwa uyikidwa phula mu ndondmeko yaza chuma yomwe ikubwerayi chaka chino. Botomani: Nduna ya zachuma yanditsimikizira Nduna ya zofalitsa nkhani a Mark Botomani ndi omwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi. A Botomani omwenso ndi phungu wa kunyumba ya malamulo wa derali ati nduna ya zachuma yawatsimikizira kuti nsewu umenewu uyambidwa chaka chino. Feasibility study inachitika kale miyezi yapitayo mwinanso munamva boma litalengezetsa kuti likufuna kampani yoti ipange zimenezo ndipo zinachitikadi. Ndakambirana kale ndi a nduna a zachuma ndipo anditsimikizira kuti nsewu umenewu awuyika mu ndondomeko ya zachuma yomwe ikubwerayi, anatero a Botomani. Iwo ati nsewu-wu omwe ndi ochoka ku Zomba Airwing kudutsa kwa Govala ndi ofunika kwambiri kaamba koti ukupita komwe kuli nyanja yachiwiri kukula mdziko muno komanso ati kumalimidwa mpunga wochuluka.
14
ANATCHEZERA Adandichotsa ntchito Zikomo Gogo Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndakhala ndikugwira ntchito kwa bwana wina mumzinda wa Blantyre kwa zaka 4. Masiku apitawa ndidaapempha holide ya masiku 10 ndipo bwanawo adavomera. Koma ndili kopuma, bwanawo adandiimbira foni kuti andichotsa ntchito ndipo palibe ndalama zimene angandipatse. Ndichitenji chifukwa ku ofesi yolemba anthu ntchito ngakhalenso kukhoti ya makampani koma sindinathandizidwe? Mutu waima. BMW, Blantyre. BMW, Ili likhale phunziro kwa tonse kuti pamene tikuyamba ntchito, tiyenera kuunikirana bwino lomwe zomwe ziyenera kuchitika pamene ntchito ikutha. Malamulo a zolemba anthu ntchito akuneneratu kuti ngati bwana akuchotsa wantchito wake, ayenera kumuuza kuti amuchotsa pakutha pa masiku 15. Awa ndi antchito amene amalandira malipiro otsika kwambiri. Chimodzimodzi, munthu siungangodzuka lero nkunena kuti bwana ndasiya ntchito. Uko ndi kuphwanya malamulo. Tsono mwati adakuchotsani muli kutchuti. Tchuti ndi gawo la ntchito yanu ndipo sikuti bwana akukuchitirani chifundo. Ndi gawo limodzi la ntchito. Munthu ngati ukusiya ntchito, ndipo uli ndi masiku amene mumayenera kupita kuntchito, masikuwo mumawerengera ndipo mukhonza kusiya ntchito pompompo. Chofunika kwambiri ndi kukambirana ndi amene akukulembani ntchito musanayambe ndipo ngati nkotheka musayinirane. Nkutheka apa kuti ku labour office kapena khoti ya makampani simungaphule kanthu chifukwa palibe umboni wa zomwe mudagwirizana. Apachibale akundifuna Anatchereza, Pali anyamata awiri a pachibale amene akuoneka kuti amandifuna. Mmodzi mwa anyamatawo ndidamudziwa kalekale ndipo wakhala akundifundira koma ndimamukana. Ndidadziwana ndi winayo chifukwa cha mbale wakeyo ndipo nsye akunditumizira mauthenga a chikondi, ati akundifuna. Ndichitenji, chifukwatu awiriwo akundisowetsa mtendere. M.E. Mponela ME, Ngati anyamatawo simukuwafunadi ndi bwino kuwauziratu, mmalo mowapatsa banga kuti aziganiza kuti mwayi ukadalipo. Mwinatu inuyo simutsindika kukana kwanuko. Komanso nkutheka kuti anyamatawo ndi nkhakamira. Mwinanso ali pampikisano kuti aone angakutengeni ndani. Muli monsemo, mphamvu zili mmanja mwanu, kulola kapena kukana. Ana owapeza avuta Zikomo Anatchereza, Ndakhala pachibwenzi ndi mkazi wina yemwe ndidalowa naye mbanja chaka chatha. Iye adabwera ndi ana ake awiri ndi abale ena ndipo polingalira kuti ndi banja, nanenso ndidakatenga mwana wanga. Iye akungokhalira kulalatira mwana wangayo ati ndi wamwano. Nthawi zina akumachita izi panja kuti a nyumba zoyandikira amve. Akuti ngakhale nditachoka sangadandaule, chonsecho ali ndi pathupi pa miyezi 7. Ndapirira mokwanira, ndithandizeni. WL, Lilongwe. WL, Musanachite chilichonse pabanja mumayenera kukambirana kaye. Momwe zikuonekera apa, mkazi wanuyo adakangotenga ana ndi abale akewo musanakambirane. Nanunso mudangoyendera yanu nkukatenga mwana wanu. Choncho kusamvana sikungalephere kubwerapo. Komatu apa palibe chifukwa chokwanira choti nkuthetsera banja.
12
Chaka chino kuli zokolola mpweche Unduna wa zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi walengeza kuti chaka chino alimi akolola matani 3.3 miliyoni a chimanga kuyerekeza ndimatani 2.6 miliyoni omwe adakololedwa chaka chatha. Izi zadziwika undunawu utachita kauniuni woyamba wa chiyembekezo cha kakololedwe kaulimi wa 2018/19 ndipo zotsatirazi zikutanthauza kuti chaka chino alimi a chimanga aonjezera makilogalamu 25 pa makilogalamu 100 aliwonse womwe tidapata chaka chatha. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Chaka chilichonse undunawo umapanga kauniuni katatu wa chiyembekezo pa zokolola kuti uwone ngati nkoyenera kuti alimi ndi boma agulitseko zina kapena ayi. Kauniuni ameneyu ndi wofunika chifukwa ndi amene amatithandiza kuona ngati mdziko mukhale chakudya chokwanira kapena ayi. Zimatithandizanso popanga mitengo ya mbewu ndi kuunikira alimi pa nkhani yogulitsa mbeu zawo, idatero nduna ya zamalimidwe Joseph Mwanamvekha. Mkulu wa bungwe la Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Pamela Kuwali wati nkhaniyi ndi yabwino bola zinthu zisatembenuke mukauniuni awiri otsatira. Iye waunikira kuti boma ndi mabungwe achilimike potsogolera alimi momwe angasungire mbewu zawo ndi kuzipezera msika wabwino kuti adzapange nazo phindu. Chomwe chimachitika nchoti poti zachuluka, mavenda amatsitsa mitengo yogulira mbewu ndiye poti alimi amakhala ndi njala ya ndalama, amangolola mtengo uliwonse osadziwa kuti akubetsa, watero Kuwali. Mbiri ya zaka za mmbuyo imasonyeza kuti zotsatira za akauniuni atatuwa zimanka zitsika chifukwa cha zochitika mdzinja monga kusintha kwa kagwedwe ka mvula, tizirombo toononga mbewu ndi matenda ena adzidzidzi. Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu watsimikiza kuti mmera mminda ukuoneka bwino ndipo ukupereka chiyembekezo chokolola zochuluka ndipo wati mafumu alandira mabungwe onse omwe aziwapeza ncholinga chophunzitsa alimi kasamalidwe ka zokolola. Ngakhale ambiri akubwekera kuti mvula ikugwa bwino chaka chino, Mwanamveka wati kuchuluka kwa zokolola nchifukwa chapologalamu ya sabuside wafetereza ndi mbeu ya makono. Iye adati boma lidapanga dala kuwonjezera chiwerengero cha anthu olandira makuponi afetereza ndi mbeu kuchoka pa 900, 000 mu 2018 kufika pa 1 miliyoni chaka chino kuti alimi ambiri apindule.
4
Mutharika Walengeza Zoyimitsa Ntchito Zonse Mdziko Muno Kwa Masiku 21 Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika walengeza kuti ntchito zonse za mdziko muno ziyima kwa masiku 21 kuyambira loweruka likudzali ati pofuna kulimbana ndi kachilombo ka Coronavirus. Mutharika wanena izi dzulo usiku kudzera mu uthenga wake wapadera omwe amalankhula ku mtundu wa aMalawi pa nkhani yokhudza nthendayi mdziko muno. Iye wati zimenezi zichitika kuyambira 12 koloko ya usiku wa loweruka pa 18 April mpaka pa 9 May 2020. Mutharika wati kuyimitsa ntchito zonseku kutha kuzawonjezeredwa ngati boma lizawone kuti zinthu sizikusintha ndipo zikuyipirabe. Iye wati maiko ambiri ataya miyoyo ya anthu ochuluka kaamba ka nthendayi ndipo mayiko onse amene azungulira dziko lino nawonso akhudzidwa ndi nthendayi choncho ndi kofunika kuti dongosolo labwino liyikidwe kaamba koti kupanda kutero anthu oposa 50,000 atha kufa mdziko muno kaamba ka nthendayi. Pamenepa iye wati ndi kofunika kuti anthu atsatire dongosololi kaamba koti ndi lothandiza kwambiri dziko lino ndipo wati pamene izi zikhale zikuchitika, boma likhalabe likupitiliza kuchita ntchito zake zopulumutsa miyoyo ya Anthu monga kuyeza Anthu omwe akukayikiridwa, kulemba ntchito a zachipatala owonjezera, kukhwimitsa chitetezo mzipata ndi malo ena onse, kupereka zipangizo zogwilira ntchito kwa a zachipatala komanso ntchito yopereka mauthenga othandiza anthu kudziwa za kapewedwe ka nthendayi. Mutharika wati pakufunika ndalama zokwana 150 billion kwacha polimbana ndi nthendayi ndipo wapempha atsogoleri ena a ndale kuti agwirane manja ndi boma pa ntchito yolimbana ndi mlirriwu. Kulengezaku kwadza patangopita maola ochepa Anthu ena osadziwika ataphwanya zipangizo za kalembera wa chisankho msukulu zina mu mzinda wa Blantyre ponena kuti bungwe la MEC silimayenera kupitilira ndi ntchitoyi pamene nmdziko muno muli mliriwu zomwe zachititsanso bungweli kuti liyimitse kalembera wachisankho mboma la Blantyre. Izi zachitikanso patangopita maola ochepa pomwe Gulu la ndale lomwe langokhazikitsidwa kumene la Citizens for Transformation (CFT) linachenjeza boma, kuti lisabwere ndi ganizo loyimitsa ntchito zonse mdziko muno kamba ka nthenda ya COVID-19, ponena kuti izi, ziyika miyoyo ya anthu ambiri pa chiwopsezo. Mtsogoleri wa gululi a Timothy Mtambo, analankhula izi lachiwiri ku Lilongwe, pa msonkhano wa atolankhani pomwe amalankhulapo pa momwe zinthu zilili mdziko muno pakadali pano. Iwo ati ndi zomvetsa chisoni kuti pakumveka za maganizowa, ndipo wati mzika zambiri za dziko lino, zitha kuvutika kwambiri kupeza zofunika pa moyo wawo, ntchito za dziko, zitaime pofuna kuteteza kufala kwa kachirombo ka Corona virus.
6
Gule wa utse ku Nsanje Mtundu ulionse umakhala ndi zinthu zokumbikira mtundu wawo kapena chikhalidwe. Umu zilinso choncho ndi mtundu wa Asena ku Nsanje komwe kuli gule wa utse. Mbomalo mudali mwambo wobzala mitengo, ndiye gule ameneyu adamuitana kuti asangalatse anthu. Abambo adafa ndi kuseka amayi akupukusa chiuno molapitsa. BOBBY KABANGO adali komweko ndipo adamuitananso kuti avine ndi mayi mmodzi. Atatha zonse, adacheza ndi mayi mmodzi motere: Poimba amagwiritsa ntchito matabwa Dzina ndani mayi? Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Ndine Fakilesi Nachikadza, ndimachokera mmudzi mwa Therere kwa T/A Malemia mboma lino. Gule wanji wokoma chonchiyu? Ameneyu ndi utse. Utse ndi gule wa amayi okhaokha. Atsikana saloledwa kuvina nawo? Sangakwanitse kuvina. Guleyutu amafunika munthu amene angavine kwa nthawi yaitali osatopa, ndiye atsikana sangakwanitse koma ife akuluakulu. Mumavina nthawi iti? Timavina kukakhala zochitika monga kulonga mfumu, ndi zochitika zilizonse monga kubzala mitengoyi. Mavinidwe ake ngotani? Limakhala gulu la amayi okhaokha, ndiye timasema timatabwa ndipo aliyense amakhala ndi matabwa awiri amene amawamenyetsa kuti zizimveka bwino. Ena amakhala akuomba mmanja ndipo onse amaimba nyimbo. Mayi mmodzi amakhala akuduka mchiuno. Iyeyu ndiye amaimirira pamene ena onse amakhala pansi. Amene akuvinayu amakhala ndi wenzulo yomwe amaimba. Mutanthauza kuti amavina ndi munthu mmodzi? Eya, koma tingathenso kumulandira chifukwa tonse timadziwa kuvina kwake. Amavina bwanji? Momwe ndikuchitiramu basi, nkhanitu ndi chiunochi kuchigwiritsa ntchito. Inuyonso tabwerani apa ndivine nanu kuti mukalembe zoona.eyatu ndi momwe timavinira guleyu. Mudayamba liti kuvina guleyu? Ine ndidabadwa ndipo ndidamupeza, timaonera makolo akuvina mpaka lero takula ndipo tikuvinanso. Nyimbo mumaimba ija mumati chiyani? Imeneyi ndi nyimbo yokamba za ubwino wa mitengo. Timati; azimayi tendene, aye! Azimaye tendene, tikabzale mitengo. Mafumu ali pomwepo, aye! Mafumu ali pomwepo tikabzale mitengo. Pagulu ponsepa amene amavina bwino ndi inuyo? Aliyense amavina bwino koma leroli anasankha ine kuti ndivine ndipo mwaonanso abambo ambiri akuyamikira kuti ndavina bwino. n Kuikira kumbuyo khalidwe loipa Wolemba: Rabecca Nsomba Nthawi zina, amayi amene akukwatiwa amauzidwa kuti asakasiyire wa ntchito kuphika chifukwa wantchitoyo akhoza kulanda banja. Enanso nkumamulangiza kuti asakaleke kudzisamala kuopa akathawidwa. Tikaonetsetsa palibe vuto ndi kusamala pakhomo, kudzisamalira ndi zina zotero, koma nzolakwika kuika zinthuzi ngati zida zothandizira kuti banja lisathe. Chifukwa polankhula motere timakhala ngati tikuvomereza kuti zina mwa izi ndi zifukwa zoyenerera popangitsa kuti bambo azichita zibwenzi chifukwa mkazi wake walephera penapake. Abambo ena amakhala ndi zofooka zina zikuluzikulu zomwe amayi amazipirira mmakomomu osaganizirakonso kuti mwina apeze mpumulo popeza chibwenzi. Nchifukwa chiyani zimaoneka zabwinobwino kuti abambo azilephera kupirira nkufika pomasirira Naphiri kuti mpaka apange naye chibwenzi chifukwa waphika bwino? Abambo otere ngachimasomaso ndipo amakhala kuti Naphiriyo amamusirira kale. Pali abambo ena autchisi, ena oti akavula nsapato fungo nyumba yonse. Sudzamupeza mayi akuti bola Joni okonza maluwa amadzisamalirako. Mmalo mwake mayi amayesetsa kuti akonze nsapato ndi sokosi za mwamuna wake kuti fungo lichepe. Koma mzimayi akamveka thukuta, ndiye bambo ali ndi chifukwa chomveka bwino choti akasake chibwenzi? Osamuuza mkazi wako za vuto lake bwa? Mundimvetse, sindikuti amayi atayirire, koma tizindikire kuti amayi amakhala ndi zofooka. Tsono zofooka za amayi zisakhale zifukwa zokwanira zoti abambo azinka nasaka akazi ena. Momwe mzimayi amapiririra zofooka za mwamuna wake, mwamunanso apirire za mkazi wake ndipo pamodzi athandizane kukonza zinthu. Osati mmalo mokonza zinthu tizipititsa patsogolo maganizidwe olakwika omati mayi azipirira pomwe bambo akangoona vuto azikhala ngati wapatsidwa chiphaso chomachita zibwenzi. Izi ndi zolakwika. Ma playoffs afika pena Wolemba BOBBY KABANGO G anizo lokhala ndi timu ya chi 16 mu ligi ya TNM lakhala loterera pamene nkhondo ya Dedza Young Soccer komanso Super League of Malawi (Sulom) yafika pa lekaleka. Dedza idatenga chiletso Lachisanu pa 11 March kubwalo lalikulu la milandu mumzinda wa Lilongwe kuletsa kuti Sulom isachititse masewero ofuna kupeza timu ya nambala 16. Chiletsocho chidaperekedwa ku Sulom Loweruka masewero oyamba pakati pa Airborne Rangers ndi Wizards atachitika kale Lachisanu. Chiletsocho chidagwira ntchito pa masewero otsatira amene amayenera akhale pakati pa Dedza ndi Airborne Lowerukalo pabwalo la Civo. Lowerukalo mmawa, Sulom idapita kubwalo kuti akachotse chiletsocho koma mpaka pofika Lachinayi chidali chisadachotsedwe. Wachiwiri kwa pulezidenti wa Sulom, Daud Suleman, polankhula Lachitatu usiku adati chiletsocho chavuta kuchotsa chifukwa jaji wake adachoka. Tidauzidwa kuti jaji wapita ku Zambia, ndiye panopa tikumva kuti jaji wina ndiye athandizire kuti chiletsocho chichoke kuti masewero ofuna kupeza timu ya nambala 16 apitirire, adatero Suleman. Timu ya Dedza ikuti ngati Sulom ikufuna kupeza timu ya nambala 16, akuyenera atenge iwo chifukwa ndiwo adathera pa nambala 13 kutsatirana ndi Wizards komanso Airborne. Koma Suleman akuti njira yosewera ma playoffs ndi yokhayo yomwe Sulom idagwirizana kuti ichitike pofuna kupeza timu imodzi yoonjezera. Ligiyi tsopano kuyambira chaka chino izikhala ndi matimu 16 osati 15 monga zakhala zikuchitikira koma bungwe la Sulom lidalengeza ganizo lochita ma playoffs patadutsa pafupifupi mwezi chithereni ligiyi. Ngati chiletsocho chichotsedwe, ndiye kuti Sulom ikuyembekezereka kulengeza tsiku lomwe ma playoffs-wa achitike. Mwini wake wa Wizards Peter Mponda akuti izi zawasokoneza kwambiri. Taononga ndalama zambiri, mayendedwe, chakudya komanso malo ogona ndi ndalama zambiri zimenezo, adatero Mponda. Wizards ndiyo idapambana mmasewero ake ndi Airborne 2-1.
15
Wa zaka 22 akufuna uphungu Machawa (kumanzere) limozdi ndi Mussa Timamva kuti achinyamata ndi atsogoleri a mawa, koma msungwana wa zaka 22 ku Nsanje wati akufuna kudzaimira chipani cha PP kudera la kumpoto mbomalo. Machawa Mcheka-Chilenje akuphunzira za chitukuko cha madera a kumidzi ndipo wati achinyamata asamaope ndale chifukwa ndi limodzi mwa magawo othandizira pachitukuko cha dziko lino. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Iye adati nchifukwa akufuna kudzapikisana nawo ndi ena amene akufuna kudzaimira PP pa chisankho cha pa May 20, 2014 mdera limene adaimirapo Gwanda Chakuamba komanso azakhali ake Esther Mcheka-Chilenje Nkhoma, yemwe adakhalapo wachiwiri kwa sipikala wa Nyumba ya Malamulo. Mdera lino muli mavuto a misewu, za umoyo, achinyamata ambiri sakupita kusukulu, zaulimi sizikuyenda chonsecho mtsinje wa Shire ndi mitsinje ina ili pafupi. Nthawi yoti achinyamata aziopa kuchita ndale idatha, adatero iye. Pomulandira, Nduna ya za Mdziko Uladi Mussa adati ichi ndi chitsanzo chabwino ndipo malamulo akumulola kutero. Malamulo oyendetsera dziko lino amaneneratu kuti ofuna kuimira uphungu akhale wa zaka 21 kapena kuposa apo. Iyeyu adakwanitsa zakazo ndipo tili ndi chikhulupiriro chonse kuti akwanitsa ntchito waiyambayo, adatero Mussa.
11
Japan Yalonjeza Kukweza Maphunziro ku Malawi Kazembe wa dziko la Japan kuno ku Malawi wati dziko lake lipitiliza kulimbika pa ntchito zokweza maphunziro mdziko muno. Kazembe-yu Satosh Iwakiri walankhula izi msabata-yi pomwe amaika mwala wa maziko pa malo omwe akufuna kumangapo zipinda zophunzilira ana, pa sukulu ya Primary ya Kapalamula mboma la Dedza. Iye wati boma la kwawo laganiza zomanga zipindazi ngati njira imodzi yofuna kuthandiza pa ntchito zotukula maphunziro pa sukulu-yi. Polankhulanso mkulu woona za maphunziro mbomalo a George Ngaiyaye anathokoza boma la Japan kamba kodzipereka pa ntchito zotukula maphunziro mbomalo. Polankhulanso mphunzitsi wamkulu pa sukulu-yi Frolence Donda wati kumangidwa kwa makalasi-wa kuthandiza kwambiri pa ntchito zokweza maphunziro pa sukuluyi. Mwa zina boma la Japan limanga nyumba zitatu za makalasi 6 ophunzilira ana pa sukulu ya Kapalamula mboma la Dedza, thanki ya madzi, ndipo zitenga ndalama zoposera 60 million kwacha.
3
Tinkakhala nyumba zoyandikana Mwayi wa banja umapezeka malo osiyanasiyana. Ena amapeza womanga naye banja mubasi, eetu paulendo, pomwe ena amakumana kutchalitchi. Koma kwa mphunzitsi wa sukulu ya utolankhani ya Malawi Institute of Journalism (MIJ) Jonathan Jere, sadathenso mtunda, koma adapeza mkhonde basi. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Pano Constance Kumwenda akutaya madzi pakhomo la Jere. Awiriwa adakwatirana chaka chathachi pa 5 December ku Mchengautuwa CCAP ndipo madyerero adachitikira ku hotelo ya Chenda, mumzinda wa Mzuzu. Komatu si kuti Jere adayenda mofewa kuti apeze mkaziyu poti adali woyandikana nyumba, ayi ndithu. Mwana wammuna adakhetsera thukuta. Jonathan ndi Constance patsiku lomwe adamanga woyera Ndimakhala moyandikana nyumba ndi makolo ake ku Chiwavi. Ndipo maso anga adayamba kudyerera pa iye patatha ingapo, adatero Jere. Iye adati kwa miyezi 6 awiriwa sankacheza koma amangoonana ngati oyandikana nyumba. Malinga ndi Jere, namwaliyu ndi namwino kuchipatala cha Mzuzu Central. Pangonopangono adayamba kumufufuza ndipo atamva zoti palibenso tambala wina yemwe amazungulirazungulira kholali, adalimba mtima. Apatu Jere adafufuza nambala yake ya foni kuchokera kwa anthu ena ndipo adaipeza. Apa awiriwa adayamba kulumikizana ndipo posakhalitsa Jere adapempha kuti akakumane poduka mphepo ndi kukambitsana ziwiri, zitatu. Komatu izi sizidatheke chifukwa namwaliyu adakanitsitsa kuti nthawi yokumana ndi Jere adalibe. Ankati popeza tidali oyandikana nyumba anthu aziyesa zachibwana, adatero Jere. Naye Jere sadagwe ulesi koma adayesayesabe mwayi wake, mpaka tsiku lina adangoti naye gululu! Sadachedwenso koma kumuuza zakukhosi kwake. Pangonopangono ndidayamba kubooleza mpaka chibwenzi chidayamba ndithu, koma padatha mwezi ndikugubira ndithu, adatero Jere. Iye adati polemekeza makolo komanso kuti kucheza kwawo kuziyenda bwino, adasamuka ndi kupeza nyumba ina kudera lina. Adaonjezeranso kuti apa sadachitenso za bobobo, koma kuyamba kukonzekera za ukwati. Koma popeza zokhoma sizilephera pa moyo, zinthu zidavuta kaamba ka mpingo. Anthu ena sadafune kuti atuluke mpingo wake ndi kulowa wanga. Komabe pa uwiri wathu tidakambirana ndi kugwirizana kuti alowa mpingo wathu, adatero Jere.
15
Khirimasi idali yovuta Lachiwiri lidali tsiku la Khirisimasi, ndipo anthu adali kalikiliki kugula katundu kuti asangalale ndi mabanja awo tsiku lokumbukira kubadwa kwa Yesu Khristulo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Monga adafotokozera ena mwa omwe tidawapeza mmalo osiyanasiyana, chaka chino Khirisimasi ikusiyana ndi zaka zina chifukwa ndalama zikusowa. Izi zidachititsa ena kugula zochepa poyerekeza ndi momwe ankachitira mmbuyomu. Ena ankaneneratu kuti kaamba ka kuvuta kwa zinthu, Khirisimasi idawalambalala ndipo adangokhalira ku mapemphero. Chithunzi chikusonyeza Dorothy Kandodo kugula katundu Lolemba.
15
Malonjezo ayamba kuoneka Boma latsopano la Tonse Alliance layamba kukwaniritsa ena mwa malonjezo ake a panyengo ya kampeni ndipo pomwe akadaulo osiyanasiyana ayamikira izi, atinso boma lisadzabwerere mmbuyo. Kukwaniritsidwa kwa malonjezowo kudayamba kuoneka Lachiwiri mNyumba ya Malamulo pomwe nduna yatsopano ya zachuma Felix Mlusu idalengeza bajeti yoyembekezera ya K722.4 biliyoni. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chakwera adalumbira Lamulungu Mlusu watcha bajetiyo dzina loti kutukula ntchito zaulimi ndi zipangizo zotsika mtengo chifukwa mtengo wa fetereza watsika kufika pa K4 495 pa thumba la 50Kg monga mwalonjezo ndipo alimi 3.5 miliyoni ndiwo akuyembekezeka kupindula. Mdziko muno muli mabanja odalira ulimi okwana 4.2 miliyoni koma ndondomeko yakale ya sabuside inkakomera alimi 900 000 kapena 1.5 miliyoni akachuluka. Mbajetiyo, boma lakonza zokwenza poyambira ndalama za malipiro apamwezi kuchoka pa K35 000 kufika pa K50,000 komanso kukwenza malipiro oyambira kudula msonkho munthu yemwe amalandira K35 000 tsopano malipiro ake awonjezekera ndi K15 000 yomwe ndiyokwanira kugula matumba atatu a fetereza pa mtengo wa K4 495 nkukhalakonso ndi zolipilira wonyamula fetelezayo.malipiro kukutanthauza kuti Chimodzimodzi kukweza malipiro oyambira kudula msonkho kufika pa K100 000 kupangitsa kuti anthu apulumutse K17 500 yomwe kale amadulidwa kutanthauza kuti nawo akhoza kugula matumba atatu a fetereza ndi ndalamayo. Koma ngakhale izi zili nkuthekera kogwedeza mapezedwe a ndalama za boma, akadaulo pa za msonkho ndi zachuma agwirizana nayo nkhaniyi. Kadaulo wazachuma Gowokani Chijere Chirwa wati nkofunikira kwambiri kuti boma lapanga momwe lapangiramu potengera umphawi wa anthu ndipo wati kangachepe komwe anthu azipulumutsa nkochuluka akagwiritsa ntchito bwino. Naye kadaulo pa zamisonkho Emmanuel Kaluluma wati ngakhale kukwenza malipiro oyambira kudula msonkho kukhudze katoleredwe ka misonkho, boma lapanga bwino kuganizira anthu. Misonkho ndi imeneyo ndipo ndiyofunikadi koma palibe nzeru kutolera ndalama kwa anthu nkuwasiya alibe pogwira chifukwa afa ndi njala, adatero Kaluluma. Mubajetiyo, boma laonjezera ndalama za thumba la ngongole za achinyamata kuchoka pa K15 biliyoni kufika pa K40 biliyoni komanso lati pofika mchaka cha 2021 likhala litatsegula mwayi 600 000 wa ntchito. Kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu mdziko Makhumbo Munthali wati boma layamba bwino pokwaniritsa malonjezo chifukwa ubale umakoma nchilungamo komanso kukhulupilika. Mukakumbukira tikucheza za kampeni ndidanenapo kuti andale azilonjeza zinthu zomwe angakwanitse chifukwa zomwezo zimadzasanduka adani awo mtsogolo maka pa kampeni ina ngati sadazikwaniritse, adatero Munthali. Naye George Phiri wodziwa za ndale wati boma likamapanga zinthu zokomera anthu ake, zinthu mdziko zimayenda komanso dziko silichedwa kutukuka. Tamverani, anthu amadziwa kuti andale amasintha miyoyo yawo akakhala pampando ndiye kuti munthuyo asade kukhosi, pamafunika naye azimvako kukoma kwa dzikolo ngati momwe layambira bomali, adatero Phiri. Akadaulowa adagwirizana pa mfundo yoti bola bomali lisasinthe momwe layambiramu chifukwa likatero anthu atsimikiza kuti andale zawo nzimodzidi.
11
Tadeyo Mliyenda: Malingaliro padziko Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndidakhala pa Wenela kudya mpweya. Minibasi zoti ndiyitanire abale anzanga, osabwera nkomwe. Ndidagwera mmaganizo. Ndidakumbukira zoti pali mkulu wina yemwe akufufuza maganizo a anthu pankhani ya bajeti. Nanga kodi njonda imeneyi pa Wenela ifika liti? Ikadzangoti yafika, ndithu ndidzayiuziratu kuti pa Wenela patukuke. Tikufuna malo abwino ogona ife oyitanira; pakhalenso khitchini yoti tizikadya ulere; apolisi asamatiphwanyire ufulu wathu wopata chuma; komanso pakhale zimbudzi zoti tikalowa kukapuma, tisamalipire. Abale anzanga, mzinda wonse wa Blantyre mulibe malo omwe munthu angayimirire mwaulele. Chonsecho akuti munthu ukagwidwa pamtengo, wakundende ndithu. Nanga zinyalala pa Wenela, mkulu wachikwama athana nazo bwanji? Ndikudziwatu mukundinena: A Tade, zoona chikwama chimanyamulidwa chija mukakhale zomanga zimbudzi pa Wenela? Simukudziwa chomwe mukunena. Pa Wenelatu ndiye pamene aliyense wofika kumene mumzinda wa Blantyre amayambira kuponda. Pamafikatu mabasi a Mafenyetsera, Munorurama, Zvakanedza ndi zina zotere kuchoka ku Bulawayo. Komanso pali basi za ku Joni zimene zimafikira pamene paja. Ndiye tangoganizani munthu wachoka ku Durban, kuthawa kutentha kwa zeno, kudzafika pa Wenela, alipire chimbudzi pomwe komwe adatchonako nzaulere. Chomwe ndikunena apa nchoti ine monga munthu wamba ndili ndi zofuna zanga pa bajeti. Chabwino, ngati mukuona kuti ndilibe mphamvu kukambapo za ndondomeko yachuma, mukufuna ndikambe za chiyani? Za kusolola ndi kuphana kudachitika ku kapitolo? Apo ndangodutsa. Kapenatu mumafuna ndikambe za Baba JT, uja ankatsogolera Male Chauvinist Pig, chipani adatisiyira Gogo uja? Wasowatu mkuluyu. Kapena ndikambe za Adona Hilida kuti afika liti pano pa Wenela kuchokera kulikonse kumene adapita? Asowatu mayi wathu okondekawa. Kodi nsalu ya paphewa akadakoleka? Nanga komwe aliko akugawanso nkhuku ndi abakha? Ndili mkati molingalira izi, ndidangoona chigulu cha anthu panyumba ina yomwe ili kuseli kwa Wenela. Ndidapita konko ndipo ndidapeza anthu ali unjiunji. Mwamuna wadzigwira yekha ndithu, ankatero anthuwo. Kufika pafupi, ndidamva kuti bambo wa mnyumbayo adatopa ndi mkazi wake ndipo adafuna kuti amusiye basi. Komatu mwamunayo sankamupezera mkaziyo chifukwa. Adali wachifundo munthu wamayi, wokonda kupemphera, wophika zakupsa, wamalangizo akupsa komanso wodziwa kusamalira mwamuna wakeyo mnjira zonse. Mwamunayo adangotopa naye mkaziyo basi. Mwamunayo adagwirizana ndi mnzake yemwe ankamwa naye: Ndikufuna kuti ndimusiye mkaziyu. Njira yabwino ndi yoti ndidzakugwire uli mmagombeza ndi mkazi wanga. Ndatopa naye. Winayo adalolera. Ndipo usiku umenewo, winayo adanyamuka msanga kuchoka kumowa. Adalunjika kunyumba yamnzakeyo ndipo adamupeza mkazi wake. Mkaziyo adalola kuti acheze. Koma asanalowe mmagombeza, mkulu uja adapempha kuti avale jekete la mwamuna wa mkaziyo. Mkazi uja adapereka jekete ndipo nkhani zili mkati, awiriwo atafunda guza limodzi, adangomva kugogoda. Asanaganize chochita, chitseko chidatseguka. Gululu, mwini nyumba wafika. Ndiye chiyani ichi Naphi! adakuwa. Mwamuna wakuba uja adati athawe, koma bambo uja adamuvula jekete. Mbalayo idathawira pakhomo nkusowa mumdima. Lero ndakugwira! Ngakhale mwamuna wakoyo wathawa, ndasunga jekete la kamwamuna kakoko. Umboni wanga kwa ankhoswe. Wagwa nayo basi, adazaza mwamuna. Jekete lili mmanja mwanulo ndi lanu ndiye mukuti umboni wanu uli pati. Kupusa eti. Tangobwerani tizigona apa, adayankha mayi uja. Abale anzanga, banja ndi chinthu chofunika, osachitengera chibwana. Inde, iye wapeza mkazi wapeza chinthu chabwino. Ndipo nkhani ili mkamwa, ndifunire zabwino zonse Paparazzi ndi anzake onse amene amalemba nkhani pomwe akusangalala tsiku lawo pa 3 May.
15
Akagwira Jere Zaka Zinayi Kaamba Kovulaza Bambo Ake Bwalo loyamba la milandu mboma la Mangochi lalamula bambo wina za zaka 40, kuti akakhale kundende kwa zaka zinayi ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kaamba komupeza olakwa pa mlandu wovulaza bambo wake. Bwalolo linamva kuti bambo-yu Idi Abdul, anavulaza bambo akewo powakhapa ndi khwangwa paphewa ati kamba kopsa mtima ndi zimene zinachitika posamusungira chakudya atafika nthawi ya usiku pakhomopo. Popeleka chigamulocho First Grade Magistrate Roy Kakutu anati zomwe mkulu-yi anachita zinali zosayenera kotero akuyenera kuti akakhale ku ndende kwa zaka zinayi kuti ena atengerepo phunziro. Idi Adbul amachokera mmudzi mwa Bwanali mdera la mfumuyayikulu Chowe mboma lomwelo la Mangochi.
7
MAM Idzudzula ADUS Pophwanya Ufulu wa Maphunziro wa Ana Wolemba: Thokozani Chapola Bungwe lalikulu la chipembedzo cha chisilamu mdziko muno la Muslim Association Of Malawi ladzudzula mpingo wa Anglican mu dayosizi ya Uppershire kuti ukuphwanya ufulu wamaphunziro kwa ophunzira a msukulu za pulayimale komanso sekondale za Mmanga mboma la Balaka. Mneneri wa bungwe lomwe lomwe limawona za chovala cha Hijab ku Muslim Association of Malawi Abdul-Salaam Fadweck wanena izi potsatira kutsekedwa kwa sukuluzi zomwe ndi za mpingo wa Anglican kamba ka kusamvana ndi anthu, pamene mpingowu unayika lamulo lakuti pasapezeke mwana wovala chovala cha Hijab nthawi ya maphunziro mu sukuluzi. Sukuluzi zakhala zili zotseka kwa sabata zoposa zitatu, ndipo malinga ndi a Fadweck zimenezi zikupereka chiopsezo kuufulu wa maphunziro kwa ophunzira pa sukuluzi. Pomwe ndikunena pano sukuluyi ndi yotseka kwa sabata zoposa zitatu tsopano zomwe sizoyenera kwa mwana wa sukulu poganiziranso kuti ena mwa iwo akuyembekezeka kulemba mayeso a Standade 8, anatero a Fadweck. Iwo ati mdziko muno palibe amene ali ndi ufulu wotseka sukulu kupatula unduna wa zamaphunziro wokha basi ndipo apempha mpingo wa Anglican kuti utsekule sukuluyi msanga. Sukulu imeneyi imathandizidwa ndi boma, aphunzitsi amalandira ndalama za ku boma zomwe zikutanthauza kuti misonkho yathunso ikumapita ku sukulu imeneyi. Pakafunika ntchito zachitukuko kaya kumanga makalasi makolo amathandizira ndipo ambiri mwa iwo amapita atavala hijab. Ndiye amalora bwanji kholo kukagwira ntchito atavala hijab koma kumukanira mwana wake kulowa mkalasi atavala hijab? anadabwa motero a Fadweck. Mkulu woyendetsa ntchito za maphunziro mu dayosizi ya Uppershire ya mpingo wa Anglican, Canon Jailosi anakana kulankhulapo kanthu pa nkhani-yi. Ndipo padakalipano unduna wa zamaphunziro sunanenebe za tsogolo la maphunziro pa sukulupa pomwe ikupitilira kukhala yotseka.
3
Othawa nkhondo akutuwa ndi njala Kwathina kukampu ya anthu othawa nkhondo mdziko la Mozambique amene akukhala ku Mwanza ndi Neno komwe anthuwa akutuwa ndi njala. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ena atha sabata ziwiri tsopano popanda chakudya ndipo amene ali bwino ndi anthu amene adabwera ndi ndalama kuchokera mdziko lawo. Gulupu Ngwenyama wa mboma la Mwanza wati anthuwa akusowa mtengo wogwira kupatula anthu amene adayenda ndi ndalama kuchokera mdziko lawo. Ndiwo ndi vuto lalikulu kwa othawa nkhondo Amene adabwera ndi ndalama ndiwo sakulira kwambiri chifukwa akumagula zakudya, koma amene adangobwera opanda kanthu ndi amene akuvutika chifukwa akungodikira thandizo la mabungwe, adatero. Gulu la anthu lidayamba kukhamukira mdziko muno kuchokera ku Mozambique komwe akugwebana pachiweniweni pakati pa otsutsa boma ndi aboma. Kumenyanako, komwe kudayamba chaka cha tha, kudafika poipitsitsa mu January pamene nzika zina za dzikolo zidayamba kuthawira mdziko la Malawi. Kampu ya Luwani ku Neno yomwe ikusunga anthu pafupifupi 1 400 njomwenso yakhudzidwa kwambiri ndi njalayi. Kampu ina ndi ya Kapise mboma la Mwanza komwe kuli anthu pafupifupi 900. Malinga ndi Ngwenyama, pali chiyembekezo kuti Lolemba likudzali bungwe la World Food Programme (WPF) ligawa chakudya kwa anthuwa. Naye Senior Chief Saimoni wa mboma la Neno wati mavuto a njala ndi osakambika chifukwa nthawi zonse kukumakhala mavuto.
11
Ndale zikuwononga ufumu Mafumu angapo ati zipani zolamula zimaononga mbiri ndi ntchito ya mafumu powakweza popanda kuyanganira mbiri ya ufumuwo komanso khalidwe la mfumuyo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Ndemangazi zatuluka Lachinayi pa 27 Sepitembala ku hotelo ya Victoria mumzinda wa Blantyre pomwe bungwe loona za malamulo la Malawi Law Commission likupitiriza kumva maganizo osiyanasiyana pantchito yokozanso malamulo okhudza mafumu. Ku msonkhanowo, womwe unasonkhanitsa anthu komanso mafumu akuchigawo cha kummwera monga ku Zomba, Chiradzulu, Blantyre, Neno, Mwanza ndi Nsanje, mafumuwo anati boma lisiye kukweza mafumu popanda kufunsa bwino akubanja, anthu ake, mafumu ozungulira komanso bwanamkubwa wa bomalo. Apa nduna ya maboma aangono ndi chitukuko cha kumudzi, Grace Zinenani Maseko, yati nzosangalatsa kuti mafumu ndiomasuka kuperekera maganizo awo kotero izi zithandiza kuti pomwe malamulo akuunikidwa zingapo zisinthe. Malamulo adziko lino okhudza ufumu, omwe adakonzedwa pa 29 Disembala 1967, amapereka mphamvu kwa mtsogoleri wa dziko lino malinga ndi gawo 4 (1) kuti atha kuloza Mfumu Yaikulu (Paramount Chief) kapena (Senior Chief). Apa T/A Mlauli ya mboma la Neno yomwe idali ku zokambiranako idati lamulo ngati ili likuyenera kukonzedwa. Iye adati pali mafumu ena omwe khalidwe lawo silikondweretsa mafumu oyandikana nawo kapena anthu omwe amawalamula kotero izi zikuyenera zidziwunikidwa mfumu isadakwezedwe. Mlauli wati zimatheka mfumu mdera mwake kukhala mopanda ntchito iliyonse yachitukuko, koma kumakwezedwa. Zalowa ndale Iye adatinso mtsogoleri akakhala ndi mphamvu zokweza mfumu mosafufuza zimasokoneza mfumuyo chifukwa amagwira ntchito mokomera chipani cha boma lolamula. Ulemerero uwu umakhala wa nthawi yochepa chifukwa boma lina likabwera samadzawonedwa bwino, adawonjezera Mlauli. T/A Mbenje ya mboma la Nsanje idati ufumu umayenera kusankhidwa ndi mbumba ya ufumuwo koma masiku ano ndale zasokoneza chilichonse. Chitsanzo kuno tili ndi nkhani ya ufumu wa Mfumu Yayikulu Tengani omwe wasokonekera ndi andale mokuti mikangano idakali mkati. Mikangano yotere ingathe ngati chilichonse chitamasiidwa kubanja. Bwanamkubwa, mafumu oyandikana ndi mfumuyo komanso abanja akuyenera adzitenga mbali pa kukwezedwa kwa mfumu, adatero Mbenje. Naye Sub T/A Nkagula ku Zomba adati mfumu iliyonse imayenera ikwezedwe ndi anthu ake chifukwa ndi amene amaona momwe ikugwirira ntchito yake mmudzimo. Anthu akavomereza adzitumiza uthenga kwa mafumu oyandikana komanso bwanamkubwa, osati boma lidzingokweza mosadzera mwa mbalizi, idatero. Naye mkulu womenyera ufulu wachibadwidwe, Billy Mayaya, wati andale masiku ano akumakweza mfumu pazifukwa zandale, osati zoti zipindulire anthu onse. Iyi ndi nkhani yoti tikambirane, boma lisamakweze mafumu monga zakhala zikuchitikira; ganizo la mafumuwa lilibwino, adatero Mayaya. Asiye ndale Maggie Banda yemwe walemba mayeso a Fomu 4 ndipo akukhala mmudzi mwa Msisya kwa T/A Mbelwa mboma la Mzuzu wati andale asiyedi kukweza mafumu chifukwa mafumu otero akumasiya ntchito yawo nkuyamba kugwira yachipani. Boma la DPP lidakweza mafumu koma ndi ochepa omwe akuwonana bwino ndi boma la PP; mutha kuonanso kuti boma la PP lakweza kale mafumu ake. Izi zalowa ndale, adatero Banda. Limbani Kaombe wa mmudzi mwa Kachepa kwa T/A Likoswe mboma la Chiradzulu wati ufumu wawonongeka chifukwa cha andale kotero padzikhala kufufuza. Mkhalapampando wa bungwe lomwe likuchita kafukufukuyu, Justice Anaclet Chipeta adati unduna wa maboma angono ndiwo wapereka ntchitoyi. Iye adati ali okhutira ndi momwe anthu komanso mafumu akuperekera maganizo awo. Ntchitoyi ichitika zigawo zonse zadziko lino.
8
Boma lipereka mavidiyo a JB, Lutepo ku ACB Boma Lachinayi lidati lapereka kubungwe lothana ndi ziphuphu la Anti-corruption Bureau (ACB) mavidiyo a mtsogoleri wakale wadziko lino Joyce Banda akukambirana ndi Oswald Lutepo yeme akumuganizira kuti ndiye adasolola ndalama za kashigeti zochulukitsitsa. Koma bungwe la ACB Lachinayi lomwelo lidati silidalandire mavidiyowo ndipo ofesi ya Banda idati siyidaone chikalata cha bomacho kuti ayankhepo kanthu. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Chikalatacho chimene chidali patsamba la boma la pa Internet chidati mafilimuwo alipo 23 ndipo awiriwo ankakumana kunyumba za boma za Sanjika, Chikoko Bay, Kamuzu Palace ndi Mzuzu State Lodge. Chikalatacho chidati: Nthawi zina awiriwo amakumana okhaokha ndipo pena pamakhala anthu ena angapo kuphatikizapo atsogoleri a chipani cha PP. Koma wachiwiri kwa mkulu wa ACB Reyneck Matemba adati bungwelo silidalandire mafilimuwo ndipo sakudziwa kalikonse pankhaniyo. Ndafunsa bwana wanga [mkulu wa ACB] ngakhalenso ofufuza amene akutsata nkhaniyi koma onse akuti sakudziwapo kanthu, adatero Matemba. Ndipo mthandizi wa Banda, Andekuche Chanthunya adati sadachione chikalatacho ndipo sangayankhepo kanthu. Lutepo adali mmodzi mwa a chipani cha PP pomwe chinali mboma. Boma latulutsa chikalatacho patatha sabata ziwiri kuhokera pomwe Lutepo adauza wailesi ya Zodiak kuti aulula Banda za momwe awiriwo amagwirizanirana kupakula ndalama zaboma. Koma mkulu wa oimira boma pamilandu Mary Kachale adati Lutepo amayenera kukanenera izo kukhoti.
7
Papa Wasankha Mkulu wa Zaumoyo ku Vatican Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco, wasankha mkulu wa bungwe lowona za umoyo ku likulu la mpingowu ku Vatican. Malinga ndi malipoti a wailesi ya Vatican, loweruka pa 18 July 2020 Papa wasankha Doctor Giovanni Battista Doglietto kukhala mkulu kapena kuti Director wa bungwe lomwe limawona za umoyo ku likulu la Mpingo ku Vatican lomwe limadziwika kuti Vatican Healthcare Services, Fondo Assistenza Sanitaria (FAS) mchiyankhulo chachitaliyana. Doctor Doglietto walowa mmalo mwa Doctor Stefano Loreti yemwe anali mkulu wa bungweli. Bungwe lowona za umoyoli la Vatican Healthcare Services limaona kuti onse amene amagwira ntchito kulikulu la Mpingo ku Vatican akulandira chisamaliro chabwino cha kuchipatala kukakhala kosoweka kutero pozindikira kuti ntchito zomwe agwira ndi zofunika kwambiri kotero akuyeneranso kusamalidwa bwino polandira chithandizo cha chipatala mu nthawi yake, watero Monsignor Luigi Misto yemwe ndi President wa bungweli pofotokozera Vatican Radio. Monsignor Misto wati likulu la mpingo wa katolika likuyenera kukhala chitsanzo chabwino pa maphunzitso a Mpingo wa Katolika otchedwa Social Teaching of the Church maka pa za ubale ndi umodzi (solidarity) ndi awo omwe akudwala ndipo akusowa chisamaliro ndipo iye wati izi zikuyenera kuyambira kulikuluko ku Vatican. Pali ena omwe sadwala nkomwe koma sasiyabe kupereka ndalama kuthumbali, umenewu ndiye ubale ndi umodzi (solidarity) ndi awo omwe amasowa chisamaliro cha kuchipatala pafupi-pafupi watero Monsignor Misto. Mwezi ndi mwezi aliyense wogwira ntchito ku likulu la Mpingo ku Vatican amapereka ndalama ku thumba la bungwe lowona za umoyoli la Vatican Healthcare Services kapena kuti Fondo Assistenza Sanitaria zomuthandizira atakhala kuti wadwala.
6
Dipo la chithyolakhola limawawa pazovuta Munthu akakwatira mkazi mongozemba osatsata ndondomeko amati wathyola khola. Nthawi ikafika yoti munthu otere alongosole banja, amalipitsidwa madipo osiyanasiyana kwa makolo ndi malume a mkaziyo ndipo limodzi mwa madipowo limatchedwa chithyolakhola. STEVEN PEMBAMOYO adacheza ndi gogo Eveline Posiano a ku Mchinji za dipoli. Choyamba agogo talongosolani kuti dipo ndi chiyani? Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Dipo ndi chidule cha malipiro ndipo monga tidziwa, malipiro amaperekedwa mwaufulu kapena mokakamizidwa kutengera ndi nthawi komanso cholinga cha malipirowo. Kupereka malipiro kapena kuti dipo mokakamizidwa pamakhala kuti pali mlandu pomwe dipo la mtendere sipakhala mlandu. Chindapusacho chimapitanso kwa amfumu Chabwino pano tikukamba za dipo la chithyolakhola, limeneli ndi dipo lanji? Ili ndi limodzi mwa madipo a milandu ndipo mlandu wake umakhala wokhudzana ndi za banja. Chifukwa chodzadzidwa nchinyamata, nthawi zina anthu amangotengana nkukwatirana osadziwitsa makolo kapena kutsatira mwambo koma imakwana nthawi yoti zinthu zilongosoledwe ndiye pamenepo ndipo pamavuta. Kuvuta kwake kotani? Chomwe chimachitika nchoti potengana mudangobana koma pachikhalidwe chathu, pokwatira mkazi, mwamuna amayenera kupeleka dipo lomwe amati chimalo ndipo ili limakhala dipo lomverera poyerekeza kuti mwatsata mwambo komanso mwalemekeza makolo. Tikakhala ngati ife Achewa, imakhala nkhuku yomwe amati ya chinkhoswe kapena ndalama yokwana kugula nkhukuyo. Pakakhala zoonjezera ndiye zimakhala zongogwirizana pakati pa mabanja awiriwo koma sizikhala ngati chithyolakhola. Tsopano timve za chithyolakhola. Chithyolakhola ndilo dipo lowawa kwambiri chifukwa akuchikazi ampangira chipsera mtima kuti udawaderera poyamba potenga mwana wawo osawadziwitsa. Kachiwiri amafuna kuti ukhale ndi mantha kuti ngati uli wankhanza, mwana wawoyo ukamusamale bwino komanso dipolo silipita kwa makolo ndi amalume okha ayi komanso amfumu chifukwa udaphotchola mmudzi mwawo, choncho nawo amayenera kupepesedwa. Akawonkhetsa zonse zomwe ukuyenera kulipira pa chithyolakhola pokha, umadziwanso kuti akulangadi. Nanga utaona kuti zanyanya, sungangomusiya mkaziyo? Poti masiku ano achinyamata alibe mantha ndi umunthu mwina zikhoza kutheka koma taganizirani poti nthawiyi yadza chifukwa chazovuta. Mwina mosakuluwika, mkazi wamwalira mwadzidzidzi ndiye sungakayike kwanu akwawo osavomereza komanso ukapita naye kwawoko amakati Iwo akufuna munthu wamoyo yemwe udaba utathyola khola lawo. Apa, ena ouma mtuma amati sitiyika kaye maliro mpaka mlandu ukambidwe ndipo zonse zoyenera zichitikiretu ndiyetu chithyolakhola chake amanena choti ukhaule chifukwa akudziwa kuti uli pa msampha osapeweka. Pamenepa, ngakhale abale ako amatha kukuthawa mukakumana ndi mtundu wovuta komanso wosamvetsa. Koma pachilungamo chake sikukhala kuvuta kungoti amadziwa kuti mukangoika maliro, mwina uthawa basi iwo apusa. Nanga akakhala kuti mkaziyo sudakamutenge kwawo adadzangokulowera mnyumba yekha? Mpomwe pamafunika kudziwa ndi kutsata mwambo pamenepo. Iweyo ngati mwamuna ndipo ukudziwa mwambo wakwanu, ukuyenera kulingalira zotsatira za kukhalira limodzi kwanuko ndipo choyenera kuchita nkuuza akwanu kuti adzamuthamangitse ngati walephera kutero wekha. Apo ayi umakauza akwanu kuti atsatire kwawo kwa mkaziyo kukafotokoza chomwe chachitika ndipo akuluakuluwo amagwirizana chochita. Apa umakhala kuti watsata mwambo chifukwa walemekeza makolo a mkaziyo pokawagwadira. Apa sipakhala za chithyolakhola ayi. Nanga mkazi oti adzakutulira chifukwa wamuchimwitsa zimakhala bwa? Kukutulira mkazi kuli ndi chisinsi chimodzi: osakana ngati ukudziwa kuti mkaziyo udamuchimwitsadi ndiwe chifukwa chomwe amafuna makolo nkuchoka manyazi kotero amangofuna kuti zinthu zilongosoke mimbayo isadaonekere patali. Apa mumangokambirana za dipo la chimalo kapena miyambo ina koma sipakhala dipo la chithyolakhola kenako mumapanga chinkhoswe nkutengana zinazo nkumakazionera kubanja komweko. Lamulo latsopano lokhudza za mabanja limati mwamuna ndi mkazi akangokhalira limodzi kokwana miyezi isanu, basi banja lakwana. Kodi apa munthu sungatetezedwe ku chithyolakhola? Choti mudziwe nchoti chikhalidwe chidakhalako kuyambira kalekale malamulo asadabwere ndipo kupatula kuti ngati nzika za dziko timayenera kutsatira malamulo, malamulo nawo sadabwere kudzaononga chikhalidwe. Zomwe mukunena inu nzamukhothi koma zachikhalidwe zimathera pabwalo la anfumu kapena mkanyumba komata. Mmenemo mulibe malamulo mukune nawo ndiye siyani kuganiza mobwerera mmbuyo kuti poti mudapita kusukulu ndiye zachikhalidwe mulibe nazo ntchito. Makolo anu tidakulira momwemu ndipo inu mwabadwira momwemu tsono tiyeni tilemekeze chikhalidwe.
1
YCW Imangira Nyumba Mayi Wachikulire Wolemba: Sylvester Kasitomu Bambo mfumu aparish ya banja loyera ayamika ntchito zomwe Bungwe la Young Christian Workers YCW likugwira mu parishiyi. Bambo mfumu a parishi-yi bambo Samson Kumkumbira ndiwo alankhula izi lamulungu pambuyo podalitsa nyumba imene bungweri lamangira banja lina lovutika ku Chilinde 1 mu mzinda wa LILONGWE. Iwo ati zomwe achinyamatawa achita ndi zonyadisa kwambiri kaamba koti apereka chitsanzo chabwino komanso chikondi chosaona nkhope poti athandiza munthu amene sali wa mpingo wawo. Polankhulapo a Francis Berekanyama omwe ndi wapampando wa bungwe la YCW ku parish-yi anati Mulungu wakwaniritsa khumbo la Gulu lawo lomwe anali nawo lofuna kumangira anthu ovutika nyumba. Monga nkhoswe yathu yosefe woyera amatiphunzitsira ifenso tikutsata mapazi ake pokhala achifundo komanso okonda ntchito za manja ngati izi, anatero a Berekanyama. Malinga ndi Berekanyama ntchito yomanga nyumbayi yatenga ndalama zokwana 650,000 komanso achinyamatawa alonjeza kuti apitiliza kuthandziza mayiyu pa mavuto ena ngakhale awamangira nyumbayi.
14
Tizipatsana ulemu moyendamu Abambo ndi anyamata, pali makhalidwe ena omwe mukuyenera kusiya. Makhalidwe onyasa, otopetsa otonza amayi ndi atsikana. Zomati muntu wamkazi akudutsa poteropo abambo ndi anyamata ena nkumayangana mwachidwi chachipongwe ngati mukumusilira munthuyo, nzoipa. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Amayi ndi atsikana ali ndi ufulu oyenda mosasowetsedwa mtendere ndi mayanganidwe otero aja. Ndiye pali miluzi ija mmalizaliza, kulizira amayiwa kaya anzanu pofuna kuti nawo achite chidwi ndi mayi kaya mtsikana amene akudutsa. Ena ndi aja simutha kuugwira mtima koma mpaka mkono wanu ugwire mtsikana kaya mayi mosamulemekeza. Palinso timamoni tosadziwika bwino tija mmapereka mmisewumu. Ena mmakhala kumachemerera kapena kunyoza ziwalo za amayi ndi atsikana akamadutsa. Nchifukwa chiyani simutha kupita pagulu la anthu nkungosamala za inu nokha osalabadirako za anthu ena? Chimavuta nchiyani kuona munthu wa mayi, nkumupatsa ulemu omwe mmapatsa abambo ndi anyamata anzanu? Chifukwatu miluziyi, mamoni, kugwirana ndi zinazi simupangira abambo anzanu. Ndithu mmaganiza kuti munthu wamayi amanka mliyendamu kuti inu mumugwire, kapena kumukuwa kaya kumuyankhulitsa zosadziwika bwino? Chimakupatsani danga loti muzisowetsa amayi mtendere nchiyani? Ili ndi khalidwe lonyasa lochokera mmaganizidwe aja oonera amayi ndi atsikana pansi, kumawayesa ngati anthu omwe mukhoza kuwazunguza mmene mungaganizire.
1
Papa Achita Misa Yokumbukira Ulendo Wake Wokacheza Pa Chilumba cha Lampedusa Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco lachitatu likudzali achita Misa yokumbukira ulendo wake wokacheza pa chilumba cha Lampedusa. Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa achita misa-yi pa 8 July 2020 pokumbukira kuti patha zaka zisanu ndi ziwiri pomwe anakacheza pa chilumba cha Lampedusa mdziko la Italy Patangopita miyezi yochepa atamusankha kukhala Papa pa 13 March 2013, Papa Francisco anakacheza pa chilumba cha Lampedusa mdziko la Italy pa 8 July 2013. Uwu unali ulendo wake woyamba kunja kwa mzinda wa Rome. Izi zikutanthauza kuti chaka chino padutsa zaka zisanu ndi ziwiri Papa Francisco atakacheza pa chilumbachi. Likulu la Mpingo wa Katolika pa dziko lonse, Vatican, lalengeza kuti pa tsikuli lachitatu pa 8 July 2020 Papayu achita Misa yokumbukira ulendo wake wokacheza pa chilumba cha Lampedusa. Papa Francisco achita Misayi mtchalichi lalingono la Casa Santa Marta ku Vatican. Malinga ndi mliri wa Coronavirus ndi anthu ochepa chabe omwe akhale nao pa Misayi yomwe ikuyembekezeka kuyamba 11 koloko mmawa nthawi ya ku Rome komanso Malawi. Ndipo zadziwika kuti ogwira ntchito mu office yomwe imaona za chitukuko cha thunthu cha munthu ku likulu la Mpingowu Dicastery for Promoting Integral Human Development ndi omwe akhale nao pa Misayi popeza nkhani ya anthu othawa kwao pa zifukwa zosiyana-siyana ili pansi pa officeyi. A Katolika pa dziko lonse la pansi ali ndi mwayi wotsatira Misayi pa wayilesi ya kanema ndi makina a intaneti. Ulendo wa Papa Francisco wokacheza pa chilumba cha Lampedusa udaonetsa poyera chidwi chomwe Papayu ali nacho pa nkhani ya anthu othawa kwao pa zifukwa zosiyana-siyana. Chilumba cha Lampedusa chimalandira anthu othawa mmaiko awo pa zifukwa zosiyana-siyana ndipo ambiri ndi ochokera mmaiko a ku Africa. Papa Francisco adaganiza zokacheza pa chilumbachi atawerenga nkhani zomvetsa chisoni za anthu ochokera ku Africa omwe amayenda ulendo wa utali pa madzi pokasakasaka moyo wina ku maiko a ku ulaya ndipo kuti ambiri a anthuwa amafera mnjira. Ali pa chilumba cha Lampedusa Papayu adachita Misa ndipo adaponya nkhata ya maluwa mmadzi a nyanja yaikulu ya Mediterranean pokumbukira onse omwe amamira pa madzi pa ulendo wopita ku chilumbachi. Malinga ndi malipoti pa 3 October mchaka cha 2013 anthu oposa 360 omwe amachokera ku Libya anamira pa nyanja yaikulu ya Mediterranean asanafike pa chilumba cha Lampedusa.
13
Moto wayaka ku Nkosini Pasanadutse nkomwe mwezi chilongere Inkosi Yamakosi Gomani Yachisanu ku Ntcheu, fumbi labuka pomwe mbali ina kubanjalo ikukakamiza wogwirizira, Rosemary Malinki kutula pansi udindo komanso kupepesa ati pa chipongwe chomwe adatulutsa pa mwambo wolonga ufumuwo. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mbaliyi yati Malinki adalankhula ngati kulibe mawa ku mwambo wolonga Mswati Willard Gomani kukhala Inkosi Gomani yachisanukapena kuti Ngwenyama pa 5 Ogasiti ku Nkosini, likulu la ufumu wachingoniku Lizulu mbomalo. Mneneri wa okhumudwawo, Dingiswayo Romeo Samson Philip Gomani, wauza Tamvani Lachiwiri msabatayi kuti tsopano abanja akukumana kukalondolera momwe ufumuwo uziyendera. Koma Malinki wati angapepese pokhapokha nkhaniyo itafika ku Nkosini kwa Gomani. Malinki wati ndi Ngwenyama yokha ili ndi mphamvu yochotsa kapena kusankha yemwe akuyenera kugwirizira ufumuwo. Dingiswayo wati mwa zina, Malinki adaphotchola pomwe amaunikira kuti mkazi naye akhoza kulowa ufumu wa Gomani pofanizira Namlangeni, yemwe ati adalamulira ngakhale adali mayi. Chatsitsa dzaye Malinki adanyanyula mbaliyi ati popitiriza kuti Namlangeni amalamulira amuna enieni osati amasiku anowa. Dingiswayo wati Malinki adapitirizanso kuti ufumuwo supita kwa ana omwe mayi awo sadalowoledwe, zomwe ati zidawanyanyulanso. Pachingoni, ufumu wathu umakhala mnyumba imodzi; susinthana. Umakhala nyumba yomweyo mpaka Yesu adzabwere, adatsendera Malinki. Apa abanjawa, motsogozedwa ndi Dingiswayo, adatulutsa uthenga mnyuzipepala Lachisanu pa 10 Ogasiti, kulengeza kuti Malinki apepese. Dingiswayo, pouza Tamvani adati mkazi sangalamule pa ufumu wa Gomani komanso Malinki sakuyenera kukhala wogwirizira pomwe mfumu yadzozedwa. Iye adatinso Malinki adalowoledwa kotero za ufumu wa Gomani sizikuyeneranso zimukhudze. Gomani IV adasiya ana atatu ndipo womaliza ndi Mswati koma onsewo akuchokera kwa amayi osiyana. Ubwino wake ana onse timakhala nawo pamodzi ngati mbumba. Mawu onena kuti ufumuwo supita kwa ana obadwira [kunja kwa banjalo] adatikwiitsa. Ichi nchifukwa tikuti apepese, adatero Dingiswayo. Koma titamufunsa kuti achita chani ngati zokambiranazo sizichitika, iye adati imeneyo ndi nkhondo komabe iwo ayesetsa kuti zokambiranazo zitheke. Pa za mafumu achingoni achikazi monga T/A Kachindamoto, iye adati akudziwa za ufumu wa Gomani. Koma mfumu yatsopanoyi idati singalankhule kanthu. Sindikudziwa yemwe angalankhule pankhaniyi. Padakakhala zoti dziko lidziwe tikadakuuzani, idatero Ngwenyamayo. Boma sililowerera Nduna ya maboma aangono ndi chitukuko cha kumudzi, Grace Zinenani Maseko, yati boma sililowerera chilichonse pa nkhaniyo. Maseko adati zomwe agwirizane a banja boma limvera zomwezo. Kaya asankha wina wogwirizira pomwe Mswati akupita kusukulu ife tivomereza, adatero. Mbiri ya ufumu wa Gomani Philip Gomani yachiwiri idabereka Willard, Samson, Lineti, Hastings, Simasi, Titus ndi ena. Willard yemwe adali Gomani wachitatu adabereka Rosemary ndi Kanjedza yemwe adaali Gomani yachinayi. Kanjedza adabereka Frank, Zwelithini ndi Mswati yemwe ndi mfumu pano koma anawa adabadwa kwa amayi osiyana. Samson adabereka Dingiswayo yemwe akukakamiza kuti Malinki apepese.
8
Mulanje yadya wani pa chitukuko Boma la Mulanje ladya wani pogwiritsa ntchito ndalama za thumba la chitukuko mdera la phungu la Constistuency Development Fund (CDF), pulogalamu yosanthira momwe thumbali likugwiritsidwira ntchito mmaboma 14 a dziko lino ya Kalondolondo yapeza. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zidadziwika Lachiwiri pamsonkhano wounikira momwe ntchito za chitukukozi zidayendera mbomali umene udachitikira ku Hapuwani Village Lodge mbomalo. Malinga ndi kafukufuku amene bungwe la Womens Legal Resource Centre (Wolrec), lomwe limagwira ntchito mogwirizana ndi Kalondolondo, magawo 73 mwa 100 aliwonse a ntchito zachitukuko mmadera a aphungu 9 a mbomalo adatha. Mkulu wa Kalondolondo Jephter Mwanza adati adakhutira ndi momwe ntchito zachitukuko zayendera ku Mulanje. Zambiri mwa ntchito za chitukuko ku Mulanje zakhala pangono kutha. Apa zili bwino poyerekeza ndi maboma ena amene kwamangidwa zinthu zosalingana ndi ndalama zomwe zidaperekedwa, adatero Mwanza. Bwanamkubwa wa boma la Mulanje Jack Nguluwe adati kuchita zinthu mosabisa ndiko kwachititsa kuti ndalama za CDF zisalowe mmatumba mwa anthu. Chaka chilichonse, dera la phungu aliyense limapatsidwa K7 miliyoni yogwirira ntchito za chitukuko zingonozingono. Ena amaganiza kuti boma likapereka ndalamazo zimapita kwa phungu ndipo iye akhoza kusolola. Sizili choncho chifukwa zimafika kuofesi kwathu ndipo phungu amangonena ntchito za chitukuko zimene anthu a mdera lake akufuna. Ofesi yathu ndiyo imagula katundu ndipo malisiti onse timasunga komanso timawapereka kwa makomiti owona zachitukuko, adatero Nguluwe. Ndipo phungu wa dera lapakati mbomalo Kondwani Nankhumwa adati mgwirizano ndiwo ukufunika pa chitukuko. Iye adatsagana ndi phungu wa kumpoto mbomalo Stephen Namacha komanso wa kumwera cha kummawa Ben Bonongwe. Popanda mgwirizano, palibe chitukuko. Timagwira ntchito limodzi osatengera kuti uyu ndi wotsutsa kapena wachipani cholamula. Izi ndizo zathandiza kuti chitukuko mboma lino chipite patsogolo, adatero Nankhumwa.
2
Mtima pansi, makuponi akubwera Boma lati anthu omwe chiyembekezo chawo chili pazipangizo zaulimi zotsika mtengo za sabuside, asataye mtima ndipo achilimike kukonza mminda mwawo kaamba kakuti makuponi ogulira zipangizozi afika sabata ikudzayi Lolemba. Chilimbikitsochi chadza pomwe anthu adali ndi nkhawa kuti mvula yayandikira komanso madera ena yagwa kale mwa ndii koma tsogolo la makuponi ogulira zipangizo silimaoneka bwinobwino. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Fisp fertiliser and seed will be handled by private traders this year Mvulayi yagwa mmadera ena mzigawo zonse kuyambira sabata zitatu zapitazo ndipo pomwe anthu ena ali jijirijijiri mminda mwawo, anthu ena amadandaula kuti mwina mwayi wogula zipangizozi ukhoza kudzafika mmera utakwinimbira. Si zongoganiza ayi, taziwonapo mmbuyomu kuti pomwe zipangizo zikufunika, kumisika kulibe kapena makuponi sadafike ndiye umayamba ntchito nkudzakhumudwa pambuyo, adatero Ammon Yesani Bakulo, mmodzi mwa alimi omwe akuyembekezera kulandira nawo makuponi kwa Chiseka mboma la Lilongwe chaka chino. Koma nduna ya zaulimi, mthirira ndi chitukuko cha madzi, George Chaponda, wati nkhawayi njopanda mtsitsi kaamba koti mkati mwa sabata ikudzayi, makuponi ayamba kufika ndipo azigawidwiratu. Ndikunena pano, makuponi adindidwa kale moti sabata yamawayi akhala akufika ndipo nthawi yomweyo azigawidwa kuti anthu ayambe kugula zipangizo. Sitikufuna kuti munthu adzadandaule patsogolo, ayi, adatero Chaponda. Mndondomeko ya chaka chino muli kusintha kungapo komwe Chaponda wati kuthandiza kupititsa patsogolo cholinga cha pologalamu ya sabuside. Kwina mwa kusinthaku ndi kukhazikitsa mitengo yatsopano ya makuponi, kutsitsa chiwerengero cha anthu omwe apindule mupologalamuyi, komanso kupereka kontirakiti kwa makampani abizinesi kuti agulitse nawo zipangizozi. Kubwera kwa makampani abizinesi ndi kumodzi mwa kusintha komwe kuthandize kwambiri ndipo kupangitsa kuti zipangizo zotsika mtengo zizipezeka pafupi ndi anthu komanso chifukwa cha mpikisano, mitengo isanyanye poti aliyense azifuna kugulitsa, adatero Chaponda. Mupologalamu ya chaka chino, mtengo wa kuponi ya feteleza wokulitsa ndi wobereketsa uli pa K15 000 pomwe mbewu za chimanga papaketi ya 5kg kuponi yake ili pa K5 000 ndipo mbewu zamtundu wa nyemba zolemera 2kg mpakana 3kg kuponi yake ili pa K2 500. Chaponda adati mitengoyi ndi yomwe boma likuwonjezera pa mlimi, osati mitengo yogulira kumsika. Mwachitsanzo, ngati thumba la feteleza lili pa K18 000, ndiye kuti boma laperekako K15 000 ndipo K3 000 yotsalayo apereke ndi mlimi, adatero Chaponda. Malingana ndi malipoti a zanyengo, chaka chino, mvula ikhoza kugwa bwino moti unduna wa zamalimidwe, mthirira ndi chitukuko cha madzi ukulimbikitsa alimi kuti alimbikire ntchito za mminda.
4
Chaponda ndi Mfulu, Alibenso Mlandu Bwalo la High Court ku Zomba lalamula kuti nduna yakale ya zamalimidwe Dr. George Chaponda ndi mfulu kaamba koti alibe mlandu woti ayankhe pa nkhani yokhudza kugula chimanga mdziko la Zambia komanso nkhani yopezeka ndi ndalama ndalama zokwana 95 million-kwacha ndi ndalama zina zakunja, kunyumba kwake. Alibenso mlandu-Chaponda Judge yemwe amamva mlanduwu Justice Redson Kapindu wati apilo yomwe bungwe la ACB linachita, inalibe mfundo zokwanira zoti mlanduwu upitilire kumvedwa choncho anati akugwirizana ndi chigamulo chomwe bwalo lalingono la Chief Resident linapereka pa 18 May 2018 kuti Dr. Chaponda alibe mlandu oti ayankhe. Mmawu ake pambuyo pa chigamulochi, Dr. Chaponda athokoza Mulungu kaamba kopambana mlanduwu. Ndipo mmawu ake, yemwe amayimira bungwe la ACB pa mlanduwu Anafi Likwanya, wati wagwirizana ndi chigamulocho ndipo waphunzira zambiri kudzera pa mlanduwu chifukwa akakonza zolakwika zonse kuti tsiku lina adzachite bwino pa milandu ina.
7
Sitilembetsa mayeso Aphunzitsi amene alembetse mayeso a Fomu 4 a chaka chino omwe ayambe pa 22 June, aopseza kuti sadzagwira ntchitoyo ngati Unduna wa Maphunziro salandira ndalama zomwe amapatsidwa akamapita kutchuthi. Izi zikudza pamene ophunzira ndi makolo ena msukulu za pulaimale akudandaula kuti sitalaka ya aphunzitsi isokoneza kukonzekera mayeso a temu yachitatu omwe ayambe kumayambiriro kwa mwezi wa July. Aphunzitsi pafupifupi 63 000 akuchita sitalaka pofuna kukakamiza boma kuti liwapatse ndalama zomwe amalandira akamapita kutchuthi za chaka cha boma cha 2016-2017 chomwe chithe pa 30 June. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Apolisi adathamangitsa ana ku Chileka Tamvani wapeza kuti pambali pa sitalaka imene yachititsanso kuti ana a sukulu za pulaimale zina apite pamsewu kudandaula kuti sakuphunzira, zokonzekera mayeso a Fomu 4 zili gwedegwede chifukwa kusamvana pakati pa boma ndi aphunzitsi kukupitirira. Mlembi wa Teachers Union of Malawi (TUM) Charles Kumchenga adati palibe mphunzitsi alembetse mayeso msukulu komanso kuyanganira mayeso a MSCE asadalandire ndalama ya tchuthi pachaka. Boma limayenera kusamalira umoyo wa oyanganira mayeso omwe ndi aphunzitsi. Ophunzira akulangika chifukwa cha kholo lathu, boma. Boma lidalemba ntchito mphunzitsi kuti asamalire ana kumidzi ndipo lili ndi mayankho pa mavuto onsewa, iye adatero. Naye mkulu wa TUM, Willie Malimba, adati aphunzitsi ndi okhumudwa chifukwa boma ndi onse okhudzidwa akukanirana zofuna zawo. Iye adati boma lingopereka ndalamazi osati kumangoyankhula zomwe zina zikulowa mabodza. Bungweli lati lipereka chenjezo ku boma ndi nthambi ya mayeso ya Malawi National Examination Board (Maneb) kuti palibe mphunzitsi ayanganire mayeso asadalandirenso ndalama ya ntchitoyi. Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a za maphunziro mdziko muno la Civil Society Education Coalition (CSEC) Benedicto Kondowe wati mayeso a MSCE akhoza kupepuka malinga ndi zomwe zikuchitikazi. Kukhumudwa komwe kulipo kudzetsa kubera mayeso. Choopsa chichitika pa maphunziro mdziko muno ngati sitisamala. Kulemba kwa mayeso a gawo lachitatu msukulu za pulaimale mu July nkosathandiza chifukwa umafunsa zomwe waphunzitsa ndipo apa ana sakuphunzira. Tisaiwalenso kuti awa ndi mayeso woti ana apite kalasi ina, iye adatero. Iye adati ndi wokhumudwa ndi kulekerera kwa boma pa nkhani ya ndalama ya tchuthiyi ndi mavuto ena aphunzitsi omwe likuyenera kukonza. Boma silimvera zokhumba za aphunzitsi ndipo avutika kwa nthawi yaitali. Nthawi yakwana yokakamiza boma kupereka zomwe ndi zawo. Kuti boma lilimbikitse maphunziro abwino, makolo alimbe mtima kulifunsa chifukwa chomwe ana awo sakuphunzira ndiponso ana achite zomwezo, adatero Kondowe. Msabatayi, aphunzitsi adalowa sabata yachiwiri akuchita sitalaka ndipo ana nawo adalowerera sitalakayo. Ana ophunzira msukulu zina ku Blantyre, Ntcheu ndi Balaka adapita pamsewu kuyambira Lolemba pofuna kukakamiza boma kumva kulira kwa aphunzitsi awo. Pambali potseka misewu ina, ana enanso adamenya ndi kuvulaza apolisi atatu ku Lunzu mumzinda wa Blantyre, pomwe anthu 23 kuphatikizapo ophunzira 9 adamangidwa ku Ntcheu. Apolisi adathamangitsa ana ku Ndirande ndi utsi okhetsa misozi. Kafukufuku wa Tamvani adasonyeza kuti ana mmaboma ambiri mdziko muno sakuphunzira. Ana ndi aphunzitsi ena sakupita ndi kusukulu komwe. Mwachitsanzo, pasukulu ya pulaimale ndi sekondale ya Katoto mumzinda wa Mzuzu, tidapeza ana ali khumakhuma kulingalira za tsogolo lawo. Ena adali kusewera mpira. Sindkuona bwino za kutsogoloku. Tikawafunsa aphunzitsi sitalaka itha liti, akutiyankha kuti sakudziwa, si zili mmanja mwawo. Ena a chifundo akumatiphunzitsa nthawi zina, adatero wophunzira wa Fomu 2.
3
Alosera mvula kugwa mochuluka Nthambi yoona za nyengo ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati mvula yamphamvu ikhala ikugwa kwa masiku angapo motsatizana. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Uwu ungakhale mpumulo polingalira momwe mbewu zafotera mminda komanso lingakhale tsoka polingalira ngati mvulayo ingachulukitse monga zidalili chaka chatha mmadera ena. Mchikalata chosonyeza momwe nyengo ikhalire masiku angapo akudzawa, nthambiyo idati mvula yamphamvuyi ikhala ikugwa dziko lonse pafupifupi sabata yatuthu kuyambira lachinayi lapitali. Kaamba ka ngamba, chimanga china chidanyala Mphepo yomwe ikuomba kuchokera mmadera osiyanasiyana, ipangitsa kuti mvula yamphamvu kwambiri izigwa makamaka kuyambira Lamulungu pa 17 January, 2016. Mmadera ambiri, anthu ayembekezere nyengo yotentha masana panthawiyi, idatero nthambiyi mchikalatacho. Mkulu wa nthambiyo Jolam Nkhokwe adati mmasiku angapo apitawa, mvula adayeserako mmadera a mchigawo chapakati ndi kumpoto pomwe mmadera a kumwera, mvulayi imagwa monyentchera. Mneneri wa nthambiyo, Ellen Kululanga, adati izi nzosadabwitsa chifukwa ndimo zimakhalira kukakhala mphepo ya El Nino monga momwe azanyengowa adalengezera kumayambiriro a mvula. Malawi ali mmphepete mwa zigawo ziwiri za Africa kumwera ndi kummawa zomwe zimapangitsa kuti kabweredwe ka mvula kazisiyana. Mvula imavutirako mchigawo cha kumwera kaamba kakuti chili mbali ya kumwera kwa Africa. Chigawo cha kumpoto chomwe chili kumbali ya kumawa kwa Africa, mvula imachulukirapo moti ndi mphepo imeneyi ya El Nino, madera a kumwera mvula ivutirapo pomwe kumpoto ndi madera ena pakati zinthu zikhalako bwino, adatero Kululanga. Ogwira ntchito zotukula ulimi mmaboma osiyanasiyana adatsimikizira nyuzipepala ya The Nation kuti ngamba yomwe idagwayi yaononga mbewu zambiri mmadera osiyanasiyana. Ena mwa omwe adatsimikizira izi ndi wachiwiri kwa oyendetsa ntchito za Blantyre ADD Aggrey Kamanga komanso otukula ntchito zaulimi mboma la Machinga Palichi Munyenyembe omwe adati mvula idadula ndipo alimi ali ndi nkhawa.
18
Moto utentha misika, njakata izinga A malonda omwe katundu wawo adapsera mmisika ya mavenda ya Tsoka ku Lilongwe komanso wa Blantyre akulira chokweza, uku akupempha boma kuti liwakongoze kangachepe koyambiranso bizinesi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Moto udatentha misikayi Lamulungu lapitali, kufikitsa chiwerengero cha misika yakupsa pa 10 mzaka ziwiri. Mneneri wa polisi kumwera komanso mkulu wa khonsolo ya mzinda wa Mzuzu ati kusasamala pakapalidwe ka magetsi kungakhale chimodzi mwa zomwe zachulutsa ngozi za moto mmisika. Mneneriyu, Davie Chingwalu, wati kupatula msika wa Blantyre womwe sakuuganizira kuti wayaka kaamba ka magetsi, zofufuza pa ngozi za misika ingapo zimatulukira zizindikiro za kusagwiritsa ntchito magesti moyenera. Iye wati nkuthekanso kuti omwe amaphika mmisika komanso moyandikana ndi misikayo sazimitsa bwino lomwe moto kapena kandulo poweruka. Mkulu wa khonsolo ya mzinda wa Mzuzu, Victor Masina, wati zofufuza pa moto omwe udatentha msika wa Mataifa mu mzindawo zidaonetsa kuti padali kusasamala kwa magetsi. Iye adati pali anthu ena omwe akamanga golosale amakokeramo okha moto wa magetsi zomwe tsiku lina zimadzabutsa moto. Pomwe Tamvani idayendera msika wa Blantyre pomwe udangopsa, mavenda adadandaula kuti ndi bwino boma kapena mabanki apereke ngongole kwa mavendawa zomwe ziwathandize kuyambiranso mabizinezi awo. Rafael Nameta Mwini sitolo ya zamagetsi ya Ranambe Electronics, Rafael Nameta, akuti wataya katundu wa pafupifupi K7.6miliyoni. Wati patapezeka ngongole, mavendawa angakhale mmagulu nkuyambiranso bizinesi. Steve Maliyoti amachita buzinesi yogulitsa lamya mumsikaku ndipo akuganiza kuti boma liyenera kuthandiza mavendawa chifukwa iwo ndi Amalawi omwe akufuna thandizo laboma. Mkulu wa khonsolo ya Blantyre, Ted Nandolo adakana kuikirapo ndemanga pa kupsa kwa msikawu, ati sadalandire lipoti la zomwe zidadzetsa motowo kumsika wa Blantyre. Koma Chingwalu adati zofufuza zikulunjika koti adayatsa moto adali ana ongoyendayenda. Iye wati mwana wina wa zaka 12 yemwe apolisiwa akumusunga mchitolokosi akuulula kuti anzake anayi ndi amene adayatsa msikawo. Iye wati akuganizira kuti apeza zenizeni kuchoka kwa mwanayo. Izi zatipatsa ntchito yogwira ana onse oyendayenda mmisika usiku. Tikawagwira tiwapereka kwa makolo awo ndipo omwe alibe makolo apita kumalo osungira ana amasiye.
2
Kasambara: Kulimbikitsa anthu mkuimba Martha Kasambara ndi woimba nyimbo za uzimu wokhala ku Mzuzu. Iye ali ndi zimbale ziwiri ndipo mu December chaka chino adzakhazikitsa chimbale chake chatsopano chotchedwa Amasamala. Mtolankhani wathu DAILES BANDA adacheza naye motere: Tikudziweni. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Ndine Martha Kasambara wa mmudzi mwa T/A Malanda Ku Chintheche mboma la Nkhata Bay. Ndili pabanja ndipo ndili ndi mwana mmodzi. Akutulutsa chimbale chachitatu: Kasambara Mbiri ya maphunziro? Ndidaphunzira pulaimale yanga pa Lilongwe LEA pomwe ndidalemba mayeso anga a Sitandade 8, sukulu ya sekondale ndidaphunzira ku Chipasula. Ndidakapanga maphunziro a uphunzitsi ku Tanzania komwe ndidaphunzitsa kwa ka nthawi pangono ndipo padakalipano ndikupanga bizinesi. Tatifotokozerani mbiri ya maimbidwe anu. Ndidayamba kuimba ndili wachichepere kwambiri koma chimbale changa choyamba ndidatulutsa mu 2008 ndipo chinkatchedwa kuti Zonse ndi Yesu, chimbale chachiwiri, Nganganga ndi Yesu, chidatuluka mu 2010. Chimbale chatsopano chotchedwa Amasamala ndichikhazikitsa mu December chaka chino. Uthenga waukulu omwe wanyamula ndi wotani? Kwakukulu uthenga omwe uli mchimbalechi ndi wa chilimbikitso kwa Akhristu anzanga mnyengo zili zonse zomwe iwo akudutsamo. Yesu amasamala anthu ake ndipo tikamudalira iye sitidzakhumudwa chifukwa chisomo chake ndi chokwanira. Kodi mfundo za nyimbo zimenezi mumazitenga kuti? Nyimbo zanga kwambiri zimachokera pa maulaliki a kutchalitchi komanso ndikamawerenga Baibulo ngakhalenso nthawi zina zinthu zomwe ndikuona ndi kukumana nazo. Ndi zinthu ziti zomwe mungakonde kuti zisinthe kumbali ya zoimba mMalawi muno? Mmalo ojambulira nyimbo mwathu mukufunika zipangizo zojambulira nyimbo za mphamvu, ngati mmene kulili ku maiko a anzathu monga ku South Africa, chifukwa nyimbo zimamveka bwino kwambiri. Phindu Mukulipeza mukuimbaku? Mmbuyomu zinthu zimavuta koma pakali pano ndi chimbale chatsopanoch tsogolo lopindula likuoneka.
9
Mafumu atsegula Njira ya kampeni Pamene kampeni yafika pachiindeinde, zipani zandale zati nzokhutira ndi momwe mafumu akuperekera mwayi wochititsa misonkhano yokopa anthu mmadera mwawo kwa zipani zotsutsa. Katswiri wa za ndale, George Phiri, wati zimaterezimatere bwenzi zikoma ndipo wayamikira mafumu potsegula njira kwa zipani zonse. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Tsopani MCP ikuchititsa misonkho yokopa anthu ku Thyolo momasuka Bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) lisadatsegulire kampeni mafumu ena amaletsa zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM kuchititsa misonkhano yokopa anthu mmadera mwawo. Mwachitsanzo, mafumu a ku Thyolo amakaniza zipani za MCP ndi UTM kuchititsa msonkhano mbomalo kaamba koti ndi kuchipinda kwa mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, ndi chipani chake cha Democratic Progressive Party [DPP]. Mneneri wa MCP, Maurice Munthali, adati mmbuyomu chipani chake chidakonza msonkhano kwa Bvumbwe mboma la Thyolo, koma mafumu adachiuza kuti ena apempha kale malo a msonkhanowo, zomwe adati zidali zabodza. Tidazindikira pammbuyo pake kuti nzabodza popeza padalibe yemwe adapempha malowo. Posachedwapa tidapemphanso ndipo adatilola. Tidachititsa msonkhano opanda vuto lililonse. Izi zikusonyeza kuti zinthu zasintha, adatero Munthali. Naye mlembi wa UTM, Patricia Kaliati, adati mmbuyomu mafumu adawaletsa kuchititsa msonkhano wokopa anthu kwa Folopeni mbomalo, komanso adauza anthu a mmidzi yawo kuti asapite ku msonkhanowo. Koma padakali pano tikapita akumatilandira nkutilola kuchititsa misonkhano opanda vuto lililonse chifukwa cha ndondomeko zomwe MEC idakhazikitsa, adatero Kaliati. MEC idasayinitsa mafumu ndondomeko zoti atsatire nthawi ya kampeni. Mwa zina, mafumu sakuyenera kukondera kapena kuletsa zipani zotsutsa kuchititsa misonkhano yokopa anthu mmadera mwawo. Mlembi wa UDF, Kandi Padambo, adati kapeni isadayambe chipani chake chikhala chikukumana ndi mikwingwirima yosiyanasiyana mchigawo chakumpoto komwe chimakachititsa misonkhano yokopa anthu. Iye adati UDF idatsala pangono kusiya kupita mchigawocho chifukwa cha mavutowo. Mmalo angapo tidabwedzedwa, koma osatiuza zifukwa zake. Koma panopa tikapita mmadera omwe aja akumatilandira nkutipatsa mwayi wochititsa misonkhano, adatero Padambo. Mfumu Lukwa ya mboma Kasungu idati ngati mafumu amachitadi zimenezo amalakwa. Katswiri wa za ndale Phiri adati nzokoma kumva kuti mafumu tsopano akupereka mwayi wochititsa misonkhano kwa zipani zonse. Iye adati zomwe mafumu akuchita nkulambula njira yoti mdziko muno mudzachitike zisankho za mtendere.
8
Akatolika Mdziko Muno Awapempha Kuti Akhazikike pa Chikhristu Akhristu a mpingo wa katolika mdziko muno awapempha kuti achilimike mmapemphero pawokha mu nyengo ino pomwe mpingowu wayamba wayimitsa zochitika zake monga mapemphero a lamulungu pofuna kuwatetedza ku kachilombo ka Coronavirus. Mlembi wa zautumiki mu arkidayosizi ya Blantyre bambo Alfred Chaima ndi amene anena ku Limbe Cathedral pothilirapo ndemanga pa nkhaniyi. Iwo ati ngakhale kuti ndi zowawa kuti tsopano palibenso kupemphera kudzera ku matchalichi ngati kale, akhristu akuyenera kumvetsetsa pa chitetezo cha mpingo ndi anthu ake pa matendawa. Ndi zinthu zowawa kuti sitimakumana ngati mpingo pamodzi ndi kupemphera koma pamene tikuchita zimenezi tikuyenera kukula mu chikhulupiriro, anatero bambo Chaima. Iwo atinso a Papa apempha kuti akhritsu asate njira zomwe a zaumoyo akupereka ndipo apemphanso kuti asapereke mpata kwa kachilombo kameneka kudzera mu kukumana ngati mpingo.
13
Apempha Makolo Achikatolika Apitirize Kuphunzitsa Ana Maphunzitso Ampingo Pamene Tchalitchi Zatsekedwa Makolo a mpingo wa katolika mdziko muno awapempha kuti apitirize kuphuzitsa ana ziphuzitso za mpingo, pano pamene mpingo wayimitsa zochitika zake kaamba ndi nthenda ya COVID-19. Mkulu wa mu ofesi yowona za utumiki wa ana, mu akidayosizi ya Blantyre Bambo Matias Thawani, apereka pempholi pothilirapo ndemanga pa udindo wa makolo mu nyengoyi. Bambo Thawani ati makolo akuyenera kukumbukira malumbiro awo amene anachita pa tsiku la ubatizo ophunzitsa ndi kuwongolera ana pa moyo wachikhristu. Monga anawa tikudziwa kuti amaphunzitsidwa ku tchalitchi, tsopano ndi udindo wa makolo kuti agwire ntchito imeneyi pozindikira kuti kunyumba ndi tchalitchi yoyambirira, anatero bambo Thawani. Iwo ayamikiranso mawailesi a mpingo wa katolika monga Radio Maria amene akumachita mapologalamu a ana monga katikisimu wa ana mupingo omwe ukuthandiza ana kuti asaiwale maphunzitso a mpingo.
13
Akwizinga wogwirira wamisala Apolisi ya Kanengo ku Lilongwe anjata bambo wa zaka 46 Nelson Chiudzu pomuganizira kuti adagwirira mai wa zaka 49 Maria. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Apolosi ati abale a mai ogwiririrayo adagwira Chiudzu akuchotsa ulemu maiyo nkumutengera kupolisi ndipo akuyembekezera kukaonekera kubwalo la milandu kukayankha mlandu ogonana ndi munthu wamisala zomwe zimatsutsana ndi ndime 139 ya malamulo a dziko lino. Mtambo: Zalakwika Nzoonadi tamumanga koma sitidapeze kuti cholinga chake chidali chiyani. Mlandu wake walembedwa kale moti nthawi iliyonse akaonekera kubwalo la milandu pa zomwe adachitazo, adatero mneneri wapoliasi ya Kanengo Laban Makalani. Iye wati Chiudzu wauza apolisi kuti wakhala paubwenzi wamseri ndi mai wozungulira mutuyo kuyambira mwezi wa December 2017 ndipo ati samaona cholakwika chilichonse pazomwe amachitazo. Mkulu oona za ufulu wa anthu Timothy Mtambo wadzudzula mchitidwewu chifukwa maiyo saganiza bwino ndipo akhoza kulola chilichonse osadziwa zotsatira zake. Ichi nchifukwa chake boma lidakhazikitsa malamulo kuti munthu wa nzeru zake sangagone kapena kupanga ubwenzi ndi wamisala kapena mwana chifukwa sadziwa chomwe akuchita, adatrero Mtambo. Iye adati anthu alunga ali ndi udindo oyanganira olumala omwe wamisala ali mgulu ndipo ngati anthu alungawo akuyambitsa kuchita nkhanza anthu oyenera kuwaterewo, ndiye kuti miyoyo ndi ufulu wawo zili pachiopsezo. Mtambo wati abale a anthu amisala akuyenera kukhala maso pa komwe mbale wawoyo akupita kapena kulowera chifukwa anthu oyipa mtima amawapezerera komwe ali okhaokha chifukwa amadziwa kuti alibe mphamvu yokana chilichonse. Mai Asina Rajab a mboma la Salima ati nthawi zina nkhanza zotere siziyamba chifukwa cha chilakolako chokha komanso zikhulupiriro zomwe asinganga ena amanamiza anthu ofuna kukhwima. Iye adati munthu wamisala ali ngati mwana yemwe sangathe kudzisamalira yekha ngati mkazi ndiye zimadabwitsa kuti abambo ena amalimba mtima nkumagona ndi munthu otereyo osalingalira za ukhondo wake ngati mkazi. Pamoyo wa mkazi pamachitika zambiri ndipo amayenera kudzisamalira mwapadera tsono zimadabwitsa kuti abambo ena saona zimenezi mpaka kumagona naye. Sichabe ayi koma pali zifukwa zina,adatero Rajab.
7
Papa Wapereka Mafuno Abwino a Pasaka kwa Akatolika Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wafunira zabwino akhristu a mpingowu pomwe akhala akuchita chaka cha kuuka kwa Ambuye Yesu. Papa Francisko Malingana ndi malipoti awailesi ya Vatican, Papa amalankhula izi mu uthenga wake pomwe amachita nawo njira ya mtanda ku likulu la mpingowu ku Vatican. Chaka chino mapempherowa achitika popanda anthu, potsata ndondomeko zomwe zayikidwa zoteteza kufala kwa nthenda ya COVID-19, ndipo akhristu a mpingo-wu anatsatira bwino mwambo-wu kudzera pa kanema, wayilesi ndi makina a intaneti. Mapemphero a chaka chino a Njira ya Mtanda adakonzedwa ndi anthu ena a ku ndende ya Padua mdziko la Italy.
13
Asaka ofukula manda ndi kutengamo ziwalo Apolisi ku Kanengo mumzinda wa Lilongwe ati akufunafuna anthu aupandu omwe adafukula manda ndi kudula ziwalo za mtembo wa mtsikana yemwe adamwalira masiku angapo apitawo mmudzi mwa Mgona, mdera la T/A Chitukula mboma la Lilongwe. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Akuti awa ndi malodza: Wisiki Pofotokoza nkhaniyi, mneneri wa polisi ya Kanengo, Esther Mkwanda, adati iwo adalandira lamya yonena kuti anthu ena achipongwe, omwe zolinga zawo sizikudziwika bwino, adafukula manda ndi kudula ziwalo zingapo za mtembo wa Maria Roja, wa zaka 18, yemwe adamuika mmandamo. Chimene chidachitika nchakuti ifeyo tidangolandira foni mmamawa yonena kuti anthu apeza manda ofukulidwa kwa Mgona. Ife tidathamangirako ndipo tidapeza kuti mandawo ndi ofukulidwadi ndipo kuti thupi lili mdzenje momwemo koma atalichotsa mbokosi lomwe adachita chophwanya, adafotokoza Mkwanda pouza Msangulutso. Adapitiriza kunena kuti adapeza kuti achipongwewo adachotsa maso, lilime, milomo, chala chamkombaphala chakumanzere, komanso ziwalo zobisika. Iye adati adachita kukhomanso bokosilo mothandizana ndi anthu a mmudzimo ndipo adaikanso thupilo mmandamo. Mkwanda adati ngakhale apolisi sadagwirebe wina aliyense pankhaniyi, iwo ayesetsa kuti omwe adachita khalidwe lachilendoli agwidwe kuti akayankhe mlandu kukhothi. Mayi Janet Wisiki, yemwe ndi mayi ake aangono a malemuyo, adati zomwe zidachitikazo ndi malodza enieni. Ine ndikuluphera kugona poganizira kuti kodi chandiona ine ndi chiyani? Kapena nditi chikunditsata ine ndi chiyani pamalodza oterewa? Kunena zoona, anthu amenewa andilaula ine. Ngakhale makolo anga zoterezi sadazionepo, adatero Wisiki, akusisima. Mayiyu, yemwe ali ndi zaka 40, kwawo kwenikweni ndi mmudzi mwa Jeriko, mdera la T/A Pemba, mboma la Dedza. Akuti adabwera ndi kukhazikika kwa Mgonako zaka 30 zapitazo. Iye ati chomvetsa chisoni chinanso nchakuti Maria, yemwe adali mwana wa mchemwali wake wamkulu, wamwalira ali wachisodzera. Malinga ndi Wisiki, Maria adamwalira atadwala malungo.
7
Malamulo a ukwati akutsutsana Kutanthauzira lamulo lokhudza maukwati a ana kukhala kovuta tsopano pamene pali kusemphana pakati pa zomwe zidalembedwa mmalamulo oyendetsera adziko lino ndi zomwe zili mmalamulo okhudza mabanja la Divorce and Relations Act. Gawo 22 ndime 6 ya malamulo a dziko lino limati palibe munthu woposa zaka 18 adzaletsedwe kukwatira kapena kukwatiwa. Ndime 7 imati munthu wa zaka pakati pa 15 ndi 18 angathe kukwatiwa kapena kukwatira ngati patakhala chilolezo kuchoka kwa makolo kapena womuyanganira. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Izi zikusemphana ndi zomwe zili mu lamulo latsopano loyendetsera maukwati zoletsa ukwati wa munthu wosaposa zaka 18. Ku Dedza, T/A Kachindamoto akuchotsa mafumu amene apezeka akuvomereza ukwati wa mwana wosaposa zaka 18. Mwa chitsanzo nyakwawa Galuanenenji idachotsedwa pampando chifukwa chovomereza ukwati wa mtsikana wa zaka 15 ngakhale makolo ake adavomereza kuti ukwatiwo uchitike. Kachindamoto akuti mphamvu akuzitenga mu malamulo oyendetsera maukwati momwe akuletsa ukwati wa mwana wosaposa zaka 18. Tsono kuti tichotse mfumu pampando, malamulo amenewa tidachita kugwirizana tokha kuno ndiye mfumu yomwe yalakwitsa ikuchotsedwa ndipo mafumu anayi achotsedwa, adatero Kachindamoto. Koma Esmie Tembenu wa Blantyre Child Justice Magistrate akuti pali kusokonekera kwazinthu chifukwa cha Divorce and Relations Act. Chifukwa cha ubwino woti ana kuti azipita kusukulu, lamulo la maukwati ndi lomwe tikugwiritsa ntchito komabe tili ndi mantha chifukwa izi si zomwe zili mmalamulo adziko lino. Ngati wina atakutengera kubwalo la milandu, angathe kukapambana mlandu chifukwa malamulo adziko lino okha ndiwo ali ndi mphamvu, adatero Tembenu. Naye mphunzitsi wa za malamulo kusukulu ya Chancellor College Edge Kanyongolo akuti pamenepa pali kusokonekera kwa zinthu komabe wati lamulo la dziko lino ndilo lili ndi mphamvu. Masiku apitawa, Kanyongolo adati pofuna kugwiritsa zomwe zili mu lamuloli, ndiye pakuyenera kukonza gawo 22 lomwe lili mmalamulo adziko lino.
1
Papa Wati Chilengedwe Chimamutengera Munthu Chifupi ndi Mulungu Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wati chilengedwe chili ndi kuthekera komutengera munthu pafupi ndi mulungu. Papa Francisco walankhula izi lachitatu ku likulu la mpingo wa katolika ku Vatican mu zolankhula zake zomwe amachita tsiku la chitatu lililonse. Iye wati chilengedwe chili ndi mphamvu yomutengera munthu pafupi ndi Mulungu popeza kudzera mu chilengedwe munthu amaona ulemerero ndi ukulu wa Mulungu. Papa Francisco waonjezeranso kunena kuti mapemphero ali ndi mphamvu yotha kugonjetsa mavuto amene munthu amakumana nawo mmoyo uno.
14
Mutharika afika mawa Mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, afika mdziko muno mawa kuchokera ku America komwe adakakhala nawo pa msonkhano wa bungwe la maiko onse la United Nations. Katswiri wa za ndale, George Phiri, wati Mutharika wachita bwino kubwera kuti adzakonze mavuto omwe agwa mdziko muno ali kunja. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wadukiza ulendo wake: Mutharika Phiri amanena za zipolowe zomwe zidachitika pakati pa ochita zionetsero ndi anyamata omwe adavala makaka a chipani cha Democratic Progressive Party (DPP). Anyamatawo adatema anthu ndi akuluakulu a bungwe la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) omwe amachita zionetsero zofuna kukakamiza wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC), Jane Ansah, kuti atule pansi udindo wake kaamba koti sadayendetse bwino zisankho za pa Meyi 21. Pofuna kukhazikitsa bata, apolisi adaponyera anthu utsi wokhetsa misonzi ndipo wina udakagwera ku chipatala cha Gulupu komwe udadzetsa mpanipani pakati pa odwala ndi madotolo mpaka mayi wina woyembekezera adakomoka nawo. Ena mwa anthu omwe adakhapidwa ndi mmodzi mwa akuluakulu a HRDC, Billy Mayaya. Adamson Muula, mmodzi mwa madokotala komanso aphunzitsi a pa sukulu ya madotolo ya College of Medicine (CoM), alembera kalata mkulu wa apolisi Duncan Mwapasa yosonyeza kukhumudwa ndi mchitidwe woponyera utsi ku chipatala. Mkulu wa bungwe la Malawi Health Equity Network, George Jobe, naye adati ndi wokhumudwa ndi mpungwepungwe womwe apolisi adadzetsa ku Gulupu. Chokhumudwitsa nchoti apolisi sakusankha malo woponya utsi wokhetsa misonzi moti wina udagwera ku Gulupu mpaka mayi woyembekezera kukomoka nawo, adatero Jobe. Ichi nchifukwa chake Phiri akuyamikira Mutharika kaamba kodukiza ulendo wake kuti azathana ndi mavutowa. Kalata yolengeza kubwera kwa Mutharika yachokera ku nyumba ya boma ndipo ikuti mtsogoleriyu atera pa bwalo la ndege la Kamuzi Internatioal Airport (KIA) Mawa.
11
Adzudzula Kampani ya Enviro-Consult Kamba Kochedwetsa Malipiro Anthu a mmudzi mwa Dauti mfumu yaikulu Mpando mboma la Ntcheu adzudzula kampani ya Enviro-Consult kaamba kosawapatsa ndalama zomwe anagwilira ntchito kuyambira mwezi wa March chaka chino. Nsewu wa Tsangano omwe ukukonzedwa Malinga ndi ena mwa anthuwa omwe anayankhula ndi Radio Maria Malawi, kampaniyi ili pa contract ndi nthambi ya Malawi Defence Force yomwe ikumanga nsewu wa Tsangano-Mwanza-Neno, ndipo inauza anthu okwana 24 kuti adzale kapinga mmbali mwa nsewuwu koma kufikira pano anthuwa akuti sanalandire ndalama iliyonse. Tinakhala tikugwira ntchito yodzala kapinga cholinga choti tipeze ndalama kupewa kuba koma mpaka pano sitinalandire ndalama, anatero mmodzi mwa anthu odandaulawo. Koma poyankhapo pa nkhaniyi mmodzi mwa akuluakulu a kampaniyi a Benjamin Mughogho avomereza za nkhaniyi koma ati vutoli ladza kaamba koti boma silinaperekebe ndalama ku kampaniyi. Nkhaniyi ndi yowona koma ifenso sitinalandire malipiro athu kuchokera ku boma koma chifukwa cha zandale zikuchitikazi ma funding sanatuluke, anatero a Mughogho.
14
Chitetezo chalowa nthenya mmalawi Anthu ena akulanga okha amene akuwaganizira kuba monga uyu Chitetezo mdziko muno chaphwasuka. Anthu akuyenda mwamantha pamene ena akuphedwa komanso katundu akubedwa molapitsa. Sabata yangothayi, zigawenga 8 zakhapa mfumu Chisesele ku Madziabango mboma la Blantyre mpaka kuipha ndi kubanso ndalama ndi mafoni. Nako ku Ntchisi zigawenga zakhapa bambo wina mpaka kupha Lachitatu msabatayi. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izitu zikutsatira kuphedwa kwa anthu awiri mboma la Dedza ndi ena awiri mboma la Ntcheu zomwe zapangitsa kuti chiwerengero cha anthu ophedwa miyezi ya June ndi July yokha chifike pa 51. Mmadera ena monga Blantyre ndi Lilongwe komanso Mzuzu anthu ayamba kulanga okha ngati agwira wakuba posakhulupiriranso apolisi. Mmiyezi yomweyi chaka chatha, chiwerengero cha anthu amene adaphedwa mu ulamuliro wa PP chidalinso chokwera. Wachiwiri kwa mneneri wa polisi mdziko muno, Mable Msefula, akutsimikiza kuti anthu 51 ndiwo aphedwa mmiyezi iwiriyi ngakhale mwezi wa July sudathe. Mwa anthu amene aphedwawa zikusonyeza kuti ambiri akuphedwera mmalo omwera mowa. Mwachitsanzo, ku Ntchisi mkulu wina waphedwa ndi mnzake atasemphana Chichewa, adatero Msefula poyankha Tamvani msabatayi. Nduna ya zachitetezo, Paul Chibingu, yati boma ndilokhumudwa ndi nkhani zophanazi komanso kuba katundu komwe kwafika ponyanya. Chibingu wati anthu akuchitira dala umbandawu malinga ndi kusintha kwa boma, koma wachenjeza kuti wina aona mbwadza. Anthu angopezerapo mwayi chifukwa cha kusintha kwa boma, akuchita mwadala. Koma unduna wanga ukudziwa izi ndipo sitikugona kufuna kupeza njira zothanirana ndi mchitidwewu. Aliyense amene akuchita izi adziwe kuti aona polekera, adatero Chibingu pouza Tamvani, koma sadanene zomwe unduna wake ukuchita pofuna kuthana ndi umbanda ndi umbava. Chibingu adati anthu asataye mtima chifukwa cholinga cha boma la DPP nkuti likhwimitse chitetezo chomwe pano chamasuka. Kubwera kwa DPP kudapereka chiyembekezo kuti chitetezo chibwereranso mdziko muno malinga ndi momwe chipanichi chidachitira panthawi yomwe chimalamula. Pulezidenti wakale, yemwenso adali mtsogoleri wa chipani cholamula cha DPP, malemu Bingu wa Mutharika, adalamula apolisi kuti aziombera ndi kupheratu zimbalangodo zoba ndi mfuti. Ngakhale lamuloli silidakomere anthu omenyera ufulu wachibadwidwe, umbanda ndi umbava udacheperako kaamba koti zimbalangondo zidayamba kuopa. Koma DPP chitengereninso boma mu May chaka chino, anthu ayamba kufika pakhomo masana kuopa zimbalangondo zomwe zikupha komanso kuba katundu. Chibingu akuti pakakhala kusintha kwa boma, anthu amalitosa dala kuti aone ukali wake. Akufuna kuyeserera ndipo tikudziwa akupanga dala, koma apolisi athu ndi ophunzitsidwa bwino ndipo zida zonse alinazo. Boma la DPP labwera ndi chitetezo ndipo zimenezi zitheka, anthu asadandaule. Chipani cha PP chitangolowa mboma mu April 2012, chitetezo chidagwedezekanso ndipo mu September anthu adayamba kupempha mtsogoleri wa nthawiyo, Joyce Banda, kuti abwezeretse lamulo lowombera ndi kupheratu (shoot to kill) lomwe lidakhazikitsidwa ndi malemu Mutharika. Kodi DPP ibweretsanso lamuloli? Apolisi amakhala ndi mfuti ndipo amadziwa nthawi yomwe angagwiritse ntchito. Sungawauze chochita chifukwa ena mukawauza za shoot to kill amazitengera pena mosagwirizanso ndi zomwe tikutanthauza, Chibingu adatero.
7
Chipani cha DPP Chati Chiyamba Misonkhano Yakathithi Posachedwa Mlangizi wa President pa nkhani za ndale a Francis Mphepo wati Chipani cha Democratic Progressive (DPP) chikhala chikuchita misonkhano yokopa anthu mwakathithi posachedwapa. Mphepo: Tikutsatira zomwe president wathu anatiuza A Mphepo anawuza Radio Maria Malawi kuti pakali pano chipani cha DPP chikutsatira zomwe adanena President Mutharika zoti anthu, asamakhale mothinana pofuna kupewa kachirombo ka Coronavirus. A Mphepo anati padakali pano wachiwiri kwa pulezidenti Mutharika pa chisankho cha pulezidenti chobwereza chomwe chikudzachi Atupele Muluzi akungopanga misonkhano yoyimayima pofuna kungocheza ndi anthu. Ife tikutsatira zomwe President wathu Professor Arthur Peter Mutharika adanena kuti titsatire njira zopewera mliri umenewu wa Coronavirus. Ndiye sikuti tangokhala ayi tiyambapo kamepni yeneiyeni posachedwapa, anatero a Mphepo. Mwapadera a Mphepo apempha atsogoleri ena a ndale kuti amvere ndi kutsatira malangizo a unduna wa zaumoyo pa kapewedwe pa mliri mwa Coronavirus pamene akuchita misonkhano yokopa anthu.
11
Chiwerengero cha Ana Odwala Chikuku Chakwera Kwambiri ku Cameroon Nduna yoona zaumoyo mdziko la Cameroon yati chiwerengero cha ana omwe apezeka matenda achikuku chakwera ndi 34 Percent mu zaka zitatu zapitazi. Dr Phanuel Habimana awuza wailesi ya BBC kuti izi zachitika kamba koti unduna wawo siunakwanitse kupereka katemera wa matendawa pomwe anakwanitsa kupereka kwa ana 75 pa hundred aliwonse mdzikolo. Iwo ati pofuna kuthana ndi matendawa akuyenera kupereka katemerayu kwa ana 95 pa handred aliwonse mdzikolo. Sabata yatha dziko la cameroon lapereka katemerayu kachiwiri mu chaka chino kwa ana omwe ndi a miyezi isanu ndi inayi kufikira zaka zisanu omwe ndi ochuluka kwambiri mdzikolo. Chiwerengero cha anthu omwe anafa ndi nthenda ya chikuku chaka chatha ndi choposa 140 sauzande padziko lonse omwe ambiri anali ana osapyola zaka zisanu. Maiko asanu omwe anakhuzidwa kwambiri ndi matendawa chaka chatha ndi a Democraticm Republic Of Congo DRC, Liberia, Madagascar, Somalia ndi Ukrane.
6
Konvenshoni ya MCP pa 28 April Pamene chipani cha Malawi Congress Party (MCP) chatsimikiza kuti msonkhano wake waukulu wokasankha atsogoleri udzachitika pa 28 ndi 29 Epulo, katswiri wa zandale Dr Mustapha Hussein wadzudzula mchitidwe wosintha malamulo oyendetsera chipani ncholinga chopatsa mpata anthu omwe sakuloledwa kupikisana nawo pamaudindo kuti atero. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Msonkhanowo ukuyembekezeka kudzachitikira ku Bingu International Conference Centre ku Lilongwe ndipo ngakhale chipanichi chidakali kuunguza ndalama za msonkhanowo akuluakulu ati ulipo. Malipoti msabatayi adati chipanichi chikukonza zokasintha malamulo ena, kuphatikizapo loti munthu asamaimire chipanichi pazisankho za mtsogoleri wa dziko koposa kawiri. Chipanichi chidati chikakambirana zosintha lamuloli kuti munthu akhoza kuimira chipanichi popanda malire, zomwe ena akuti nzongufuna kuti mtsogoleri wa chipanichi, John Tembo, adzaimirenso chipanicho chaka chikubwerachi. Yemwe akuyendetsa zokonzekera msonkhano waukulu wa chipanichi, Joseph Njobvuyalema, watsimikiza kuti MCP ikuunikanso malamulo ake komanso kuti tsopano yakhazikitsa masiku omwe chipanichi chidzapange msonkhanowo. Nzoona kuti tikuunikanso malamulo a chipani chathu koma chifukwa chake ndi choti malamulowa ngakale kwambiri moti pali zina ndi zina zofunika kusintha kuti zizifanana ndi nthawi. Padakalipano ntchitoyi ili mkati ndipo chilichonse chiunikidwa kuphatikizapo ndime yomwe imakamba za utsogoleri wa chipani. Omwe akufuna kudzapikisana nawo pamaudindo osiyanasiyana auzidwa kale kuti azikatenga zikalata kulikulu lathu kusonyeza kuti chilichonse chili mmalo, adatero Njobvuyalema. Koma Hussein wati kusintha malamulo a chipani panthawi yoti msonkhano waukulu wayandikira kungabweretse chikaiko pakati pa otsatira chipani komaso omwe satsatira chipanicho. Lamulo ndi lamulo, palibe chifukwa chosinthira chifukwa zimenezi zimapangitsa kuti chipani chizilephera kutsatira bwino mfundo za demokalase. Zikayamba choncho ndiye kuti ngakhale kutsogoloko anthu omwe ali ndi zolinga zawozawo azidzangosintha malamulo kuti ziwayendere mapeto ake anthu sakhulupiriranso chipanicho, adatero Hussein. Pa za msonkhano waukuluwo, Njobvuyalema adati ngakhale pali chitsimikizo choti msonkhanowo udzakhalako pa 28 ndi pa 29 mwezi uno, chipanichi sichinamalize kutolera ndalama zodzayendetsela msonkhanowo koma ali ndi chiyembekezo kuti pofika masikuwa ndalamazo zidzakhala zitakwana. Njobvuyalema adatinso anthu odzapikisana nawo pamipando yosiyanasiyana sanadziwikebe ndipo akuyembekezera kuti adziwika likulu lawo likatulutsa mndandanda wa anthu omwe akatenga zikalata zosonyeza khumbo lopikisana nawo. Msabatayi, mkulu wa mpingo wa Assemblies of God mbusa Lazarus Chakwera adati akufuna kudzapikisana nawo pampando wa mtsogoleri wa chipanicho. Mmbuyomu, mlembi wamkulu wa chipanicho Chris Daza naye adati akufuna kudapikisana nawo. Palinso phungu wa pakati mboma la Nkhotakota, Edwin Banda yemwe naye wati mpandowu akuufuna. Komanso mkulu wa bungwe la alimi la Farmers Union of Malawi (FUM) Felix Jumbe Lachitatu adalengeza kuti watula pansi udindowo ndipo akulowa ndale. Iye adatinso akufuna kupikisana nawo pampando wa pulezidenti. Tawalandira a Jumbe kuti apikisane nawo ndipo ngati sanatenge zikalata zimene ofuna kupikisana nawo akutenga, ayenera kutero, adatero Njobvuyalema. Zipani zina monga Peoples Party (PP) ndi United Democratic Front (UDF) zidasankha kale maudindo a mzipani zawo komaso odzaziyimira pampando wa mtsogoleri nthawi ya zisankho. Hussein wati kusankha atsogoleri nthawi yabwino kumathandiza chipani kukonzekera mokwanira zisankho zisanafike.
11
Akugulitsa magazi ku Mangochi Kaamba ka kusowa magazi pachipatala cha Mangochi, anthu ena ozungulira chipatalacho akugulitsa magazi awo kwa odwala osoweka mwazi pamtengo wa K7 000 pa lita. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zidadziwika pamene mayi wina, Hawa Ntila, adabereka mapasa ku Makanjira adatumizidwa kuchipatalacho ndipo Lamulungu adapereka K7 000 ndipo Lolemba adaperekanso ndalama yomweyo kuti apeze magazi. Mneneri wa unduna wa zaumoyo Henry Chimbali adatsimikza nkhaniyi. Ntila amagwira ntchito kubungwe lothandiza amayi pa za malamulo la Women and Law in Southern Africa (Wilsa). Mkulu wabungweli Seodi White adati adakwiya nazo. Mpaka K14 000? Ndidafunsa kuti chikuchitika nchiyani, adatero iye. Ena mwa ogulitsa magaziwo ndi anyamata a kabaza pachipatalapo. Bungwe loona za magazi la Malawi Blood Transfusion lati vutoli lagwa chifukwa anthu sakupereka magazi mokwanira.
7
Maphunziro a chidyerano cha chimbudzi athandiza Moyo wasintha ndipo kamphepo kayaziyazi kakudutsa tsopano mmidzi 13 yozungulira dera la T/A Njewa ku Lilongwe anthu atasintha khalidwe lochitira chimbudzi paliponse nkuyamba kugwiritsa ntchito zimbudzi. Zaka 51 chilandirireni ufulu odzilamulira, anthu kuderali amadalirabe tchire ndi kuseli kwa mitengo akafuna kudzithandiza kufikira pomwe bungwe la Plan International lidawafikira ndi maphunziro akuipa kochitira chimbudzi paliponse. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Bungweli lidaphunzitsa anthuwa kuti akamachitira chimbudzi paliponse ndiye kuti akuchita chidyerano cha zopambukazo pakati pa wina ndi mnzake zomwe zingawabweretsere matenda otsegula mmimba ndi mmapapo kaamba kafungo loipa. Njewa adatsimikiza kuti kwanthawi yaitali anthu mdera lake samadziwa kufunika kwa chimbudzi ndipo mmimba mukafunda amangolowa patchire nkukadzithandiza ndipo adati pachifukwachi, mderali mumabuka matenda osiyanasiyana pafupipafupi. Padalibe zoti wamkulu kapena mwana ayi. Aliyense amati akamva mmimba, kokapumira kudali kutchire ndiye padalibe zaulemu chifukwa nthawi zina mwana amatha kupezerera wamkulu akudzipeputsa komanso matenda samati abwera liti, adatero Njewa. Iye adati nthawi zina alendo amadziwira fungo kuti afika mdera la Njewa chifukwa chimbudzi chidali ponseponse mpaka liti, adatero Njewa. Iye adati nthawi zina alendo amadziwira fungo kuti afika mdera la Njewa chifukwa chimbudzi chidali ponseponse mpaka anthu kumachita nkhawa poyenda mtchire kuopa kuponda chimbudzi cha munthu wina. choyamba adafotokozera anthuwo kuti amadyerana chimbudzi pazomwe amachitazo. Mlongoti adafotokoza kuti zidawatengera miyezi iwiri kuti anthu amvetsetse momwe amadyera chimbudzi cha anzawocho ndipo atamvetsetsa adayamba kukumba zimbudzi zomwe akugwiritsa ntchito pano. Lidali dera lomvetsa chisoni kwambiri pankhani yaukhondo. Poona kuti tivutika kumvana nawo msanga, tidagwiritsa ntchito chionetsero.
18
Tanzania Itulutsa Maina Amuna a Pabanja pa Internet Wolemba: Glory Kondowe Unduna woona zamaboma angono mu mzinda wa Dar Es Salaam mdziko la Tanzania akuti utulutsa mayina amuna onse omwe ali pabanja pa tsamba lake la pa makina a internet. Mmodzi mwa akulu-akulu mu unduna-wu a Paul Makonda auza atolankhani mdzikomo, kuti unduna-wu wachita izi pofuna kuteteza amayi omwe akhala akuchitiridwa nkhanza zosiyanasiyana monga kusiyidwa mabanja kamba kokwatiwa ndi amuna omwe ali kale pabanja. Pamenepa a Paul Makonda alangiza amayi omwe saali pabanja kuti pomwe apezana ndi mwamuna amene akufuna kuti amange naye banja adziyamba amufufuza pa tsambali pofuna kupewa kukwatiwa ndi amuna achinyengo-wa.
14
Nyumba ya Malamulo Yatsiriza Zokambirana Zake By Richard Makombe ads/2019/07/parl3-300x168.jpg" alt="" width="671" height="376" />Nyumba ya malamulo ya Malawi Nyumba ya malamulo lero yatsiliza mkumano wake womwe aphungu akhala akukambirana zinthu zosiyanasiyana zokhudza dziko lino. Mtsogeri wa dziko lino Professor Peter Mutharia ndi yemwe anatsegulira zokambiranazi pa 21 June chaka chino pomwe mwazina aphunguwa anakambirana za ndondomeko yoyendetsera dziko lino kwa miyezi inayi kuyambira mwezi uno kufikira mwezi wa October. Mmawu ake potsiliza zokambiranazi, mtsogoleri wa mbali yotsutsa boma a Robin Lowe anathokoza aphunguwa kamba kodzipereka pa zokambirana ngakhale kuti ena samakhalanawo pa zokambiranazi. Komabe ndili okhumudwa kamba koti aphungu ena samaikapo chidwi pa zokambirana zina zomwe zimachitika mnyumbayi, anatero a Lowe. Mtsogoleri wa nyumbayi kumbali ya boma a Kondwani Nankhumwa poyankhulapo anati ndiokhudzidwa ndi momwe aphungu otsutsa amayankhulira mnyumbayi pomwe anati nthawi zambiri amanyoza mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika. Kumayambiliro a mkumanowu, aphungu otsatira chipani cha Malawi Congress (MCP) anatuluka mnyumbayi pomwe mtsogoleri wa dziko lino Professor Peter Mutharika amayankhula potsegulira msonkhano wa aphunguwa kunyumba ya Malamulo mu mzinda wa Lilongwe, kamba koti sakuvomereza kuti ndi mtsgoleri wa dziko lino koma iwo anapita kunyumbayi kukakambirana za ndondomeko ya chuma yoyendetsera dziko lino. Mwazina kwa nthawi yoyamba mu mbiri ya dziko lino aphunguwa anasankha a Catherine Gotani Hara kukhala sipikala wanyumba ya malamulo.
11
Bande Athokoza Anthu a Dera Lake Pomuvotera Wolemba: Sylvester Kasitomu Phungu wa dera la ku mvuma kwa mdzinda wa Blantyre a John Bande wayamikira anthu a mdera-li kamba komukhulupilira ndi kumusankhanso pa mpando wa phungu wa ku nyumba ya malamulo pa chisankho cha pa 21 May ngakhale iyeyo pa nthawi ya misonkhano yokopa wanthu anali ali mdziko la South Africa kukalandira thandizo la makhwala. A Bande alankhula izi ku tchalitchi la Chikapa la mparish ya Nthawira mu arch-dayosizi ya Blantyre pomwe tchalitchili limakondwelera nkhoswe yake yomwe ndi Maria Mfumukazi ya Mtendere. Iwo ati anthu amderali anawonetsa kuwakhulupilira powasankha kuti ayimire derali ngati phungu wakunyumba ya malamulo ngakhale anali akudwala kotero adzipereka pa ntchito zotukula delaro. Pamene timachita campaign ndinali ndiri ku chipatala mdziko la South Africa. Ndithokoze Mulungu kaamba koti ndikupeza bwino tsopano ndiponso anthu anandikhulupirira ngakhale ine panalibepo. Ndipemphe akhristu anzanga kuti tigwirane manja popempherera mtendere mdziko muno maka pa nkhani za ndale zomwe sizikuyenda bwino, anatero a Bande. A Bande omwe ndi oyima paokha, pa chisankhochi anapeza mavoti pafupifupi 26 thousand pomwe amene amapikitsa naye kwambiri a Alex Chimwala a chipani cha DPP anapeza mavoti osachepera 6,000 zomwe zikusonyeza kuti anthu anawakhulupilira kwambiri kuti atha kuwathandiza pa ntchito zotukula dera la ku mvuma kwa mzinda wa Blantyre.
11
Chiwerengero cha akaidi chakwera Chiwerengero cha akaidi chakwera Chiwerengero cha akaidi mndende za mdziko muno chikunka chikwera. Mmodzi wa akulu owona za ndende mdziko muno, Masauko Wiscot, wati chiwerengero cha akaidi chachoka pa 14 430 chaka chatha nkufika pa 15 000 chaka chino. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akaidi akudzadzana kwambiri mndende za mdziko lino Malingana ndi mkuluyu, ndende za mdziko muno zimayenera kusunga akaidi apakati pa 5 000 ndi 7 000 okha. Akabwerebwere ndiwo akuchititsa kuti chiwerengero cha akaidi chizikwera kwambiri mndende za mdziko muno, adatero Wiscot. Akaidi omwe Msangulutso yalankhula nawo adati nthawi yowawa kwambiri mndende imakhala yogona. Iwo adati pogona amachita kusanjana ngati matumba ndi kumapumirana, zomwe anadandaula kuti zimaika miyoyo yawo pachiopsezo chotenga matenda osiyanasiyana. Ndili ku ndende ya Maula timasowa chakudya, malo wogona, komanso zofunda, adatero mmodzi mwa anthu omwe adalawapo ukaidi. Koma Wiscot adati akuluakulu a ndende mogwirizana ndi azamalamulo akuunikanso malamulo oyendetsera ndende za mdziko muno ndi cholinga chothana ndi mavuto omwe akaidi amakumana nawo. Ndende zathu zidamangidwa kalekale chiwerengero cha anthu mdziko muno chili chochepa. Nawo malamulo athu ndi akalekale. Choncho tiyenera kuwaunika mogwirizana ndi momwe zinthu zasintha mdziko muno, adatero mkuluyu. Pofuna kuchepetsa vuto la kudzadza kwambiri kwa akaidi mndende, Wiscot adati boma likumanga zipinda zowonjezera. Nkhani zomwe zimatisautsa kwambiri ndi malo wogona, chakudya ndi zaumoyo. Pofuna kuthana ndi vuto la chakudya, tikumalima tokha mbewu zosiyanasiyana. Boma lidatikomeranso mtima potipatsa dotolo woti azithandiza akaidi, iye adatero. Koma wapampando wa komiti yapadera younika za malamulo oyendetsera ntchito zandende mdziko muno, Ken Manda, adati njira yapafupi yochepetsera vuto la kudzadzana mndende ndi kulimbikitsa ukaidi wa kumudzi. Njira yapafupi yochepetsera vuto lakuchulukana mndende za mdziko muno ndi kulimbikitsa ukaidi wakumudzi. Anthu omwe apalamula milandu ingonoingon akuyenera kugwirira ukaidi wawo kumudzi osati mndende. Kumanga zipinda zogonamo ndi njira yabwino, koma imatenga nthawi yayitali pamene ukaidi wa kumudzi ndi yapafupi, adatero Manda. Mmodzi mwa akuluakulu omenyera ufulu wa anthu mdziko muno, Timothy Mtambo, adati mkaidi ali ndi ufulu womwe munthu wina aliyense ali nawo.
11
Sukulu ya St. Anthony Ipempha Mabungwe Athandize Posamalira Chilengedwe Sukulu ya primary ya atsikana ya St. Anthony ku Thondwe mboma la Zomba, yapempha mabungwe omwe si aboma kuti ayike chidwi pothandiza sukulu zosiyanasiyana pobwenzeretsa chilengedwe mdziko muno. Mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi, Sr. Agness Kapatu alankhula izi lachitatu pomwe Radio Maria Malawi, imafuna kudziwa zomwe sukuluyi ikuchita pofuna kubwenzeretsa chilengedwe. Iwo ati padakali pano mogwirizana ndi makolo akudzala kapinga kuzungulira sukuluyi potsatira mavuto omwe sukuluyi yakhala ikukumana nawo mu nyengo yamvula pomwe nthaka imakokoloka zomwenso wati zimapereka chiopsezo kuzipinda zophunzilira pa sukuluyi. Pasukulu pano nthaka inankoloka ndi mvula zomwe zimachititsa kuti nthawi zambiri mvula ikamagwa ma block ambiri azigumuka, anatero Sister Kapatu. Mwazina iwo ayamika mgwirizano womwe ulipo pakati pa aphunzitsi ndi makolo pa sukuluyi ponena kuti izi zatheka kaamba koti pali mgwirizano wabwino pakati pawo. Pamenepa Sister Kapatu anapezerapo mwayi opempha mabungwe akomanso anthu ena akufuna kwabwino kuti atahandizepo pa ntchito yokonzanso sukuluyi kaamba koti ntchitoyi ikufuna zipangizo zambiri zomwe ndizofuna ndalama zokwanira. Bungwe la Emmanuel International akuti ndilomwe likuthandiza ntchitoyi popereka zipangizo zogwirira ntchitoyi.
18
CCMP Ipempha Atolankhani Alimbikitse Nkhani za Kusinntha kwa Nyengo Wolemba: Sylvester Kasitomu Atolankhani nkhani mdziko muno, awapempha kuti akhale patsogolo kumemeza zakusintha kwa nyengo mdziko muno. Mkulu wa project ya Climate Challenge Malawi Programme kudzera ku bungwe la CADECOM, a Mercy Chirambo, anena izi pambuyo pa mkumano womwe anali nawo ndi atolankhani ndi cholinga chowazindikilitsa zaudindo wawo pothandiza kuzindikiritsa anthu zakusintha kwanyengo komanso chilungamo pa nkhani yakusintha kwa nyengo. Mayi Chirambo ati ntchitoyi ikuyangana ngodya zitatu zomwe zithandize kwambiri kufuna kuchepetsa kusintha kwa nyengo ndi kuonongeka kwa zachilengedwe mdziko muno. Ngakhale nyengo yasitha koma ife tinachiwona chanzeru kuti tikhale ndi mkumano ndi atolankhani kaamba koti iwo ndi amene ali ndi kuthekera kouza anthu zakufunika kosamala zachilengedwe, anatero mayi Chirambo, Mwazina iwo ati dziko lino likukumana ndi mavuto ambiri omwe akudza kaamba kakusintha kwa nyengo monga kusowa kwa madzi zomwe zikubwezeretsa mbuyo ntchito za ulimi umene anthu ambiri madalira mdziko muno. Project ya Climate Challenge Malawi Programme kudzera ku mbungwe la CADECOM, ikugwira ntchito mmaboma a Zomba, Balaka, Machinga komanso Chikwawa.
18
Alamulidwa Zaka Zinayi Kaamba ka Kuba Bwalo lachiwiri lamilandu mboma la Balaka lalamula mamuna wina wa zaka 33 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavula-gaga kwa zaka zinayi kaamba kopezeka olakwa pa mlandu wakuba. Malinga ndi wachiwiri kwa wofalitsa nkhani za apolisi mbomalo Sergeant Precious Makuta, mamunayu Jofrey Sidreck anapalamula mulanduwu pa 20 November chaka chatha pomwe anabera a Eliot Ndalowa ndalama zokwana 2 Hundred Thousand pa shop Uptown mbomalo. Bwaloli linamva kuti Sidreck anatenga ndalamayi kwa mzawoyi ndi cholinga choti amusungire pomwe nzawoyi anali atamwa mowa. Kutacha mmawa mwini ndalamayu analawira kwa Sidreck kukafunsa za ndalama yake ndipo Sidreck anakana kuti sanatenge ndalamayi zomwe zinamuchititsa kukadandaula ku polisiyi. Ku bwaloli, Sidreck anapezeka olakwa ndipo Second Grade Magistrate Victor Sibu anati wapereka chilangochi kuti ena omwe ali khalidwe ngati ili atengerepo phunziro. Jofrey Sidreck amachokera mmudzi wa Chingombe mdera la mfumu yayikulu Makwangwala mboma la Ntcheu.
7
Mafumu asalidwa pogawa chimanga Ntchito yogawa chakudya kwa anthu osoweratu pogwira ili mkati koma kafukufuku wathu wasonyeza kuti mafumu sakukhutira ndi momwe ntchitoyi ikuyendera makamaka pa kasankhidwe ka anthu olandira chakudyachi. Kafukufukuyu wapeza kuti mabungwe ambiri omwe akuthandizana ndi boma pa ntchitoyi akusankha okha anthu oti alandire chakudya ndipo nthambi yolimbana ndi mavuto ogwa mwadzidzidzi ya Department of Disaster Management Affairs (DoDMA) yati njirayi ichepetsa katangale. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Akuti midzi yambiri yasiyidwa: Lukwa Mmbuyomu, mbiri ya ntchito yogawa chakudya kapena zipangizo zina mmidzi pogwiritsa ntchito mafumu ndi makomiti a mmidzi idada ndi nkhani ya katangale pa kasankhidwe ka anthu olandira. Koma mafumu auza Tamvani kuti njira yomwe ikutsatidwa tsopanoyi ndiyo ingapititse patsogolo katangale chifukwa anthu osayenera kulandira akhoza kupeza danga kaamba koti olembawo sakudziwa za mmadera. Tikungomva kuti anthu akulembedwa maina kuti akalandire chakudya kapena ndalama ife mafumu osatengapo mbali ndiye mapeto ake, anthu osayenera kupindula nawo akupezeka pamndandanda, adatero Senior Chief Chapananga wa ku Chikwawa. Mfumu yaikulu Chadza ya ku Lilongwe idati chifukwa choti anthu omwe akuchita kalemberayu sadziwa bwinobwino madera omwe akugwiramo ntchitowo, midzi yambiri ikudumphidwa kusiya anthu ambiri padzuwa. Anthu omwe akuchita kalembera sadziwa malire kuti adayenda bwanji kapena kuti kuli anthu ochuluka bwanji. Pachifukwachi, midzi yambiri ikudumphidwa; mwachitsanzo, mdera langa lino, muli Senior Group Mwenda yemwe ali ndi mafumu 80 komanso anthu 6 000 omwe adumphidwa, adatero Chadza. Senior Chief Lukwa wa ku Kasungu adati mwa mafumu opitirira 200 a mdera lake, mafumu 6 okha ndiwo alowa mukalembera wa anthu olandira chakudya kutanthauza kuti midzi yambiri yasiyidwa ndipo avutika. Mfumu yaikulu Chindi ku Mzimba adati iye adangomva kuti anthu ena alembedwa maina ndipo kuti ena ayamba kulandira chakudya koma osadziwa komwe zikuchokera ndi momwe zikuyendera. Adalembana okha komweko ife sizidatikhudze ayi komanso zoti anthu akulandira chakudya tikungomva. Mwachitsanzo, ndidangomva mphekesera kuti cha ku Edingeni anthu adalandirako chimanga koma ndilibe umboni, adatero Chindi. Mneneri wa nthambi ya Dodma Jeremiah Mphande adati njira yomwe ikugwiritsidwa ntchito posankha anthu ndiyamakono komanso yothandiza kuchepetsa chinyengo ndi katangale yemwe adalipo kale. Njirayi yomwe akuitcha Unified Beneficiary Registry (UBR) imatenga kaundula wa anthu ovutika nkuwayika mmagulu potengera mavutikidwe awo ndipo kuchoka apo amazindikira thandizo loyenera kupereka ku maguluwo. Kuchoka pa mndandandawu, amthandizi pakhomo, amatengapo anthu awo, a ntchito za chitukuko amatengaponso ndipo ofunika thandizo la chakudya nawo amachoka momwemo. Njirayi imachepetsa kulakwitsa kowonjezera kapena kuchotsera anthu mu kaundula, adatero Mphande. Malingana ndi DC wa mboma la Lilongwe, Charles Makanga, bomali lidatsatadi njira yatsopano pofuna kuthetsamavuto ena omwe adalipo mnjira yakale monga kulowetsa ndale za pamudzi mupologalamu. Chomwe chimachitika mundondomeko yakale nchakuti mafumu amayenera kugwirira ntchito limodzi ndi makomiti monga Village Development Committee (VDC) ndi Area Development Committee (ADC) koma pamakhala kuyendana mmbali. Tili ndi zitsanzo zambiri zomwe kumapezeka kuti mfumu payekha walemba maina kapena anyamata ena a mukomiti alemba maina kwa okha ndiye zimasokoneza pologalamu, adatero Makanga.
8
Evance Masina: Mapanga awiri samuvumbwitsa Pali mwambi woti ndigwire uku ndi uku pusi anagwa chagada. Penanso amati mapanga awiri avumbwitsa, kutanthauza kuti ndibwino kuchita chinthu chimodzi panthawi imodzi kuti zikuyendere. Koma Evance Masina akutha bwanji sukulu ndi kusewera mpira mkalabu komanso nkumachita bwino mzonse? DAILES BANDA adacheza naye motere: Akufunitsitsa atadzasewerapo kunja Ndikudziwe mnyamata. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ndine Evance Masina wa zaka 18. Ndimachokera mmudzi mwa Ntamba T/A Nkalo mboma la Chiradzulu. Ndine wachinayi mbanja la ana asanu. Pakadalipano ndikuphunzira pasekondale ya Moyale ku Mzuzu komwe ndili mu Fomu 3. Umatchuka kwambiri chifukwa chosewera mpira, kodi udayamba bwanji kusewera? Mpira ndidayamba kalekale ndili mwana koma zenizeni ndidayamba kusewera wa Under-12. Ndinkasewera timu ya Young Buffalo ya ku Mzuzu konkuno. Nditadutsa zaka 12 ndidapitiriza kusewera ku Young Buffalo mtimu ya Under-14. Padachitika zovuta zinazake zomwe zidandichititsa kuti ndikayambe kusewera ku Chiputula United mtimu ya Under-20. Mchaka cha 2014 ndi pomwe ndidayamba kusewera mutimu ya Fish Eagles komwe ndili mpaka pano. Timuyi ikutsogola muligi ya chikho cha FMB ku Mzuzu kuno ndi mapointi 38. Wachinyako zigoli zingati kutimiyu? Ndachinya zigoli 26 mumasewero okwana 14 mchikho chimenechi. Chisangalalo chako ndi chotani pokhala amene wachinya zigoli zambiri mligiyi? Ndine wosangalala kwambiri chifukwa si chinthu chapafupi kuchita zoterezi. Pokhala mwana wasukulu zochita zimandichulukira. Ichi ndi chinthu chomwe ndakhala ndikufuna nditakwaniritsa mmoyo mwanga ndipo ndine wokondwa kuti ndachikwaniritsa. Umakwaniritsa bwanji kupanga za sukulu ndi za mpira? Ndimayesetsa kupanga pulani momwe ndichitire tsiku ndi tsiku ndi cholinga choti ndizitsatira bwinobwino zomwe ndikufunika kuchita kupewa kusokoneza zochita zina. Masomphenya ako? Chachikulu chomwe ndimafuna nditakwaniritsa ndi kusewera mutimu yaikulu mMalawi muno monga Silver Strikers, komanso mutimu ya dziko. Ndimafunitsitsanso nditadzasewerako mutimu yakunja. Osewera amene amakusangalatsa ndi ati? Ndimasangalatsidwa ndi maseweredwe a Chawanangwa Kaonga wa timu ya Silver Strikers komanso James Rodriguez amene amasewera mutimu ya Real Madrid. Umakonda kuchita chiyani ukakhala sukusewera mpira? Ndimakonda kuonerera mafilimu ndi kumvetsera nyimbo. Achinyamata anzako uwalangiza zotani? Alimbikire pachilichonse kuti adzakhale opambana.
10
Papa Wadzudzula Mchitidwe wa Tsankho ku America Mtsogoleri wa mpingo wa katolika pa dziko lonse Papa Francisco wadzudzula mchitidwe wa tsankho pakati pa anthu ponena kuti ndi tchimo. Waphedwa kamba ka tsankho-Floyd Malinga ndi malipoti a wayilesi ya Vatican, Papa walankhula izi lachitatu ku likulu la mpingo ku Vatican. Papa walankhula izi podzudzula kuphedwa kwa mzika ina ya chikuda ya dziko la United States of America, George Floyd yemwe anthu akukhulupilira kuti adaphedwa chifukwa cha mchitidwe wa tsankho mdzikolo pakati a anthu a khungu loyera ndi lakuda. Iye wati tsankho ndi tchimo pamaso pa Mulungu ndipo wadzudzulu zipolowe zomwe zakhala zikuchitika mdziko la United States of America pambuyo pa kuphedwa kwa mkuluyu ponena kuti palibe chabwino chomwe chingadze powononga katundu komanso nyumba zosiyanasiyana kaamba kokwiya ndi izi. Papa wapempha uneneri wa Amayi Maria aku Guadalupe yemwe ndi nkhoswe ya dziko la America kuti chilungamo, mtendere ndi kukhululukirana ziwonekere pakati pa anthu mdzikolo.
14
Mayi wamalonda avulazidwa ku bt Titha Masamba, wa zaka 31, akumva ululu wadzaoneni. Kuti ayende akuyenera agwirire ndodo; sangagone chafufumimba koma chammbali kapena chagada; moyo wamtendere watha. Akuti adamuphera tsogolo lake: Masamba kumva ululu kunyumba kwake Akuti izitu zili chonchi chifukwa cha bala lomwe lili pabondo lake la kumanja lomwe lidasokedwa kuchipatala pambuyo pokhapidwa ndi chikwanje. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Pa Wenela pasintha zedi Ulendo wa mayiyu wokagulitsa mandasi pa 7 July ndi womwe udabweretsa mavutowa pomwe anthu ena, omwe akuwaganizira kuti ogwira ntchito kukhonsolo ya mzinda wa Blantyre (city rangers) amene adamuchita chiwembu pomulanda malonda ake komanso kumuvulaza ndi chikwanje. Masamba akuti atangomwalira amuna ake mu 2007, iye adayamba geni yogulitsa mandasi kuti azisamalira banja lake la ana awiri. Malo amene amagulitsira malonda akewo akuti ndi ku Cold Storage pafupi ndi Kamuzu Stadium mumzindawu. Monga mwa nthawi zonse, patsiku la ngozilo, adauyatsa ulendo wokapha makwacha. Pafupi ndi Cold Storage pali njanje ndiye ndidaika malonda anga chapafupi ndi msewu womwe umadutsa pamwamba pa njajeyo kuti ndikataye madzi ndisadalowere ku Cold Storage, adatero Masamba. Pamene ndimati ndikatenge malondawo, ndidangoona galimoto ya City, yoyera ndipo mmbalimu idali ya sefa. Idadzaima pafupi ndi pomwe padali mandasiwo ndipo adali mgalimotomo adatsika natenga beseni la mandasilo. Ena adandigwira ndipo ndidawauza kuti angotenga mandasiwo asalimbane nane koma zidakanika. Mayiyu, yemwe akukhala ku Makhetha mumzindawu, akuti anthuwo adamubudulira malondawo ndipo mosakhalitsa zodabwitsa zidamuchitikira. Mmodzi adatulutsa chikwanje ndipo adandikhapa nacho pabondopa. Kaamba ka ululu kuchokera apo sindikumbukanso chomwe chidachitika ndipo ndidangozindikira ndili pabedi kuchipatala ku Queens cha mma 4 koloko madzulo, adatero. Iye akuti adazindikiranso kuti K4 500 yomwe adamanga pansalu yake palibe. Idali ndalama yomwe ndimati ndiwatumizire agogo anga ku Dedza. Agogowa amadaliranso ine akafuna thandizo, adatero iye. Chichitikireni cha izi, mayiyu akungobuula ndi ululu kunyumba kwake. Geni sangachitenso, moyo tsopano wasanduka wovuta. Mneneri wa khonsolo ya Blantyre Anthony Kasunda akuti wangomva za nkhaniyi koma akufufuza kaye ngatidi adali antchito awo amene adachitira chipongwe mayiyu. Ndikudabwa chifuma malo amene mayiwa akukamba ife sitifikako. Ndiye zikundidabwitsa kuti zatheka bwanji kuti mayiwa avulazidwe ndi anthu amene akuti ndi akhonsolo ya Blantyre, adatero Kasunda, amene akuganiza kuti mwina angakhale anthu ena omwe achita izi. Pamene Kasunda akufufuza, moyo wa Masamba uli pachiswe chifukwa ana ake akudalira iye kuti asake chakudya cha tsiku ndi tsiku komanso zofunikira kusukulu. Andiphera tsogolo. Tikadya ndiye kuti ndachita geni. Nawo mpamba udathera kuchipatala. Chochita chikundisowa, adalira mayiyu pocheza naye kunyumba kwake.
7
2019: Chaka cha mbiri pa zisankho Chaka cha 2019 chidzalowa mmbiri ya dziko la Malawi ngati chaka chomwe atsogoleri azipani adakwekwetsana koopsa komanso koyamba mukhoti pankhani yokhudza zotsatira za chisankho cha pulezidenti. Pa 21 May 2019 Amalawi adalawirira kukandanda pa mzere kuti akasankhe atsogoleri awo monga ma Khansala, Aphungu ndi Pulezidenti koma nyanga zidakola pa zotsatira za mpando wa Pulezidenti. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Sadatule pansi udindo: Ansah Pa 27 May 2019, bungwe la MEC lidalengeza kuti Peter Mutharika wa Democratic Progressive Party (DPP) adapambana pachisankho cha Pulezidenticho. Malingana ndi bungwe la MEC, Mutharika adapeza mavoti 38.67 mwa 100 alionse, Lazarus Chakwera wa Malawi Congress Party (MCP) adapeza 35.41 ndipo Saulos Chilima wa UTM Party adapeza 20.24. Zotsatirazo zidabweretsa mpungwepungwe waukulu moti Chilima ndi Chakwera adakasuma ku khothi ngati odandaula woyamba ndi wachiwiri mu mndandanda omwewo. Atsogoleri awiriwa akuti Mutharika ndi MEC ngati woyankha mlandu woyamba ndi wachiwiri mndandanda omwewo adasokoneza chisankho cha Pulezidenti ndipo akufuna khoti ligamule kuti chisankhocho chichitikenso. Chidadzutsa zonse ndi zikalata zolembapo momwe anthu avotera pomwe kudapezeka kuti zikalata zambiri zidafufutidwa ndi utoto wotchedwa Tippex komanso mamonitala ena sadasayine zikalata zina. Mlandu utayambika, padali kukolanakolana pa mfundo za mboni koma mlandu udayamba kuwoneka mutu mboni imodzi ya Chakwera Daud Suleman ataonetsa khoti momwe anthu ena omwe samayenera kulowa mmakina a internet a MEC, ankagulugushira mmakinawo. Umboni wina omwe udavuta udali wa mkulu wa bungwe la MEC Sam Alfandika yemwe adafunsidwa kuti alongosole bwino momwe Tippex adakapezekera mmalo owerengera mavoti, momwe adayankhira madando onse 147 monga momwe Ansah adanenera polengeza zotsaira komanso kuti ndani adavomereza kugwiritsa ntchito zotsatira zokonzedwa ndi Tippex. Alfandika yemwe patsiku loyamba adatuluka thukuta lochita kusamba mpaka khoti kuimitsidwa, adalephera kupereka maminitsi a zokambirana za makomishonala a MEC poyankha madando ndipo adavomera kuti Tippex adapezeka mmalo owerengera mavoti. Mboni ya Mutharika Ben Phiri yemwe ndi nduna ya maboma aangono ndi chitukuko cha mmidzi adavomereza kuti chisankho chidakumana ndi zokhoma zambiri koma adati vuto lidali bungwe la MEC pogwiritsa ntchito anthu omwe sadaphunzitsidwe mokwanira. Mlanduwo ukuyendetsedwa kukhoti lapadera lomwe likumvedwa ndi oweruza 5 omwe ndi Healey Potani, Mike Tembo, Dingiswayo Madise, Ivy Kamanga ndi Redson Kapindu. Mmwezi wa June 2019, Khothili lidakana pempho la woimirira Mutharika ndi MEC loti mlanduwo angowusiya chifukwa wodandaula sadatsate ndondomeko zoyenera zosumira koma khothi lidati mlanduwo upitilire. Mlanduwu ukunka kumapeto tsopano koma wakumana nzokhoma zambiri monga ziletso ndi kuimaima makamaka pomwe a mbali yoyankha mlandu adapempha sabata ziwiri zoti akatolere umboni kwa omwe amayanganira mmalo oponyera voti. Panyengoyi padamveka mphekesera yoti okatolera umboniwo amaopseza kapena kukakamiza ndi kunyengerera oyanganira mmalowo oponyera votiwo kuti azisayinira zikalata zomwe zidagwira ntchito koma zosasayina ndi kupereka umboni wabodza. Pachifukwachi, otsatira zipani za MCP ndi UTM adayamba kuthotha anthuwo akafika mdera lawo zomwe zidapangitsa kuti ntchitoyo ayionjezere ndi sabata ina. Sabata yathayi, mbali zonse zokhudzidwa pa mlanduwo kuphatikizapo abwenzi a khoti Malawi Law Society (MLS) ndi Women Lawyers Association (WLA) adamaliza kupereka zindunji za mfundo zawo ndipo nkhani yatsala mmanja mwa majaji kuti agamule.
11
Akayidi Atsopano Adziyezedwa Coronavirus-MPS Nthambi ya ndende mdziko muno ya Malawi Prison Service (MPS) yati idziyamba yayeza akayidi omwe angomangidwa kumene ngati ali ndi kachirombo ka Coronavirus. Malinga ndi wofalitsa nkhani za nthambiyi, Superintendent Chimwemwe Shawa, njirayi ithandiza kuti anthu omwe akukayamba kumene ukayidi wawo asafikitse nthendayi mndendezi. Adziyamba ayezedwa kaye Tikugwira ntchito limodzi ndi anthu azachipatala powonetsetsa kuti akayidi omwe akubwera azikayamaba ayezedwa kaye asanalowe mu ndende, anatero Supretendent Shawa. Pa nkhani yomwe mtsogoleri wa dziko lino ananena yoti akayidi omwe anapalamula milandu ingonoingono atulutsidwe, Shawa wati padakalipano maina a akayidi omwe ayerekedzedwa kuti atulutsidwe aperekedwa ku komiti yomwe ikuwona za nkhaniyi. Iwo anati, Ndende za mdziko muno ndi zodzadza ndipo akayidi sangakwanitse kumakhala motalikirana 1 mita koma ife tikuyesetsa kuti akayidiwa apungulidwe ndipo zonse zaperekedwa ku komiti yowona zimenezi.
6
Atsatsidwa kugula anthu kawiri Njonda ina yomwe ikuchita bizinesi yake ya golosale ndi chigayo pa boma ku Dowa yadandaula kuti anthu akuiwonongera mbiri chifukwa yatsatsidwapo anthu kawiri konse. Stanley Ishmael adauza Msangulutso kuti zimenezi ndizongofuna kumuonongera mbiri yake chifukwa iyeyu sagula anthu. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Anthu akakhala, basi amangoganiza kuti timapanga zimenezo, koma sichoncho. Sindipanga zimenezo, adatero Ishmael. Malinga ndi Ishmael, miyezi yapitayo, amayi ena adafika pagolosale yakeyo kukatsatsa amuna awo pomwe sabata yatha mnyamata wina adamutsatsa msuweni wake wa zaka 20 pomutchula kuti nkhuku yoyera. Ishmael adalongosola kuti adadzidzimuka sabata yathayi ataitanidwa ndi mzake wina kuti kwabwera kalata yake kuchokera kwa mkulu wina wa zaka 26 wochokera mmudzi mwa Chinyanya T/A Chiwere mboma la Dowa. Mkalatamo adalongosola zoti wakhala akulota katatu konse ndikumufunsa ngati ali ndi nkhuku yoyera, adalongosola Ishmael. Iye adati apa awiriwo adamuitanitsa mkuluyo kuti adzawalongosolele zomwe amatanthauza mkalatamo. Apa adatiuza kuti umphawi wamuvuta ndipo ali ndi munthu woti akufuna kundigulitsa. Izi zidandiopsa ndipo ndidakaitula nkhaniyi kupolisi komwe adandiuza zochita, adatero Ishmael. Iye adati mkuluyo adamtumiza msuweni wake wa zaka 20 yemwe amamtsatsayo kugolosale ya Ishmael ati kuti akamuone. Malinga ndi Ishmael, adamuitanitsanso mkuluyo kuti adzalongosole bwino za malondawo. Sadachedwe ayi. Adabweradi, apa nkuti nditawauza kale apolisi ndipo apolisiwo adatipeza tikukambirana za mtengo womwe panthawi yomwe amammangayi adali asadatchule, iyer adatero. Koma Ishmael adati apolisiwo atangofika pamalopo mkuluyo adayamba kukana kuti sichoncho, koma apolisi adamumanga kuti akayankhire komweko.
7
Dziko La Malawi Lili Ndi Kuthekera Kochita Zinthu Palokha Chisankho chatsopano cha mtsogoleri wa dziko akuti chawonetsa kuti dziko la Malawi lili ndi kuthekera kochita zinthu zina za chitukuko palokha, mosadalira thandizo lochoka ku maiko kapena mabungwe ena. Mmodzi mwa anthu amene amalankhulapo pa zinthu zosiyanasiyana mdziko muno Coxley Kamange, wanena izi pamene amathilirapo ndemanga pa momwe chisankhochi chayendera. Anthu kuponya voti yawo pa chisankhocho Chisankhochi chachitika ndi ndalama zochokera ku boma popanda thandizo lililonse lochokera ku mabungwe omwe nthawi zambiri amathandizira pa chuma komanso kuzawonelera momwe chikuyendera. Kamange wati zimenezi zikutanthauza kuti ndalama zomwe boma limatolera kudzera mmisonkho ndi zokwanira kuchitira zinthu zina ndipo watinso anthu a mdziko la Malawi ali ndi kuthekera koyendetsa bwino zinthu ndi nzeru zawo. Mmene ayendetsera zinthu Dr. Kachale komanso mmene boma lakwaniritsira boma kupereka ndalama zochititsira chisankhochi, dziko la Malawi likhala chitsanzo cha mayiko ena kuti mayiko asamaziyanganire pansi koma kuti atha kukwanitsa kuyendetsa zinthu pawokha, anatero a Kamange. Mwazina iwo alimbikitsa omwe apambane pa chisankhochi kuti asangalale mosaphwanya ufulu wa ena komanso omwe atagonje kuti avomereze.
2
Zipani zisaope achinyamata Bungwe lolimbikitsa achinyamata pa ndale mu Africa la Centre for Young Leaders in Africa (CYLA), lapempha zipani zandale mdziko muno kuti zisaope kugwira ntchito ndi achinyamata. Malingana ndi mtsogoleri wa pulogalamu yotchedwa Programme for Young Politicians in Africa (PYPA) ku bungwe la CYLA wochokera mdziko la Zambia, Anna Mate, achinyamata asakhale chiopsezo koma chitetezo pa ndale za mchipani. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Mate: Achinyamata ndi ambiri Mate wati zipani zambiri zimene bungwe la CYLA lagwira nazo ntchito zimaonetsa kuti zikupereka mfundo zokhwima ndi cholinga choti achinyamata azichita mantha nkubwerera mmbuyo pa ndale. Ife monga olimbikitsa achinyamata pa ndale tidakumana ndi akuluakulu a zipani zandale zokhazikika mdziko muno ndipo tawalimbikitsa kuti agwire limodzi ntchito ndi achinyamata pa ndale, adatero Mate. Iye adati ali ndi chikhulupiliro kuti uthengawu wadza mnthawi yake potengera kuti nzika za dziko lino zikukonzekera kukaponya voti ya patatu chaka cha maya. Iye adatinso zipani zomwe zatsogoza achinyamata mmaudindo zimakhala ndi mwayi waukulu wopititsa patsogolo kuchuluka kwa owatsatira potengera kuti achinyamata ndi omwe akutenga gawo lalikulu la chiwerengero cha dziko lino. Iwo apemphanso achinyamata kuthandizana komanso kulimbikitsana pamene akufuna kutengapo gawo pa ndale. Pakadali pano CYLA ikupitirira kufikira achinyamata ndi cholinga chowadzindikiritsa za udindo wawo pa ndale za dziko lino kuphatikizapo kuwalimbikitsa kukaponya voti pa zisankho za patatu za chaka cha mawa. Pothirirapo ndemanga yemwe akufuna kudzaimira chipani cha Malawi Congress Party (MCP), ku Salima Gerald Phiri adati zipani zayamba kuthandiza oyimira posatengera zaka za munthu. Atsogoleri asamangotigwiritsa ntchito achinyamata poyambitsa zipolowe basi. Nthawi yakwana yoti tigwire ntchito limodzi ndi akuluakulu popanda kuopsezedwa, adatero Phiri.
11
Mtambo walowa ndale Yemwe adali wapampando wa gulu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) Timothy Mtambo wati wasintha nthabwa ndipo pano wayamba ndale zenizeni. Mtambo wati waganiza zoyamba ndale ndipo wati cholinga chake chachikulu nkuthandizira mgwirizano wa zipani za Malawi Congress Party (MCP) ndi UTM Party kuchotsa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wa Democratic Progressive Party (DPP) pampando. Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Mtambo kulankhula pazionetsero zina mmbuyomu Iye wayambitsa gulu la ndale lomwe silidafike pa chipani ndipo akulitcha Citizens for Transformation (CFT) ndipo wati ndi wokwiya kwambiri ndi momwe chipani cha DPP chasokonezera dziko la Malawi. Ndakhala ndikulingalira za dziko lino kuyambira pomwe tidapeza ufulu wa demokalase mu 1994 ndipo ndaona kuti dziko lathu laonongeka kwambiri chifukwa cha ulamuliro wopanda masomphenya, adetero Mtambo polengeza zakutembenuka kwake Lachitatu ku Lilongwe. Kadaulo pa ndale George Thindwa wati ngakhale Mtambo wasiya anzake padzuwa, iye watembenuka nthawi yabwino chifukwa akhonza kukwaniritsa zolinga zake mosavuta komanso mosadikira nthawi yaitali. Ngati mwamumvetsa, akuti akufuna kuthandizana ndi mgwirizano wa MCP ndi UTM kuchotsa Mutharika pampando. Masomphenya awa ndi nthawiyi walondola chifukwa ngati amapanga za mseri, tsopano amasuka, watero Thindwa. Pogwirizana naye, kadaulo wina Mustafa Hussein wati Mtambo wachita bwino chifukwa wayamba ndale ataona kale momwe ndalezo zimakhalira ndiye sakavutika kukwaniritsa zolinga zake. Mtambo wakhala akutsogolera zionetsero zosiyanasiyana mdziko muno ndipo wakumana ndi zambiri pantchitoyi. Iyeyu ali ngati wandale kale yemwe wakumana ndi zokhoma ndiye waganiza bwino, watero Hussein. Naye kadaulo pa kayendetsedwe ka zinthu mdziko Makhumbo Munthali wati ngakhale pakhonza kukhala mafunso pa ganizo la Mtambo losiya kutsogolera HRDC, zolinga zake sizikadakwaniritsidwa akadakakamira ku gululo. Ali ndi zolinga zomveka koma sakadazikwanitsa akadakhala ku HRDC. Iyeyu amayenera ndithu kukhala paufulu ngati wandale ndithu mpomwe zimuyendere bwino. Ife timuika mmapemphero kuti akwaniritse zofuna zake, watero Munthali. Akadaulo atatuwa agwirizananso pa mfundo yoti kuchoka kwa Mtambo sikungasokoneze gulu lonse chifukwa mapulogalamu onse a bungwe amapangira limodzi ndi anzake omwe wawasiya ndiye iwowo apitiriza pomwe iye wasiyira. Koma nduna ya zachitetezo cha mdziko Nicholas Dausi ndi nduna ya zofalitsa nkhani Mark Botoman ati sakudabwa kuti Mtambo wabwera poyera ndi ndale chifukwa iwo adadziwa kale kuti mkuluyu ndi wandale. Asatiphimbe mmaso kuti lake ndi gulu chabe ayi koma kuti ndi chipani cha ndale. Ganizo lake silalero ndipo labwera ngati chithokozo kuchipani cha MCP ndipo muona amupatsa mpando waukulu kuchipani,adatero Dausi.
11
Sensasi ili mkati Pamene kalembera wa anthu ndi nyumba ali mkati, mafumu ena ati akuyembekezera kuti mavuto amene amakumana nawo achepa chifukwa boma limagwiritsa ntchito zotsatira za kalemberayo popereka zofunika kwa Amalawi. Kalemberayo, amene amachitika pakatha zaka 10 zilizonse, adayamba pa 3 mwezi uno ndipo akuyembekezeka kudzatha pa 23. Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Masankhidwe a nduna autsa mapiri pa chigwa Malonjezo ayamba kuoneka Wogwira ntchito ya kalembera kulembera banja lina ku Lilongwe Polankhula ndi Tamvani, T/A Mlauli ya ku Mwanza, T/A Chindi ku Mzimba komanso T/A Mkanda ku Mchinji adanena payekhapayekha kuti ali ndi chiyembekezo kuti mavuto amene adza kaamba ka kukula kwa chiwerengero achepa. Vuto lalikulu limene tili nalo ndi la madzi. Ngakhale anthu akumanga nyumba zofolera ndi malate, madzi tikumwabe mzitsime zosasaamalika. Izi zimadzetsa matenda amene timakavutikanso nawo kuchipatala, adatero Mkanda. T/A Chindi adati ngakhale kuli mavuto ena monga kusowa vuto la zaumoyo, nkhani yamadzi siyimugoneka tulo. Amayi amadzuka mbandakucha kukatunga madzi dzuwa litakwera. Kungochedwa pangono ndiye kuti pakhomo pawo. Mukhonza kuona ngati madzi akukanganiranawo ndi a pampope, koma ayi ndi a pachitsime, adatero Chindi. T/A Mlauli wa ku Neno idati vuto la madzi likusautsa, makamaka mchilimwe pomwe dzuwa likuomba kwambiri. Iye adati izi zikukhudzaa kwambiri dera lake limene ndi lotentha kwambiri. Akukonza zina ndi zina, koma pa nkhani ya madzi, tisanamizanepo zinthu zikuyipirayipira. Mijigo ili apo ndi apo koma chiwerengero cha anthu ofuna madzi abwino chikungokwererabe, adatero Mlauli. Kalemberayu akuyamba kumene, padali mavuto osiyanasiyana, kuphatikizapo la kuchedwa kwa malipiro a ogwira ntchitoyi 25 000 pomwe adangolandira K20 000 mmalo mwa K120 000 imene amayenera kulandira ataphunzira ntchitoyi. Ogwira ntchito enanso adandaula kuti sanapeze nawo lamya zogwirira ntchitoyo. Vuto lina lidali la kubedwa kwa zipangizo za ogwira ntchitoyi ku Ntcheu. Mneneri wa nthambi yoona za kalemberayu ya National Statistical Office (NSO) Kingsley Manda adatsimikiza za mavutowa koma adati zonse zili tayale tsopano. Chilichose chilibwino, onse adalandira ndalama zawo, tawatsimikizira kuti mayunitsi afika sabata ino koma awo amafuna lamyawo, tawafotokozera kuti lamya nzawokhawo omwe akuyenda mmidzi kutenga mafigala, adatero Manda. Iye adati vuto lalikulu lomwe lidalipo lidali lokhudza netiweki yotumizira ma figala makamaka mmadera momwe mulibe netiweki koma vutolonso adalikonza. Padali vuto la netiweki mmadera ena ndiye poti makina omwe tikugwiritsa ntchito ngolira netiweki kuti tilumikizane, tidapereka galimoto zomwe akumagwiritsa ntchito kuyenda kukafika pomwe pali netiweki nkutumiza, adatero Manda. Mmodzi mwa owelengera anthuwa ku Mpsupsu mboma la Zomba amene sanadzitchule dzina adati pa tsiku akumawerenga makomo osachepera 40. Iye adati ngakhale nyumba za derali zili patalipatali koma akumakwanitsa kuwerenga anthu ochuluka chotere chifukwa kufunsa mafunso pogwiritsa ntchito tablet sizikumatenga nthawi kuti atsirize. Mmodzi wa anthu amene awerengedwa kwa Jali mboma la Zomba Lones Kamwana adati mphindi zosaposera 45 zimene adafunsidwa mafunso akuti mphindizi zidali zopindulitsa kwa iye mwini ngakhalenso ku dziko. Mafunso ake akumufukula munthu kuchokera pa phata zinthu zimene a Malawi tikayankha mwachilungamo zithandizira kuti dziko lathu lino likhale lotukuka, adatero Kamwana. Kalembera wa mchaka cha 2008 chiwerengero cha anthu chidapezeka kuti ndi 13 077 160. Lipoti la kalemberayu limasonyeza kuti anthu 48 mwa anthu 100 aliwonse amamwa madzi a pamjigo, anthu 18 pa 100 aliwonse amamwa mzitsime zosatetezedwa. Lipotili likusonyezaso kuti anthu 43 pa 100 amakhala mnyumba zawedewede, anthu 34 pa 100 amakhala mnyumba zowonekako bwino ndipo 23 pa 100 aliwose amakhala mnyumba zolongosoka. Malinga ndi NSO, chiwerengero cha Amalawi chikhonza kufika pa 17 931 637 chaka chino.
11
JB achotsa Kachali ku EC Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda wabweza moto, ndipo wachotsa wachiwiri wake Khumbo Kachali pampando woyanganira bungwe la chisankho la Electoral Commission (EC). Chisale watuluka nkumangidwanso Sipakala waimitsa Nyumba ya Malamulo Chakwera akwanitse malonjezoHRDC Izi zadza ena atahauka, ponena kuti kusankhidwa kwa Kachali paudindowo, kukadachititsa kuti EC idzayendetse chisankho cha 2014 mokondera chipani cha PP. Banda adaika Kachali paudindowo sabata ziwiri zapitazo, pomwe amasankha nduna zatsopano. Polengeza za kusintha maganizoko, nduna yofalitsa nkhani Moses Kunkuyu adati ngakhale Banda sakuona kuti zidalakwika kuika Kachali pampandowo, chifukwa amangomupatsa mphamvu zomwe mtsogoleri wadziko ali nazo, malinga ndi ndime 6 ya malamulo oyendetsera chisankho, wamvera zofuna za anthu ndipo wachotsa Kachali. Ndimeyo imanena kuti bungwe la EC liyenera kufotokoza momwe zinthu zikuyendera kwa mtsogoleri wa dziko lino ndipo woimira anthu pa milandu Wapona Kita adati mtsogoleri wa dziko linonso amapatsidwa mphamvu zouza ena agwire ntchito zina zomwe akadagwira. Koma mphunzitsi wa za malamulo kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College Dr Mwiza Nkhata adati mtsogoleri wa dziko lino sakadasiira ntchitoyo kwa wachiwiri wake. Bungwe loyendetsa chisankho liyenera kuima palokha ndiye zitheka bwanji kuti wina amene akukhudzidwa ndi chisankho aziliyanganira? adatero Nkhata. Mawuwa akuphera mphongo zomwe akadaulo ena a zamalamulo adanena mmbuyomu monga mkulu wa bungwe la oimira anthu pamlandu John Gift Mwakhwawa, mkulu wa EC Maxon Mbendera ndi azipani zina.
11
Ana avala umasiye Makolo akali moyo Nthawi ya nkhomaliro yakwana, pamsika wa Manje mumzinda wa Blantyre ambiri akudya nsima pamene ena akusaka chakudya. Pa Wenela pasintha zedi ANatchereza Tidakumana ku sukulu ku Chiradzulu Kuponya maso patali pali ana atatu, Fakili wa zaka 8, Pemphero, 7, ndi Yamikani 4. Pemphero lawo nkuti apeze chakudya. Anawa aima pafupi ndi mpanda wa mfumu Misesa. Tikufuna tipemphe mango, tilibe chakudya, adatero Fakili, uku akutonthoza Yamikani amene akulira chifukwa chomukaniza kutoleza makoko a mango. Uwu ndiye umasiye omwe anawa auvala makolo awo ali moyo. Zonsezo zikuchitika chifukwa makolowo sakumwetsana madzi. Kumenyana kwa njobvu, wovutika ndi udzu. Fakili akulephera kufotokoza bwinobwino chomwe chidachitika kuti ayambe kukhala moyo wovutika choncho. Fakili (Kumanja) ndi abale ake Yamikani ndi Pemphero Amayi sakutifuna. komanso ababa adachoka koma pena amatisaka, adatero iye. Mfumu Misesa ikuti anawa si achilendo mdera lake. Gulupuyu akuti patha mwezi anawo akungoyendayenda mdera lake. Kunyumba kwanga agona masiku awiri, adatero iye. Uko atawathyolera mango kuti azikukuta, Misesa adati banja la makolo a anawo lidatha ndipo kuchokera pa nthawiyo, anawo akhala akuzunzika. Ndidawaitana onse kuti tikambirane koma zidakanika. Mkazi akuti iye adapeza banja lina ndipo sangasunge anawa pamene bamboyo ali ndi chidwi chowasunga koma akuti sangathe chifukwa alibe pokhala komanso ntchito idatha, adatero Misesa. Lolemba Msangulutso udakumana ndi bambo wa anawa. Bamboyo, Dave Singano adati mtima wosunga anawo ali nawo koma sangathe chifukwa alibe thandizo. Zikundiwawa kuti anawa akuzunzika komabe palibe chomwe ndingachite chifukwa ndilibe thandizo. Ndilibenso pogona, ndiye ngakhale ndiwatenge akagona potani? adatero Singano. Bamboyu adati patha zaka zitatu chisiyirane ndi mkazi wake. Iye adati adathetsa banja lake pomuganizira mkaziyo kuti akumuyenda njomba. Panthawiyo ndinkagwira ntchito ya ulonda. Ndiye anthu ena adanditsina khutu kuti ndikachoka kukumabwera mwamuna mnyumbamo. Nditakambirana ndi mkazi wanga sitidamvane ndipo banja lidatha, adatero. Singano akuti adagwirizana ndi mkazi wake komanso amfumu kuti anawo akakhala ndi mkaziyo ndipo iye azipereka thandizo. Panthawiyo zidachitika momwemo, koma kungotha miyezi yochepa adasintha pamene adati sangakwanitse kukhala ndi anawo poti wapeza mwamuna wina. Ndidakhala ndi anawo komabe nanenso zidandisokonekera, ntchito idatha, adandichotsa palendi. Ndikadatani? adatero Singano. Iye adati patha chaka chimodzi tsopano anawa akukhala wokha, komabe ndikapeza thandizo ndimawasaka. Monga dzana [Lamulungu] ndidawatenga ndipo ndidakagona nawo ku Chilobwe kwa mnzanga, adatero iye. Naye mkazi wa bamboyu akuti adauza bwalo la mfumu Misesa kuti sangatenge anawo chifukwa adakwatiwanso. Adauza bwalo kuti anawa sakuwatenga, patsikulo adabwera ndi mwamuna wake watsopanoyo. Nditamuitananso kuti tidzakambirane sadabwere mpaka lero, adatero Misesa. Gawo 60 loteteza ana, limati kholo lolephera kusamala ana ake liyenera kunjatidwa. Misesa akuti nkhaniyi idapita kupolisi ndipo apolisi adanjata bamboyo koma adamutulutsa tsiku lomwelo. Koma mkulu womenyera ufulu wa ana kubungwe la Centre for Childrens Affairs Malawi, Moses Busher adadzidzimuka ndi nkhaniyo ndipo adati makolowa akuyenera kunjatidwa. Iye adati bungwe lawo litengera nkhaniyo kukhoti la ana. Ngati bungwe lomenyera ufulu wa ana, nkhaniyo sitiyisiya mpaka anawa athandizidwe. Mayi akuyenera kusunga anawo mosayangana kuti wakwatiwa kapena ayi ndipo bamboyo akuyenera kumawathandiza. Tifufuza ndipo ana amenewa athandizidwa, adatero Busher. Atafunsidwa ngati ndikololedwa kuti anawa atengedwe ndi banja lina kukawasunga ngati ana awo, Busher adati ndizotheka pokhapokha ndondomeko itatsatidwa. Koma poona kuti makolo awo onse alipo ndipo izi zangochitika chifukwa cholekerera, zifukwa zotenga anawa kukhala ako sizikumveka, adaonjeza. Pamene mutu wa nkhaniyi ukufufuzidwa, moyo wa anawo udakali pamavuto adzaoneni. Kusukulu sapita, pogona ndi kubowo kwa uvuni ya njerwa, mkalasi, apo ayi apemphe pakhomo pa eni. Chakudya chawo ndi mango, misonga ya mzimbe ndipo akadya bwino ndiye kuti banja lina lawagawira.
15